‘Pitirizani Kuyenda Mogwirizana ndi Kristu’
“Chifukwa chake, monga momwe munalandira Kristu Yesu Ambuye, pitirizani kuyenda mogwirizana ndi iye.”—AKOLOSE 2:6, NW.
1, 2. (a) Kodi Baibulo limati bwanji ponena za moyo wotumikira Yehova mokhulupirika wa Enoke? (b) Kodi Yehova watithandiza motani kuyenda naye, monga momwe Akolose 2:6, 7 akusonyezera?
KODI munaonapo kamnyamata kakang’ono kakuyenda ndi atate wake? Kamnyamatako kamatsanzira zonse zimene atate wake akupanga poyenda, ndipo kamasangalala nawo kwambiri atate wake; atatewo amakathandiza, iwonso nkhope yawo itawala ndi chikondi ndi chikondwerero mwa mwana wawo. Moyenerera, Yehova amagwiritsira ntchito fanizo limeneli pofotokoza moyo wotumikira iye mokhulupirika. Mwachitsanzo, Mawu a Mulungu amanena kuti munthu wokhulupirikayo Enoke “anayendabe ndi Mulungu [woona].”—Genesis 5:24; 6:9.
2 Monga momwe atate wachikondi amathandizira mwana wawo kuyenda nawo, Yehova watipatsa thandizo labwino koposa. Anatumiza Mwana wake wobadwa yekha padziko lapansi. Pamayendedwe ake onse pamene anali pano padziko lapansi, Yesu Kristu anatsanzira ndendende Atate wake wakumwamba. (Yohane 14:9, 10; Ahebri 1:3) Choncho kuti tiyende ndi Mulungu, tiyenera kuyenda ndi Yesu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chifukwa chake monga momwe munalandira Kristu Yesu Ambuye, pitirizani kuyenda mogwirizana ndi iye, ozika mizu ndi omangirika mwa iye ndiponso okhazikika m’chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kusefukira ndi chikhulupiriro m’chiyamiko.”—Akolose 2:6, 7, NW.
3. Malinga nkunena kwa Akolose 2:6, 7, kodi nchifukwa ninji tinganene kuti kuyenda mogwirizana ndi Kristu kumafuna zambiri zoposa kungobatizidwa?
3 Chifukwa chofuna kuyenda mogwirizana ndi Kristu, kufunitsitsa kutsatira mapazi ake angwiro, ophunzira Baibulo oona mtima amabatizidwa. (Luka 3:21; Ahebri 10:7-9) Padziko lonse lapansi, mu 1997 mokha, anthu oposa 375,000 anatenga sitepe lofunika kwambiri limeneli—avareji ya anthu oposa 1,000 tsiku lililonse. Chiwonjezeko chimenechi nchochititsa chidwi! Komabe, mawu a Paulo olembedwa pa Akolose 2:6, 7 akusonyeza kuti pali zambiri zofunika poyenda mogwirizana ndi Kristu zoposa kungobatizidwa basi. Verebu lachigiriki lotembenuzidwa kuti “pitirizani kuyenda” limafotokoza chinthu chochitika mosalekeza, chosatha. Ndiponso, Paulo akuwonjezera kuti kuyenda ndi Kristu kumaloŵetsapo zinthu zinayi: kukhala wozika mizu mwa Kristu, kumangiriridwa mwa iye, kukhazikika m’chikhulupiriro, ndi kukhala ndi chiyamiko chochuluka. Tiyeni tikambitsirane mfundo zimenezi iliyonse payokha kuti tione mmene zimatithandizira kupitiriza kuyenda mogwirizana ndi Kristu.
Kodi Ndinu ‘Wozika Mizu mwa Kristu’?
4. Kodi kukhala ‘wozika mizu mwa Kristu’ kumatanthauzanji?
4 Paulo akulemba kuti choyamba tifunikira kukhala ‘ozika mizu mwa Kristu.’ (Yerekezerani ndi Mateyu 13:20, 21.) Kodi munthu angachitenji kuti akhale wozika mizu mwa Kristu? Eya, mizu ya chomera sionekera poyera, koma njofunika kwambiri ku chomeracho—imachipangitsa kukhala chokhazikika ndipo imapereka chakudya. Mofananamo, chitsanzo cha Kristu ndi chiphunzitso chake zimatisonkhezera choyamba mosaonekera, ndipo zimakhazikika m’maganizo ndi m’mitima mwathu. Mmenemo zimatikhutiritsa ndi kutilimbitsa. Pamene tizilola kulamulira maganizo athu, zochita zathu, ndi zosankha zathu, timasonkhezeredwa kupatulira moyo wathu kwa Yehova.—1 Petro 2:21.
5. Kodi tingachitenji kuti ‘tikulitse chilakolako’ cha chakudya chauzimu?
5 Yesu anali wokonda chidziŵitso chochokera kwa Mulungu. Ndipotu anachiyerekezera ndi chakudya. (Mateyu 4:4) Inde, pa Ulaliki wake wa pa Phiri, anagwira mawu mabuku asanu ndi atatu osiyanasiyana a m’Malemba Achihebri nthaŵi 21. Kuti titsanzire chitsanzo chake, tiyenera kuchita zomwe mtumwi Petro akutilimbikitsa kuchita—‘kukulitsa chilakolako’ cha chakudya chauzimu “monga makanda obadwa chatsopano.” (1 Petro 2:2, NW) Ngati khanda lobadwa chatsopano likufuna chakudya, ilo limaonetseratu kuti lili ndi njala yaikulu. Ngati panopo si mmene tikumverera ponena za chakudya chauzimu, mawu a Petro akutilimbikitsa ‘kukulitsa’ chilakolako chimenecho. Motani? Njirayi yopezeka pa Salmo 34:8 ingathandize: “Talaŵani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino.” Ngati nthaŵi zonse ‘timalaŵa’ Mawu a Yehova, Baibulo, mwinamwake kuŵerengamo chigawo china tsiku lililonse, tidzaona kuti nchokhutiritsa mwauzimu ndiponso nchabwino. M’kupita kwa nthaŵi, chilakolako chathu cha Mawuwo chidzakula.
6. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kusinkhasinkha pa zimene taŵerenga?
6 Komabe, nkofunika kwambiri kuti tikadya chakudya tizichipukusa bwino. Choncho tiyenera kusinkhasinkha pa zimene taŵerenga. (Salmo 77:11, 12) Mwachitsanzo, pamene tiŵerenga buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, mutu uliwonse umatipindulitsa kwambiri ngati tidzifunsa kuti: ‘Kodi nkhaniyi ikundisonyezanji ponena za umunthu wa Kristu, ndipo ndingautsanzire motani pamoyo wanga?’ Kusinkhasinkha kumeneko kudzatithandiza kutsatira zimene tiphunzira. Ndiyeno, tikafuna kupanga chosankha, tingadzifunse zimene Yesu akanachita. Ngati tapanga chosankha chathu motsatira zimenezo, timapereka umboni wakuti tilidi ozika mizu mwa Kristu.
7. Kodi chakudya chotafuna chauzimu tiyenera kuchiona motani?
7 Paulo akutilimbikitsanso kudya “chakudya chotafuna,” choonadi chozama cha Mawu a Mulungu. (Ahebri 5:14) Kuti tichite zimenezi, cholinga chathu choyamba chingakhale kuŵerenga Baibulo lonse lathunthu. Ndiyeno pali nkhani zina zoyenera kuphunziridwa, monga nsembe ya dipo ya Kristu, mapangano osiyanasiyana amene Yehova anapanga ndi anthu ake, kapena ena mwa mauthenga aulosi a m’Baibulo. Pali zoŵerenga zochuluka zimene zidzatithandiza kudya ndi kupukusa chakudya chotafuna chimenechi chauzimu. Kodi cholinga cha kuloŵetsa chidziŵitso chimenechi nchiyani? Sindicho kupeza chifukwa chodzitukumulira, koma kukulitsa chikondi chathu kwa Yehova ndi kuyandikira kwa iye. (1 Akorinto 8:1; Yakobo 4:8) Ngati timaloŵetsa chidziŵitso chimenechi mofunitsitsa, kuchitsatira ife eni, ndi kuthandiza nacho ena, tidzakhala tikutsanziradi Kristu. Zimenezi zidzatithandiza kukhala ozika mizu bwino mwa iye.
Kodi ‘Mukumangiriridwa mwa Kristu’?
8. Kodi ‘kumangiriridwa mwa Kristu’ kumatanthauzanji?
8 Pambali yachiŵiri ya kuyenda mogwirizana ndi Kristu, Paulo akusiya mofulumira chitsanzo choyamba ndi kupita pachina—kuchoka pachitsanzo cha chomera kupita pachitsanzo cha nyumba. Poganiza za nyumba imene ikumangidwa, sitimangoganiza za maziko ake komanso za nyumba yeniyeniyo imene ikumangidwa moonekera poyera, mwa kugwira ntchitoyo mwakhama. Mofananamo, tiyenera kuchita khama kuti tikulitse mikhalidwe ndi zizoloŵezi zofanana ndi za Kristu. Khama limenelo limaonekeratu, monga momwe Paulo analembera Timoteo kuti: “Kukula mtima kwako [“kupita patsogolo kwako,” NW] kuonekere kwa onse.” (1 Timoteo 4:15; Mateyu 5:16) Kodi ndi ziti mwa ntchito zachikristu zimene zimatimangirira?
9. (a) Kuti titsanzire Kristu mu utumiki wathu, kodi zina mwa zolinga zofikirika zimene tingaike nziti? (b) Kodi tikudziŵa motani kuti Yehova akufuna kuti tizisangalala nawo utumiki wathu?
9 Yesu anatipatsa ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa za uthenga wabwino. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Iye anapereka chitsanzo chabwino koposa mwa kulalikira molimba mtima ndiponso mogwira mtima. Nzoona kuti sitidzakhala ndi luso lofanana ndi limene anali nalo. Komabe, mtumwi Petro anatiikira cholinga ichi: “Mumpatulikitse Ambuye Kristu m’mitima yanu; okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa cha chiyembekezo chili mwa inu, komatu ndi chifatso ndi mantha.” (1 Petro 3:15) Ngati mukuona kuti simuli “okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira,” musataye mtima. Ikani zolinga zosavuta kukwaniritsa zimene zidzakuthandizani kukhala wotero m’kupita kwa nthaŵi. Kukonzekera pasadakhale kungakuthandizeni kusinthasintha ulaliki wanu ndi kuphatikizapo lemba limodzi kapena malemba aŵiri. Mungaike zolinga za kugaŵira mabuku ambiri ofotokoza Baibulo, kupanga maulendo ambiri obwereza, kapena kuyambitsa phunziro la Baibulo. Musasamale kwambiri za unyinji—monga chiŵerengero cha maola, zimene mwagaŵira, kapena maphunziro—koma luso. Kuika zolinga zosavuta kukwaniritsa ndi kuyesetsa kuzikwaniritsa kungatithandize kuti tisangalale ndi kudzipereka kwathu mu utumiki. Nzimene Yehova amafuna—kuti tizimtumikira “ndi chikondwerero.”—Salmo 100:2; yerekezerani ndi 2 Akorinto 9:7.
10. Kodi ndi ntchito zina ziti zachikristu zimene tiyenera kuchita, ndipo kodi zimenezi zimatithandiza motani?
10 Palinso ntchito zimene timachita mumpingo zimene zimatimanga mwa Kristu. Ntchito yofunika koposa ndiyo ya kusonyeza chikondi kwa wina ndi mnzake, popeza kuti chimenecho ndicho chizindikiro cha Akristu oona. (Yohane 13:34, 35) Pamene tikuphunzira, ambiri a ife timayandikana kwambiri ndi mphunzitsi wathu, ndipo zimenezo nzachibadwa. Komabe, kodi tsopano sitingatsatire uphungu wa Paulo wakuti ‘tifutukuke’ mwa kudziŵanso ena mumpingo? (2 Akorinto 6:13, NW) Akulu nawonso amafuna chikondi chathu ndi chiyamikiro chathu. Mwa kugwirizana nawo, kuwapempha ndi kulandira uphungu wawo wa m’Malemba, tidzawapeputsira zedi ntchito yawo yolimbayo. (Ahebri 13:17) Panthaŵi imodzimodziyo, zimenezi zidzatithandizira kumangiriridwa mwa Kristu.
11. Kodi ndi lingaliro loyenera lotani limene tiyenera kukhala nalo ponena za ubatizo?
11 Ubatizo nchochitika chosangalatsa! Komabe, sitiyenera kuyembekezera kuti mbali zonse za moyo wathu pambuyo pa ubatizowo zidzakhala zosangalatsa mofananamo. Mbali yaikulu ya kumangiriridwa kwathu mwa Kristu imaloŵetsapo “kuyenda bwino m’kachitidwe kamodzimodzika.” (Afilipi 3:16, NW) Zimenezi sizikutanthauza kukhala ndi moyo wosasangalatsa, wonyong’onya. Zimangotanthauza kuyendabe mumzere wowongoka—m’mawu ena, kukulitsa zizoloŵezi zabwino zauzimu ndi kuzitsatira tsiku lililonse, chaka chilichonse. Kumbukirani kuti, “iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.”—Mateyu 24:13.
Kodi ‘Mukukhazikika m’Chikhulupiriro’?
12. Kodi kukhala ‘wokhazikika m’chikhulupiriro’ kumatanthauzanji?
12 Pamfundo yake yachitatu yofotokoza kuyenda kwathu mogwirizana ndi Kristu, Paulo akutilimbikitsa kuti tikhale “okhazikika m’chikhulupiriro.” Baibulo lina limati, “otsimikizika ponena za chikhulupiriro,” popeza kuti liwu lachigiriki limene Paulo anagwiritsira ntchito lingatanthauze “kutsimikizira ndiponso kupanga chinthu kukhala chosasinthika mwalamulo.” Pamene tikukula m’chidziŵitso, timakhala ndi zifukwa zowonjezereka zoonetsetsera kuti chikhulupiriro chathu mwa Yehova Mulungu chili ndi maziko olimba ndiponso, kwenikweni, nchokhazikitsidwa mwalamulo. Chotsatirapo chake ndicho kukhazikika kolimba kwambiri. Kumakhala kovuta kwambiri kuti dziko la Satana litipambutse. Zimenezi zimatikumbutsa uphungu wa Paulo wakuti “tipitirire kutsata ukulu msinkhu.” (Ahebri 6:1) Ukulu msinkhu ndi kukhazikika zimayendera limodzi.
13, 14. (a) Kodi Akristu a m’zaka za zana loyamba a ku Kolose anayang’anizana ndi zinthu zotani zomwe zikanawononga kukhazikika kwawo? (b) Kodi mtumwi Paulo ayenera kuti anada nkhaŵa ndi chiyani?
13 Akristu a ku Kolose m’zaka za zana loyamba anayang’anizana ndi zinthu zofuna kusokoneza kukhazikika kwawo. Paulo anachenjeza kuti: “Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake [“mwa filosofi yake,” NW], ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu.” (Akolose 2:8) Paulo sanafune Akolose, amene anali atakhala nzika za “ufumu wa Mwana wa chikondi chake [cha Mulungu],” kuti atengedwe, kusokonezedwa kuchoka mumkhalidwe wawo wodalitsidwa wauzimu. (Akolose 1:13) Kusokonezedwa ndi chiyani? Paulo anatchula “filosofi,” nthaŵi yokhayo imene mawuwa akuonekera m’Baibulo. Kodi anali kunena za afilosofi achigiriki, monga Plato ndi Socrates? Ngakhale kuti ameneŵa anali oti angasokoneze Akristu oona, m’masikuwo, mawu akuti “filosofi” anali ndi matanthauzo ambiri. Nthaŵi zambiri anali kutanthauza magulu ndi masukulu ambiri ophunzitsa malingaliro osiyanasiyana—ngakhalenso magulu achipembedzo. Mwachitsanzo, Ayuda a m’zaka za zana loyamba monga Josephus ndi Philo ankatcha chipembedzo chawo kuti filosofi—mwinamwake kuti chikhale chokopa.
14 Mafilosofi ena amene anadetsa nkhaŵa Paulo, anali achipembedzo. Pambuyo pake m’chaputala chimodzimodzicho cha m’kalata yake kwa Akolose, anatchula za anthu amene ankaphunzitsa kuti, “Usaikapo dzanja, usalaŵa, usakhudza,” akumasonya ku mbali za m’Chilamulo cha Mose zimene zinathetsedwa ndi imfa ya Kristu. (Aroma 10:4) Kuwonjezera pamafilosofi achikunja, panalinso zisonkhezero zina zoti zikanawononga mkhalidwe wauzimu wa mpingowo. (Akolose 2:20-22) Paulo anachenjeza za filosofi imene inali mbali ya “zoyamba za dziko lapansi.” Ziphunzitso zonyenga zimenezo zinali za anthu.
15. Kodi tingapeŵe motani kupambutsidwa ndi malingaliro amene timayang’anizana nawo nthaŵi zambiri osagwirizana ndi malemba?
15 Kuchirikiza malingaliro ndi maganizo a anthu osazikidwa kwenikweni pa Mawu a Mulungu kungawonongetse kukhazikika kwachikristu. Ifeyo lerolino tiyenera kuchenjera ndi zinthu zowononga zimenezi. Mtumwi Yohane analimbikitsa kuti: “Okondedwa, musamakhulupirira mawu ouziridwa alionse, koma yesani mawu ouziridwawo kuona ngati achokera kwa Mulungu.” (1 Yohane 4:1, NW) Choncho ngati mnzanu wakusukulu ayesa kukutsimikizirani kuti kutsatira malamulo a m’Baibulo nkwachikale, kapena ngati mnansi wanu amafuna kukusonkhezerani kuti mukhale wokonda chuma, kapena ngati wogwira naye ntchito akukukakamizani mwamachenjera kuti mulakwire chikumbumtima chanu chophunzitsidwa Baibulo, kapenanso ngati wokhulupirira mnzanu alankhula mawu oipa ponena za ena a mumpingo malinga ndi kapenyedwe ka iyemwini, musamvetsere zimene akunena. Chotsani zimene sizikugwirizana ndi Mawu a Mulungu. Pamene tikuchita zimenezo, tidzakhalabe okhazikika pamene tikuyenda mogwirizana ndi Kristu.
“Kusefukira ndi Chikhulupiriro m’Chiyamiko”
16. Kodi mfundo yachinayi yofunika poyenda mogwirizana ndi Kristu ndi iti, ndipo tingafunse kuti chiyani?
16 Mfundo yachinayi yofunika poyenda mogwirizana ndi Kristu imene Paulo anatchula ndiyo yakuti tiyenera kukhala ‘osefukira ndi chikhulupiriro m’chiyamiko.’ (Akolose 2:7) Mawu akuti “kusefukira” amatikumbutsa za mtsinje wosefukira m’magombe ake. Zimenezi zikupereka lingaliro lakuti kwa ife monga Akristu, kuyamikira kwathu kuyenera kukhala kopitirizabe kapena kuti chinthu chachizoloŵezi. Aliyense wa ife angachite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndine woyamikira?’
17. (a) Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti tonse tili ndi zambiri zoziyamikira, ngakhale panthaŵi zovuta? (b) Kodi ndi mphatso zina ziti zochokera kwa Yehova zimene inuyo mumayamikira kwambiri?
17 Ndithudi, tonsefe tili ndi chifukwa chabwino chokhalira osefukira ndi chiyamiko kwa Yehova masiku onse. Ngakhale panthaŵi zovuta koposa, pangakhale zinthu zazing’ono zimene zingatitonthoze nthaŵi zina. Pamene bwenzi lisonyeza chifundo. Wokondedwa atikhudza motonthoza. Tulo tabwino tausiku titipatsanso nyonga. Chakudya chokoma chithetsa njala yathu. Kuimba kwa mbalame, kuseka kwa mwana, thambo lowala la bluu, kamphepo kotsitsimula—zonsezi ndi zinanso zambiri zingatichitikire patsiku limodzi. Nkosavutadi kunyalanyaza mphatso zimenezi. Kodi zonse sizoyenera kuzinenera zikomo? Zonse zimachokera kwa Yehova, Magwero a “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro.” (Yakobo 1:17) Ndiponso watipatsa mphatso zazikulu zoposa zimenezi—mwachitsanzo, moyo weniweniwo. (Salmo 36:9) Ndiponso, watipatsa mwayi wodzakhala ndi moyo kosatha. Kuti apereke mphatso imeneyi, Yehova anadzimana koposa mwa kutumiza Mwana wake wobadwa yekha, “amene anamkonda kwambiri.”—Miyambo 8:30, NW; Yohane 3:16.
18. Kodi tingamyamikire motani Yehova?
18 Ndiyetu mawu a wamasalmowa ngoonadi: “Nkokoma kuyamika Yehova.” (Salmo 92:1) Mofananamo, Paulo anakumbutsa Akristu a ku Tesalonika kuti: “M’zonse yamikani.” (1 Atesalonika 5:18; Aefeso 5:20; Akolose 3:15) Aliyense wa ife angafune kukhala woyamikira kwambiri. Mapemphero athu sayenera kungokhala ochonderera Mulungu pazosoŵa zathu basi. Zimenezo zimakhala bwino pamalo ake. Koma yerekezerani kuti muli ndi bwenzi limene limakulankhulani kokha pamene likufuna kenakake kwa inu! Choncho bwanji osapemphera kwa Yehova kungomyamikira ndi kumtamanda? Mapemphero oterowo amamsangalatsa chotani nanga pamene ayang’ana pansi padziko losayamikirali! Phindu linanso nlakuti mapemphero oterowo angatithandize kusumika maganizo athu pambali zolimbikitsa za moyo, kutikumbutsa za madalitso athu.
19. Kodi kalembedwe ka Paulo pa Akolose 2:6, 7 kakusonyeza motani kuti tonsefe tingapitirizebe kuwongolera kuyenda kwathu ndi Kristu?
19 Kodi sizodabwitsa kuona kuchuluka kwa chitsogozo chanzeru chimene chingapezeke m’ndime imodzi ya Mawu a Mulungu? Uphungu wa Paulo wakuti tipitirize kuyenda ndi Kristu uli chinthu chimene aliyense wa ife ayenera kulabadira. Choncho tiyeni titsimikize mtima kukhala ‘ozika mizu mwa Kristu,’ “omangirika mwa Iye,” “okhazikika m’chikhulupiriro,” ndiponso ‘osefukira ndi chiyamiko.’ Uphungu umenewu ngwofunika kwambiri makamaka kwa obatizidwa chatsopano. Koma umakhudza tonsefe. Lingalirani za mmene muzu waukulu umapitirizirabe kukula ukumazama kwambiri ndiponso mmene nyumba yomwe ikumangidwa imapitirizirabe kutalika. Choncho kuyenda kwathu ndi Kristu kulibe mapeto. Pali mpata waukulu woti tipitirize kukula. Yehova adzatithandiza ndi kutidalitsa, popeza akufuna kuti tipitirize kosaleka kuyenda ndi iye ndi Mwana wake wokondedwa.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi kuyenda mogwirizana ndi Kristu kumafunanji?
◻ Kodi kukhala ‘wozika mizu mwa Kristu’ kumatanthauzanji?
◻ Kodi tingachitenji kuti ‘timangiriridwe mwa Kristu’?
◻ Kodi nchifukwa ninji kukhala ‘wokhazikika m’chikhulupiriro’ kuli kofunika kwambiri?
◻ Kodi tili ndi zifukwa ziti zokhalira ‘osefukira ndi chiyamiko’?
[Chithunzi patsamba 10]
Mizu ya mtengo ingakhale yosaonekera, koma imapereka chakudya ku mtengowo ndi kuulimbitsa kuti usagwe