-
Tizikhala Osiyana ndi Anthu a M’dzikoliNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2018 | January
-
-
3. Kodi ndi ndani amasonyeza makhalidwe otchulidwa pa 2 Timoteyo 3:2-5?
3 Mtumwi Paulo analemba kuti ‘masiku otsiriza adzakhala nthawi yovuta’ ndipo anatchula makhalidwe oipa okwana 19 amene anthu adzakhala nawo pa nthawiyo. Makhalidwe amene anatchulawo ndi ofanana ndi amene anatchulidwa pa Aroma 1:29-31. Koma pa 2 Timoteyo 3:2-5 Paulo anagwiritsa ntchito mawu amene sanatchulidwenso pena paliponse m’Malemba Achigiriki. Iye asanatchule makhalidwe oipawa, anayamba ndi mawu akuti “anthu adzakhala . . . “ Ponena kuti “anthu,” Paulo ankasonyeza kuti anthu ambiri, kaya amuna kapena akazi, adzasonyeza makhalidwe oipa. Koma sikuti munthu aliyense amakhala ndi makhalidwe oipawa. Tikutero chifukwa chakuti Akhristu amayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino.—Werengani Malaki 3:18.
-
-
Tizikhala Osiyana ndi Anthu a M’dzikoliNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2018 | January
-
-
4. Kodi mungafotokoze bwanji anthu odzitukumula ndiponso onyada?
4 Paulo atanena kuti anthu ambiri adzakhala odzikonda komanso okonda ndalama, analembanso kuti anthu adzakhala odzimva, odzikweza, odzitukumula ndiponso onyada. Munthu amasonyeza makhalidwe amenewa chifukwa choganiza kuti ndi wapamwamba kuposa ena potengera luso lake, maonekedwe ake, chuma chake kapena udindo wake. Anthu amakhalidwe amenewa amalakalaka kuti ena aziwatama kapena kuwasirira. Katswiri wina analemba kuti munthu wonyada kwambiri amadziona kuti ndi wapadera moti tingati amadzilambira yekha. Anthu ena amanena kuti khalidwe lonyada ndi lonyansa kwambiri moti ngakhale anthu onyadawo amanyansidwa ndi anthu ena amene ali ndi khalidweli.
-
-
Tizikhala Osiyana ndi Anthu a M’dzikoliNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2018 | January
-
-
8. (a) Kodi masiku ano anthu ena amaona bwanji nkhani yosamvera makolo? (b) Kodi Malemba amalangiza ana kuti azichita chiyani?
8 Paulo anafotokozanso mmene anthu a m’masiku otsiriza azidzachitira zinthu ndi anthu ena. Iye analemba kuti ana adzakhala osamvera makolo. N’zoona kuti anthu ambiri amaona kuti zimenezi si vuto ndipo mabuku, mafilimu ndiponso mapulogalamu a pa TV amalimbikitsa ana kukhala osamvera. Koma khalidweli ndi limene limasokoneza mabanja ambiri. Anthu akhala akudziwa mfundo imeneyi kuyambira kalekale. Mwachitsanzo, kale ku Greece munthu akamenya makolo ake ankamulanda ufulu wake. Komanso ku Rome, munthu akamenya bambo ake ankalangidwa mofanana ndi amene wapha munthu. Malemba Achiheberi komanso Malemba Achigiriki amalangizanso ana kuti azilemekeza makolo awo.—Eks. 20:12; Aef. 6:1-3.
-
-
Tizikhala Osiyana ndi Anthu a M’dzikoliNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2018 | January
-
-
10, 11. (a) Kodi ndi makhalidwe oipa ati amene anthu osakonda anzawo amasonyeza? (b) Kodi Akhristu oona amasonyeza chikondi kwa ndani?
10 Paulo anatchula makhalidwe ena oipa amene anthu amasonyeza chifukwa chosakonda anzawo. Iye atatchula anthu “osamvera makolo” anatchula anthu osayamika, ndipo m’pomveka chifukwa anthu otere sayamikira zinthu zabwino zimene ena awachitira. Ananena kuti anthu adzakhala osakhulupirika komanso osafuna kugwirizana ndi anzawo. Ananenanso kuti anthu adzakhala achiwembu komanso onyoza, omwe amanena zinthu zonyoza anzawo ngakhalenso Mulungu. Anatinso anthu adzakhala onenera anzawo zoipa, kapena kuti anthu amene amafalitsa miseche n’cholinga choti awononge mbiri ya anthu ena.a
-