Maphunziro Okhala ndi Cholinga
“Ukaphunzitsa wolungama adzawonjezera kuphunzira.”—MIYAMBO 9:9.
1. Kodi Yehova amayembekezera chiyani kwa atumiki ake ponena za chidziŵitso?
YEHOVA ali “Mulungu wanzeru.” (1 Samueli 2:3) Amaphunzitsa atumiki ake. Mose ananeneratu kuti mitundu ya m’nthaŵi yake ikanena za Israyeli kuti: “Ndithu mtundu waukulu uwu, ndiwo anthu anzeru ndi akuzindikira.” (Deuteronomo 4:6) Akristu owona mofananamo ayenera kukhala achidziŵitso. Ayenera kukhala ophunzira abwino koposa a Mawu a Mulungu. Kusonyeza chifuno cha kuphunzirako, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ifenso, . . . , sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi chizindikiritso cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi chidziŵitso cha mzimu, kuti mukayende koyenera [Yehova, NW] kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m’chizindikiritso cha Mulungu.”—Akolose 1:9, 10.
2. (a) Kodi chofunikira nchiyani kuti mupeze chidziŵitso cholongosoka? (b) Kodi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova lachitaponji pankhaniyi?
2 Kuphunzira ndi lingaliro lakupeza chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi zifuno zake kumafunikiritsa maphunziro achikatikati. Koma anthu ambiri amene afikira pakuphunzira chowonadi cha Mawu a Mulungu amakhala m’maiko kumene analibiretu kapena anali ndi mwaŵi wochepa wakupeza maphunziro oyenerera. Analibe mwaŵiwo. Kugonjetsa vuto limeneli, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova kwa zaka zambiri tsopano lakhala likulangiza kuti, kumene ali ofunikira, makalasi ophunzitsira kulemba ndi kuŵerenga ayenera kulinganizidwa m’mipingo. Zoposa zaka 30 zapitazo, nyuzipepala ya ku Brazil Diário de Mogi inafalitsa nkhani ya mutu wakuti “Mboni za Yehova Zikumenya Nkhondo Motsutsana ndi Kusadziŵa Kuŵerenga ndi Kulemba.” Inanena kuti: “Mlangizi woyeneretsedwa amakhala wokonzekera . . . moleza mtima kuphunzitsa ena kuwerenga ndi kulemba. . . . Ophunzira, chifukwa cha mikhalidwe yeniyeniyo yowasonkhezera kukhala aminisitala a Mulungu, ayenera kukulitsa chidziŵitso chawo cha chilankhulidwe kotero kuti adzipereka nkhani.” Motero mazana ambiri a anthu padziko lonse akhala okhoza kukhala ophunzira abwino a Mawu a Mulungu. Amachita maphunziro ofunika ameneŵa ndi cholinga chachikulu m’maganizo.
Maluso Ofunikira Kukhala Aminisitala Ogwira Mtima
3, 4. (a) Kodi nchifukwa ninji Akristu owona amakondwerera maphunziro? (b) Kodi mu Israyeli mkhalidwe unali wotani, ndipo ndimaphunziro oyenerera ati amene ali osapeŵeka m’mipingo yathu lerolino?
3 Akristu owona ali okondwerera m’maphunziro, osati chifukwa chakungofuna kukhala ophunzira, koma kuti akhale atumiki ogwira mtima a Yehova. Kristu anapatsa Akristu onse ntchito ya “kupanga ophunzira mwa anthu a mitundu yonse, . . . mukumawaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndakulamulirani.” (Mateyu 28:19, 20, NW) Kuti aphunzitse ena, iwo eniwo ayenera kuphunzira choyamba, ndipo zimenezi zimafunikiritsa njira zabwino zophunzirira. Ayenera kukhala ndi luso lakupenda Malemba mosamalitsa. (Machitidwe 17:11) Kuti akwaniritse ntchito yawo, amafunikiranso kukhala okhoza kuŵerenga mosadodoma.—Wonani Habakuku 2:2; 1 Timoteo 4:13.
4 Monga momwe tinawonera m’nkhani yapita, pali chifukwa chabwino cha kukhulupirira kuti, kwakukulukulu, ngakhale achichepere mu Israyeli wakale anadziŵa kuŵerenga ndi kulemba. (Oweruza 8:14; Yesaya 10:19) Aminisitala Achikristu lerolino afunikira kulemba manotsi abwino pamene akupita ku umboni wa kunyumba ndi nyumba. Amalemba makalata, amalemba nsonga pamisonkhano, ndi kulemba ndemanga m’nkhani yokaiphunzira. Zonsezi zimafunikira kalembedwe koŵerengeka bwino. Kusunga zolembedwa mumpingo Wachikristu kumafunikira chidziŵitso chachikatikati cha masamu.
Mapindu Akuphunzira Sukulu Mokwanira
5. (a) Kodi liwu lakuti “sukulu” linayamba bwanji? (b) Kodi ndimwaŵi wotani umene achichepere ayenera kuumvetsetsa bwino?
5 Mokondweretsa, liwu lakuti “sukulu” limachokera ku liwu Lachigiriki skho·leʹ, limene poyambirira linatanthauza “kupuma” kapena kugwiritsira ntchito nthaŵi ya kupuma kuchita kanthu kofunikira kwambiri, monga ngati kuphunzira. Pambuyo pake linadzatanthauza malo kumene kuphunzira koteroko kunachitidwa. Zimenezi zikusonyeza kuti, panthaŵi ina, okhupuka okha—mu Girisi ndi maiko ena ochuluka—ndiwo anali ndi nthaŵi yakupuma yakuphunzira. Kwakukulukulu gulu la ogwira ntchito wamba linakhalabe muumbuli. Lerolino, m’maiko ambiri ana ndi achichepere amapatsidwa nthaŵi yakuphunzira. Mboni zachichepere ziyeneradi kutenga mwaŵiwo kuti akhale atumiki achidziŵitso ndi okhoza a Yehova.—Aefeso 5:15, 16.
6, 7. (a) Kodi ndimapindu ena ati akukhala ndi maphunziro oyenerera? (b) Kodi kuphunzira chinenero chachilendo kungakhale kothandiza m’njira zotani? (c) Kodi chimachitika nchiyani lerolino pakati pa achichepere ambiri pamene amaliza sukulu?
6 Chidziŵitso choyambirira cha histoli, jogirafe, sayansi, ndi zina zotero chidzathandiza Mboni yachichepere kukhala mminisitala wachikatikati. Sukulu yawo idzawaphunzitsa osati kokha maphunziro ambiri komanso njira zophunzirira. Akristu owona saleka kuphunzira pamene amaliza sukulu. Komabe, zimene amapindula m’kuphunzira kwawo zimadalira kwenikweni pa kudziŵa kwawo maphunziriridwe. Ponse paŵiri maphunziro akudziko ndi amumpingo angawathandize kukulitsa maluso awo akuganiza. (Miyambo 5:1, 2) Pamene akuŵerenga adzakhala okhoza bwino kuzindikira chimene chiri chofunika, chimene chimafunikira kulembedwa kapena kulowezedwa.
7 Mwachitsanzo, kuphunzira chinenero chachilendo sikudzangokulitsa luso la maganizo a achichepere komanso kuwapangitsa kukhala othandiza kwambiri ku gulu la Yehova. M’nthambi zina za Watch Tower Society, achichepere ambiri awona kukhala kwaphindu kukhala okhoza kulankhula kapena kuŵerenga bwino Chingelezi. Ndiponso, aminisitala Achikristu onse ayenera kuyesayesa kukhala odziŵa kukamba bwino m’chinenero chawo. Mbiri yabwino ya Ufumu imafunikira kufotokozedwa m’njira yomvekera bwino, ya galamala yomvekera bwino. Maumboni amasonyeza kuti m’dziko lerolino, achichepere ambiri pamene amaliza sukulu amakhalabe ndi vuto la kulemba ndi kulankhula bwino ndipo ngakhale kuchita masamu okhweka; ndipo amangokhala ndi chidziŵitso chosamvekera bwino cha histole ndi jogirafe.
Maphunziro Okwanira
8. Kodi ndimalemba ati amene amagwira ntchito pa nkhani ya maphunziro akudziko ndi luso la munthu lakudzichirikiza?
8 Chifukwa chake, imeneyi ikuwonekera kukhala nthaŵi yoyenerera yakulingalira kaimidwe kamaganizo ka Mkristu ku maphunziro akudziko. Kodi ndimalamulo a Baibulo ati amene ali oyenerera pankhani imeneyi? Choyamba, m’maiko ambiri kugonjera koyenerera kwa “Kaisara” kumafunikira kuti makolo Achikristu atumize ana awo kusukulu. (Marko 12:17; Tito 3:1) Kwa Mboni zachichepere, m’ntchito yawo ya kusukulu ayenera kukumbukira Akolose 3:23, amene amati: “Chiri chonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa [Yehova, NW], osati kwa anthu ayi.” Lamulo lachiŵiri lophatikizidwapo ndi lakuti Akristu ayenera kukhala okhoza kudzichirikiza, ngakhale ngati ali aminisitala amene ndiapainiya anthaŵi yonse. (2 Atesalonika 3:10-12) Ngati ngokwatira, mwamuna ayenera kusamalira bwino mkazi wake ndi ana ake amene angabadwe, ndi zotsalapo pang’ono zopatsa osoŵa ndi kuchirikiza ntchito yolalikira yakwawoko ndi yadziko lonse.—Aefeso 4:28; 1 Timoteo 5:8.
9, 10. (a) Kodi nchiyani chimene chimawonekera kukhala chikhoterero m’maiko ambiri? (b) Kodi nchiyani chimene minisitala mpainiya angalingalire kukhala malipiro oyenerera?
9 Kodi Mkristu wachichepere amafunikira maphunziro ochuluka motani kotero kuti amvere malamulo a Baibulo amenewa ndi kufitsa mathayo ake Achikristu? Zimenezi zimasiyana m’maiko osiyanasiyana. Komabe, kukuwonekera kuti chikhoterero chochuluka m’maiko ambiri nchakuti mlingo wa kuphunzira wofunikira kuti munthu adzilandira malipiro oyenera tsopano ngwokwera kuposa mmene unaliri zaka zingapo zapitazo. Malipoti ochokera ku nthambi za Watch Tower Society m’mbali zosiyanasiyana za dziko akusonyeza kuti m’maiko ambiri nkovuta kupeza ntchito za malipiro oyenerera pambuyo pakumaliza maphunziro oyambirira ofunidwa ndi lamulo kapena m’maiko ena ngakhale pambuyo pakumaliza sukulu yasekondale.
10 Kodi mawuwa “malipiro oyenerera” akutanthauzanji? Amasonya ku ntchito zolandira ndalama zambiri. Webster’s Dictionary imafotokoza kuti “oyenera” m’nkhaniyi akutanthauza “okwanira, okhutiritsa.” Mwachitsanzo, kodi nchiyani chimene chinganenedwe kukhala “chokwanira” kwa awo ofuna kukhala aminisitala apainiya a mbiri yabwino? Oterewa kwenikweni afunikira ntchito yaganyu kupeŵa “kulemetsa” abale awo kapena mabanja awo. (1 Atesalonika 2:9) Malipiro awo anganenedwe kukhala “okwanira,” kapena “okhutiritsa,” ngati zimene amalandirazo zimawalola kukhala ndi moyo woyenerera ndi kuwapatsa nthaŵi yokwanira ndi mphamvu kuchita uminisitala wawo Wachikristu.
11. Kodi nchifukwa ninji achichepere ena asiya utumiki waupainiya, ndipo ndi funso lotani limene likudzutsidwa?
11 Kodi chimachitika kaŵirikaŵiri nchiyani lerolino? Kwanenedwa kuti m’maiko ena achichepere okhala ndi cholinga chabwino asiya sukulu pambuyo pakumaliza maphunziro ofunikira kotero kuti akhale apainiya. Iwo sanaphunzire ntchito iriyonse kapena ziyeneretso za ntchito yakudziko. Ngati iwo sanathandizidwe mwandalama ndi makolo awo, amafunikira kupeza ntchito yaganyu. Ena anavomereza ntchito zimene zikawafunikiritsa kugwira ntchito maola ambiri kuti apeze ndalama zambiri. Pomakhala otopa mwakuthupi, anasiya uminisitala waupainiya. Kodi oterowo angachite chiyani kuti akhoze kudzichirikiza mwandalama ndi kubwereranso mu utumiki waupainiya?
Lingaliro Lachikatikati la Maphunziro
12. (a) Ponena za maphunziro, kodi ndi malingaliro aŵiri ati onkitsa amene Mkristu ayenera kupeŵa? (b) Kwa atumiki odzipatulira a Yehova ndi ana awo, kodi maphunziro ayenera kukhala ndi cholinga chotani?
12 Lingaliro lachikatikati la maphunziro lingathandize. Kwa achichepere akudziko ochuluka, maphunziro ndiwo chizindikiro cha kutchuka, chinthu chowathandiza kuyesayesa kukhala apamwamba, mfungulo ya kukhupuka m’moyo wa zinthu zakuthupi. Kwa ena, kuphunzira ndiyo ntchito yofunika kumalizidwa mwamsanga monga momwe kungathekere. Malingaliro ameneŵa saali oyenerera kwa Akristu owona. Pamenepa, kodi nchiyani nanga chimene chinganenedwe kukhala “lingaliro lachikatikati”? Akristu ayenera kuwona maphunziro monga njira yopezera zotulukapo zokhumbika. M’masiku omaliza ano, cholinga chawo ndicho kutumikira Yehova kwambiri ndi mogwira mtima monga momwe kungathekere. Ngati, m’dziko limene akukhala, maphunziro ochepa kapena ngakhale akusekondale akawapezera kokha ntchito yopereka malipiro osakwanira kudzichirikiza monga apainiya, pamenepo maphunziro owonjezereka kapena kosi ingalingaliridwe. Izi zidzakhala ziri ndi chonulirapo chenicheni cha kuchita utumiki wanthaŵi zonse.
13. (a) Kodi mlongo wina mu Philippines wakhoza bwanji kupitiriza utumiki wake waupainiya pamenenso akukwaniritsa thayo lakuyang’anira banja lake? (b) Kodi ndichenjezo lotani lapanthaŵi yake?
13 Ena aloŵa makosi amene awapatsa mwaŵi wa ntchito zowatheketsa kuyambanso utumiki wanthaŵi zonse. Mlongo wina ku Philippines ndiye anali woyang’anira banja, koma anafuna kuchita upainiya. Nthambi inasimba kuti: “Anakhoza kutero chifukwa anachita maphunziro owonjezereka akumuyeneretsa kukhala akauntanti.” Nthambi imodzimodziyo ikusimba kuti: “Tiri ndi ambiri amene akuchita maphunziro ndipo panthaŵi imodzimodziyo akhoza kulinganiza maprogramu awo kuchita upainiya. Kwakukulukulu amakhala ofalitsa abwinopo popeza kuti ali akhama pophunzira, pokhapokha ngati sakufikira pakukhumba mopambanitsa zolondola zakudziko.” Ndemanga yomalizirayi iyenera kutipatsa kanthu kena kokalingalira. Cholinga cha maphunziro owonjezereka, kumene zimenezi ziri zoyenerera, sichiyenera kuiŵalidwa kapena kusinthidwa kukhala chonulirapo chofuna zinthu zakuthupi.
14, 15. (a) Kodi nchifukwa ninji sipayenera kuikidwa malamulo okakamiza ponena za maphunziro? (b) Kodi ndimaphunziro akudziko otani amene abale ena amathayo anachita, koma kodi nchiyani chimene chakwaniritsa chosoŵacho?
14 M’maiko angapo, masukulu asekondale amapereka makosi antchito amene angakonzekeretse ntchito Mkristu wachichepere panthaŵi imene akamaliza maphunziro. Ngakhale pamene zimenezi siziri zotero, m’maiko ena achichepere anzeru okhala ndi maphunziro ochepa akusukulu amapeza ntchito zaganyu zimene amalandira ndalama zokwanira kuchita upainiya. Chotero sipayenera kukhala malamulo ankhokera osonkhezera kapena kutsutsa maphunziro apamwamba.
15 Ambiri amene tsopano akutumikira m’mathayo monga oyang’anira oyendayenda, pamalikulu a Sosaite, kapena pa iriyonse ya nthambi zake anali ndi maphunziro oyambirira okha. Anali apainiya okhulupirika, sanaleke kuphunzira, anaphunzitsidwa ntchito, ndipo apatsidwa mathayo okulirapo. Sali achisoni ndi zosankha zimene anapanga. Kumbali ina, ena a anzawo anasankha kupeza maphunziro a payunivesite nasiya kupita patsogolo mwauzimu, potsamwitsidwa ndi nthanthi zowononga chikhulupiriro ndi “nzeru ya dziko lino.”—1 Akorinto 1:19-21; 3:19, 20; Akolose 2:8.
Kuŵerengera Mtengo
16. (a) Kodi ndani ayenera kusankha kaya maphunziro owonjezereka akufunikira, ndipo kodi nchiyani chimene chiyenera kuikidwa poyamba m’maganizo? (b) Kodi nchiyani chimene chiyenera kulingaliridwa?
16 Kodi ndani ayenera kusankha kaya Mkristu wachichepere ayenera kuchita maphunziro owonjezereka kapena kosi? Malamulo a Baibulo a umutu amagwira ntchito panopo. (1 Akorinto 11:3; Aefeso 6:1) Pa maziko ameneŵa makolo adzafunadi kuthandiza ana awo kusankha ntchito ndiponso maphunziro amene angafunikire. M’maiko ambiri zosankha za maphunziro ndi ntchito ziyenera kuchitidwa pasadakhale pamene munthu akali ku sekondale. Imeneyo ndiyo nthaŵi pamene makolo ndi achichepere Achikristu afunikira kufuna chitsogozo cha Yehova m’kupanga chosankha chanzeru, ali ndi zabwino zaufumu pamalo oyamba m’maganizo. Achichepere ali ndi zikhoterero ndi maluso achibadwa osiyana. Makolo anzeru adzalingalira zimenezi. Ntchito yonse yowona mtima njolemekezeka, ikhale ya ovolosi kapena ya thayi. Pamene kuli kwakuti dziko limakweza ntchito za mu ofesi ndi kunyoza ogwira ntchito zolimba za manja, Baibulo silitero ayi. (Machitidwe 18:3) Chotero pamene makolo ndi Akristu achichepere lerolino, pambuyo pakupenda mosamalitsa ndi mwapemphero maubwino ndi kuipa kwake, asankha kapena kukana maphunziro pambuyo pa sukulu ya sekondale, ena mumpingo sayenera kuwasuliza.
17. Kodi ndichosankha chotani chimene makolo ena monga Mboni apangira ana awo?
17 Ngati makolo Achikristu mwathayo asankha kupezera ana awo maphunziro owonjezereka pambuyo pasukulu yasekondale, chimenecho ndichosankha chawo. Nthaŵi ya maphunziro ameneŵa imasiyanasiyana malinga ndi mtundu wa ntchito yosankhidwa. Chifukwa cha ndalama ndiponso kutheketsa ana awo kuchita utumiki wanthaŵi zonse mwamsanga monga momwe kungathekere, makolo Achikristu ambiri asankhira ana awo maphunziro a nthaŵi yaifupi m’masukulu ophunzitsa ntchito kapena maluso ena. M’nkhani zina achichepere afunikira kuphunzira maluso ena kuchokera m’makampani ena koma nthaŵi zonse ali ndi chonulirapo chakuchita utumiki wa kwa Yehova moyo wawo wonse.
18. Ngati makosi owonjezereka achitidwa, kodi nchiyani chiyenera kukumbukiridwa?
18 Ngati makosi owonjezereka ayambidwa, ndithudi cholinga sichiyenera kukhala kupambana koposa kapena kukalimira ntchito yapamwamba yakudziko. Makosi ayenera kusankhidwa mosamala. Magazini ano agogomezera maupandu a maphunziro apamwamba, ndipo atero molungamitsa, popeza kuti maphunziro apamwamba kwambiri amatsutsa “chiphunzitso cholamitsa” cha Baibulo. (Tito 2:1; 1 Timoteo 6:20, 21) Ndiponso, kuyambira m’ma 1960, masukulu ambiri amaphunziro apamwamba akhala malo odzaza ndi kusayeruzika ndi chisembwere. “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” watsutsa mwamphamvu kuloŵa m’malo okhala ngati amenewo. (Mateyu 24:12, 45) Komabe, kuyenera kuvomerezedwa kuti, masiku ano achichepere amayang’anizana ndi maupandu ameneŵa m’masukulu asekondale ndi m’makoleji ndipo ngakhale kuntchito.—1 Yohane 5:19.a
19. (a) Kodi ndikusamala kotani kumene kuyenera kuchitidwa ndi awo osankha kuchita makosi owonjezereka apanyumba? (b) Kodi ndimotani mmene ena agwiritsira ntchito maphunziro kuubwino wawo?
19 Ngati pakhala chosankha cha kuwonjezera maphunziro, nkoyenerera kwa Mboni yachichepere, ngati ndiiko komwe kuli kotheka, kuchitira zimenezi akumakhala kunyumba, kumene angathe kusunga mkhalidwe wake wabwino wozikidwa pa phunziro Lachikristu, kufika pamisonkhano, ndi ntchito yolalikira. Poyambirira penipeni kaimidwe kayenera kuchitidwa pa malamulo a Baibulo. Kuyenera kukumbukiridwa kuti Danieli ndi anzake atatu Achihebri anali andende mu Babulo pamene anakakamizidwa kuchita maphunziro apamwamba, koma iwo anasunga umphumphu wawo mosalekeza. (Danieli, chaputala 1) Pamene kuli kwakuti amaika zabwino zauzimu patsogolo, Mboni zachichepere zambiri m’maiko angapo zachita makosi kuti akhoze kuchita ntchito yaganyu monga maakauntanti, ogulitsa, aphunzitsi, otembenuza, omasulira kapena ntchito ina iriyonse imene ikawachirikiza m’ntchito yawo yaikulu yaupainiya. (Mateyu 6:33) Ochuluka a achichepere ameneŵa pomalizira akhala oyang’anira oyendayenda kapena odzipereka pa Beteli.
Anthu Ophunzira, Ogwirizana
20. Kodi nkusiyana kotani kwaudziko kumene kulibe malo pakati pa anthu a Yehova?
20 Pakati pa anthu a Yehova, kaya ntchito ya munthu ndi ya ovolosi, ya thayi, ya ulimi, kapena mautumiki ena, onse afunikira kukhala ophunzira abwino a Baibulo ndi aphunzitsi okhoza. Maluso opezedwa ndi onse mwakuŵerenga, kuphunzira, ndi kuphunzitsa amawonekera kuchotsa kusiyana kumene dziko limaika pakati pa ogwira ntchito za manja ndi za muofesi. Zimenezi zimachititsa chigwirizano ndi kulemekezana kumene kwakukulukulu kumawonekera pakati pa ogwira ntchito odzifunira pa nyumba za Beteli ndi pomanga nyumba za Watch Tower Society, kumene mikhalidwe yauzimu iri yofunika ndi kuti aliyense ayenera kukhala nayo. Kunoko, anthu achidziŵitso cha ntchito ya mu ofesi amagwira ntchito limodzi ndi ogwira ntchito zamanja mokondwera, onse akumasonyeza chikondi choyamikira wina ndi mnzake.—Yohane 13:34, 35; Afilipi 2:1-4.
21. Kodi chonulirapo cha Akristu achichepere chiyenera kukhala chotani?
21 Makolo, tsogozani ana anu ku chonulirapo chokakhala ziŵalo zopindulitsa za chitaganya cha dziko latsopano! Akristu achichepere, gwiritsirani ntchito mwaŵi wa maphunziro monga njira yodzikonzekeretsa kukhazikitsa mokwanira mwaŵi m’kutumikira Yehova! Monga ophunzitsidwa, nonsenutu tsimikizirani kukhala ziŵalo zokonzekeretsedwa bwino za chitaganya cha teokratiki ponse paŵiri tsopano ndipo kosatha mu “dziko lapansi latsopano” lolonjezedwa ndi Mulungu.—2 Petro 3:13; Yesaya 50:4; 54:13; 1 Akorinto 2:13.
[Mawu a M’munsi]
a Wonaninso Nsanja ya Olonda (Chingelezi) ya September 1, 1975, tsamba 542-4.
Yesani Chikumbukiro Chanu
◻ Kodi nchifukwa ninji Akristu owona ali okondwera ndi maphunziro?
◻ Kodi ndimalingaliro ati onkitsa a maphunziro amene Akristu owona ayenera kupeŵa?
◻ Kodi ndimaupandu otani akuwonjezera maphunziro amene ayenera kulingaliridwa, ndipo ndi kusamala kotani kumene kuyenera kuchitidwa?
◻ Kodi nkusiyana kotani kwaudziko kumene kulibe malo pakati pa anthu a Yehova?
[Chithunzi patsamba 16]
Mwakuphunzira mwakhama, Akristu achichepere angakhale ziŵalo zothandiza za chitaganya cha dziko latsopano
[Chithunzi patsamba 19]
Maphunziro owonjezereka, ngati asankhidwa, ayenera kusonkhezeredwa ndi chikhumbo cha kutumikira Yehova bwinopo