“Mphamvu Yoposa Yachibadwa”
KODI ndimavuto ochuluka motani amene Mkristu angapirire? Lerolino, Akristu kuzungulira padziko lonse amayang’anizana ndi umphaŵi, kusŵeka kwa banja, kuchita tondovi, utenda, nkhondo, ndi mazunzo. Kodi nkwanzeru kuwayembekezera kusunga umphumphu mosasamala kanthu za zonsezi? Mtumwi Paulo anati kunalidi tero. Iye analemba kuti ‘Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.’—Afilipi 4:13.
Mbiri yasonyeza kuti nyonga yochokera kwa Yehova iridi yokwanira kuchitira zinthu zonse. Mwachitsanzo, mkati mwa ulamuliro wa Nazi m’Jeremani, Mboni za Yehova zinakumana ndi chizunzo chankhanza. Kodi izo zinapirira? Bukhu lakuti Les Bibelforscher et le nazisme (Ophunzira Baibulo ndi Chinazi) limati: “Mosasamala kanthu za kumenyedwa konseko, ziwopsezo, ndi ziletso, mosasamala kanthu ndi kunyazitsidwa poyera, kuponyedwa m’ndende ndi kumangidwa m’misasa yachibalo, Ophunzira Baibulo [Mboni za Yehova] sanadzilole konse ‘kuphunzitsidwanso.’”
M’misasa yachibaloyo, Mbonizo zinazindikiridwa ndi kachizindikiro kobiriŵira kambali zitatu koikidwa pamalaya awo ndipo zinasankhulidwamo kukazunzidwa mwapadera. Kodi zimenezo zinazilefula? Bruno Bettelheim, katswiri wa zamaganizo ananena kuti izo “modabwitsa sizinangosonyeza ulemu waukulu waumunthu ndi kudzisungira mwamakhalidwe, koma zinawonekera kukhala zotetezeredwa ku zokumana nazo zimodzimodzizo zimene mwamsanga zinawononga anthu olingaliridwa kukhala ogwirizana bwino lomwe ndi mabwenzi anga openda maganizo ndi inemwini.”
Inde, zinali ‘zokhoza zonse.’ Chifukwa? Chifukwa chakuti zinadalira Yehova. Paulo anati: ‘Tiri nacho chuma ichi m’zotengera zadothi, kuti [mphamvu yoposa yachibadwa ikhale ya Mulungu osati yochokera mwa ife, NW].’ (2 Akorinto 4:7) Pamene mukumana ndi mkhalidwe wopereka chiyeso, dalirani Yehova motsimikizirika kuti mupeze chithandizo. Mutalimbikitsidwa ndi mphamvu yoposa yachibadwa imene amapereka, mudzakhoza kupirira.—Luka 11:13.