Yehova Ndi “Wobwezera Mphoto Iwo Akum’funa Iye”
“Iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.”—AHEBRI 11:6.
1, 2. Kodi n’chifukwa chiyani atumiki ena a Yehova amadziona ngati osafunika?
MLONGO wina dzina lake Barbara anati: “Ndakhala Mboni ya Yehova kwa zaka pafupifupi 30, koma sindinadzimvepo kuti ndine woyenerera kutchulidwa kuti Mboni ya Yehova.a Inde, ndachitapo upainiya ndipo ndatumikiraponso m’njira zina zapadera zosiyanasiyana, koma palibe chilichonse mwa zimenezi chomwe chimandikhutiritsa mumtima mwanga kuti ndine woyenerera kutchulidwa kuti Mboni ya Yehova.” Mbale wina dzina lake Keith anatchulaponso maganizo angati amenewa. Iye anati: “Nthawi zina ndakhala ndikudziona ngati wopanda ntchito, chifukwa choti atumiki a Yehova amayenera kukhala osangalala pa zifukwa zambiri, koma ineyo sindinali wosangalala. Motero ndinayamba kudziimba mlandu n’kungowonjezera vuto langalo.”
2 Atumiki ambiri a Yehova akale ndi amakono, anakhalapo ndi maganizo oterewa. Kodi nthawi zina inunso mumakhala ndi maganizo otere? N’kutheka kuti inuyo mavuto sakuchokani, koma anzanu amaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino, alibe mavuto ndipo n’ngosangalala. Motero, mungayambe kuganiza kuti Yehova sakusangalala nanu ndiponso simuwerengedwa pamaso pake. Koma musafulumire kuganiza choncho. Baibulo limatitsimikizira kuti: “[Yehova] sanapeputsa ndipo sananyansidwa ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanam’bisira nkhope yake; koma pom’fuulira Iye, anamva.” (Salmo 22:24) Mawu aulosiwa, omwe akunena za Mesiya, amasonyeza kuti Yehova amamva mapemphero a anthu ake okhulupirika ndiponso kuti amawayankha.
3. N’chifukwa chiyani nafenso timakhudzidwa nawo mavuto a m’dzikoli?
3 Palibe munthu amene savutika ndi zosautsa za m’dziko lino. Ngakhale anthu a Yehova amavutika nazo. Tikukhala m’dziko lolamulidwa ndi mdani wamkulu wa Yehova, yemwe ndi Satana Mdyerekezi. (2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19) Atumiki a Yehova satetezedwa mozizwitsa. M’malo mwake iwo ndiwo anthu amene Satana amawasakasaka kwambiri. (Yobu 1:7-12; Chivumbulutso 2:10) Motero, pakali pano tiyenera ‘kupirira m’masautso’ ndi ‘kulimbikira kupemphera’ mpaka nthawi imene Mulungu anaika idzakwane, ndipo tisamakayikire kuti Yehova amatisamalira. (Aroma 12:12) Tisalole mavuto a m’dzikoli kutipatsa maganizo olakwika akuti Mulungu wathu Yehova, satikonda.
Anthu Akale Amene Ali Zitsanzo za Kupirira
4. Perekani zitsanzo za atumiki okhulupirika a Yehova amene anapirira zosautsa zosiyanasiyana.
4 Atumiki a Yehova ambiri akale anapirira masautso. Mwachitsanzo, Hana “anali ndi mtima wowawa” chifukwa analibe mwana, motero ankaona kuti Mulungu wamuiwala. (1 Samueli 1:9-11) Mmene mfumukazi yopha anthu Yezebeli inkasakasaka Eliya, iye anachita mantha n’kupemphera kwa Yehova kuti: “Kwafikira, chotsani tsopano moyo wanga, Yehova; popeza sindili wokoma woposa makolo anga.” (1 Mafumu 19:4) Ndipo mtumwi Paulo ayenera kuti anasautsidwa kwambiri chifukwa cha kupanda ungwiro kwake. N’chifukwa chake ananena kuti: “Pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko.” Iye ananenanso kuti: “Munthu wosauka ine.”—Aroma 7:21-24.
5. (a) Kodi Hana, Eliya, ndi Paulo anapatsidwa mphoto m’njira yotani? (b) Kodi tingapeze chilimbikitso chotani m’Mawu a Mulungu tikamadziona ngati opanda ntchito?
5 Inde, tikudziwa kuti Hana, Eliya, ndi Paulo onse anapirira potumikira Yehova, ndipo Iye anawapatsa mphoto zosaneneka. (1 Samueli 1:20; 2:21; 1 Mafumu 19:5-18; 2 Timoteo 4:8) Komabe, iwowa anavutika ndi maganizo osiyanasiyana, kuphatikizapo chisoni, kuthedwa nzeru, ndiponso mantha. Choncho siziyenera kutidabwitsa nthawi zina tikamavutika maganizo. Komabe, kodi mungachitepo chiyani ngati mavuto akukuchititsani kukayikira ngati Yehova amakukondanidi? Mungathe kulimbikitsidwa ndi Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, mu nkhani ya m’mbuyoyi, tinakambirana mawu a Yesu akuti Yehova amawerenga ‘tsitsi lonse la m’mutu mwanu.’ (Mateyu 10:30) Mawu olimbikitsawa amasonyeza kuti Yehova amaganizira kwambiri mtumiki wake aliyense. Taganiziraninso chitsanzo cha Yesu cha mpheta chija. Kodi ngati Yehova salephera kuona ngakhale mpheta imodzi yokha yogwa pansi, anganyalanyaze bwanji mavuto anu?
6. Kodi Baibulo lingalimbikitse bwanji anthu amene amadziona ngati osafunika?
6 Kodi n’zothekadi kuti anthu opanda ungwiro akhale amtengo wapatali pamaso pa Mlengi wamphamvuyonse, Yehova Mulungu? Inde n’zothekadi. Ndipotu pali ndime zambirimbiri m’Baibulo zimene zimatitsimikizira mfundo imeneyi. Tikamaganizira mozama za ndime zimenezi, nafenso tinganene mawu a wamasalmo akuti: “Pondichulukira zolingalira zanga m’kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.” (Salmo 94:19) Tiyeni tiganizire mfundo zina zotonthoza zopezeka m’Mawu a Mulungu, zimene zitithandize kumvetsa bwino mfundo yakuti Mulungu amationa kuti ndife anthu ofunika ndiponso kuti amatipatsa mphoto tikamapitiriza kuchita zofuna zake.
Anthu ‘Akeake’ a Yehova
7. Kodi ndi ulosi wolimbikitsa wotani umene Yehova ananena kwa mtundu wolowerera wa Israyeli kudzera mwa Malaki?
7 M’zaka za m’ma 400 B.C.E. zinthu zinaipa kwambiri pakati pa Ayuda. Ansembe ankavomereza kuti pa guwa la Yehova aziperekapo nsembe za ziweto zosayenerera kuperekedwa nsembe. Oweruza ankakondera. Zinthu monga maula, mabodza, chinyengo, ndiponso chigololo zinafala ponseponse. (Malaki 1:8; 2:9; 3:5) Malaki anauza mtundu wolowerera kwambiriwu ulosi wodabwitsa kwambiri. Ulosi wake unali wakuti m’tsogolo Yehova adzathandiza anthuwa kuti Iyeyo ayambenso kuwayanja. Lembalo limati: “Ndipo adzakhala anga anga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wake wom’tumikira.”—Malaki 3:17.
8. Kodi n’chifukwa chiyani mfundo ya pa lemba la Malaki 3:17 ingagwirenso ntchito kwa a khamu lalikulu?
8 Ulosi wa Malaki wakwaniritsidwanso masiku ano kwa Akristu odzozedwa, amene ali mumtundu wauzimu wokhala ndi anthu 144,000. Anthu a mumtundu umenewu ndi ‘akeakedi’ a Yehova kapena kuti “anthu a mwini wake.” (1 Petro 2:9) Ulosi wa Malaki ungalimbikitsenso anthu a “khamu lalikulu,” amene “akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera.” (Chivumbulutso 7:4, 9) Anthu amenewa amakhala khola limodzi ndi odzozedwa, n’kumayang’aniridwa ndi Mbusa m’modzi, Yesu Kristu.—Yohane 10:16.
9. N’chifukwa chiyani anthu a Yehova ali ‘akeake’ kapena kuti amtengo wapatali kwa iyeyo?
9 Kodi Yehova amawaona bwanji anthu amene amasankha kuti azim’tumikira? Malinga ndi mawu a pa Malaki 3:17, iye amawaona mmene bambo wokonda mwana wake amaonera mwanayo. Taonani kuti pa lembali Yehova akunena kuti anthuwo ndi “anga anga.” Mabaibulo ena amamasulira mawuwa kuti “anthu amtengo wapatali kwambiri kwa ine,” ndiponso kuti “chuma changa.” Kodi n’chifukwa chiyani Yehova amaona kuti anthu amene amam’tumikira n’ngamtengo wapatali kwambiri? Chifukwa choyamba n’chakuti Yehova ndi Mulungu wodziwa kuyamikira. (Ahebri 6:10) Iye amayandikira anthu amene amam’tumikira mwa mtima wonse ndipo amawaona kuti n’ngamtengo wapatali.
10. Kodi Yehova amateteza bwanji anthu ake?
10 Taganizirani chinthu chamtengo wapatali kwambiri chimene muli nacho chimene mumachitenga kuti n’chanuchanu. Kodi chinthu chimenecho simuyesetsa kuchiteteza? Yehova amateronso ndi anthu ‘akeake.’ N’zoona kuti iye sateteza anthu ake kuti asakumane ndi mayesero ndiponso mavuto onse a m’moyo uno. (Mlaliki 9:11) Koma Yehova angathe kuteteza mwauzimu atumiki ake okhulupirika ndipo amaterodi. Iye amawapatsa mphamvu zimene iwo amafunikira kuti athe kupirira chiyeso china chilichonse. (1 Akorinto 10:13) N’chifukwa chake Mose anauza anthu akale a Mulungu, Aisrayeli, kuti: “Khalani amphamvu, limbikani mitima . . . Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; Iye sadzakusowani, kapena kukusiyani.” (Deuteronomo 31:6) Yehova amapereka mphoto kwa anthu ake. Iye amawaona kuti ndi ‘akeake,’ kapena kuti ndi amtengo wapatali.
Yehova Ndi “Wopereka Mphoto”
11, 12. Kodi kuzindikira kuti Yehova ndiye Wopereka Mphoto kungatithandize bwanji kulimbana ndi maganizo odzikayikira?
11 Umboni wina wakuti Yehova amaona kuti atumiki ake ndi anthu amtengo wapatali ndi wakuti iye amawapatsa mphoto. Iye anauza Aisrayeli kuti: “Mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.” (Malaki 3:10) Inde dalitso lalikulu kwambiri limene Yehova adzapatse atumiki ake ndilo moyo wosatha. (Yohane 5:24; Chivumbulutso 21:4) Mphoto yosaneneka imeneyi imasonyeza kuti chikondi ndiponso kuwolowa manja kwa Yehova n’kwakukulu zedi. Imasonyezanso kuti ndithu, iye amaonadi kuti onse amene amasankha kumutumikira n’ngamtengo wapatali. Tikafika pozindikiradi kuti Yehova ndi Wopereka Mphoto mowolowa manja sitingamavutike kwambiri ndi maganizo odziona ngati kuti Mulungu satiyanja. Ndipotu Yehova amatilimbikitsa kuti tizimuona kuti ndi Wopereka Mphoto. Paulo analemba kuti: “Iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.”—Ahebri 11:6.
12 Inde, n’zoona kuti timatumikira Yehova chifukwa chomukonda, osati chifukwa chongoti anatilonjeza mphoto. Komabe, kuyembekezera mphoto, sikulakwa kapenanso kuchita dyera. (Akolose 3:23, 24) Yehova amapatsa mphoto anthu onse amene amam’funa mwa mtima wonse chifukwa chakuti Iyeyo amawakonda ndipo amawaona kuti n’ngamtengo wapatali kwambiri.
13. Kodi n’chifukwa chiyani kupereka dipo kuli chizindikiro chachikulu kwambiri chakuti Yehova amatikonda?
13 Chimene chimasonyeza bwino kwambiri kuti anthu angathe kukhala amtengo wapatali kwambiri kwa Yehova ndicho dipo limene Yehova anapereka. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Dipo limene Yehova anapereka kudzera mwa Yesu Kristu limasonyezeratu kuti n’zosatheka kuti Yehova asatikonde ndiponso kuti tikhale opanda ntchito kwa iye. Chifukwatu ngati Yehova analolera kutigula pamtengo waukulu kwambiri chonchi, kupereka Mwana wake wobadwa yekha, ndiye kutitu amatikonda kwambiri.
14. Kodi n’chiyani chimasonyeza mmene Paulo ankaonera dipo?
14 Motero maganizo odziona ngati wopanda ntchito akakufikirani, ganizirani za dipo. Inde, mphatso imeneyi muziiona ngati mphatso imene Yehova wakupatsani inuyo panokha. Izitu n’zimene mtumwi Paulo anachita. Kumbukirani kuti iye anati: “Munthu wosauka ine.” Koma kenaka anapitiriza kunena kuti: “Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu.” Pauloyu anatinso Yesu Kristu “anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.” (Aroma 7:24, 25; Agalatiya 2:20) Ponena zimenezi Paulo sanali kudzichemerera. Koma ankangosonyeza kuti sankakayikira kuti Yehova ankamuona kuti anali wofunika kwambiri pamaso pake. Monga Paulo, inunso muyenera kuyamba kuona kuti nsembe ya dipo ndi mphatso yanuyanu yochokera kwa Mulungu. Yehova sali chabe Wopulumutsa wamphamvu komanso ndi Wopereka Mphoto wachikondi.
Samalani ndi “Machenjerero” a Satana
15-17. (a) Kodi anthu akakhala ndi maganizo odziona ngati opanda ntchito Mdyerekezi amapezerapo mpata wotani? (b) Kodi tingalimbikitsidwe motani ndi zimene Yobu anakumana nazo?
15 Komabe, mwina zingakuvuteni kukhulupirira kuti mawu ouziridwa okulimbikitsani amene ali m’Mawu a Mulungu amanenadi za inuyo. Mwina mungaone kuti mphoto yodzakhala ndi moyo kosatha m’dziko latsopano la Mulungu ndi yoyenerera anthu enaake, koma osati munthu ngati inuyo ayi. Ngati mumamva choncho kodi mungatani?
16 N’zosakayikitsa kuti mukudziwa mawu a Paulo olimbikitsa Aefeso kuti: “Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11) Tikamaganizira za misampha ya Satana, mwina timaganiza msanga za zinthu monga kukonda ndalama ndiponso chiwerewere, ndipotu sikulakwa kuganiza choncho. Mayesero amenewa asocheretsapo anthu ambiri a Mulungu akale ngakhalenso a masiku ano. Komabe, sitiyenera kunyalanyaza msampha winanso wa Satana. Msampha umenewu ndiwo zinthu zimene Satana amayesa kuchita kuti anthu azikhulupirira kuti Yehova Mulungu sawakonda.
17 Anthu akakhala ndi maganizo oterewa Mdyerekezi amapezerapo mwayi woyesa kuwachotsa m’manja mwa Mulungu. Kumbukirani mawu awa, amene Bilidadi anauza Yobu, kuti: “Potero munthu akhala bwanji wolungama kwa Mulungu? Kapena wobadwa ndi mkazi akhala woyera bwanji? Tawonani, ngakhale mwezi ulibe kuwala; ndi nyenyezi siziyera pamaso pake; kopambana kotani nanga munthu, ndiye mphutsi! Ndi wobadwa ndi munthu, ndiye nyongolotsi!” (Yobu 25:4-6; Yohane 8:44) Tangoganizirani mmene mawu amenewa anamufoolera Yobu? Motero musalole kuti Satana akufooleni. Komanso Satana amafunika kusamala naye kuti mukhalebe olimba mtima ndiponso kuti musafooke ngakhale pang’ono mukamayesetsa kuchita zinthu zoyenera. (2 Akorinto 2:11) Ngakhale kuti Yehova anamuwongolera Yobu pa maganizo ake ena, anamupatsa mphoto chifukwa cha kupirira. Mphoto yake inali yom’patsa mowirikiza kawiri zinthu zonse zimene anataya.—Yobu 42:10.
Yehova “Ali Wamkulu Woposa Mitima Yathu”
18, 19. Kodi Mulungu ‘amaposa mitima yathu,’ motani ndipo kodi ‘amazindikira zonse’ motani?
18 N’zoona kuti zingakhale zovuta kuthetsa maganizo odziona ngati munthu wosafunika, ngati maganizowa atilowerera kwambiri. Komano mzimu wa Yehova ungathe kukuthandizani kuti pang’onopang’ono muthane ndi ‘zinthu zozikika molimba . . . zokwezeka zotsutsana ndi kudziwa kwathu Mulungu.’ (2 Akorinto 10:4, 5, NW) Maganizo omadziona ngati munthu wopanda ntchito akakuchulukirani, ganizirani mawu a Yohane akuti: “Umo tidzazindikira kuti tili ochokera m’choonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pake, mmene monse mtima wathu utitsutsa; chifukwa Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu, nazindikira zonse.”—1 Yohane 3:19, 20.
19 Kodi mawu akuti “Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu” amatanthauza chiyani? Nthawi zina mtima wathu ungathe kutichititsa kudziona ngati achabechabe, makamaka zophophonya zathu zikaonekera kwambiri kwa ifeyo. Kapenanso mwina tinakulira m’moyo womadziona ngati munthu wopanda ntchito, ngati kuti palibe chimene tingachite chovomerezeka kwa Yehova. Mawu a mtumwi Yohane amatitsimikizira kuti Yehova amaposa maganizo oterewa. Zophophonya zathu amangozipitirira n’kumaona zabwino zimene tingathe kuchita. Amadziwanso zolinga zathu ndi zimene tikuyesa kuchita. Davide analemba kuti: “Adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:14) Inde, Yehova amatidziwa kuposa mmene timadzidziwira eni akefe!
“Korona Wokongola” ndi “Korona Wachifumu”
20. Kodi ulosi wa Yesaya wonena za kubwezeretsa Aisrayeli kwawo, umasonyeza kuti Yehova amaona bwanji atumiki ake?
20 Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova anapatsa anthu ake akale chiyembekezo chodzawabwezeretsa kwawo. Pamene anali ku Babulo ku ukapolo, mawu olimbikitsawa anawathandiza kwambiri anthuwa poti anali atataya mtima. Poganizira za nthawi imene adzawabwezeretse kwawo, Yehova anati: “Udzakhalanso korona wokongola m’dzanja la Yehova, korona wachifumu m’dzanja la Mulungu wako.” (Yesaya 62:3) Mawu amene Yehova ananenawa anawalemekezetsa kwambiri anthu ake. Iye wachitanso chimodzimodzi masiku ano ndi mtundu wake wa Israyeli wauzimu. Zikungokhala ngati kuti anaukweza pamwamba kuti anthu onse auone n’kuukhumbira.
21. Kodi mungatani kuti musakayikire ngakhale pang’ono kuti Yehova adzakupatsani mphoto chifukwa chopirira mokhulupirika?
21 Ngakhale kuti ulosi umenewu umakwaniritsidwa makamaka kwa odzozedwa, umasonyezanso ulemerero umene Yehova amapereka kwa anthu onse amene amam’tumikira. Motero mukamakayikira kuti Yehova amakukondani, kumbukirani kuti ngakhale kuti ndinu wopanda ungwiro, kwa Yehovayo mungathe kukhala wofunika kwambiri ngati “korona wokongola” ndiponso “korona wachifumu.” Motero pitirizani kusangalatsa mtima wake poyesetsa kuchita zimene iye amafuna. (Miyambo 27:11) Mukamatero simungakayikire ngakhale pang’ono kuti Yehova adzakupatsani mphoto chifukwa chopirira mokhulupirika.
[Mawu a M’munsi]
a Mayina ena tawasintha.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi ndife ‘akeake’ a Yehova m’njira yotani?
• N’chifukwa chiyani m’pofunika kuona kuti Yehova ndi Wopereka Mphoto?
• Kodi ndi “machenjerero” otani a Satana amene tiyenera kusamala nawo?
• Kodi Mulungu “ali wamkulu woposa mitima yathu” m’njira yotani?
[Chithunzi patsamba 26]
Paulo
[Chithunzi patsamba 26]
Eliya
[Chithunzi patsamba 26]
Hana
[Chithunzi patsamba 28]
Mawu a Mulungu ali ndi mfundo zambiri zolimbikitsa