‘Unditengerekonso Mipukutu, Makamaka Yazikopa Ija’
MTUMWI PAULO ananena mawu ali pamwambawa popempha mmishonale mnzake Timoteyo kuti amubweretsere mipukutu. Kodi Paulo ankanena za mipukutu ya mtundu wanji? N’chiyani chinamuchititsa kupempha zimenezi? Nanga tikuphunzira chiyani pa zimene Paulo anapemphazi?
Pofika zaka za m’ma 60 C.E. pamene Paulo analemba mawu amenewa, mabuku 39 a Malemba Achiheberi anali atawagawa m’mabuku okwanira 22 kapena 24. Pafupifupi buku lililonse liyenera kuti linali mpukutu pawokha. Pulofesa wina dzina lake Alan Millard ananena kuti ngakhale kuti mipukutu imeneyi inkakhala yodula, “munthu wopeza bwino ndithu sankavutika kuipeza.” Anthu ena ankatha kupeza mwina mpukutu umodzi. Mwachitsanzo, nduna ya ku Itiyopiya inali ndi mpukutu m’galeta lake ndipo inali “kuwerenga mokweza m’buku la mneneri Yesaya.” Iye anali “munthu waulamuliro pansi pa Kandake, mfumukazi ya Itiyopiya. Iye anali woyang’anira chuma chonse cha mfumukaziyo.” Choncho ayenera kuti anali ndi ndalama zokwanira moti anakwanitsa kupeza mipukutu ina ya Malemba.—Mac. 8:27, 28.
Popempha Timoteyo, Paulo analemba kuti: “Unditengerekonso chovala champhepo chimene ndinachisiya ku Torowa kwa Karipo ndi mipukutu, makamaka yazikopa ija.” (2 Tim. 4:13) Mawu amenewa akusonyeza kuti Paulo ayenera kuti anali ndi mabuku ambiri. N’zosachita kufunsa kuti pa mabuku amene iye ankasungira, Mawu a Mulungu ndi amene ankawaona kuti ndi amtengo wapatali. Ponena za mawu akuti ‘mipukutu yazikopa’ pa vesili, katswiri wamaphunziro a Baibulo dzina lake A. T. Robertson anati: “Mipukutu ya mtundu umenewu iyenera kuti inali makope a mabuku a Chipangano Chakale. Tikutero popeza kuti chikopa n’chodula [komanso sichitha msanga] kuposa mapepala agumbwa.” Kuyambira ali wamng’ono, Paulo ‘anaphunzitsidwa ndi Gamaliyeli,’ yemwe anali mphunzitsi wa Chilamulo cha Mose wolemekezedwa ndi anthu onse. Choncho Paulo ayenera kuti anapeza mipukutu yakeyake ya Mawu a Mulungu.—Mac. 5:34; 22:3.
Mmene Akhristu Ankagwiritsira Ntchito Mipukutu
Komatu anthu amene ankatha kupeza mipukutu ya Malemba Opatulika anali ochepa. Ngati ndi choncho, kodi Akhristu ambiri ankapeza bwanji mpata wowerenga kapena kumvetsera Mawu a Mulungu? Kalata yoyamba imene Paulo analembera Timoteyo itithandiza kupeza yankho. Iye analemba kuti: “Pamene ukundiyembekezera, pitiriza kukhala wodzipereka powerenga pamaso pa anthu.” (1 Tim. 4:13) Kuyambira nthawi ya Mose, anthu a Mulungu ankawerenga mokweza pa gulu ndipo izi ndi zimene zinkachitikanso pa misonkhano ya Akhristu.—Mac. 13:15; 15:21; 2 Akor. 3:15.
Popeza Timoteyo anali mkulu, iye anayenera “kukhala wodzipereka” powerenga mokweza n’cholinga choti athandize anthu amene analibe makope awoawo a Malemba. N’zosakayikitsa kuti anthu onse ankamvetsera mwatcheru wina akamawerenga mokweza Mawu a Mulungu n’cholinga choti asaphonye mawu alionse. Ndipo akafika kunyumba, makolo ndi ana ayenera kuti ankakambirana zimene zinkawerengedwa pa misonkhano.
Mpukutu wa Yesaya wodziwika kwambiri umene unapezedwa pafupi ndi Nyanja Yakufa ndi wautali mamita 7.3. Mpukutu umodzi uyenera kuti unali wolemera chifukwa chokhala ndi ndodo mbali zonse ziwiri ndiponso chikuto. N’kutheka kuti Akhristu ambiri akamalalikira sankatha kunyamula mipukutu yambiri. Ngati Paulo anali ndi mipukutu yakeyake ya Malemba, iye ayenera kuti sankatha kunyamula mipukutu yonse n’kumayenda nayo. Zikuoneka kuti mipukutu ina anaisiya kwa Karipo amene ankakhala ku Torowa.
Zimene Tingaphunzire kwa Paulo
Paulo ataikidwa m’ndende kachiwiri ku Roma komanso asanapemphe Timoteyo kuti amubweretsere mipukutu, analemba kuti: “Ndamenya nkhondo yabwino. Ndathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake. . . . Kuyambira panopa mpaka m’tsogolo, andisungira chisoti chachifumu chachilungamo.” (2 Tim. 4:7, 8) Iye ayenera kuti analemba mawu amenewa cha m’ma 65 C.E. pa nthawi imene Mfumu Nero anali kuzunza Akhristu. Ataikidwa m’ndende ulendo wachiwiriwu, zinali zoopsa kwambiri ndipo anazindikira kuti watsala pang’ono kuphedwa. (2 Tim. 1:16; 4:6) M’pake kuti Paulo anafunitsitsa kuti mipukutu yake akhale nayo pafupi. Ngakhale kuti ankadziwa kuti wamenya nkhondo yabwino mpaka pa mapeto, iye anafunitsitsa kupitiriza kudzilimbitsa mwauzimu pophunzira Mawu a Mulungu.
Zikuoneka kuti Timoteyo anali kukhalabe ku Efeso pamene Paulo ankapempha kuti abweretse mipukutuyo. (1 Tim. 1:3) Ulendo wochoka ku Efeso kupita ku Roma kudutsa ku Torowa unali pafupifupi makilomita 1,600. M’kalata yomweyi, Paulo anauza Timoteyo kuti: “Uchite chilichonse chotheka kuti ufike kuno nyengo yachisanu isanayambe.” (2 Tim. 4:21) Baibulo silinena ngati Timoteyo anakwera ngalawa kuti afike ku Roma pa nthawi imene Paulo ankafuna.
Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Paulo anapempha zokhudza “mipukutu, makamaka yazikopa”? Paulo anali wofunitsitsa kupitiriza kuphunzira Mawu a Mulungu pa nthawi yovuta imeneyi. Apa zikuonekeratu kuti kuchita zimenezi n’kumene kunamuthandiza kuti nthawi zonse azikhala wolimba mwauzimu, wakhama ndiponso wolimbikitsa kwa anthu ambiri.
Masiku ano, ndife odala kwambiri chifukwa tikhoza kukhala ndi Baibulo lonse lathunthu. Ena mwa ife tili ndi Mabaibulo angapo ndiponso osiyanasiyana. Mofanana ndi Paulo, tiyenera kukhala ndi mtima wofunitsitsa kumvetsa bwino Malemba. Pa makalata 14 amene Paulo anauziridwa kulemba, kalata yake yachiwiri yopita kwa Timoteyo inali yomaliza. Pempho lake lakuti ‘unditengereko mipukutu, makamaka yazikopa ija,’ analilemba kumapeto kwa kalata imeneyi. Ndipo pa zinthu zimene ankafuna, pempho limeneli linali chimodzi mwa zinthu zomaliza zomwe analemba.
Kodi inunso mukufunitsitsa kumenya nkhondo yabwino mpaka pa mapeto ngati mmene Paulo anachitira? Kodi mukufuna kukhalabe olimba mwauzimu ndiponso okonzeka kugwira ntchito yochitira umboni pa nthawi yonse imene Ambuye adzafuna? Ngati mukufuna zimenezi, chitani zimene Paulo analimbikitsa Akhristu kuchita. Nthawi zonse muyenera ‘kusamala ndi zimene mumachita komanso zimene mumaphunzitsa.’ Mungachite zimenezi pophunzira Baibulo mwakhama nthawi zonse. Ubwino wake ndi wakuti masiku ano anthu ambiri akhoza kulipeza ndipo ndi losavuta kuwerenga kusiyana ndi mipukutu yakale ija.—1 Tim. 4:16.
[Mapu/Chitunzi pamasamba 18, 19]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Efeso
Torowa
Roma