-
Kodi Mukukalimira?Nsanja ya Olonda—1990 | September 1
-
-
Kodi Mukukalimira?
“Ngati mwamuna aliyense akukalimira malo antchito a woyang’anira, iye akukhumba ntchito yabwino kwambiri.”—1 TIMOTEO 3:1, “NW.”
1. Kodi ndikukwaniritsidwa kwa cholinga chotani kumene kuli kofunika koposa kwa Mboni za Yehova?
MBONI ZA YEHOVA ziri ndi zolinga zoyenerera zimene zimatsogozedwa ndikuchitidwa mwanjira yaumulungu. Izi sizodabwitsa, popeza kuti Mulungu wawo ali ndi zolinga zolemekezeka ndipo nthaŵi zonse amakwaniritsa zifuno zake. (Yesaya 55:8-11) Atumiki a Yehova sayenera kufanana ndi anthu opanda cholinga chabwino ndikukhala ndi moyo mosasamala akumachita zochepa kupindulitsa aliyense koma iwo okha basi. Chinthu chachikulu kopambana kwa Mboni za Mulungu ndicho kukwaniritsidwa kwa cholinga cholemekezeka chakulengeza uthenga wa Ufumu ndikugaŵana ndi ena chidziŵitso chopatsa moyo cha Mawu a Mulungu—Salmo 119:105; Marko 13:10; Yohane 17:3.
2. Kodi ndicholinga chotani cha amuna Achikristu chotchulidwa ndi Paulo pa 1 Timoteo 3:1?
2 M’gulu la Yehova, mulinso zolinga zina zolemekezeka. Mtumwi Paulo anasonyeza chimodzi cha zimenezi pamene analemba kuti: “Mawuwa ali okhulupirika, ngati mwamuna aliyense akukalimira malo antchito a woyang’anira, iye akukhumba ntchito yabwino kwambiri.” Mwamuna woteroyo amafuna kukwaniritsa chinachake kaamba ka ubwino wa ena. Iye akukhumba “ntchito yabwino kwambiri,” osati moyo wosavuta ndi ulemerero. Matembenuzidwe ena amati: “Nzowonadi kunena kuti mwamuna wosumika mtima wake pautsogoleri ali ndi chikhumbo choyenerera.”—1 Timoteo 3:1, Phillips.
Maupandu kwa Akulu
3, 4. Kodi nchifukwa ninji mwamuna wokalimira kukhala woyang’anira ayenera kuchinjiriza mtima wake?
3 Kodi munthu amene amasumika mtima wake pakukhala woyang’anira Wachikristu amakhala ndi “chikhumbo choyenerera” mwanjira yotani? Eya, chikhumbo ndicho kulakalaka kwachangu kukwaniritsa cholinga chakutichakuti. Nzowona, pali zolinga zoyenerera ndi zosayenerera. Koma ngati modzichepetsa mwamuna akalimira udindo wa woyang’anira kaamba kofuna kutumikira ena, utumiki wake umaperekedwa ndizolinga zabwino ndipo ungatulukire m’madalitso auzimu. Komabe afunikira kuchinjiriza mtima wake.—Miyambo 4:23.
4 Anthu ena okhala ndi chikhumbo amafunafuna ulemerero. Ena amafuna kulamulira anthu anzawo. Umbombo wofuna kutchuka kapena ulamuliro uli wofanana ndi muzu wovunda umene ungapangitse mtengo wowonekera kukhala wolimba kugwera pansi. Mkristu nayenso angagonjere chikhumbo chokhala ndi cholinga cholakwika choterocho. (Miyambo 16:18) “Ndalemba kanthu kumpingo,” anatero mtumwi Yohane, “komatu Deotrofe uja, wofuna kukhala wamkulu wa iwo [“wofuna kukhala mutu wa aliyense,” Phillips], satilandira ife. Momwemo, ndikadza ine, ndidzakumbutsa ntchito zake zimene achitazi, za kunena zopanda pake pa ife ndi mawu oipa; ndipo popeza izi sizimkwanira, salandira abale iye yekha, ndipo ofuna kuwalandira awaletsa, nawataya kunja powatulutsa mumpingo.” (3 Yohane 9, 10) Chikhumbo cha Diotrefe sichinali Chachikristu. Kudzitama ndi kulondola chikhumbo cha kulamulira ena ziribe malo pakati pa otsatira owona a Yesu.—Miyambo 21:4.
5. Kodi oyang’anira ayenera kukhala ndi maganizo otani posamalira mathayo awo?
5 Woyang’anira Wachikristu amene amasamalira mathayo ake ndi cholinga chabwino sadzalondola zikhumbo zadyera. Iye adzalingalira ntchito yabwino kwambiri imeneyi yakukhala wong’anira Wachikristu kukhala mwaŵi wopatsidwa ndi Mulungu ndipo adzaŵeta nkhosa za Mulungu “osati mokangamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.” (1 Petro 5:2, 3) Inde, oyang’anira ayenera kudziyang’anira motsutsana ndi kukhala wonyada ndi kufunafuna kugwiritsira ntchito mphamvu molakwa.
6. Kodi nchifukwa ninji mkulu sayenera kuchita umbuye pa anthu a Mulungu?
6 Mkulu sayenera kuchita ufumu pa Akristu ena, popeza kuti iye ali wantchito mnzawo, osati ‘mbuye wa chikhulupiriro chawo.’ (2 Akorinto 1:24) Pamene atumwi ena anafuna malo apamwamba, Yesu anati: “Mudziŵa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye awo, ndipo akulu awo amachita ufumu pa iwo. Sikudzakhala chomwecho kwa inu ayi; koma amene aliyense akafuna kukhala wamkulu mwa inu, adzakhala mtumiki wanu; ndipo amene aliyense akafuna kukhala woyamba mwa inu, adzakhala kapolo wanu, monga Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:20-28) Mkulu saali Mbusa Wamkulu koma ali kokha mbusa wamng’ono. Ngati achita umbuye pankhosa, amasonyeza mzimu wakunyada. Pakakhala makamaka upandu waukulu ngati anyenga ena kuti amthandize kupititsa patsogolo zikhumbo zake zakunyada. Miyambo imati: “Yense wonyada mtima anyansa Yehova; zowonadi sadzapulumuka chilango.”—Miyambo 16:5.
7, 8. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwa akulu Achikristu kukhala odzichepetsa? (b) Perekani chitsanzo cha mkulu wodzichepetsa.
7 Motero akulu Achikristu ayenera ‘kudzichepetsa pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu.’ Kunyada kumatsekereza munthuyo kukhala wogwiritsiridwa ntchito mwauzimu, popeza kuti odzichepetsa okha ndiwo ali mumkhalidwe woyenera wamtima ndi maganizo kuchita chifuniro cha Mulungu. “Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.” (1 Petro 5:5, 6) Inde, Yehova amadalitsa amaganizo odzichepetsa. Amuna oyeneretsedwa amaikidwa kuchokera mwa oterewa kutumikira monga akulu Achikristu.
8 Mbiri yamakono ya Mboni za Yehova yadzaza ndi zochitika za utumiki wa wodzichepetsa woperekedwa ndi anthu owopa Mulungu. Mwachitsanzo, lingalirani W. J. Thorn, wofatsayo, amene kale anali pilgrim, kapena woyang’anira woyendayenda, ndi wogwira ntchito pa Beteli kwanthaŵi yaitali. Ponena za iye, Mkristu wina anati: “Sindidzaiŵala, sindidzaiŵala konse mawu amene Mbale Thorn ananena amene andithandiza kufikira lerolino. Iye anati, ndikugwira mawu ake, ‘pamene ndiyamba kudziringalira mopambanitsa, ndimapita pangondya, kunena kwake titero, ndikunena kwa ine ndeka kuti: “Ha, fumbi lachabechabe iwe. Kodi uli nchiyani chonyandira?”’” Eya, ndimkhalidwe woyamikirika chotani nanga kwa akulu ndi ena kuusonyeza! Kumbukirani, “mphotho ya chifatso ndi kuwopa Yehova ndiyo chuma, ndi ulemu, ndi moyo.”—Miyambo 22:4.
Chikhumbo Chopatsidwa ndi Mulungu cha Kutumikira
9. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti chikhumbo chakutumikira monga mkulu nchopatsidwa ndi Mulungu?
9 Kodi chikhumbo cha kutumikira monga woyang’anira nchopatsidwa ndi Mulungu? Inde, popeza kuti mzimu wa Yehova umapereka chisonkhezero, kulimba mtima, ndi nyonga kupereka utumiki wopatulika kwa iye. Mwachitsanzo, kodi nchiyani chimene chinachitika pamene otsatira a Yesu ozunzidwawo anapempherera kulimba mtima kuti alalikire? “Panagwedezeka pamalo pamene adasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nalankhula mawu a Mulungu molimbika mtima.” (Machitidwe 4:27-31) Popeza kuti mzimu woyera unapereka zotulukapo zotero, ungasonkhezerenso munthu kukalimira.
10. (a) Kodi nchifukwa chimodzi chotani chimene chingalepheretse mwamuna Wachikristu kukalimira? (b) Ngati Mulungu atipatsa mwaŵi wautumiki, kodi tingakhale otsimikizira zachiyani?
10 Kodi nchifukwa ninji Mkristu wokula msinkhu sangakhale akukalimira? Iye angakhale munthu wauzimu komabe nkudziringalira kukhala wosakwanira. (1 Akorinto 2:14, 15) Ndithudi, tiyenera kukhala ndi malingaliro odzichepetsa aife eni, tikumadziŵa zopereŵera zathu. (Mika 6:8) Mmalo modzitamandira tikumaganiza kuti ndife oyeneretsedwa bwino koposa onse kaamba ka thayo linalake, ndibwino kukumbukira kuti “nzeru iri ndi odzichepetsa.” (Miyambo 11:2) Koma tiyeneranso kuzindikira kuti ngati Mulungu atipatsa mwaŵi wakutumikira, adzaperekanso nyonga yofunikira yochitira. Monga momwe Paulo ananenera kuti: “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.”—Afilipi 4:13.
11. Kodi Mkristu amene sakukalimira chifukwa chakudzilingalira kusakhala ndi nzeru yokwanira kupatsa uphungu angachite chiyani?
11 Mkristu angalephere kukalimira chifukwa chodziringalira kukhala wopanda nzeru yokwanira kupereka uphungu. Eya, mwinamwake iye angapeze nzeru mwakukhala wophunzira Mawu a Mulungu mwaphamphu, ndipo ndithudi iye ayenera kupempherera nzeruyo. Yakobo analemba kuti: “Koma wina wa inu ikamsoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye. Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndikuŵinduka nayo. Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye; munthu wamitima iŵiri akhala wosinkhasinkha panjira zake zonse.” (Yakobo 1:5-8) Poyankha pemphero, Mulungu anapatsa Solomo “mtima wanzeru ndi wakuzindikira” umene unamkhozetsa kusiyanitsa chabwino ndi choipa poweruza. (1 Mafumu 3:9-14) Mkhalidwe wa Solomo unali wapadera, koma mwakuphunzira mwaphamphu ndi thandizo la Mulungu, amuna oikiziridwa mathayo ampingo angapatse ena uphungu mwachilungamo. “Yehova apatsa nzeru; Kudziŵa ndi kuzindikira kutuluka mkamwa mwake.”—Miyambo 2:6.
12. Ngati mwamuna wina saakukalimira chifukwa cha nkhaŵa, kodi nchiyani chimene chingamthandize?
12 Nkhawa yakutiyakuti ingalepheretse munthu kukalimira. Angalingalire kuti sadzatha kusenza thayo lolemera lakukhala mkulu. Ngakhale Paulo anavomereza kuti: “Pali chondisindikiza tsiku ndi tsiku, [nkhaŵa ya, NW] mipingo yonse.” (2 Akorinto 11:28) Koma mtumwiyo anadziŵa zimene anayenera kuchita atakhala ndi nkhaŵa, popeza analemba kuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Inde, pemphero ndi kukhulupirira Mulungu zingathandize kuthetsa nkhaŵa.
13. Kodi munthu angapemphere motani ngati akukaikira kukalimira?
13 Ngati nkhaŵa ikupitirizabe, munthu wokaikira kukalimira angapemphere monga momwe anachitira Davide kuti: “Mundisanthule, Mulungu, nimudziŵe mtima wanga; mundiyese nimudziŵe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndiri nawo mayendedwe [okaikira, NW] nimunditsogolere panjira yosatha.” (Salmo 139:23, 24) Mosasamala kanthu za umene ungakhale mkhalidwe wa malingaliro athu “okaikira” kapena “ankhaŵa,” Mulungu angatithandize kuwalaka kotero kuti tipange kupita patsogolo muuzimu. (Wonani The New International Version.) Kwanenedwa bwino m’salmo lina kuti: “Pamene ndinati, literereka phazi langa, chifundo chanu, Mulungu, chinandichirikiza. Pondichulukira zolingalira zanga mkati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.”—Salmo 94:18, 19.
Tumikirani Mokondwa Monga Momwe Yehova Amafunira
14. Kodi nchifukwa ninji munthu amene sakukalimira ayenera kupempherera mzimu woyera wa Mulungu?
14 Ngati chifukwa cha nkhaŵa, malingaliro akukhala wosakwanira, kapena kupanda chisonkhezero, mwamuna Wachikristu alephera kukalimira, kukakhaladi koyenera kupempherera mzimu wa Mulungu. Yesu anati: “Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu Wakumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?” (Luka 11:13) Popeza kuti mtendere ndi kudziletsa ziri pakati pa zipatso za mzimu, mzimu umenewu ungatithandize kulaka nkhaŵa kapena malingaliro akukhala wosakwanira.—Agalatiya 5:22, 23.
15. Kodi ndimapemphero amtundu wanji amene angathandize osoŵa chisonkhezero chakudzipereka kaamba ka mwaŵi wautumiki?
15 Bwanji ponena za kupanda chisonkhezero? Monga Akristu obatizidwa, tifunikira kupemphera kuti Mulungu atipangitse kuchita chomkondweretsa. Davide anapempha kuti: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova . . . Munditsogolere m’chowonadi chanu ndipo mundiphunzitse.” (Salmo 25:4, 5) Mapemphero onga limeneli adzatithandiza kupeŵa njira yolakwika, ndipo tingapemphere mwanjira yofananayo ngati tiribe chisonkhezero chakukalimira. Tingapemphe Yehova kutipangitsa kufuna kulandira mwaŵi wa kutumikira. Kwenikweni, ngati tipempherera mzimu wa Mulungu ndikugonjera ku chilangizo chake, mosakayikira tizadzipereka enife ngati mwaŵi wakutumikira uperekedwa kwa ife. Ndiiko komwe, atumiki a Mulungu sangafune mwanjira iriyonse kukaniza mzimu wake.—Aefeso 4:30.
16. Kodi ndimaganizo otani amene amapereka chisonkhezero champhamvu chakukalimirira mathayo amumpingo?
16 Pokhala ndi “maganizo a Kristu,” timapeza chisangalalo m’kuchita chifuniro cha Mulungu. (1 Akorinto 2:16, NW) Yesu adali ndi maganizo ofanana ndi a wamasalmo, amene adati: “Kuchita chikondwerero chanu kundikonda, Mulungu wanga; Ndipo malamulo anu ali mkati mwa mtima mwanga.” (Salmo 40:8) Kristu anati: “Tawonani, ndafika kudzachita chifuniro chanu,” ndipo iye anali wotero kufikira imfa pamtengo wozunzirapo. (Ahebri 10:9, 10) Chikhumbo chakuchita chirichonse chothekera muutumiki wa Yehova chimapereka chifuno champhamvu chakukalimirira mathayo ampingo.
Yang’anani Mtsogolo
17. (a) Kodi nchifukwa ninji amuna amene tsopano sakutumikira mokwanira monga momwe anachitira kale sayenera kulefulidwa? (b) Kodi mwaŵi waukulu koposa ngwotani?
17 Chifukwa chamavuto athanzi kapena zifukwa zina, ena amene kale anasamalira ntchito zofunika zampingo alibe mwaŵi woterowo pakalipano. Amenewa sayenera kulefulidwa. Tidziŵa kuti amuna okhulupirika ambiri amene ali osathanso kutumikira mokwanira monga momwe anachitira kale akadali oima nji monga osunga umphumphu. (Salmo 25:21) Ndithudi, akulu anthaŵi yaitali odzichepetsa angapitirizebe kuthandiza ndi chidziŵitso chawo mwakukhalabe m’bungwe la akulu. Ngakhale kuti akulepheretsedwa ndi ukalamba kapena zolepheretsa zina, safunikira kutula udindo. Pakali pano, Mboni ya Yehova iriyonse iyamikiretu mwaŵi wabwino koposa, ‘wakulankhula za ulemerero wa ufumu wa Mulungu’ monga olemekeza dzina lake loyera.—Salmo 145:10-13.
18. (a) Ngati mkulu kapena mtumiki wotumikira wachotsedwa pakukhala mkulu, kodi nchiyani chimene chingafunikire? (b) Kodi ndimaganizo abwino otani amene mkulu wina wochotsedwa pakukhala mkulu anasonyeza?
18 Ngati inu panthaŵi ina munali mkulu kapena mtumiki wotumikira koma tsopano simukutumikiranso muudindo umenewo, khalani otsimikizira kuti Mulungu akukusamaliranibe, ndipo mwinamwake adzakupatsani mwaŵi wosayembekezereka mtsogolo. (1 Petro 5:6, 7) Ngati mufunikira kupanga masinthidwe, khalani wofunitsitsa kuvomereza cholakwa ndikuchiwongolera mwachithandizo cha Mulungu. Ena amene achotsedwa pakukhala akulu akhala ndi maganizo osakhala achikristu, ndipo oŵerengeka akhala osagwira ntchito kapena agwa pa chowonadi. Koma nkwanzeru chotani nanga kukhala wofanana ndi awo amene asonyeza mzimu wabwino! Mwachitsanzo, pamene mkulu amene adatumikira kwazaka zambiri m’Central America anachotsedwa pakukhala mkulu, anati: “Kumandivutitsa maganizo kwambiri kuti ndinatayikiridwa ndi mwaŵi umene ndinaŵerengera kwanthaŵi yaitali. Komabe ndidzagwira ntchito zolimba m’njira iriyonse imene abale adzafuna kundigwiritsira ntchito ndikuchitapo kanthu kuti ndipezenso mwaŵi wanga wautumiki.” M’kupita kwanthaŵi, mbale ameneyo anapatsidwanso mwaŵi wakutumikira monga mkulu.
19. Kodi ndi uphungu woyenera wotani umene uyenera kuperekedwa kwa mbale amene wachotsedwa pakukhala mkulu kapena mtumiki wotumikira?
19 Pamenepa, ngati munachotsedwa pakukhala mkulu kapena mtumiki wotumikira, sungani mkhalidwe wakudzichepetsa. Peŵani maganizo oipa amene akakulepheretsani kuyeneretsedwa kaamba ka mwaŵi wamtsogolo. Mzimu waumulungu umadzetsa ulemu. Mmalo molefulidwa, sumikani maganizo pa mmene Yehova akudalitsira utumiki wanu kapena banja lanu. Limbikitsani banja lanu mwauzimu, chezerani odwala, ndipo limbikitsani ofooka. Koposa zonse, yamikirani mwaŵi wanu wakutamanda Mulungu ndi kulengeza mbiri yabwino monga mmodzi wa Mboni za Yehova.—Salmo 145:1, 2; Yesaya 43:10-12.
20. Kodi ndimotani mmene bungwe la akulu lingathandizire munthu amene anali woyang’anira kapena mtumiki wotumikira?
20 Bungwe la akulu liyenera kuzindikira kuti kuchotsedwa pakukhala mkulu kungachititse kupsinjika maganizo kwa amene anali woyang’anira kapena mtumiki wotumikira, ngakhale ngati angatule mwaŵi umenewo modzifunira. Ngati sanachotsedwe mumpingo, ndipo akulu akuwona kuti mbaleyo ali wokhwethemulidwa maganizo, iwo ayenera kupereka thandizo lachikondi lauzimu. (1 Atesalonika 5:14) Iwo ayenera kumthandiza kuzindikira kuti ali wofunika mumpingo. Ngakhale ngati uphungu wakhala wofunikira, sikungatenge nthaŵi yaitali kuti munthu wodzichepetsa ndi woyamikira alandirenso mwaŵi wowonjezereka wakutumikira mumpingomo.
21. Kodi ndani amene anayembekezera mwaŵi wautumiki, ndipo kodi ndimalingaliro otani amene akuperekedwa kwa amene akuuyembekezera lerolino?
21 Ngati mukukalimira, mungafunikire kuyembekezera kwanthaŵi yakutiyakuti musanalandirenso mwaŵi wautumiki. Musakhale wosaleza mtima. Mose anayembekezera zaka 40 Mulungu asanamgwiritsire ntchito kumasula Aisrayeli muukapolo waku Igupto. (Machitidwe 7:23-36) Asanasankhidwe monga mloŵa mmalo wa Mose, Yoswa anatumikira kwanthaŵi yaitali monga kalinde wake. (Eksodo 33:11; Numeri 27:15-23) Davide anayembekezera nthaŵi yakutiyakuti asanaikidwe pampando wachifumu wa Israyeli. (2 Samueli 2:7; 5:3) Petro ndi Yohane Marko mwachiwonekere anali ndi nyengo zakuyengedwa. (Mateyu 26:69-75; Yohane 21:15-19; Machitidwe 13:13; 15:36-41; Akolose 4:10) Chotero ngati tsopano inu mulibe mathayo ampingo, Yehova angakhale akukulolani kuti muumbidwe mwakupeza chidziŵitso chowonjezereka. Mulimonse mmene zingakhalire, funafunani thandizo la Mulungu pamene mukukalimira, ndipo iye angakudalitseni ndi mwaŵi wowonjezereka wautumiki. Pakali pano, gwirani ntchito mwakhama kuti muyeneretsedwe kaamba ka mathayo ampingo ndikusonyeza mkhalidwe wa Davide, amene analengeza kuti: “Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova; Ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lake loyera kunthaŵi zanthaŵi.”—Salmo 145:21.
-
-
Kodi Mukukalimira?Nsanja ya Olonda—1990 | September 1
-
-
[Chithunzi patsamba 19]
W. J. Thorn anakhazikitsa chitsanzo chabwino monga mkulu wodzichepetsa
-