Lingaliro la Baibulo
Kodi Mmene Mumapesera ndi Mmene Mumavalira Zilidi Nkanthu kwa Mulungu?
“Monga momwe mpambo wa mitu yankhani umatiuza zimene zili m’buku, . . . Momwemonso chizoloŵezi choonekera, ndi zovala za mwamuna kapena mkazi, zimatiuza mmene iye alili.”—Philip Massinger, wolemba maseŵero wa ku England.
M’ZAKA za zana lachitatu C.E., wolemba nkhani zatchalitchi, Titus Clemens anapanga mpambo wautali wamalamulo okhudza kavalidwe ndi kapesedwe. Ankaletsa anthu kudzikometsera ndi kuvala nsalu zokongola ndi zamitundu yambiri. Akazi sankayenera kupaka tsitsi lawo mankhwala olisintha mtundu kapena “kudzola zinthu zotchera msampha wachinyengo,” ndiko kuti, “kudzipaka penti.” Amuna ankawalangiza kupala tsitsi lapamutu pawo chifukwa “mutu wometa unali . . . kumpangitsa mwamuna kuoneka wolemekezeka,” koma ndevu sankayenera kuzimeta chifukwa “zimapangitsa nkhope ya munthu kulemekezeka ndi kuoneka kuti ndi mwamunadi.”a
Ndiyeno patapita zaka mazana ambiri, mtsogoleri wa Aprotestanti, John Calvin anapanga malamulo ochita kutchula mitundu yazovala ndi maonekedwe ake zimene otsatira ake anayenera kuvala. Mphete ndi mikanda zinali kuonedwa monga zonyansa, ndipo mkazi akanaponyedwa m’ndende chifukwa chopesa tsitsi lake “mopangitsa amuna kumcheukira.”
Kuletsa zinthu kopambanitsa ngati kumeneko kumene atsogoleri achipembedzo akhala akuchita kwa zaka zambiri, kwapangitsa anthu ena oona mtima kudzifunsa kuti, Kodi Mulungu alinazodi kanthu zoti ndimavala chiyani? Kodi amaletsa mafashoni ena kapena kugwiritsira ntchito mafuta odzikongoletsera? Kodi Baibulo limaphunzitsa chiyani?
Nkhani Yodziŵa Mwini
Chosangalatsa nchakuti, monga momwe kwalembedwera pa Yohane 8:31, 32, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ngati mukhala inu m’mawu anga, . . . mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” Inde, Yesu anaphunzitsa zinthu zoona ncholinga chakupepuzira anthu mitolo yolemetsa imene inapangidwa ndi miyambo ndi ziphunzitso zonyenga. Zinali ziphunzitso zakupumulitsa “akulema ndi akuthodwa.” (Mateyu 11:28) Yesu, ngakhale Atate wake, Yehova Mulungu, samafuna kulamulira anthu pamoyo wawo mpaka kufikira pakuwaletsa kuchita zimene maganizo awo akufuna kuchita pankhani zaumwini. Yehova amawafuna kuti akhale anthu akulu misinkhu, “amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.”—Ahebri 5:14.
Choncho, Baibulo silimapereka malamulo otchula chimodzichimodzi okhudza kavalidwe ndi kapesedwe kapena mafuta odzikongoletsera, kusiyapo malamulo achindunji amene anapatsa Ayuda mwa Chilamulo cha Mose omwe anali owathandiza kulekana ndi anthu a mitundu yoyandikana nayo ndi makhalidwe awo a dama. (Numeri 15:38-41; Deuteronomo 22:5) M’dongosolo lachikristu, kupesa ndi kuvala zangokhala nkhani yodzisankhira mwini.
Komabe, zimenezo sizikutanthauza kuti Mulungu alibe nazo kanthu zoti timavala chiyani, kapena kuti ‘chilichonse nchololeka.’ Si choncho ayi, Baibulo lili ndi malangizo abwino amene amasonyeza mmene Mulungu amaganizira pankhani yakavalidwe ndi kapesedwe.
“Ndi Manyazi ndi Chidziletso”
Mtumwi Paulo analemba kuti akazi achikristu ayenera ‘kudziveka okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golidi kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali.’ Momwemonso, Petro analangiza kuti kudzikometsera kwa akazi “kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golidi.”—1 Timoteo 2:9; 1 Petro 3:3.
Kodi Petro ndi Paulo akusonyeza kuti akazi ndi amuna achikristu sayenera kusamala kaonekedwe kawo? Ayi ndithu! Kunena zoona, Baibulo limatchula amuna ndi akazi ena okhulupirika amene ankavala mphete ndi kudzola mavuta onunkhira. Estere asanapite kokaonana ndi Mfumu Ahaswero, anadzikometsera ndi mafuta amitundumitundu onunkhira. Ndipo Yosefe anavekedwa zovala zabafuta ndi unyolo wagolidi.—Genesis 41:42; Eksodo 32:2, 3; Estere 2:7, 12, 15.
Mawu akuti “wodziletsa,” amene Paulo anagwiritsira ntchito, amatithandiza kuumvetsetsa uphunguwo. Liwulo m’chigiriki limasonyeza kukhala wodekha ndi wodziletsa. Limatanthauza kusadziona wekha ngati wofunika kwambiri, kusafuna kudzionetsera. Mabaibulo ena amalitanthauzira liwu limeneli kuti “mochenjera,” “mwanzeru,” “wabwino,” kapena “wodziletsa.” Mkhalidwe umenewu ngwofunika kwambiri kwa akulu achikristu.—1 Timoteo 3:2.
Choncho, Malemba akamatiuza kuti tiyenera kuvala ndi kupesa mwaulemu, akutilimbikitsa kupeŵa masitayelo osakhala bwino amene angakhumudwitse ena ndi kutiwonongera mbiri yathu ndiponso yampingo wachikristu. M’malo mopambanitsa kusamala kaonekedwe kawo mwa kudzikometsera kunja, anthu oopa Mulungu ayenera kusonyeza kudekha maganizo ndi kumasamala makamaka “munthu wobisika wamtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa.” Petro anatero kuti mkhalidwe umenewo “ndiwo wamtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.”—1 Petro 3:4.
Akristu ali “choonetsedwa ku dziko lapansi.” Afunikira kusamala za mmene amaonekera kwa ena, makamaka poganizira kuti anapatsidwa lamulo lakulalikira uthenga wabwino. (1 Akorinto 4:9; Mateyu 24:14) Choncho, sangalole chilichonse, kuphatikizapo kaonekedwe kawo, kulepheretsa anthu kumvetsera uthenga wofunika umenewo.—2 Akorinto 4:2.
Ngakhale kuti masitayelo amasiyanasiyana kulikonse, Baibulo limapatsa anthu malangizo omveka, abwino, owathandiza kusankha mwanzeru. Malinga ngati anthu atsatira mapulinsipulo ameneŵa, Mulungu amalolera mwaufulu ndi mwachikondi kuti anthu onse azivala ndi kupesa monga mmene amakondera.
[Mawu a M’munsi]
a Anthu anayesapo kuchirikiza malamulo oletsa zinthu ameneŵa mwa kupotoza Malemba. Ngakhale kuti Baibulo silimanena zinthu ngati zimenezo, wazaumulungu wina wotchuka wotchedwa Tertullian ankaphunzitsa kuti popeza mkazi ndiye anachititsa “tchimo loyamba, ndi manyazi . . . a kutembereredwa kwa anthu,” akazi ayenera “kuyendayenda monga Hava, akumalira ndi kulapa.” Mpaka analimbikira kunena kuti mkazi wokongola mwachibadwa ayenera kumabisa kukongola kwakeko.—Yerekezerani ndi Aroma 5:12-14; 1 Timoteo 2:13, 14.