Thandizani Ena Kuyenda Moyenera Yehova
“Ifenso, . . . sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, . . . kuti mukayende koyenera Ambuye kukam’kondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino.”—AKOLOSE 1:9, 10.
1, 2. Kodi n’chiyani makamaka chimene chingatipatse chimwemwe ndi chikhutiro?
“TIMAKHALA mu kalavani pafamu. Mwa kukhala ndi moyo wosalira zambiri, timakhala ndi nthaŵi yambiri yofikira anthu ndi uthenga wabwino. Takhala ndi mwayi waukulu wopeza madalitso a kuthandiza anthu ambiri kupatulira miyoyo yawo kwa Yehova.”—Mwamuna ndi mkazi wake, atumiki anthaŵi zonse ku South Africa.
2 Kodi simungavomereze kuti kuthandiza anthu ena kumadzetsa chimwemwe? Ena amayesa nthaŵi zonse kuthandiza odwala, osauka, ndi osungulumwa—ndipo akatero amakhutira m’maganizo. Akristu oona ali otsimikiza kuti kuuza ena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu ndilo thandizo lalikulu kopambana limene angapereke. Ndi njira yokhayi imene ingathandize ena kuti alandire dipo la Yesu, akhale ndi unansi wabwino ndi Mulungu, ndi kuti akhale ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.—Machitidwe 3:19-21; 13:48.
3. Kodi ndi thandizo lotani limene tiyenera kuliganizira?
3 Komabe, bwanji nanga za kuthandiza aja amene akutumikira kale Mulungu, omwe akuyenda pa “Njirayo”? (Machitidwe 19:9) N’zoona kuti nthaŵi zonse mwachita nawo chidwi kwambiri, koma mwina simungaone mmene mungachitire zoposerapo kapena kuwonjezera thandizo lomwe mukupereka. Mwinamwake mkhalidwe wanu ungaoneke kuti ukukulepheretsani kuwathandiza mokwanira, mwakutero kuchepetsa chikhutiro chimene mungakhale nacho. (Machitidwe 20:35) Pa mbali zonse ziŵirizi, tikhoza kutengapo phunziro m’buku la Akolose.
4. (a) Kodi Paulo polembera Akolose anali mumkhalidwe wotani? (b) Kodi Epafra anachita mbali yanji?
4 Pamene mtumwi Paulo amalembera Akristu a ku Kolose, iye anali paukaidi wapanyumba ku Roma, ngakhale kuti amatha kulandira alendo. Monga momwe mungayembekezere, Paulo anagwiritsa ntchito ufulu wochepa umene anali nawo kulalikira za Ufumu wa Mulungu. (Machitidwe 28:16-31) Akristu anzake anatha kum’chezera Paulo, mwina ena a iwo amamangidwa naye limodzi nthaŵi zina. (Akolose 1:7, 8; 4:10) Mmodzi anali mlaliki wokangalika Epafra wochokera ku mzinda wa Kolose ku Frugiya, m’dziko la malo okwera kum’maŵa kwa Efeso mu Asia Minor (lerolino ndi Turkey). Epafra anathandiza kwambiri pokhazikitsa mpingo ku Kolose, ndipo anagwira ntchito zolimba pothandiza mipingo yapafupi ya Laodikaya ndi Herapoli. (Akolose 4:12, 13) Kodi n’chifukwa chiyani Epafra anapita kukaonana ndi Paulo ku Roma, ndipo tingatengepo phunziro lanji pa kulabadira kwa Paulo?
Thandizo Lenileni kwa Akolose
5. Kodi Paulo analemberanji zimene analembazo kwa Akolose?
5 Pofuna kukakambirana ndi Paulo za mikhalidwe ya mumpingo wa Kolose, Epafra anayenda ulendo wovuta wa ku Roma. Iye anasimba za chikhulupiriro cha Akristuwo, chikondi chawo, ndi khama lawo la kulalikira. (Akolose 1:4-8) Komabe, ayenera kuti anafotokozanso za mikhalidwe yoipa yododometsa moyo wauzimu wa Akolosewo. Paulo anayankha mwa kulemba kalata youziridwa imene inadzudzula malingaliro ena amene anali kufalitsidwa ndi aphunzitsi onyenga. Iye anatsindika kwambiri za mbali yofunika kwambiri imene Yesu Kristu ayenera kuchita.a Kodi thandizo lakelo linali kungotsindika mfundo zazikulu za m’Baibulo? Ndi njira zina ziti zimene akanathandizira Akolosewo, ndipo tingatengepo maphunziro otani pankhani ya kuthandiza ena?
6. Kodi Paulo anatsindika makamaka za chiyani m’kalata yake yopita kwa Akolose?
6 Kumayambiriro kwa kalata yake, Paulo anaunika mtundu wina wa thandizo umene tingaunyalanyaze. Inali njira yoperekera thandizo lenileni kuchokera kutali, inde, Paulo ndi Epafra anali kutali kwambiri ndi Kolose. Paulo anapereka chitsimikizo chakuti: “Tiyamika Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu ndi kupempherera inu nthaŵi zonse.” Inde, ameneŵa anali mapemphero achindunji kwa Akristu a ku Kolose. Paulo anawonjezera kuti: “Mwa ichi ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu.”—Akolose 1:3, 9.
7, 8. Kodi ndi nkhani iti imene imatchulidwa kaŵirikaŵiri m’mapemphero aumwini ndi a mpingo?
7 Timadziŵa kuti Yehova ndi “Wakumva pemphero,” choncho tiyenera kukhala ndi chidaliro chakuti ali wokonzeka kumva mapemphero athu amene timapereka mogwirizana ndi chifuniro chake. (Salmo 65:2; 86:6; Miyambo 15:8, 29; 1 Yohane 5:14) Nanga bwanji pankhani ya kupempherera ena? Kodi mapemphero athu amakhala otani?
8 Kaŵirikaŵiri, tingaganize ndi kupempherera ‘abale athu ali m’dziko.’ (1 Petro 5:9) Kapena tingam’fikire Yehova popempherera Akristu ndi anthu ena amene ali kudera kumene kwachitika ngozi inayake. Pamene ophunzira a m’zaka za zana loyamba okhala kumadera ena anamva za chilala ku Yudeya, ayenera kuti anapereka mapemphero ambirimbiri kaamba ka abale awo ngakhale asanawatumizire ndalama za chithandizo. (Machitidwe 11:27-30) M’masiku athu ano, mapemphero opempherera abale onse padziko kapena gulu linalake la abale amamveka kaŵirikaŵiri kumisonkhano yachikristu, kumene ambiri afunikira kumva ndi kutha kunena kuti “Amen.”—1 Akorinto 14:16.
Tchulani Zinthu Mwachindunji M’pemphero
9, 10. (a) Kodi ndi zitsanzo ziti zomwe zimasonyeza kuti kupempherera anthu mwachindunji n’koyenera? (b) Kodi zinachitika motani kuti Paulo afunikire kum’pempherera mwachindunji?
9 Komabe, Baibulo limatipatsa zitsanzo za mapemphero opempherera anthu ena mwa kutchula mayina a anthuwo, mmodzi ndi mmodzi. Ganizirani za mawu a Yesu pa Luka 22:31, 32. Pamenepo iye anali limodzi ndi atumwi ake 11 okhulupirikawo. Onsewo anafunikira thandizo la Mulungu kuti akathane ndi nthaŵi zovuta zomwe zinali patsogolo pawo, ndipo Yesu anawapempherera. (Yohane 17:9-14) Komabe, Yesu anatchulapo Petro, akumapempherera wophunzirayo mwapadera. Nazi zitsanzo zina: Elisa anapemphera kuti Mulungu athandize munthu mmodzi payekha, mtumiki wake. (2 Mafumu 6:15-17) Mtumwi Yohane anapemphera kuti Gayo akhalebe ndi moyo wathanzi wakuthupi ndi wauzimu. (3 Yohane 1, 2) Ndipo mapemphero ena anali opempherera magulu ena a anthu.—Yobu 42:7, 8; Luka 6:28; Machitidwe 7:60; 1 Timoteo 2:1, 2.
10 Makalata a Paulo amasonyeza nkhani ya mapemphero achindunji kwambiri. Iye anapempha kuti pemphero liperekedwe lopempherera iye yekha kapena iye limodzi ndi anzake. Pa Akolose 4:2, 3 timaŵerenga kuti: “Chitani khama m’kupemphera, nimudikire momwemo ndi chiyamiko; ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mawu, kuti tilankhule chinsinsi cha Kristu; chimenenso ndikhalira m’ndende.” Onaninso zitsanzo zinazi: Aroma 15:30; 1 Atesalonika 5:25; 2 Atesalonika 3:1; Ahebri 13:18.
11. Pamene Epafra anali ku Roma, kodi ankapempherera ndani?
11 Mnzake wa Paulo ku Roma anachitanso chimodzimodzi. “Akulankhulani inu Epafra ndiye wa kwa inu, . . . wakulimbira chifukwa cha inu m’mapemphero ake masiku onse.” (Akolose 4:12) Mawu amene anawamasulira kuti “wakulimbira” angatanthauze “kulimbikira,” monga ankachitira katswiri wa maseŵero a pidigoli m’nthaŵi zamakedzana. Kodi Epafra ankangopempherera moona mtima okhulupirira onse padziko kapena ankapemphereranso olambira oona paokha omwe ankakhala ku Asia Minor? Paulo anasonyeza kuti Epafra ankapempherera mwachindunji aja okhala mu Kolose. Epafra ankadziŵa za mkhalidwe wawo. Sitikudziŵa mayina a onsewo, komanso sitikudziŵa mavuto amene anakumana nawo, koma tangoyerekezani zothekera. Mwinamwake Lino wachinyamatayo ankalimbana ndi nzeru za filosofi zimene zinafala panthaŵiyo. Ndiponso Rufo mwina anafunikira nyonga yolimbana ndi chikoka cha zizoloŵezi zake zakale zachiyuda. Pokhala ndi mwamuna wosakhulupirira, kodi Persida anafunikira chipiriro ndi nzeru kuti athe kulera ana ake mwa Ambuye? Ndipo kodi Asunkrito, amene anadwala matenda osachira, anafunikira chitonthozo choŵirikiza? Inde, Epafra anali kuwadziŵa a mumpingo wake, ndipo anawapempherera mwakhama chifukwa chakuti iye, limodzi ndi Paulo, anafuna kuti odzipereka oterowo ayende moyenera Yehova.
12. Kodi tingapereke motani mapemphero aumwini achindunji kwambiri?
12 Kodi mukuonapo chitsanzo kwa ife—njira imene tingathandizire ena? Monga taonera, mapemphero apoyera pamisonkhano yachikristu kaŵirikaŵiri sakhala achindunji kwenikweni, chifukwa cha omvetsera osiyanasiyana. Koma mapemphero athu aumwini ndi a banja angathe kukhala achindunji kwambiri. Ngakhale kuti nthaŵi zina tingapemphe Mulungu kutsogolera ndi kudalitsa oyang’anira oyendayenda onse kapena abusa auzimu, kodi nthaŵi zina sitingakhale olunjika kwambiri? Mwachitsanzo, bwanji osapemphera mwa kutchula dzina la woyang’anira dera amene akuchezera mpingo wanu kapena wochititsa Phunziro la Buku la Mpingo? Afilipi 2:25-28 ndi 1 Timoteo 5:23 amasonyeza nkhaŵa ya Paulo kwa munthu payekha ponena za thanzi la Timoteo ndi Epafrodito. Kodi ifenso tingasonyeze chidwi ngati chimenecho kwa odwala amene timawadziŵa ndi mayina awo?
13. Kodi ndi nkhani ziti zoyenera kutchula m’mapemphero athu aumwini?
13 N’zoona kuti tiyenera kupeŵa kuloŵerera nkhani za ena, koma ndi koyenera kuti m’mapemphero athu tionetse chidwi chenicheni kwa aja amene timawadziŵa ndi kuwadera nkhaŵa. (1 Timoteo 5:13; 1 Petro 4:15) Mbale angachotsedwe ntchito, ndipo sitingathe kum’patsa ina. Komabe, tikhoza kum’tchula dzina m’mapemphero athu ndi kunena za vuto lakelo. (Salmo 37:25; Miyambo 10:3) Kodi tikudziŵapo za mlongo wina wosakwatiŵa amene wafika msinkhu wachikulirepo koma wopanda mwamuna ndi ana chifukwa chokaniratu kukwatiŵa ndi wina aliyense “koma mwa Ambuye”? (1 Akorinto 7:39) Bwanji osapempha Yehova m’mapemphero anu aumwini kuti am’dalitse ndi kum’thandiza kukhalabe wokhulupirika mu utumiki wake? Chitsanzo china, akulu aŵiri angakhale atapereka uphungu kwa mbale wina amene analakwa. Bwanji aliyense wa akuluwo osam’tchula dzina mbaleyo m’mapemphero awo aumwini nthaŵi ndi nthaŵi?
14. Kodi mapemphero achindunji amakhudzana motani ndi kuthandiza ena?
14 Mipata ilipo yambiri yakuti muphatikize m’mapemphero anu aumwini anthu amene mumadziŵa kuti amafunikira chichirikizo cha Yehova, chitonthozo chake, nzeru yake, ndi mzimu wake woyera, kapena chilichonse cha zipatso za mzimuwo. Chifukwa cha mtunda kapena zoletsa zina, mungaone kukhala wopereŵera pa chithandizo chachindunji chimene mungapereke. Koma musaiŵale kuwapempherera abale ndi alongo anu. Mumadziŵa kuti amafuna kuyenda moyenera Yehova, koma kuti atero mosalekeza angafunikiredi thandizo. Mbali yofunikira kwambiri ya thandizolo ndi mapemphero anu.—Salmo 18:2; 20:1, 2; 34:15; 46:1; 121:1-3.
Yesetsani Kulimbikitsa Ena
15. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chidwi pa chigawo chomaliza cha Akolose?
15 Komabe, pemphero lakhama ndi lachindunji si ndiyo njira yokha yothandizira ena, makamaka amene ali pafupi nanu amenenso mumawakonda. Buku la Akolose limamveketsa bwino zimenezo. Akatswiri ambiri a Baibulo amanena kuti Paulo atapereka malangizo achiphunzitso ndi uphungu wogwira ntchito, anawonjezera malonje kapena moni wakewake. (Akolose 4:7-18) Mosiyana ndi zimenezo, taona kale kuti ndime yomalizayi ya buku limeneli ili ndi uphungu wapadera, ndipo pali zambiri zoti n’kuphunzira pa chigawo chimenechi.
16, 17. Kodi tinganene chiyani za abale otchulidwa pa Akolose 4:10, 11?
16 Paulo analemba kuti: “Aristarko wam’ndende mnzanga akulankhulani inu, ndi Marko, msuwani wa Barnaba (amene munalandira zolamulira za kwa iye; akafika kwanu, mum’landire iye), ndi Yesu, wotchedwa Yusto, ndiwo a mdulidwe; iwo okha ndiwo antchito anzanga a mu Ufumu wa Mulungu, ndiwo akundikhalira ine chonditonthoza mtima.”—Akolose 4:10, 11.
17 Kumeneko Paulo anazindikira abale amene anafunikira kuwaganizira mwapadera. Anati iwo anali pakati pa odulidwa, a mtundu wachiyuda. Ku Roma kunali Ayuda odulidwa ambiri, ndipo ena panthaŵiyo anakhala Akristu. Chikhalirechobe, amene Paulo anawatchulawo anam’thandiza iye. Zikuoneka kuti iwo sanazengereze kuyanjana ndi Akristu amene sanali Ayuda, ndipo ayenera kuti anasangalala pogwira ntchito ndi Paulo yolalikira kwa Akunja.—Aroma 11:13; Agalatiya 1:16; 2:11-14.
18. Kodi Paulo anawathokoza motani ena amene anali limodzi naye?
18 Taonani ndemanga ya Paulo yakuti: “Ndiwo akundikhalira ine chonditonthoza mtima.” Iye anagwiritsa ntchito liwu lachigiriki limene limapezeka pokhapo m’Baibulo. Otembenuza ambiri amalimasulira kuti “kutonthoza.” Komabe, pali liwu lina lachigiriki (pa·ra·ka·le’o) limene kaŵirikaŵiri limamasuliridwa kuti “kutonthoza.” Paulo anagwiritsa ntchito liwu limenelo m’malo ena a kalata imeneyi koma osati pa Akolose 4:11.—Mateyu 5:4; Machitidwe 4:36; 9:31; 2 Akorinto 1:4; Akolose 2:2; 4:8.
19, 20. (a) Kodi lingaliro lake ndi lotani la mawu amene Paulo anagwiritsa ntchito ponena za abale omwe ankam’thandiza ku Roma? (b) Kodi abalewo ayenera kuti anam’thandiza Paulo m’njira zotani?
19 Aja amene Paulo anawatchula ayenera kuti anapereka chitonthozo choposa chija chapakamwa chabe. Liwu lachigiriki lomasuliridwa kuti “chonditonthoza mtima” pa Akolose 4:11 nthaŵi zina analigwiritsa ntchito m’zolemba zina kutanthauza mankhwala othandiza munthu wovutika maganizo. Baibulo lakuti New Life Version limati: “Anandithandiza kwabasi!” Baibulo la Today’s English Version limanena mawu akuti: “Anali chithandizo chachikulu kwa ine.” Kodi abale achikristu amenewo omwe anam’yandikira Paulo ayenera kuti anachitanji pom’thandiza?
20 Paulo anatha kukhala ndi alendo, koma panali zinthu zambiri zimene sakanatha kuchita, monga kukagula zinthu zofunikira—chakudya ndi zovala m’nyengo yachisanu. Kodi mipukutu ya Malemba oti aziŵerenga akanaipeza bwanji, kapena akanagula bwanji zolembera. (2 Timoteo 4:13) Kodi simukuwaona abalewo m’maganizo mwanu akuthandiza Paulo pa zosoŵa zake, kum’chitira zinthu ngati kukam’gulira zinthu ndi kum’pitira kumene anawatuma? Mwina ankafuna kukayendera ndi kukalimbikitsa mpingo wakutiwakuti. Pokhala womangidwa, sakanatha, choncho abalewo anamuyendera maulendowo Paulo, kunyamula mauthenga ake, ndi kum’bweretsera malipoti. Zolimbikitsa kwabasi!
21, 22. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chidwi pa mawu a pa Akolose 4:11? (b) Kodi ndi njira zina ziti zimene tingagwiritse ntchito chitsanzo cha aja omwe anali ndi Paulo?
21 Zimene Paulo analemba za kukhala ‘chotonthoza mtima’ zimatithandiza kuzindikira mmene tingathandizire ena. Iwo angakhale akuyenda moyenera Yehova ponena za miyezo ya makhalidwe, kufika pamisonkhano yachikristu, ndi kutenga mbali m’ntchito yolalikira. Pazimenezo tiyenera kuwathokoza. Komabe, kodi tingachite zoposerapo, tikumakhala ‘chotonthoza mtima’ monga mmene ena anakhalira kwa Paulo?
22 Ngati mukudziŵapo mlongo amene mwanzeru wachita mogwirizana ndi uphungu wakuti ‘asunge unamwali wake’ koma yemwe tsopano alibe achibale apafupi, kodi mungam’phatikize m’zochitika zina za banja lanu, mwinamwake kumuitanira kuchakudya kapena kukaphwando ka mabwenzi kapena achibale? (1 Akorinto 7:37, NW) Bwanji osam’limbikitsa kuti apite nanu paulendo wa kumsonkhano kapena kutchuthi. Kapena m’pempheni kuti akakuperekezeni panthaŵi yoyenera kokagula zakudya. Mungachitenso chimodzimodzi kwa akazi amasiye kapena amuna ofedwa akazi awo, kapena aja amene tsopano sakuthanso kuyendetsa galimoto. Kungakhale kopindulitsa kwa inu kumvetsera zokumana nazo zawo kapena kuphunzira luso lawo pa zinthu za masiku onse ngati kusankha zipatso zabwino kapena kusankha zovala za ana. (Levitiko 19:32; Miyambo 16:31) Chotsatirapo chachibadwa chingakhale kuzama kwa ubwenzi wanu. Zikatero kungakhale kosawavuta kukupemphani kuti mukawagulire mankhwala, kapena zina zotero. Abale aja omwe anali ndi Paulo ku Roma ayenera kuti anapereka chithandizo chenicheni, cholimbikitsa, chimenenso inu mungapereke. Kalelo ndi tsopano lino dalitso lina n’lakuti chikondi chimalimba, ndipo ndife otsimikiza mtima kutumikira Yehova mogwirizana ndi mokhulupirika.
23. Ndi bwino kuti aliyense wa ife aziwonongera nthaŵi yake pochita chiyani?
23 Aliyense wa ife akhoza kuganizira za mikhalidwe yomwe yatchulidwa m’nkhani ino. Iyo yangokhala zitsanzo, koma ingatikumbutse zochitika zenizeni zimene tingakhalepo ‘otonthoza mtima’ kwa abale ndi alongo athu. Mfundo si yakuti ifenso titengere maganizo a anthu olimbikitsa za kusintha umoyo ndi chikhalidwe cha anthu ayi. Chimenecho sichinali cholinga cha abale otchulidwa pa Akolose 4:10, 11. Iwo anali ‘antchito anzawo a mu Ufumu wa Mulungu.’ Chilimbikitso chimene anapereka chimakhudzana kwambiri ndi mfundo imeneyo. Zikhalenso chimodzimodzi kwa ife.
24. Kodi chifukwa chachikulu n’chiyani chimene timapempherera ndi kuyesetsa kulimbikitsa ena?
24 Chifukwa chimene timatchulira ena mayina awo m’mapemphero athu aumwini ndi kuyesetsa kuwalimbikitsa ndi ichi: Timakhulupirira kuti abale ndi alongo athu amafuna ‘kuyenda moyenera Ambuye kukam’kondweretsa monsemo.’ (Akolose 1:10) Mfundo imeneyi imakhudzana ndi kanthu kena kamene Paulo anatchula polemba za mapemphero a Epafra okhudza Akolose, kuti akathe ‘kuima amphumphu ndi otsimikiza kotheratu za chifuniro chonse cha Mulungu.’ (Akolose 4:12, NW) Kodi aliyense wa ife payekha angachite zimenezo motani? Tiyeni tione.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, masamba 490-1, ndi “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial,” masamba 226-8, ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mwazindikira?
• Ndi motani mmene tingakhalire othandiza kwambiri m’mapemphero athu aumwini?
• Kodi Akristu ena anali ‘otonthoza mtima’ motani kwa Paulo?
• Kodi ndi m’mikhalidwe iti imene tingakhale ‘otonthoza mtima’?
• Kodi cholinga chenicheni n’chotani chimene timapempherera ndi kuyesetsa kulimbikitsa abale ndi alongo athu?
[Chithunzi patsamba 18]
Kodi mungatengeko Mkristu wina pamene banja lanu likupita kokacheza?
[Mawu a Chithunzi]
Ndi chilolezo cha Green Chimney’s Farm