-
Mmene Mungathandizire Amene Akudwala Matenda AmaganizoNsanja ya Olonda (Yogawira)—2023 | No. 1
-
-
‘Muzilankhula molimbikitsa.’—1 ATESALONIKA 5:14.
Mnzanuyo akhoza kukhala ndi nkhawa kapena angamalimbane ndi vuto lodziona kuti ndi wachabechabe. Mungamulimbikitse kwambiri komanso kumutonthoza, mukamamutsimikizira kuti mumamukonda ngakhale musakudziwa zoti munene.
-
-
Mmene Mungathandizire Amene Akudwala Matenda AmaganizoNsanja ya Olonda (Yogawira)—2023 | No. 1
-
-
‘Muzikhala oleza mtima.’—1 ATESALONIKA 5:14.
Si nthawi zonse pamene mnzanuyo angakhale womasuka kufotokoza maganizo ake. Muzimutsimikizira kuti ndinu wokonzeka kumumvetsera pa nthawi ina iliyonse yomwe angafune kukufotokozerani maganizo ake. Chifukwa cha matenda amene akudwalawo, iye akhoza kuchita kapena kulankhula zinthu zina zimene zingakukhumudwitseni. Ndipo nthawi zina, akhoza kusintha zinthu zimene munapangana kuti muchitire limodzi kapenanso akhoza kukwiya zosadziwika bwino. Choncho, muzichita naye zinthu moleza mtima komanso kumumvetsa pa nthawi imene mukumuthandizayo.—Miyambo 18:24.
-