Mutu 3
Makiyi Aŵiri a Ukwati Wokhalitsa
1, 2. (a) Kodi cholinga chinali chakuti ukwati ukhale kwa utali wotani? (b) Kodi zimenezi nzotheka motani?
PAMENE Mulungu anagwirizanitsa mwamuna ndi mkazi woyamba muukwati, panalibe chilichonse chosonyeza kuti mgwirizanowo udzakhala wakanthaŵi chabe. Adamu ndi Hava anayenera kukhala pamodzi kwa moyo wonse. (Genesis 2:24) Muyezo wa Mulungu wa ukwati wolemekezeka ndiwo kugwirizana pamodzi kwa mwamuna mmodzi ndi mkazi mmodzi. Chisembwere chokha chochitidwa ndi mmodzi wa okwatiranawo kapena onse aŵiri ndicho chimapereka maziko a Malemba a chisudzulo ndi chilolezo cha kukwatiranso.—Mateyu 5:32.
2 Kodi nzotheka kuti anthu aŵiri akhale pamodzi mwachimwemwe kwa moyo wonse? Inde, ndipo Baibulo limasonyeza zinthu zofunika kwambiri ziŵiri, kapena makiyi, amene amathandiza kutheketsa zimenezi. Ngati onse aŵiri mwamuna ndi mkazi agwiritsira ntchito makiyi ameneŵa, adzakhoza kutsegula khomo loloŵera ku chimwemwe ndi madalitso ambiri. Kodi makiyi ameneŵa nchiyani?
KIYI YOYAMBA
3. Kodi ndi mitundu ya chikondi itatu iti imene okwatirana ayenera kukhala nayo?
3 Kiyi yoyamba ndiyo chikondi. Komabe, pali mitundu yosiyanasiyana ya chikondi m’Baibulo. Umodzi ndiwo chikondi chachibwenzi kwa munthu wina, mtundu wa chikondi chimene chimakhala pakati pa mabwenzi apamtima. (Yohane 11:3) Mtundu wina ndiwo chikondi chimene chimakhala pakati pa apabanja. (Aroma 12:10, NW) Wachitatu ndiwo kukondana kokopeka mtima pakati pa mwamuna ndi mkazi. (Miyambo 5:15-20) Ndithudi, mwamuna ndi mkazi ayenera kukulitsa mitundu yonseyi ya chikondi. Koma pali mtundu wachinayi wa chikondi, wofunika kwambiri kuposa inayo.
4. Kodi mtundu wachinayi wa chikondi ndi wotani?
4 M’chinenero choyambirira cha Malemba Achigiriki Achikristu, liwu la mtundu wachinayi umenewu wa chikondi ndilo a·gaʹpe. Liwuli lagwiritsidwanso ntchito pa 1 Yohane 4:8, pamene timauzidwa kuti: “Mulungu ndiye chikondi.” Zoona, “tikonda ife, chifukwa anayamba [Mulungu] kutikonda.” (1 Yohane 4:19) Mkristu amakhala ndi chikondi choterocho choyamba kwa Yehova Mulungu ndiyeno kwa anthu anzake. (Marko 12:29-31) Liwu lakuti a·gaʹpe limagwiritsidwanso ntchito pa Aefeso 5:2, pamene pamati: “Yendani m’chikondi monganso Kristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m’malo mwathu.” Yesu anati chikondi cha mtundu umenewu chidzazindikiritsa otsatira ake oona: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano [a·gaʹpe] wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Onaninso mmene a·gaʹpe yagwiritsidwira ntchito pa 1 Akorinto 13:13 kuti: “Zitsala chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi, zitatu izi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi [a·gaʹpe].”
5, 6. (a) Kodi nchifukwa ninji chikondi chili chachikulu kuposa chikhulupiriro ndi chiyembekezo? (b) Kodi pali zifukwa zina ziti zosonyeza kuti chikondi chimathandiza ukwati kukhalitsa?
5 Kodi nchiyani chimachititsa chikondi cha a·gaʹpe kukhala chachikulu kuposa chikhulupiriro ndi chiyembekezo? Chifukwa chakuti chimazikidwa pa mapulinsipulo—mapulinsipulo olungama—aja opezeka m’Mawu a Mulungu. (Salmo 119:105) Imeneyo ndiyo nkhaŵa yopanda dyera yofuna kuchitira ena zoyenera ndi zabwino pamaso pa Mulungu, kaya wochitiridwayo akuoneka kukhala woyenera zimenezo kapena ayi. Chikondi chotero chimakhozetsa okwatirana kutsatira uphungu wa Baibulo wakuti: “[Pitirizani, NW] kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso.” (Akolose 3:13) Okwatirana okondana ali ndi ‘chikondano chenicheni [a·gaʹpe] mwa iwo okha,’ ndipo amachikulitsa ‘pakuti chikondano chikwirira unyinji wa machimo.’ (1 Petro 4:8) Onani kuti chikondi chimakwirira zolakwa. Sichimazichotsa, pakuti palibe munthu wopanda ungwiro amene angakhale wosalakwa.—Salmo 130:3, 4; Yakobo 3:2.
6 Pamene chikondi chotero kwa Mulungu ndi kwa wina ndi mnzake chikulitsidwa pakati pa okwatirana, ukwati wawo umakhalitsa ndipo umakhala wachimwemwe, pakuti “chikondi sichitha nthaŵi zonse.” (1 Akorinto 13:8) Chikondi ndicho “chomangira cha mtima wamphumphu.” (Akolose 3:14) Ngati muli wokwatira, kodi inu ndi mnzanu mungakulitse motani mtundu wa chikondi chimenechi? Ŵerengani pamodzi Mawu a Mulungu, ndipo kambitsiranani za iwo. Phunzirani za chitsanzo cha Yesu cha chikondi ndipo yesani kumtsanzira iye, kulingalira ndi kuchita zinthu mofanana naye. Ndiponso, pezekani pamisonkhano yachikristu, kumene Mawu a Mulungu amaphunzitsidwa. Ndipo pemphererani chithandizo cha Mulungu kuti mukulitse mtundu wokwezeka wa chikondi chimenechi, chimene chili chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu.—Miyambo 3:5, 6; Yohane 17:3; Agalatiya 5:22; Ahebri 10:24, 25.
KIYI YACHIŴIRI
7. Kodi ulemu nchiyani, ndipo ndani ayenera kusonyeza ulemu muukwati?
7 Ngati anthu aŵiri okwatirana amakondana kwenikweni, pamenepo adzakhalanso ndi ulemu kwa wina ndi mnzake, ndipo ulemu ndiwo kiyi yachiŵiri muukwati wachimwemwe. Ulemu wamasuliridwa kukhala “kuŵerengera ena, kuwalemekeza.” Mawu a Mulungu amalangiza Akristu onse, kuphatikizapo amuna ndi akazi kuti: “Mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.” (Aroma 12:10) Mtumwi Petro analemba kuti: “Amuna inu, khalani nawo [akazi anu] monga mwa chidziŵitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu.” (1 Petro 3:7) Mkazi akulangizidwa ‘kukhala ndi ulemu waukulu kwa mwamuna wake.’ (Aefeso 5:33, NW) Ngati mukufuna kulemekeza munthu, mumakhala wokoma mtima kwa munthuyo, mumalemekeza malo ake ndi malingaliro ake, ndi kukhala wokonzeka kuchita zilizonse zabwino zimene akupemphani kuchita.
8-10. Kodi ndi njira zina zotani zimene zingathandize kuchititsa ukwati kukhala wokhazikika ndi wachimwemwe?
8 Awo ofuna kukhala ndi ukwati wabwino amasonyeza ulemu kwa anzawo a muukwati mwa ‘kusapenyerera zawo za iwo okha, koma kupenyereranso za anzawo [a muukwati].’ (Afilipi 2:4) Iwo samangolingalira zabwino za iwo okha—limene lili dyera. M’malo mwake, amalingaliranso zabwino za anzawo a muukwati. Ndithudi, amaika patsogolo zabwino za mnzawo.
9 Ulemu udzathandiza okwatirana kuzindikira kuti pamakhala kusiyana malingaliro. Sikwanzeru kuyembekezera kuti anthu aŵiri angakhale ndi malingaliro ofanana pa chinthu chilichonse. Chimene chingakhale chofunika kwa mwamuna chingakhale chosafunika kwenikweni kwa mkazi, ndipo chimene mkazi amakonda chingakhale chisali chimene mwamuna amakonda. Koma aliyense ayenera kulemekeza malingaliro ndi zosankha za mnzake, malinga ngati sizimapyola malire a malamulo ndi mapulinsipulo a Yehova. (1 Petro 2:16; yerekezerani ndi Filemoni 14.) Ndiponso, aliyense ayenera kulemekeza malo a mnzake mwa kusamunenera mawu onyoza kapena njerengo zomunyazitsa, kaya pakati pa anthu kapena mseri.
10 Inde, chikondi kwa Mulungu ndi kwa wina ndi mnzake ndi kulemekezana ndiko makiyi aŵiri ofunika kwambiri muukwati wachipambano. Kodi angagwiritsidwe ntchito motani m’mbali zina zofunika kwambiri za moyo wa okwatirana?
UMUTU WONGA WA KRISTU
11. Mwa Malemba, kodi mutu wa muukwati ndani?
11 Baibulo limatiuza kuti mwamuna analengedwa ndi mikhalidwe yomkhozetsa kukhala mutu wa banja wachipambano. Motero, mwamuna ali ndi thayo pamaso pa Yehova la kusamalira mkazi wake ndi ana ake mwauzimu ndi mwakuthupi. Afunikira kupanga zosankha zoyenera zimene zimasonyeza chifuniro cha Yehova ndi kukhala chitsanzo chabwino m’makhalidwe aumulungu. “Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye. Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa Eklesia.” (Aefeso 5:22, 23) Komabe, Baibulo limanena kuti mwamunanso ali ndi mutu wake, Uyo wokhala ndi ulamuliro pa iye. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndifuna kuti mudziŵe, kuti mutu wa munthu [“mwamuna,” NW] yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” (1 Akorinto 11:3) Mwamuna wanzeru amaphunzira mmene angachitire umutu mwa kutsanzira mutu wake, Kristu Yesu.
12. Kodi ndi chitsanzo chabwino chotani chimene Yesu anapereka chosonyeza kugonjera ndi kuchita umutu?
12 Yesunso ali ndi mutu wake, Yehova, ndipo amagonjera kwa Iye bwino lomwe. Yesu anati: “Sinditsata chifuniro changa, koma chifuniro cha Iye wondituma ine.” (Yohane 5:30) Chitsanzo chabwino kwenikweni! Yesu ndiye “wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Iye anadzakhala Mesiya. Anali kudzakhala Mutu wa mpingo wa Akristu odzozedwa ndi Mfumu yosankhidwa ya Ufumu wa Mulungu, pamwamba pa angelo onse. (Afilipi 2:9-11; Ahebri 1:4) Mosasamala kanthu za malo okwezeka amenewo ndi ziyembekezo zaulemerero zimenezo, munthuyo Yesu sanali waukali, sanali wosalolera, kapena wolamulira mopambanitsa. Iye sanali wotsendereza, nthaŵi zonse wofuna kuti ophunzira ake amvere iye. Yesu anali wachikondi ndi wachifundo, makamaka kwa oponderezedwa. Iye anati: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa lili lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.” (Mateyu 11:28-30) Kunali kosangalatsa kukhala naye pamodzi.
13, 14. Kodi mwamuna wachikondi amachita motani umutu wake, mwa kutsanzira Yesu?
13 Mwamuna wofuna banja la moyo wachimwemwe amachita bwino kulingalira za mikhalidwe yabwino ya Yesu. Mwamuna wabwino samakhala waukali ndi wolamulira, wogwiritsira ntchito umutu wake molakwa monga mkwapulo kwa mkazi wake. M’malo mwake, amamukonda ndi kumlemekeza. Ngati Yesu anali “wodzichepetsa mtima,” koposa kotani nanga mwamuna, amene amalakwa, mosiyana ndi Yesu. Pamene iye alakwa, amafuna mkazi wake kumkomera mtima. Chotero, mwamuna wodzichepetsa amavomereza zolakwa zake, ngakhale kuti kutchula mawu akuti, “Pepa; unali bwino,” kungakhale kovuta. Kumakhala kosavuta kwa mkazi kulemekeza umutu wa mwamuna wodekha ndi wodzichepetsa, osati wonyada ndi wouma khosi. Ndiyeno, mkazi waulemu nayenso amapepesa pamene alakwa.
14 Mulungu analenga mkazi ndi mikhalidwe yabwino imene angagwiritsire ntchito kuchititsa ukwati kukhala wachimwemwe. Mwamuna wanzeru amazindikira zimenezi ndipo samamtsekereza. Akazi ambiri amaoneka kukhala achifundo chachikulu ndi atcheru, mikhalidwe yofunikira posamalira banja ndi maunansi aumunthu. Kaŵirikaŵiri, mkazi amakhala ndi changu cha kusamalira nyumba kuti ikhale malo okondweretsa kukhalamo. “Mkazi wangwiro” wolongosoledwa m’Miyambo chaputala 31 anali ndi mikhalidwe yabwino yambiri ndi maluso odabwitsa, ndipo banja lake linapindula nawo kwambiri. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mtima wa mwamuna wake ‘unamkhulupirira.’—Miyambo 31:10, 11.
15. Kodi mwamuna angasonyeze motani chikondi chonga cha Kristu ndi ulemu kwa mkazi wake?
15 Kumalo ena, ulamuliro wa mwamuna umachitidwa mopambanitsa, kwakuti ngakhale kumufunsa funso kumaonedwa kukhala kupanda ulemu. Iye angachitire mkazi wake monga kapolo. Kuchita umutu kolakwa kumeneko kumachititsa kusamvana osati ndi mkazi yekha komanso ndi Mulungu. (Yerekezerani ndi 1 Yohane 4:20, 21.) Ndiponso, amuna ena amanyalanyaza kutsogolera, akumalola akazi awo kulamulira m’nyumba. Mwamuna amene ali wogonjera kwa Kristu samalima pamsana mkazi wake kapena kumlanda ulemu wake. M’malo mwake, amatsanzira chikondi chodzimana cha Yesu ndipo amachita monga mwa uphungu wa Paulo wakuti: “Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha m’malo mwake.” (Aefeso 5:25) Kristu Yesu anakonda otsatira ake kwambiri kwakuti anawafera iwo. Mwamuna wabwino amayesayesa kutsanzira mkhalidwe wopanda dyera umenewo, akumafuna zabwino za mkazi wake, m’malo mwa kumamulamulira. Pamene mwamuna ali wogonjera kwa Kristu ndi kusonyeza chikondi chonga cha Kristu ndi ulemu, mkazi wake adzasonkhezereka kugonjera kwa iye.—Aefeso 5:28, 29, 33.
KUGONJERA KWA MKAZI
16. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene mkazi ayenera kusonyeza paunansi wake ndi mwamuna wake?
16 Panthaŵi inayake Adamu atalengedwa kale, “Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.” (Genesis 2:18) Mulungu analenga Hava monga “womthangatira,” osati monga wopikisana naye. Ukwati sunayenera kukhala monga chombo chokhala ndi oyendetsa aŵiri opikisana. Mwamuna anafunikira kuchita umutu mwachikondi, ndipo mkazi anayenera kusonyeza chikondi, ulemu, ndi kugonjera kofunitsitsa.
17, 18. Kodi ndi njira zina ziti zimene mkazi angakhalire wothandiza weniweni kwa mwamuna wake?
17 Komabe, mkazi wabwino amachita zoposa kugonjera chabe. Amayesa kukhala wothandiza weniweni, akumakhala wochirikiza mwamuna wake pazosankha zimene apanga. Ndithudi, zimenezo zimakhala zopepuka pamene iye akuvomereza zosankha za mwamuna. Koma ngakhale pamene sakuvomereza, chichirikizo chake chingathandize chosankha cha mwamuna kukhala ndi chotulukapo cha chipambano kwambiri.
18 Mkazi angathandize mwamuna wake kukhala mutu wabwino m’njira zinanso. Angasonyeze chiyamikiro pa zoyesayesa zake za kutsogolera, m’malo mwa kumsuliza kapena kumchititsa kuona kuti sangamkhutiritse konse. Pochita ndi mwamuna wake m’njira yabwino, ayenera kukumbukira kuti “mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu,” osati pamaso pa mwamuna wake yekha. (1 Petro 3:3, 4; Akolose 3:12) Bwanji ngati mwamuna saali wokhulupirira? Kaya akhale wokhulupirira kapena wosakhulupirira, Malemba amalimbikitsa akazi kuti “akonde amuna awo, akonde ana awo, akhale odziletsa, odekha, ochita m’nyumba mwawo, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mawu a Mulungu angachitidwe mwano.” (Tito 2:4, 5) Ngati pabuka nkhani za chikumbumtima, mwamuna wosakhulupirira angalemekeze malingaliro a mkazi wake ngati aperekedwa ndi “chifatso ndi mantha.” Amuna ena osakhulupirira ‘akodwa popanda mawu mwa mayendedwe a akazi; pakuona mayendedwe [awo] oyera ndi kuwopa [kwawo].’—1 Petro 3:1, 2, 15; 1 Akorinto 7:13-16.
19. Bwanji ngati mwamuna apempha mkazi wake kuswa lamulo la Mulungu?
19 Nanga bwanji ngati mwamuna apempha mkazi wake kuchita chinthu chimene Mulungu amaletsa? Ngati zimenezo zichitika, ayenera kukumbukira kuti Mulungu ndiye Wolamulira wamkulu. Ayenera kutsatira chitsanzo cha zimene atumwi anachita pamene anauzidwa ndi olamulira kuti aswe lamulo la Mulungu. Machitidwe 5:29 amati: “Anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.”
KULANKHULANA KWABWINO
20. Kodi ndi mbali yofunika iti imene imafuna chikondi ndi ulemu?
20 Chikondi ndi ulemu nzofunikanso pambali ina ya ukwati—ya kulankhulana. Mwamuna wachikondi amakambitsirana ndi mkazi wake za ntchito za mkaziyo, mavuto ake, malingaliro ake pankhani zosiyanasiyana. Mkazi amafunikira zimenezi. Mwamuna amene amatenga nthaŵi kulankhula ndi mkazi wake ndi kumvetseradi zimene amanena amasonyeza chikondi chake ndi ulemu kwa iye. (Yakobo 1:19) Akazi ena amadandaula kuti amuna awo amangolankhula nawo kwa nthaŵi yochepa kwambiri. Zimenezo nzachisoni. Inde, m’nthaŵi zino za kutanganidwa, amuna angakhale akumakhala kuntchito maola ochuluka, ndipo mikhalidwe yovuta yazachuma ingachititse akazi ena kuloŵanso ntchito. Koma aŵiri okwatirana afunikira kupatula nthaŵi kaamba ka wina ndi mnzake. Kupanda kutero, adzakhala ndi moyo wayekhawayekha. Zimenezo zingatsogolere ku mavuto aakulu ngati angayambe kufunafuna woyanjana naye wachifundo kunja kwa kakonzedwe ka ukwati.
21. Kodi malankhulidwe oyenera amathandiza motani kuchititsa ukwati kukhala wachimwemwe?
21 Njira imene akazi ndi amuna amalankhulira ili yofunika kwambiri. “Mawu okoma ndiwo . . . otsekemera m’moyo ndi olamitsa mafupa.” (Miyambo 16:24) Kaya mnzanu wa muukwati ali wokhulupirira kapena wosakhulupirira, uphungu wa Baibulo umagwirabe ntchito: “Mawu anu akhale m’chisomo, okoleretsa,” ndiko kuti, oyenera. (Akolose 4:6) Pamene wina tsiku silinamuyendere bwino, mawu angapo okoma mtima ndi achifundo ochokera kwa mnzake wa muukwati angamtonthoze mtima kwambiri. “Mawu oyenera apanthaŵi yake akunga zipatso zagolidi m’nsengwa zasiliva.” (Miyambo 25:11) Mawu omveka bwino ndi kusankha bwino mawu nkofunika kwambiri. Mwachitsanzo, wina angauze mnzake ndi mawu aukali ndi olamulira kuti: “Tseka chitseko icho!” Koma mawuŵa angakhale “okoleretsa” chotani nanga ngati akambidwa ndi liwu labata, ndi lachifundo kuti, “Kodi ungatseke chitseko?”
22. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene okwatirana ayenera kukhala nayo kuti akhale ndi kulankhulana kwabwino?
22 Kulankhulana kwabwino kumakhalapo pamene pali kulankhulana ndi mawu ofatsa, kupenyana kwabwino ndi magesichala ake, kukoma mtima, kumvetsetsana, ndi kumverana chifundo. Mwa kulimbikira kusunga kulankhulana kwabwino, onse aŵiri mwamuna ndi mkazi adzakhala omasuka kutchula zosoŵa zawo, ndi kukhalanso otonthozana ndi othandizana m’nthaŵi zovuta kapena za kupsinjika. “Lankhulani motonthoza kwa opsinjika mtima,” amalimbikitsa motero Mawu a Mulungu. (1 Atesalonika 5:14, NW) Zidzakhalapo nthaŵi pamene mwamuna kapena mkazi adzakhala wopsinjika mtima. Akhoza ‘kulankhula motonthozana,’ akumalimbikitsana.—Aroma 15:2.
23, 24. Kodi chikondi ndi ulemu zingathandize motani pamene pali kusiyana malingaliro? Perekani chitsanzo.
23 Okwatirana amene amasonyezana chikondi ndi ulemu sadzaona kusiyana malingaliro kulikonse kukhala chothetsa nzeru chachikulu. Adzayesayesa zolimba ‘kusaŵaŵirana mtima.’ (Akolose 3:19) Onse aŵiri ayenera kukumbukira kuti “mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo.” (Miyambo 15:1) Samalani kuti musanyazitse kapena kusuliza mnzanu amene akulankhula motulutsa zakukhosi. M’malo mwake, onani malankhulidwe amenewo kukhala mpata wa kuzindikira malingaliro a mnzanuyo. Chapamodzi, yesani kuthetsa mikangano ndi kugwirizana pachimodzi.
24 Kumbukirani chochitika pamene Sara anapereka lingaliro kwa mwamuna wake Abrahamu, la njira yothetsera vuto koma yosiyana ndi malingaliro ake. Komabe, Mulungu anauza Abrahamu kuti: “Umvere iwe mawu ake.” (Genesis 21:9-12) Abrahamu anamvera, ndipo anadalitsidwa. Mofananamo, ngati mkazi apereka lingaliro la chinthu chosiyana ndi chimene mwamuna wake akuganiza, mwamunayo ayenera choyamba kumvetsera. Panthaŵi imodzimodzi, mkazi sayenera kupondereza pokambitsirana koma ayenera kumvetsera zimene mwamuna wake akufuna kunena. (Miyambo 25:24) Ngati mwamuna kapena mkazi aumirira panjira yake nthaŵi zonse, kumeneko ndiko kupanda chikondi ndi kupanda ulemu.
25. Kodi kulankhulana kwabwino kungathandizire motani kupeza chimwemwe m’maunansi athithithi a ukwati?
25 Kulankhulana kwabwino kulinso kofunika pankhani ya kugonana kwa okwatirana. Dyera ndi kusadziletsa kungawononge kwambiri unansi wathithithi umenewu wa muukwati. Kulankhulana komasuka, limodzi ndi kuleza mtima, nkofunika kwambiri. Pamene aliyense mopanda dyera afuna ubwino wa mnzake, kugonana sikumakhala vuto lalikulu kaŵirikaŵiri. Pankhani imeneyi, mofanana ndi zina, “munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.”—1 Akorinto 7:3-5; 10:24.
26. Ngakhale kuti ukwati uliwonse umakhala ndi nthaŵi zabwino ndi zoipa, kodi kumvetsera Mawu a Mulungu kungathandize motani okwatirana kupeza chimwemwe?
26 Ndi uphungu wabwino chotani nanga wa Mawu a Mulungu! Zoona, ukwati uliwonse umakhala ndi nthaŵi zabwino ndi zoipa. Koma pamene okwatirana atsatira malingaliro a Yehova, monga momwe Baibulo likusonyezera, ndi kuzika unansi wawo pa chikondi cha pulinsipulo ndi ulemu, angakhale ndi chidaliro chakuti ukwati wawo udzakhala kwa nthaŵi yaitali ndi wachimwemwe. Mwakutero adzalemekezana ndi kulemekezanso Woyambitsa ukwati, Yehova Mulungu.