Kumatumikira monga Ogwira Ntchito Anzake Okhulupirira a Yehova
“Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chiri chokoma. Ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda kukoma mtima kwa chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?”—MIKA 6:8, NW.
1. Ndi pa maziko a Malemba otani pamene onse a atumiki a Yehova lerolino angatchedwe “antchito anzake”?
MTUMWI Wachikristu Yohane analemba kuti: “Tawonani chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tiri ife otere.” (1 Yohane 3:1) Ndipo mtumwi Paulo ananena za iyemwini ndi mnzake Apolo: “Ndife antchito anzake a Mulungu.” (1 Akorinto 3:9) Ndemanga zonse ziŵiri zimenezi zinapangidwa ndipo zikulankhula ponena za otsarira odzozedwa a Yesu Kristu. Koma m’chenicheni izo zimagwira ntchito kwa atumiki onse owona a Mulungu. Chotero izo zingalembedwenso kuti: ‘Tawonani chikondi Atate watipatsa, kuti tikhale antchito anzake a Yehova.’
2. Nchifukwa ninji chiri chothekera kwa atumiki a Yehova kukhala antchito anzake?
2 Kodi chiri chothekera motani kaamba ka anthu ofooka, opanda ungwiro kukhala antchito anzake a Mlengi wamkulu, yemwe ali wosayerekezeka m’mphamvu ndi nzeru, wangwiro m’chilungamo, ndiponso munthu wa chikondi? Ichi chiri chothekera chifukwa chakuti makolo athu oyambirira anapangidwa m’chifaniziro cha Mlengi ndi wogwira ntchito mnzake, Mawu, kapena Logos. (Genesis 1:26, 27; Yohane 1:1) Chotero makolo athu oyambirira anapatsidwa mlingo wa nzeru, chilungamo, mphamvu, ndi chikondi. Chimenecho ndicho chifukwa chake Yehova akanena kwa atumiki ake a padziko lapansi kupyolera mwa mneneri wake kuti: “Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chiri chokoma. Ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda kukoma mtima kwa chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?”—Mika 6:8, NW.
3. Nchiyani chimene chikusonyezedwa pa Mika 6:8, ndipo nchiyani chimene chikufunika kwa munthu asanakhale mmodzi wa ogwira ntchito anzake a Yehova?
3 Pamene tiŵerenga mawu akuti, “Ndipo Yehova afunanji nawe, . . . ?” chimasonyeza kuti zomwe zimatsatira moyenerera zimafupikitsa bwino thayo la ‘munthu’ kulinga kwa Mulungu ndi anthu anzake. Kuti ndi kumlingo wotani kumene ichi chiridi tero chidzawonekera pamene tipitiriza kukambitsirana kwathu. Ndithudi, si aliyense amene angayende ndi Yehova. Mwaŵi umenewu unasungidwa kwa awo omwe ‘akumana naye mwapangano,’ kunena kwake titero. (Amosi 3:3) Motani? Mwa kupanga kudzipereka kodzipatulira kwa Yehova ndi kusonyeza ichi mwa ubatizo wa m’madzi, monga mmene chasonyezedwera m’nkhani yapita. Chotero, nchiyani chimene Mika 6:8 amatanthauza kwa anthu amenewa?
‘Kuchita Cholungama’
4. Kwakukulukulu, nchiyani chimene chimatanthauza “kuchita cholungama”?
4 Kuti tiyambe, pali chifuno cha “kuchita cholungama.” Monga ogwira ntchito anzake a Yehova Mulungu, tiyenera kusunga chikumbumtima chabwino. “Kuchita cholungama” m’chenicheni kumatanthauza kuchita chimene chiri chabwino, chimene Mulungu amafuna kwa ife. Ichi chimatanthauza kuti tiyenera kukwaniritsa mathayo athu, lofunikira kwambiri likumakhala kupereka kudzipereka kotheratu kwa Yehova. (Nahumu 1:2) Iye samalekerera mkangano. Ife m’chenicheni sitingakhale kapolo wa ambuye aŵiri.—1 Akorinto 10:22; Mateyu 6:24.
5. Ndimotani mmene Yesu anasonyezera kuti anakonda cholungama ndi kuda choipa?
5 Ndiponso, kuti “tichite cholungama,” tiyenera ‘kukonda cholungama ndi kuda choipa,’ monga mmene Yesu Kristu anachitira. Chifukwa cha chikondi chake kaamba ka chilungamo, iye anadzisunga iyemwini “wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa.” (Masalmo 45:7; Ahebri 7:26) Ndipo chifukwa chakuti Yesu anada choipa, chinali ndi mkwiyo wolungama kuti iye anadzudzula mwamphamvu atsogoleri a chipembedzo onyenga ndi adyera a m’tsiku lake.—Mateyu 23:13-36; Yohane 8:44.
6. Nchifukwa ninji timafunikira zoposa chabe chidziŵitso cha maganizo chakuti tiyenera kupewa chimene chiri choletsedwa chifukwa chakuti chiri choipa?
6 Monga mmene chingawonedwere kuchokera ku chitsanzo cha Yesu, sichiri chokwanira kukonda chilungamo. Tiyenera kuda—inde, kuipidwa, kunyansidwa, kuda kotheratu, kukhala ndi chisonkhezero champhamvu cha kuchoka—ku choipa. Chifukwa chakuti chikhoterero chathu chiri choipa kuyambira ku ubwana ndipo mitima yathu iri yonyenga, yachiwembu, tifunikira koposa chabe kuvomereza m’maganizo kuti chimene chiri choipa chiri choletsedwa. (Genesis 8:21; Yeremiya 17:9) Kusiyapo kokha ngati titsutsa mwamphamvu zikhoterero zochimwa ndi ziyeso, tingagonjere ku zinyengo zake. Tiyenera kukhala ndi kukana kwamphamvu kofananako kaamba ka choipa kumene Pinehasi anasonyeza pamene anagwiritsira ntchito nthungo kupyoza aŵiri ogwirizana m’kulambira koipa kwa Baala wa Peori.—Numeri 25:5-8.
7. Ndi umboni wotani umene tiri nawo wakuti Yehova sagwiritsira ntchito monga antchito anzake awo amene ali oipa?
7 Yehova safuna ndipo sadzagwiritsira ntchito monga ogwira ntchito anzake anthu aliwonse omwe ali oipa. Ichi chikumveketsedwa bwino pa Masalmo 50:16-18, kumene timaŵerenga: “Koma kwa woipa Mulungu ananena: ‘Uli nawo chiyani malemba anga kulalikira, ndi kutchula pangano langa pakamwa pako? Popeza udana nacho chilangizo, nufulatira mawu anga. Pakuwona mbala, uvomerezana nayo; nuchita nawo achigololo.’”
8. Ndi chochitika chotani chimene chimamveketsa chitonzo chimene tingapangitse mwakugonjera ku kachitidwe koipa?
8 Tingakhale otanganitsidwa mu utumiki wa Yehova, kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Koma ngati sitiri osamalitsa kusonyeza kudziletsa, tingachimwe chifukwa cha zofooka zakuthupi ndi kubweretsa chitonzo pa dzina la Yehova. Chotero, zaka zoŵerengeka zapita mkulu anachita chigololo ndi mlongo wauzimu yemwe anali ndi mwamuna wosakhulupirira. Pa madzulo pamene kuchotsedwa kwa yemwe anali mkuluyo kunalengezedwa, mwamuna wokwiitsidwayo analoŵa m’Nyumba ya Ufumu ndi mfuti yaing’ono ndi kuwombera zipolopolo pa aŵiri olakwawo. Palibe ndi mmodzi wa iwo amene anaphedwa, koma tsiku lotsatira imeneyi inali nkhani ya pa tsamba loyambirira m’nyuzipepala yaikulu koposa mu United States! Ndithudi, kuchita choipa kumabweretsa chitonzo.—Miyambo 6:32.
9. Mogwirizana ndi Miyambo 4:23, nchiyani chimene tiyenera kuchinjiriza, ndipo nchifukwa ninji?
9 Moyenerera, chotero, tikuchenjezedwa: “Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.” (Miyambo 4:23) Inde, tiyenera kudzilanga ife eni ponena za zimene tilola mitima yathu yophiphiritsira kukhalapo. Mowonjezerekawonjezereka, wailesi ya kanema, magazini, ndi mitundu ina yofalitsa nkhani imawonetsa zinthu zodetsedwa, kuphatikizapo zithunzithunzi za maliseke. Chotero, tiyenera kukhala osankha ponena za zimene timawonera, kumvetsera, ndi kuŵerenga. Kuletsa malingaliro kwaumwini kuli kofunika koposa! Mwachitsanzo, chingakhale chopepuka kupeza chisangalalo kuchokera ku kulingalira zosangulutsa za kugonana m’maganizo mwathu, zinthu zimene sitingalingalire kuyesa kuzichita m’moyo weniweni. (Mateyu 5:28) Koma kaŵirikaŵiri kulingalira koteroko kumatulukapo m’kachitidwe koipa. M’malo mokhalirira m’malingaliro pa zinthu zoterozo, chotero, lolani ife tisonyeze chipatso cha mzimu woyera cha kudziletsa ndi kukhalirira pa zinthu zondandalitsidwa pa Afilipi 4:8.—Agalatiya 5:22, 23.
“Kukonda Kukoma Mtima kwa Chifundo”
10, 11. (a) Ndi kusiyana kotani kumene kungapangidwe pakati pa kukhulupirika ndi kukhulupirira? (b) Ndimotani mmene Mwana wa Mulungu anasonyezera kukhulupirika ndi kukhulupirira?
10 Chofunikira chachiŵiri chotchulidwa pa Mika 6:8 chiri chakuti “tikonde kukoma mtima kwa chifundo.” “Kukonda kukhulupirika” iri njira imene The New English Bible imaŵerengera pano. Mawu a m’munsi mu New World Translation Reference Bible amasonyeza kuti liwu la Chihebri cheʹsedh, logwiritsiridwa ntchito “kukoma mtima kwa chifundo,” lingagwiritsiridwenso ntchito monga “kukoma mtima kwa chikondi” kapena “chikondi chokhulupirika.” Mogwirizana ndi otanthauzira mawu, “kukhulupirira kumasonyeza kukana kwamphamvu ku chiyeso chirichonse cha kusiya kapena kunyenga.” “Kukhulupirira kumawonjezera ku kukhulupirika lingaliro la kufuna kuimira pambali ndi kumenyera kaamba ka munthu kapena chinthu, ngakhale motsutsana ndi zinthu zamphamvu.” Mosangalatsa, m’Malemba timapezanso kusiyana kochepera m’kugwiritsira ntchito kwa mawu amenewo. Mwachitsanzo, liwu lakuti “kukhulupirira” siligwiritsiridwa ntchito ndi zinthu zopanda moyo. Koma liwu lakuti “kukhulupirika” mobwerezabwereza limatero. Chotero, mwezi umatchedwa, “mboni yokhulupirika ya kuthambo.” (Masalmo 89:37) Kenaka, kachiŵirinso, mawu a Mulungu amanenedwa kukhala okhulupirika, kunena kuti, odalirika.a (Chivumbulutso 21:5; 22:6) Kukhulupirira, ngakhale kuli tero, kumaperekedwa kokha kwa Yehova Mulungu ndi atumiki ake ovomerezeka. Mofananamo, ponena za Yehova, timaŵerenga kuti: “Ndi munthu wokhulupirira mudzachita mokhulupirika.”—2 Samueli 22:26, NW.
11 Mwana wa Mulungu anali wokhulupirika ndi wokhulupirira kwa Yehova kumwamba. Padziko lapansi, iye anapita pansi pa mayeso monga munthu Yesu Kristu ndi kutsimikizira mwa kumvera kwake kuti iye anali ponse paŵiri wokhulupirika ndi wokhulupirira monga munthu. Ichi chikusonyezedwa ndi Ahebri 5:7-9, pamene timaŵerenga kuti: “[Kristu, NW] m’masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa iye amene anakhoza kumpulumutsa iye mu imfa, ndipo anamveka popeza anawopa Mulungu. Ngakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo; ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera iye chifukwa cha chipulumutso chosatha.”
Ziyeso za Kukhulupirika
12. Pa nthaŵi zina, nchiyani chimene chingayese kukhulupirika kwathu, ndipo ndimotani mmene ena achitira ku ziyeso zotero?
12 Kukhulupirika kwa Yehova Mulungu kumafunikira kuti tikhalenso okhulupirika kwa atumiki ake padziko lapansi, Akristu anzathu. Mtumwi Yohane akuchimveketsa bwino ichi pamene iye akutikumbutsa ife kuti: “Iye wosakonda mbale wake amene wamuwona, sakhoza kukonda Mulungu amene sanamuwona.” (1 Yohane 4:20) Kupanda ungwiro kwa ena kungayese kukhulupirika kwathu m’chimenechi. Mwachitsanzo, pamene akwiitsidwa, ena asonyeza kufooka m’kukhulupirika kwawo ku gulu la Yehova mwa kusapita ku misonkhano ya Chikristu. Chiyeso china cha kukhulupirika kwathu kwa abale athu chimabuka pamene awo amene Yehova akugwiritsira ntchito m’kutenga chitsogozo alakwa m’kuweruza. Mobwerezabwereza, zophophonya zoterozo zagwiritsiridwa ntchito ndi ena monga chodzikhululukira cha kutenga pobisalira ndi kudzilekanitsa iwo eni kuchoka ku gulu lowoneka ndi maso la Yehova. Koma kodi njira yawo ya kachitidwe imalungamitsidwa? Kutalitali!
13. Nchifukwa ninji kudzipatula kuchoka ku gulu la Yehova kuli kosalungamitsidwa, ndipo kodi ndi zosankha zosiyanapo zotani zimene zimadzipereka izo zokha kwa osakhulupirika oterowo?
13 Nchifukwa ninji anthu oterowo sali olungamitsidwa m’kusiya gulu la Mulungu? Chifukwa Mawu ake amatitsimikizira ife: “Akukonda chilamulo chanu [Yehova], ali nawo mtendere wambiri, ndipo alibe chokhumudwitsa.” (Masalmo 119:165) Ndiponso, tikulamuliridwa “kukhala nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha, pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo.” (1 Petro 4:8; Miyambo 10:12) Kuwonjezerapo, tangoyerekezani kuti munthu anadzipatula mwini yekha kuchoka ku anthu a Yehova. Ndi kuti kumene iye angapite? Kodi iye samayang’anizana ndi nkhani imodzimodzimoyo imene atumwi a Yesu anakumana nayo pamene iye anawafunsa iwo ngati anafuna kuchoka? Mtumwi Petro molondola anayankha kuti: “Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha.” (Yohane 6:68) Kulibe kwina kulikonse kumene tingapite, koma ku “Babulo Wamkulu,” ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, kapena m’zogwirira za “chirombo” cha ndale zadziko cha Satana. (Chivumbulutso 13:1; 18:1-5) Mokulira, osakhulupirika omwe asiya gulu lowoneka ndi maso la Yehova apanga ubwenzi ndi awo amene ali mu “Babulo Wamkulu” wosalemekeza Mulungu.”
“Khalani Odzichepetsa M’kuyenda ndi Mulungu Wanu”
14, 15. (a) Ndi tanthauzo lotani limene liwu la Chingelezi lakuti “kudzichepetsa” liri nalo? (b) Ndi tanthauzo liti la “kudzichepetsa” limene tiri odera nalo nkhaŵa pano, ndipo kaamba ka zifukwa zotani? (c) Nchifukwa ninji Akristu ayenera ‘kuika chiyerekezero chodzichepetsa pa kuthekera kwawo kapena kuyenera’?
14 Liwu la Chingelezi lakuti “wodzichepetsa” liri ndi matanthauzo ambiri. Ilo lingalozere ku chija chimene chiri chodekha, “chokhala ndi polekezera mu mlingo, ukulu, kapena mkhalidwe.” Kapena chingakhale ndi tanthauzo la kuyera, “kusunga kuyenera kwa chovala ndi mkhalidwe.” (1 Timoteo 2:9) Kenaka pali tanthauzo la “kudzichepetsa” kumene tiri odera nako nkhaŵa mwapadera, kumene kuli, kukhala wozindikira za malekezero a wina kapena “kuika ziyerekezo zodekha pa kuthekera kwa mwini kapena kuyenera.” Sitingakhale mmodzi wa ogwira ntchito anzake a Yehova ngati timaika pamwamba malingaliro a ife eni, kukokera chisamaliro kwa ife eni m’malo mwa kupereka chisamaliro choyamba kwa Yehova Mulungu.
15 ‘Kuika chiyerekezo chochepera pa kuthekera kwathu ndi kufunika’ liri tanthauzo lowonekera limene tiyenera kugwirizanitsa ku liwu la Chihebri losonyezedwa monga “kudzichepetsa” pa Mika 6:8. Ichi chiri chowonekera kuchokera ku njira mu imene liwulo lagwiritsiridwa ntchito m’kuwoneka kwake kokha m’Malemba a Chihebri. Pa Miyambo 11:2 ilo likusiyanitsidwa osati ndi kuipa kwa mkhalidwe woipa wa kugonana koma ndi kudzikuza, komwe kumatulukapo kuchokera ku kudzilingalira mokwezeka inumwini. Pamenepo timaŵerenga kuti: “Pakudza kudzikuza padzanso manyazi; koma nzeru iri ndi odzichepetsa.” Kukhala wodzichepetsa kumayendera limodzi ndi kukhala ndi kuwopa Yehova, komwenso kumagwirizana ndi nzeru. (Masalmo 111:10) Munthu wodzichepetsa amawopa Yehova chifukwa chakuti amazindikira kusiyana kokulira kumene kulipo pakati pa iye ndi Mulungu, pakati pa kulungama ndi mphamvu ya Yehova ndi kupanda ungwiro kwake ndi kufooka. Chotero, munthu wodzichepetsa amagwirira ntchito chipulumutso chake ndi mantha ndi kunjenjemera.—Afilipi 2:12.
16. Ndi malemba ena ati amene amasonyeza chifukwa chimene Akristu ayenera kukhalira odzichepetsa?
16 Pali zifukwa zambiri zimene ogwira ntchito anzake a Yehova ayenera kukhalira odzichepetsa! Mosasamala kanthu za nzeru imene tingakhale nayo, mphamvu ya kuthupi imene tingakhale nayo, kapena ngakhale kuchuluka kwa chuma cha kuthupi chimene tingakhale nacho, tiribe maziko a kudzitukumulira. (Yeremiya 9:23) Nchifukwa ninji ayi? Chifukwa cha prinsipulo lolembedwa pa 1 Akorinto 4:7: “Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandira?” Tiribenso chifukwa chirichonse cha kudzitamandira chifukwa cha zipatso za utumiki wathu, popeza nchiyani chimene timaŵerenga pa 1 Akorinto 3:6, 7? Pamenepo Paulo ananena kuti: “Ndinawoka ine, anathirira Apolo; koma Mulungu anakulitsa. Chotero sali kanthu kapena wowokayo, kapena wothirirayo, koma Mulungu amene akulitsa.” Mawu a Yesu pa Luka 17:10 ayeneranso kutithandiza ife kukhala odzichepetsa, popeza iye ananena kuti: “Chotero inunso mmene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, ‘Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.’”
17. Nchifukwa ninji kukhala wodzichepetsa mowonadi kuli njira ya nzeru?
17 Kukhala odzichepetsa ndithudi iri njira yanzeru. Kudzichepetsa kumatitheketsa ife kukhala okwaniritsidwa ndi mwaŵi uliwonse umene tingakhale nawo wa kutumikira. Ngati tiri odzichepetsa, sitidzayesa kuwala modzitukumula koma tidzakhala okwaniritsidwa kudzitsogoza ife eni monga “wochepa.” (Luka 9:48) Kenaka, kachiŵirinso, tidzakhala ndi mkhalidwe wa wamasalmo, yemwe analengeza kuti: “Pakuti tsiku limodzi m’mabwalo anu likoma koposa masiku ambirimbiri akukhala pena. Kukhala ine wapakhomo m’nyumba ya Mulungu wanga, kundikonda ine koposa kugonera m’mahema a choipa.” (Masalmo 84:10) Kuwonjezerapo, ngati tiri odzichepetsa, tidzakhala ndi chikondi chimene chidzatisonkhezera ife kutenga chitsogozo m’kulemekeza ena.—Aroma 12:10.
Kudzichepetsa kuli Koyenera kwa Achichepere
18. (a) Nchifukwa ninji kudzichepetsa mwapadera kuli koyenera kwa achichepere? (b) Kufunika kwa kudzichepetsa kumasonyezedwa ndi cholembera chiti chokhudza achichepere amakono?
18 Chiri makamaka choyenera kuti Akristu achichepere adziveke iwo eni ndi chovala cha kudzichepetsa. Ndi chitsanzo chabwino chotani nanga chimene Elihu anapereka kaamba ka iwo! Ngakhale kuti anali ndi mayankho olondola, iye anali wofunitsitsa kudikira mwaulemu kufikira amuna achikulire atalankhula. (Yobu 32:6, 7) Kaŵirikaŵiri, achichepere ali oyedzamira ku kudzimva kukhala odzidalira, kukhala ozindikira pang’ono za malekezero awo. Chifukwa chakuti iwo ali ndi mphamvu yakuthupi ndipo apeza chidziŵitso chinachake, iwo amayedzamira ku kunyalanyaza achikulire awo. Koma chidziŵitso sichiri chofanana ndi nzeru, imene iri kugwiritsira ntchito kwa chidziŵitso. Chodziŵika koposa chiri cholembera chomvetsa chisoni chimene achichepere amakono akupanga mu United States. Kumeneko, 63 peresenti ya omangidwa kaamba ka maupandu a akulu amaphatikizapo anthu achichepere kufika ku zaka 24 zakubadwa, 30 peresenti ya omangidwawo ikumakhala awo a zaka za pansi pa 18. Chikusimbidwanso kuti “kuyendetsa galimoto ataledzera kapena osonkhezeredwa ndi anamgoneka chiri chochititsa chachikulu cha imfa pakati pa anthu a ku America a zaka za 15-24.” M’dziko limenelo, “maukwati owonjezerekawonjezereka a zaka za pakati pa 13 ndi 19 amathera m’kulekana,” pamene chikunenedwa kuti “maukwati angathe kukhala kwa nthaŵi yaitali ngati mkwatibwi ndi mkwati ali ndi zaka zowonjezereka zoŵerengeka za nzeru kumbuyo kwawo pamene apita paguwa.”
19. Ndi uphungu wa m’Malemba wotani umene achichepere adzachita bwino kuwutenga ku mtima?
19 Chotero, uli wanzeru chotani nanga, uphungu wa Mawu a Mulungu! Moyenerera, umalangiza achichepere kulemekeza atate awo ndi amawo, kukhala omvera kwa iwo mu chirichonse. (Aefeso 6:1-3; Akolose 3:20) Makamaka achichepere ayenera kusunga ku mtima uphungu wanzeru uwu: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako. Umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ako.”—Miyambo 3:5, 6.
20. Ndi mphoto zotani zimene anthu onse odzipereka ndi obatizidwa angayembekezere ngati alabadira Mika 6:8?
20 Ndi mphotho zotani zimene tonsefe tingayembekezere ngati, pambuyo pa kusonyeza kukhulupirira kwathu Yehova mwa kudzipereka ndi ubatizo wa m’madzi, ‘tichita cholungama, kusonyeza chikondi changwiro, ndipo tiri odzichepetsa m’kuyenda ndi Mulungu wathu’? Chofunika koposa cha zonse, tidzakhala ndi chivomerezo cha Yehova chifukwa cha kufikiritsa zifuno zake ndipo mwakutero tidzakondweretsa mtima wake mwa kugawanamo m’kuyeretsa dzina lake lalikulu ndi lowopsya. (Miyambo 27:11) Ndiponso, tidzazindikira m’miyoyo yathu yeniyeni chowonadi cha lamulo lakuti “chipembedzo chipindula zonse popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno ndi la moyo ulinkudza.”—1 Timoteo 4:8.
[Mawu a M’munsi]
a Ku mbali ya kumpoto kwa United States, kuli chiŵiya chotenthetsera madzi chimene kwa zaka zambiri, pa avereji, chinkaphulika kamodzi pa mphindi 65 zirizonse. Icho chotero chinadzipezera dzina lake, Wokhulupirika Wakale.
Ndi Ati Omwe Ali Mayankho Anu?
◻ M’chigwirizano ndi Mika 6:8, nchiyani chimene chikufunikira kuti “tichite cholungama”?
◻ Ndi chiyambukiro chotani chimene kukhulupirira Yehova kuli nako pa unansi wathu ndi Akristu anzathu?
◻ Nchifukwa ninji tifunikira ‘kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu’?
◻ Nchifukwa ninji kudzichepetsa mwapadera kuli koyenera kwa Akristu achichepere?
[Chithunzi patsamba 17]
Kodi mumachinjiriza mtima wanu mwakukhala wosankha ponena za zimene mumawona, kumvetsera, ndi kuŵerenga?
[Chithunzi patsamba 18]
Petro anadziŵa kuti kunalibe kwina kulikonse kumene akanapita chifukwa chakuti Yesu anali ndi “mawu a moyo wosatha.” Kodi mwagamulapo kukhala wokhulupirika ku gulu la Yehova?