Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Pa Afilipi 2:9 Paulo ananena za Yesu kuti: “Mulungu anamkwezetsa iye, nampatsa dzina limene liposa maina [ena, NW] onse.” Kodi dzina latsopano limeneli nlotani? Ndipo ngati Yesu ali wamng’ono kwa Yehova, kodi dzina la Yesu lili loposa maina ena onse motani?
Afilipi 2:8, 9 amati: “Ndipo popezedwa m’maonekedwe ngati munthu [Yesu], anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pa [mtengo wozunzirapo, NW]. Mwa ichinso Mulungu anamkwezetsa iye, nampatsa dzina limene liposa maina ena onse.”
Chigawo chimenechi sichikutanthauza kuti popeza kuti Yehova ndiye yekha ali ndi dzina limene liposeratu maina ena onse, ndiye kuti Yesu ayenera kukhala munthu mmodzimodziyo amene ali Yehova. Monga momwe mawu a mu nkhani ya chaputala 2 cha Afilipi amasonyezera, Yesu analandira dzina lake lokwezekalo atauka. Zimenezo zisanachitike, analibe dzinalo. Komanso, nthaŵi zonse Yehova wakhala wapamwamba, ndipo malo ake sanasinthe. Kulandira dzina lapamwamba kwenikweniko kwa Yesu, dzina loposa limene anali nalo asanatumikire pa dziko lapansi kumasonyeza kuti iyeyo sali munthu mmodzimodziyo amene ali Yehova. Pamene Paulo ananena kuti Yesu anapatsidwa dzina loposa maina ena onse, anatanthauza kuti tsopano Yesu anali ndi dzina lokwezeka kwambiri pa zolengedwa zonse za Mulungu.
Kodi dzina lokwezeka la Yesulo nlotani? Yesaya 9:6 amatithandiza kuyankha. Polosera za Mesiya, Yesu, amene adzafika vesilo limati: “Ulamuliro udzakhala pa pheŵa lake, ndipo adzamucha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu [W]amphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa [M]tendere.” Pano “dzina” la Yesu nlogwirizanitsidwa ndi malo ake apamwamba ndi ulamuliro, limenenso timalizindikira kukhala “dzina limene liposa maina ena onse” lotchulidwa pa Afilipi 2:9. Bondo lililonse likulamulidwa kupinda kwa Yesu movomereza malo ake apamwamba a ulamuliro umene Yehova wampatsa—malo a ulamuliro wapamwamba koposa kuposa woperekedwa ku cholengedwa chilichonse. Mawu akuti “ena” a m’matembenuzidwe ameneŵa sali m’malembo Achigiriki, koma analembedwa chifukwa cha lingaliro la vesilo. “Dzina” la Yesu silili loposa dzina lake koma lili loposa dzina la cholengedwa china chilichonse.
Tili achimwemwe chotani nanga kugwirizana ndi angelo okhulupirika onse ndi anthu pogwada movomereza dzina la Yesu! Timachita zimenezi mwa kugonjera Yesu wokhala pamalo okwezeka ndi amphamvu operekedwa kwa iye ndi Yehova—“kuchitira ulemu Mulungu Atate.”—Afilipi 2:11; Mateyu 28:18.