Aumphaŵi Komabe Olemera Zingatheke Bwanji?
Zaka mazana ambiri zapitazo munthu wina wanzeru anapemphera kuti asakhale waumphaŵi. Nchifukwa ninji anapempha motero? Chifukwa chakuti anaopa kuti umphaŵi ungayambitse makhalidwe ndi ntchito zimene zingasokoneze unansi wake ndi Mulungu. Umboni wake ukupezeka m’mawu ake akuti: “Mundidyetse zakudya zondiyenera . . . kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.”—MIYAMBO 30:8, 9.
KODI zimenezi zikutanthauza kuti nkosatheka kwa munthu waumphaŵi kutumikira Mulungu mokhulupirika? Kutalitali! Kuyambira kalekale, atumiki a Yehova Mulungu osaŵerengeka akhulupirikabe kwa iye mosasamala kanthu za kuvutika chifukwa cha umphaŵi. Choncho, nayenso Yehova amakonda amene amamkhulupirira ndipo amawathandiza.
Okhulupirika Akale
Mtumwi Paulo iye mwini anayang’anizana ndi nthaŵi zosoŵa. (2 Akorinto 6:3, 4) Iye anafotokozanso za “mtambo waukulu” wa mboni zakale Chikristu chisanadze, ena a iwo “ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa zambuzi, nakhala osoŵa . . . osokerera m’[zi]pululu, ndi m’mapiri, ndi m’mapanga, ndi m’mauna a dziko.”—Ahebri 11:37, 38; 12:1.
Mmodzi wa okhulupirikawa anali mneneri Eliya. Mkati mwa chirala cha zaka zitatu ndi theka, Yehova anampatsa chakudya mosalekeza. Poyamba, Mulungu anatuma makungubwi kukapereka mkate ndi nyama kwa mneneriyo. (1 Mafumu 17:2-6) Pambuyo pake, Yehova mozizwitsa anaŵirikizanso ufa ndi mafuta zimene mkazi wamasiye anapatsa Eliya. Sichinali chakudya chapamwamba ayi, koma chinasungabe moyo wa mneneriyo, mkaziyo, ndi mwana wake.
Mofananamo, Yehova anadyetsa mneneri wokhulupirika Yeremiya pamene anali pamavuto azachuma. Yeremiya anapulumuka pamene Ababulo anazinga Yerusalemu, pamene anthu ‘anadya chakudyacho monga mwa muyeso, ndi mosamalira.’ (Ezekieli 4:16) Mkupita kwa nthaŵi, njala inakula kwambiri mumzindamo kotero kuti azimayi ena anadya ana awo. (Maliro 2:20) Ngakhale kuti Yeremiya anali m’bwalo la kaidi, Yehova anapitirizabe kumpatsa ‘mkate woumba’ tsiku ndi tsiku “mpaka unatha mkate wonse wa m’mudzi.”—Yeremiya 37:21.
Choncho, Yeremiya, mofanana ndi Eliya, anali ndi chakudya chochepa. Malemba satiuza za chimene Yeremiya ankadya kapena kuti ankadya kangati pamene mkate unatha m’Yerusalemu. Komabe, tikudziŵa kuti Yehova anamdyetsa ndipo iye anapulumuka m’nthaŵi imeneyo ya njala yadzaoneni.
Lerolino, umphaŵi umapezeka kulikonse padziko lapansi. Malinga ndi kunena kwa United Nations, umphaŵi wadzaoneni uli ku Afirika. Mu 1996, nkhani yofalitsidwa ndi UN inanena kuti: “Theka la anthu a ku Afirika ngaumphaŵi.” Ngakhale kuti pali mavuto aakulu chotere azachuma, anthu omachulukirachulukirabe a ku Afirika akugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Baibulo m’moyo wawo ndipo akutumikira Mulungu mokhulupirika, nchidaliro chakuti adzawachirikiza. Talingalirani za zitsanzo zina za mbali ina ya dziko lathuli laumphaŵi.
Kukhalabe Woona Mtima
Michael,a amene amakhala ku Nigeria, ndi mlimi amene amalera ana asanu ndi mmodzi. “Nkovuta kukhala woona mtima pamene ulibe ndalama zothandizira banja lako,” iye akutero. “Komabe, pamene lingaliro la kuba lindifikira, ndimakumbukira Aefeso 4:28, amene amati: ‘Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake.’ Choncho, pamene ndiyang’anizana ndi chiyeso, ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi ndalamazi ndazigwirira ntchito?’”
“Mwachitsanzo,” akuwonjezera motero Michael, “pamene ndinali kuyenda tsiku lina, ndinaona chikwama chitagwa kuchokera panjinga yamoto. Ndinalephera kuimitsa woyendetsa njingayo, ndiye ndinangonyamula chikwamacho ndipo ndinapeza kuti chinali chodzaza ndi ndalama! Pogwiritsira ntchito khadi ya munthuyo imene inali m’chikwamamo, ndinapeza mwini wake ndipo ndinabwezera chikwamacho kwa iye.”
Kuthetsa Kupsinjika Maganizo
Munthu wina ku North Africa anati: “Umphaŵi uli [ngati] kugwera m’dzenje lozama, mmene ungaone kuwala ndiponso anthu akudutsa, koma sungathe kufuula kuti upeze chithandizo kapena makwerero oti utulukiremo.” Ndicho chifukwa chake umphaŵi nthaŵi zambiri umadzetsa kupsinjika maganizo ndi kukhumudwa! Ngakhale atumiki a Mulungu angaone chuma cha ena nkumaganiza kuti kukhulupirika nkosapindulitsa. (Yerekezerani ndi Salmo 73:2-13.) Kodi malingaliro otero angathetsedwe motani?
Peter, wa ku West Africa, anapuma pantchito ya boma atagwira ntchitoyo kwa zaka 19. Tsopano iye kwakukulukulu amadalira ndalama zochepa za penshoni. “Pamene ndiyang’anizana ndi zokhumudwitsa,” akutero Peter, “ndimakumbukira zimene ndinaŵerenga m’Baibulo ndi zofalitsa za Watch Tower Society. Dongosolo lakaleli lili pafupi kutha, ndipo tikuyembekezera dongosolo labwino.
“Ndiponso ndimaganizira za 1 Petro 5:9, amene amati: ‘Ameneyo [Satana] mumkanize okhazikika m’chikhulupiriro, podziŵa kuti zoŵaŵa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m’dziko.’ Choncho, sindikuvutika ndekha. Malangizo amenewa amathandiza kuthetsa malingaliro okhumudwitsa ndi opangitsa kupsinjika maganizo.”
“Komanso,” akuwonjezera motero Peter, “Yesu anachita zozizwitsa zambiri pamene anali padziko lapansi, koma sanalemeretse mwakuthupi ngakhale ndi mmodzi yemwe. Nanga ndingayembekezerenji kuti iye andilemeretse?”
Mphamvu ya Pemphero
Kuyandikira kwa Yehova Mulungu m’pemphero ndi njira ina yothetsera kupsinjika maganizo. Pamene Mary anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova mu 1960, am’banja lake anamtayirira. Pokhala wosakwatiwa ndiponso m’zaka zake za m’ma 50, iye ngwofooka ndipo ali ndi zochepa zakuthupi. Komabe, ngwachangu mu utumiki wachikristu.
Mary akuti: “Nditakhumudwa, ndimapemphera kwa Yehova. Ndimadziŵa kuti palibenso wina amene angandithandize koposa Iye. Ndaphunzira kuti pamene ukhulupirira Yehova, Iye amakuthandiza. Nthaŵi zonse ndimakumbukira mawu awa a Mfumu Davide, opezeka pa Salmo 37:25 akuti: ‘Ndinali mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.’
“Ndimapezanso chilimbikitso pa zokumana nazo za abale ndi alongo achikristu okalamba zofotokozedwa mu Nsanja ya Olonda. Yehova Mulungu anawathandiza, choncho ndimadziŵa kuti adzapitirizanso kundithandiza. Amandidalitsa pa ntchito yanga yogulitsa fufu [chakudya chokonzedwa ndi ufa wachinangwa], ndipo ndimatha kupeza zosoŵa zanga za tsiku ndi tsiku. Nthaŵi zina ndikakhala wopanda ndi ndalama yomwe ndipo ndikusoŵa chochita, Yehova amatumiza munthu wina kudzandipatsa mphatso ndipo amati, ‘Mlongo, chonde kwayani izi.’ Yehova sanandikhumudwitsepo.”
Kupindula ndi Phunziro la Baibulo
Mboni za Yehova zimapindula ndi phunziro la Mawu a Mulungu, Baibulo, ndipo aumphaŵi pakati pawo amateronso. John wazaka 60 amatumikira monga mpainiya (wolalika Ufumu wanthaŵi zonse) ndiponso ndi mtumiki wotumikira mumpingo. Iye amakhala m’nyumba yosanjika kamodzi yosamangidwa bwino ndi yosalimba mmene mumakhala mabanja 13. Chipinda chake ndi m’likhole lapansi momwemo, anangotchingako ndi matabwa. Mkati mwake muli mipando iŵiri yakale ndi thebulo lodzaza ndi zothandizira kuphunzira Baibulo. Iye amagona pamkeka.
John ankapeza pafupifupi dollar imodzi patsiku pamene ankagulitsa mkate, koma pamene analetsa tirigu wochokera m’maiko akunja, ntchito yakeyo inatha. Iye akunena kuti: “Nthaŵi zina zinthu zimandivuta kwambiri, koma ndimapitirizabe kuchita upainiya. Yehova ndiye amandichirikiza. Ndimagwira ntchito iliyonse imene ndingapeze ndipo sindidalira munthu kuti andithandize kapena kuti andipatse chakudya, komabe abale a mumpingo amandithandiza kwambiri. Amandithandiza kufunafuna ntchito ndipo nthaŵi zina amandipatsa ndalama.
“Ndimapatula nthaŵi yoŵerenga Baibulo ndi zofalitsa za Watch Tower Society. Ndimaŵerenga m’mamaŵa pamene m’nyumbamo mulibe phokoso ndipo ndimaŵerenganso madzulo titakhala ndi magetsi. Ndimadziŵa kuti ndiyenera kupitirizabe ndi phunziro langa laumwini.”
Kuphunzitsa Ana Kuti Adzapeze Moyo
Daniel ndi mwamuna wofedwa mkazi amene ali ndi ana asanu ndi mmodzi. Mu 1985 iye anachotsedwa ntchito imene anaigwira kwa zaka 25, koma anapezanso ntchito yogulitsa m’sitolo. “Tili pamavuto azachuma m’banja muno,” iye akutero. “Tsopano timadya kamodzi kokha patsiku. Nthaŵi ina tinagona ndi njala kwa masiku atatu. Tinkangogonera madzi basi.”
Daniel ndi mkulu mumpingo. “Sindilephera kufika pamisonkhano yachikristu, ndipo ndine wokangalika m’ntchito yateokrase,” iye akutero. “Patakhala ntchito inayake pa Nyumba ya Ufumu, ndimayesetsa kuti ndipezekepo. Ndipo zinthu zitandivuta, ndimakumbukira mawu a Petro kwa Yesu, olembedwa pa Yohane 6:68 akuti: ‘Ambuye, tidzamuka kwa yani?’ Ngati ndisiya kutumikira Yehova, ndidzamuka kwa yani? Mawu a Paulo opezeka pa Aroma 8:35-39 amandilimbitsanso mtima chifukwa chakuti amati palibe chimene chingakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu ndi Kristu. Awa ndiwo maganizo omwe ndimaphunzitsa ana anga mobwerezabwereza. Ndimawauza mobwerezabwereza kuti sitiyenera konse kusiya Yehova.” Changu cha Daniel, pamodzi ndi phunziro la Baibulo lapabanja la nthaŵi zonse, zapindulitsa kwambiri ana ake.
Mzimu Wopatsa
Wina angaganize kuti anthu amene ali paumphaŵi wadzaoneni sangathe kupereka zopereka zopititsira patsogolo ntchito ya Ufumu. Koma sizili choncho. (Yerekezerani ndi Luka 21:1-4.) Mboni zina ku Ghana zimene ntchito yawo ndi ulimi zimadulako minda yawo kuti mbali inayo azibzalako mbewu zopititsira patsogolo ntchito ya Ufumu wa Mulungu. Atagulitsa zokolola za chigawo cha munda wawocho, ndalama zake zonse amazigwiritsira ntchito imeneyo, imene imaphatikizapo kupereka zopereka pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova yakwawoko.
Joan, amene amakhala ku Central Africa, ndi mpainiya. Pofuna kusamalira mwamuna wake wopuwala ndi anthu ena anayi, iye amagulitsa mkate. Pamene mpingo wawo unafuna mabenchi oika m’Nyumba ya Ufumu, banja la Joan linaganiza zopereka ndalama zonse zimene anali nazo. Zimenezi zinapangitsa kuti akhale opanda ndalama. Ndiyeno, tsiku lotsatira, mosayembekezera konse winawake anadzabweza ngongole imene anatenga kalekale, kuwapatsa ndalama zimene sankayembekezera kuti adzazilandira nkomwe!
Joan ngosangalala ndipo sadera nkhaŵa za ndalama mosayenerera. “Ndimafotokozera Yehova m’pemphero mmene zinthu zilili, kenaka ndimapita mu utumiki wakumunda. Timadziŵa kuti palibe chiyembekezo chodalirika chakuti zinthu zingakhale bwino m’dongosolo lino la zinthu. Komabe, timadziŵa kuti Yehova adzatipatsa zosoŵa zathu.”
Kuchita Khama
Mboni za Yehova zimadziŵika chifukwa cha kukondana kwawo. (Yohane 13:35) Amene ali ndi ndalama amathandiza Akristu anzawo osoŵa. Kaŵirikaŵiri imakhala mphatso ndipo nthaŵi zina kupezerana ntchito.
Mark, amene amakhala ku Congo, ngwakhate. Linapundula zala zake zakumapazi ndi zakumanja. Choncho, iye amayenda ndi ndodo. Pamene Mark anaganiza zotumikira Yehova, anayamba kusintha makhalidwe. M’malo mopemphapempha chakudya monga momwe ankachitira kale, anayamba kulima chakechake. Anaumbanso njerwa zosatentha, zomwe ankagulitsa.
Ngakhale kuti ngwolemala, Mark anayamba kugwira ntchito mwakhama. Potsirizira pake anagula malo ndi kumangapo nyumba yabwino ndithu. Tsopano, Mark akutumikira monga mkulu mumpingo ndipo akulandira ulemu m’tauni yonseyo. Tsopano amathandiza anthu ena osoŵa.
Nzoona kuti m’madera ambiri ntchito nzosoŵa. Mkulu wina wachikristu amene amatumikira pa imodzi ya maofesi a nthambi za Watch Tower Society ku Central Africa analemba kuti: “Abale ambiri kuno ali paulova. Ena amayesa kuyamba ntchito yodzigwirira, koma izi nzovuta. Ena poona kuti adzavutikabe mulimonse mmene angachitire, aganiza zongoiŵala za chuma chakuthupi ndi kuyamba utumiki waupainiya. Pamene achita zimenezo, ambiri amapeza chithandizo chokulirapo kusiyana ndi ntchito yamalipiro ochepa kapena kusalipidwa.”
Yehova Amasamalira Anthu Ake
Yesu Kristu ponena za iye mwini anati: “Nkhandwe zili nazo nkhwimba, ndi mbalame zakumwamba zisa, koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu.” (Luka 9:58) Mofananamo, mtumwi Paulo analemba kuti: “Kufikira nthaŵi yomwe ino timva njala, timva ludzu, tili amaliseche, tikhomedwa, tilibe pokhazikika.”—1 Akorinto 4:11.
Onse aŵiri Yesu ndi Paulo anasankha kukhala ndi moyo wachikatikati pazachuma kuti akwaniritse bwino lomwe utumiki wawo. Akristu ambiri lerolino ngaumphaŵi chifukwa chakuti zoyesayesa zawo zinalephera. Komabe, iwo amatsatira mapulinsipulo a Baibulo m’moyo wawo ndipo amafunafuna kutumikira Mulungu mwachangu. Iwo amadziŵa kuti Yehova amawakonda kwambiri pamene alabadira chilimbikitso choona cha Yesu chakuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo [zinthu zakuthupi] zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:25-33) Ndiponso, atumiki a Mulungu aumphaŵiwa ali ndi umboni wakuti “madalitso a Yehova alemeretsa.”—Miyambo 10:22.
[Mawu a M’munsi]
a Maina a m’nkhaniyi asinthidwa.
[Bokosi patsamba 6]
Kodi “Akuchita Mawu” Ndani?
MALINGA ndi voti ya Gallup mu 1994, 96 peresenti ya Aamereka “amakhulupirira Mulungu kapena mzimu waponseponse.” Kulinso “matchalitchi ambiri ku United States malinga ndi chiŵerengero chake cha anthu kuposa dziko lina lililonse Padziko Lapansi,” inatero magazini ya U.S.News & World Report. Ngakhale kuti pali maonekedwe otero achipembedzo, woŵerenga mavoti amene wagwira ntchitoyi kwa nthaŵi yaitali George Gallup, Jr., akuti: “Zenizeni nzakuti, Aamereka ambiri sadziŵa chimene amakhulupirira kapena chifukwa chake.”
Kufufuza kosamalitsa kwavumbulanso kuti anthu ambiri amachita zosemphana ndi zikhulupiriro zawo zachipembedzo. Mwachitsanzo, “odziŵa za chikhalidwe cha anthu anena kuti m’madera ena amene muli upandu kwambiri m’dzikoli ndi malo amenenso anthu ake ambiri amakhulupirira kwambiri chipembedzo ndiponso amapembedza kwambiri,” akutero wolemba Jeffery Sheler.
Zimenezi nzosadabwitsa. Chifukwa ninji? Popeza kuti kalekale m’zaka za zana loyamba, mtumwi Paulo anachenjeza Akristu anzake kuti achenjere ndi amene “avomereza kuti adziŵa Mulungu, koma [amene] ndi ntchito zawo amkana Iye.” (Tito 1:16) Ndiponso, Paulo anauza mnyamatayo Timoteo kuti “masiku otsiriza” adzadziŵika ndi anthu “akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana.”—2 Timoteo 3:1, 5.
Komabe, Akristu oona amayesetsa kutsatira lamulo la Yesu Kristu lakuti “mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse.” (Mateyu 28:19) Mwakutero iwo ‘amakhala akuchita mawu, osati akumva okha.’—Yakobo 1:22.
[Chithunzi patsamba 7]
Phunziro la Baibulo limapindulitsa anthu ambiri padziko lonse