Sungani Chikhulupiriro mwa Mulungu ndi Kristu
Mfundo Zazikulu Kuchokera mu Akolose
CHIKHULUPIRIRO mwa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu nchofunika kaamba ka chipulumutso. Koma kusunga chikhulupiriro choterocho kuli chitokoso. Zimenezo zidali tero kwa Akristu a ku Kolose, mzinda wokhala kum’mawa kwa Efeso mu Asia Minor. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti kumeneko aphunzitsi onyenga anakhulupirira molakwika kuti chipulumutso chinadalira pa mdulidwe, chimene munthu amadya, ndikusunga zikumbikiro zakutizakuti.
Pamenepo, nchomvekera kuti mtumwi Paulo adali wodera nkhaŵa za ubwino wauzimu wa Akristu a ku Kolose, ndipo anafunadi kuti iwo asunge chikhulupiriro chawo mwa Mulungu ndi Kristu. Choncho chakumapeto kwa kuikidwa m’ndende koyamba kwa mtumwiyo m’Roma (pafupifupi 60-61 C.E.), iye anawalembera Akolose kalata yolinganizidwira kutsutsa malingaliro olakwa ndikumangirira chikhulupiriro chawo. Tiyeni tiwone mmene nafenso tingapindulire ndi mawu ake achikondi.
Yamikirani Malo a Kristu
Koyambirira kwa kalata yake, Paulo anagogomezera chiyamikiro kaamba ka malo a Yesu. (1:1–2:12) Iye anawayamikira Akolose chifukwa cha chikhulupiriro chawo m’chigwirizano ndi Kristu ndi chikondi chawo cha pa akhulupiriri anzawo. Paulo anatchula za ukulu wa Kristu kukhala mwa Amene zinthu zina zonse zinalengedwa, Mutu wa mpingo, ndiwoyamba kubadwa wa akufa. Kuyanjanitsidwa ndi Mulungu kumatheketsedwa mwa Kristu, mwa iye mwabisidwa chuma chonse cha nzeru ndi chidziŵitso. Polingalira zonsezi, Akristu ayenera kuyendabe mogwirizana ndi Kristu ndipo asalole winawake kuwatenga monga mnkhole kupyolera mwa nthanthi za anthu.
Kupyolera mwa Kristu, Mulungu anachotsa Lamulo. (2:13-23) Ilo linakhomeredwa mophiphiritsira pa mtengo umene Yesu anaferapo. Ziyeneretso za Lamulo zidali kokha “mthunzi wa zirinkudzazo; koma thupi ndi la Kristu.” Mwakumamatira kwa Kristu, iwo sakalola munthu aliyense kuwalanda mphotho ya moyo wosafa kumwamba.
Yamikirani Mulungu ndi Kristu
Kenaka Paulo anafulumiza Akolose kuvala umunthu watsopano ndikugonjera ku ulamuliro wa Yesu Kristu. (3:1-17) Mwakusumika maganizo awo pa zinthu zakumwamba, iwo akakhala akuika zikondwerero zauzimu mmalo oyamba m’moyo. Ichi chinafunikira kuchotsa maganizo ndi kalankhulidwe koipa. Iwo akakhala odalitsidwa chotani nanga ngati akadziveka ndi mikhalidwe yonga ngati chifundo, kudzichepetsa maganizo, ndi chikondi! Mtendere wa Kristu ukalamulira mitima yawo ngati akachita zonse m’dzina la Yesu, akumathokoza Mulungu mwa iye.
Kuyamikira Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu kuyeneranso kusonkhezera maunansi a Mkristu ndi ena. (3:18–4:18) Akazi okwatiwa, amuna okwatira, ana, akapolo, ndi ambuye anayenera kukwaniritsa ntchito zawo moopa Mulungu ndikuzindikira Kristu. Ndipo kulimbikira m’pemphero ndi kuyenda mwanzeru nzofunika chotani nanga!
Kalata ya Paulo kwa Akolose ingatithandize kupeŵa ziphunzitso zonyenga zimene zingatilande mphotho ya moyo. Chigogomezero cha mtumwiyo pa kuzindikira ulamuliro wa Yehova ndi Mwana wake chingakhale ndi chiyambukiro chabwino pa zochita zathu ndi ena. Ndipo tatsimikiziridwa madalitso olemera ngati tisunga chikhulupiriro chathu mwa Mulungu ndi Kristu.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 26]
Kalata ya ku Laodikaya: “Pamene mudamwerenga kalata uyu,” Paulo anaŵalembera motero Akolose, “amwerengenso mu Mpingo wa ku Laodikaya, ndi inunso muwerenge wa ku Laodikaya.” (Akolose 4:16) Laodikaya udali mzinda wolemera wa kumadzulo kwa Asia Minor, wogwirizanitsidwa ndi misewu ku mizinda yonga ngati Filadelfeya ndi Efeso. Mwachidziŵikire, ntchito ya Paulo mu Efeso inafikira ku Laodikaya, ngakhale kuti iye sanatumikireko kumeneko. Iye anatumiza kalata kwa Akristu a ku Laodikaya, ngakhale kuti akatswiri ena amakhulupirira kuti inali kope ya kalata imene analembera Aefeso. Kalata ya ku Laodikaya sikupezeka m’Baibulo, mwinamwake chifukwa chakuti iribe chidziŵitso chimene tikuchifunikira lerolino, kapena mwinamwake inabwereza nsonga zomwe zinakwaniritsidwa bwino lomwe ndi makalata ena.
[Chithunzi]
Mabwinja a ku Laodikaya