Kodi Mungazime Nyali Yofuka?
YESU KRISTU analalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwa anthu a mitundu yonse. Ambiri a iwo anali oponderezedwa, olefuka. Koma Yesu anawapatsa uthenga wolimbitsa mtima. Iye anali ndi chifundo pa anthu ovutika.
Wolemba Uthenga Wabwino Mateyu anatchula za chifundo cha Yesu mwa kusonya ku ulosi wolembedwa ndi Yesaya. Kugwira mawu omwe anakwaniritsidwa ndi Kristu, Mateyu analemba kuti: “Bango lophwanyika sadzalityola, ndi nyali yofuka sadzaizima, kufikira iye adzatumiza chiweruzo chikagonjetse.” (Mateyu 12:20; Yesaya 42:3) Kodi mawuŵa amatanthauzanji, ndipo kodi ndi motani mmene Yesu anakwaniritsira ulosi umenewu?
Kupenda Ulosiwo
Kaŵirikaŵiri bango limamera m’matenjetenje ndipo si chomera cholimba. “Bango lophwanyika” lingakhale lofooka kwenikweni. Motero kukuoneka kuti likuimira anthu oponderezedwa kapena anthu ovutika monga mwamuna wa dzanja lopuwala amene Yesu anachiritsa pa Sabata. (Mateyu 12:10-14) Koma bwanji ponena za nyali yogwiritsiridwa ntchito muulosi umenewu?
M’zaka za zana loyamba C.E. nyali yofala ya m’nyumba inali kambiya kakang’ono kadothi kokhala ndi chogwirira. Nyaliyi kaŵirikaŵiri inali kudzazidwa ndi mafuta a azitona. Chingwe chinkakoka mafutawo pamwamba kudyetsera laŵi. Indetu, “nyali yofuka” ingakhale ija imene ili pafupi kuzima.
Yesu analengeza uthenga wake wotonthoza kwa anthu ambiri amene mophiphiritsira anali ngati bango lophwanyika, lofota ndi lomakunthidwa. Anthu ameneŵa analinso ngati nyali yofuka chifukwa chakuti mphamvu yawo ya moyo yotsala inali pafupi kuzima. Iwo analidi oponderezedwa ndi olefuka. Komabe, Yesu sanatyole bango lophwanyika lophiphiritsira kapena kuzima nyali yofuka yophiphiritsira. Mawu ake achikondi, ofeŵa, ndi achifundo sanawonjezere kulefuka ndi kupanikizika kwa anthu ovutika. M’malo mwake, mawu ake ndi mmene anachitira nawo zinawalimbikitsa.—Mateyu 11:28-30.
Lerolinonso, ambiri afunika kuwachitira chifundo ndi kuwalimbikitsa chifukwa akuyang’anizana ndi mavuto olefula mtima. Ngakhale atumiki a Yehova samakhala olimba nthaŵi zonse. Nthaŵi zina iwo amafanana ndi nyali zofuka. Motero Akristu ayenera kukhala olimbikitsa—kuuzirira moto, titero kunena kwake—motero akumalimbikitsana wina ndi mnzake.—Luka 22:32; Machitidwe 11:23.
Monga Akristu tikufuna kukhala omangirira. Sitimayesa dala kufooketsa aliyense wofuna chithandizo cha kuuzimu. Ndithudi, timafuna kutsanza chitsanzo cha Yesu pa kulimbikitsa ena. (Ahebri 12:1-3; 1 Petro 2:21) Chifukwa chabwino choganizirira mwakuya ponena za mmene timachitira ndi ena nchakuti tingathe kutyola mosadziŵa aliyense wodza kwa ife kaamba ka chilimbikitso. Mosakayikira sitikufuna ‘kuzima nyali yofuka.’ Kodi ndi zitsogozo za Malemba zotani zimene zingatithandize pankhaniyi?
Ziyambukiro za Kusuliza
Ngati Mkristu ‘agwidwa nako kulakwa kwakuti, awo auzimu, ambweze wotereyo mu mzimu wa chifatso.’ (Agalatiya 6:1) Komabe, kodi kungakhale koyenera kufunafuna zolakwa za ena ndi kugwiritsira ntchito mpata uliwonse kuwawongolera? Kapena kodi kungakhale bwino kuwakankha kuti achite bwinopo mwa kuwasonyeza kuti kuyesayesa kwawo kumene akupanga nkosakwanira, mwinamwake kuwachititsa kukhala ndi malingaliro a liwongo? Palibe umboni woti Yesu anachita zoterezi. Ngakhale kuti kuthandiza ena kuwongolera kungakhale chifuno chathu, awo osulizidwa mopanda chifundo angalefulidwe m’malo mwa kulimbikitsidwa. Ngakhale kusuliza koyenera kungakhale kolefula ngati kuchitidwa mopambanitsa. Ngati zoyesayesa zabwino koposa za Mkristu wakhama zingosulizidwa, mwinamwake iye angasiye ndi kunena kuti, ‘Nkuyeseranji nkomwe?’ Ndithudi, akhoza kunyanyaliratu zonse.
Pamene kuli kwakuti kupereka uphungu wa m’Malemba nkofunika, sindiwo mzimu umene akulu oikidwa kapena ena mumpingo ayenera kudziŵika nawo. Misonkhano ya Chikristu kwenikweni simakhalapo kaamba ka kupereka ndi kumvetsera uphungu. M’malo mwake, timakumana nthaŵi zonse kuti timangirirane ndi kulimbikitsana wina ndi mnzake kotero kuti onse asangalale ndi mayanjano awo ndi utumiki wawo wopatulika kwa Mulungu. (Aroma 1:11, 12; Ahebri 10:24, 25) Zimakhala bwino chotani nanga pamene tizindikira kusiyana pakati pa kulakwa kwakukulu ndi kuphophonya chabe kumene mwa nzeru ndi mwa chikondi tinganyalanyaze!—Mlaliki 3:1, 7; Akolose 3:13.
Anthu amamva chilimbikitso mwamsanga kuposa kusuliza. Kwenikweni, pamene anthu aona kuti asulizidwa mosayenerera, iwo angaumirire zolimba khalidwe losulizidwalo! Koma pamene ayamikiridwa moyenerera, iwo amalimbikitsidwa, ndipo zimawasonkhezera kuwongolera. (Miyambo 12:18) Chifukwa chake monga Yesu, tiyeni tikhale olimbikitsa ndipo ‘tisazime nyali yofuka.’
Bwanji Ponena za Kuyerekezera?
Kumvetsera zokumana nazo zabwino za Akristu ena kungakhale kosonkhezera kwambiri. Yesu iyemwini anasangalala pamene anamva za chipambano cha ophunzira ake polalikira uthenga wa Ufumu. (Luka 10:17-21) Mofananamo, pamene timva za chipambano, chitsanzo chabwino, kapena umphumphu wa okhulupirira anzathu, timalimbikitsidwa ndipo timakhala otsimikiza kwambiri kusachoka panjira yathu ya Chikristu.
Komabe, bwanji ngati nkhani ina yasimbidwa m’njira yonga ngati yonena kuti, ‘Simungapambane Akristu ameneŵa, ndipo muyenera kuchita bwino kuposa mmene mukuchitira’? Kodi womvetsera mwachionekere angapange makonzedwe amphamvu a kuwongolera? Nkotheka kuti angalefulidwe ndipo mwinamwake kusiya, makamaka ngati kaŵirikaŵiri pamakhala kuyerekezera kapena kupereka chithunzi chotero. Zimenezi zingafanane kwenikweni ndi kholo lofunsa mwana wake kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji sungakhale ngati mbale wako?’ Mawu ameneŵa angachititse kuipidwa ndi kulefulidwa, koma sangalimbikitse nkomwe akhalidwe labwinopo. Kuyerekezera kungakhale ndi zotulukapo zofananazo pa achikulire, ngakhale kuwachititsa kuipidwa m’njira ina ndi awo amene amawayerekezera nawo.
Sitingayembekezere onse kugwira ntchito mofanana mu utumiki wa Mulungu. M’fanizo lina la Yesu, mbuye wina anapatsa akapolo ake talente limodzi, matelente aŵiri, kapena asanu a siliva. Ameneŵa anapatsidwa “kwa iwo onse monga mwa nzeru zawo.” Akapolo aŵiri amene anachita malonda mwanzeru ndi kuchulukitsa matalente awo anawayamikira chifukwa anali okhulupirika, ngakhale kuti ntchito zawo zinali ndi zotulukapo zosiyana.—Mateyu 25:14-30.
Mtumwi Paulo moyenerera analemba kuti: “Koma yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.” (Agalatiya 6:4) Motero, kuti tikhaledi olimbikitsa kwa ena, tiyenera kuyesayesa kupeŵa kuyerekezera koipa.
Njira Zina Zomangiririra
Kodi tingachite motani kuti tilimbikitse olefuka ndi kupeŵa ‘kuzima nyali yofuka’? Chabwino, kupereka chilimbikitso sikuchita kufuna kulondola njira yoikika. Komabe, nkwachionekere kuti mawu athu adzalimbikitsa ena ngati tigwiritsira ntchito miyezo ya Baibulo. Kodi ina ya iyo ndi iti?
Khalani Wodzichepetsa. Pa Afilipi 2:3, Paulo anatilangiza ‘kusachita kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake.’ M’malo mwake, tiyenera kulankhula ndi kuchita modzichepetsa. ‘Ndi kudzichepetsa mtima tiyenera kuyesa anzathu otiposa ife eni.’ Paulo sananene kuti tiyenera kudziyesa opanda pake. Komabe, tiyenera kuzindikira kuti munthu aliyense ngwotiposa m’njira ina yake. Liwu la Chigiriki pano lotembenuzidwa kuti “omposa” limapereka lingaliro lakuti munthu “samayang’ana pa ubwino wake, ndipo amalingirira mosamala za mikhalidwe ya wina imene amamposa nayo.”(New Testament Word Studies, yolembedwa ndi John Albert Bengel, Voliyumu 2, tsamba 432) Ngati tichita zimenezi ndi kuyesa ena kukhala otiposa, tidzachita nawo mofatsa.
Sonyezani Ulemu. Mwa kunena malingaliro athu moona mtima, tingamveketse bwino kuti tili ndi chidaliro mwa alambiri okhulupirika anzathu, tikumawaona monga anthu okhumba kukondweretsa Mulungu. Koma tinene kuti afunika chithandizo cha kuuzimu. Pamenepo tiyeni tipereke chithandizocho m’njira yaulemu. Paulo anati: “Mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.”—Aroma 12:10.
Khalani mvetseri wabwino. Inde, kuti tilimbikitse awo amene akuyang’anizana ndi mavuto olefula, tifunikira kukhala amvetseri abwino, osati aphungu. M’malo mwa kupereka malingaliro a msangamsanga ndi apatalipatali, tiyeni tidekhe ndi kupereka zitsogozo za Malemba zimene zidzathandizadi pa mavuto omwe alipowo. Ngati sitikudziŵa zonena, kufufuza za m’Baibulo kudzatithandiza kulankhula motonthoza ndi kulimbikitsa ena.
Khalani achikondi. Awo amene tifuna kulimbikitsa tiyenera kuwakonda. Pamene tisonyeza chikondi chathu kwa atumiki anzathu a Yehova, chiyenera kupyola pa kungowachitira zabwino. Chiyenera kuchoka pansi pa mtima. Ngati tili ndi chikondi chotere pa anthu onse a Yehova, mawu athu adzakhala olimbikitsa kwambiri kwa iwo. Ngakhale pamene tidzafunikira kupereka lingaliro la kuwongolera, mwachionekere zimene tidzanena sizidzatengedwa m’njira ina kapena kuwononga zinthu ngati chifuno chathu sindicho kungonena malingaliro athu koma kupereka thandizo lachikondi. Monga momwe Paulo ananenera momvekera bwino kuti, “chikondi chimangirira.”—1 Akorinto 8:1; Afilipi 2:4; 1 Petro 1:22.
Nthaŵi Zonse Khalani Omangirira
Mu “masiku otsiriza” ano oŵaŵitsa, anthu a Yehova akuyang’anizana ndi mayesero ambiri. (2 Timoteo 3:1-5) Nchifukwa chake nthaŵi zina amavutika mpaka pamene pamaoneka ngati pamalekezero a chipiriro chawo. Monga atumiki a Yehova, moona sitimafuna kunena kapena kuchita zinthu zimene zingachititse alambiri anzathu kudzimva ngati nyali zofuka zimene zili pafupi kuzima.
Motero, nkofunika chotani nanga kuti tilimbikitsane wina ndi mnzake! Tiyeni tiyeseyese mulimonse mmene tingathere kukhala omangirira mwa kukhala odzichepetsa ndi aulemu kwa alambiri anzathu olefuka. Pamene atiuza za kukhosi timvetsetsetu mosamala ndi kuyesayesa nthaŵi zonse kuwathandiza mwa kuwasonyeza Mawu a Mulungu, Baibulo. Koposa zonse, tiyeni tisonyeze chikondi, popeza chipatso cha mzimu woyera wa Yehova chimenechi chidzatithandiza kulimbikitsana wina ndi mnzake. Tisalankhuletu kapena kuchita mwa njira iliyonse imene ‘ingazime nyali yofuka.’