Gwiranibe Ntchito Yake ya Chipulumutso Chanu!
“Okondedwa, . . . gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira.”—AFILIPI 2:12.
1, 2. Kodi ndi zikhulupiriro zofala zotani zimene zapangitsa anthu ambiri kuganiza kuti sangalamulire mmene moyo wawo udzakhalira?
“KODI munabadwa choncho?” Posachedwapa, funso limenelo linalembedwa pachikuto cha magazini inayake yotchuka. Mmunsi mwa mutuwo munali mawu akuti: “Umunthu, mkhalidwe, ngakhale zosankha pamoyo. Kafukufuku waposachedwapa akusonyeza kuti zonsezo ndi chibadwa.” Mawu ngati amenewo angapangitse ena kuganiza kuti palibe zambiri zimene angachite kuti alamulire moyo wawo.
2 Ena ali ndi nkhaŵa yakuti popeza makolo awo sanawalere bwino kapena kuti aphunzitsi awo sanawaphunzitse bwino, ndiye basi moyo wawo udzakhala wamavuto. Iwo angaganize kuti nzolembedwa kuti adzachita zolakwa zomwe makolo awo anachita, kutsata zofooka zawo zazikulu, kukhala osakhulupirika kwa Yehova—mwachidule, kusasankha bwino. Kodi ndi zimene Baibulo limaphunzitsa? Kunena zoona, alipo anthu ena opembedza amene amalimbikira kunena kuti Baibulo limaphunzitsa zimenezi, chiphunzitso cha kuikiratu zamtsogolo. Malinga ndi chiphunzitso chimenechi, kale kwambiri Mulungu anaikiratu zochitika zonse pamoyo wanu.
3. Kodi Baibulo lili ndi uthenga wotani wolimbikitsa wonena za kukhoza kwathu kusenza udindo wolamulira tsogolo lathu?
3 Zikhulupiriro zosiyana zonsezi zikunena chimodzi: Mulibe ufulu wosankha, simungalamulire mmene moyo wanu udzakhalira. Uthenga umenewo umalefula, si choncho kodi, ndipo kulefuka kumawonjezera mavutowo. Miyambo 24:10 imati: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” Komabe tikulimbikitsidwa kudziŵa kuti malinga ndi Baibulo, ‘tingagwire ntchito yake ya chipulumutso chathu.’ (Afilipi 2:12) Kodi tingalimbitse motani chidaliro chathu m’chiphunzitso cholimbikitsa chimenechi cha m’Malemba?
Ntchito ‘Yomanga’ Imene Timachita Mkati Mwathu
4. Ngakhale kuti 1 Akorinto 3:10-15 amalankhula za kumanga ndi zomangira zosagwira moto, kodi zimenezi sizitanthauza chiyani?
4 Talingalirani fanizo la mtumwi Paulo lopezeka pa 1 Akorinto 3:10-15. Pamenepo, akulankhula za ntchito yachikristu yakumanga, ndipo pulinsipulo la fanizo lake limagwira ntchito pa utumiki wamkati ndi wakunja. Kodi akutanthauza kuti ngati wophunzira pomaliza pake wasankha kutumikira Yehova nakhalabe m’zimene wasankhazo umakhala udindo wa aja okha amene anamphunzitsa? Ayi. Paulo anali kugogomezera kufunika kwakuti mphunzitsi achite zonse zotheka pantchitoyo yomanga. Koma monga momwe tinaphunzirira m’nkhani yapita, sanali kunena kuti wophunzira alibe ufulu wosankha pankhaniyi. Zoona, fanizo la Paulo lasumika pa ntchito imene timachita mwa anthu ena, osati kudzimanga ife eni. Zimenezi zili choncho chifukwa Paulo akunena kuti ntchito yomanga yosachitidwa bwino ikuwonongeka pamene womangayo akupulumutsidwa yekha. Komanso, Baibulo nthaŵi zina limagwiritsa ntchito fanizo limenelo pantchito imene timaichita mkati mwathu.
5. Kodi ndi Malemba ati omwe asonyeza kuti Akristu ayenera kugwira ntchito ‘yomanga’ mkati mwawo?
5 Mwachitsanzo, talingalirani Yuda 20, 21 yemwe amati: “Inu, okondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mu Mzimu Woyera, mudzisunge nokha m’chikondi cha Mulungu.” Panopa Yuda akugwiritsa ntchito liwu lachigiriki lomwelo la “kumanga” lomwe Paulo akugwiritsa ntchito mu 1 Akorinto chaputala 3, koma mfundo yake ikukhala ngati ndi yakuti timadzimangirira tokha pa maziko a chikhulupiriro chathu. Luka, polemba fanizo la Yesu la munthu amene anamanga nyumba yake pathanthwe, akugwiritsa ntchito liwu lomwelo lachigiriki la “maziko” lomwe Paulo akugwiritsa ntchito m’fanizo lake la kumanga kwachikristu. (Luka 6:48, 49) Ndiponso, polimbikitsa Akristu anzake kupita patsogolo mwauzimu, Paulo akugwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa a kukhala wokhazikika pa “maziko.” Inde, Mawu a Mulungu amaphunzitsa kuti timachita ntchito ‘yomanga’ mkati mwathu.—Aefeso 3:15-19; Akolose 1:23; 2:7.
6. (a) Fotokozani mwa fanizo mmene wophunzira wachikristu aliyense amakhalirako chifukwa cha ntchito yomanga yochitira limodzi ndi ena. (b) Kodi wophunzira aliyense payekha ali ndi udindo wotani?
6 Kodi kumanga Mkristu ndi ntchito ya munthu mmodzi? Chabwino, tinene kuti mukufuna kumanga nyumba. Mupita kwa mmisiri wa mapulani kuti mukagule mapulaniwo. Pamene kuli kwakuti mukufuna kuchita ntchito yaikulu nokha, muitanitsa womanga kuti adzagwire nanu ntchitoyo ndi kukulangizani za njira zabwino koposa. Akaika maziko olimba, kukuthandizani kumvetsa mapulaniwo, kukuuzani zomangira zabwino kwambiri zoti mugule, ndipo ngakhale kukuphunzitsani zambiri pa kamangidwe, mudzavomereza kuti wachita bwino kwambiri. Nanga bwanji ngati munyalanyaza zimene wakuuzani, mukugula zomangira zotchipa kapena zosalimba, mpaka osatsata ndi mapulani omwe amene munakagula kwa mmisiri uja wa mapulani? Kunena zoona simungaimbe mlandu womanga uja kapena mmisiri wa mapulani ngati nyumba yagwa! Momwemonso, wophunzira aliyense wachikristu amakhalapo chifukwa cha ntchito yomanga yochitira limodzi ndi ena. Yehova ndiye mmisiri mwinimapulani. Amachirikiza Mkristu wokhulupirika amene, monga mmodzi wa “antchito anzake a Mulungu,” amaphunzitsa ndi kumanga wophunzira. (1 Akorinto 3:9) Komanso wophunzira ali ndi mbali yake yoti achite. Pomaliza, amadziyankhira mlandu chifukwa cha moyo wake. (Aroma 14:12) Ngati akufuna kukhala ndi mikhalidwe yabwino yachikristu, alimbikire kuti aipeze, kuimanga mwa iye.—2 Petro 1:5-8.
7. Kodi Akristu ena amakhala ndi mavuto otani, ndipo nchiyani chingawatonthoze?
7 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti chibadwa, malo, ndi luso la aphunzitsi athu nzopanda pake? Ayi. Mawu a Mulungu amavomereza kuti chilichonsecho nchofunika ndi kuti chili ndi mphamvu. Zizoloŵezi zambiri zoipa komanso zauchimo nchibadwa ndipo zimavuta kwambiri kulimbana nazo. (Salmo 51:5; Aroma 5:12; 7:21-23) Maleredwe a makolo ndi mkhalidwe wa panyumba zingawakhudze kwambiri ana—m’njira yabwino kapena yoipa. (Miyambo 22:6; Akolose 3:21) Yesu anatsutsa atsogoleri achipembedzo achiyuda chifukwa cha zotsatirapo zoipa za chiphunzitso chawo kwa ena. (Mateyu 23:13, 15) Lero, zinthu ngati zimenezo zimatikhudza ife tonse. Mwachitsanzo, anthu ena a Mulungu ali ndi mavuto awo chifukwa cha zovuta za paubwana. Amenewa afunikira tiwakomere mtima ndi kuwachitira chifundo. Ndipo uthenga wa m’Baibulo uyenera kuwatonthoza wakuti sadzachita zolakwa zimene makolo awo anachita kapena kukhala osakhulupirika. Talingalirani mmene mafumu ena akale a Yuda amasonyezera mfundo imeneyi.
Mafumu a Yuda—Anadzisankhira Okha
8. Kodi Yotamu anaona chitsanzo chotani choipa mwa atate wake, koma anasankha zotani?
8 Uziya anakhala mfumu ya Yuda ali wamng’ono zedi wazaka 16 ndipo analamulira zaka 52. Mbali yaikulu ya nthaŵi imeneyi ‘anachita zowongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita atate wake Amaziya.’ (2 Mafumu 15:3) Yehova anamdalitsa mwa kumpatsa zilakiko zambiri pankhondo. Koma mwachisoni, kupambana kwakeko kunampangitsa kunyada. Anadzikweza napandukira Yehova mwa kufukiza nsembe paguwa la nsembe m’kachisi, ntchito imene inali ya ansembe okha. Uziya anadzudzulidwa koma m’malo mwake anakwiya. Kenako anachepetsedwa—anakanthidwa ndi khate ndipo anakakamizika kukhala kwayekha moyo wake wonse. (2 Mbiri 26:16-23) Kodi Yotamu mwana wake anatani ataona zimenezi? Mnyamatayo akanasonkhezeredwa mosavuta ndi atate wake ndipo akanaipidwa ndi chilango cha Yehova. Anthu ambiri akanamsonkhezera moipa popeza anapitirizabe kupembedza kwawo kolakwika. (2 Mafumu 15:4) Koma Yotamu anasankha yekha. “Anachita zoongoka pamaso pa Yehova.”—2 Mbiri 27:2.
9. Kodi ndani ena amene akanamsonkhezera Ahazi kuchita chabwino, koma kodi moyo wake unakhala wotani?
9 Yotamu analamulira zaka 16, ndipo anali wokhulupirika kwa Yehova nthaŵi yonseyo. Chotero Ahazi mwana wake anali ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha atate wake wokhulupirika. Ndipo panalinso ena amene akanamlimbikitsa Ahazi. Anali ndi mwayi pokhala ndi moyo panthaŵi imene aneneri okhulupirika Yesaya, Hoseya, ndi Mika anali okangalika kunenera m’dzikolo. Komabe, sanasankhe bwino. “Sanachita zoongoka pamaso pa Yehova ngati Davide kholo lake.” Anapanga mafano a Baala nawalambira, ndipo anawotcha ngakhale ana ake ena ndi moto, kuwapereka nsembe kwa milungu yakunja. Ngakhale kuti panali amene akanamsonkhezera kuchita chabwino, iye analephereratu monga mfumu ndiponso monga mtumiki wa Yehova.—2 Mbiri 28:1-4.
10. Kodi Ahazi anali atate wamtundu wotani, koma kodi Hezekiya mwana wake anasankha zotani?
10 Pankhani ya kulambira koyera, nkovuta kuganiza za atate wina woipa kuposa Ahazi. Komabe, Hezekiya mwana wake sakanasankha amene akanakhala Atate wake! Ana aang’ono amene Ahazi anapha mwa kuwapereka nsembe kwa Baala angakhale anali abale akeake a Hezekiya. Kodi mkhalidwe umenewu woipa umene Hezekiya anakuliramo unaikiratu tsogolo lake kuti adzakhala wosakhulupirika kwa Yehova? Ayi. Hezekiya anakhala mmodzi wa mafumu angapo a Yuda abwino kwambiri—munthu wokhulupirika, wanzeru, ndi wokondedwa. “Yehova anali naye.” (2 Mafumu 18:3-7) Ndipotu, pali chifukwa chokhulupirira kuti Hezekiya adakali kalonga wachinyamata anali mlembi wouziridwa wa Salmo la 119. Ngati zilidi choncho, nzosavuta kuona chifukwa chake angakhale atalemba mawu akuti: “Moyo wanga wasungunuka ndi [wakhala usakugona chifukwa cha, NW] chisoni.” (Salmo 119:28) Mosasamala kanthu za mavuto ake osautsa, Hezekiya analola Mawu a Yehova kumtsogoza pamoyo wake. Salmo 119:105 limati: “Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.” Inde, Hezekiya anadzisankhira yekha—kuchita zoyenera.
11. (a) Ngakhale kuti atate wake anali chitsanzo chabwino, kodi kupandukira Yehova kwa Manase kunali koipa motani? (b) Kodi Manase anasankha zotani kumapeto kwa moyo wake, ndipo tingaphunzireponji?
11 Komano chodabwitsa nchakuti mwa mmodzi wa mafumu a Yuda abwino koposa munatuluka mmodzi wa mafumu oipitsitsa zedi. Manase mwana wa Hezekiya analimbikitsa kupembedza mafano, zamizimu, ndi chiwawa chochuluka pamlingo umene sunachitikepo. Nkhaniyo imati “Yehova analankhula ndi Manase ndi anthu ake,” mwinamwake mwa aneneri. (2 Mbiri 33:10) Ayuda amati Manase analabadira zimenezo mwa kulamula kuti Yesaya achekedwe pakati. (Yerekezerani ndi Ahebri 11:37.) Kaya zimenezo nzoona kapena ayi, Manase sanamverebe machenjezo alionse a Mulungu. Ndipotu anatentha ana ake ena amoyo monga nsembe, monga momwe Ahazi gogo wake anachitira. Komano munthu woipa ameneyu atakumana ndi zovuta zazikulu pambuyo pake m’moyo, analapa nasintha njira zake. (2 Mbiri 33:1-6, 11-20) Chitsanzo chake chikutiphunzitsa kuti ngati munthu walakwitsa zinthu kwambiri sizitanthauza kuti sangaomboledwe. Atha kusintha.
12. Kodi ndi zinthu ziti zosiyana zimene Amoni ndi Yosiya mwana wake anasankha pankhani ya kutumikira Yehova?
12 Amoni mwana wa Manase akanatengerapo phunziro pa kulapa kwa atate wake. Koma iye anasankha zolakwika zokhazokha. Kwenikweni Amoni “anachulukitsa kupalamula kwake” kufikira ataphedwa. Yosiya mwana wake anasiyana ndi iye ndipo zinali zolimbikitsa. Yosiya mwachionekere anasankha kutengerapo phunziro pa zimene zinachitikira agogo ake. Anayamba kulamulira ali ndi zaka zisanu ndi zitatu zokha. Atakwanitsa zaka 16 zokha, anayamba kufunafuna Yehova ndiyeno anakhala mfumu yokhulupirika yopereka chitsanzo chabwino. (2 Mbiri 33:20–34:5) Anadzisankhira yekha—kuchita zoyenera.
13. (a) Kodi tikuphunzirako chiyani kwa mafumu a Yuda amene tapenda? (b) Kodi chiphunzitso cha makolo nchofunika motani?
13 Kupenda kwachidule mafumu asanu ndi aŵiri a Yuda kumeneku kukutiphunzitsa zazikulu. Nthaŵi zina, mafumu oipitsitsa anali ndi ana abwino koposa komanso mafumu abwino koposa anali ndi ana oipitsitsa. (Yerekezerani ndi Mlaliki 2:18-21.) Zimenezi sizikuchepetsa kufunika kwa chiphunzitso cha makolo. Makolo amene amaphunzitsa ana awo malinga ndi njira ya Yehova amapatsa ana awo mwayi wabwino kwambiri wakuti akhale atumiki okhulupirika a Yehova. (Deuteronomo 6:6, 7) Koma ana ena, ngakhale kuti makolo awo okhulupirika amayesetsa, amasankha kutsata njira yolakwika. Ana ena, ngakhale kuti amakhala ndi chitsanzo choipa cha makolo, amasankha kukonda Yehova ndi kumtumikira. Pokhala ndi dalitso lake, moyo wawo umawayendera bwino. Kodi inu nthaŵi zina mumadabwa kuti zidzakuchitikirani nziti? Pamenepo talingalirani zina za zitsimikizo za Yehova zakuti mungathe kusankha zoyenera!
Yehova Amakukhulupirirani!
14. Kodi tidziŵa bwanji kuti Yehova amamvetsa kupereŵera kwathu?
14 Yehova amaona zonse. Miyambo 15:3 imati: “Maso a Yehova ali ponseponse, nayang’anira oipa ndi abwino.” Za Yehova Mfumu Davide inati: “Maso anu anaona ngakhale mluza wanga, ndipo m’buku lanu ziŵalo zake zonse zinalembedwamo, ponena za masiku pamene zinaumbidwa ndi pamene panalibe nchimodzi chomwe mwa izo.” (Salmo 139:16, NW) Chotero Yehova amadziŵa zizoloŵezi zoipa zimene mukulimbana nazo—kaya zinabwera mwa chibadwa kapena munakhala nazo chifukwa cha zinthu zina zimene simukanaletsa. Amamvetsadi mmene zimenezi zakukhudzirani. Amamvetsa kupereŵera kwanu bwinonso kukuposani. Ndipo ngwachifundo. Samafuna zambiri kwa ife kusiyapo zimene tingathe kuchita.—Salmo 103:13, 14.
15. (a) Kodi china chimene chingatonthoze aja amene anapwetekedwa mwadala ndi ena nchiyani? (b) Kodi Yehova amalemekeza aliyense wa ife mwa kutipatsa udindo wotani?
15 Komanso, Yehova sationa ngati anthu amene sitingachite chilichonse kudzithandiza chifukwa cha mikhalidwe yakutiyakuti. Ngati kale tinakumana ndi zovuta, tingatonthozedwe ndi chitsimikizo chakuti Yehova amada khalidwe loipa ladala lililonse. (Salmo 11:5; Aroma 12:19) Koma kodi adzatiteteza pa zotsatirapo zoipa ngati titembenukanso ndipo mwadala kusankha zolakwika? Ayi. Mawu ake amati: “Yense adzasenza katundu wake.” (Agalatiya 6:5) Yehova amalemekeza chilichonse cha zolengedwa zake zaluntha mwa kuchipatsa udindo wochita chabwino ndi kumtumikira. Zili monga momwe Mose anauzira mtundu wa Israyeli kuti: “Ndichititsa mboni lero kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbewu zanu.” (Deuteronomo 30:19) Yehova ali ndi chidaliro chakuti ifenso tingasankhe zoyenera. Tidziŵa bwanji zimenezo?
16. Kodi tingakhoze motani ‘pogwira ntchito yake ya chipulumutso chathu’?
16 Onani kuti mtumwi Paulo analemba kuti: “Potero, okondedwa anga, . . . gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira; pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.” (Afilipi 2:12, 13) Liwu lake lachigiriki lotembenuzidwa kuti ‘kugwira’ panopa limatanthauza kumaliza chinachake. Chotero palibe aliyense wa ife amene zinalembedwa kuti adzalephera kapena kusiya. Ndithudi Yehova Mulungu ali ndi chidaliro chakuti tingamalize ntchito imene watipatsa kuchita—ntchito yodzetsa chipulumutso chathu—apo ayi sakanauzira mawu ngati amenewo. Koma kodi tingakhoze motani? Si mwa nyonga yathu ayi. Tikanakhala olimba zedi mwa ife tokha, bwenzi sipakufunikira “mantha, ndi kunthunthumira.” M’malo mwake, Yehova ‘amachita mwa ife,’ mzimu wake woyera ukumagwira ntchito m’maganizo ndi mtima wathu, kutithandiza “kufuna ndi kuchita.” Pokhala ndi thandizo lachikondi limenelo, kodi pali chifukwa china chilichonse chimene tingalepherere kusankha zoyenera m’moyo ndi kuzitsatira? Ayi!—Luka 11:13.
17. Kodi ndi masinthidwe otani amene tingapange, ndipo Yehova amatithandiza motani kutero?
17 Pali zopinga zimene tiyenera kugonjetsa—mwinamwake zizoloŵezi zoipa pamoyo wathu ndi zinthu zina zoipa zimene zingapotoze maganizo athu. Ngakhale zili choncho, tingagonjetse zimenezi mwa thandizo la mzimu wa Yehova! Monga momwe Paulo analembera Akristu a ku Korinto, Mawu a Mulungu ali ndi mphamvu yokwanira kupasula ngakhale “malinga.” (2 Akorinto 10:4) Kwenikweni, Yehova angatithandize kupanga masinthidwe aakulu. Mawu ake amatilimbikitsa ‘kuvula umunthu wakale’ ndi ‘kuvala umunthu watsopano, umene unalengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.’ (Aefeso 4:22-24) Kodi mzimu wa Yehova ungatithandizedi kupanga masinthidwe amenewo? Inde! Mzimu wa Mulungu umabala zipatso mwa ife—mikhalidwe yokongola yamtengo wapatali imene tonsefe timafuna kukhala nayo. Woyamba mwa imeneyi ndi chikondi.—Agalatiya 5:22, 23.
18. Kodi munthu aliyense woganiza akhoza kusankha chiyani, ndipo chimenechi chiyenera kutithandiza kukhala otsimikiza kuchita chiyani?
18 Chimenechi ndicho choonadi chachikulu chomasula. Yehova Mulungu ali ndi mphamvu yosatha yoonetsera chikondi, ndipo ife tinapangidwa m’chifanizo chake. (Genesis 1:26; 1 Yohane 4:8) Choncho tingasankhe kukonda Yehova. Ndipo chikondi chimenecho—osati moyo umene tinali nawo kale, osati zolakwa zongotengera, osati chibadwa chathu chokonda kuchita zoipa—chingatikonzere tsogolo lathu. Chikondi cha Yehova Mulungu nchimene Adamu ndi Hava anafunikira kuti akhalebe okhulupirika m’Edene. Aliyense wa ife afunikira chikondi chomwecho kuti apulumuke Armagedo ndi kupambana chiyeso chomaliza pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu. (Chivumbulutso 7:14; 20:5, 7-10) Aliyense wa ife, kaya mikhalidwe yathu ili yotani, tingakulitse chikondi chimenecho. (Mateyu 22:37; 1 Akorinto 13:13) Titsimikizetu mtima kukonda Yehova ndi kukulitsa chikondi chimenecho muyaya wonse.
Kodi Muganiza Bwanji?
◻ Kodi ndi zikhulupiriro zotani zofala zimene zimatsutsa chiphunzitso chabwino cha Baibulo chakuti munthu adzadziyankhira mlandu?
◻ Kodi ndi ntchito yotani yomanga imene Mkristu aliyense ayenera kuchita mkati mwake?
◻ Kodi zitsanzo za mafumu a Yuda zikusonyeza motani kuti munthu aliyense amachita kudzisankhira yekha?
◻ Kodi Yehova amatitsimikizira motani kuti tingasankhe zoyenera m’moyo, ngakhale kuti tazingidwa ndi zinthu zoipa?
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi chibadwa chanu chinaikiratu tsogolo lanu?
[Chithunzi patsamba 17]
Ngakhale kuti atate wake anali chitsanzo choipa, Mfumu Yosiya anasankha kutumikira Mulungu