‘Kanani Nkhani Zachabe’
BAIBULO nlodzala ndi zokumana nazo ndi nkhani zonena za anthu. Sitimangosangalala kuziŵerenga komanso timapindula nazo. Mtumwi Paulo analembera mpingo Wachikristu wa ku Roma kuti: “Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.”—Aroma 15:4.
Paulo mwiniyo anali kusimba zokumana nazo. Baibulo limanena za Paulo ndi Barnaba pamapeto paulendo wawo woyamba waumishonale: “Pamene anafika ku Antiokeya [wa ku Suriya] nasonkhanitsa mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nawo.” (Machitidwe 14:27) Mosakayikira abalewo analimbikitsidwa kwambiri ndi zokumana nazo zimenezi.
Komabe, sizokumana nazo zonse zimene zili zomangirira. Mouziridwa, Paulo anachenjeza Timoteo kuti: “Koma nkhani zachabe ndi za akazi okalamba ukane.” (1 Timoteo 4:7) Ndipo kwa Tito analemba kuti Akristu okhulupirika ayenera kukhala “osasamala nthanu zachabe za Chiyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana nacho chowonadi.”—Tito 1:14.
Kodi nkhani kapena nthanu zachabe zimenezi zinali chiyani? Mawu onse aŵiriwo amachokera ku liwu Lachigiriki lakuti myʹthos (m’Chingelezi, “myth”; m’Chicheŵa, “nthano”). The International Standard Bible Encyclopaedia ikunena kuti liwuli limafotokoza “nkhani (yachipembedzo) imene sili yogwirizana konse ndi zenizeni.”
Dziko la m’nthaŵi ya Paulo linali lodzala ndi nkhani zoterozo. Chitsanzo chimodzi ndibuku la apocrypha la Tobit, lolembedwa mwinamwake zaka mazana aŵiri isanafike nthaŵi ya Paulo. Nkhani imeneyi imanena za Tobit, Myuda wopembedza, amene anachita khungu pamene chitosi cha mbalame chinagwera m’maso mwake. Pambuyo pake, anatumiza mwana wake, Tobias, kukalongerera ngongole. Ali panjira, motsogozedwa ndi mngelo, Tobias anatenga mtima, chiŵindi, ndi ndulu ya nsomba. Ndiyeno anakumana ndi mkazi wamasiye, amene ngakhale kuti anakwatiwa nthaŵi zisanu ndi ziŵiri, anakhalabe namwali chifukwa chakuti mwamuna aliyense amaphedwa ndi chiŵanda usiku waukwati. Atauzidwa ndi mngeloyo, Tobias anakwatira mkaziyo ndi kuthamangitsa chiŵandacho mwakuwotcha mtima ndi chiŵindi cha nsombayo. Pambuyo pake Tobias anabwezeretsa kuona kwa atate wake ndi ndulu ya nsombayo.
Mwachionekere, nthano imeneyi siyowona. Kuwonjezera pakukhala kwake yopeka ndi yokhudza malaulo, ili ndi zophophonya. Mwachitsanzo, cholembedwacho chimanena kuti Tobit anaona zonse ziŵiri chipanduko cha mafuko akumpoto ndi kutengedwa ukapolo kwa Aisrayeli kupita ku Nineve, zochitika za m’mbiri ya Israyeli zimene kuchitika kwake kunasiyana ndi zaka 257. Komabe, nkhaniyo imanena kuti Tobit anali ndi zaka 112 zakubadwa panthaŵi imene anamwalira.—Tobit 1:4, 11; 14:1, The Jerusalem Bible.
Nthano zoterozo nzachilendo pa “chitsanzo cha mawu a moyo” a chowonadi olengezedwa ndi atumiki okhulupirika a Mulungu. (2 Timoteo 1:13) Izo zili zongoyerekezera chabe, zosemphana ndi zenizeni za mbiri, mtundu wa zinthu zosimbidwa ndi akazi okalamba osapembedza. Zimenezi zinali nkhani zimene zinayenera kukanidwa ndi Akristu.
Kuyesa Mawu a Chowonadi
Nkhani zofananazo nzambiri lerolino. Paulo analemba kuti: “Pakuti idzafika nthaŵi imene [anthu] sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu . . . adzalubza dala pachowonadi, nadzapatukira kutsata nthanu zachabe.” (2 Timoteo 4:3, 4) M’mbali zina zadziko lapansi, nthano za matsenga nzofala ndi zochuluka. Chotero, Akristu mwanzeru “amayesa mawu” a nkhani zachipembedzo kuti aone ngati zili zogwirizana ndi Baibulo.—Yobu 12:11.
Mwachionekere, zambiri sizogwirizana ndi Baibulo. Mwachitsanzo, m’mbali zambiri za dziko nkofala kumva nkhani zimene zimachirikiza lingaliro lakuti moyo wa munthu sumafa. Nkhani zimenezi zimafotokoza mmene munthu amafera, ndi kuonekeranso kaya m’thupi la khanda lobadwa kumene, monga mzimu, monga chinyama, kapena monga munthu kumalo ena.
Komabe, Mawu a Mulungu amasonyeza kuti miyoyo ya anthu sili yosafa; miyoyo imafa. (Ezekieli 18:4) Ndiponso, Baibulo limanena kuti akufa alibe moyo m’manda, sakhoza kuganiza, kulankhula, kapena kuchita chilichonse. (Mlaliki 9:5, 10; Aroma 6:23) Motero, awo amene amanyengedwa ndi nkhani zachabe zimene zimachirikiza lingaliro lakuti moyo sumafa, monga mmene Paulo ananenera, ‘amapatuka’ pa “chiphunzitso cholamitsa” cha Baibulo.
Nthano za Matsenga
Nthano zina zimasumika pa zochita za mfiti ndi obwebweta. Mwachitsanzo, m’mbali zina za Afrika, nthumwi za zoipa zimenezi zimanenedwa kuti zili ndi mphamvu zowopsa, zokhoza kudzisanduliza kapena kusanduliza ena kukhala zokwaŵa, anyani, ndi mbalame; kukhala zokhoza kuuluka mlengalenga kukachita ntchito yawo; kukhala zokhoza kuoneka ndi kuzimiririka; kukhala zokhoza kupyola zipupa; ndi kukhala zokhoza kuona zinthu zokwiriridwa pansi pa nthaka.
Kuchuluka kwa nkhani zoterozo, limodzi ndi chikhulupiriro chofala mwa izo, kungasonkhezere ena mumpingo Wachikristu kukhulupiriranso kuti nzowona. Iwo angalingalire kuti popeza kuti anthu wamba sangachite zinthu zoterozo, awo amene amalandira mphamvu zauchiŵanda kuchokera kwa zolengedwa zauzimu, ziŵanda, angachite zinthu zimenezo. Amene amaonekera kukhala maziko a kulingalira koteroko ndi zimene zili pa 2 Atesalonika 2:9, 10, pamene pamati: “Kudza kwake [kwa wosayeruzikayo, NW] kuli monga mwa machitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama; ndi m’chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuwonongeka, popeza chikondi cha chowonadi sanachilandira, kuti akapulumutsidwe iwo.”
Pamene kuli kwakuti nzowona kuti lembali likusonyeza kuti Satana ali wokhoza kuchita ntchito zamphamvu, likutchula kuti Satana alinso woyambitsa wa “zizindikiro ndi zozizwa zonama,” limodzinso ndi “chinyengo chonse cha chosalungama.” Mosasintha, Baibulo limasonyeza Satana kukhala wonyenga wamkulu amene ‘akunyenga dziko lonse lapansi.’ (Chivumbulutso 12:9) Iye ali katswiri pakuchititsa anthu kukhulupirira zinthu zimene sizili zowona.
Chifukwa cha zimenezi, ngakhale umboni ndi zonena za amene anali oloŵetsedwa m’kukhulupirira mizimu ndi ufiti kaŵirikaŵiri zimakhala zosadalirika. Anthu oterowo angakhulupirire mowona mtima kuti anaona, kumva, kapena kukumana ndi zinthu zina; komabe, kwenikweni iwo sanatero. Mwachitsanzo, pali awo amene amaganiza kuti analankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Koma anali mikhole yonamizidwa, yonyengedwa ya chinyengo chausatana. Baibulo limanena kuti akufa ‘atsikira kuli chete.’—Salmo 115:17.
Polingalira za mbiri ya chinyengo ya Mdyerekezi, kuwona kwa nthano zamatsenga kuyenera kukayikiridwa kwambiri. Zambiri zili malingaliro opeka a kukhulupirira malaulo, amene amakulitsidwa ndi kusimbidwa kaŵirikaŵiri.
Kufalitsa nthano zotero kumachirikiza zifuno za atate wa bodza, Satana Mdyerekezi. (Yohane 8:44) Zimasonkhezera chikondwerero m’machitachita a matsenga amene ali onyansa kwa Yehova. (Deuteronomo 18:10-12) Zimakola anthu muukonde wa mantha ndi kukhulupirira malaulo. Nkosadabwitsa kuti Paulo anachenjeza Akristu ‘kusasamala nkhani zachabe.’—1 Timoteo 1:3, 4.
Kukana Umboni wa Ziŵanda
Komabe, bwanji ngati nkhaniyo ikuonekera kukhala yowona? Nthaŵi zina zokumana nazo zimasimbidwa za mizimu kapena okhulupirira mizimu akuvomereza ukulu wa Yehova ndi chowonadi cha Mboni zake. Kodi Akristu ayenera kubwereza nkhani zoterozo?
Ayi, sayenera kutero. Baibulo limanena kuti pamene mizimu yonyansa inafuula kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu, iye “anailimbitsira mawu kuti isamuulule iye.” (Marko 3:12) Mofananamo, pamene mzimu wambwebwe unasonkhezera msungwana wina kuzindikiritsa Paulo ndi Barnaba monga “akapolo a Mulungu wa kumwambamwamba” ndi ofalitsa a “njira ya chipulumutso,” Paulo anatulutsa mzimuwo mwa iye. (Machitidwe 16:16-18) Yesu, Paulo, ndi aliyense wa olemba Baibulo sanalole ziŵanda kuchitira umboni chifuno cha Mulungu kapena atumiki ake osankhidwa.
Nkofunikanso kudziŵa kuti Yesu Kristu anakhala kumalo a mizimu asanabwere padziko lapansi. Iye anamdziŵa bwino lomwe Satana. Komabe, Yesu sanakondweretse ophunzira ake ndi nkhani zonena za zochita za Satana, ndiponso sanapereke tsatanetsatane wa zimene Mdyerekezi angakhoze kuchita ndi zimene sangakhoze. Satana ndi ziŵanda zake sanali mabwenzi a Yesu. Iwo anali opitikitsidwa, opanduka, odana ndi zopatulika, ndipo anali adani a Mulungu.
Baibulo limatiuza zimene tifunikira kudziŵa. Limafotokoza kuti ziŵanda ndani, mmene zimasokeretsera anthu, ndi mmene tingazipeŵere. Limasonyeza kuti Yehova ndi Yesu ngamphamvu kwambiri kuposa ziŵanda. Ndipo limatilangiza kuti ngati titumikira Yehova mokhulupirika, mizimu yoipa singativulaze kwachikhalire.—Yakobo 4:7.
Pamenepo, pali chifukwa chabwino chimene Akristu amakanira nkhani zachabe, nkhani zimene zimangochirikiza zifuno za awo amene amatsutsana ndi Mulungu. Monga momwe Yesu ‘anachitira umboni chowonadi,’ otsatira ake amachitanso momwemo lerolino. (Yohane 18:37) Mwanzeru amalabadira uphungu wa m’Baibulo wakuti: “Zinthu zilizonse zowona . . . zilingirireni izi.”—Afilipi 4:8.
[Chithunzi patsamba 31]
Mitundu yonse ya matsenga iyenera kupeŵedwa ndi Akristu owona