Mutu 8
‘Kulimbana ndi Makamu a Mizimu Yoipa’
ANTHU ambiri amaseka akamva kuti pali mizimu yoipa. Komatu si nkhani yoseketsa. Kaya anthu amakhulupirira kapena sakhulupirira, mizimu yoipa ilipodi, ndipo imayesa kuvutitsa aliyense. Olambira Yehova nawonso imawavutitsa. Ndipotu, ndi amene imawafuna kwambiri. Pankhaniyi, mtumwi Paulo anatichenjeza kuti: “Tili nako kulimbana, osati ndi mwazi ndi thupi, koma ndi maboma [osaoneka], ndi maulamuliro, ndi olamulira a dzikoli a mdima uno, ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba.” (Aefeso 6:12, NW) Masiku ano makamu a mizimu yoipa akuvutitsa anthu kwambiri kuposa mmene anali kuchitira m’mbuyomo. Izi zili choncho chifukwa chakuti Satana anachotsedwa kumwamba ndipo ndi wokwiya kwambiri, podziŵa kuti nthaŵi yake yatsala pang’ono.—Chivumbulutso 12:12.
2 Kodi n’zotheka kupambana nkhondo yolimbana ndi makamu a mizimu omwe ndi amphamvu kuposa anthu? Inde n’zotheka, ngati tidalira Yehova kotheratu. Tiyenera kumumvera ndi kulabadira Mawu ake. Mwa kuchita zimenezi tingapeŵe kuvulaza thupi lathu, kukhala ndi khalidwe loipa, ndiponso kuvutika maganizo, zomwe zimachitikira anthu amene Satana amawalamulira.—Yakobo 4:7.
Olamulira a Dzikoli M’malo Akumwamba
3 Yehova amatilongosolera bwino mmene zinthu zilili padziko lapansi monga momwe amazionera ali kumwamba, chifukwa kumeneko iye ali pamalo abwino oonerapo zonse. Iye anaonetsa mtumwi Yohane masomphenya mmene Satana anaoneka monga “chinjoka chofiira, chachikulu.” Satanayo anali wokonzeka kulikwira Ufumu Waumesiya wa Mulungu, ngati zikanatheka, pamene unangokhazikitsidwa kumene kumwamba mu 1914. Atalephera zimenezo, Satana anagundika kutsutsa oimira Ufumuwo padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:3, 4, 13, 17) Kodi Satana akumenya nkhondoyi motani? Akutero kupyolera mwa anthu omuimira.
4 Kenako Yohane anamuonetsa chilombo chokhala ndi mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi, chomwe chinali ndi ulamuliro “pa fuko lililonse, ndi anthu, ndi manenedwe, ndi mitundu.” Chilombo chimenecho chimaimira maulamuliro onse andale padziko lonse. Yohane anamuuza kuti “chinjoka [Satana Mdyerekezi] chinamupatsa iye [chilombo] mphamvu yake, ndi mpando wachifumu wake, ndi ulamuliro waukulu.” (Chivumbulutso 13:1, 2, 7) Inde, Satana ndiye amapatsa mphamvu komanso ulamuliro maboma a anthu. Choncho, monga analembera mtumwi Paulo, “makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba” ndiwo ‘olamulira enieni a dzikoli,’ ndi amene amalamulira maboma a anthu. Aliyense wofuna kulambira Yehova ayenera kumvetsetsa tanthauzo la zimenezi.—Luka 4:5, 6.
5 Ngakhale kuti olamulira andale ambiri amati amapembedza, palibe dziko n’limodzi lomwe limene limagonjera ulamuliro wa Yehova kapenanso wa Mfumu imene waiika, Yesu Kristu. Onse amaumirira kuti akhalebe ndi mphamvu. Monga mmene nkhani ya mu Chivumbulutso imasonyezera, lerolino “mizimu ya ziwanda” ikusonkhanitsa olamulira a dzikoli ku “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse” pa Armagedo.—Chivumbulutso 16:13, 14, 16; 19:17-19.
6 Tsiku lililonse, miyoyo ya anthu imasokonezeka ndi kukangana pa zandale, zachikhalidwe cha anthu, zachuma, ndi zachipembedzo zomwe zimagaŵanitsa anthu. Pa mikangano imeneyi anthu ambiri, mwa zolankhula zawo kapena zochita zawo, amakonda kukhala kumbali ya dziko lawo, fuko lawo, mtundu wawo, kapena ya olemera kaya osauka anzawo. Ngakhale pamene anthu sakuchita nawo mkangano winawake, kaŵirikaŵiri iwo amapezeka kuti akukondera mbali inayake. Koma kaya iwo akutsatira munthu uti, mabungwe ati kapenanso mfundo zotani, kodi iwo amakhala pambuyo pa ndani makamaka? Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Ndiyeno, kodi munthu angapeŵe bwanji kusokeretsedwa limodzi ndi anthu ena onse? Angapeŵe ngati achirikiza Ufumu wa Mulungu wokha ndiponso ngati satenga nawo mbali ngakhale pang’ono m’mikangano ya dzikoli.—Yohane 17:15, 16.
Njira Zamachenjera za Woipayo
7 M’mbiri yonse, Satana wayesa kupatutsa anthu pa kulambira koona mwa kuwazunza powanyoza ndi powachitira nkhanza. Komanso wagwiritsa ntchito njira zobisika kwambiri, njira zaukathyali ndi zamachenjera. Mochenjera zedi waika anthu ambiri mu mdima pogwiritsa ntchito chipembedzo chonyenga, wawachititsa kuganiza kuti akutumikira Mulungu. Posamudziŵa bwino Mulungu ndiponso posakonda choonadi, iwo angakopeke ndi mapembedzedwe achilendo ndi otenga mtima kapena angachite chidwi ndi ntchito zozizwitsa. (2 Atesalonika 2:9, 10) Koma tikuchenjezedwa kuti, ngakhale pakati pa amene nthaŵi ina anali kulambira m’choonadi, ‘ena adzatayika nasamalira mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziŵanda.’ (1 Timoteo 4:1) Kodi zimenezi zingachitike motani?
8 Mdyerekezi amapezera mpata mwamachenjera pa zofooka zathu. Kodi timaopabe anthu? Ngati ndi choncho, tikhoza kugonjera ngati achibale kapena anansi athu atatikakamiza kuchita nawo miyambo imene inayambitsidwa ndi chipembedzo chonyenga. Kodi ndife onyada? Ngati ndi choncho ndiye kuti tingakhumudwe popatsidwa uphungu kapena ngati ena savomereza malingaliro athu. (Miyambo 15:10; 29:25; 1 Timoteo 6:3, 4) M’malo mosintha kalingaliridwe kathu kuti kagwirizane ndi chitsanzo cha Kristu, tingamakonde kumvera anthu amene ‘amatinyerenyetsa m’makutu’ mwa kunena kuti kungoŵerenga Baibulo ndi kukhala munthu wabwino n’zokwanira. (2 Timoteo 4:3, NW) Satana alibe nazo kanthu kuti kaya tachita kuloŵa chipembedzo china kapena tidakali m’chipembedzo chathu chomwecho; kwa iye chofunika n’chakuti sitikulambira Yehova m’njira imene Mulungu amalongosola m’Mawu ake ndi mwa gulu lake.
9 Mochenjera Satana amakopanso anthu kuti azikhutiritsa zilakolako zawo zabwinobwino m’njira zolakwika. Wachita zimenezi pa chilakolako cha kugonana. Pokana makhalidwe abwino a m’Baibulo, anthu ambiri m’dzikoli amaona kuti palibe cholakwika kuti anthu osakwatirana azigonana kapenanso amati ndiyo njira imene iwo angatsimikizire kuti ndi anthu akuluakulu. Nanga bwanji amene ali pabanja? Ambiri amachita chigololo. Ndipo ngakhale pakhale palibe amene wachita chigololo m’banjamo, anthu ambiri amasudzulana kapena kupatukana kuti athe kuloŵana ndi munthu wina. Cholinga cha Satana pochita zinthu mosadziŵika bwino n’choti anthu azisangalala panopo, kuwachititsa kunyalanyaza zimene zidzawachitikira iwo limodzi ndi anthu ena m’kupita kwanthaŵi, ndiponso makamaka kunyalanyaza ubwenzi wawo ndi Yehova ndi Mwana wake.—1 Akorinto 6:9, 10; Agalatiya 6:7, 8.
10 Chilakolako china chabwinobwino ndicho kusangalala. Kusangalala kwabwino kungapumuze thupi, maganizo, ndipo kungachititse mtima kukhala m’malo. Koma kodi timachitanji pamene mochenjera Satana agwiritsa ntchito nthaŵi yosangalala kuti asiyanitse kaganizidwe kathu ndi ka Mulungu? Mwachitsanzo, timadziŵa kuti Yehova amada chiwerewere ndi chiwawa. Ngati mafilimu, mapulogalamu a wailesi yakanema, kapena maseŵero a zisudzo akuonetsa zimenezi, kodi timangoonererabe osachitapo kalikonse? Kumbukiraninso kuti Satana adzaonetsetsa kuti zinthu zoterezi zikuipiraipira pamene nthaŵi yake yoti aponyedwe kuphompho ikuyandikira, chifukwa “anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.” (2 Timoteo 3:13; Chivumbulutso 20:1-3) Motero nthaŵi zonse tiyenera kukhala maso kuti tipeŵe njira za Satana.—Genesis 6:13; Salmo 11:5; Aroma 1:24-32.
11 Tikudziŵanso kuti anthu amene amachita zilizonse zokhulupirira mizimu, monga kuombeza maula, ufiti, kapena kulankhula ndi akufa, amam’nyansa Yehova. (Deuteronomo 18:10-12) Pokumbukira zimenezi, sitingaganize zopita kwa obwebweta, ndipo sitingalole kuti abwere panyumba pathu kukachita zochita zawo zauchiŵanda. Koma kodi tingamvetsere zonena zawo ngati ataonekera pa wailesi yathu yakanema kapena pa Intaneti? Ngakhale kuti sitingalole sing’anga kutichiritsa, kodi mwana wathu wakhanda tikhoza kumumanga kachingwe pamkono poganiza kuti kangamuteteze m’njira inayake? Podziŵa kuti Baibulo limaletsa kulodza ena, kodi tingalole wamatsenga kutichiritsa mwamasalamusi?—Agalatiya 5:19-21.
12 Baibulo limati dama ndi chidetso chilichonse zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe (ndi zolinga zolakwika) mwa ife. (Aefeso 5:3-5) Koma bwanji ngati nkhani zimenezo zikutchulidwa m’nyimbo zoimbidwa mwaluso ndi zogunda bwino? Kodi tidzayamba kubwereza mawu ake amene amalimbikitsa kugonana popanda kukwatirana, kugwiritsa ntchito mankhwala kuti munthu asokonezeke bongo, ndi machimo ena? Kapena, pamene tikudziŵa kuti sitiyenera kutengera khalidwe la anthu amene amachita zinthu zoterozo, kodi timafuna kuti anthu azitifananitsa ndi anthu amenewo mwa kutengera kavalidwe kawo, mmene amakonzera tsitsi lawo, kaya kalankhulidwe kawo? Satana amagwiritsa ntchito njira zobisikatu kwambiri pokopa anthu kuti aziganiza molakwika ngati iyeyo! (2 Akorinto 4:3, 4) Kuti tisagwere m’njira zake zamachenjera, tiyenera kupeŵa kutengeka ndi dziko. Tifunika kukumbukira nthaŵi zonse amene ali “olamulira a dzikoli a mdima uno” ndipo tilimbane nawo ndi mtima wonse.—1 Petro 5:8.
Okonzeka Kupambana
13 Yesu asanafe anauza atumwi ake kuti: “Limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi Ine.” (Yohane 16:33) Iwonso akanatha kupambana chimodzimodzi. Patapita zaka ngati 60, mtumwi Yohane analemba kuti: “Koma ndani iye wolilaka dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu?” (1 Yohane 5:5) Timasonyeza chikhulupiriro choterocho mwa kumvera malamulo a Yesu ndi kudalira Mawu a Mulungu, monganso anachitira Yesuyo. N’chiyaninso china chofunikira? Nthaŵi zonse tikhale mu mpingo umene iye ndiye Mutu wake. Tikachimwa, tiyenera kulapa ndi mtima wonse ndi kupempha Mulungu kuti atikhululukire pogwiritsa ntchito nsembe ya Yesu. Mwa kuchita zimenezi ifenso tikhoza kupambana, ngakhale kuti ndife opanda ungwiro ndiponso timalakwa.—Salmo 130:3, 4.
14 Kuti tithe kupambana, tifunika kuvala “zida zonse za Mulungu,” osanyalanyaza ngakhale chimodzi. Tsegulani Baibulo lanu pa Aefeso 6:13-17, ndipo ŵerengani za zida zimenezi. Ndiyeno, onani momwe chida chilichonse chingakutetezereni mwa kuyankha mafunso otsatiraŵa.
“Mutadzimangira m’chuuno mwanu ndi choonadi”
Ngakhale kuti choonadi timachidziŵa, kodi kuphunzira nthaŵi zonse, kusinkhasinkha pa choonadi cha m’Baibulo, ndi kupezeka pa misonkhano kumatiteteza motani? (1 Akorinto 10:12, 13; 2 Akorinto 13:5; Afilipi 4:8, 9)
“Chapachifuwa cha chilungamo”
Kodi chilungamo chimenechi n’chilungamo cha ndani? (Chivumbulutso 15:3)
Perekani chitsanzo chosonyeza kuti kulephera kutsatira njira zolungama za Yehova kumavulaza munthu mwauzimu. (Deuteronomo 7:3, 4; 1 Samueli 15:22, 23)
“Mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere”
Kodi timatetezeka motani mapazi athu akamatanganidwa nthaŵi zonse kutipititsa kokalankhula ndi anthu za makonzedwe a Mulungu a mtendere? (Salmo 73:2, 3; Aroma 10:15; 1 Timoteo 5:13)
“Chikopa [chachikulu, NW] cha chikhulupiriro”
Ngati tili ndi chikhulupiriro cholimbadi, kodi tidzachitanji pamene ena atichititsa kukayikira kapena kuopa? (2 Mafumu 6:15-17; 2 Timoteo 1:12)
“Chisoti cha chipulumutso”
Kodi chiyembekezo cha chipulumutso chimathandiza bwanji munthu kupeŵa msampha wodera nkhaŵa kwambiri zachuma? (1 Timoteo 6:7-10, 19)
“Lupanga la Mzimu”
Kodi nthaŵi zonse tiyenera kudalira chiyani polimbana ndi zinthu zofuna kutigonjetsa kapenanso zofuna kugonjetsa ena mwauzimu? (Salmo 119:98; Miyambo 3:5, 6; Mateyu 4:3, 4)
Kodi chinanso n’chiyani chimene chili chofunika kwambiri kuti tipambane nkhondo yauzimu? Kodi tiyenera kuchigwiritsa ntchito kaŵirikaŵiri motani? M’malo mwa ndani? (Aefeso 6:18, 19)
15 Monga asilikali a Kristu, tili m’gulu lalikulu la ankhondo amene akumenya nkhondo yauzimu. Ngati tikhala tcheru ndi kugwiritsa ntchito bwino zida zonse za Mulungu, sitidzavulala kaya kuphedwa pa nkhondo imeneyi. Koma tidzatha kulimbikitsa atumiki a Mulungu anzathu. Tidzakhala okonzeka ndi ofunitsitsa kuponya nkhondo nthaŵi zonse mosamupatsa mpata Satana polalikira uthenga wabwino wa Ufumu Waumesiya wa Mulungu, boma lakumwamba limene iye amalitsutsa kwambiri.
Bwerezani Zomwe Mwakambirana
• N’chifukwa chiyani olambira Yehova satenga nawo mbali m’mikangano ya dzikoli?
• Kodi zina mwa njira zamachenjera zimene Satana amagwiritsa ntchito povulaza Akristu mwauzimu ndi ziti?
• Kodi zida zauzimu zimene Mulungu amapereka zimatiteteza motani pa nkhondo yathu yauzimu?
[Mafunso]
1. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuona zochita za mizimu yoipa ngati nkhani ya masewera?
2. Kodi zingatheke bwanji kupambana nkhondo yolimbana ndi mizimu yamphamvu zoposa za anthu?
3. Kodi Satana amatsutsa kwambiri ndani, ndipo amachita zimenezi motani?
4. Kodi ndani amene amapatsa mphamvu maboma a anthu, ndipo tikudziŵa bwanji?
5. Kodi lerolino olamulira andale akuwasonkhanitsira kuti?
6. N’chifukwa chiyani tifunika kusamala kuti tisakhale kumbali ya dziko la Satana?
7. Kodi mmene Satana akugwiritsira ntchito chipembedzo chonyenga zikusonyeza bwanji kuti ndi wochenjera?
8. Kodi Satana angatikopere bwanji m’chipembedzo chonyenga ngakhale kuti tikulambira Yehova?
9. Kodi mochenjera Satana amagwiritsa ntchito motani chilakolako cha kugonana pokwaniritsa zolinga zake?
10. Kodi Satana amayesa kusintha maganizo athu pa zachiwerewere ndi chiwawa pogwiritsa ntchito chiyani?
11. Kodi ngakhale munthu amene akudziŵa zoona zake za kukhulupirira mizimu angagwere mu msampha umenewu m’njira zotani ngati sali watcheru?
12. (a) Kodi nyimbo zimagwiritsidwa ntchito motani kuti zitichititse kukhala ndi maganizo amene timawadziŵa kuti ndi olakwika? (b) Kodi kavalidwe ka munthu, mmene amakonzera tsitsi lake, kapena kalankhulidwe kake kangasonyeze motani kuti amakopeka ndi anthu a khalidwe limene Yehova sagwirizana nalo? (c) Kodi n’chiyani chimene tifunika kuchita kuti tipeŵe kugwera m’njira zamachenjera za Satana?
13. Kodi n’zotheka bwanji kuti aliyense angathe kupambana dziko limene Satana amalilamulirali, ngakhale kuti ndife opanda ungwiro?
14. Ŵerengani Aefeso 6:13-17, ndipo kambiranani phindu la chida chauzimu chilichonse pogwiritsa ntchito mafunso ndi malemba amene ali m’ndime ino.
15. Kodi tingatani kuti tiponye nkhondo yauzimu nthaŵi zonse?
[Zithunzi patsamba 76]
Mitundu ikusonkhanitsidwa ku Armagedo