Sonyezani Chikondwerero Chaumwini mwa Ena
“Munthu yense asapenyerere zake za iye yekha komanso apenyerere za mnzake.”—AFILIPI 2:4.
1, 2. Kodi nziti zimene ziri zifukwa zina zosonyezera chikondwerero chaumwini mwa ena?
TIRI ndi zifukwa zabwino za kusonyezera chikondwerero chaumwini mwa ena. Mwachitsanzo, anthu anzathu ayenera kutikondweretsa chifukwa timasiyana wina ndi mnzake. Mkhalidwe wa kapangidwe wa maselo a thupi lathu umakhala ndi kapangidwe kathu kachibadwa. Iko kali kosiyana kotero kuti nthumwi zofufuza upandu zawonjezera mkhalidwe wa “kapangidwe” ku ndandanda yawo ya njira zodziŵira zinthu.
2 Palinso zifukwa zina zimene timasiyanirana ndipo nzosangalatsa monga munthu payekha. Kuyambira pa kutenga mimba, timakhudzidwa ndi chisonkhezero cha malo otizinga. Pali umboni wokulira wakuti ana osabadwa amavomereza ku zomwe zimachitika kunja kwa mimba. Kenaka, pambuyo poloŵa m’dziko monga odziimira patokha okhoza kupuma, kapena miyoyo, mkhalidwe ndi njira za makolo athu zimatiyambukira. Pamene tikukula, tingakhale mwana yekha kapena tingakhale ndi abale ndi alongo ndi kukhalako ndi mbali m’kuwasamalira. Kuyanjana koteroko kapena kusoŵeka kwake kuli ndi chiyambukiro pa kakulidwe kathu. Zimene timaŵerenga, kuphunzira ku sukulu, ndi kupenyerera pa wailesi yakanema zimayambukiranso zolingalira ndi zochita zathu.
3. M’chigwirizano ndi Afilipi 2:4, kodi ndi chikondwerero chotani chimene tiyenera kukhala nacho mwapadera mwa ena?
3 Chotero, kusiyana kwathu kumakulitsa chikondwerero mwa ena. Komatu mtumwi Paulo anakumbukira chifukwa china chachikulu cha kukhalira ndi chikondwerero mwa ena. Chotero, iye anafulumiza Akristu anzake ‘kusapenyerera zake za iye yekha, koma kupenyereranso za mnzake.’ (Afilipi 2:4) M’malo mofunafuna mwaŵi wathu wokha, tiyenera kukondweretsedwa mwapadera mu uzimu wa ena. Pamenepa, kodi nziti zimene ziri njira zina zimene timasonyezera chikondwerero chaumwini choterocho mwa ena?
Zikondwerero Zauzimu ndi Kusiyana kwa Umunthu
4. Mogwirizana ndi Aefeso 4:22-24, kodi ndi masinthidwe otani amene amakulitsa chikondwerero chathu chauzimu mwa ena?
4 Chikondwerero chathu chauzimu mwa ena chimakulitsidwa pamene mwaumwini timagwiritsira ntchito chidziŵitso Chamalemba ndi kuphunzira kutsanzira chitsanzo cha Yesu Kristu. (1 Petro 2:21) Monga Akristu owona, tiyenera ‘kuvula umunthu wakale umene ugwirizana ndi njira yanu yakale ya khalidwe’ ndi kugwirira ntchito pa kuuloŵa m’malo ndi “umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi kukhulupirika.” (Aefeso 4:22-24, NW) Chotero, mikhalidwe yadyera imaloŵedwa m’malo ndi kudera nkhaŵa kwachikondi, kolingalirika kaamba ka ena.—Yesaya 65:25.
5. Kodi nchifukwa ninji pali kusiyana kwa maumunthu mu mpingo Wachikristu, kudzutsa funso lotani?
5 Ngakhale kuti kusintha kwa umunthu kwakhala kozizwitsa pakati pa anthu za Yehova, zikhoterero zochimwa zimatsalabe. Ngakhale Paulo anavomereza kuti: “Pamene ndifuna kuchita chabwino, choipa chiriko.” (Aroma 7:21) Ndithudi, pali mikhalidwe ina yobadwa nayo ndi yotengera, ndipo iyi imatizindikiritsa ife. Ena ali ndi luso la kupanga zinthu, ena ali ndi nzeru ya kusanthula. Pamene kuli kwakuti ena ngwofatsa ndi osamasuka, ena ngamayanjano ndi okonda kucheza. Pamenepa, kodi umodzi wa mpingo Wachikristu ungasungidwe motani pakati pa kusiyana kwa umunthu koteroko?
6. Kodi ndimotani mmene tiyenera kuwonera kusiyana kwa umunthu, ndipo kodi ndimotani mmene mungachitire chitsanzo chimenechi?
6 Kuti tisonyeze chikondwerero chaumwini mwa ena ndi kusungabe umodzi Wachikristu, tiyenera kukhala otsimikiza ndi omvetsetsa. Popeza kuti Mulungu samafuna ungwiro kuchokera kwa ife, sitiyenera kuufuna kuchokera kwa Akristu anzathu. Kuwonjezerapo, Yehova samayembekeza kuti atumiki ake onse akhale ofanana ndendende. Mu mpingo Wachikristu, tonsefe tiri ndi malo ndipo tingagwiritsire ntchito maluso athu obadwa nawo, opatsidwa ndi Mulungu kupititsa patsogolo ntchito yake. (1 Akorinto 12:12-26) Ngati tikhala otanganidwa kugwira ntchito pansi pa Mutu wa mpingo, Yesu Kristu, sitidzakhala ndi nthaŵi ya kuyang’ana anzathu mowasuliza. (1 Akorinto 4:1-4) Monga mmene wopanga zosemasema amadziŵira, chipangizo chirichonse chinapangidwira ntchito yake. Kodi nyondo ingapange chiboo chabwino chimene choboolera chimapanga? Kodi chopalira chogwiritsidwa ntchito kupalira matabwa chingakhomerere bwino msomali? Ayi, popeza kuti chipangizo chirichonse chiri ndi ntchito yake yoyenerera.
7. Pamene tikugawanamo chapamodzi mu utumiki wa Ufumu, kodi nchiyani chimene tiyenera kusunga m’maganizo koposapo?
7 Ngwowona chotani nanga mawu a nyimbo Yaufumu yakuti “Utumiki Wosangalatsa”! Imatifulumiza kuti: “Mokondwa titumikire Mfumu’yo, podza nazo mphatso ku ntchito yake.” Zowona, tingakhale tiribe luso lokhumbirika. Komabe, timaika ntchito imene tagaŵiridwa monga Mboni za Yehova m’malo oyamba m’maganizo ndipo timadzipereka ife eni ku iyo ndi mtima wonse. Monga mmene nyimboyo ikuwonjezera kuti: “Nkana utumiki’wo ukachepa, chikondi chathu chikuwonekera.”—“Kuyimba ndi kutsagana ndi nyimbo za malimba m’mitima mwanu,” nyimbo 58.
Onani Ena Kukhala Okuposani
8. Kodi umodzi umachilikizidwa motani mwa kugwiritsira ntchito zimene Paulo ananena pa Afilipi 2:1-3?
8 Umodzi umachilikizidwanso mwa kulingalira ena kukhala okuposani. Paulo adalemba kuti: “Ngati tsono muli chitonthozo mwa Kristu, ngati chikhazikitso cha chikondi, ngati chiyanjano cha mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni, kwaniritsani chimwemwe changa, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala nacho chikondi chomwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi.” Onani kuti mtumwiyo akuwonjezera kuti: “Musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini.”—Afilipi 2:1-3.
9. Kodi kukhala wopikisanitsa ndi wotsata ulemerero wopanda pake kumatanthauzanji, ndipo kodi tingapeŵe motani zikhoterero zimenezi?
9 Posalingalira ena kukhala omposa, munthu wopikisanitsa amasonyeza “chikhoterero choipa kaŵirikaŵiri ndipo chotopetsa cha kukangana ndi kuyambana.” (Webster’s New Collegiate Dictionary) Chikhoterero chimenechi chingamawonekere mu “makani a mawu.” (1 Timoteo 6:4) Ndithudi, cholinga cha mawu ndi maganizo otulutsidwa chiyenera kukhala chodera nkhaŵa chachikulu. Chotero peŵani kukhala m’tsanziri wopambanitsa wa mawu ogwiritsidwa ntchito polankhula kapena m’zinthu zolembedwa. Ndipo kodi bwanji ngati lingaliro losiyana la chikhulupiriro chinachake labweretsedwa kwa inu? Mokhulupirika mamatirani ku chidziŵitso Chamalemba choperekedwa ndi Mulungu kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Ndiiko nkomwe, mmenemo ndi mmene tinaphunzirira chowonadi poyambapo. Kuzindikira zimenezi kumatithandiza kupeŵa kukhala ndi ulemerero wopanda pake, uku ndiko kuti, kudzimva kukhala wofunika mopambanitsa.
Kulitsani Chikondwerero Chaumwini mwa Ena
10. Kodi ndi kugwiritsira ntchito kotani kwa Afilipi 2:4 kumene kuyenera kupangidwa mu mpingo?
10 Kumbukirani kuti Paulo akutifulumiza ‘kusapenyerera zathu zokha, koma kupenyereranso za ena.’ (Afilipi 2:4) Kodi izi zimatanthauzanji? Mongadi mmene kuwona zotizinga kungatithandizire mu uminisitala wakumunda, momwemonso kusonyeza chikondwerero mu ubwino wa ena mu mpingo kudzatipatsa mwaŵi wa kulimbitsa chomangira cha chikondi chimene chimatigwirizanitsa. Akulu ali ndi thayo lapadera la kusonyeza kudera nkhaŵa kaamba ka akhulupiriri anzawo, popeza kuti mwambi umati: “Udziwitsitse zoŵeta zako ziri bwanji.” (Miyambo 27:23) Ndithudi, tonsefe tingathe ndipo tiyenera kukhala omvetsera ku zosoŵa za akhulupiriri anzathu.—1 Petro 2:17.
11. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala otchera khutu pamene tikulankhula kwa abale ndi alongo athu auzimu?
11 Njira ina yopititsira patsogolo umodzi ndi kukulitsa chikondwerero mwa ena ndiyo kutenga nthaŵi ya kulankhulana bwino ndi abale ndi alongo anu auzimu. Dziŵani zimene akulingalira. Izi zingachitidwe pamene muchezera nyumba zawo, kuchiyambi ndi pamapeto pa misonkhano pa Nyumba Yaufumu, ndi pakati pa zigawo pa misonkhano yathu. Ndipo mvetserani mosamalitsa pamene akulankhula. Izi zikatanthauza kuti tikamva mavuto amene akuyang’anizana nawo, komabe tingakhale okhoza kuthandiza kunyamula katundu wawo ndipo chotero kukwaniritsa lamulo la Kristu. (Agalatiya 6:2) Komabe, chinachake chofunika kuposa kulankhula ndi abale athu chidzachinjiriza umodzi wa mpingo. Kodi icho nchiyani?
Sonyezani Chifundo cha pa Mnansi
12. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kusonyeza chifundo cha pa mnansi?
12 Chifundo cha pa mnansi chimapititsanso patsogolo umodzi Wachikristu. Pokhala ndi zididikizo zomawonjezeka za moyo, tonsefe timafunikira kusonyeza mkhalidwe umenewu. Lolani kuti tisakhale nkomwe owumirira pa zimene tiri nazo m’maganizo kotero kuti tilephere kulingalira malingaliro a ena. Monga chitsanzo: Pamene wotengamo mbali m’programu ya Msonkhano Wautumiki anangofika kumene, mkulu analankhula naye mwamsanga ponena za nkhani ina imene inafunikira kulengezedwa. Ku kudabwitsidwa ndi kuchititsidwa manyazi kwa mkuluyo, wotengamo mbaliyo anamuyang’ana, kumwetulira, ndi kunena kuti: “Choyamba, mwaswera bwanji Mbale!” Nkhani yofunika kulengezedwayo inakambitsiridwa pambuyo pa kupatsana moni kwaubwenzi ndipo mbaleyo anapumitsidwa. Mkuluyo anaphunzira phunziro lotani nanga! Musamakhala wofulumira kwenikweni, mwakutero mukumaiŵala zinthu za nthaŵi zonse zimene zimapanga unansi wanu ndi ena kukhala wosangalatsa.
13. Kodi chifundo cha pa mnansi chimafulumiza akulu kuchita chiyani pochita ndi Akristu anzawo?
13 Chifundo cha pa mnansi chimafulumiza akulu kusonyeza chifundo ndi zikhoterero zina zabwino. Nthaŵi zina, amuna ameneŵa ayenera kukhala ofatsa, “monga mmene mlezi afukata ana ake a iye yekha.” (1 Atesalonika 2:7) Kuthandiza anthu ena kumafunikira kuleza mtima ndi chilikizo lachikondi. Awo amene ataya ‘chikondi chimene anali nacho poyamba’ angafunikire kusonkhezeredwa ku ntchito yokulira ndipo angafunikire thandizo kuti ayamikire kufulumira kwa nthaŵi zathu. (Chibvumbulutso 2:4; 2 Timoteo 4:2; Ahebri 6:11, 12) Mofanana ndi Paulo, akulu ali ndi “chikondi chokoma mtima” kwa Akristu oyanjana nawo, kuwachenjeza ndi kuwatonthoza ‘ndi cholinga chakuti muyenera kupitirizabe kuyenda moyenera Mulungu.’—1 Atesalonika 2:8, 11, 12.
14. Kodi ndi umboni wotani umene Paulo anapereka wakuti anali ndi chifundo cha pa mnansi?
14 Paulo anasiyira akulu chitsanzo chabwino cha kusonyezera chikondi chokoma mtima kaamba ka ubwino wa abale ndi alongo auzimu. Iye analemba kuti: “Popanda zakunjazo pali chosindikiza tsiku ndi tsiku, chilabadiro cha mipingo yonse.” Popeza kuti Paulo anali ndi kudera nkhaŵa koteroko, iye akatha kufunsa kuti: “Afooka ndani wosafooka inenso? Akhumudwitsidwa ndani, wosatenthanso ine?” Ngati ndinu mkulu, kodi muli ndi chifundo cha pa mnansi choterocho?—2 Akorinto 11:28, 29.
Kupindula Mbale Wanu
15. Pamene mavuto aakulu abuka pakati pa abale, kodi ndi uphungu wotani wa Yesu wa pa Mateyu 18:15 umene uyenera kutsatiridwa, ndipo kodi cholinga chake chiyenera kukhala chiyani?
15 Kusonyeza chifundo cha pa mnansi kumapititsa patsogolo umodzi pakati pa atumiki a Yehova. Komabe, pa zochitika za kamodzikamodzi, kusemphana kwaumwini kungabuke. Pamene nkhani zowopsya zaloŵetsedwamo, Akristu ayenera kutsatira uphungu wa Yesu pa Mateyu 18:15-17. Onani sitepi loyambirira. Ndilo kulankhula ndi mbale wanu mwamseri kotero kuti ‘muvumbule chophophonya chake.’ Kodi cholinga chanu chiyenera kukhala chotani? Nkulekeranji, ‘kuti mupindule mbale wanu’! Yesu anati: “Ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.” Mosangalatsa, kulankhula pamodzi mwamseri kaŵirikaŵiri kumakhala kumene kumafunika kuti mubwezeretse unansi wamtendere pakati pa inu ndi mlambiri wa Yehova mnzanu.
16. Kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa ngati mwawona kuti mbale wanu ali ndi mlandu ndi inu?
16 Ngati mwaona kuti mbale wanu ali ndi mlandu ndi inu, tsatirani uphungu wa Yesu wa “kuyanjana ndi mbale wanu.” (Mateyu 5:24) Kambitsiranani nkhaniyo mu mkhalidwe wabata, wachifundo, mukumayesera kumvetsetsa lingaliro la wina ndi mzake. Mwanjira imeneyi, mwinamwake nkhaniyo ingathetsedwe ndipo mtendere wa mpingo ungasungidwe.
Kupindula Osakhulupirira
17, 18. Kodi ndi uphungu wotani umene Petro anapereka kwa akazi Achikristu okhala m’nyumba zogaŵikana mwachipembedzo?
17 Umodzi wa mikhalidwe yovuta kwambiri yogwiritsira ntchito malamulo a makhalidwe abwino Amalemba uli mkati mwa nyumba yogaŵikana mwachipembedzo. Akristu ambiri amagwira ntchito mokhulupirika pamene akuyesera kuchita ndi zokhumudwitsa ndi zovuta zochititsidwa ndi kusoŵeka kwa umodzi wauzimu mu ukwati wawo. Kodi angathandizidwe motani?
18 Chifukwa chosonyeza chikondwerero chaumwini mwa ena, mosangalala akulu amapereka thandizo lauzimu kwa awo okhala m’nyumba zogaŵikana mwachipembedzo. Mwachitsanzo, chisamaliro chingalunjikitsidwe ku uphungu wa Petro wonena za mkhalidwe wa akazi Achikristu amene ali mu vuto loterolo. Iye akuwauza iwo kugonjera kwa amuna awo, ngakhale kuti ndi osakhulupirira ndipo ndi “osamvera mawu.” Kodi nkukhaliranji ogonjera? “Ndi cholinga chakuti . . . iwo akakodwe [kapena, akapindulidwe] popanda mawu kupyolera mwa khalidwe la akazi awo.” (1 Petro 3:1; Kingdom Interlinear) Koma kodi kugwiritsira ntchito uphungu umenewu nkokhutiritsa motani?
19. Perekani chitsanzo chosonyeza phindu la kugwiritsira ntchito 1 Petro 3:1.
19 Mkazi wotchedwa Vera akuvomereza kuti pamene anakhala Mkristu kwa nthaŵi yoyamba, ankalankhula mokhazikika kwa mwamuna wake ponena za chowonadi cha Baibulo, ndipo mwamunayo anatopetsedwa nazo. “Potsatira uphungu Wamalemba wolandiridwa kuchokera kwa mkulu,” iye akuwonjezera kuti, “ndinasankha kuti chikakhala bwino kukhala wochenjera ndi kudikira kaamba ka nthaŵi yabwino.” Kwakukulukulu, Vera anagwiritsira ntchito 1 Petro 3:1, ngakhale kuti anakhala woyamba kuyambitsa mwamuna wake, Barry, kukambitsirana malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo. Pambuyo pake mwamunayo analongosola kuti: “Mkati mwa zakazi, ndawona kuti Galamukani! [magazine inzake ya Nsanja ya Olonda] inawoneka m’malo achilendo m’nyumba. Inali ndi nkhani zothandiza ndipo nthaŵi zina nkhanizo zisanamveke.” Monga chotulukapo, pambuyo pa zaka 20 za kusagwirizana, Barry ndi Vera ali achimwemwe kukhala ogwirizana mu utumiki wa Yehova.
20. Kodi ndi thandizo lotani limene akulu angapereke kwa amuna Achikristu okhala m’nyumba zogaŵikana mwachipembedzo?
20 Mwamuna wokhulupirira amakumana ndi mavuto aakulu ngati mkazi wake ali wotsutsa ku chowonadi Chachikristu ndi kusonkhezera ana awo motsutsana naye. Kusonyeza chikondwerero chaumwini mwa mwamuna woteroyo, akulu angapereke chisamaliro ku malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo. Mwachitsanzo, chingasonyezedwe kuti mosasamala kanthu za chitsutso cha mkazi wake, iye ndiye mutu wabanja ndipo ayenera kuŵapatsa ana ake chilangizo Chamalemba. (Aefeso 6:4) Iye angalimbikitsidwe kukhala ndi mkazi wake “monga mwa chidziŵitso,” kusonyeza chikondwerero mu zimene amachita ndi kumuthandiza ndi ntchito zapanyumba ndi kusamalira ana. (1 Petro 3:7) Pamwamba pa zonse, mwamuna wokhulupirirayo ndi atate ayenera kulimbikitsidwa kusunga njira zolankhulana kukhala zotseguka kotero kuti adziŵe zimene ziri mu mtima mwa chiŵalo chirichonse cha banja lake. Akuluwo angamulimbikitsenso kupitirizabe kuyesera kuthandiza mkazi wake ndi mawu ‘okoleretsedwa ndi mchere,’ mochenjera akumapereka chowonadi Chamalemba kwa mkaziyo pa nthaŵi yoyenera.—Akolose 4:6.
21. Kodi ndimotani mmene mkazi wosakhulupirira angathandizidwire kupeza chikondwerero m’chowonadi?
21 Kusonyeza chikondwerero mwa achibale a Akristu a m’mabanja ogaŵikana mwachipembedzo nthaŵi zina kumadzutsa chivomerezo ku uthenga wa Ufumu. Kuti tichitire chitsanzo: Mwamuna wina Wachikristu anakhumudwitsidwa chifukwa chakuti mkazi wake anakhala akumutsutsa iye mwaukali kwa zaka zambiri. Mkulu anadzipereka kupitako ndi kuthandiza ndi kukambitsirana kwa Baibulo. Akumafika panyumbapo, mkuluyo analonjera mkaziyo mosangalala akumafunsa kuti: “Kodi ungalole kukhala nafe?” Chiitano chaubwenzicho chinasangalatsa mkaziyo kotero kuti mwachimwemwe anagwirizana nawo m’kukambitsiranako. Posakhalitsa analandira chowonadi ndipo anayamba kulalikira kwa ena.
22. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kusonyeza chikondwerero chaumwini mwa wina ndi mnzake?
22 Chotero, monga Mboni za Yehova, tiyeni ‘tichite zonse chifukwa cha uthenga wabwino.’ (1 Akorinto 9:23) Ndithudi, “monga tiri nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) Lolani kuti tisonyeze chikondwerero chaumwini mwa wina ndi mnzake kotero kuti chikondi chichuluke mu ubale wathu wadziko lonse.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji, chimene tiyeneradi kusonyezera chikondwerero mwa ena?
◻ Ndimotani mmene tingakulitsire chikondwerero chaumwini mwa akhulupiriri anzathu?
◻ Ndimotani mmene akulu angasonyezere chifundo cha pa mnansi?
◻ Nchiyani chimene chingatulukepo ngati tisonyeza chikondwerero chaumwini mwa osakhulupirira?
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Monga mmene chipangizo chirichonse chinapangidwira ntchito yake, onse mu mpingo Wachikristu angagwiritsire ntchito maluso awo opatsidwa ndi Mulungu kupititsa patsogolo ntchito ya Mulungu
Kuti mupititse patsogolo umodzi Wachikristu, sonyezani chikondwerero chaumwini mwa ena
[Chithunzi patsamba 18]
Paulo anasiyira akulu chitsanzo chabwino cha mmene angasonyezere kudera nkhaŵa kwachikondi kaamba ka akhulupiriri anzawo