Kuvumbula “Munthu Wosayeruzika”
“Tulukani m’menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, . . . kuti mungalandireko ya miliri yake.”—CHIBVUMBULUTSO 18:4.
1, 2. (a) Kodi munthu wosayeruzika angazindikiridwe motani? (b) Kodi kapenyedwe ka Mulungu nkotani kwa awo odzinenera kumtumikira koma ali aliŵongo lamwazi? (Mateyu 7:21-23)
MAWU a Mulungu ananeneratu za kudza kwa “munthu wosayeruzika.” Iwo ananeneratunso kuti mbali yosayeruzika imeneyi ‘ikachotsedwa ndi kuwonongedwa’ ndi Wakupha wakumwamba wa Mulungu, Kristu Yesu. (2 Atesalonika 2:3-8) Monga mmene nkhani zomwe zapitazo zasonyezera, munthu wosayeruzikayo ali atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu. Nthaŵi ya kumbuyoko iwo anakana chowonadi cha Mawu a Mulungu ndi kutenga ziphunzitso zachikunja, zonga ngati Utatu, moto wa helo, ndi kusafa kwa moyo. Kuwonjezerapo, iwo anatulutsa ntchito zosiyana ndi malamulo a Mulungu. Mofanana ndi awo amene Paulo anachenjeza Tito, “avomereza kuti adziŵa Mulungu, koma ndi ntchito zawo amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.”—Tito 1:16.
2 Yesu adanena kuti: “Yang’anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma mkati mwawo ali afisi olusa.” Aneneri onyenga akabala “zipatso zoipa.” (Mateyu 7:15-17) Umboni wa zipatso zoipa za atsogoleri achipembedzo ndi uja wa liŵongo lawo lalikulu la mwazi. Kwa zaka mazanamazana iwo achilikiza nkhondo zamtanda, zilango, ndi nkhondo zimene zakhetsa mwazi wa mamiliyoni angapo. Iwo apempherera ndi kudalitsa mbali zonse zoloŵetsedwa m’nkhondo m’zimene ziŵalo za chipembedzo chawo zaphana. Mosiyanako, mtumwi Paulo anali wokhoza kunena kuti: “Ndiribe kanthu ndi mwazi wa anthu onse.” (Machitidwe 20:26) Atsogoleri achipembedzo sali tero. Kwa oterowo Mulungu akulengeza kuti: “Pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.”—Yesaya 1:15.
3. Kodi ndi zochitika zadziko zapadera zotani zomwe zikuyandikira mofulumira?
3 Nthaŵi ya Mulungu ya kupereka chiweruzo chake motsutsana ndi munthu wosayeruzika ikuyandikira mofulumira. Posachedwapa, monga mmene Yesu ananeneratu, “kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitike chiyambire chiyambi cha dziko kufikira tsopano, inde, ndipo sichidzachitikanso.” (Mateyu 24:21, NW) Nthaŵi ya mavuto yosayerekezeka imeneyo idzayamba ndi kuphedwa kwa Babulo Wamkulu, ulamuliro wadziko wa chipembedzo chonyenga, womwe umaphatikiza zipembedzo za Dziko Lachikristu. Mbali za ndale zadziko ‘zidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzampsyereza ndi moto.’ (Chibvumbulutso 17:16) Chisautso chachikulu chidzatha ndi kuwonongedwa kwa otsala a dziko la Satana pa Armagedo, “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.”—Chibvumbulutso 16:14, 16; 19:11-21.
Olamulidwa Kukonda Ena
4. Kodi nchiyani chimene awo olambira Mulungu “mumzimu ndi m’chowonadi” ayenera kusunga m’maganizo?
4 Popeza kuti zochitika zogwedeza dziko zimenezi ziri pafupi kuchitika pa dziko lokhalidwa ndi anthu, kodi ndi mathayo otani amene ali pa awo “olambira . . . Atate mumzimu ndi m’chowonadi”? (Yohane 4:23) Choyamba, ayenera kukumbukira kuti Yesu adati: “Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m’chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m’chikondi chake. . . . Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu. Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu.”—Yohane 15:10-14; 1 Yohane 5:3.
5, 6. (a) Kodi nchiyani chimene Yesu analamula ophunzira ake kuchita chomwe chikawazindikiritsa iwo? (b) Kodi limeneli linali lamulo latsopano m’lingaliro lotani?
5 Chotero Akristu owona ali ndi thayo la kukonda anthu ena, makamakadi tero kwa abale ndi alongo awo Achikristu m’maiko onse. (Machitidwe 10:34; Agalatiya 6:10; 1 Yohane 4:20, 21) Ndithudi, Akristu okha okha ayenera kukhala ndi ‘chikondano chenicheni mwa iwo okha.’ (1 Petro 4:8) Mtundu umenewo wa chikondi pa mlingo wa dziko lonse umawazindikiritsa kukhala alambiri owona, popeza Yesu adanena kuti: “Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”—Yohane 13:34, 35.
6 Kodi nchiyani chimene chinali chatsopano m’lamulo limenelo? Kodi Ayuda pansi pa Chilamulo cha Mose sadapatsidwa lamulo lakuti, “Uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha”? (Levitiko 19:18) Inde, koma Yesu anasonyeza chinachake chowonjezera pamene adanena kuti, “Monga ndakonda inu.” Chikondi chake chinaphatikizapo kupereka moyo wake kaamba ka ena, ndipo ophunzira ake ayenera kukhala ofunitsitsa kuchita zofananazo. (Yohane 15:13) Umenewo unali muyezo wapamwamba wa chikondi, popeza kuti nsembe yoteroyo sinafunidwe ndi Chilamulo cha Mose.
7. Kodi ndi chipembedzo chiti chimene chalabadira lamulo la chikondi m’zaka za zana lino?
7 M’zaka za zana lathu, kodi ndi chipembedzo chiti chimene chalabadira lamulo limeneli la chikondi? Motsimikizirikadi osati zipembedzo za Dziko Lachikristu, popeza kuti zaphana m’mamiliyoni m’nkhondo ziŵiri zadziko ndi kukanthana kwina. Ndi Mboni za Yehova zimene zamvera lamulo la chikondilo dziko lonse. Izo zasunga uchete wotheratu m’nkhondo za mitundu, popeza kuti Yesu adanena kuti atsatiri ake sayenera ‘kukhala mbali yadziko.’ (Yohane 17:16) Chotero, iwo anganene monga mmene adachitira Paulo, kuti “alibe kanthu ndi mwazi wa anthu onse.” Mwachitsanzo, onani mbali yotsegulira ya chigamulo chotengedwa ndi atumiki a Yehova pa msonkhano wa ku Washington, D.C., pa November 27, 1921:
“Monga Akristu okalamira mofunitsitsa kutsatira ziphunzitso za Kristu Yesu Ambuye wathu ndi Atumwi ake, timasungirira: kuti nkhondo ndiyodzetsa chipanduko, yowononga makhalidwe abwino ndi chitonzo kwa anthu Achikristu; kuti malamulo a makhalidwe abwino ophunzitsidwa ndi Ambuye Yesu Kristu amaletsa Akristu opatulikitsidwa kudziloŵetsa m’nkhondo, kukhetsa mwazi kapena chiwawa cha mtundu uliwonse.”
8. Kodi nchiyani chimene cholembera cha mbiri yakale chimanena ponena za Mboni za Yehova mkati mwa Nkhondo Yadziko ya II?
8 Kodi kapenyedwe kameneko kanagwiritsiridwa bwanji m’Nkhondo Yadziko ya II? M’nkhondo yoipitsitsa imeneyo ya m’mbiri ya anthu, anthu 50 miliyoni anaphedwa. Koma palibe ndi mmodzi yense amene anaphedwa ndi mmodzi wa Mboni za Yehova! Mwachitsanzo, chifupifupi atsogoleri achipembedzo onse a ku Germany anachilikiza Chinazi mwachangu kapena mwamseri. Mosiyanako, Mboni za Yehova zokhala mu ulamuliro wa Chinazi zinasungabe uchete wosamalitsa ndipo zinakana kulambira Hitler kapena kukhala mbali ya magulu ake ankhondo. Chotero, iwo sanaphe aliyense wa abale awo auzimu a m’maiko ena, kapenadi wina aliyense. Ndipo Mboni za Yehova m’maiko ena onse zinakhalanso zauchete.
9. Kodi nchiyani chinachitika kwa Mboni za Yehova mu Germany ndi Austria pansi pa ulamuliro wa Nazi?
9 Mboni za Yehova zambiri zapereka miyoyo yawo m’malo mwa mabwenzi awo m’kumvera lamulo la chikondilo. Kubwereramo kwa bukhu lakuti Kirchenkampf in Deutschland (Nkhondo Yamatchalitchi mu Germany), lolembedwa ndi Friedrich Zipfel, kukunena za Mboni kuti: “Maperesenti makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi ziŵiri a ziŵalo za gulu laling’ono la chipembedzo limeneli anali minkhole ya kuzunza kwa National Socialism [Nazi]. Mmodzi mwa atatu a iwo anaphedwa, kaya mwa kuphedwa, machitidwe ena achiwawa, njala, matenda kapena ntchito yachibalo. Kuipa kwa kuchitiridwaku kunalibe chowonerapo chakumbuyo ndipo kunali chotulukapo cha chikhulupiriro chosagonjetseka chomwe sichidamvane ndi nthanthi za National Socialism.” Mu Austria, 25 peresenti ya Mboni za Yehova anaphedwa, kumenyedwa mpaka imfa, kapena kufa ndi matenda kapena kulefuka m’misasa ya Nazi.
10. Kodi ndi chidaliro chotani chimene awo amene anafa chifukwa cha kulabadira lamulo la chikondi analinacho?
10 Awo ophedwera chikhulupiriro kaamba ka kumvera lamulo la chikondi anali ndi chidaliro chakuti “Mulungu sali wosalungama kuti adzaiŵala ntchito [yawo], ndi chikondicho [adachiwonetsera] ku dzina lake.” (Ahebri 6:10) Iwo anadziŵa kuti “dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake, koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.” (1 Yohane 2:17) Iwo adali ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha kuukitsidwa ndi moyo wosatha m’maganizo.—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.
11. Kodi atumiki a Yehova ali apadera mwa njira yanji, ndipo kodi ndi ulosi wotani umene ukukwaniritsidwa mwa iwo?
11 Atumiki a Yehova ndi apadera m’kumvera lamulo lonenedwa ndi Petro ndi atumwi ena m’bwalo lalikulu lamilandu: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” (Machitidwe 5:29) Chifukwa chakuti Mboni za Yehova zimachita zimenezi, izo zachilikizidwa ndi ‘mzimu woyera, umene Mulungu amapatsa kwa omumvera iye.’ (Machitidwe 5:32) Imeneyo ndiyo mphamvu imene imawatheketsa kukwaniritsa ulosi wa pa Yesaya 2:2-4. Iwo unaneneratu kuti m’nthaŵi yathu kulambira kowona kukakhazikitsidwanso ndikuti anthu kuchokera m’mitundu yonse ndi zipembedzo akathamangirako. Chotulukapo chimodzi chikakhala chakuti: “Iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” Popeza kuti atumiki a Yehova akukonzekera moyo m’dziko latsopano lamtendere, iwo sadzaphunziranso nkhondo. Iwo amaphunzira lamulo la chikondi.—Yohane 13:34, 35.
12. Kodi nchiyani chimene awo olabadira lamulo la chikondi ayenera kuchita kaamba ka ena?
12 Popeza kuti chikondi Chachikristu chimaphatikizapo ‘kukonda mnzako monga udzikonda iwe mwini,’ atumiki a Mulungu sangakhale adyera ponena za zimene amadziŵa. (Mateyu 22:39) Padakali enanso ambiri omwe angafune kutumikira Mulungu ndi kukhala m’dziko lake latsopano. Pamene nthaŵi idakalipo, awanso afunikira kuphunzira ponena za lamulo la chikondi ndi zowonadi zina zambiri zogwirizana ndi Wolamulira Wachilengedwe Chonse, Yehova Mulungu. Iwo ayenera kuphunzitsidwa kuti Yehova yekha ndi woyenerera kulambira kwathu ndi mmene kulambirako kuyenera kuchitidwira. (Mateyu 4:10; Chibvumbulutso 4:11) Awo omwe aphunzira kale zinthu zimenezi ali ndi thayo la kuuza ena ponena za izo kotero kuti nawonso angadze m’chiyanjo cha Yehova.—Ezekieli 33:7-9, 14-16.
Kuvumbula Munthu Wosayeruzika
13. Monga mbali ya umboni wathu wa dziko lonse, kodi nchiyani chimene tiyenera kudziŵikitsa, ndipo nchifukwa ninji?
13 Yesu adanena kuti “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14, NW) Monga mbali ya umboni wa dziko lonse umenewu, atumiki a Mulungu ali ndi thayo la kudziŵikitsa chiweruzo chake motsutsana ndi chipembedzo chonyenga, makamaka atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu. Awa ali onyansa kwenikweni m’maso mwa Mulungu chifukwa chakuti amadzinenera kukhala Achikristu. Iwo afunikira kuvumbulidwa kotero kuti awo ofuna kutumikira Mulungu angamasulidwe ku chisonkhezero chawo ndipo angatenge masitepi olondola kaamba ka chipulumuko. Monga mmene Yesu adanenera kuti: “Chowonadi chidzakumasulani.”—Yohane 8:32.
14. Kodi ndi uthenga womvekera wotani umene uyenera kulengezedwa ponena za chipembedzo chonyenga?
14 Chotero, Mboni za Yehova ziyenera kudziŵikitsa uthenga wouziridwa uwu wonena za chipembedzo chonyenga: “Tulukani m’menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake; pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira m’Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake. . . . Chifukwa chake miliri yake idzadza m’tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapsereza ndi moto; chifukwa [Yehova, NW] Mulungu wouweruza ndiye wolimba.”—Chibvumbulutso 18:4-8.
15. Kodi ndimotani mmene chaka cha 1914 chinachitira mbali m’ndandanda ya nthaŵi ya Yehova, ndipo chinatulukapo nchiyani pambuyo pa Nkhondo Yadziko ya I?
15 Maulosi a Baibulo amasonyeza kuti “masiku otsiriza” a dongososlo iri la zinthu anayamba m’chaka choipitsitsa cha 1914. (2 Timoteo 3:1-5, 13; Mateyu 24:3-13) Chiyambire chaka chimenecho tikukhala “m’nthaŵi ya chimaliziro.” (Danieli 12:4) Chiyambiredi pambuyo pa Nkhondo Yadziko ya I, mogwirizana ndi ndandanda ya nthaŵi ya Yehova, atumiki ake anayamba mwamphamvu kufutukula kulengeza kwawo kwa Ufumu wa Mulungu monga mmene zinanenedweratu pa Mateyu 24:14. Iwo anayambanso kuvumbula chipembedzo chonyenga mwamphamvudi, makamaka gulu la atsogoleri achipembedzo osayeruzika a Dziko Lachikristu lopatuka.
16. Kodi ndimotani mmene kuvumbula munthu wosayeruzika kwakhalira kwamphamvu mowonjezereka kwa zaka zoposa 70?
16 Kwa zaka zoposa 70 tsopano, ndi mphamvu zokulakulabe, atumiki a Mulungu agalamutsa anthu za zochita zachinyengo za munthu wosayeruzika. Padali kokha zikwi zoŵerengeka za Mboni zomwe zinkachita chimenechi pambuyo pa Nkhondo Yadziko ya I. Koma tsopano iwo ali “mtundu wamphamvu” wa atumiki okangalika oposa mamiliyoni atatu ndi theka olinganizidwa m’mipingo yoposa 60,000 pa dziko lonse lapansi. (Yesaya 60:22) Pa ukulu wofutukuka, atumiki a Mulungu akulengeza mwachangu Ufumu wa Mulungu kukhala chiyembekezo chokha cha mtundu wa anthu ndipo, pa nthaŵi imodzimodziyo, akuvumbula chimene atsogoleri achipembedzo alidi—munthu wosayeruzika wachinyengo.
Kodi Nchifukwa Ninji Ali Amphamvu Chotero?
17. Kodi nchifukwa ninji atumiki a Yehova avumbula mwamphamvu munthu wosayeruzika?
17 Kodi nchifukwa ninji atumiki a Yehova avumbula mwamphamvu munthu wosayeruzikayu zaka zonsezi? Chifukwa chakuti mamiliyoni a khamu lalikulu la nkhosa za Yehova omwe ali kale panjira yonkira ku chipulumutso ayenera kuchinjirizidwa ku dziko la Satana ndi chipembedzo chake chonyenga. (Yohane 10:16; Chibvumbulutso 7:9-14) Kuwonjezerapo, pokhapo ngati atsogoleri achipembedzo avumbulidwa, anthu owona mtima omwe sadakhalebe mbali ya nkhosa za Mulungu sakadziŵa mmene angapeŵere njira yolakwika. Chotero ayenera kudziŵitsidwa, mongadi mmene Yesu anadziŵitsira anthu pamene adanena za atsogoleri achipembedzo achinyengo a m’tsiku lake kuti: “Ali atsogoleri akhungu. Ndipo ngati wakhungu amtsogolera wakhungu, onse awiri adzagwa m’mbuna.”—Mateyu 15:14; onaninso 2 Akorinto 4:4; 11:13-15.
18. Kodi nchiyani chimene ofunafuna chowonadi afunikira kudziŵa?
18 Atsogoleri achipembedzo ali mbali ya dziko la Satana. (Yohane 8:44) Koma ilo ndi dziko limene Mulungu posachedwapa adzaphwanya kulichotseratu. (2 Petro 3:11-13; 1 Yohane 2:15-17) Chotero Mawu a Mulungu akuchenjeza kuti: “Iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.” (Yakobo 4:4) Atsogoleri achipembedzo amanyalanyaza chenjezo limenelo ndi kupitirizabe kusakanizana m’zochitachita za ndale zadziko. Iwo amauza atsatiri awo kuti dziko labwinopo lidzabwera kupyolera m’zoyesayesa za andale zadziko. Koma chimenechi ndi chiyembekezo chonyenga, popeza kuti dziko iri lokhala pansi pa Satana liri paulendo wakutha. Chotero anthu amene amayang’ana ku dziko iri kaamba ka chiyembekezo akunyengedwa. Ayenera kuuzidwa chowonadi chonena za kumene dzikoli likupita ndi chimene chidzaliloŵa m’malo.—Miyambo 14:12; 19:21; Mateyu 6:9, 10; Chibvumbulutso 21:4, 5.
19. Kodi ndimotani mmene udziko wa atsogoleri achipembedzo ena wavumbulidwira pa zowulutsira nkhani m’nthaŵi zaposachedwapa?
19 Udziko wa atsogoleri ena achipembedzo wavumbulidwa m’zowulutsira nkhani m’nthaŵi zaposachedwapa, mwachitsanzo njira yamoyo yopambanitsa ndi yokonda zosangulutsa ya atsogoleri achipembedzo ena a pa TV. Mlembi wina wamakono wa nyimbo anapanga nyimbo yokhala ndi mutu wakuti: “Kodi Yesu Akadavala [koloko] ya Rolex ya [$10,000] pa Chiwonetsero Chake Chapawailesi Yakanema?” Nyimboyo imapitiriza kuti: “Kodi Yesu angakhale wa ndale zadziko Iye atabweranso pa dziko lapansi, kukhala ndi nyumba Yake yachiŵiri m’Palm Springs [yosangulutsa] ndi kuyesera kubisa ubwino Wake?” Kuwonjezerapo, atsogoleri achipembedzo owonjezerekawonjezereka amalekerera kapena kuchitadi kugonana kofanana ziŵalo. Ngakhaledi tsopano Tchalitchi Chachikatolika mu United States chikulipira madola mamiliyoni angapo m’zivulazo zolipirira ansembe okhala ndi liŵongo la kuipsya ana mwa kugonana.—Aroma 1:24-27; 1 Akorinto 6:9, 10.
20. Kodi nchifukwa ninji atumiki a Mulungu ayenera kupitirizabe kuvumbula munthu wosayeruzika?
20 Kuchita zoipa koteroko sikunganyalanyazidwe ndi atumiki a Mulungu koma kuyenera kuvumbulidwa kaamba ka ubwino wa ena. Khamu lalikulu la nkhosa zina liyenera kuchinjirizidwa kwa aja omwe angawatsogolere kuswa malamulo a Mulungu. Ndipo awo ‘akuwusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zochitidwa’ afunikira kufufuzidwa ndi kusonkhanitsidwa ku chitsogozo chochinjiriza cha Mbusa Wamkulu, Yehova Mulungu, ndi “mbusa wabwino,” Kristu Yesu.—Ezekieli 9:4; Yohane 10:11; Miyambo 18:10.
21. Kodi nchiyani chimene Mboni za Yehova zidzapitirizabe kulengeza?
21 Chotero, anthu a Mulungu sadzazengereza kulengeza kubwezera kwake motsutsana ndi dziko lonse la Satana, kuphatikizapo munthu wosayeruzika wake, atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu. Iwo adzalengeza molimba mtima uthenga wa pa Chibvumbulutso 14:7 wakuti: “Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake.” Ndipo adzaphatikiza m’chilengezo chimenechi chenjezo lofulumira la Chibvumbulutso 18:4 lonena za chipembedzo chonyenga: “Tulukani m’menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, . . . kuti mungalandireko ya miliri yake.”
Mafunso a Kubwereramo:
◻ Kodi nchiyani chidzakhala mathedwe a munthu wosayeruzika, ndipo nchifukwa ninji?
◻ Kodi ndi thayo lanji limene atumiki a Yehova ali nalo kulinga kwa ena?
◻ Kodi ndimotani mmene anthu a Yehova akhalira omasuka ku mwazi wa anthu onse?
◻ Kodi tiyenera kuchitanji ponena za Babulo Wamkulu?
◻ Kodi nchifukwa ninji tidzapitirizabe ndi uthenga wathu wamphamvu kulinga kwa munthu wosayeruzika?
[Chithunzi patsamba 23]
Atumwiwo anauza khoti lalikulu kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu”
[Chithunzi patsamba 24]
Anthu owona mtima afunikira kudziŵa kumene dziko ndi zipembedzo zake zikupita