Chifukwa Chimene Timafunikira Chidziŵitso Cholongosoka
“Ndicho chifukwa chakenso ife, kuyambira pa tsiku limene tinamva za icho, sitinaleke kukupemphererani ndi kupempha kuti mukadzazidwe chidziŵitso cholongosoka cha chifuniro chake mu nzeru zonse ndi kuzindikira kwauzimu.”—AKOLOSE 1:9, “NW.”
1. Chitirani chitsanzo kusiyana pakati pa chidziŵitso chachisawawa ndi cholongosoka.
CHIFUPIFUPI aliyense amadziŵa koloko, koma kodi ndiangati amene amadziŵa mmene imagwirira ntchito? Inu mungakhale ndi lingaliro lachisawawa, koma kodi mungaimasule, kuikonza, ndikuikanso mbali zake zonse pamodzi? Wopanga koloko angaterodi. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti ali ndi chidziŵitso cholongosoka, chozindikira mmene koloko imagwirira ntchito. Ndipo chimenecho chimachitira chitsanzo kusiyana pakati pa chidziŵitso chachisawawa ndi cholongosoka.
2. Kodi ndi kusiyana kotani pakati pa mitundu iŵiri ya chidziŵitso kumene mwaona pa nkhani ya chipembedzo?
2 Mamiliyoni a anthu ali ndi lingaliro lachisawawa ponena za Mulungu. Iwo amanena kuti amakhulupirira Mulungu, ngakhale kuti zochita zawo kaŵirikaŵiri zimasiyana ndi kudzinenera kumeneko. M’mishonale wina nthaŵi zina ankafunsa mwininyumba kuti: “Monga m’Katolika, inu muyenera kukhulupirira Mulungu, kodi ndakhoza?” Ndipo yankho, ndi gesichala loloza kumwamba linkakhala lakuti: “Bwanawe, ndimakhulupirira kuti kuyenera kukhala chinachake kumeneko.” Kodi mungatche chimenecho kukhala chidziŵitso cholongosoka ndi chozindikira Mulungu? Kutalitali. Ndipo kaŵirikaŵiri chotulukapo cha kusatsimikizirika koteroko chiri chakuti mkhalidwe wa awo odzinenera kukhala Akristu suli Wachikristu. (Yerekezerani ndi Tito 1:16.) Mkhalidwe wotulukapo umakhala wonga umene Paulo anaulongosola kuti: “Monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m’chidziŵitso cholongosoka, Mulungu anawapereka iwo ku mkhalidwe wosavomerezeka wa maganizo.”—Aroma 1:28, NW.
3. Kodi nchiyani chimene chimatulukapo pamene anthu akana chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu?
3 Kodi kusoŵeka kwa chidziŵitso cholongosoka kumeneko kunatulukapo chiyani m’zaka za zana loyamba? Anthu anali kuchita “zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani; akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu awo, opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi chachibadwidwe, opanda chifundo.” Kusoŵa kwawo chidziŵitso cholongosoka kunatanthauza kuti mitima yawo sinasonkhezeredwe kuchita machitidwe olungama.—Aroma 1:28-31; Miyambo 2:2, 10.
Kodi Kusiyana Nkotani?
4, 5. Mogwirizana ndi akatswiri Achigriki, kodi ndikuti kumene kuli kusiyana pakati pa gnoʹsis ndi e·piʹgno·sis?
4 Kusiyana kumeneku pakati pa chidziŵitso chachisawawa ndi cholongosoka kwasonyezedwa m’Malemba Achigriki. Chigriki choyambirira chimanena za gnoʹsis, chidziŵitso, ndi e·piʹgno·sis, chidziŵitso cholongosoka. Choyambiriracho, mogwirizana ndi katswiri Wachigriki W. E. Vine, chimatanthauza “choyambirira kufunafuna kudziŵa, kufunsa, kufufuza,” makamaka kwa chowonadi chauzimu m’mawu ozungulira a Malemba.
5 Mogwirizana ndi katswiri Wachigriki Thayer, e·piʹgno·sis imatanthauza “chidziŵitso chotsimikizirika ndi cholondola.” Ndipo mumpangidwe wake wa mneni, limatanthauza “kukhala wozoloŵerana ndi chinachake mokwanira, kudziŵa; kudziŵa molongosoka, kudziŵa bwino.” W. E. Vine akunena kuti e·piʹgno·sis “imatanthauza chidziŵitso chenicheni kapena chokwana, kudziŵa, kuzindikira.” Iye akuwonjezera kuti iyo imalongosola “chidziŵitso chofikapo kapena chokwana, kugawanamo kokulira kwa wodziŵa m’chinthu chodziwidwa, mwakutero chikumamusonkhezera iye mwamphamvu.” (Kanyenye ngwathu.) Monga mmene tidzawonera, mawu otsirizira amenewo ali ofunika koposa kwa Mkristu.
6. Kodi ndi alembi a Baibulo ati amene amagwiritsira ntchito mawu akuti “chidziŵitso” ndi “chidziŵitso cholongosoka,” ndipo kodi nchifukwa ninji chidziŵitso cholongosoka chiri chofunika?
6 Alembi aŵiri okha a Baibulo ndi amene amagwiritsira ntchito liwu Lachigriki lakuti e·piʹgno·sis. Iwo ali Paulo ndi Petro, omwe amagwiritsira ntchito liwulo ku chiwonkhetso cha nthaŵi 20.a Pambali pa Luka, ndi okhawonso amene amagwiritsira ntchito liwu la gnoʹsis, Paulo akumaligwiritsira ntchito ilo nthaŵi 23 ndipo Petro nthaŵi 4. Chotero zolembera zawo ziri chitsogozo chamtengo ponena za kufunika kwa chidziŵitso cholongosoka m’chiyembekezo cha chipulumutso. Monga mmene Paulo ananenera kwa Timoteo kuti: “Pakuti ichi nchokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu; amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pa [chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi, NW].”—1 Timoteo 2:3, 4.
Chifukwa Chimene Chidziŵitso Cholongosoka Chiri Chofunika
7. (a) Kuti chikhale chaphindu, kodi ndimotani mmene chidziŵitso chiyenera kutiyambukira ife? (b) Kodi ndi ngozi yotani imene imakhalapo titanyalanyaza chidziŵitso?
7 Chotero, kupeza chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi monga momwe chaphunzitsidwira m’Baibulo kuli mfungulo yopulumukira. Komabe, chidziŵitso chimenecho chiyenera kufika pamtima, pokhala pa zisonkhezero. Icho sichingakhalemo monga kachitidwe ka luntha kapena maphunziro. Kuwonjezerapo, mwamsanga chitapezedwa, chidziŵitso cha chowonadi chimayenera kugwiritsiridwa ntchito ndi kukonzedwanso chatsopano. Kodi nchifukwa ninji ziri tero? Chifukwa chakuti chikumbukiro, mofanana ndi mnofu wosagwiritsiridwa ntchito, chingafooke ndi kusoŵa kanthu, zitatero tinganyalanyaze uzimu wathu mosavuta ndi kuyamba kupatuka ndi kudzandira m’chikhulupiriro chathu. Tingafooketse kugwiririra kwathu pa “chidziŵitso cha Mulungu.” Mofulumira, kudzandira kumeneku kungawonekere m’kufooka kwa luntha lathu la kuganiza ndipo ngakhale mkhalidwe wosakhala Wachikristu.—Miyambo 2:5; Ahebri 2:1.
8. Kodi ndi phindu lotani limene Solomo anawona m’nzeru ndi chidziŵitso?
8 Pamenepa, timayamikira chifukwa chimene Solomo, pamene anali wokhulupirika, anakuza nzeru, kuzindikira, ndi luntha la kuganiza. Iye analemba kuti: “Pakuti nzeru idzaloŵa m’mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziŵa, kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakuchinjiriza; kukupulumutsa ku njira yoipa.”b (Miyambo 2:10-12) Mawu ameneŵa amatanthauza kuti tiyenera kuyambitsa chikhumbo chofunitsitsa cha chidziŵitso cholongosoka, chimene chingayambukire mtima ndi moyo weniweniwo. Kuwonjezerapo, chiri maziko a mphamvu zabwino za kuganiza. Ndipo kodi nchifukwa ninji ichi chiri chofunika chotero lerolino?
9. Kodi ndani ena amene ali adani a uzimu Wachikristu?
9 Tikukhala ndi moyo “m’masiku otsiriza” pamene, monga mmene Paulo analosera, zafika “nthaŵi zotsendereza” kapena “nthaŵi zamavuto.” (2 Timoteo 3:1, Revised Standard Version; The New English Bible) Chikukhala chovuta koposapo kusungabe umphumphu wathu Wachikristu m’dziko lonyonyotsokali. Miyambo Yachikristu, mapindu, ndi miyezo ikusekedwa ndi kunyodoledwa. Chikhulupiriro cha Mboni za Yehova chikuwukiridwa ku mbali zonse—ndi atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu amene amada uthenga Waufumu umene timapita nawo kunyumba ndi nyumba, ndi ampatuko amene amagwirizana ndi atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu, ndi akatswiri a zamankhwala amene amafuna kukakamiza kutithira mwazi ndi ana athu, ndi asayansi osakhulupirira mwa Mulungu amene amakana kukhulupirira Mulungu ndi chilengedwe, ndi awo amene amayesera kutikakamiza kulakwira uchete wathu. Chitsutso chonse chimenechi chimaunjikidwa ndi Satana, wolamulira wa mdima ndi umbuli, mdani wa chidziŵitso cholongosoka.—2 Akorinto 4:3-6; Aefeso 4:17, 18; 6:11, 12.
10. Kodi ndi zididikizo zotani zimene zingabwere motsutsana nafe, ndipo kodi timafunikira chiyani kuti tizigonjetse?
10 Zitsenderezo zingachulukire m’moyo wa tsiku ndi tsiku kuti zisonkhezere Mkristu kuchita zimene ena akuchita, kaya kukhale kumwa mankhwala ogodomalitsa, kumwa mopambanitsa, kuchita chisembwere ndi chiwawa, kuba, kunama, kunyenga, kulova ku sukulu, kapena kungofunadi moyo wadyera wa zosangulutsa. Chimenecho ndicho chifukwa chake chidziŵitso cholongosoka chiri chofunika koposa. Chidziŵitso chokwana cha Mawu ndi chifuno cha Mulungu chingasonkhezere mwamphamvu kuganiza ndi kachitidwe kathu m’njira yabwinopo.—Aroma 12:1, 2.
Mwana Woloŵerera Wamakono
11, 12. Kodi ndi chokumana nacho cha moyo weniweni chotani chimene chimasonyeza kupusa kwa kukana chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi?
11 Tingafanizire ichi ndi nkhani yeniyeni ya moyo wa mwamuna wachichepere amene, pamene anali ndi chifupifupi zaka 14 zakubadwa ndipo ali kale Mkristu wobatizidwa, chikondi chake cha chowonadi chinayesedwa. Mofanana ndi achichepere ambiri, iye anakonda maseŵera, makamaka mpira. Koma panabuka vuto. Sukulu yake inaseŵera mpira usiku umodzimodziwo umene mpingo unali kuchita misonkhano yake. Uzimu wake sunali wolimba mokwanira kuti nkusiyanitsa molondola phindu lochepera la mpira litayerekezeredwa ku phindu losatha la kupezeka pa misonkhano Yachikristu ndi mayi wake wamasiye ndi mbale ndi mlongo wake aang’ono. Chotero iye analeka kuchita mogwirizana ndi chidziŵitso cholongosoka ndipo anasankhapo kusiya chowonadi. Pomalizira pake, anachotsedwa. Pambuyo pake, iye anapitiriza nazo ndi kuchita ntchito yausilikali, kumene iye anadziloŵetsa m’mankhwala ogodomalitsa.
12 Mu 1986, pamene mwamuna wachichepere ameneyu anachotsedwa mu usilikali, anadzagalamuka, ndipo analemba kalata kwa bwenzi la banja limene linatumikira pa komiti yachiweruzo imene inamuchotsa iye. Mu iyo iye ananena kuti: “Ndine wachimwemwe kukhala wokhoza kukusimbira nkhani zinazake zofunika: Ndabwereranso m’chowonadi. . . . Ndayamba kuzindikira chimene mtumwi Paulo ananena pa 2 Akorinto 4:4, kuti pali mulungu wa dongosolo lino la zinthu amene akuchititsa khungu maganizo. Kwa nthaŵi yaitali, ndakhala wakhungu mwauzimu ku zinthu zimene zinkandichitikira. Pamene ndinachoka m’chowonadi, sindinadziŵe ngozi imene ndinadziloŵetsamo. Koma ndi kupita kwa nthaŵi, ndipo ndiyamikadi Yehova Mulungu, ndakhala wokhoza kuvomereza momvekera kuti ndinali wolakwa m’njira ya kachitidwe kanga koipa.”—Yerekezerani ndi Luka 15:11-24.
13. Ngati alapa mowonadi, kodi nchiyani chimene chingakhale chotulukapo chotsimikizirika kwa ena amene agwa m’mbali mwa njira? (2 Timoteo 2:24-26)
13 Mwamuna wachichepere ameneyu wabwereranso panjira ya chidziŵitso cholongosoka. Tsopano ali wokhoza “kuyenda koyenera [Yehova] kukamukondweretsa monsemo.” Iye angathenso “kubala ziphatso mu ntchito yonse yabwino, [ndi kuwonjezeka m’chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu, NW]” pamene akulondola kusonkhana kwake ndi mpingo Wachikristu. Ndipo ndi dalitso lotsitsimula chotani nanga limene iye wakhala ku banja lake mwa kukhalanso wotsanza Kristu! Kodi mukudziŵa za zitsanzo zina zofanana ndi ichi?—Akolose 1:9, 10; Mateyu 11:28-30.
Zotulukapo Zoipa za Kunyalanyaza Uzimu
14. (a) Kuti tipeŵe kugwa, kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita? (b) Kodi nchiyani chimene chachitika kwa Akristu ena?
14 Kodi ndi phunziro lotani limene lingaphunziridwe kuchokera ku chochitikachi ndi zina zofanana nacho? Kuti titangopeza chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi, tiyenera kukonzanso chatsopano mokhazikika magwero auzimu a maganizo kotero kuti tisagwe. Chuma chathu chauzimu chingathe mphamvu ngati tinyalanyaza phunziro laumwini ndi labanja, misonkhano Yachikristu, ndi utumiki. Pamenepa kodi nchiyani chimene chingachitike? Yemwe panthaŵi ina anali Mkristu wolimba angapatuke pa chikhulupiriro, mwinamwake ngakhale kugwera m’mikhalidwe yoipa, yonga ngati chisembwere, kapena kugwera m’mbuna ya kukaikira ndi kusadziŵitsidwa bwino kotsogolera ku mpatuko. (Ahebri 2:1; 3:12; 6:11, 12) Mopusa, ena abwereradi ku chiphunzitso Chachibabulo cha Utatu ndi kusafa kwa moyo!
15. Kodi ndi chenjezo lotani limene Petro anapereka ponena za kugwa?
15 Mawu a Petro alidi oyenerera: “Pakuti ngati, adatha kuthawa zodetsa za dziko lapansi mwa chizindikiritso cha Ambuye ndi Mpulumutsi Yesu Kristu, akodwanso nazo, nagonjetsedwa, zotsiriza zawo zidzaipa koposa zoyambazo. Pakuti pakadakhala bwino kwa iwo akadakhala osazindikira njira ya chilungamo, ndi poizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo. Chidawayenera iwo cha nthanthi yowona, Galu wabwerera ku masanzi ake, ndi nkhumba idasambayi yabwerera kukunkhulira m’thope.”—2 Petro 2:20-22.
16. (a) Kodi ndimotani mmene ena asokeretsedwera m’nthaŵi za posachedwapa? (b) Kodi osokeretsedwawo agwera m’machitidwe otani a makhalidwe?
16 Amene amakana chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi kaŵirikaŵiri amasankha njira yolakwika. Iwo samalandiranso thayo la kupezeka mokhazikika pa misonkhano Yachikristu kapena kutengamo mbali mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba. Ena amabwereradi ku kusuta! Ena amakhala osangalala kuti sadzafunikiranso kuwoneka osiyana pa nkhani ya uchete Wachikristu ndi kugwiritsira molakwa mwazi. Ha, ndi ufulu wotani nanga! Tsopano iwo angavoteredi chimodzi cha zipani za ndale zadziko za “chirombo.” (Chibvumbulutso 13:1, 7) Chotero, monga miyoyo yosachilimika, ena anyengedwa ndi kupatutsidwa pa njira yolungama ya chidziŵitso cholongosoka ndi aja amene, pamene kuli kwakuti ‘amawalonjeza ufulu, nawonso ndi akapolo ku chivundi.’—2 Petro 2:15-19.
17. Kodi ndi ngozi yotani imene iripo kwa awo amene amagwa pa chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi?
17 Pokhapo ngati otereŵa alapa ndi kubwerera ku chowonadi, amadzivumbula iwo eni ku chiweruzo chimene Paulo anandandalitsa: “Pakuti tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziŵitso cha chowonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo, koma kulindira kwina koopsya kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuononga otsutsana nawo.” Ndi kopanda nzeru ndi kosawona patali chotani nanga mmene kuliri kusiya chidziŵitso cholongosoka cha Yehova Mulungu ndi Kristu Yesu mmalo moyanja ziphunzitso zampatuko za Dziko Lachikristu!—Ahebri 6:4-6; 10:26, 27.
Changu Ndi Chidziŵitso Cholongosoka
18. Mogwirizana ndi Paulo, kodi nchifukwa ninji atsogoleri achipembedzo Achiyuda analephera kulandira Kristu?
18 Atsogoleri achipembedzo Achiyuda a m’tsiku la Paulo analidi ndi chidziŵitso cha Malemba Achihebri. Koma kodi icho chinali chidziŵitso cholongosoka? Kodi chinawayandikitsa kwa Kristu monga Mesiya wolonjezedwa? Paulo akutsutsa kuti iwo anali otanganitsidwa koposa kukhazikitsa chilungamo chawochawo kupyolera m’Chilamulo kotero kuti sanakhoze kudzigonjetsera iwo eni kwa “Kristu [amene ali] chimaliziro cha lamulo.” Chotero Paulo akanena za iwo kuti: “Pakuti ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma simonga mwa [chidziŵitso cholongosoka, NW].”—Aroma 10:1-4.
19, 20. (a) Kodi ndimotani mmene tingapezere chidziŵitso cholongosoka? (b) Kodi ndi mafunso otani amene atsala oti ayankhidwe?
19 Chotero kodi tingachipeze motani chidziŵitso cholongosoka chimenechi? Mwa phunziro laumwini ndi kusinkhasinkha, limodzi ndi pemphero ndi kupezeka pa misonkhano. Ichi chimatanthauza kupatsanso mphamvu kokhazikika kwa mabatiri athu auzimu, kunena kwake titero. Sitingathe kudalira kokha pa chidziŵitso chimene tinapeza poyambapo pamene tinalandira chowonadi. Tidzafunikira kudya chakudya cholimba chauzimu mopitirizabe, kupeza chidziŵitso cholongosoka, kupyolera m’phunziro laumwini losamalitsa. Chotero uphungu wa Paulo ngoyenerera: “Chakudya chotafuna chiri cha anthu akulu misinkhu, amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Mwa ichi, polekana nawo mawu a chiyambidwe cha Kristu, tipitirire kutsata ukulu msinkhu; osaikanso maziko a kutembenuka mtima kusiyana nazo ntchito zakufa, ndi a chikhulupiriro cha pa Mulungu . . . Ndipo ichi tidzachita, akatilola Mulungu.”—Ahebri 5:14–6:3.
20 Mafunso tsopano ndi akuti, Kodi ndi zipangizo zotani zimene tiri nazo zotithandiza kupeza chidziŵitso cholongosoka? Ndipo polingalira miyoyo yathu yotanganitsidwa, kodi ndi liti pamene tingaphunzire Mawu a Mulungu? Nkhani yotsatira idzalingalira nsongazi ndi zina zogwirizana nazo.
[Mawu a M’munsi]
a Monga momwe landandalitsidwira mu Comprehensive Concordance of the New World Translation of the Holy Scriptures, tsamba 17; ndiponso Filemoni 6 (Onani The Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures.).
b Kuti mupeze kumvetsetsa kwabwino kwa magwero a tanthauzo la mawu akuti “chidziŵitso,” “luntha la kuganiza,” “nzeru,” ndi ena opezeka m’Miyambo, onani Insight on the Scriptures, Volyumu 2, masamba 180, 1094, 1189, yofalitsidwa m’Chingelezi ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Mafunso Ofunika Kuyankha
◻ Kodi nkuti kumene kuli kusiyana pakati pa “chidziŵitso” ndi “chidziŵitso cholongosoka”?
◻ Kodi nchifukwa ninji chidziŵitso cholongosoka chiri chofunika chotero m’masiku ano otsiriza?
◻ Kodi ndimotani mmene ena angayesedwere ndi kugwa pa chowonadi?
◻ Kodi ndi chenjezo lotani limene Petro akutipatsa ponena za kukana chidziŵitso cholongosoka?
◻ Kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita kuti tipeze ndi kusungabe chidziŵitso cholongosoka?