Lingaliro la Baibulo
Kodi Mulungu Amakondwera Kutiona Tikuvutika?
MUNTHUYO akuvutika ndi kulemera kwa mtanda waukulu wamtengo, akuyenda mopupulika kupyola makamu pamene mwazi ukuchucha m’korona wa minga pamutu pake. Atafika pamalo “ophera,” akulambalitsidwa pamtandapo; misomali yaikulu ikukhomeredwa m’manja mwake. Iye akudzungunyuka ndi ululu pamene misomaliyo ikuboola mnofu. Pamene mtandawo ukuimikidwa chiriri, ululuwo ukukhala waukulu kwambiri. Malinga ndi kunena kwa magazini a Panorama, a ku Philippines, madzoma opweteka otero amasonyezedwa nthaŵi zonse mkati mwa kukumbukira Holy Week ku Philippines.
Zimene zafotokozedwazo ndizo kuyerekezera kwamakono kosonyeza kuvutika kwa Yesu. Koma munthu ameneyu sakungosonyeza chochitika cha m’seŵero. Misomali, mwazi, ululu—zonsezo zili zenizeni.
Kwina, Aroma Katolika odzipereka amaonedwa akudzikwapula poyera m’kukhumba kwawo kumva mavuto a Kristu. Chifukwa ninji? Ena amachita zimenezi pokhulupirira kuti kuvutika kwawo kudzatulutsa zozizwitsa, monga ngati kuchiritsa okondedwa awo odwala. Ena amakuchita kuti alipirire machimo amene, amaopera kuti, alibe chikhululukiro pokhapo ngati mwazi wa iwo eni utakhetsedwa. Buku lakuti The Filipinos likufotokoza kuti: “Ululu ndiwo choyeretsa maganizo ndi moyo chabwino. . . . Wochimwayo amaganiziridwa kuti watuluka mu ululumo atayeretsedwa machimo ndi kumasulidwa ku mavuto.”
Komabe, kudzimvetsa ululu sikumachitidwa ndi Akatolika a ku Philippines okha. Anthu a zipembedzo zosiyanasiyana ndi a m’maiko osiyanasiyana amakhulupirira kuti kudzizunza kumakhala ndi mphotho kwa Mulungu.
Mwachitsanzo, m’kufunafuna kwake choonadi, Siddhārtha Gautama, Wachibuda, anasiya mkazi wake ndi mwana wamwamuna nathaŵira kuchipululu, kumene anakakhala ndi moyo wodzizunza kwa zaka zisanu ndi chimodzi. Iye anachita zinthu zodzizunza ndi zomvetsa ululu kwa maola ambiri ndipo pambuyo pake ananena kuti anachirira pa kampunga kamodzi patsiku kwanthaŵi yaitali, anawonda kwambiri kwakuti anati: “Khungu la mimba yanga linamatirira ku fupa la msana wanga.” Koma palibe kudzizunza kwa mtundu uliwonse kumene kunadzetsa chidziŵitso chimene anafunafuna.
Mofananamo, Ahindu oyendayenda a ku India analoŵa m’kudzilanga kosiyanasiyana kumene nthaŵi zina kunali kowopsa kwambiri—kugona pakati pa moto, kuyang’ana dzuŵa kufikira atachita khungu, kuimirira ndi mwendo umodzi kapena m’kaimidwe kena kovuta kwa nthaŵi yaitali kwambiri. Phindu la kudzizunza kwina linalingaliridwa kukhala lalikulu kwambiri moti nkukhala lokhoza kutetezera mzinda pa kuukiridwa ndi adani.
Mofananamo, Baibulo limanena za olambira Baala amene anadzitema “monga makhalidwe awo ndi mipeni ndi nthungo, kuti mwazi wawo unali chuchuchu” m’kuyesayesa kosaphula kanthu kuti amvedwe ndi mulungu wawo.—1 Mafumu 18:28.
“Muzisautsa Miyoyo Yanu”
Pamene kuli kwakuti Yehova analamula mtundu wake wosankhika kuti: “muzisautsa miyoyo yanu,” zimenezi makamaka zimazindikiridwa kukhala zikutanthauza kusala kudya. (Levitiko 16:31, NW) Kusala kudya kumeneko kunali chisonyezero cha chisoni ndi kulapa machimo kapena kunachitidwa pamene anali pamikhalidwe yovuta. Motero, kusala kudya sikunali mpangidwe wa chilango wa kudzivulaza koma kunasonyeza kudzichepetsa kwa munthu pamaso pa Mulungu.—Ezara 8:21.
Komabe, panali Ayuda ena amene analingalira molakwa kuti ululu weniweniwo wa kuzunza moyo unali ndi mphotho yake ndi kuti unaumiriza Mulungu kuwapatsa kanthu kena mobwezera. Pamene mphothoyo sinaperekedwe, iwo modzikuza anafunsa Mulungu za malipiro amene analingalira kukhala owayenerera: “Bwanji ife tasala kudya, ndipo inu simuona? Ndi bwanji ife tavutitsa moyo wathu, ndipo inu simusamalira?”—Yesaya 58:3.
Koma iwo anali olakwa. Kusala kudya koyenera kwachipembedzo sikunaloŵetsemo kudzizunza, kuvulaza thupi ndi njala monga ngati kuti ululu wathupi kapena kupweteka kwenikweniko kunali ndi mphotho iliyonse. Malingaliro ovutitsidwa kwambiri akanathetsa njala yawo. Ngati maganizo agwidwa ndi mavuto aakulu, thupi silingafune chakudya. Zimenezi zimasonyeza kwa Mulungu malingaliro opweteka kwambiri a munthu wosala kudyayo.
Kodi Mulungu Amakondwera ndi Ululu wa Kudzizunza?
Kodi Mlengi wachikondi amapeza chimwemwe chilichonse mwa kuonerera anthu akudzizunza? Pamene kuli kwakuti nzoona kuti panthaŵi zina Akristu angakakamizike kukhala ‘olaŵana ndi Kristu zoŵaŵa zake,’ zimenezi sizikutanthauza kuti amafunafuna mavuto kapena kukhala ofera chikhulupiriro.—1 Petro 4:13.
Ndithudi, Yesu sanali konse munthu wodzizunza. Atsogoleri achipembedzo anadandula chifukwa chakuti ophunzira ake sanasale kudya, ndipo anamutchadi kuti “munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo.” (Mateyu 9:14; 11:19) Yesu anasonyeza mkhalidwe wachikatikati mu zonse ndipo sanafune zopyola pa mlingo woyenera kwa iye mwini kapena kwa ena.—Marko 6:31; Yohane 4:6.
M’Malemba palibe malo alionse amene timapeza maziko a kudzizunza, monga ngati kuti kudzimana ife eni zofunika kapena ngakhale zinthu zabwino za moyo kungadzetse chiyanjo cha Mulungu. Onani zimene mawu a mtumwi Paulo amanena ponena za machitidwe opweteka otero: “Zimene zili nawotu manenedwe a nzeru m’kutumikira kwa chifuniro cha mwini wake, ndi kudzichepetsa, ndi kusalabadira thupi; koma zilibe mphamvu konse yakuletsa chikhutitso cha thupi.”—Akolose 2:23.
Martin Luther, pamene anali mgulupa, anadzizunza kwenikweni. Komabe, pambuyo pake, anatsutsa machitachita amenewo, akumati iwo analimbikitsa lingaliro la njira ziŵiri zopita kwa Mulungu, yapamwamba ndi yotsika, pamene kuli kwakuti Malemba anangophunzitsa za njira imodzi yomka kuchipulumutso—kupyolera mwa kusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu Kristu ndi Atate wake, Yehova. (Yohane 17:3) Komanso, miyambo yopweteka inaonedwa ndi ena kukhala mpangidwe wa chipulumutso chaumwini.
Buku lakuti Church History in Plain Language limathirira ndemanga pa mkhalidwe wakudzizunza: “Kuchirikiza kuyesayesa konseko kunali lingaliro lolakwika la munthu. Moyo, mgulupa anatero, waikidwa m’goli ndi thupi monga wandende wa mtembo. Limenelo si lingaliro la Baibulo la moyo wa munthu.” Inde, lingaliro lenilenilo lakuti ululu wa kudzivulaza ungakondweretse Mulungu mulibemo m’Malemba. Maziko ake amapezeka mu lingaliro lonyenga la Chignosti lakuti chinthu chilichonse chogwirizanitsidwa ndi thupi nchoipa ndipo chiyenera kuchitiridwa mwankhanza monga momwe kungathekere kotero kuti munthu apeze chipulumutso.
Popeza kuti Yehova akufuna kuti tikhale achimwemwe, kutumikira Mulungu wokondwera wotero sikuli nkhani ya kukhala odzizunza. (Mlaliki 7:16) Motero, m’Malemba mulibiretu malo amene timauzidwa kuti kudziika pa mavuto kotero ndiko njira ya kuchipulumutso. Mosiyana ndi zimenezo, Mawu a Mulungu amasonyeza poyera kuti mwazi wa Kristu, limodzi ndi kusonyeza chikhulupiriro chathu mwa uwo, ndizo zimene zimatiyeretsera machimo onse.—Aroma 5:1; 1 Yohane 1:7.