‘Kukwatulidwa Kukakumana ndi Ambuye’—Motani?
KUFINIMPHA kwa nthaŵi yofikira ku mapeto a dongosolo loipa liripoli kukupitirizabe mosasinthika. Mwa kupita kwa ola lirilonse, mphindi iriyonse, kamphindi kalikonse, tikuyandikira zochitika zochititsa thumanzi zoloseredwa kalekale. Kodi kutengedwa m’thupi ndiko chimodzi cha zimenezi? Ngati kuli, pamenepo kudzachitika liti ndipo motani?
Liwulo “kutengedwa m’thupi” silimawonekera m’Baibulo. Koma okukhulupirira amatchula mawu a mtumwi Paulo pa 1 Atesalonika 4:17 monga maziko a chikhulupiriro chawo. Tiyeni tipende lemba limeneli mogwirizana ndi mawu ake apatsogolo ndi apambuyo. Paulo analemba kuti:
“Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziŵa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo. Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nawuka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu. Pakuti ichi tinena kwa inu m’mawu a [Yehova, NW], kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo. Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mawu a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Ambuye adzayamba kuuka; pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nawo pamodzi m’mitambo, kukakumana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthaŵi zonse. Chomwecho, tonthozanani ndi mawu awa.”—1 Atesalonika 4:13-18.
Mpingo mu Tesalonika unali watsopano pang’ono pamene Paulo analembera kalata yake yoyamba kwa Akristu kumeneko pafupifupi mu 50 C.E. Ziwalo za mpingowo zinali zovutitsidwa maganizo chifukwa chakuti ena a iwo anali “kugona mu imfa.” Komabe, zimene Paulo analemba zinatonthoza Atesalonika ndi chiyembekezo cha chiukiriro.
“Kukhalapo” kwa Kristu
Pamene anali kutsimikizira kuti Akristu okhulupirika akufa panthaŵiyo akaukitsidwa, Paulo anatinso: “Otsalira kufikira [kukhalapo, NW] kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo.” (Vesi 15) Ndithudi, apadera, ndiwo mawu a mtumwiyo osonya ku “kukhalapo” kwa Ambuye. Panopa lemba la chinenero choyambirira limagwiritsira ntchito liwu Lachigiriki lakuti pa·rou·siʹan, limene kwenikweni limatanthauza “kukhala limodzi.”
Pamene mtsogoleri wa Boma wa dziko lina achezetsa dziko lina, kaŵirikaŵiri masiku a kukhalapo kwake amalengezedwa. Zimenezi zakhala choncho ndi kukhalapo kwa Ambuye Yesu Kristu. Nsanja ya Olonda mosadukiza yapereka umboni kwa ophunzira ulosi wa Baibulo owona mtima kuti kukhalapo kwa Yesu mu mphamvu ya Ufumu wakumwamba kunayamba mu 1914. Zochitika kuyambira chaka chimenecho zikuchitira umboni kukhalapo kosawoneka kwa Yesu. (Mateyu 24:3-14) Chotero mwa kunena kuti Akristu ena okhala ndi moyo m’kukhalapo kwa Ambuye “akakwatulidwa nawo m’mitambo, kukakumana ndi Ambuye m’mlengalenga,” Paulo anatanthauza kuti opulumuka amenewo akakumana ndi Kristu, osati m’mlengalenga mwa dziko lapansi, koma malo akumwamba osawoneka kumene Yesu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. (Ahebri 1:1-3) Koma kodi amenewo ndani?
“Israyeli wa Mulungu”
Malemba amanena zochuluka ponena za Aisrayeli akuthupi ndiponso amalankhula za “Israyeli wa Mulungu” wauzimu. Okhulupirira Achiyuda ndi Akunja anali kudzapanga chiŵerengero chokwanira cha kagulu kameneka ka odzozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, kapena mphamvu yogwira ntchito. (Agalatiya 6:16; Aroma 11:25, 26; 1 Yohane 2:20, 27) Bukhu la Chivumbulutso limasonyeza kuti chiŵerengero chonse cha Israyeli wauzimu ndicho 144,000, amene onse akusonyezedwa kukhala ndi Mwanawankhosayo, Yesu Kristu, pa Phiri la Ziyoni lakumwamba. Limodzi ndi Kristu, iwo akakhala mafumu ndi ansembe kumwamba. (Chivumbulutso 7:1-8; 14:1-4; 20:6) Ophatikizidwa pakati pawo akakhala anthu amene anali kuyanjana ndi mipingo mu Tesalonika ndi kwina konse, mosasamala kanthu za chiyambi cha fuko lawo ndi mtundu.—Machitidwe 10:34, 35.
Ziŵalo zokhulupirika zirizonse za Israyeli wauzimu zisanalandire mphotho yakumwamba, zikafunikira kukhala ndi phande m’chochitika chakutichakuti. Monga momwe Yesu anafera pa mtengo wozunzirapo asanalandire chiukiriro chake ku moyo wakumwamba, choteronso Akristu okhala ndi chiyembekezo chakumwamba ayenera kufa asanalandire mphotho yawo. (1 Akorinto 15:35, 36) Zimenezo zikakhala choncho ponena za ziŵalo za Israyeli wauzimu zokhala ndi moyo m’zaka za zana loyamba C.E., ndi ponena za anthu otero okhala ndi moyo lerolino.
Atatha kutchula “kukhalapo kwa Ambuye,” Paulo anasonya kunthaŵi pamene Aisrayeli auzimu okhulupirika amene adamwalira akalandira mphotho yawo yakumwamba. Iye analemba kuti: “Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mawu a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Ambuye adzayamba kuuka.” (Vesi 16) Chifukwa chake, pamene kukhalapo kwa Yesu monga Mfumu kunayamba, tikayembekezera chiukiriro chakumwamba kuyamba, kuyambira ndi Israyeli wauzimu amene anali atafa kale monga osunga umphumphu. (1 Akorinto 15:23) Iwo tsopano akutumikira limodzi ndi Yesu kumwamba. Koma bwanji ponena za Akristu odzozedwa ochepekerawo amene akali chikhalirebe padziko lapansi? Kodi iwo amayembekezera kutengedwa m’thupi?
“Kukwatulidwa”—Motani?
Atatha kutchula Akristu odzozedwa amene anali atafa, Paulo anawonjezera kuti: “Pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nawo pamodzi m’mitambo, kukakumana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthaŵi zonse.” (vesi 17) “Amoyo” akakhala awo okhala ndi moyo m’nthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu. Iwo “akakwatulidwa” kukakumana ndi Ambuye Yesu. Monga momwe kunaliri ndi Akristu okhulupirika oyambirira, imfa yaumunthu iri yofunika kwa iwo kuti akagwirizane ndi Kristu kumwamba.—Aroma 8:17, 35-39.
Polembera Akristu a m’Korinto, Paulo anati: “Ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kuloŵa Ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichiloŵa chisavundi. Tawonani, ndikuwuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika, m’kamphindi, m’kutwanima kwa diso, palipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.” (1 Akorinto 15:50-52) Atafa okhulupirika mkati mwa kukhalapo kwa Kristu, aliyense wa otsalira a Israyeli wauzimu amalandira nthaŵi yomweyo mphotho yake yakumwamba. “M’kutwanima kwa diso,” iye amaukitsidwa monga cholengedwa chauzimu ndi “kukwatulidwa” kukakumana ndi Yesu ndi kukatumikira monga wolamulira mnzake mu Ufumu wakumwamba. Koma bwanji ponena za ena onse olambira Yehova? Pamene mapeto adongosolo loipa lino akuyandikira, kodi nawonso adzakwatulidwira kumwamba?
Kupulumuka—Koma Osati mwa Kutengedwa m’Thupi
Popeza kuti kukhalapo kwa Yesu monga mfumu kunayamba mu 1914, ife tsopano tiri mkati mwenimweni mwa “nthaŵi yachimaliziro” chadziko lino. (Danieli 12:4) Paulo anachenjeza kuti: “Koma za nthaŵizo ndi nyengozo, abale, sikufunika kuti tidzakulemberani. Pakuti inu nokha mudziŵa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku. Pamene angonena, Mtendere ndi chisungiko, pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.” (1 Atesalonika 5:1-3) Koma Akristu ogalamuka adzapulumuka. Motani?
Mfuu yakuti “Mtendere ndi chisungiko!” ndiyo kalambula bwalo wa nyengo imene Yesu anaitcha “chisautso chachikulu.” Pofotokoza “khamu lalikulu” la okhulupirika amene ali ndi chiyembekezo chakukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso wa dziko lapansi, bukhu la Chivumbulutso limati: “Iwo ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:9, 14; Luka 23:43) Ayi, chiyembekezo chawo sindicho kutengedwa m’thupi. Mmalomwake, iwo ali ndi chiyembekezo cha kupulumuka pompano pa dziko lapansi. Kudzikonzekeretsera chimenechi, iwo ayenera kukhalabe ogalamuka mwauzimu. Kodi inu mungachite ichi motani ndi kupulumuka mapeto a dongosolo lino?
Mufunikira ‘kudikira mutavala chapachifuŵa cha chikhulupiriro ndi chikondi; ndi chisoti monga chiyembekezo cha chipulumutso.’ (1 Atesalonika 5:6-8) Tsopano ndiyo nthaŵi yakupereka chisamaliro ku Mawu a ulosi a Mulungu, Baibulo. Pamene nthaŵi ikupita kufikira mapeto a dongosolo lino, labadirani uphungu wa Paulo wakuti: “Musanyozere maulosi. Tsimikizirani zinthu zonse; gwiritsitsani chabwinocho.” (1 Atesalonika 5:20, 21, NW) Chotero, Mboni za Yehova zikukulandirani ku Nyumba zawo Zaufumu, kumene mungagawane nazo kuphunzira maulosi a Baibulo ndi mbali zina za Mawu ouziridwa a Mulungu.
Pamene mukula m’chidziŵitso cholongosoka ndi chikhulupiriro, mudzazindikira kufunyululidwa kwa chifuno cha Yehova Mulungu cha kuchotsa m’chilengedwe chake adani ndi kubwezeretsa dziko lapansi kukhala paradaiso. Mwakusonyeza chikhulupiriro, mungakhalenso pakati pa opulumuka chisautso chachikulu, muli ndi mwaŵi wa kulandiranso mamiliyoni amene adzaukitsidwira ku moyo pa dziko lapansi. Ndipo chidzakhala chisangalalo chotani nanga kukhala ndi moyo mu Ufumu wa Mulungu m’manja a Yesu Kristu ndi olamulira anzake, amene ‘adzakhala atakwatulidwa kukakumana ndi Ambuye’ mwa kuukitsidwira ku moyo kumalo a kumwamba!
Pamenepa, kodi nchiyani chimene chiri chiyembekezo cha Malemba chowona cha anthu onse omvera? Sindicho kutengedwa m’thupi. Mmalomwake, ndicho moyo wosatha padziko lapansi muulamuliro wa Ufumu wa Mulungu.
[Chithunzi patsamba 7]
Opulumuka chisautso chachikulu adzalandira oukitsidwira ku moyo pa dziko lapansi la paradaiso muulamuliro wa Yesu ndi wa awo “okwatulidwira” kumwamba