Musasiye Okhulupirira Anzanu
M’BALE wina dzina lake Jarosław ndi mkazi wake Beata anati: “Kwa zaka 10, tinatengeka kwambiri ndi kuchita malonda ndipo chuma tinali nacho ndithu. Ngakhale kuti tinaleredwa m’choonadi, tinasochera kwambiri ndipo tinalibe mphamvu mwauzimu moti zinali zovuta kwambiri kuti tibwerere.”a
M’bale wina dzina lake Marek anati: “Chifukwa cha kusintha kwa moyo ndiponso ndale m’dziko la Poland, ndinkangokhalira kuchotsedwa ntchito. Zimenezi zinandikhumudwitsa kwambiri. Ndinkaopa kuyambitsa bizinezi yangayanga chifukwa choona kuti ndilibe luso pa nkhani za bizinezi. Kenako ndinaganiza zoti ndiyese ndipo ndinkaona kuti zindithandiza kusamalira banja langa popanda kusokoneza moyo wanga wauzimu. Koma patapita nthawi, ndinazindikira kuti ndinalakwitsa.”
M’dzikoli zinthu zikukwera mitengo kwambiri ndiponso ntchito zikusowa. Izi zachititsa kuti anthu ena asasankhe zinthu mwanzeru chifukwa chosowa mtengo wogwira. Abale ambiri aganiza zowonjezera maola amene amagwira ntchito, kupezanso ntchito yachiwiri kapena kuyambitsa bizinezi yawo ngakhale kuti sadziwa zambiri pa nkhani za bizinezi. Iwo amaganiza kuti akapeza ndalama zambiri zizithandiza banja lawo ndipo sipangakhale vuto lililonse lauzimu. Komabe zinthu zotigwera mwadzidzidzi ndiponso kusokonekera kwa chuma padzikoli kungasokoneze mapulani ndiponso zolinga zabwino. Zoterezi zachititsa ena kugwera mumsampha wa dyera n’kunyalanyaza zinthu zauzimu pofuna kupeza chuma.—Mlal. 9:11, 12.
Abale ndi alongo ena atengeka kwambiri ndi zinthu za m’dziko moti alibenso nthawi yophunzira Baibulo paokha, yopita ku misonkhano kapena yolalikira. N’zosachita kufunsa kuti khalidwe limeneli limasokoneza kulambira kwawo ndiponso ubwenzi wawo ndi Yehova. Izi zimachititsa kuti asokonezenso ubwenzi wofunika kwambiri ndi ‘abale ndi alongo awo m’chikhulupiriro.’ (Agal. 6:10) Ena mwapang’onopang’ono amachoka mu ubale wachikhristu. Tiyeni tione bwinobwino nkhani yosiya abale ndi alongo athu.
Udindo Wathu kwa Okhulupirira Anzathu
Abale ndi alongofe, timakhala ndi mipata yambiri yosonyeza kuti timakonda kwambiri anzathu. (Aroma 13:8) N’kutheka kuti inuyo mwaonapo mu mpingo wanu anthu ‘osautsika opempha thandizo.’ (Yobu 29:12) Anthu ena amasoweratu zinthu zofunika kwambiri pa moyo. Mtumwi Yohane anatikumbutsa za mwayi umene umakhalapo chifukwa cha zimenezi. Iye anati: “Aliyense amene ali ndi zinthu zofunika pa moyo, n’kuona m’bale wake zikumusowa, koma osamusonyeza m’bale wakeyo chifundo chachikulu, kodi munthu ameneyu amakonda Mulungu?”—1 Yoh. 3:17.
Mwina mwathandizapo anthu oterewa mowolowa manja. Komatu sikuti ife timangofunika kuthandiza abale athu ndi zinthu zakuthupi zokha. Ena angapemphe thandizo chifukwa cha kusungulumwa kapena kukhumudwa. Iwo angamavutike chifukwa chodziona kuti ndi opanda pake, kudwala matenda aakulu, apo ayi imfa ya munthu amene amamukonda. Tikhoza kuwalimbikitsa mwa kuwamvetsera ndi kulankhula nawo. Tikamachita zimenezi, timasonyeza kuti timafuna kuwathandiza mwauzimu ndiponso kuwakhazika mtima pansi. (1 Ates. 5:14) Izi zimathandiza kuti tizikondana kwambiri ndi abale athu.
Chifukwa cha udindo wawo, abusa achikhristu makamaka angakhale oyenera kuthandiza anthu mwa kuwamvetsera mwachifundo, kukhala omvetsa zinthu ndiponso kupereka malangizo a m’Malemba mwachikondi. (Mac. 20:28) Akamatero, oyang’anira amatsanzira mtumwi Paulo amene ‘ankakonda’ abale ndi alongo ake auzimu.—1 Ates. 2:7, 8.
Koma kodi Mkhristu akachoka mu gulu la nkhosa, n’chiyani chimachitikira udindo wake kwa okhulupirira anzake? Nkhani yokonda chuma imakhudza aliyense ngakhale oyang’anira. Ndiyeno, kodi chingachitike n’chiyani ngati Mkhristu atakopeka ndi nkhani imeneyi?
Kulemedwa ndi Nkhawa za Moyo
Monga taonera, tikhoza kuda nkhawa ngati tikugwira ntchito mwakhama kwambiri pofuna kupeza zinthu zofunika m’banja lathu ndipo tingayambe kuona kuti zinthu zauzimu si zofunika kwambiri. (Mat. 13:22) Marek, amene tam’tchula poyamba uja, anati: “Bizinezi yanga itasokonekera ndinaganiza zopita kunja kukagwira ntchito. Ndinanyamuka n’kukagwira ntchito kwa miyezi itatu n’kubwera. Nditangokhala kanthawi kochepa ndinapitanso kwa miyezi ina itatu n’kubwera ndipo kenako ichi chinangokhala chizolowezi changa. Mkazi wanga amene sanali m’choonadi anavutika kwambiri maganizo chifukwa cha zimenezi.”
M’banja lawo zinthu sizinkayenda bwino. Komatu si zokhazi. Marek anapitiriza kuti: “Ndinkagwira ntchito maola ambiri pamalo otentha koopsa. Kuwonjezera pamenepo, ndinkakhala ndi anthu a makhalidwe oipa omwe ankakonda kudyera anzawo masuku pamutu. Iwo ankangokhala ngati zigawenga. Ndinasokonezeka maganizo kwambiri ndipo ndinkaona kuti ndikuponderezedwa. Ndinalibiretu nthawi yodzisamalira ndekha ndipo ndinayamba kukayikira zoti ndingathandize ena.”
Mavuto amene anabwera chifukwa cha zimene Marek anasankha ayenera kutichititsa kuganiza mofatsa. Nthawi zina zingaoneke kuti kupita kunja kungachepetse mavuto a zachuma, koma kodi sikungayambitsenso mavuto ena? Mwachitsanzo, kodi banja lanu lingakhudzidwe bwanji mwauzimu ndiponso mwamaganizo? Kodi ulendo wanu sungachititse kuti musiyane ndi mpingo wachikhristu? Kodi sungatisokonezere mwayi wotumikira okhulupirira anzathu?—1 Tim. 3:2-5.
Inunso mukudziwa kuti si anthu okhawo amene amapita kunja omwe amatanganidwa kwambiri ndi ntchito. Taganizirani za Jarosław ndi mkazi wake Beata. M’baleyu anati: “Poyamba tinali ndi zolinga zabwinobwino. Titangokwatirana kumene tinayamba kabizinezi kogulitsa masoseji. Koma titayamba kupindula kwambiri, tinaganiza zokulitsa bizinezi yathu. Tsopano tinkakhala ndi nthawi yochepa kwambiri moti tinayamba kuphonya misonkhano yachikhristu. Pasanapite nthawi yaitali ndinasiya upainiya ndiponso kutumikira monga mtumiki wothandiza. Tinatengeka ndi ndalama zimene tinkapeza moti tinakuza kwambiri bizinezi yathu n’kusonkherana ndalama ndi munthu wina wosakhulupirira. Kenako ndinkapita kumayiko ena kukapangana ndi anthu za bizinezi ya madola mamiliyoni ambiri. Sindinkapezekapezeka pakhomo ndipo ubwenzi wanga ndi mkazi wanga komanso mwana wathu unayamba kusokonekera. Bizinezi yathu imene inapita patsogoloyi inachititsa kuti pang’onopang’ono tiyambe kugona mwauzimu. Popeza tinasiyana ndi mpingo sitinkaganiza n’komwe za abale athu.”
Kodi pamenepa tikuphunzirapo chiyani? Mtima wofuna kukhala ndi moyo wabwinopo ungakole Mkhristu n’kumuchititsa kuti azirale mwauzimu mpaka kufika potaya “malaya ake akunja,” omwe ndi chizindikiro chake chachikhristu. (Chiv. 16:15) Izi zingachititse kuti tisiyane ndi abale athu amene poyamba tikanatha kuwathandiza.
Dzifufuzeni Moona Mtima
Mwina tingaganize kuti, ‘Zimenezi sizingandichitikire.’ Koma tonse tingachite bwino kuganizira kwambiri zinthu zimene ndi zofunikadi pa moyo. Paulo analemba kuti: “Sitinabwere ndi kanthu m’dziko, ndipo sitingatulukemo ndi kanthu. Choncho, pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.” (1 Tim. 6:7, 8) N’zoona kuti moyo umasiyana m’dziko lililonse. Zinthu zimene anthu okhala m’mayiko otukuka angaone ngati n’zofunika kwa munthu aliyense zikhoza kukhala zosafunikira kwenikweni m’mayiko ena.
Kaya moyo ndi wotani kumene tikukhala, tiyenera kuganizira mawu otsatira a Paulo. Iye anati: “Anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero ndi mumsampha. Iwo amakodwa ndi zilakolako zambiri zowapweteketsa ndiponso amachita zinthu mopanda nzeru. Zinthu zimenezi zimawawononga ndi kuwabweretsera mavuto.” (1 Tim. 6:9) Msampha umatcheredwa malo obisika kuti ukole nyama modzidzimutsa. Ndiye kodi tingatani kuti tisakoledwe ndi ‘zilakolako zambiri zopweteketsa’?
Tikamaika zinthu zofunika kwambiri pa malo oyamba tidzapeza nthawi yochitira zinthu za Ufumu monga kuphunzira Baibulo patokha. Kuphunzira kotereku ndiponso kupemphera kungathandize Mkhristu kukhala “woyenerera bwino ndi wokonzeka mokwanira” kuthandiza ena.—2 Tim. 2:15; 3:17.
Kwa zaka zingapo akulu achikondi ankathandiza ndiponso kulimbikitsa Jarosław. Izi zinachititsa kuti ayambe kusintha kwambiri moyo wake. Iye anati: “Tsiku lina pamene tinali kukambirana ndi akulu, anandithandiza kwambiri ndipo anagwiritsa ntchito chitsanzo cha m’Malemba cha wolamulira wachinyamata yemwe anali wachuma. Mnyamatayu ankafuna moyo wosatha koma sankafuna kusiya chuma chake. Ndiyeno mosamala anandithandiza kuzindikira zimene ndingaphunzire pa nkhaniyo. Izi zinanditsegula maso kwambiri.”—Miy. 11:28; Maliko 10:17-22.
Jarosław anadzifufuza moona mtima ndipo anaganiza zosiya kuchita mabizinezi akuluakulu. Patapita zaka ziwiri zokha, iye ndi banja lake anadzakhalanso amphamvu mwauzimu. Panopa iye akutumikira abale ake monga mkulu. Jarosław anati: “Ndikaona abale akutanganidwa kwambiri ndi mabizinezi mpaka kufika ponyalanyaza moyo wawo wauzimu, ndimawafotokozera zimene zinandichitikira kuti ndiwathandize kuzindikira kuopsa komangidwa m’goli ndi anthu osakhulupirira. Si chinthu chapafupi kukana njira zokopa zopezera chuma komanso kupewa kuchita chinyengo.”—2 Akor. 6:14.
Nayenso Marek anaphunzira madzi atafika m’khosi. Ngakhale kuti atapita kunja anapeza ntchito yapamwamba n’kumathandiza banja lake, ubwenzi wake ndi Mulungu komanso ndi abale ake unasokonekera. Koma kenako anadzasintha zimene ankaika pa malo oyamba. Iye anati: “Kwa zaka zambiri zochita zanga zinkafanana ndi za Baruki amene ‘anali kufunafuna zinthu zazikulu.’ Ndiyeno ndinapemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima n’kumufotokozera nkhawa zanga zonse. Panopa ndayambanso kuona zinthu mwauzimu.” (Yer. 45:1-5) Tsopano Marek akuyesetsa kuti ayenerere kugwira “ntchito yabwino” yokhala woyang’anira mu mpingo.—1 Tim. 3:1.
Marek amapereka chenjezo kwa aliyense amene akuganiza zopita kunja kukafufuza ntchito yabwino. Iye amati: “Munthu akapita kunja, zimakhala zosavuta kuti akodwe m’misampha ya dziko loipali. Iye amavutika kulankhulana ndi ena chifukwa chosadziwa bwino chilankhulo cha m’dzikolo. N’zoona kuti pobwerera munthu amakhala ndi ndalama koma amakhalanso ndi mabala auzimu amene angatenge nthawi yaitali kuti apole bwinobwino.”
Kugawa bwino nthawi yogwirira ntchito yakuthupi komanso yokwaniritsa udindo wathu kwa abale ndi alongo kungathandize kuti tizisangalatsa Yehova. Tingaperekenso chitsanzo kwa anthu ena kuti nawonso azisankha zinthu mwanzeru. Anthu olemedwa ndi nkhawa amafunika kuthandizidwa, kuchitiridwa chifundo ndiponso kupatsidwa chitsanzo chabwino ndi abale ndi alongo awo. Akulu mu mpingo ndiponso anthu ena okhwima mwauzimu angathandize okhulupirira anzawo kuti aziona zinthu mwauzimu komanso kuti azipewa kusokonezedwa ndi nkhawa za moyo.—Aheb. 13:7.
Choncho tiyeni tisasiye okhulupirira anzathu chifukwa chotanganidwa kwambiri ndi ntchito zakuthupi. (Afil. 1:10) M’malomwake, tiyeni tikhale ‘olemera kwa Mulungu’ pamene tikuika zinthu za Ufumu patsogolo pa moyo wathu.—Luka 12:21.
[Mawu a M’munsi]
a Mayina ena tawasintha.
[Zithunzi patsamba 21]
Kodi ntchito yanu imachititsa kuti musamapezeke pa misonkhano?
[Zithunzi patsamba 23]
Kodi mumagwiritsa ntchito mwayi wanu wothandiza abale ndi alongo anu auzimu?