Chikhulupiriro Chachikristu Chidzayesedwa
“Si onse ali nacho chikhulupiriro.”—2 ATESALONIKA 3:2.
1. Kodi mbiri yasonyeza motani kuti si onse ali ndi chikhulupiriro chenicheni?
M’MBIRI yonse ya munthu, pakhala amuna, akazi ndi ana okhala nacho chikhulupiriro chenicheni. Inde, titero kuti “chenicheni” chifukwa mamiliyoni a anthu ena aonetsa mtundu wa chikhulupiriro chongotengeka maganizo, kungokhulupirira popanda maziko kapena chifukwa chenicheni. Chikhulupiriro choterocho kaŵirikaŵiri chaphatikizapo milungu yonama kapena mitundu ya kulambira yosemphana ndi Wamphamvuyonse, Yehova, ndiponso ndi Mawu ake ovumbulidwa. Nchifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Si onse ali nacho chikhulupiriro.”—2 Atesalonika 3:2.
2. Nchifukwa chiyani kuli kofunika kupenda chikhulupiriro chathu?
2 Komabe mawu a Paulo amasonyeza kuti panthaŵiyo ena anali nacho chikhulupiriro choona, mofananamo leronso alipo ena omwe ali nacho. Ambiri oŵerenga magazini ino amakhumba kukhala nacho chikhulupiriro choonacho ndi kuchikulitsa—inde, chikhulupiriro chogwirizana ndi chidziŵitso cholongosoka cha choonadi chaumulungu. (Yohane 18:37; Ahebri 11:6) Kodi zilinso choncho kwa inu? Ngati zili choncho, nkofunika kuti muzindikire nimukhale wokonzekera chifukwa chikhulupiriro chanu chidzayesedwa. Nchifukwa chiyani tikunena choncho?
3, 4. Nchifukwa chiyani tiyenera kuonera kwa Yesu ponena za ziyeso za chikhulupiriro chathu?
3 Tiyenera kuvomereza kuti Yesu Kristu ngwofunika kwambiri pachikhulupiriro chathu. Ndithudi, Baibulo limamutcha Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu. Amatchedwa choncho chifukwa cha zimene ananena ndi kuchita, makamaka mmene anakwaniritsira maulosi. Iye analimbitsa maziko akuti anthu akhazikitsepo chikhulupiriro choona. (Ahebri 12:2; Chivumbulutso 1:1, 2) Ngakhale ndi choncho, timaŵerenga kuti Yesu ‘anayesedwa m’zonse monga mwa ife, koma wopanda uchimo.’ (Ahebri 4:15) Inde, chikhulupiriro cha Yesu chinayesedwa. M’malo motilefula kapena kutichititsa mantha, zimenezo ziyenera kutilimbikitsa.
4 Mwa kukumana ndi mayesero aakulu mpaka imfa pamtengo wozunzirapo, Yesu “anaphunzira kumvera.” (Ahebri 5:8) Anapereka umboni wakuti anthu atha kusungabe chikhulupiriro chenicheni, ngakhale atakumana ndi ziyeso zotani. Zimenezo nzoona makamaka tikaganiza zimene Yesu ananena pouza otsatira ake kuti: “Kumbukirani mawu amene Ine ndinanena kwa inu, kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake.” (Yohane 15:20) Ndiponso, ponena za otsatira ake a m’nthaŵi yathu ino, Yesu analosera kuti: “Amitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.”—Mateyu 24:9.
5. Kodi Malemba amasonyeza motani kuti tidzakumana ndi ziyeso?
5 Kumayambiriro kwa zaka za zana lino, chiweruzo chinayambira mkati mwenimweni mwa nyumba ya Mulungu. Malemba ananeneratu kuti: “Yafika nthaŵi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani? Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndi kuyesetsa kokhakokha, munthu wosapembedza ndi wochimwa adzaoneka kuti?”—1 Petro 4:17, 18.
Chikhulupiriro Chiyesedwa—Chifukwa Chiyani?
6. Nchifukwa chiyani chikhulupiriro choyesedwa chili chaphindu?
6 M’lingaliro lina, chikhulupiriro chosayesedwa chilibe mtengo wotsimikizirika, ndipo mtundu wake umakhala wosadziŵika. Mungachifanizire ndi cheke chimene sichinasinthidwe. Mungakhale mutalandira cheke pantchito imene mwagwira, kapena cha katundu amene mwagulitsa, ngakhalenso mwina kuchilandira monga mphatso. Chekecho chingaoneke chamtengo wake, koma kodi chilidi chotero? Kodi chilidi cha mtengo wa ndalama zosonyezedwapo? Mofanafanamo, chikhulupiriro chathu sichiyenera kukhala cha maonekedwe okha, chisakhale chapakamwa chabe. Chiyenera chiyesedwe ngati tikufuna kutsimikizira kuti chili chenicheni ndi cha mtengo wake. Pamene chikhulupiriro chathu chiyesedwa, tingapeze kuti ncholimba komanso chaphindu. Chiyesocho chingavumbulenso mbali zina za chikhulupiriro chathu zofunikira kukonza ndi kulimbitsa.
7, 8. Kodi ziyeso pa chikhulupiriro chathu zimachokera kuti?
7 Mulungu amalola chizunzo ndi ziyeso zina za chikhulupiriro kutifikira. Timaŵerenga kuti: “Munthu poyesedwa, asanena, ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu.” (Yakobo 1:13) Nangano ndani kapena nchiyani chimachititsa mayesero otero? Ali Satana, dziko, ndi thupi lathu lopanda ungwiro.
8 Tingavomereze kuti Satana ali ndi chisonkhezero champhamvu pa dzikoli, pa kalingaliridwe kake komanso njira zake. (1 Yohane 5:19) Ndipo mwina tikudziŵanso kuti iye amakolezera chizunzo pa Akristu. (Chivumbulutso 12:17) Koma kodi timakhulupiriranso kuti Satana amayesetsa kutisocheza kudzera m’matupi athu opanda ungwiro, akumatikhumbiza zokopa za dziko, ndi cholinga choti titenge nyamboyo, kuti tipandukire Mulungu ndi kutaya chiyanjo cha Yehova? Komabe, sitiyenera kudabwa nazo njira za Satana, pakuti anagwiritsira ntchito machenjera ofananawo poyesa kunyenga Yesu.—Mateyu 4:1-11.
9. Kodi tingapindule motani ndi zitsanzo za chikhulupiriro?
9 Mwa Mawu ake ndi mpingo wachikristu, Yehova amatisonyeza zitsanzo zabwino za chikhulupiriro zimene tingatsanzire. Paulo analangiza kuti: “Abale, khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang’anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife chitsanzo chanu.” (Afilipi 3:17) Monga mmodzi wa atumiki odzozedwa a Mulungu a m’zaka za zana loyamba, Paulo anali wotsogola pochita ntchito za chikhulupiriro chinkana kuti anakumana ndi mayesero aakulu. Ngakhale kumapeto kuno kwa zaka za zana la 20, tili nazo zitsanzo zabwino zofananazo za chikhulupiriro. Mawu a pa Ahebri 13:7 akugwirabe ntchito mwamphamvu pa ife mofanana ndi panthaŵi imene Paulo anawalemba: “Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu Mawu a Mulungu; ndipo poyang’anira chitsiriziro cha mayendedwe awo mutsanze chikhulupiriro chawo.”
10. Kodi ndi zitsanzo ziti zapadera za chikhulupiriro zimene tili nazo m’nthaŵi yathu ino?
10 Malangizo amenewo amakhala amphamvu makamaka pamene tionetsetsa khalidwe la otsalira odzozedwa. Titha kusinkhasinkha za chitsanzo chawo ndi kutsanzira chikhulupiriro chawo. Chawocho ndi chikhulupiriro chenicheni choyengedwa mwa mayesero. Mwakuyamba pang’onopang’ono kalelo m’ma 1870, tsopano akhala gulu la abale achikristu kuzungulira dziko lonse lapansi. Monga zipatso za chikhulupiriro ndi chipiriro cha odzozedwawo kuyambira nthaŵiyo, tsopano Mboni za Yehova zoposa mamiliyoni asanu ndi theka zikulalikira ndi kuphunzitsa za Ufumu wa Mulungu. Mpingo wa padziko lonse wamakono wa alambiri oona achangu uli umboni wa chikhulupiriro choyesedwa.—Tito 2:14.
Chikhulupiriro Chiyesedwa Ponena za 1914
11. Kodi 1914 inali yapadera motani kwa C. T. Russell ndi anzake?
11 Kudakali zaka zambiri nkhondo yoyamba ya dziko lonse isanabuke, otsalira odzozedwa ankalengeza kuti 1914 chikakhala chaka chapadera mu ulosi wa Baibulo. Komabe, zina mwa ziyembekezo zawo nthaŵi yake inali isanakwane, ndipo malingaliro awo pa zimene zinali kudzachitika sanali olondola kwenikweni. Mwachitsanzo, C. T. Russell, pulezidenti woyambirira wa Watch Tower Society, limodzi ndi anzake anaona kuti ntchito yaikulu yolalikira inali yofunikira. Iwo ankaŵerenga kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Koma kodi kagulu kawo kochepako kakanaitha bwanji ntchito yonseyo?
12. Kodi mmodzi wa anzake a Russell analabadira motani choonadi cha Baibulo?
12 Tamverani mmene zimenezi zinakhudzira A. H. Macmillan, mnzake wa Russell. Macmillan anabadwira ku Canada, ndipo anali asanakwanitse zaka 20 pamene anapeza buku la Russell lakuti The Plan of the Ages (1886). (Bukuli, lotchedwanso The Divine Plan of the Ages, linakhala Voliyumu 1 ya mpambo wa mabuku ofalitsidwa kwambiri otchedwa Studies in the Scriptures. Voliyumu 2, yotchedwa The Time Is at Hand [1889], inasonya 1914 kukhala mapeto a “nthaŵi zawo za anthu akunja.” [Luka 21:24]) Usiku womwewo umene Macmillan anayamba kuŵerenga bukulo, analingalira kuti: “Eya, zimenezi zikumveka ngati choonadi!” M’chilimwe cha 1900, iye anakumana ndi Russell pamsonkhano wa Ophunzira Baibulo, dzina la Mboni za Yehova panthaŵiyo. Posapita nthaŵi, Macmillan anabatizidwa nayamba kugwira ntchito limodzi ndi Mbale Russell palikulu la Sosaite ku New York.
13. Kodi ndi vuto lanji limene Macmillan ndi anzake anaona pofuna kukwaniritsa Mateyu 24:14?
13 Malinga ndi mmene ankaŵerengera Baibulo, Akristu odzozedwa amenewo anati 1914 chinali chaka chosinthirapo zinthu m’chifuniro cha Mulungu. Koma Macmillan limodzi ndi ena anazizwa mmene ulaliki ukanachitidwira m’nthaŵi yochepa yotsalayo kuti ufikire mitundu yonse malinga ndi kunena kwa Mateyu 24:14. Pambuyo pake iye anati: “Ndikukumbukira kuti tinkakambirana zimenezo kaŵirikaŵiri ndi Mbale Russell, ndipo iye ankangoti, ‘Taonani mbale, mommuno mu New York tili ndi Ayuda ochuluka kuposa amene ali ku Yerusalemu. Tili ndi Maairishi ambiri kuno kuposa amene ali ku Dublin. Ndiponso tili ndi Mataliyana ambiri kuno kuposa amene ali ku Rome. Moti ngati tiwafikira onsewo, kumeneko kukakhala kulifikira dziko lonse ndi uthengawo.’ Koma zimenezo sizinakhutiritse maganizo athu kwenikweni. Choncho tinaganiza zokonza ‘Seŵero Lapakanema.’”
14. Isanafike 1914, kodi ndi ntchito yapadera yotani imene inayambidwa?
14 Ha, mmene “Seŵero Lapakanema la Chilengedwe” limenelo linakhalira kalambula bwalo nanga! Linaphatikiza zithunzi zoyenda ndi masilaidi amaonekedwe achibadwa, zogwirizanitsidwa ndi nkhani za Baibulo limodzi ndi nyimbo pamalekodi a galamafoni. Mu 1913, Nsanja ya Olonda yachingelezi inati ponena za msonkhano wa ku Arkansas, U.S.A.: “Onse anavomereza kuti nthaŵi yafika yogwiritsira ntchito zithunzi zoyenda pophunzitsa choonadi cha Baibulo. . . . [Russell] anafotokoza kuti anagwira ntchito papulani imeneyi zaka zitatu ndipo tsopano anali ndi zithunzi zomalizidwa mazana ambiri, zimene mosakayika konse zidzakopa makamu aakulu ndi kubukitsa Uthengawo, komanso kuthandiza anthu kukhalanso ndi chikhulupiriro mwa Mulungu.”
15. Kodi “Seŵero Lapakanema” linakhala ndi zotulukapo zotani?
15 “Seŵero Lapakanema” limenelo linachitadi zimenezo pambuyo pakuonetsedwa koyamba m’January 1914. Nawa malipoti ochokera mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya 1914:
April 1: “Mbusa wina, ataona zigawo ziŵiri anati, ‘Ndangoona theka lokha la SEŴERO LAPAKANEMA LA CHILENGEDWE, koma landiphunzitsa kale zochuluka za Baibulo kuposa zimene ndinaphunzira pakosi yanga ya zaka zitatu kuseminale yophunzitsa zaumulungu.’ Myuda wina ataiona anati, ‘Ndikuchoka pano ndili Myuda wabwinopo kuposa mmene ndinalili pobwera.’ Ansembe angapo achikatolika ndi avirigo abwera kudzaonerera SEŴEROLI ndipo akuthokoza kwabasi. . . . Tangomaliza magawo khumi ndi aŵiri a SEŴEROLO . . . Komabe, tafikira kale mizinda 31 . . . Anthu oposa 35,000 tsiku lililonse amaonerera, kumvetsera, kukhumbira, kulingalira ndipo amadalitsidwa.”
June 15: “Zithunzizo zandipangitsa kukhala wokangalika polalikira Choonadi, ndipo zaŵirikiza chikondi changa kwa Atate Wakumwamba ndi Mbale wathu Wamkulu Yesu. Ndimapemphera tsiku ndi tsiku kuti Mulungu adalitse kwambiri SEŴERO LAPAKANEMA LA CHILENGEDWE ndi onse othandiza kulionetsa . . . Ine mtumiki wanu mwa Iye, F. W. KNOCHE.—Iowa.”
July 15: “Tili osangalala kuona maganizo abwino amene zithunzizo zasiya mumzinda uno, ndipo tili otsimikiza kuti umboni umenewu woperekedwa ku dziko ukugwiritsidwanso ntchito posonkhanitsa ambiri amene akudzionetsa kuti ali chuma chosankhidwa ndi Ambuye. Tikudziŵa ophunzira Baibulo akhama ochulukirapo amene tsopano akugwirizana ndi Kaguluko panopo chifukwa cha ntchito ya Seŵero Lapakanema. . . . Ndine mlongo wanu mwa Ambuye, EMMA L. BRICKER.”
November 15: “Tili otsimikiza kuti mudzasangalala kumva za umboni wodabwitsa umene ukuperekedwa ndi SEŴERO LAPAKANEMA LA CHILENGEDWE ku The London Opera House, ku Kingsway. Dzanja lotsogolera la Ambuye laonekera modabwitsa m’mbali iliyonse ya chionetsero chimenechi kwakuti abale akusangalala kwambiri . . . Panali omvetsera osauka ndi olemera omwe komanso amitundu yosiyanasiyana; taonanso atsogoleri achipembedzo ambiri pakati pa omvetsera. Mlaliki wina wachipembedzo . . . anapempha matikiti kuti abwere limodzi ndi mkazi wake kudzaonerera. Mkulu wina wa Church of England wafika kudzaonerera SEŴEROLO nthaŵi zambiri, ndipo . . . wabweranso ndi anzake ambiri kuti adzaone okha. Mabishopu aŵiri abweranso, limodzi ndi anthu ena angapo amaudindo.”
December 1: “Ine ndi mkazi wanga tikuthokozadi Atate wathu Wakumwamba kaamba ka dalitso lalikululi ndi lamtengo wapatali limene latifika kudzera mwa inu. SEŴERO LAPAKANEMA lanulo lokongola choncho ndilo lationetsa Choonadi kuti tichilandire. . . . Tili ndi mabuku anu asanu ndi limodzi a mutu wakuti KUPHUNZIRA MALEMBA. Mabukuwa ngothandiza kwambiri.”
Kuchita Nazo Ziyeso Panthaŵiyo
16. Kodi nchifukwa chiyani 1914 inabweretsa chiyeso pa chikhulupiriro?
16 Kodi anatani Akristu oona mtima ndi odzipereka ameneŵa, ataona kuti chiyembekezo chawo cha kugwirizana ndi Ambuye mu 1914 sichinakwaniritsidwe? Odzozedwa amenewo anapyola m’nthaŵi yovuta kwenikweni. Nsanja ya Olonda yachingelezi ya November 1, 1914, inalengeza kuti: “Tikumbukire kuti tili m’nyengo yoyesedwa.” Ponena za ichi, buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom (1993) limati: “Zakazo 1914 mpaka 1918, zinalidi ‘nyengo yoyesedwa’ kwa Ophunzira Baibulo.” Kodi iwo akanalola chikhulupiriro chawo kuyengedwa komanso malingaliro awo kuwongoleredwa kuti agwire ntchito yaikuluyo yomwe inali patsogolo pawo?
17. Kodi odzozedwa okhulupirika anatani 1914 itadutsa adakali padziko lapansi?
17 Nsanja ya Olonda yachingelezi ya September 1, 1916, inati: “Tinaganiza kuti ntchito Yotuta yosonkhanitsa Tchalitchi [odzozedwa] inayenera kutha zisanathe Nthaŵi za Akunja; koma zimenezi sizinatchulidwe m’Baibulo . . . Kodi tili achisoni poona kuti ntchito Yotuta ikupitiriza? . . . Maganizo athu tsopano, abalenu, ayenera kukhala othokoza Mulungu kwambiri, okulitsa chiyamikiro chathu kaamba ka Choonadi chokongolachi chimene Iye watipatsa kuti tichione ndi kudziŵika nacho, ndi kutinso tichuluke m’changu chodziŵitsa ena za Choonadicho.” Chikhulupiriro chawo chinayesedwadi, koma iwo analimbana ndi chiyesocho nachigonjetsa. Choncho Akristufe tiyenera kuzindikira kuti ziyeso za chikhulupiriro zingakhale zambiri ndi zosiyanasiyana.
18, 19. Kodi ndi ziyeso zina zotani za chikhulupiriro zimene anthu a Mulungu anakumananso nazo atangomwalira Mbale Russell?
18 Mwachitsanzo, otsalira anakumana ndi mtundu wina wa chiyeso atangomwalira Mbale Charles T. Russell. Chimenecho chinalidi chiyeso pa chikhulupiriro chawo. Kodi ndani anali “kapolo wokhulupirika” wa pa Mateyu 24:45? Ena anaganiza kuti anali Mbale Russell iyemwiniyo, ndipo anakana kugwirizana ndi makonzedwe atsopano a gulu. Ngati iye ndiye analidi kapoloyo, kodi abalewo anayenera kuchitanji tsopano iye atamwalira? Kodi akanayenera kutsatiranso munthu mmodzi woikidwa mwatsopano, kapena tsopano inali nthaŵi yozindikira kuti Yehova sanali kugwiritsira ntchito munthu mmodzi, koma gulu lonse la Akristu monga chiŵiya chake, kapena monga kagulu kake kakapolo?
19 Chiyeso china chinafika pa Akristu oona mu 1918 pamene akuluakulu adziko, mosonkhezeredwa ndi atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu, ‘anakonza chiwembu mwa lamulo’ polimbana ndi gulu la Yehova. (Salmo 94:20, KJ) Panabuka chizunzo chaukali chothana ndi Ophunzira Baibulo ndipo chinafalikira ku North America ndi ku Ulaya. Chitsutsocho chosonkhezeredwa ndi atsogoleri achipembedzo chinafika pachimake pa May 7, 1918, pamene boma la U.S.A., linapereka zikalata zomangira J. F. Rutherford ndi anzake angapo, kuphatikizapo A. H. Macmillan. Anawanamizira mlandu woukira boma, ndipo akuluakulu a boma ananyalanyaza kuchonderera kwawo koonetsa kuti anali osalakwa.
20, 21. Malinga ndi kuneneratu kwa Malaki 3:1-3, ndi ntchito yotani imene odzozedwa anachita?
20 Ngakhale kuti panthaŵiyo iwo sanaizindikire kwenikweni, ntchito yoyeretsa inali mkati, yonenedwa pa Malaki 3:1-3 kuti: “Ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani pooneka iye? Pakuti [mthenga wa chipangano] adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka; ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golidi ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m’chilungamo.”
21 Pamene Nkhondo Yadziko I inali pafupi kutha, ena mwa Ophunzira Baibulo anakumana ndi chiyeso china cha chikhulupiriro—chakuti kaya adzasunga uchete wathunthu pankhondo za dziko kapena ayi. (Yohane 17:16; 18:36) Ena analephera. Choncho mu 1918, Yehova anatumiza “mthenga wa chipangano,” Kristu Yesu, ku kakonzedwe ka kachisi Wake wauzimu kuti akayeretse kagulu ka alambiri Ake ku maŵanga a dziko. Aja amene anadzipereka pakuonetsa chikhulupiriro choona anaphunzira mwa chochitikacho napita patsogolo, akumalalikirabe mokangalika.
22. Kodi tidzakambitsirananso mbali ziti ponena za ziyeso za chikhulupiriro?
22 Zimene takambitsiranazi, cholinga chake sindicho kungosimba zochitika zakale basi. Nzokhudzana mwachindunji ndi mkhalidwe wauzimu wamakono wa mpingo wa Yehova kuzungulira dziko lonse lapansi. Komano m’nkhani yotsatira, tiyeni tidzaone zina mwa ziyeso za chikhulupiriro zimene anthu a Mulungu akukumana nazo lerolino, komanso tidzaone mmene ifenso tingazilakire.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Nchifukwa chiyani anthu a Yehova ayenera kuyembekezera kuti chikhulupiriro chawo chidzayesedwa?
◻ Kodi panali zoyesayesa zotani pofuna kufalitsa uthenga wa Mulungu isanafike 1914?
◻ Kodi “Seŵero Lapakanema” linali chiyani, ndipo zotulukapo zake zinali zotani?
◻ Kodi zochitikazo m’zaka za 1914-18 zinadzetsa ziyeso zotani kwa odzozedwa?
[Chithunzi patsamba 12]
Chakumapeto kwa zaka za zana la 19 ndi kumayambiriro kwa zaka za zana la 20, anthu m’maiko ambiri ankaphunzira Baibulo mogwiritsira ntchito mabuku akuti “Millennial Dawn,” amene pambuyo pake anadzatchedwa “Studies in the Scriptures”
[Chithunzi patsamba 13]
Kalata yochokera kwa C. T. Russell yokhala ndi mawu oyamba ojambulidwa mmene anati: “‘Seŵero Lapakanema la Chilengedwe’ limaonetsedwa ndi a IBSA—International Bible Students Association. Cholinga chake ndicho kupereka malangizo kwa anthu onse limodzi ndi mfundo zina zachipembedzo ndi zasayansi, zochirikiza Baibulo”
[Chithunzi patsamba 15]
Demetrius Papageorge anayenda uku ndi uku akumaonetsa “Seŵero Lapakanema la Chilengedwe.” Pambuyo pake, anaponyedwa m’ndende chifukwa cha uchete wake wachikristu