NKHANI YOPHUNZIRA 31
“Sitikubwerera M’mbuyo”
“Choncho sitikubwerera m’mbuyo.”—2 AKOR. 4:16.
NYIMBO NA. 128 Tipirire Mpaka Mapeto
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Kodi Akhristufe tiyenera kuchita chiyani kuti timalize mpikisano wokapeza moyo?
AKHRISTUFE tili pa mpikisano wokalandira moyo. Kaya tangoyamba kumene mpikisanowu kapena tinayamba kalekale, tiyenera kupitirizabe mpaka mapeto. Malangizo amene Paulo anapereka kwa Akhristu a ku Filipi angatilimbikitse kuti timalize nawo bwinobwino. Pamene Paulo ankawalembera kalatayi, Akhristu ena mumpingowo anali atatumikira Yehova kwa zaka zambiri. N’zoona kuti ankatumikira mokhulupirika koma Paulo ankawakumbutsa kuti apitirize kuthamanga pa mpikisanowo mopirira. Iye ankafuna kuti Akhristuwo atengere chitsanzo chake ‘choyesetsa kuchita khama mpaka atapeza mphoto.’—Afil. 3:14.
2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti malangizo a Paulo kwa Afilipi anali a pa nthawi yake?
2 Malangizo amene Paulo anapereka kwa Akhristu a ku Filipi anali a pa nthawi yake. Tikutero chifukwa Akhristuwo anakhala akuzunzidwa kuchokera pamene mpingowo unayamba. Mavutowo anayamba pamene Paulo ndi Sila anafika ku Filipi cha m’ma 50 C.E., atauziridwa ndi Mulungu kuti: “Wolokerani ku Makedoniya.” (Mac. 16:9) Atafika anakumana ndi mzimayi wina dzina lake Lidiya amene ‘anali kumvetsera ndipo Yehova anatsegula kwambiri mtima wake’ kuti amve uthenga wabwino. (Mac. 16:14) Pasanapite nthawi yaitali, anabatizidwa limodzi ndi anthu a m’banja lake. Koma Mdyerekezi anabweretsa mavuto ambiri. Anthu amumzindawo anagwira Paulo ndi Sila n’kupita nawo kwa akuluakulu a boma ndipo anawanamizira kuti akuyambitsa chisokonezo. Kenako anawamenya, kuwaika m’ndende ndipo patapita nthawi anawalamula kuti achoke mumzindawo. (Mac. 16:16-40) Koma iwo sanabwerere m’mbuyo. Kodi abale ndi alongo amumpingo umene unali utangokhazikitsidwa kumenewo anatani? N’zosangalatsa kuti nawonso anapirira. N’zosakayikitsa kuti analimbikitsidwa kwambiri ndi chitsanzo cha Paulo komanso Sila.
3. Kodi Paulo ankadziwa chiyani, nanga tikambirana mafunso ati?
3 Paulo sankafuna kubwerera m’mbuyo. (2 Akor. 4:16) Koma ankadziwa kuti afunika kumaganizira kwambiri za cholinga chake kuti athamange mpaka pa mapeto. Kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha Paulo? Kodi ndi zitsanzo ziti zamasiku ano zimene zikusonyeza kuti tikhoza kupirira ngakhale pamene tikukumana ndi zinthu zofooketsa? Nanga kodi zimene tikuyembekezera zingatilimbikitse bwanji kuti tisabwerere m’mbuyo?
KODI CHITSANZO CHA PAULO CHINGATITHANDIZE BWANJI?
4. Kodi Paulo ankachita chiyani ngakhale kuti zinthu sizinali bwino pa moyo wake?
4 Taganizirani mmene zinthu zinalili pa moyo wa Paulo pa nthawi imene ankalembera kalata Akhristu a ku Filipi. Iye anali pa ukaidi wosachoka pakhomo ku Roma ndipo analibe ufulu wambiri wolalikira. Koma ankachita khama kulalikira kwa anthu odzamuona komanso kulemba makalata opita kumipingo yakutali. Masiku anonso, Akhristu amene sangathe kuchoka panyumba amalalikira kwa anthu amene amabwera kudzawaona. Amalembanso makalata olimbikitsa kwa anthu amene sangakumane nawo mu utumiki.
5. Malinga ndi zimene Paulo analemba pa Afilipi 3:12-14, kodi ndi zinthu ziti zimene zinamuthandiza kuti asamasokonezedwe?
5 Paulo sanalole kuti zinthu zabwino kapena zoipa zimene anachita m’mbuyo zimusokoneze. Paja iye ananena kuti “ndikuiwala zinthu zakumbuyo ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo,” kutanthauza kuti ankafuna kumaliza bwinobwino mpikisano. (Werengani Afilipi 3:12-14.) Kodi ndi zinthu ziti zimene Paulo sanalole kuti zizimusokoneza? Choyamba, panali zinthu zambiri zotamandika zimene anachita ali m’chipembedzo chachiyuda. Koma ankaona zinthu zonsezo ngati “mulu wa zinyalala.” (Afil. 3:3-8) Chachiwiri, iye sankalola kuti asokonezeke chifukwa chodziimba mlandu kuti anazunza kwambiri Akhristu. Chachitatu, iye sankaganiza kuti wachita kale zokwanira potumikira Yehova. Paulo anakwanitsa kuchita zambiri ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto monga kumangidwa, kumenyedwa, kugendedwa, kusweka kwa sitima komanso kusowa chakudya ndi zovala. (2 Akor. 11:23-27) Ngakhale kuti anali atachita kale zambiri komanso kukumana ndi mavuto, Paulo ankaona kuti afunika kuchitabe khama. Ndi mmene zililinso ndi ifeyo.
6. Kodi zina mwa “zinthu zakumbuyo” zimene tiyenera kuziiwala ndi ziti?
6 Kodi tingatsanzire bwanji Paulo pa nkhani ‘yoiwala zinthu zakumbuyo’? Enafe timafunika kusiya kudziimba mlandu pa zinthu zimene tinalakwitsa m’mbuyomu. Kuti tisiye kudziimba mlandu, tingachite bwino kuphunzira mozama nkhani ya dipo la Khristu. Kuphunzira, kuganizira mozama komanso kupempherera nkhani ya dipoyi kungatithandize kuti tisiye kudziimba mlandu kwambiri. Ndipo mwina tikhoza kusiyiratu kudzizunza chifukwa cha machimo amene Yehova anakhululuka kale. Kodi n’chiyaninso chimene tingaphunzire pa chitsanzo cha Paulo? Anthu ena mwina anasiya ntchito yapamwamba n’cholinga choti azichita zambiri potumikira Mulungu. Ngati ndi choncho, tikhoza kuiwala zinthu zakumbuyo popewa kulakalaka zinthu zimene tikuganiza kuti tikanazipeza tikanakhala kuti tikugwirabe ntchitoyo. (Num. 11:4-6; Mlal. 7:10) “Zinthu zakumbuyo” zikhozanso kukhala zimene tinakwanitsa kuchita kapena mavuto amene tinapirira. N’zoona kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ukhoza kulimba ngati titaganizira mmene iye wakhala akutidalitsira kapena mmene watithandizira m’mbuyomu. Koma si bwino kungokhutira ndi zimenezo n’kumaganiza kuti tachita zokwanira.—1 Akor. 15:58.
7. Malinga ndi 1 Akorinto 9:24-27, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipambane pa mpikisano wokalandira moyo? Perekani chitsanzo.
7 Paulo anamvetsa mawu a Yesu akuti: “Yesetsani mwamphamvu.” (Luka 13:23, 24) Iye ankadziwa kuti ayenera kutsanzira Yesu n’kumayesetsa mwamphamvu mpaka mapeto. N’chifukwa chake anayerekezera moyo wa Akhristu ndi mpikisano wothamanga. (Werengani 1 Akorinto 9:24-27.) Munthu amene ali pa mpikisano amaganizira kwambiri cholinga chake chokafika kumapeto ndipo salola kuti zinthu zina zimusokoneze. Mwachitsanzo, anthu ochita mpikisano wothamanga masiku ano angamadutse m’misewu yokhala ndi malonda komanso zinthu zina zomwe zingawasokoneze. Ndiye kodi mukuganiza kuti munthu amene ali pa mpikisano angaime kuti aone malonda? Ngati akufuna kupambana pa mpikisanowo, sangachite zimenezi. Ifenso tiyenera kupewa zinthu zimene zingatisokoneze pa mpikisano wokalandira moyo. Tikamaganizira kwambiri cholinga chathu komanso kuyesetsa mwakhama ngati mmene Paulo anachitira, tidzalandira mphoto.
ZINTHU ZIMENE ZINGATIFOOKETSE POTUMIKIRA YEHOVA
8. Kodi tikambirana mavuto atatu ati?
8 Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene zingatifooketse. Zinthu zake ndi izi: (1) Ngati zimene tinkayembekezera sizikuchitika, (2) matenda kapena ukalamba ndiponso (3) mavuto anthawi yaitali. Kukambirana zimene anthu ena achita atakumana ndi mavuto amenewa kungatithandize kwambiri.—Afil. 3:17.
9. Kodi chingachitike n’chiyani ngati zinthu zimene tikuyembekezera sizikuchitika?
9 Ngati zimene tinkayembekezera sizikuchitika. Anthufe timalakalaka zinthu zabwino zimene Yehova watilonjeza. Mneneri Habakuku ankalakalaka kuti Yehova athetse mavuto amene anali mu Yuda koma Yehova anamuuza kuti ‘aziyembekezerabe.’ (Hab. 2:3) Koma ngati zimene tikuyembekezera zikuoneka kuti zikuchedwa, tikhoza kufooka. Mwinanso tikhoza kufika potaya mtima. (Miy. 13:12) Izi n’zimene zinachitikira anthu ena kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900. Pa nthawiyo, Akhristu odzozedwa ambiri ankayembekezera kulandira mphoto yawo kumwamba mu 1914. Koma izi sizinachitike. Kodi anthu okhulupirika anatani ataona kuti zimene ankayembekezera sizikuchitika?
10. Kodi banja lina linatani litaona kuti zimene linkayembekezera sizinachitike?
10 Chitsanzo chabwino ndi cha Akhristu awiri okhulupirika amene analipo pa nthawiyo. M’bale Royal Spatz anabatizidwa mu 1908 ali ndi zaka 20. Iye sankakayikira kuti watsala pang’ono kupita kumwamba. M’baleyo atafunsira mlongo wina dzina lake Pearl mu 1911, anamuuza kuti: “Paja ukudziwa bwino zimene zichitike mu 1914, eti? Ndiye ngati tikufuna kukwatirana, bola tikwatirane msangamsanga.” Kodi banjali linafooka litaona kuti silinapite kumwamba mu 1914? Ayi, chifukwa cholinga chawo chachikulu chinali kutumikira Yehova mokhulupirika osati kulandira mphoto. Iwo ankafunitsitsa kuti athamange pa mpikisano wawo mopirira. Ndipo awiri onsewa anatumikira Yehova mwakhama komanso mokhulupirika kwa zaka zambiri mpaka pamene anamaliza moyo wawo wapadziko lapansi. N’zosachita kufunsa kuti nanunso mumalakalaka Yehova atayeretsa dzina lake, kusonyeza kuti ndi woyenera kulamulira komanso kukwaniritsa malonjezo ake onse. Dziwani kuti zinthu zimenezi zidzachitika pa nthawi imene Yehova akuona kuti ndi yoyenera. Pamene tikudikira nthawi imeneyo, tiyeni tizitumikira Mulungu mwakhama ndipo tisafooke chifukwa chakuti zinthu zimene tinkayembekezera sizikuchitika.
11-12. N’chifukwa chiyani sitiyenera kubwerera m’mbuyo ngakhale pamene tikudwala kapena takalamba? Perekani chitsanzo.
11 Matenda kapena ukalamba. Mosiyana ndi wothamanga pa mpikisano, sitifunikira mphamvu zenizeni kuti tilimbitse chikhulupiriro chathu potumikira Yehova. Ndipo anthu ambiri amene akudwala kapena ndi okalamba amayesetsabe kukhala amphamvu mwauzimu. (2 Akor. 4:16) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Arthur Secord.b Pamene m’baleyu anali ndi zaka 88, anali atatumikira pa Beteli kwa zaka 55. M’baleyu sankapeza bwino ndipo tsiku lina mlongo wina amene ndi nesi anafika pabedi lake kuti amuthandize. Atamuyang’ana anamulankhula mokoma mtima kuti: “M’bale Secord, inutu mwachita zambiri potumikira Yehova.” Koma m’baleyu sankaganizira kwambiri zimene wachita kale. Iye anayang’ana nesiyo, kumwetulira, kenako n’kunena kuti: “Aaa mukunena zoona. Komatu nkhani yagona pa zimene tingachite kuyambira panopa osati zimene tachita kale.”
12 Mwina mwakhala mukutumikira Yehova kwa nthawi yaitali koma panopa mukulephera kuchita zambiri chifukwa cha matenda kapena ukalamba. Ngati ndi choncho, musataye mtima. Dziwani kuti Yehova amayamikira zinthu zonse zimene mwachita pomutumikira m’mbuyomu. (Aheb. 6:10) Ndipo musaiwale kuti kutumikira Yehova ndi mtima wonse sikutanthauza kuchita zinthu zambiri. Chofunika n’kukhala ndi mtima wofunitsitsa kutumikira Yehova komanso kuchita zonse zimene mungakwanitse. (Akol. 3:23) Yehova amadziwa zimene tingathe kuchita ndipo sayembekezera kuti tizichita zimene sitingakwanitse.—Maliko 12:43, 44.
13. Kodi chitsanzo cha banja lina chingatithandize bwanji kuti tikhalebe okhulupirika ngakhale kuti takumana ndi mavuto ambiri?
13 Mavuto anthawi yaitali. Atumiki a Yehova ena akhala akukumana ndi mavuto kapena kuzunzidwa kwa nthawi yaitali. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi M’bale Anatoly Melnik.c Pamene anali ndi zaka 12 zokha, bambo ake anamangidwa kenako n’kutumizidwa ku Siberia pa mtunda wa makilomita 7,000 kuchokera kwawo ku Moldova. Patangotha chaka chimodzi, Anatoly, mayi ake ndi agogo ake awiri anatumizidwanso ku Siberia. Kenako anayamba kupita kumisonkhano kumudzi wina wa pa mtunda wa makilomita 30 kunja kukuzizira koopsa komanso kuli sinowo. Patapita nthawi, M’bale Melnik anakhala kundende kwa zaka zitatu moti anasiyana ndi mkazi wake Lidiya komanso mwana wake wamkazi wachaka chimodzi. Ngakhale kuti banjali linakumana ndi mavuto kwa nthawi yaitali, iwo ankatumikirabe Yehova mokhulupirika. Panopa, M’bale Anatoly ali ndi zaka 82 ndipo akutumikira mu Komiti ya Nthambi ku Central Asia. Mofanana ndi banjali, ifenso tizichita zonse zimene tingathe potumikira Yehova komanso kupitiriza kupirira mavuto amene tikukumana nawo.—Agal. 6:9.
CHIYEMBEKEZO CHATHU CHIMATILIMBIKITSA
14. Kodi Paulo ankadziwa kuti ayenera kuchita chiyani kuti akapeze mphoto?
14 Paulo sankakayikira kuti adzakwaniritsa cholinga chake n’kumaliza mpikisano umene ankathamanga. Popeza anali Mkhristu wodzozedwa, ankayembekezera kudzapeza “mphoto ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba.” Koma ankadziwa kuti ayenera ‘kuyesetsabe’ kuti adzapeze mphotoyo. (Afil. 3:14) Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo chochititsa chidwi kuti athandize Afilipi kumvetsa kufunika koyesetsabe kukwaniritsa cholinga chawo.
15. Kodi Paulo anagwiritsa ntchito bwanji chitsanzo cha kukhala nzika polimbikitsa Afilipi kuti ‘aziyesetsabe’ kukapeza mphoto yawo?
15 Paulo anakumbutsa Afilipi kuti anali nzika zakumwamba. (Afil. 3:20) N’chifukwa chiyani ankafunika kukumbukira zimenezi? Pa nthawi imeneyo, anthu ankafunitsitsa kukhala nzika yachiroma.d Koma Akhristu odzozedwa anali nzika za malo abwino kwambiri ndipo akanatha kupeza phindu lalikulu kuposa kukhala nzika yachiroma. N’chifukwa chake Paulo analimbikitsa Afilipi kuti ‘makhalidwe awo akhale oyenera uthenga wabwino wa Khristu’ kapena kuti azichita zinthu monga nzika zakumwamba. (Afil. 1:27) Akhristu odzozedwa amasiku ano amapereka chitsanzo chabwino akamayesetsabe kuti akapeze mphoto yawo yokakhala ndi moyo wosatha kumwamba.
16. Kaya tikuyembekezera kukakhala kumwamba kapena padzikoli, kodi tiyenera kupitiriza kuchita chiyani mogwirizana ndi Afilipi 4:6, 7?
16 Kaya tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha kumwamba kapena padzikoli, tiyenera kuyesetsabe kuti tidzapeze mphotoyi. Mulimonse mmene zilili pa moyo wathu, sitiyenera kuyang’ana zinthu zam’mbuyo kapena kulola chilichonse kuti chitilepheretse kutumikira Yehova mokhulupirika. (Afil. 3:16) N’kutheka kuti zinthu zimene tinkayembekezera sizikuchitika, apo ayi tikudwala kapena takalamba. Mwinanso takhala tikukumana ndi mavuto kapena kuzunzidwa kwa zaka zambiri. Ngakhale zili choncho, ‘tisamade nkhawa ndi kanthu kalikonse.’ Koma tizingopemphera kwa Mulungu mopembedzera ndipo iye adzatipatsa mtendere umene umaposa chilichonse chimene tingaganizire.—Werengani Afilipi 4:6, 7.
17. Kodi tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?
17 Mofanana ndi wothamanga amene amayesetsa kuthamanga kwambiri akatsala pang’ono kumaliza mpikisano, tiyeni tiziyesetsa kuti timalize mpikisano wathu wokapeza moyo. Tizichita zonse zimene tingathe mogwirizana ndi mmene zilili pa moyo wathu kuti tikapeze mphoto yathu yabwino kwambiri. Koma kodi n’chiyani chingatithandize kupirira pochita zimenezi? Munkhani yotsatira tidzakambirana zimene zingatithandize kuika zinthu zofunika pamalo oyamba komanso ‘kutsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.’—Afil. 1:9, 10.
NYIMBO NA. 79 Athandizeni Kukhala Olimba
a Kaya takhala tikutumikira Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe timafunika kusinthabe zinthu zina kuti tikhale Akhristu abwino kwambiri. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti asabwerere m’mbuyo. M’kalata imene analembera Akhristu a ku Filipi, muli mfundo zimene zingatithandize kuti tipirire pa mpikisano wokalandira moyo. Munkhaniyi tikambirana zimene tingachite kuti titsatire malangizo a Paulo amenewa.
b Onani mbiri ya moyo wa M’bale Secord mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya June 15, 1965, pa mutu wakuti, “My Part in Advancing Right Worship.”
c Onani mbiri ya moyo wa M’bale Melnik mu Galamukani ya November 8, 2004, pamutu wakuti, “Ndinaphunzitsidwa Kukonda Mulungu Kuyambira Ndili Mwana.”
d Mzinda wa Filipi unkalamuliridwa ndi Aroma choncho anthu ake anali ndi ufulu ngati nzika zachiroma. N’chifukwa chake chitsanzo chimene Paulo anagwiritsa ntchito chinali chothandiza.