Baibulo ndi Buku Lapadera
Anthu pachifukwa chabwino alitcha buku logulidwa koposa padziko lonse lapansi. Ambiri amaŵerenga Baibulo ndipo amalikonda kuposa buku lina lililonse. Pakali pano, lafalitsidwa (lathunthu kapena chigawo chake) makope ngati mamiliyoni zikwi zinayi m’zinenero zoposa 2,000.
Komabe, kudzinenera kwake kwa Baibulo kuti linachokera kwa Mulungu kumachititsa chidwi kwambiri kuposa chiŵerengero cha makope ake ofalitsidwa. “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu,” analemba tero Paulo, mtumwi wachikristu. (2 Timoteo 3:16) Kodi zimenezi zikutanthauzanji? Mawuwo “adaliuzira Mulungu” (Chigiriki, the·oʹpneu·stos) tanthauzo lake lenileni ndilo “opumidwa ndi Mulungu.” Liwu lina lachigiriki logwirizana nalo ndilo pneuʹma, kutanthauza “mzimu.” Choncho, zimatanthauza kuti mzimu woyera wa Mulungu unasonkhezera anthu olilemba, kuwapumira mophiphiritsa, kotero kuti buku lomwe linakhalapo linatchedwadi Mawu a Mulungu, osati a munthu ayi. Inde, ambiri omwe aŵerenga Baibulo amadabwa nako kugwirizana kwake, kunena kwake zoona pa zasayansi, kuona mtima kwa alembi ake ndi kusabisa kanthu kwawo, ndipo makamaka maulosi ake okwaniritsidwa—zimene zachititsa aŵerengi anzeru mamiliyoni ambiri kukhulupirira kuti buku limeneli linachokera kwa wina wake wamkulu kuposa anthu.a
Koma kodi Mulungu anasamala kwambiri motani potsogoza kulembedwa kwa Baibulo? Ena amati liwu lililonse m’Baibulo analilankhula ndiye. Ena amati iye anangouzira malingaliro opezeka m’Baibulo, osati mawu ake ayi. Komatu kuuzira sikungakhale kwanjira imodzi, pakuti Mulungu ‘analankhula ndi makolo mwa aneneri m’manenedwe ambiri.’ (Ahebri 1:1; yerekezerani ndi 1 Akorinto 12:6.) M’nkhani yotsatira, tidzapenda njira zimene Mulungu analankhulira kwa alembi aumunthu okwanira ngati 40 omwe analemba Baibulo.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati mufuna kudziŵa zambiri, onani masamba 53-4, ndi 98-161 m’buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.