Lemekezani Anthu Opatsidwa Ulamuliro pa Inu
“Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, chitirani mfumu ulemu.”—1 PETRO 2:17.
1, 2. Kodi masiku ano anthu amawaona motani aulamuliro? Chifukwa chiyani?
“ANA ali ndi ufulu wonse. Saopanso makolo.” Anadandaula motero mayi wina. “Tsutsani Aulamuliro” limatero pepala lina lomata pagalimoto. Zimenezo ndi zinthu ziŵiri zokha zosonyeza mkhalidwe umene uli paliponse lerolino, monga mudziŵa. Kusalemekeza makolo, aphunzitsi, mabwana apantchito, ndi akuluakulu a boma n’kofala padziko lonse lapansi.
2 Ena sanganene zambiri koma angangoti, ‘Kupereka ulemu wanga kwa anthu aulamuliroŵa n’kuwononga.’ Nthaŵi zinadi, zimenezo zingachitike. Nthaŵi zonse timamva nkhani zonena za akuluakulu a boma achinyengo, mabwana apantchito adyera, aphunzitsi osachita bwino ntchito yawo, ndi makolo ankhanza. Ubwino wake, ndi Akristu ochepa okha amene amaona anthu aulamuliro mumpingo mofananamo.—Mateyu 24:45-47.
3, 4. N’chifukwa chiyani Akristu ayenera kuchitira ulemu anthu aulamuliro?
3 Pokhala Akristu, ‘tiyenera kukhala’ aulemu kwa maulamuliro a boma. Mtumwi Paulo analangiza Akristu kuti “amvere maulamuliro aakulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.” (Aroma 13:1, 2, 5; 1 Petro 2:13-15) Paulo anaperekanso chifukwa chabwino chomvera maulamuliro a m’banja pamene anati: “Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye. Ana inu, mverani akubala inu m’zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.” (Akolose 3:18, 20) Akulu a mumpingo tiyenera kuwachitira ulemu chifukwa chakuti ‘mzimu woyera unawaika oyang’anira, kuti aŵete mpingo wa Mulungu.’ (Machitidwe 20:28) Timachitira ulemu anthu aulamuliro pofuna kulemekeza Yehova. Ndithudi, nthaŵi zonse timatsogoza kulemekeza ulamuliro wa Yehova m’moyo wathu.—Machitidwe 5:29.
4 Pamene tikuganizira za ulamuliro wa Yehova wapamwamba koposa, tiyeni tisanthule zitsanzo za anthu ena amene sanalemekeze aulamuliro ndi ena amene anawalemekeza.
Opanda Ulemu Atsutsidwa
5. Kodi Mikala anasonyeza kupanda ulemu kotani kwa Davide, ndipo kodi chotsatira chake chinali chiyani?
5 Mbiri ya Mfumu Davide ingatisonyeze mmene Yehova amaonera anthu amene amanyoza ulamuliro wopatsidwa ndi Mulungu. Pamene Davide anabweretsa likasa la chipangano ku Yerusalemu, mkazi wake Mikala “[a]naona mfumu Davide alikuvina ndi kuseŵera pamaso pa Yehova, nam’peputsa mumtima mwake.” Mikala anayenera kuona Davide osati monga mutu wa banja basi komanso monga mfumu ya dzikolo. Komabe, iye anafotokoza malingaliro ake molalata, amvekere: “Ha! Lero mfumu ya Israyeli inalemekezeka ndithu, amene anavula lero pamaso pa adzakazi a anyamata ake, monga munthu woluluka avula wopanda manyazi!” Chotsatira chake chinali chakuti Mikala sanaone mwana ndi mmodzi yemwe.—2 Samueli 6:14-23.
6. Kodi Yehova anachiona motani chipongwe cha Kora kwa odzozedwa Ake?
6 Chitsanzo choipitsitsa cha kusalemekeza utsogoleri wateokalase woikidwa ndi Mulungu ndi cha Kora. Monga mbadwa ya Kohati, iye analitu ndi mwayi waukulu zedi wotumikira Yehova pachihema chokumanako! Koma anaonabe Mose ndi Aroni, atsogoleri odzozedwa ndi Mulungu a Aisrayeli, kukhala olakwitsa zinthu kwambiri. Kora, atagwirizana ndi akalonga ena a m’Israyeli, anauza Mose ndi Aroni mopanda mantha kuti: “Khamu lonse n’lopatulika, onseŵa, ndipo Yehova ali pakati pawo; mudzikuza bwanji pa msonkhano wa Yehova?” Kodi Yehova anauona bwanji mzimu wa Kora ndi wa anzake om’khalira kumbuyo? Mulungu anaona khalidwe lawolo monga kusalemekeza Yehova iye mwini. Ataona onse a kumbali yawo akumezedwa ndi nthaka, Kora ndi akalonga 250 aja anawonongedwa ndi moto wa Yehova.—Numeri 16:1-3, 28-35.
7. Kodi “atumwi oposatu” analidi ndi chifukwa chotsutsira ulamuliro wa Paulo?
7 Mumpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba, munali ena amene ankanyalanyaza ulamuliro wateokalase. “Atumwi oposatu” mumpingo wa ku Korinto sanali kum’lemekeza Paulo. Anam’suliza kuti sadziŵa kuyankhula, nati: “Maonekedwe a thupi lake n’ngofooka, ndi mawu ake n’ngachabe.” (2 Akorinto 10:10; 11:5) Kaya Paulo ankayankhula mwaluso kapena ayi, anayenerabe kulandira ulemu monga mtumwi. Koma kodi kuyankhula kwa Paulo kunalidi kwachabe? Nkhani zake zapoyera zolembedwa m’Baibulo zimapereka umboni wakuti anali munthu wodziŵa kutsitsa mfundo. Eetu, Paulo atacheza mwachidule ndi Herode Agripa II, yemwe anali ‘wodziŵa bwino . . . mafunso onse a mwa Ayuda,’ anapangitsa mfumuyo kufika ponena kuti: “Ndi kundikopa pang’ono ufuna kundiyesera Mkristu”! (Machitidwe 13:15-43; 17:22-34; 26:1-28) Komabe, atumwi oposatu ku Korinto amati mawu ake n’ngachabe! Kodi Yehova anauona motani mzimu wawo? Mu uthenga wa oyang’anira a mumpingo wa Aefeso, Yesu Kristu anayankhula mothokoza awo amene anakana kukopeka ndi anthu ‘amene anadzitcha okha atumwi, koma sanali atumwi.’—Chivumbulutso 2:2.
Kuwalemekeza Ngakhale Kuti Ndi Opanda Ungwiro
8. Kodi Davide anasonyeza motani kuti analemekeza ulamuliro umene Yehova anapatsa Sauli?
8 M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene analemekeza anthu aulamuliro, ngakhale pamene aulamulirowo anagwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwa. Chitsanzo chimodzi chabwino chotere ndi cha Davide. Mfumu Sauli, yemwe ankalamulira panthaŵiyo, anachita nsanje ndi zimene Davide anachita nafuna kumupha. (1 Samueli 18:8-12; 19:9-11; 23:26) Komabe, ngakhale kuti Davide anali ndi mpata woti n’kumupha Sauli, Davideyo anati: “Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.” (1 Samueli 24:3-6; 26:7-13) Davide ankadziŵa kuti Sauli ndiye wolakwa, koma anazisiya m’manja mwa Yehova kuti am’weruze. (1 Samueli 24:12, 15; 26:22-24) Ponena za Sauli kapena poyankhula naye, Davide sanayankhule monyoza.
9. (a) Kodi Davide anamva bwanji posautsidwa ndi Sauli? (b) Kodi tingadziŵe bwanji kuti ulemu wa Davide kwa Sauli unali weniweni?
9 Kodi Davide anavutika maganizo pamene anali kuzunzidwa motero? “Oopsa afunafuna moyo wanga,” analira motero Davide kwa Yehova. (Salmo 54:3) Iye anatsanulira mtima wake kwa Yehova nati: “Ndilanditseni kwa adani anga, Mulungu wanga. . . . Amphamvu andipangira chiwembu: Wosachimwa, wosalakwa ine, Yehova, wosawapatsa chifukwa ine, athamanga nadzikonza; galamukani kukomana nane, ndipo penyani.” (Salmo 59:1-4) Kodi inunso munamvapo chimodzimodzi—kuti palibe chimene munalakwa kwa munthu waulamuliro, koma anapitirizabe kukusautsani? Davide sanalephere kusonyeza ulemu kwa Sauli. Sauli atamwalira, m’malo mosangalala, Davide analemba nyimbo yachisoni yakuti: “Sauli ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m’miyoyo yawo. . . . Anali nalo liŵiro loposa chiwombankhanga, anali amphamvu koposa mikango. Ana aakazi inu a Israyeli, mulirire Sauli.” (2 Samueli 1:23, 24) Chitsanzo chogwira mtima zedi cha ulemu weniweni kwa wodzozedwa wa Yehova, ngakhale kuti Sauli analakwira Davide!
10. Kodi Paulo anapereka chitsanzo chotani chabwino cha kulemekeza ulamuliro woperekedwa ndi Mulungu wa bungwe lolamulira, ndipo zimenezi zinapangitsa chiyani?
10 M’nthaŵi yachikristu, tikupezamonso zitsanzo zabwino kwambiri za anthu amene analemekeza ulamuliro woperekedwa ndi Mulungu. Mwachitsanzo, tiyeni titenge Paulo. Iye analemekeza zosankha za bungwe lolamulira la mpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba. Paulendo wa Paulo womaliza wa ku Yerusalemu, bungwe lolamulira linam’langiza kuti adziyeretse mwamwambo kuti asonyeze ena kuti sakudana ndi Chilamulo cha Mose. Akanafuna, Paulo akanaganiza kuti: ‘Ndi abale omwewanso amene poyambapo anandiuza kuti nditulukemo m’Yerusalemu pamene moyo wanga unali pangozi. Tsopano akufuna kuti ndisonyeze poyera kuti ndimalemekeza Chilamulo cha Mose. Agalatiya ndinawalembera kale kalata yowauza kuti asamatsatirenso Chilamulo chimenecho. N’kapita kukachisi, mwina ena adzakhala ndi chithunzi cholakwika, n’kundiona ngati kuti ndayamba kugwirizana ndi gulu la odulidwa.’ Koma palibe umboni wosonyeza kuti Paulo analingalira motero. Popeza kuti panalibe mfundo yachikhalidwe chachikristu imene inaswedwa, iye analemekeza ndipo anatsatira uphungu wa bungwe lolamulira la m’zaka za zana loyamba. Zitangotero Paulo anachita kulanditsidwa ku gulu la Ayuda lomwe linam’galukira, ndipo kenako anakhala zaka ziŵiri m’ndende. Pomalizira pake, chifuniro cha Mulungu chinachitika. Paulo anachitira umboni pamaso pa akuluakulu a boma a ku Kaisareya ndipo boma linalipira ulendo wake wa ku Roma kukachitira umboni pamaso pa Kaisara weniweniyo.—Machitidwe 9:26-30; 21:20-26; 23:11; 24:27; Agalatiya 2:12; 4:9, 10.
Kodi Mumasonyeza Ulemu?
11. Kodi maulamuliro a boma tingawalemekeze motani?
11 Kodi anthu okhala ndi ulamuliro mumawasonyeza ulemu woyenerera? Akristu akulamulidwa kuti ‘apereke kwa anthu onse mangawa awo; . . . ulemu kwa eni ake a ulemu.’ Inde, kugonjera kwathu “maulamuliro aakulu” sikukhoma misonkho yokha basi komanso kulemekeza aulamuliro mwa khalidwe lathu ndi zoyankhula zathu. (Aroma 13:1-7) Tikakhala kuti tikulamulidwa ndi akuluakulu a boma ovuta, kodi timatani? M’Chigawo cha Chiapas, ku Mexico, akuluakulu a boma m’dera linalake analanda minda ya mabanja 57 a Mboni za Yehova chifukwa chakuti Akristu ameneŵa sankachita nawo zikondwerero zina zachipembedzo. Pamisonkhano yomwe inachitidwa kuti akambirane nkhaniyo, Mbonizo, zitavala mwaukhondo, zinayankhula mwaulemu. Patapita nthaŵi yoposa chaka chimodzi, nkhaniyo inagamulidwa mowakomera. Ulemu wawo unachititsa chidwi ena mwa omwe ankangomvetsera nawo nkhaniyo moti anthuwo anafunanso kukhala Mboni za Yehova!
12. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kuti mkazi akhale ndi ‘ulemu wakuya’ kwa mwamuna wake wosakhulupirira?
12 Kodi mungasonyeze motani ulemu kwa ulamuliro woperekedwa ndi Mulungu m’banja? Atalongosola za chitsanzo cha Yesu cha kuzunzika ndi zoipa, mtumwi Petro anati: “Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mawu, akakodwe opanda mawu mwa mayendedwe a akazi; pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu [“ulemu wanu wakuya,” NW].” (1 Petro 3:1, 2; Aefeso 5:22-24) Panopa Petro anagogomeza kufunika kwa mkazi kugonjera kwa mwamuna wake ndi ‘ulemu wakuya,’ ngakhale kuti amuna ena angakhale osayenerera ulemu chifukwa cha zochita zawo. Ulemu wa mkazi ungakope mtima wa mwamuna wake wosakhulupirira.
13. Kodi akazi angachitire motani ulemu amuna awo?
13 M’nkhani ya m’malemba ameneŵa, Petro akutisonyeza chitsanzo cha Sara, amene mwamuna wake, Abrahamu, anali chitsanzo chabwino kwambiri cha chikhulupiriro. (Aroma 4:16, 17; Agalatiya 3:6-9; 1 Petro 3:6) Kodi akazi okhala ndi amuna okhulupirira ayenera kuwapatsa ulemu wocheperapo kusiyana ndi umene akazi okhala ndi amuna osakhulupirira akupatsa amuna awo? Bwanji ngati simukugwirizana ndi mwamuna wanu pamfundo inayake? Yesu anapereka uphungu wina umene ungagwiritsidwe ntchito pamikhalidwe yosiyanasiyana yokhudza nkhaniyi, pamene anati: “Amene akakukakamiza [“ngati munthu waulamuliro akukakamiza,” NW] kum’perekeza njira imodzi, upite naye ziŵiri.” (Mateyu 5:41) Kodi mumam’chitira ulemu mwamuna wanu mwa kutsatira zofuna zake? Ngati mukuona kuti zimenezi n’zovuta kwambiri, m’fotokozereni malingaliro anu okhudza nkhaniyo. Musayese kuti akudziŵa mmene mukumvera. Koma pom’fotokozera malingaliro anu, fotokozani mwaulemu. Baibulo limatilangiza kuti: “Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa, kuti mukadziŵe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.”—Akolose 4:6.
14. Kodi kulemekeza makolo kumaphatikizapo chiyani?
14 Nanga ananu? Mawu a Mulungu amalamula kuti: “Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi n’chabwino. Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano).” (Aefeso 6:1-3) Mutha kuona kuti kumvera makolo anu kukuyerekezeredwa ndi ‘kulemekeza atate wanu ndi amanu.’ Liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti ‘kulemekeza’ limatanthauzanso “kuona chinthu chinachake kukhala chofunika kwambiri” kapena “kudziŵa kufunika kwa” chinthu chinachake. Chotero, kukhala womvera si kutsatira monyinyirika malamulo amene mumawaona ngati oumitsa zinthu. Mulungu akukupemphani kuona makolo anu kukhala a mtengo wapatali ndi kuona chitsogozo chawo kukhala chofunika kwambiri.—Miyambo 15:5.
15. Kodi ana angasunge motani ulemu wawo ngakhale ngati akuona kuti makolo awo akulakwitsa?
15 Ngati makolo anu amachita zinthu zimene zimakupangitsani kuti musawachitire ulemu, bwanji pamenepo? Yesani kuona zinthu malinga ndi mmene iwo akuzionera. Kodi sindiwo ‘anakubalani’ ndi kukusamalani? (Miyambo 23:22) Kodi si chikondi chimene amafuna kukusonyezani? (Ahebri 12:7-11) Yankhulani mwaulemu kwa makolo anu, kulongosola modzichepetsa mmene mukumvera. Ngakhale ngati atayankha m’njira yosakusangalatsani, peŵani kuyankhula nawo mwamwano. (Miyambo 24:29) Kumbukirani mmene Davide anasungira ulemu wake kwa Sauli ngakhale pamene mfumuyo inasiya kutsatira uphungu wa Mulungu. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuugwira mtima. “Tsanulirani mitima yanu pamaso pake,” anatero Davide. “Mulungu ndiye pothaŵirapo ife.”—Salmo 62:8; Maliro 3:25-27.
Lemekezani Atsogoleri
16. Kodi tingaphunzireponji pa zitsanzo za aphunzitsi onyenga ndi angelo?
16 Akulu a mumpingo amaikidwa ndi mzimu woyera, koma ndi opandabe ungwiro ndipo amalakwabe. (Salmo 130:3; Mlaliki 7:20; Machitidwe 20:28; Yakobo 3:2) Chotero, ena mumpingo sangasangalale nawo akulu. Kodi tiyenera kutani ngati tikuganiza kuti zinazake mumpingo sizikuyendetsedwa bwino, kapena ngati zikuoneka choncho? Taonani kusiyana kwa aphunzitsi onyenga a m’zaka za zana loyamba ndi angelo: “Osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, [aphunzitsi onyengawo] santhunthumira kuchitira mwano akulu; popeza angelo, angakhale awaposa polimbitsa mphamvu, sawaneneza kwa Ambuye mlandu wakuchita mwano [“sawanenera zamwano, sachita zimenezo pofuna kulemekeza Yehova,” NW].” (2 Petro 2:10-13) Pamene kuli kwakuti aphunzitsi onyengawo ankachitira mwano “akulu” amene anapatsidwa udindo mumpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba, angelo sanayankhule zamwano ponena za aphunzitsi onyengawo amene anali kugaŵanitsa abale. Angelo, pokhala amphamvupo ndiponso pokhala ozindikira bwino chilungamo kusiyana ndi anthu, ankadziŵa zimene zinali kuchitika mumpingo. Komabe, “pofuna kulemekeza Yehova,” chiweruzo anachisiya m’manja mwa Mulungu.—Ahebri 2:6, 7; Yuda 9.
17. Kodi chikhulupiriro chanu chimakhudzidwa motani mukayang’anizana ndi mavuto amene mukuganiza kuti akulu ndi olakwa?
17 Ngakhale kuti nkhani inayake siikuyendetsedwa bwino, kodi sitiyenera kukhala ndi chikhulupiriro mwa Yesu Kristu monga Mutu wamoyo wa mpingo wachikristu? Kodi iye sakudziŵa zimene zikuchitika mumpingo wake wapadziko lonse lapansi? Kodi sitiyenera kulemekeza njira yake yosamalira nkhaniyo pokumbukiranso kuti ali ndi mphamvu yowongolera zinthu? Kodi ‘ifenso ndife yani kuti tiweruze anzathu?’ (Yakobo 4:12; 1 Akorinto 11:3; Akolose 1:18) Bwanji osam’tulira nkhaŵa zanu Yehova m’mapemphero?
18, 19. Kodi mungachitenji mukaona kuti mkulu walakwa?
18 Chifukwa cha kupanda ungwiro kwa anthu, pangabuke mavuto ena ndi ena. Zingachitikenso kuti mwina mkulu n’kulakwa ndi kukhumudwitsa ena. Tikachitapo kanthu mopupuluma pazinthu zoterozo palibe chimene chidzasintha. Mwinanso m’pamene vutolo lingakule. Awo amene ali ndi kuzindikira kwauzimu adzadikira kuti Yehova awongolere zinthu ndi kupereka chilango chilichonse chimene chingafunikire panthaŵi yodziŵa iye mwini komanso m’njira yake.—2 Timoteo 3:16; Ahebri 12:7-11.
19 Bwanji ngati nkhani inayake ikukusoŵetsani mtendere? M’malo momauza ena mumpingo, bwanji osafikira akulu mwaulemu kuti akuthandizeni? Popanda kunena zoipa zilizonse, longosolani mmene zakukhudzirani. Nthaŵi zonse khalani ndi “chifundo” kwa akuluwo, ndiponso musataye ulemu wanu pamene mukuwafotokozera malingaliro anu. (1 Petro 3:8) Musayambe kuyankhula monyoza, koma khalani ndi chikhulupiriro chakuti iwo ndi achikulire m’Chikristu. Landirani chilimbikitso cha m’Malemba chilichonse chimene angakupatseni mokoma mtima. Ndipo ngati zikuoneka kuti m’pofunikabe kuwongolera, dalirani Yehova kuti adzatsogolera akuluwo kuchita zabwino ndi zoyenera.—Agalatiya 6:10; 2 Atesalonika 3:13.
20. Kodi m’nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?
20 Komano, padakali mbali inanso yofunika kuilingalira pankhani ya kulemekeza aulamuliro. Kodi anthu opatsidwa ulamulirowo sayenera kulemekeza anthu awo? Tiyeni tipende zimenezo m’nkhani yotsatira.
Kodi Mungayankhe Motani?
• Kodi tili ndi chifukwa chabwino chotani cholemekezera aulamuliro?
• Kodi Yehova ndi Yesu amaona motani anthu amene salemekeza ulamuliro woperekedwa ndi Mulungu?
• Kodi tili ndi zitsanzo zabwino zotani za awo amene analemekeza anthu opatsidwa ulamuliro?
• Kodi tingachite motani ngati tikuona kuti munthu waulamuliro pa ife walakwitsa penapake?
[Chithunzi patsamba 12]
Sara analemekeza kwambiri ulamuliro wa Abrahamu ndipo anali wachimwemwe
[Chithunzi patsamba 13]
Mikala analephera kulemekeza ulamuliro wa Davide monga mutu wa banja komanso mfumu
[Chithunzi patsamba 15]
“Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova”
[Chithunzi patsamba 16]
Bwanji osam’tulira nkhaŵa zanu Yehova m’mapemphero?