Sonyezani Chikhulupiriro mwa Yehova—Mwa Kuchita Zinthu Zophunziridwa
“Khulupirira Yehova ndipo chita chokoma; khala m’dziko, ndipo tsata chowonadi.”—Masalmo 37:3.
1, 2. (a) Nchiyani chomwe chiyenera kukhala chotulukapo chokhumbiridwa cha phunziro laumwini? (b) Yakobo akupereka fanizo lotani, ndipo kodi kuyang’ana kolongosoledwa ndi iye kuli koipa?
PHUNZIRO la wina la Mawu a Mulungu siliri kokha kaamba ka chimwemwe chaumwini. Phunziro liyenera kukhala njira ya kukulitisira chikhulupiriro mwa Yehova. (Miyambo 3:1-5) Mawu a wamasalmo pamwambapo akusonyeza kuti kukhulupirira kwa umulungu, m’kubwezera, kumadziwonetsera iko kokha mwa munthu mwa ‘kuchita kwake chokoma.’
2 Yakobo anafulumiza kuti: “Khalani akuchita mawu, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha. Pakuti ngati munthu ali wakumva mawu, wosati wakuchita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang’anira nkhope yake ya chibadwidwe chake m’kalirole. Pakuti wadziyang’anira yekha nachoka, naiwala pompaja anali wotani.” (Yakobo 1:22-24) Chotero kuyang’ana kumeneku sikunayenera kukhala kokha kuyang’ana mofulumira. Liwu la Chigriki kaamba ka kuyang’ana mofulumira. Liwu la Chigriki kaamba ka “kuyang’ana” lomwe lagwiritsidwa ntchito pano mokulira “limasonyeza kachitidwe ka maganizo m’kumvetsetsa nsonga zinazake ponena za chinthu.”—An Expository Dictionary of New Testament Words, lolembedwa ndi W. E. Vine; yerekezani ndi Machitidwe 7:31, Kingdom Interlinear.
3. Ndimotani mmene munthu angayang’anire pa kalirole mwamsanga ndi kuiwala amene “iye ali”?
3 Chotero, tangolingalirani, munthu akudzisanthula iyemwini pa kalirole, mwinamwake akumapeza chithunzithunzicho kukhala choseketsa. Iye angawone chibwano chowirikiza kaŵiri chomwe chinadza chifukwa cha kudya mopambanitsa ndi kumwa mopambanitsa, zikope zotupa pansi pa maso ake chifukwa cha kusowa tulo, ndi makwinya pa mphumi pake chifukwa cha zodera nkhaŵa zokhalirira. Atadziyang’ana iyemwini mwachindunji, iye amagamulapo kupanga masinthidwe okulira m’zizoloŵezi ndi njira ya moyo. Kenaka “amachoka.” Ndi chithunzithunzi chodabwitsachi chitachokeratu m’maso, iye “mwamsanga amaiwala,” osati mokulira chimene iye amawoneka, koma “mtundu wa munthu amene iye ali.” Chigamulo chake cha kupanga masinthidwe chimapita.
4. Ndimotani mmene fanizo la Yakobo likugwirizanirana ndi kuphunzira kwathu Malemba?
4 Mofananamo, mungakhale wophunzira wokhoza wa Baibulo. Komabe, ndimotani mmene mumavomerezera ku chimene mumawona m’kalirole wa Mawu a Mulungu? Pamene zophophonya zauzimu ndi mawanga zawunikiridwa, kodi chimenecho chimakupangitsani inu kukhala wodera nkhaŵa kokha kwa kamphindi, kapena kodi mumapanga chogamulapo champhamvu kuwongolera zolakwikazo? Yokobo anawonjezera kuti: “Koma iye wakupenyerera m’lamulo langwiro ndilo laufulu natero chipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakuchita ntchito, adzakhala wodala m’kuchita kwake.” (Yakobo 1:25) Wamasalmo anapemphera kuti: “Mundiyendetse mopita malamulo anu [Yehova], pakuti ndikondwera mmenemo.”—Masalmo 119:33.
Zimene Zochita Zathu Zimanena Ponena za Ife
5. (a) Nchiyani chimene zochita zathu zimanena ponena za ife? (b) Kodi ndi ngozi yotani imene ikudikira awo amene “amachita mhulupulu”?
5 Ndithudi, chimene timachita kapena kuzolowera kuchita chimatsimikizira chimene tiri mkati. Ndipo mwamsanga kapena pambuyo pake munthu amawonetsera “munthu wa mkati” mwa chimene amachita kaya chabwino kapena choipa. (Masalmo 51:6) Anatero Solomo: “Ngakhale mwana adziŵika ndi ntchito zake ngati ntchito yake iri yoyera ngakhale yolungama.” (Miyambo 20:11) Ichi chinali chowona ponena za Yakobo ndi Esau pamene anali achichepere. Pamene nthaŵi inapita, zochita za Esau zingapangitsa kusoweka kwake chiyamikiro chauzimu kuwonekera. (Genesis 25:27-34; Ahebri 12:16) Ichi chakhalanso chowona ponena za zikwi zomwe zinadzinenera kukhala zokhulupirira mwa Yehova koma zomwe zinatsimikizira kukhala amene Baibulo limachita “wakuchita mphulupulu.” (Yobu 34:8) Wamasalmo analemba kuti: “Pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake, chitero kuti adzawonongeke kosatha.”—Masalmo 92:7.
6. Kodi nchifukwa ninji chiri chofunikira kuti tipange chikhulupiriro chathu mwa Yehova kuwonekera tsopano?
6 Chiŵerengero cha anthu oipa chikukula, ndipo kuwonongedwa kwawo kudzakhala posachedwapa; Mulungu sadzalekelera oipa ku nthaŵi zosatha. (Miyambo 10:29) Chotero chiri chofunika koposa kuti tipange chikhulupiriro chathu mwa Yehova kuwonekera mwa kuchita zimene timaphunzira. “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma,” akuchenjeza tero Petro. (1 Petro 2:12) Kodi ndi mbali zina ziti, chotero, zimene tingawongolere?
Zochita Zathu Ndi Ena
7. Nchifukwa ninji tiyenera kukhala ochenjera m’kuchita kwathu ndi “awo akunja”?
7 Mbali imodzi ingakhale mkhalidwe wathu wochitira ndi ena. Miyambo 13:20 imachenjeza kuti: “Ukayenda ndi opusa udzapwetekedwa.” Kulephera kugwiritsira ntchito uphungu wouziridwa umenewu, ena adzilola iwo eni kukhala ozoloŵerana mopambanitsa ndi anthu a kudziko pa ntchito ndi pa sukulu. Mbale wina wokwatira anakhala wodzilowetsamo koposa mu mkhalidwe woipa ndi mkazi pa ntchito yake. Iye anagwirizananso ndi ogwira nawo ntchito a amuna pa maulendo ku malo okhazikitsidwa a kumaloko omwera, kutulukapo m’kukhala kwake woledzera. Ndithudi, tifunikira “kupitiriza kuyenda mu nzeru ndi iwo akunja.”—Akolose 4:5.
8. Ndimotani mmene ena angawongolere m’zochita zawo ndi Akristu anzawo?
8 Koma bwanji ponena za zochita zathu ndi Akristu anzathu? Tangoyerekezani, mwachitsanzo, kuti muli mu ngongole ya ndalama kwa mbale. Kodi inu mukafunikira kuchedwa mopambanitsa kumubwezera iye, mukumalingalira kuti chifukwa mbaleyo akuwoneka kukhala wolemera, inu mukaifunikira iyo kuposa iye? “Woipa akongola osabweza,” amatero Masalmo 37:21. Kapena ngati inu muli wolemba ntchito, kodi mumagwiritsira ntchito prinsipulo lakuti “Wogwira ntchito ayenera kulipira kwake” pamene chibwera ku kulipira Mboni zolembedwa ntchito? (1 Timoteo 5:18) Paulo anali wokhoza kunena ponena za kachitidwe kake: “M’chiyero ndi kuwona mtima kwa umulungu . . . tinadzisunga pa dziko lapansi, koma koposa kwa inu.”—2 Akorinto 1:12.
Kavalidwe ndi Kapesedwe Kodzichepetsa
9. Ndi zikhoterero zotani m’kavalidwe ndi kapesedwe zimene zawonedwa ndi akulu ena?
9 Woyang’anira woyendayenda mmodzi mu Germany analongosola Akristu ena a kumaloko monga “mbadwo wa nsapato zoseŵerera tenisi” chifukwa cha kuvala kwawo zovala zomwe timakhala nazo pochita zinthu wamba pa msonkhano. Ofesi ya nthambi inawonjezera kuti opezeka pa msonkhano ena “amakhalirira pa kukhala ovala mosasamala,” ngakhale kuti “gulu lokulira la abale athu amavala modzichepetsa.” Dziko lina mofananamo likusimba kuti “kusoweka kwa ukhondo waumwini liri vuto kuno . . . Abale ena samavala zovala zoyera. Iwo amasiya tsitsi lawo losapesa ndi lakuda pamene akupita ku misonkhano kapena mu utumiki wa m’munda.” Chiri chofunika chotani nanga kaamba ka atumiki a Yehova kukhala aukhondo ndi audongo mu mbali zonse!—2 Akorinto 7:1.
10. (a) Ndi prinsipulo lotani limene liyenera kutsogoza kusankha kwathu kwa kavalidwe ndi kapesedwe? (b) Ndi liti pamene uphungu ungakhale woyenerera, ndipo ndimotani mmene tiyenera kuvomerezera ku iwo?
10 Tifunikira “kuvala modzichepetsa, ndi ulemu ndi kuyenera,” makamaka pamene tikudzilowetsa m’machitachita auzimu. (1 Timoteo 2:9, New International Version) Nkhani siri yakuti kaya sitaelo ina iri yatsopano mopambanitsa koma kaya ngati iri yoyenerera kaamba ka mmodzi wodzinenera kukhala mtumiki wa Mulungu. (Aroma 12:2; 2 Akorinto 6:3) Zovala zomwe timakhala nazo pochita zinthu wamba kapena zothina zingacheutse kuchoka ku uthenga wathu. Masitaelo omwe mwachidziŵikire ndipo mwadala amapangitsa amuna kuwoneka monga akazi kapena akazi kuwoneka monga amuna ali motsimikizirika kunja kwa dongosolo. (Yerekezani ndi Deuteronomo 22:5) Ndithudi, miyambo ya kumaloko imasiyana, mogwirizana ndi nyengo, zofunikira za ntchito, ndi zina zotero, kotero kuti mpingo Wachikristu sumapanga malamulo amphamvu ndi ofulumira kukwaniritsa ubale wa dziko lonse. Ndiponso akulu sayenera kukakamiza zokonda zawo zaumwini pa nkhosa. Ngakhale kuli tero, ngati sitaelo ya kapesedwe ya wofalistsa wa Ufumu mwachisawawa imasokoneza mpingo kapena kucheutsa kuchoka ku utumiki, uphungu wachifundo uli woyenerera. Kodi inu mukavomereza ku uphungu woterowo modzichepetsa, kusonyeza chikhulupiriro mwa Yehova?—Ahebri 12:7.
Kukhulupirira Mulungu Kupereka kaamba ka Ofunafuna Ufumu
11. Ndimotani mmene ena agwidwira m’kulondola zinthu zakuthupi, ndipo nchifukwa ninji ichi chiri chopanda nzeru?
11 “Koma muthange mwafuna ufumu ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:33) Chiri chomvetsa chisoni chotani nanga pamene ena alephera kulabadira mawu amenewo! Akumameza nthano ya chisungiko cha zachuma, iwo mopusa amalondola chuma, maphunziro a kudziko, ndi ntchito za kudziko, “akumatama kulemera kwawo.” (Masalmo 49:6) Solomo anachenjeza kuti: “Usadzitopetse kuti ulemere. . . . Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu yowuluka mlengalenga.”—Miyambo 23:4, 5.
12. Ndimotani mmene awo omwe akulondola chuma ‘amadzipyozera iwo eni ndi zowawa zambiri’?
12 Mtumwi Paulo mowonjezera akuchenjeza kuti: “Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama, chimene ena pochikhumba anasokera, nataya chikhulupiriro nadzipyoza ndi zowawa zambiri.” (1 Timoteo 6:10) M’kufunsidwa mu U.S.News & World Report, Dr Douglas LaBier ananena kuti amuna ndi akazi ambiri achichepere m’kulondola chuma “amasimba malingaliro a kusakhutiritsidwa, kudera nkhaŵa, kupsyinjika, kupanda kanthu, misala, limodzinso ndi kudandaula konse kwa kuthupi—kupweteka kwa mutu, kupweteka kwa msana, mvauto a m’mimba, kusowa tulo, mavuto a kudya.”
13. Nchifukwa ninji chiri chabwino koposa kukhala okwaniritsidwa ndi “chakudya ndi chofunda”?
13 Awo amene amakhulupirira mwa Yehova kupereka kaamba ka iwo amadzipatula iwo eni ku zowawa ndi zodera nkhaŵa zambiri. Zowona, kukhala okhutiritsidwa ndi kokha “chakudya ndi chofunda” chingatanthauze muyezo wa makhalidwe odzichepetsa mokulira. (1 Timoteo 6:8) Koma “chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo.” (Miyambo 11:4) M’kuwonjezerapo, pamene tiwonjezera utumiki wathu kwa Yehova, timadziika ife eni pa mzera kaamba ka “madalitso a Yehova” omwe “alemeretsa, ndipo sawonjezerapo chisoni.”—Miyambo 10:22.
“Funani Mtendere ndi Kuulondola”
14, 15. (a) Ndi mtundu wotani wa nkhani zimene nthaŵi zina zasokoneza mtendere wa mipingo? (b) Kodi mtendere ungalondoledwe motani pamene kusamvana kwabuka?
14 Njira ina yosonyezera chikhulupiriro chathu mwa Yehova iri “kufuna mtendere ndi kuulondola” pakati pa akhulupiriri anzathu. (1 Petro 3:10-12) Nthaŵi zina, ngakhale ndi tero, nkhani zazing’ono zingaloledwe kukhala magwero a mkangano wokulira pakati pa abale; kukongoletsa kwa Nyumba ya Ufumu, masinthidwe m’magawo a mpingo, mathayo a Phunziro la Bukhu, kusamalira kwa zoperekedwa za magazini ndi mabukhu. Kapena, m’nkhani zina, m’malo mwa kuthetsa mikangano yaumwini kapena ya malonda mu mzimu wa Mateyu 18:15-17, abale aleka kulankhulana wina ndi mnzake kapena asokoneza mpingo ndi mkangano wawo.
15 Yakobo ananena kuti: “Chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere.” (Yakobo 3:18) M’chikondwerero cha mtendere, chotero, khalani oyedzamira ku kukhoterera ku zokonda kapena malingaliro a ena, ngakhale kunyalanyaza kuyenera kwaumwini. (Yerekezani ndi Genesis 13:5-12.) Mwachitsanzo, ngati mipingo iŵiri imagawana Nyumba ya Ufumu, mpingo umodzi suyenera kutenga malo akuti holoyo ndi “yathu” ndipo chotero iri ndi ufulu wa kulamulira nthaŵi zosonkhanira kapena nkhani zina ku mpingo winawo. Ulemu wachibadwa ndi kugwirizana ziyenera kukhalapo.
16. Nchiyani chomwe chiri phindu la kuzindikira dongosolo la teokratiki m’nyumba ndi mu mpingo?
16 Mikangano yambiri ingapewedwe pamene tizindikira kokha dongosolo la teokratiki ndi kusunga malo athu oyenerera. (1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:22-27) Pamene akazi alemekeza zokhumba za amuna awo, ana malamulo a makolo awo, atumiki otumikira zitsogozo zochokera kwa akulu, machitidwe awo amachita “kaamba ka makulidwe a [mpingo] kufikira chinango chake mwa chikondi.” (Aefeso 4:16) Chitalingaliridwa, nthaŵi zina amuna, makolo, ndi akulu amaphophonya. (Aroma 3:23) Koma kodi kuwukira, kudandaula, kapena kutsutsa zitsogozo zolunjikitsidwa bwino zimawongolera mkhalidwewo? Chikakhala chabwinopo chotani nanga kusunga malo athu ogawiridwa ndi Mulungu ndi kufuna mtendere!
Kudzikakamiza Ife Eni m’Munda
17. Ndi zifukwa zotani zimene ena amapereka chifukwa cha kukhala kokha ndi kugawanamo kochepera mu ntchito yolalikira? (b) Ndimotani mmene Yesu analimbikitsira Akristu kuvomereza ku zididikizo za lerolino?
17 Kwa ambiri, ngakhale ndi tero, chitokoso chachikulu koposa chiri kukwaniritsa ntchito ya Chikristu yolalikira mbiri yabwino. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Ena ali kokha ndi kugawanamo kochepera mu utumiki wa m’munda, mwinamwake akumanena kuti zididikizo za kupeza ndalama zothandizira ndi kusamalira banja zimachipangitsa icho kukhala chovuta kaamba ka iwo kuchita zochulukira. Chitalingaliridwa, zididikizo za “masiku otsiriza” ziri zowopsya. (2 Timoteo 3:1) Yesu, ngakhale kuli tero, anachenjeza molimbana ndi kukhala ‘olemetsedwa ndi zodera nkhaŵa za moyo.’ Pamene mikhalidwe ikuipiraipirabe, Akristu ayenera ‘kuweramuka ndi kutukula mitu yawo.’ (Luka 21:28, 34) Imodzi ya njira yabwino koposa ya “Kuchirimika” molimbana ndi zowukira za Satana iri kukhala ndi “mapazi athu ovekedwa ndi makonzedwe a uthenga wabwino”—mokhazikika kugawanamo m’kulalikira!—Aefeso 6:14, 15.
18. Nchiyani chomwe chingakhale chifukwa chimene ena amalekera kukhala ndi kugawanamo kokwanira mu ntchito yolalikira?
18 Kubwerera m’tsiku la Paulo, Akristu ambiri (chifupifupi m’mipingo ina) anali “kutsata za iwo okha, si za Kristu Yesu.” (Afilipi 2:21) Kodi ichi chingakhale chowona ponena za ena pakati pathu lerolino? Mwinamwake iwo akulephera kuwona kufunafuna Ufumu monga mmene anachitira munthu yemwe anapeza “miyala ya mtengo wapatali” kaamba ka imene iye akapanga kudzipereka nsembe kulikonse. (Mateyu 13:45, 46) Akumagonjera ku zikondwerero zaumwini, iwo amatenga mzera wotsutsa wochepera wa kupereka kokha utumiki wochepa. Kumbukirani, ngakhale ndi tero, kuti chikondi kaamba ka Yehova ndi kwa mnzathu chimasonkhezera Akristu owona kulalikira, ngakhale ngati kuyamba kulankhula kwa alendo kumakhala kotsutsana ndi chikoterero chathu chachibadwa.—Mateyu 22:37-39.
19. Nchifukwa ninji Yehova amaipidwa ndi zoyesayesa zofunda, ndipo ndimotani mmene tingasanthulire utumiki wathu weniweni kwa iye?
19 Ngati sitifulumizidwa kulalikira, kenaka chikondi chathu kaamba ka Yehova ndi chikhulupiriro chathu mwa iye chiri chochepera mofanana ndi kuzindikira kwa maganizo. “Umudziŵe Mulungu wa atate wako ndi kumtumikira ndi mtima wangwiro,” Davide anachenjeza Solomo, “pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingalira za maganizo.” (1 Mbiri 28:9) Yehova sapusitsidwa ndi kuyesayesa kofunda. Ngakhale kugawanamo mokhazikika mu utumiki wa m’munda sikumamkwaniritsa iye ngati tikupereka kokha mbali yochepa ya chimene tikanachita ngati tinali ‘kudzikakamiza ife eni mwamphamvu.’ (Luka 13:24) Mkristu aliyense chotero ayenera kupanga phindu lowona mtima la kugawanamo kwake mu utumiki wa m’munda ndi kudzifunsa iyemwini: ‘Kodi ine ndithudi ndikuchita zonse zimene ndingathe?’ Mwinamwake masinthidwe m’zoyambirira zathu afunikira kupangidwa.
Kusonkhezeredwa “Kuchita Zabwino” ndi Zitsanzo za Ena
20. Nchifukwa ninji chiri choyenerera kusanthula zitsanzo zabwino zoikidwa ndi Akristu anzathu?
20 Utumiki wathu kwa Mulungu sumachitidwa mwa “kuyerekeza ndi munthu wina.” (Agalatiya 6:4) Mosasamala kanthu za icho, zitsanzo zabwino za ena kaŵirikaŵiri zingatisonkhezere ife kuchita zowonjezereka. Mtumwi Paulo iyemwini ananena kuti: “Khalani akunditsanza ine, monga inenso ndiri wakutsanza Kristu.” (1 Akorinto 11:1) Kenaka, lingalirani, nthaŵi yochulukira imene abale athu akuthera mu utumiki wa m’munda mwezi uliwonse. Mu United States, avereji ya maora ya ofalitsa yakwera kuchokera pa maora 8.3 mu 1979 kufika ku maora 9.7 mu 1987! Abale athu akhala akuwonjezera mokhazikika nthaŵi imene amawononga m’munda. Kodi chimemecho chiri chowona ponena za inu?
21. Nchiyani chomwe chafulumiza ambiri kulowa mu ntchito ya upainiya? Chitirani chitsanzo.
21 Atasonkhezeredwa ndi zitsanzo zachangu za ena, unyinji wochulukira wakhala ukulowa mu ntchito ya upainya wokhazikika. Mu California (U.S.A.) mlongo wachichepere wotchedwa Angela analandira ntchito yopereka chiyeso, kuphatikizapo kulipiriridwa maphunziro ku koleji yomwe angasankhe. Angela, m’malomwake, anasankha utumiki wa nthaŵi zonse. Chifukwa chake? “Mwakuyanjana ndi apainiya ambiri, ndinali wokhoza kuwona chimwemwe chozama chenicheni ndi chikhutiritso osati kokha ndi iwo eni koma ndi unansi wawo ndi Yehova. Ndinafuna kukhala ndi chimwemwe chozama ndi chikhutiritso chimenechi.”
22. Ndi ati omwe ali mapindu a kuchita zinthu zophunziridwa?
22 Kodi mukufuna “chimwemwe chozama ndi chikhutiritso”? Chotero “khulupirirana Yehova ndi kuchita chokoma”! Lolani chimene mumadziŵa chikusonkhezereni inu kuchita kuthekera kwanu konse mu utumiki wa Yehova. Kuchita zinthu zophunziridwa kudzapanga kupita kwanu patsogolo kwauzimu kuwonekera kwa onse ndipo kudzapindulitsa ena m’njira yopulumutsa moyo. (1 Timoteo 4:15, 16) Chotero, lolani kuti tonsefe, tivomereze ku mawu a Paulo pa Afilipi 4:9. “Zimeneso mudaziphunzira ndi kuzilandira ndi kuzimva ndi kuziwona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.”
Nsonga kaamba ka Kubwereramo
◻ Nchiyani chomwe chiyenera kukhala chivomerezo chathu ku kuyang’anira pa kalirole wa Mawu a Mulungu?
◻ Ndimotani mmene tingawongolere mu mkhalidwe wathu wa kuchitira ndi ena?
◻ Nchifukwa ninji chiri chopanda nzeru kulondola zinthu zakuthupi?
◻ Ndimotani mmene tingafunire mtendere mu mpingo?
◻ Nchiyani chomwe chiyenera kutisonkhezera ife kukhala ndi kugawanamo kokwanira mu utumiki wa m’munda?
[Chithunzi patsamba 16]
Sichiri chokwnaira kuwona zophophonya ndi mabanga auzimu. Tiyenera kugwirirapo ntchito kuwongolera izo!
[Zithunzi patsamba 18]
Awo olondola chuma kaŵirikaŵiri amabweretsa “zowawa zambiri” pa iwo eni