“Zopempha Zanu Zidziwike kwa Mulungu”
“M’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.”—AFILIPI 4:6.
1. Kodi tili ndi mwayi wolankhulana ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani umenewu uli mwayi wosaneneka?
KODI mutapempha kuti muonane ndi wolamulira wa dziko lanu, mungauzidwe chiyani? Mwina mungalandire yankho laulemu kuchokera ku ofesi ya wolamulirayo, koma n’zokayikitsa kwambiri kuti mungaloledwe kukalankhula ndi wolamulira weniweniyo. Komatu si choncho ndi Yehova Mulungu, Wolamulira wamkulu koposa, yemwenso ndi Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse. Tingathe kum’fikira tili kulikonse komanso panthawi iliyonse imene tingafune. Mapemphero ovomerezeka amam’fika nthawi zonse. (Miyambo 15:29) Izitu n’zosangalatsa kwambiri! Motero, posonyeza kuyamikira zimenezi, tiyenera kupemphera nthawi zonse kwa Mulungu, yemwe amatchedwa “Wakumva pemphero,” ndipotu m’pake kuti amatchedwa choncho.—Salmo 65:2.
2. Kodi chofunika n’chiyani kuti Mulungu amve mapemphero athu?
2 Koma wina angafunse kuti, ‘Kodi Mulungu amamva mapemphero otani? Baibulo limatchula chinthu chimodzi chofunika kuti mapemphero amvedwe, ponena kuti: “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kum’kondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” (Ahebri 11:6) Inde, monga tinafotokozera m’nkhani yoyamba ija, chinthu chofunika kwambiri pom’fikira Mulungu ndicho chikhulupiriro. Mulungu n’ngokonzeka kumva mapemphero a anthu amene amam’fikira, koma anthuwo ayenera kum’fikira mwa chikhulupiriro, ayenera kuchita ntchito zabwino, kukhala oona mtima, ndiponso kukhala ndi mtima wowongoka.
3. (a) Monga anasonyezera mapemphero a anthu akale okhulupirika, kodi ndi mfundo zotani zimene tingatchule m’mapemphero athu? (b) Kodi mapemphero athu angakhale a mitundu yotani?
3 Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu m’nthawi yake kuti: “Musadere nkhawa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.” (Afilipi 4:6, 7) Baibulo lili ndi zitsanzo zambiri za anthu amene anauza Mulungu nkhawa zawo. Ena mwa anthu amenewa ndi Hana, Eliya, Hezekiya, ndi Danieli. (1 Samueli 2:1-10; 1 Mafumu 18:36, 37; 2 Mafumu 19:15-19; Danieli 9:3-21) Tiyeni titengere chitsanzo chawo. Onaninso kuti mawu a Paulo akusonyeza kuti mapemphero athu angathe kukhala a mitundu yosiyanasiyana. Iye anatchula za chiyamiko, kutanthauza pemphero loyamikira Mulungu pa zimene amatichitira. M’pemphero lotereli tingathenso kutchulamo mfundo zotamanda Mulungu. Pembedzero ndi pempho lonenedwa modzichepetsa komanso modandaula. Ndipo ifeyo tinganene zopempha zathu, kapena kuti mapemphero ochita kutchula chinthucho. (Luka 11:2, 3) Tate wathu wakumwamba amasangalala tikam’fikira m’njira zonsezi.
4. Ngakhale kuti Yehova amadziwa zosowa zathu zonse, n’chifukwa chiyani timam’pemphabe zinthu?
4 Ena angafunse kuti, ‘Kodi si paja Yehova amakhala akudziwa zosowa zathu zonse?” Inde, amadziwa. (Mateyu 6:8, 32) Nangano n’chifukwa chiyani amafunabe kuti tizimuuza nkhawa zathu? Taganizirani chitsanzo ichi: Mwinisitolo angakonze zopereka mphatso kwa ena mwa makasitomala ake. Komabe, kuti alandire mphatso yawoyo, makasitomalawo ayenera kupita kwa mwinisitoloko n’kukaitenga. Amene sakufuna kuchita zimenezi angasonyeze kuti mphatsoyo sakuifuna kwenikweni. Ifenso ngati sitimuuza Mulungu zopempha zathu m’pemphero, tingasonyeze kuti zinthu zimene Yehova amapereka tilibe nazo ntchito kwenikweni. Yesu anati: “Pemphani, ndipo mudzalandira.” (Yohane 16:24) Tikatero, timasonyeza kuti tikum’daliradi Mulungu.
Kodi Tizim’fika Bwanji Mulungu?
5. N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera m’dzina la Yesu?
5 Yehova sapereka malamulo ambirimbiri a mmene tiyenera kupempherera. Komabe m’pofunika kuti tidziwe njira yoyenera yom’fikira Mulungu, yolongosoledwa m’Baibulo. Mwachitsanzo, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti: ‘Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m’dzina langa.’ (Yohane 16:23) Motero, timafunika kupemphera m’dzina la Yesu, pozindikira kuti Yesu ndiye njira yokhayo imene madalitso a Mulungu amafikira kwa anthu onse.
6. Kodi popemphera tizikhala kapena kuima motani?
6 Kodi tizikhala kapena kuima motani tikamapemphera? Baibulo silinenapo kalikonse kosonyeza kuti mapemphero amamvedwa tikakhala kapena kuima m’njira inayake. (1 Mafumu 8:22; Nehemiya 8:6; Marko 11:25; Luka 22:41) Chofunika ndicho kupemphera kwa Mulungu moona mtima ndiponso ndi mtima wowongoka.—Yoweli 2:12, 13.
7. (a) Kodi tanthauzo la “Ame” n’chiyani? (b) Kodi popemphera, mawuwa amayenera kutchulidwa m’njira zotani?
7 Nanga bwanji zotchula mawu akuti “Ame,” kapena kuti “Amen”? Malemba amasonyeza kuti nthawi zambiri, amenewa ndi mawu oyenera kuwatchula pomaliza mapemphero athu, makamaka tikamapemphera pagulu. (Salmo 72:19; 89:52) Mwachidule, mawu a Chihebri akuti ʼa·menʹ amatanthauza kuti “ndithudi.” Buku lina lolembedwa ndi McClintock ndi Strong limafotokoza kuti kunena “Ame” pomaliza pemphero kumasonyeza “kutsimikizira mawu amene anenedwa m’pempherowo, ndi kupempha kuti akwaniritsidwe.” Motero, pomaliza pemphero mwa kunena “Ame” mochokera pansi pa mtima, munthu wopempherayo amasonyeza kuti zimene wanena m’pempherolo wazinena ndi mtima wonse. Popemphera moimira mpingo, Mkristu akamaliza pemphero lake ndi mawu amenewa, anthu amene akumvetsera pempherolo angavomereze ponenanso kuti “Ame” chamumtima kapena mokweza, kusonyeza kuti akugwirizana kwambiri ndi zimene wanenazo.—1 Akorinto 14:16.
8. Kodi mapemphero athu ena angafanane bwanji ndi mapemphero a Yakobo kapena Abrahamu, ndipo tingaonetse chiyani chifukwa chopemphera m’njira imeneyi?
8 Nthawi zina Mulungu amatisiya kuti tionetse kuti tikukhudzidwa kwambiri bwanji ndi nkhani zimene tikupempherera. Motero tingafunike kuchita zangati zimene anachita Yakobo, amene analimbana ndi mngelo usiku wonse kuti adalitsidwe. (Genesis 32:24-26) Ndipo nthawi zina pangafunike kuti tikhale ngati Abrahamu, amene anapemphera kwa Yehova mobwerezabwereza kuti athandize Loti ndi munthu aliyense wolungama amene akanapezeka mu Sodomu. (Genesis 18:22-33) Ifenso tingachite chimodzimodzi pom’dandaulira Yehova za zinthu zimene zili zofunika kwa ifeyo, ndipo tingatero pom’tchulira za chilungamo chake, kukoma mtima kwake, ndiponso chifundo chake.
Kodi Tingapemphe Chiyani?
9. Kodi n’chiyani chimene tiyenera kuchiganizira kwambiri popemphera?
9 Kumbukirani kuti Paulo anati: ‘M’zonse . . . zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.’ (Afilipi 4:6) Motero, mapemphero apatokha angakhudze mbali zosiyanasiyana za moyo wathu. Komano chinthu chofunika kuchiganizira kwambiri m’mapemphero athu chizikhala zofuna za Yehova. Danieli anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pankhani imeneyi. Aisrayeli atalangidwa chifukwa cha machimo awo, Danieli ananena mawu otsatirawa pochonderera Yehova kuti awachitire chifundo: ‘Musachedwe, chifukwa cha inu nokha, [“chifukwa cha dzina lanu,” NW] Mulungu wanga.’ (Danieli 9:15-19) Kodi mapemphero athu amasonyeza kuti zinthu zimene timaziganizira kwambiri ndizo kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova ndi kukwaniritsidwa kwa chifuniro chake?
10. Kodi tikudziwa bwanji kuti sikulakwa kupempherera nkhani zotikhudza ifeyo patokha?
10 Komabe ndi bwinonso kupempherera zinthu zotikhudza ifeyo patokha. Mwachitsanzo, monga wamasalmo, tingathe kupemphera kuti tifike pomvetsa zinthu zauzimu m’njira yozama. Iye anapemphera kuti: “Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.” (Salmo 119:33, 34; Akolose 1:9, 10) Yesu “anapereka mapemphero ndi mapembedzero . . . kwa Iye amene anakhoza kum’pulumutsa Iye muimfa.” (Ahebri 5:7) Potero anasonyeza kuti sikulakwa kupemphera kwa Mulungu kuti atipatse mphamvu tikamakumana ndi zoopsa kapena ziyeso. Pouza ophunzira ake pemphero la chitsanzo, Yesu anatchulapo nkhani zotikhudza ifeyo patokha, monga kukhululukira zolakwa zathu ndi kupeza chakudya chathu cha tsiku ndi tsiku.
11. Kodi pemphero lingatithandize bwanji kuti tisagonjetsedwe ndi ziyeso?
11 M’pemphero la chitsanzo lija Yesu anatchulamo pempho lakuti: “Musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.” (Mateyu 6:9-13) Pambuyo pake iye analangiza kuti: “Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m’kuyesedwa.” (Mateyu 26:41) Pemphero n’lofunika kwambiri tikakhala pachiyeso. Tingakhale pachiyeso chonyalanyaza mfundo za m’Baibulo kuntchito kapena kusukulu. Anthu amene si Mboni angatiitane kuti tichite nawo zinthu zinazake zokayikitsa. Iwo angatiuze kuchita zinazake zosemphana ndi mfundo za makhalidwe abwino. Panthawi zimenezi, n’chinthu chanzeru kutsatira malangizo a Yesu oti tipemphere; kupemphera pasadakhale komanso pamene takumana ndi chiyesocho, kupempha Mulungu kuti atithandize kuti tisagonjetsedwe ndi chiyesocho.
12. Kodi tingapemphere chifukwa cha mavuto otani, ndipo tingayembekeze kuti Yehova atani nawo mapemphero athuwo?
12 Atumiki a Mulungu masiku ano amakumana ndi zovuta ndiponso zinthu zosiyanasiyana zodetsa nkhawa. Anthu ambiri amakhala ndi nkhawa chifukwa cha matenda ndiponso maganizo. Ziwawa zochulukazi zimachititsa moyo wathu kukhala wovuta. Mavuto a zachuma amachititsa kuti kupeza zinthu zofunika pamoyo kuzikhala kovuta. N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova amamvetsera atumiki ake akamamuuza mavuto amenewa. Ponena za Yehova, lemba la Salmo 102:17 limati: “Anasamalira pemphero la iwo akusowa konse, osapepula pemphero lawo.”
13. (a) Kodi ndi nkhani ziti zotikhudza ifeyo patokha zomwe zili zoyenera kuzitchula m’pemphero? (b) Tchulanipo chitsanzo cha pemphero lotero?
13 Kwenikweni, nkhani iliyonse yokhudza utumiki wathu kwa Yehova ndiponso ubwenzi wathu ndi iyeyo ndi nkhani yabwino kuitchula m’pemphero. (1 Yohane 5:14) Ngati mukufunikira kuchita zinazake pa nkhani ya ukwati, ntchito, kapenanso kuwonjezera utumiki wanu, musazengereze kumuuza Mulungu ndi kumupempha kuti akutsogolereni. Mwachitsanzo, mtsikana wina ku Philippines ankafuna kuchita nawo utumiki wa nthawi zonse koma sakanatha kudzisamalira chifukwa sanali pantchito. Iye anati: “Tsiku lina Loweruka, ndinapemphera kwa Yehova n’kunena mwachindunji kuti ndikufuna kuchita upainiya. Tsiku lomwelo ndikulalikira, ndinagawira buku kwa mtsikana wina. Ndiye ndinadabwa kumva mtsikanayo akundiuza kuti: ‘Mudzabwere kusukulu kwathu Lolemba m’mawa.’ Ndiye ndinam’funsa kuti, ‘Ndidzatani?’ Iye anandiuza kuti kusukuluko akufuna munthu mwamsangamsanga woti am’lembe ntchito. Nditapita anandilemba ntchito nthawi yomweyo. Zonsezi zinachitika mosayembekezereka.” Mboni zambirimbiri padziko lonse zakumanapo ndi zoterezi. Motero, musazengereze kumuuza Mulungu madandaulo anu mochokera pansi pa mtima.
Nanga Bwanji Tikachimwa?
14, 15. (a) N’chifukwa chiyani munthu sayenera kusiya kupemphera ngakhale atachimwa? (b) Kupatulapo kupemphera payekha, kodi n’chinthu chinanso chiti chomwe chingathandize munthu amene wachimwa?
14 Kodi pemphero lingathandize bwanji ngati munthu wachimwa? Chifukwa cha manyazi, anthu ena akachimwa amasiya kupemphera. Komatu zimenezi si nzeru zabwino ayi. Mwachitsanzo: Oyendetsa ndege amadziwa kuti akasochera m’mwambamo, angathe kulankhulana ndi anthu amene ali pansi, omwe amathandiza ndege makamaka zikamanyamuka ndi kutera. Komano kodi chingachitike n’chiyani ngati woyendetsa ndege atazengereza kulankhulana ndi anthu amenewa chifukwa chochita manyazi kuti wasochera? Ndithu pangachitike ngozi! Ndi mmenenso zimakhalira munthu akachimwa n’kumachita manyazi kulankhulana ndi Mulungu, munthuyo amadziika m’mavuto ena. Kuchita manyazi chifukwa chochimwa kusamachititse munthu kusiya kulankhulana ndi Yehova. Ndipotu Mulungu amalimbikitsa anthu amene achita machimo akuluakulu kuti apemphere kwa iye. Mneneri Yesaya analimbikitsa ochimwa m’nthawi yake kuti apemphere kwa Yehova powauza kuti: “Iye adzakhululukira koposa.” (Yesaya 55:6, 7) N’zoona kuti wochimwayo amafunika ‘kupepesa Yehova’ pokonza kaye mtima wake, kusiya tchimolo, ndi kulapa mochokera pansi pa mtima.—Salmo 119:58; Danieli 9:13.
15 Pali chifukwa chinanso chimene pemphero lilili lofunika munthu akachimwa. Wophunzira Yakobo ananena mawu otsatirawa pankhani ya munthu wofunika thandizo lauzimu. Iye anati: “Adziitanire akulu a mpingo, ndipo apemphere pa iye, . . . ndipo Ambuye adzamuukitsa.” (Yakobo 5:14, 15) Inde, munthu ayenera kuulula yekha tchimo lake kwa Yehova, koma angathenso kupempha akulu kuti amupempherere. Zimenezi zingam’thandize kuchira mwauzimu.
Mayankho a Mapemphero
16, 17. (a) Kodi Yehova amayankha bwanji mapemphero? (b) Ndi nkhani ziti zimene zikusonyeza kuti ntchito yolalikira imayendera limodzi ndi pemphero?
16 Kodi mapemphero amayankhidwa bwanji? Ena amayankhidwa mwamsanga ndiponso moonekeratu. (2 Mafumu 20:1-6) Ena amatenga nthawi ndipo mayankho ake amakhala ovuta kuona. Monga mmene Yesu anasonyezera m’fanizo la mkazi wamasiye amene anapita kwa woweruza mobwerezabwereza, tingafunike kum’fikira Mulungu mobwerezabwereza. (Luka 18:1-8) Komabe tisakayike kuti tikamapemphera mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, n’zosatheka Yehova kutiuza kuti: ‘Usandivute.’—Luka 11:5-9.
17 Anthu a Yehova aona mapemphero awo ambiri akuyankhidwa. Zimenezi zimachitika kwambiri pautumiki wathu wakumunda. Mwachitsanzo, alongo awiri achikristu ku Phillipines ankagawira mabuku ofotokoza Baibulo m’dera lakumidzi la dzikoli. Atapatsa mayi wina kapepala kofotokoza Baibulo, mayiyo misozi inalengeza m’maso. Iye anati: “Dzulo usiku ndinapemphera kuti Mulungu anditumizire munthu kudzandiphunzitsa Baibulo, ndipo sindikukayika kuti limeneli ndi yankho la pemphero langalo.” Posakhalitsa, mayiyo anayamba kupita kumisonkhano ku Nyumba ya Ufumu. M’chigawo china kum’mwera cha kum’mawa kwa Asia, mbale wina ankachita mantha kulalikira m’dera linalake limene muli chitetezo chokhwima. Komabe iye anapemphera kwa Yehova ndipo analimba mtima n’kufika panyumba ina m’deralo. Atafika pakhomo loyamba la nyumbayo, anagogoda ndipo munatuluka mtsikana. Mbaleyo atalongosola chimene wabwerera, mtsikanayo anayamba kulira. Anati wakhala akufunafuna a Mboni za Yehova ndipo anapemphera kwa Mulungu kuti am’thandize kuwapeza. Mbaleyo anasangalala kwambiri kuthandiza mtsikanayo kupezana ndi anthu a mpingo wa Mboni za Yehova m’deralo.
18. (a) Kodi tizitani mapemphero athu akayankhidwa? (b) Ngati timagwiritsa ntchito bwino mpata uliwonse wopemphera tisamakayikire za chiyani?
18 N’zoona kuti pemphero ndi mphatso yamtengo wapatali zedi. Yehova n’ngokonzeka kumva mapemphero athu ndi kuwayankha. (Yesaya 30:18, 19) Koma tiyenera kukhala maso kuti tione mmene Yehova akuyankhira mapemphero athu. Nthawi zina sawayankha monga mmene tikuganizira. Komabe tikaona kuti iye ndiye wayendetsa zinthu, tisamaiwale kum’thokoza ndi kum’tamanda. (1 Atesalonika 5:18) Komanso, nthawi zonse tizikumbukira mawu a mtumwi Paulo otilimbikitsa, akuti: “M’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.” Inde, gwiritsani ntchito bwino mpata uliwonse polankhulana ndi Mulungu. Potero, mudzaona kuti zimene Paulo ananena zokhudza anthu amene mapemphero awo amayankhidwa n’zoonadi. Iye anati: “Mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu.”—Afilipi 4:6, 7.
Kodi Mungayankhe?
• Kodi mapemphero athu angakhale a mitundu yotani?
• Kodi tiyenera kupemphera motani?
• Kodi tingatchule nkhani zotani m’mapemphero athu?
• Kodi pemphero limathandiza bwanji munthu akachimwa?
[Zithunzi patsamba 29]
Kupemphera mochokera pansi pa mtima kumatithandiza kusagonja tikakumana ndi ziyeso
[Zithunzi patsamba 31]
Kudzera m’pemphero, timathokoza Mulungu, kumuuza nkhawa zathu, ndiponso zopempha zathu