NKHANI YOPHUNZIRA 30
Pitirizani Kukonda Yehova ndi Anthu
“Tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzera m’chikondi.”—AEF. 4:15.
NYIMBO NA. 2 Dzina Lanu Ndinu Yehova
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Kodi ndi mfundo za choonadi ziti zomwe munazidziwa mutayamba kuphunzira Baibulo?
KODI mumakumbukira zinthu zomwe munadziwa mutayamba kuphunzira Baibulo? Muyenera kuti munadabwa mutadziwa kuti Mulungu ali ndi dzina. Mwinanso munamva bwino mutazindikira kuti Mulungu sazunza anthu kumoto. Mosakayikira munasangalalanso mutadziwa kuti pali chiyembekezo chakuti mudzaonananso ndi okondedwa anu omwe anamwalira ndipo muzidzakhala nawo m’paradaiso padzikoli.
2. Kuwonjezera pa kuphunzira mfundo za choonadi cha m’Baibulo, kodi munachitanso chiyani kuti mupite patsogolo? (Aefeso 5:1, 2)
2 Pamene munkaphunzira kwambiri Mawu a Mulungu, m’pamenenso munayamba kukonda kwambiri Yehova. Chikondicho chinakulimbikitsani kuti muzitsatira zimene munkaphunzira. Munkasankha zochita mwanzeru mogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Munasintha mmene munkaonera zinthu komanso khalidwe lanu chifukwa munkafuna kusangalatsa Mulungu. Mofanana ndi mwana amene amatsanzira kholo lake lachikondi, inunso munkatsazira Atate wanu wakumwamba.—Werengani Aefeso 5:1, 2.
3. Kodi tingadzifunse mafunso ati?
3 Mwina tingadzifunse kuti: ‘Kodi panopa ndimakonda kwambiri Yehova kuposa mmene ndinkamukondera nditangokhala kumene Mkhristu? Kungochokera pamene ndinabatizidwa, kodi ndimaganiza kapena kuchita zinthu ngati Yehova, makamaka posonyeza chikondi kwa abale ndi alongo?’ Ngati ‘chikondi chimene munali nacho poyamba’ chayamba kuchepa, musafooke. Zimenezi zinachitikiraponso Akhristu a mu nthawi ya atumwi. Yesu sanasiye kuwakonda, ndipo ifenso sangasiye kutikonda. (Chiv. 2:4, 7) Iye amadziwa kuti tingayambirenso kukhala ndi chikondi ngati chimene tinali nacho titangodziwa kumene choonadi.
4. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi?
4 Nkhaniyi itithandiza kuona zimene tingachite kuti tipitirize kukonda Yehova komanso anthu. Kenako tiona madalitso ena omwe tingapeze chifukwa chokonda kwambiri Yehova komanso anthu ena.
PITIRIZANI KUKONDA YEHOVA
5-6. Kodi ndi mavuto ati omwe mtumwi Paulo anakumana nawo pa utumiki wake, nanga n’chiyani chinamuthandiza kupitirizabe kutumikira Yehova?
5 Mtumwi Paulo ankasangalala potumikira Yehova, koma ankakumananso ndi mavuto ambiri. Nthawi zambiri iye ankayenda maulendo ataliatali ndipo nthawi imeneyo sizinali zophweka kuchita zimenezi. Pa maulendo akewa, nthawi zina ankakumana ndi “zoopsa za m’mitsinje” komanso “zoopsa za achifwamba pamsewu.” Nthawi zinanso anthu otsutsa ankamuchitira zankhanza. (2 Akor. 11:23-27) Komanso si nthawi zonse pamene Akhristu anzake ankasonyeza kuti ankayamikira khama lake lofuna kuwathandiza.—2 Akor. 10:10; Afil. 4:15.
6 N’chiyani chinathandiza Paulo kuti apitirizebe kutumikira Yehova? Iye anaphunzira zambiri zokhudza makhalidwe a Yehova m’Malemba komanso pa zimene zinamuchitikira. Paulo sankakayikira kuti Yehova Mulungu ankamukonda. (Aroma 8:38, 39; Aef. 2:4, 5) Ndipo nayenso anayamba kumukonda kwambiri. Paulo anasonyeza kuti ankakonda Yehova ‘potumikira oyera ndi kupitiriza kuwatumikira.’—Aheb. 6:10.
7. Kodi ndi chinthu chimodzi chiti chomwe chingatithandize kuti tizikonda kwambiri Yehova?
7 Chinthu china chomwe chingatithandize kuti tipitirize kukonda kwambiri Mulungu ndi kuphunzira Mawu ake mwakhama. Mukamawerenga Baibulo, muziyesa kuona mmene zomwe mwawerengazo zikukuthandizirani kudziwa zokhudza Yehova. Muzidzifunsa kuti: ‘Kodi nkhaniyi ikusonyeza bwanji kuti Yehova amandikonda? Kodi ikundithandiza kudziwa zifukwa ziti zondichititsa kukonda Yehova?’
8. Kodi pemphero lingatithandize bwanji kuti tipitirize kukonda kwambiri Mulungu wathu?
8 Kupemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima nthawi zonse kungatithandizenso kuti tizimukonda kwambiri. (Sal. 25:4, 5) Tikamatero, iye amayankha mapemphero athu. (1 Yoh. 3:21, 22) Mlongo wina wa ku Asia dzina lake Khanh, ananena kuti: “Poyamba ndinkangokonda Yehova chifukwa cha zimene ndinkadziwa zokhudza iye, koma ndinayamba kumukondanso kwambiri nditaona mmene ankayankhira mapemphero anga. Zimenezi zinandilimbikitsa kuti ndizichita zinthu zomwe zimamusangalatsa.”b
MUZIKONDA KWAMBIRI ANTHU ENA
9. Kodi Timoteyo anasonyeza bwanji kuti ankapita patsogolo pa nkhani yokonda abale ndi alongo?
9 Patapita zaka kuchokera pamene anakhala Mkhristu, Paulo anakumana ndi wachinyamata wina dzina lake Timoteyo. Wachinyamatayu ankakonda Yehova komanso anthu. Paulo anauza Akhristu a ku Filipi kuti: “Ndilibe wina wamtima ngati [Timoteyo], amene angasamaledi za inu moona mtima.” (Afil. 2:20) Palembali, iye sankanena zokhudza mmene Timoteyo ankachitira zinthu mwadongosolo kapena luso lake lolankhula pagulu, koma n’zoonekeratu kuti ankachita chidwi ndi mmene Timoteyo ankakondera abale ndi alongo. Mosakayikira, abale ndi alongo ankayembekezera mwachidwi maulendo a Timoteyo okachezera mipingo yawo.—1 Akor. 4:17.
10. Kodi Anna ndi mwamuna wake anasonyeza bwanji kuti ankakonda abale ndi alongo awo?
10 Ifenso timafunafuna njira zothandizira abale ndi alongo athu. (Aheb. 13:16) Taganizirani zimene zinachitikira Anna amene tamutchula munkhani yapita ija. Pambuyo pa mphepo ina yamkuntho, iye ndi mwamuna wake anapita kukaona banja lina la Mboni ndipo anapeza kuti denga la nyumba yawo linali litawonongeka. Chifukwa cha mphepoyo, zovala zawo zonse zinada. Anna ananena kuti: “Tinatenga zovala zawozo n’kukazichapa, ndipo tinakawapatsa titazisita komanso kuzipinda bwinobwino. Kwa ife, zimenezi sizinali nkhani yaikulu, koma zinathandiza kuti tizigwirizana nawo kwambiri mpaka pano.” Kukonda abale ndi alongo awo, kunachititsa Anna ndi mwamuna wake kuti awathandize.—1 Yoh. 3:17, 18.
11. (a) Kodi zimene timachita posonyeza ena chikondi zimawakhudza bwanji? (b) Mogwirizana ndi Miyambo 19:17, kodi Yehova amatani tikamasonyeza ena chikondi?
11 Tikamakonda komanso kukomera mtima anthu ena, nthawi zambiri iwo amaona zimene timachita potsanzira Yehova pa nkhani ya mmene amaganizira komanso kuchitira zinthu. Ndipo akhoza kuyamikira kwambiri zimene tingachite powasonyeza kukoma mtima kuposa mmene tingaganizire. Khanh yemwe tamutchula kale uja, amasangalala akakumbukira mmene ena anamuthandizira. Iye anati: “Ndimayamikira kwambiri alongo onse omwe ankanditenga akamakalalikira. Ankabwera kudzanditenga kunyumba, kundiitanira chakudya komanso kudzandisiya. Panopa ndi pamene ndimazindikira kuti ankafunika kuchita khama kuti azichita zimenezi ndipo ankazichita chifukwa cha chikondi.” N’zoona kuti si onse amene angayamikire zomwe tawachitira. Ponena za anthu amene ankamuthandiza, Khanh ananena kuti: “Ndimalakalaka nditawabwezera zabwino zomwe anandichitira, koma sindimadziwa kumene onsewa amakhala. Komabe, Yehova amadziwa ndipo ndimamupempha kuti aziwadalitsa.” Khanh ananena zoona. Yehova amadziwa ngakhale zinthu zing’onozing’ono zomwe timachita pokomera mtima ena. Iye amaona kuti zimenezi ndi nsembe yamtengo wapatali komanso ngongole yomwe adzabweze.—Werengani Miyambo 19:17.
12. Kodi abale angasonyeze bwanji kuti amakonda ena mumpingo? (Onaninso zithunzi.)
12 Ngati ndinu m’bale, kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakonda ena komanso kudzipereka kuti muwathandize? M’bale wina wachinyamata dzina lake Jordan anafunsa mkulu kuti amuthandize kudziwa zimene angachite kuti azithandiza ena mumpingo. Mkuluyu anamuyamikira chifukwa cha zimene iye ankakwanitsa kuchita ndipo anamupatsa malangizo okhudza zimene angachite kuti apitirize kuchita zimenezi. Iye anauza Jordan kuti azifika mwamsanga ku Nyumba ya Ufumu n’cholinga choti azipereka moni, aziyankha pamisonkhano, nthawi zonse azilalikira ndi anthu a m’kagulu kake ka utumiki komanso azifufuza njira zothandizira ena. Jordan atayamba kutsatira malangizowa, sikuti ankangophunzira maluso atsopano, koma anayambanso kukonda kwambiri abale ndi alongo ake. Iye anaphunzira mfundo yakuti si kuti m’bale akakhala mtumiki wothandiza amayamba kuthandiza ena, koma amapitiriza kuthandiza ena.—1 Tim. 3:8-10, 13.
13. Kodi chikondi chinathandiza bwanji m’bale wina dzina lake Christian kuti ayambirenso kutumikira monga mkulu?
13 Bwanji ngati m’mbuyomu munatumikirapo ngati mkulu kapena mtumiki wothandiza? Yehova amakumbukira zimene munkachita pomutumikira ndiponso kuti munkachita zimenezo chifukwa cha chikondi. (1 Akor. 15:58) Iye amaonanso chikondi chomwe mukupitiriza kusonyeza. M’bale wina dzina lake Christian anakhumudwa ataimitsidwa kutumikira monga mkulu. Komabe, iye anafotokoza kuti, “Ndinasankha kuti ndizichita zonse zomwe ndingathe potumikira Yehova chifukwa chomukonda, kaya ndili pa udindo kapena ayi.” Patapita nthawi, iye anaikidwanso kukhala mkulu. Christian anavomereza kuti: “Ndinkazengereza kuti ndivomerenso kutumikira. Koma ndinaona kuti ngati Yehova mwachifundo chake wandilola kuti nditumikirenso ngati mkulu, ndiyenera kutumikira chifukwa chokonda iyeyo komanso abale ndi alongo anga.”
14. Kodi mukuphunzira chiyani pa zimene ananena mlongo wina wa ku Georgia?
14 Atumiki a Yehova amasonyezanso kuti amakonda anthu ena. (Mat. 22:37-39) Mwachitsanzo, mlongo wina wa ku Georgia dzina lake Elena, ananena kuti: “Poyamba ndinkangolalikira chifukwa chokonda Yehova. Koma pamene ndinayamba kukonda kwambiri Atate wanga wakumwamba, ndinayambanso kukonda kwambiri anthu. Ndinkayesa kuganizira mavuto amene akukumana nawo komanso nkhani zimene zingawafike pamtima. Ndikamachita kwambiri zimenezi, ndi pamenenso ndinkafunitsitsa kuwathandiza.”—Aroma 10:13-15.
MADALITSO OMWE TINGAPEZE CHIFUKWA CHOKONDA ENA
15-16. Mogwirizana ndi zithunzi, kodi ndi madalitso ati omwe timapeza chifukwa chokonda ena?
15 Tikamakonda abale ndi alongo athu, timathandizanso anthu ena. Mliri wa COVID-19 utangoyamba, m’bale wina dzina lake Paolo ndi mkazi wake anathandiza alongo ambiri achikulire kudziwa mmene angagwiritsire ntchito zipangizo zawo zamakono polalikira. Mlongo wina yemwe poyamba zinkamuvuta kugwiritsa ntchito chipangizo chake chamakono anadziwa mmene angachitire zimenezi. Chifukwa cha izi, iye anakwanitsa kuitanira achibale ake ku Chikumbutso ndipo okwana 60 anachita nawo mwambowu kudzera pa vidiyokomfelensi. Zimene Paolo ndi mkazi wake anachita zinathandiza kwambiri mlongoyu komanso achibale ake. Patapita nthawi, mlongoyu analembera Paolo kuti: “Zikomo chifukwa chophunzitsa achikulirefe. Sindidzaiwala mmene Yehova amasonyezera kuti amatiganizira komanso khama lanu.”
16 Zochitika ngati zimenezi zinaphunzitsa Paolo mfundo yofunika kwambiri. Iye anakumbutsidwa kuti chikondi n’chofunika kwambiri kuposa kudziwa zinthu kapena luso lachibadwa. Iye anati: “Poyamba ndinali woyang’anira dera. Panopa ndazindikira kuti ngakhale kuti mwina ofalitsa anaiwala nkhani zomwe ndinkakamba, amakumbukirabe zomwe ndinkachita powathandiza.”
17. Kodi tikamasonyeza ena chikondi timathandizanso ndani?
17 Tikamasonyeza ena chikondi, ifenso timapindula m’njira imene sitimaganizira. Jonathan, yemwe amakhala ku New Zealand, anaona kuti zimenezi ndi zoona. Loweruka lina masana kukutentha, iye anaona mpainiya wina akulalikira m’mbali mwa msewu. Kenako anaganiza kuti azilowa mu utumiki limodzi ndi mpainiyayo masana a Loweruka lililonse. Pa nthawiyi sanazindikire kuti zimene anachita mokoma mtimazi zidzamuthandiza iyeyo. Jonathan anavomereza kuti, “Pa nthawiyo sindinkakonda kulalikira. Koma nditaona mmene mpainiyayo ankaphunzitsira komanso kuti zinthu zinkamuyendera bwino mu utumiki, ndinayamba kukonda kwambiri ntchito yolalikira. Iye anakhala mnzanga wabwino yemwe anandithandiza kuti ndikhale wolimba mwauzimu, ndizikonda kulalikira komanso ndikhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova.”
18. Kodi Yehova amafuna kuti tizichita chiyani?
18 Yehova amafuna kuti tizimukonda kwambiri komanso tizikonda ena. Monga mmene taphunzirira, tingamakonde kwambiri Yehova ngati timawerenga komanso kuganizira Mawu ake, ndiponso kupemphera kwa iye nthawi zonse. Tikhozanso kumakonda kwambiri abale ndi alongo athu powathandiza m’njira zosiyanasiyana. Pamene chikondi chathu chikukula, tidzakhala pa ubwenzi wabwino kwambiri ndi Yehova komanso banja lathu lauzimu. Ndipo tidzasangalala ndi zimenezi mpaka kalekale.
NYIMBO NA. 109 Tizikondana Kwambiri Kuchokera Mumtima
a Kaya tangophunzira kumene choonadi kapena takhala tikutumikira Yehova kwa nthawi yaitali, tonsefe timafunika kupitiriza kupita patsogolo. Munkhaniyi tikambirana njira yofunika imene tingachitire zimenezi, yomwe ndi kupitiriza kukonda Yehova ndi anthu. Tikamaphunzira, ganizirani mmene mwasonyezera kale kuti mukupita patsogolo komanso mmene mungapitirizire kuchita zimenezi.
b Mayina ena asinthidwa.