Mutu 12
Magwero Apamwamba Kwambiri a Nzeru
“Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.” (Salmo 104:24) Inde, kuchokera kuulemerero wa chilengedwe chachikulucho kukafika pakukongola kwakanthaŵi kwa maluŵa, chilengedwe chimachitira umboni nzeru yosayerekezereka ya Mlengi wake. Luso lazopangapanga la m’zaka zino za zana la 20 limawoneka ngati losanunkha kanthu poliyerekezera ndi ntchito za Mulungu. Ngati Baibulo liri Mawu a Mulungu, tikaliyembekezeranso kupereka umboni wa nzeru imene iri yoposa maluso a munthu. Kodi iro limatero?
1. (Phatikizamoni mawu oyamba.) (a) Kodi nkuti kumene timawona umboni wa nzeru yosayerekezeka ya Mulungu? (b) Kodi ndiuphungu wotani umene Baibulo limapereka ponena za nzeru?
BAIBULO limagogomezera kufunika kwa nzeru. Limanena kuti: “Nzeru ipambana,” ndipo “tatenga nzeru; m’kutenga kwako konseko utenge luntha.” (Miyambo 4:7) Limavomerezanso kuti anthufe kaŵirikaŵiri timasoŵa nzeru, ndipo limatilimbikitsa kuti: “Wina wa inu ikamsoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, ndi wosatonza.”—Yakobo 1:5.
2. Kodi munthu angawonjezere motani nzeru yake?
2 Kodi ndimotani mmene Mulungu ‘amaperekera nzeru modzala manja’? Njira imodzi ndiyo mwa kutilimbikitsa kumvetsera ku Baibulo ndi kuphunzira kuchokera mu iro. Bukhu la Baibulo la Miyambo limatifulumiza kuti: “Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru, kulodzetsa mtima wako kukuzindikira; . . . udzazindikira kuwopa Yehova ndi kumdziŵadi Mulungu. Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziŵa ndi kuzindikira kutuluka mkamwa mwake.” (Miyambo 2:1, 2, 5, 6) Pamene tigwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo ndi kuwona mmene uliri wogwira ntchito, timafikira pakuzindikira kuti umaimiradi nzeru yaumulungu.
Maneno a Nzeru
3, 4. (a) Kodi Baibulo limanenanji ponena za kupanda pake kwa kukonda ndalama? (b) Kodi ndikukhala pachikatikati kwabwino kotani kumene Baibulo limasonyeza m’kupereka uphungu kwa ife ponena za phindu la ndalama?
3 Kuti tizindikire zimenezi bwino kwambiri, tiyeni tiyang’ane pamavesi oŵerengeka a Baibulo. Lingalirani mawu anzeru aŵa: “Awo amene ali otsimikizira kukhala olemera amagwera m’ziyeso zambiri ndi m’misampha ndi zikhumbo zambiri zopusa ndi zovulaza . . . pakuti kukonda ndalama ndiko muzu wa mtundu uliwonse wa zinthu zovulaza.” (1 Timoteo 6:9, 10, NW) Yerekezerani zimenezi ndi lingaliro lamakono—pafupifupi la m’chitaganya cha maiko a Kumadzulo—limene limalimbikitsa anthu kulondola ndalama monga chonulirapo chawo chachikulu. Mwachisoni, ambiri amapeza chuma chimene iwo amafunafuna ndipo komabe amakhala ndi lingaliro la kukhala opereŵera ndi osakhutira. Katswiri wophunzira za maganizo ananena kuti: “Kukhala Nambala 1 ndi wolemera sikumakupangitsa kukhala wokhutira, kukhutiritsidwa, kukhala wolemekezedwa kwenikweni kapena wokondedwa.”1
4 Sikuti munthu weniweni angathe kupatuka kotheratu pandalama. Baibulo limasonyeza nzeru yachikatikati yoyenera pamene iro limanena kuti: “Nzeru itchinjiriza monga momwe ndalama zitchinjirizira; koma kuposa kwa chidziŵitso nkwakuti nzeru imasunga wamoyo mwini wake.” (Mlaliki 7:12, NW) Motero, Baibulo limatithandiza kuwona kuti ndalama, pamene kuli kwakuti nzofunika, sizofunika koposa. Ziri chabe njira yofikira zonulirapo, ndipo ziri za phindu lochepa ngati tiribe nzeru ya kuzigwiritsira ntchito moyenera.
5, 6. (a) Kodi nchifukwa ninji uphungu wa Baibulo wa kupeŵa mayanjano oipa uli wanzeru? (b) Kodi timapindula motani ndi “kuyenda ndi anthu anzeru”?
5 Mawu a Baibulo aŵa alinso owona: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mzawo wa opusa adzapwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Kodi munayamba mwawona mmene mabwenzi athu amakhalira ndi chiyambukiro champhamvu pa ife? Chitsenderezo cha ausinkhu wawo chatsogolera achichepere ambiri kuloŵa m’kuledzera, kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala oledzeretsa, ndi chisembwere. Ngati tisakanikirana ndi awo amene amagwiritsira ntchito kutukwana, ife potsirizira pake timadzipeza ife eni tikugwiritsira ntchito kutukwana. Kuyendera limodzi ndi anthu osawona mtima kumakhoterera kutipangitsa kukhala osawona mtima. Zowonadi, monga momwe Baibulo limaneneranso kuti, “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.”—1 Akorinto 15:33.
6 Kumbali ina, mayanjano abwino angathe kutichititsa kuwongokera. Mwa ‘kuyenda ndi anzeru,’ ife tidzakhala anzeru ife enife. Zizolowezi zabwino zimatsalira, monga momwedi zoipa zimachitira. Kachiŵirinso, Baibulo limasonyeza nzeru yaikulu m’kutilimbikitsa kusankha mayanjano athu mosamalitsa.
7. Kodi nchiyani chimene chimapangitsa Baibulo kukhala lapadera monga magwero a uphungu?
7 Baibulo liri ndi malingaliro ambiri oterowo otithandiza kutsogoza miyoyo yathu. Monga magwero a chilangizo, liri lapadera. Uphungu wake nthaŵi zonse uli wopindulitsa. Suuli wa kungonenedwa chabe, ndipo sumachititsa konse chivulazo pa ife. Uphungu wochuluka wa Baibulo uli wosafanana ndi wina uliwonse. Amene amaugwiritsria ntchito m’miyoyo yawo, ndi kuwona mmene umagwirira ntchito nthaŵi zonse kaamba ka ubwino wawo, amafikira pa kuzindikira Baibulo kukhala magwero apadera anzeru.
Malamulo a Mkhalidwe Abwino Anzeru
8. Kodi ndimotani mmene Baibulo lingatithandizire ngakhale pamene tiyang’anizana ndi mkhalidwe umene suunatchulidwemo mwachindunji?
8 Komabe, bwanji ngati, tiyang’anizana ndi mkhalidwe umene suukutchulidwa mwachindunji m’Baibulo? Kaŵirikaŵiri, timapeza malamulo a makhalidwe abwino ochuluka otitsogoza. Mwachitsanzo, ambiri panthaŵi ina m’miyoyo yawo amakumana ndi chosankha ponena za chizoloŵezi cha kusuta fodya. Popeza fodya anali wosadziŵika ku Middle East m’masiku a Yesu, Baibulo silimamtchula. Komabe, pali malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo oyenerera amene angathandize kupanga chosankha chanzeru.
9-11. Kodi malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo amatithandiza motani kufika pachosankha chanzeru m’nkhani za kugwiritsira ntchito fodya, ndipo kodi timapindula motani mwa kutsatira malamulo a makhalidwe abwino ameneŵa?
9 Pamene kusuta fodya, kuli kwakuti kumasimbidwa kuti kumapereka lingaliro la kukondwera ndi kumasula thupi, kwenikweni kumaloŵetsamo kukokera zoipitsa zomamatira kuziloŵetsa m’mapapu. Wosuta fodya amaipitsa thupi lake, kudzanso zovala zake ndi mpweya womzungulira. Ndiponso, kusuta fodya nkomwerekeretsa. Anthu amene amafuna kusiya kaŵirikaŵiri amakuwona kukhala kovuta kwambiri. Tiri ndi zimenezi m’maganizo, tingathe kuyang’ana ku Baibulo kaamba ka chithandizo m’kupanga chosankha chanzeru ponena za kusuta fodya.
10 Choyamba, lingalirani vuto la kumwerekera. Mtumwi Paulo, pamene anali kulankhula za zakudya, anati: “Sindidzalamulidwa nacho chimodzi.” (1 Akorinto 6:12) Paulo anali waufulu kudya chakudya chirichonse, koma iye anadziŵa kuti anthu ena kalero anali ndi zikumbumtima zosachedwa kuvutika. Chotero iye anati iye saanali “womwerekera” kuzakudya zakutuzakuti kwakuti iye sakanatha kuzileka ngati iye anafunikira kutero mmalo mwakuti asakhumudwitse ena. Ngati munthu sangathe kuleka kusuta fodya—kapena kufunafuna fodya—iye ndithudi ‘akulamulidwa’ naye. Chotero mawu a Paulo onena za nkhani ya chakudya ali chitsogozo chabwino kaamba ka kugwiritsiridwa ntchito kwa fodya. Sitiyenera kudzilola ife eni kukhala akapolo a chizoloŵezi.
11 Chachiŵiri, lingalirani nkhani ya kuipitsa. Baibulo limanena kuti: “Tidzikonzere tokha kuleka chodetsa cha thupi ndi cha mzimu.” (2 Akorinto 7:1) Mosakaikira kusuta fodya ndiko chodetsa, kapena choipitsa, thupi. Kuwopsa kwa kuipitsa kumeneku kukuwonedwa m’chenicheni chakuti, malinga ndi kunena kwa Gulu Lapadziko Lonse la Zaumoyo, kumachititsa anthu oposa miliyoni imodzi kufa mofulumira chaka chirichonse. Ngati titsatira malamulo a khalidwe labwino a Baibulo onena za kukhala woyera ku zodetsa zathupi, tidzatetezeredwa kumaupandu aakulu kwambiri a thanzi ochokera m’kusuta fodya, kudzanso mankhwala oledzeretsa ndi zodetsa zina.
Mawu Opindulitsa
12. Kodi nchifukwa ninji uphungu wa Baibulo nthaŵi zonse umagwirizanitsidwa ndi thanzi lathu lakuthupi ndi la malingaliro?
12 Sitiyenera kukhala odabwa kuti kutsatira uphungu wa Baibulo kumatitetezera m’njira yakuthupi. Uphungu wa Baibulo umachokera kwa Mulungu. Mlengi wathu, ali ndi chidziŵitso chokwanira chonena za mmene ife tapangidwira ndi zimene tifuna. (Salmo 139:14-16) Uphungu wake nthaŵi zonse ngwogwirizanitsidwa ndi thanzi lathu lakuthupi ndi la malingaliro.
13, 14. Kodi nchifukwa ninji iri njira yanzeru kutsatira uphungu wa Baibulo wa kusanena mabodza?
13 Zimenezi zikuwonedwa muuphungu wa kusanena mabodza. Mabodza andandalikidwa pakati pa zinthu zisanu ndi ziŵiri zimene Yehova amazida, ndipo bukhu la Chivumbulutso limandandalika abodza pakati pa awo amene sadzakhala ndi malo m’dziko latsopano la Mulungu. (Miyambo 6:19; Chivumbulutso 21:8) Mosasamala kanthu za zimenezi, kunama kuli kofalikira. Magazine ena a bizinesi anati: “U.S. akukhala ndi kuyambika koipa kwambiri kwa kukwangwanutsa, chinyengo ndi kugwiritsira ntchito molakwa kofananako m’mbiri yake.”2
14 Komabe, ngakhale kuti kunama kuli kofala monga momwe kulirimu, iko nkoipira chitaganya ndipo nkoipiranso munthuyo. Mkonzi wa magazine Clifford Longley molunjika anena kuti: “Mabodza amavulaza wonamayo ndi wonamizidwa, pamlingo wawo waukulu kopambana, mwa kuleketsa kugwirizana kofunika kwambiri kumeneku pakati pa maganizo ndi zenizeni.”3 The American Journal of Psychiatry imafotokoza kuti: “Chiyambukiro cha pamalingaliro a anthu onamizidwa mabodza chingathe kukhala chosakaza. Zosankha zazikulu za moyo zingazikidwe pa chidziŵitso chonama chokhulupiriridwa kukhala cholondola. Mabodza angathenso kukhala ndi ziyambukiro zoipa pa onama iwo eniwo.”4 Ha, nkwabwino kwambiri chotani nanga kunena zowona, monga momwe Baibulo mwanzeru limalangizira!
15, 16. Kodi ndim’njira zotani kuliri kotipindulitsa kutsatira uphungu wa Baibulo wa kusonyeza chikondi kwa ena?
15 M’njira ina yotsimikizira kwambiri, Baibulo limatiuza kuti tiyenera kukhala odera nkhaŵa ndi ena, kusonyeza chikondi kwa iwo, ndi kukhala othandiza kwa iwo. Mawu a Yesu ali odziŵika bwino anati: “Chifukwa chake, zinthu zonse, zimene mufuna kuti anthu akuchitireni, inunso mofananamo muwachitire iwo.”—Mateyu 7:12, NW.
16 Ha, dziko likanakhala labwino kwambiri chotani nanga ngati munthu aliyense akanatsatira lamulo limeneli! Ndiponso, malinga ndi kunena kwa kufufuzidwa kwa maganizo kumene kunachitika mu United States, anthu akanamva bwino kwambiri. Anthu 1 700 amene anafunsidwa anasimba kuti kuthandiza ena kunawapatsa lingaliro la kudekha ndi mpumulo pa vuto la kusokonezeka maganizo kogwirizanitsidwa ndi kupsinjika maganizo konga ngati kupweteka kwa mutu ndi kusasa mawu. Lipotilo likutsiriza kuti: “Pamenepo, kukuwonekera kuti, kudera nkhaŵa ena ndiyodi mbali ya mkhalidwe wa munthu mofanana ndi kudzidera nkhaŵa.”5 Zimenezi zikutikumbutsa lamulo la Baibulo lakuti: “Uzikonda mnansi wako monga iwe mwini.” (Mateyu 22:39; yerekezerani ndi Yohane 13:34, 35.) Nkwachibadwa kudzikonda ife eni. Koma kuti tikhale athanzi mwamalingaliro, Baibulo limanena kuti tifunikira kuchititsa chikondi chodzikonda ife eni chimenecho kukhala cholingana ndi kukonda ena.
Ukwati ndi Makhalidwe Abwino
17. Kodi nchifukwa ninji uphungu wa Baibulo nthaŵi zina umawonekera kukhala wachikale?
17 Pamene kuli kwakuti uphungu wa Baibulo umapereka umboni wa nzeru yozama, nthaŵi zonse silimanena zinthu zimene anthu amafuna kuti zimvedwe. Kaŵirikaŵiri, limasulizidwa kukhala lachikale. Kodi nchifukwa ninji ziri choncho? Chifukwa chakuti pamene kuli kwakuti uphungu wa Baibulo uli kaamba ka ubwino wathu wa nthaŵi yaitali, kaŵirikaŵiri kuugwiritsira ntchito kumafunikira kudzilanga ndi kudziletsa; ndipo mikhalidwe imeneyi siiri yokondedwa lerolino.
18, 19. Kodi ndiiti imene iri miyezo ya Baibulo kaamba ka ukwati ndi chikhalidwe chamtima?
18 Tengani nkhani ya ukwati ndi makhalidwe abwino. Miyezo ya Baibulo panopa iri yankhokera kwambiri. Imafotokoza wa muukwati mmodzi, mwamuna mmodzi kaamba ka mkazi mmodzi. Ndipo pamene limatchula zochitika zonkitsa kumene chisudzulo kapena kulekana kungakhale kothekera, kaŵirikaŵiri iro limanena kuti chomangira cha ukwati nchamoyo wonse. “Kodi simunaŵerenge kuti iye amene anaŵalenga iwo kuyambira pachiyambi anaŵalenga iwo mwamuna ndi mkazi ndipo anati, ‘Kaamba ka chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya atate ŵake ndi amake nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzakhala thupi lomodzi’? Kotero kuti saalinso aŵiri, koma thupi limodzi. Chotero, chimene Mulungu wachigwirizanitsa pamodzi munthu asachilekanitse.”—Mateyu 19:4-6, NW; 1 Akorinto 7:12-15.
19 Ndiponso, Baibulo limanena kuti malo amodzi okha a kugonana kwachikondi ndiwo mkati mwa chomangira cha ukwati. Iro limaletsa kusonyezana chikondi koteroko kunja kwa ukwati. Timaŵerenga kuti: “Kaya adama, kapena olambira mafano, kapena achigololo, kapena amuna a kusirira zifuno zosakhala zachilengedwe, kapena amuna amene amagona ndi amuna . . . sadzaloŵa ufumu wa Mulungu.”—1 Akorinto 6:9, 10, NW.
20. Kodi miyezo ya Baibulo ya chikhalidwe chamtima ikunyalanyazidwa mofala m’njira yotani lerolino?
20 Lerolino, miyezo imeneyi ikunyalanyazidwa mofala. Profesala wachikhalidwe David Mace akuti: “Mkati mwa zaka za zana lino chikhalidwe chathu chakhala ndi masinthidwe aakulu kwambiri, ndipo miyambo yamakedzana yambiri ndi timagulu tagwedezeka kwambiri kuyambira pamaziko pake penipeni. Ukwati nawonso ukuphatikizidwa.”6 Machitachita a kugonana osadziletsa ali ofala. Kugonana pakati pa anyamata ndi asungwana omayendera limodzi kaŵirikaŵiri kumawonedwa kukhala mkhalidwe wanthaŵi zonse. Kukhala pamodzi ukwati usanachitike—‘kuti utsimikizire’—kuli kwakaŵirikaŵiri. Ndipo pamene aŵiri angokwatirana, kugonana kunja kwaukwati nkozoloŵereka.
21. Kodi nchiyani chimene chatulukapo m’kunyalanyazidwa kofala kwa miyezo ya Baibulo ya ukwati ndi chikhalidwe chamtima?
21 Kodi mkhalidwe wa chikhalidwe chamtima wosadziletsa umenewu wadzetsa chimwemwe? Ayi, suunadzetse kanthu kena kusiyapo chipwirikiti—ndipotu chipwirikiti chowonongetsa zinthu kwambiri—chomachititsa kupanda chimwemwe ndi mabanja osweka. Palinso chaola cha nthenda zopatsana mwa kugonana zonenedwa mwachindunji kukhala zochokera kumkhalidwe wosadziletsa. Kufalikira kwa chindoko, chinzonono, ndi chikhuthula, pakati pa zina, kuli kosalamulirika. M’zaka zaposachedwa, uhule ndi machitachita a kugonana kwa ofanana ziŵalo kwafulumizitsa kufalikira kwa AIDS. Pali chaola cha asungwana achichepere osakwatiwa okhala ndi ana pamene iwo eniwo sanachoke konse muubwana. Ladies’ Home Journal inanena kuti: “Chigogomezero pa kugonana chimene chinasonyeza zaka za m’ma 60 ndi m’ma 70 sichinadzetse chimwemwe cha anthu npang’ono pomwe koma kuvutika kowopsa kwa anthu.”7
22. Kodi nchiyani chimene chimadzetsa chimwemwe chachikulu kopambana, pankhani ya chikhalidwe chamtima?
22 Chotero, tsopano tikumva mawu onga ngati otsatirapoŵa onenedwa ndi profesala wa zachikhalidwe Carlfred B. Broderick: “Mwinamwake takula mokwanira kulingalira kuti kaya ngati sikudzatikhalira bwino kwambiri kupeŵa kugonana ukwati usanachitike monga njira yochitira zinthu imene iri yokhutiritsa bwino kwambiri zosoŵa za nzika zathu ndi ufulu wa zoyenera zawo: ufulu kumatenda, ufulu kumimba zosafunika.”8 Ndithudi, muyezo wa Baibulo wa chikhalidwe chabwino watsimikizira, m’kupita kwa nthaŵi, kudzetsa chimwemwe chachikulu kopambana.
Malamulo a Makhalidwe Abwino Amene Amagwiradi Ntchito
23. (a) Ngati ukwati uli wopanda chimwemwe, kodi chisudzulo ndicho chothetsera vuto chokha chothekera? (b) Kodi ndiziti zimene ziri ziŵiri za mfungulo za ukwati wachimwemwe ndi wokhazikika?
23 Popeza kuti ukwati unalinganizidwira kukhala kwaumoyo wonse, tifunikira kudziŵa mmene tingauchititsire kupambana. Ena apereka lingaliro lakuti kuli bwino kwambiri kuchoka muukwati wopanda chimwemwe koposa kukhalamobe ndi kukhala wachisoni. Koma pali njira ina: kugwirira ntchito pa kuthetsa zovuta zimene zikuchititsa kupanda chimwemwe. Imeneyi ndiyo mbali ina imene Baibulo limathandiza. Tawona kale mmene limatilangizira kukhala wokhulupirika kwa mnzathu wa muukwati, ndipo imeneyi ndiyo mfungulo imodzi ya ukwati wachimwemwe ndi wokhazikika. Ina ndiyo kuzindikira kuti pangangokhala mutu umodzi wokha muukwati, ndipo Baibulo limanena kuti ayenera kukhala mwamuna. Mkazi akupatsidwa uphungu wa kukhala wochirikiza kwa mwamuna wake ndi kusalimbiralimbira malo ake antchito. Kumbali ina, mwamuna, akuuzidwa kugwiritsira ntchito udindo wake kaamba ka ubwino wa mkazi wake ndi kusakhala wadyera.—1 Akorinto 11:3; 1 Timoteo 2:11-14.
24, 25. Kodi ndimotani mmene Baibulo limalimbikitsira amuna ndi akazi kukwaniritsa ntchito zawo zoyenera muukwati?
24 Kwa mwamuna, Baibulo limanena kuti: “Amuna afunikira kuti azikonda akazi awo monga matupi awo a iwo eni. Iye amene akonda mkazi wake akudzikonda iye mwini, Pakuti mwamuna sanadane nalo ndi kale lonse thupi lake.” (Aefeso 5:28, 29, NW) Mwamuna wachikondi amagwiritsira ntchito ulamuliro wake m’njira yolingalira. Iye amakumbukira kuti ngakhale kuli kwakuti iye ali mutu, mkazi wake ayenera kulingaliridwa ndi kufunsidwa. Ukwati ngwochitira zinthu limodzi, osati kulamulira motsendereza.
25 Uphungu wa Baibulo kwa akazi umaphatikizapo mawu aŵa: “Mkazi ayenera kukhala ndi ulemu waukulu kaamba ka mwamuna wake.” (Aefeso 5:33) Iye amalemekeza mwamuna wake chifukwa cha malo ake antchito, ndipo ulemu wake udzasonyezedwa mwa kumchirikiza kwake, monga momwedi chikondi cha mwamuna wake chidzasonyezedwa mwa kudera naye nkhaŵa. Kwa anthu ambiri oganiza amakono, chilangizo chonga ngati chimenechi chiri chosalandirika kotheratu. Koma ochitira limodzi zinthu amene amazika maunansi awo pachikondi ndi kulemekeza—monga momwe Baibulo limalangizira—ngachimwemwe nthaŵi zonse.
26. Kodi miyezo ya Malemba kaamba ka ukwati imagwiradi ntchito? Fotokozani mwafanizo.
26 Chenicheini chakuti uphungu wa Baibulo m’mbali imeneyi umagwiradi ntchito chikuwonekera m’chokumana nacho chochokera ku Nyanja Zakummwera. Aŵiri okwatirana kumeneko, atakhala zaka khumi ali limodzi, anali okhutiritsidwa maganizo kuti ukwati wawo unali kulephera. Chotero anayamba kulinganiza kulekana. Ndiyeno mkaziyo analankhula ndi mmodzi wa Mboni za Yehova. Pamodzi, iye ndi Mboniyo anaphunzira chilangizo cha Baibulo kaamba ka okwatirana. Mwamunayo akusimba kuti: “Pamene mkazi wanga anali kuphunzira malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo, iye anapanga kuyesayesa kuwagwiritsira ntchito m’moyo wake. M’nthaŵi ya milungu yoŵerengeka, ndinayamba kuwona masinthidwe ena.” Atadabwa, iye anavomereza kuloŵamo m’phunziro la mkazi wake la Baibulo ndipo anaphunzira uphungu wa Baibulo kaamba ka amuna okwatira. Chotulukapo chake? Iye akuti: “Tsopano tapeza maziko a moyo weniweni wa banja wachimwemwe.”
27. Kodi ndikugwiritsidwa ntchito kwa malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo ati kumene kungathe kuthandiza Akristu amene akuvutika ndi umphaŵi wa zachuma?
27 Mbali ina kumene uphungu wa Baibulo watsimikizira kukhala wothandiza ndiyo kulimbana ndi umphaŵi. Mwachitsanzo, kusuta fodya ndi uchidakwa, zonse ziŵiri ziri zotsutsana ndi malamulo a Baibulo a makhalidwe abwino, zimawawanya chuma chakutichakuti. (Miyambo 23:19-21) Ndiponso, Baibulo limavomereza kugwira ntchito mwakhama, popeza kuti kaŵirikaŵiri munthu wogwira ntchito zolimba angathe kupeza njira yodyetsera banja lake kuposa waulesi kapena uyo amene amagonjera kukutaya mtima. (Miyambo 6:6-11; 10:26) Ndiponso, kulabadira misampha yotsutsana ndi kukhala ‘wosirira awo amene akuchita chisalungamo’ kumachititsa munthuyo kusatembenukira kuzinthu zoterozo zonga ngati upandu kapena kutchova juga monga njira yochepetsera umphaŵi. (Salmo 37:1, NW) Machitachita oterowo angawonekere kukhala opekera njira yothetsera mavuto yofulumira pamavuto azachuma, koma zotulukapo zake za nthaŵi yaitali ziri zowawa kwambiri.
28-30. (a) Kodi ndimotani mmene kugwiritsira ntchito malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo kunathandizira mkazi wina Wachikristu kulimbana ndi umphaŵi? (b) Kodi zokumana nazo za zikwizikwi za Akristu okhala m’mikhalidwe ya umphaŵi wazachuma zimatsimikiziranji?
28 Kodi uphungu umenewu umathandizadi awo amene ali osauka kwambiri, kapena kodi iri nthanthi ya m’maganizo chabe? Yankho ndilo lakuti, chilangizocho chimagwira ntchito, monga momwe zokumana nazo zambiri padziko lonse zasonyezera. Kutenga chitsanzo chimodzi chokha, mkazi wina Wachikristu mu Asia anadzipeza iye mwini ali mkazi wamasiye, wopanda ndalama iriyonse yobwera m’nyumba, ndi wokhala ndi mwana wamwamuna wachichepere wooti asamaliridwe. Kodi Baibulo linamthandiza motani iye ndi mwana wake wamwamunayo?
29 Iye anali wogwira ntchito wachangu, monga momwe Baibulo limalangizira, ndipo anayamba kusoka zovala ndi kumazigulitsa. Chifukwa chakuti iye anali wowona mtima ndi wodalirika, monga momwenso Baibulo limalangizira, iye posapita nthaŵi anakhala ndi omgula anthaŵi zonse. (Akolose 3:23) Pamenepo, iye anasandutsa chipinda chaching’ono m’nyumba yake kukhala malo aang’ono odyerako chakudya ndipo anadzuka pafupifupi 4 koloko mbandakucha tsiku lirilonse kukonza chakudya chogulitsa, ndipo zimenezi zinawonjezera ndalama zawo zopezedwa. “Ngakhale kuli choncho,” iye akutero, “tifunikira kukhala ndi moyo wosadya ndalama zambiri.” Koma iye akukumbukira chilangizo cha Baibulo chakuti: “Pokhala nacho chakudya ndi chofunda, tidzakhutira ndi zinthu zimenezi.”—1 Timoteo 6:8, NW.
30 Iye akuwonjeza kuti: “Ngakhale kuli kwakuti ndikukhala ndi moyo pafupi ndi umphaŵi, sindiri woipidwa kapena wokwiya. Chowonadi cha Baibulo chimandidzadza ndi lingaliro lotsimikizirika.” Ndiponso, iye wapeza kuti lonjezo lapadera limene Yesu anapereka lagwiradi ntchito kwa iye. Iye anati: “Pamenepo, pitirizanibe, kufunafuna choyamba ufumu ndi chilungamo chake, ndipo zinthu zina zonsezi [zosoŵa zakuthupi] zidzawonjezeredwa kwa inu.” (Mateyu 6:33, NW) Chokumana nacho chake chakhala chakuti mwa kuika utumiki wake kwa Mulungu poyamba mmoyo wake, iye nthaŵi zonse amalandira, mwanjira ina, zosoŵa zakuthupi. Zokumana nazo za dona Wachikristu ameneyu, pamodzi ndi za Akristu ena zikwizikwi osoŵa mwachuma padziko lonse, zimawonjezera kuumboni wakuti uphungu wa Baibulo umagwiradi ntchito.
31. Kodi nchiyani chimene chimachitika pamene titsatira uphungu wa Baibulo, ndipo kodi chenicheni chimenechi chimachitira umboni chiyani?
31 M’mutu uno, tangokhudzapo chabe pachuma chochuluka cha uphungu ndi chilangizo zimene Baibulo liri nazo, ndipo tawona zochitika zoŵerengeka chabe kumene uphungu umenewu wagwira ntchito. Zokumana nazo zotchulidwazo zingathe kuwirikizidwa nthaŵi zikwi zambiri. Kaŵirikaŵiri, pamene anthu atsatira Baibulo, amapindula. Pamene iwo alinyalanyaza, iwo amavutika. Palibe chiungwe chirichonse chauphungu, makedzana kapena wamakono, umene uli wopindulitsa mosasinthasintha ndi umene umagwira ntchito kwa anthu a mafuko onse. Uphungu wanzeru wonga umenewu sungakhale nzeru yachikale chabe. Chenicheni chakuti Baibulo liri nzeru imeneyo chiri umboni wamphamvu wakuti liri Mawu a Mulungu.
[Mawu Otsindika patsamba 168]
Kaimidwe kamaganizo ka kuthandiza kamapindulitsa aliyense
[Chithunzi patsamba 163]
Kuyenda ndi anthu anzeru kumatipangitsa kukhala anzeru, koma kuyanjana ndi anthu opusa kudzatiyambukira moipa
[Chithunzi patsamba 165]
Kusuta fodya kuyenera kupeŵedwa chifukwa chakuti nkosemphana ndi malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo
[Chithunzi patsamba 171]
Awo amene amatsatira uphungu wa Baibulo muukwati ali ndi maziko amphamvu kaamba ka chimwenwe
[Chithunzi patsamba 173]
Kugwiritsira ntchito uphungu wa Baibulo kumathandiza anthu kulimbana ndi zovuta zazikulu zaumphaŵi