-
Zimene Azimayi Angaphunzire kwa YunikeNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2022 | April
-
-
MUZIPHUNZITSA ANA ANU MWA ZOCHITA ZANU
12. Mogwirizana ndi 2 Timoteyo 1:5, kodi chitsanzo cha a Yunike chinathandiza bwanji Timoteyo?
12 Werengani 2 Timoteyo 1:5. A Yunike ankapereka chitsanzo chabwino kwa Timoteyo. Iwo ayenera anamuphunzitsa kuti chikhulupiriro chenicheni chimaphatikizapo zochita za munthu. (Yak. 2:26) Mosakayikira, Timoteyo ankaona kuti zochita za mayi ake zinkasonyeza kuti ankakonda kwambiri Yehova. Ankaonanso kuti kutumikira Yehova kunkawathandiza mayi akewo kukhala osangalala. Ndiye kodi chitsanzo cha a Yunike chinamuthandiza bwanji? Monga mmene mtumwi Paulo anafotokozera, iye anakhala ndi chikhulupiriro cholimba ngati cha mayi ake. Komatu izi sizinangochitika mwamwayi. Timoteyo ankaona chitsanzo cha mayi ake ndipo ankafunitsitsa kuwatsanzira. Mofanana ndi zimenezi, masiku ano alongo ambiri athandiza anthu a m’banja mwawo kuyamba kutumikira Yehova, “osati ndi mawu” koma zochita. (1 Pet. 3:1, 2) Inunso mungachite zimenezi. Motani?
13. N’chifukwa chiyani mayi ayenera kumaona kuti ubwenzi wake ndi Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri?
13 Muziona kuti ubwenzi wanu ndi Yehova ndi chinthu chofunika kwambiri. (Deut. 6:5, 6) Mofanana ndi azimayi ambiri, mumalolera kudzimana zinthu zambiri. Mumasala tulo ndipo mumagwiritsa ntchito nthawi, ndalama ndi zinthu zina kuti muzipezera ana anu zinthu zofunika pa moyo. Koma simuyenera kutanganidwa kwambiri ndi zinthu zimenezi mpaka kusoweratu nthawi yolimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova. Nthawi zonse muzipeza nthawi yopemphera pa nokha, kuphunzira Baibulo komanso kusonkhana. Mukamachita zimenezi, mudzalimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova komanso kupereka chitsanzo chabwino kwa anthu a m’banja lanu ndi anthu ena.
-
-
Zimene Azimayi Angaphunzire kwa YunikeNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2022 | April
-
-
16. Kodi chitsanzo cha mlongo yemwe ali ndi ana chingathandize bwanji ena?
16 Alongo omwe muli ndi ana, kumbukirani kuti chitsanzo chanu chimathandizanso ena. Ganizirani mmene chitsanzo cha a Yunike chinathandizira mtumwi Paulo. Iye ankadziwa kuti chikhulupiriro chopanda chinyengo cha Timoteyo ‘chinayamba kukhazikika mwa a Yunike.’ (2 Tim. 1:5) Kodi ndi liti pamene Paulo anaona kwa nthawi yoyamba chikhulupiriro cha a Yunike? N’kutheka kuti ndi pa ulendo wake woyamba waumishonale pomwe anakumana ndi a Loisi ndi a Yunike ku Lusitara ndipo mwina anawathandiza kukhala Akhristu. (Mac. 14:4-18) Tangoganizani, pamene Paulo ankalembera Timoteyo kalata patatha zaka 15, ankakumbukirabe ntchito zosonyeza chikhulupiriro za a Yunike ndipo anawagwiritsa ntchito ngati chitsanzo choyenera kutengera. N’zosakayikitsa kuti chikhulupiriro chawo chinalimbikitsa kwambiri mtumwi Paulo komanso Akhristu ena. Ngati mukulera nokha ana kapena muli m’banja losiyana zipembedzo, dziwani kuti kukhulupirika kwanu kumathandiza komanso kulimbikitsa ena.
-