Kodi N’chiyani Chingatithandize Kulunjika Nawo Bwino Mawu a Choonadi?
PANTHAŴI ina wopenda maseŵero wa nyuzipepala ina anapita kukaonera seŵero. Iye sanalikonde seŵerolo ndipo litatha analemba kuti: “Ngati mukufuna kuona zinthu zosasangalatsa ndiye musalephere kukaona seŵeroli.” Kenako, okonza seŵeroli anafalitsa mawu oitanira anthu mwa kugwira mawu omwe wopenda seŵero uja analemba. Anagwira mawu akuti: “Musalephere kukaona seŵeroli!” Mawu oitanirawa ananena ndendende zimene wopenda seŵerolo analemba, koma sanalembe nkhani yonse ndipo anam’potozera mfundo yake.
Chitsanzo chimenechi chikusonyeza mmene kuona nkhani yonse mmene mukupezeka mawuwo kulili kofunika. Kungotenga mawu ochepa chabe a nkhani kungapereke tanthauzo lolakwika, monga mmene Satana anatanthauzira molakwika Malemba pamene ankayesa Yesu. (Mateyu 4:1-11) Mosiyana ndi zimenezi, kuona nkhani yonse pamene pali mawuwo, kumatithandiza kuti tipeze tanthauzo lolondola la mawuwo. Pachifukwa chimenechi, poŵerenga lemba m’Baibulo, ndibwino kuti nthaŵi zonse tione nkhani yonse kuti timvetse bwino zimene wolemba ankanena.
Lunjikani Nawo Bwino
Mawu akuti nkhani amene tawagwiritsa ntchito muno akutanthauza mbali za mawu olembedwa kapena mawu omwe munthu walankhula omwe ali pambuyo kapena patsogolo pa liwu kapena ndime, omwe nthaŵi zambiri amathandiza kumveketsa tanthauzo la liwulo kapena ndimeyo. Angatanthauzenso zochitika kapena mfundo zimene zili zogwirizana ndi zochitika zinazake ndi zina zotero. Kuona mmene nkhani yonse ya pa lemba ilili n’kofunika kwambiri chifukwa cha zimene mtumwi Paulo analemba kwa Timoteo kuti: “Uchite changu kudzionetsera kwa Mulungu wovomerezeka, wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.” (2 Timoteo 2:15) Kuti tilunjike nawo bwino Mawu a Mulungu, tifunika kuwamvetsa bwino ndiyeno n’kufotokozera ena moona mtima ndi molondola. Kulemekeza Wolemba Baibulo, Yehova, kudzatichititsa kuyesetsa kuchita zimenezi, ndipo kuona nkhani yonse kudzatithandiza kwambiri.
Zochitika Pamene Anali kulemba Timoteo Wachiŵiri
Mwachitsanzo, tiyeni tipende buku la m’Baibulo la Timoteo Wachiŵiri.a Tiyamba kupenda bukuli mwakuona zochitika pamene anali kulilemba. Kodi ndani analemba Timoteo Wachiŵiri? Analilemba liti? Kodi polemba bukuli zinthu zinali bwanji? Ndiyeno tingafunse kuti, Kodi moyo wa Timoteo yemwe dzina lake ndilo dzina la bukuli unali wotani? N’chifukwa chiyani anafunika zomwe zili m’bukuli? Mayankho a mafunso ameneŵa adzatithandiza kwambiri kuzindikira phindu la bukuli ndiponso kuona mmene bukuli lingakhalire laphindu kwa ife masiku ano.
Mavesi oyambirira a Timoteo Wachiŵiri amasonyeza kuti bukuli ndi kalata imene mtumwi Paulo analembera Timoteo. Mavesi ena amasonyeza kuti, pamene Paulo ankalilemba anali ku ndende chifukwa cha uthenga wabwino. Anthu ambiri atamusiya, Paulo anaona ngati anali pafupi kumwalira. (2 Timoteo 1:15, 16; 2:8-10; 4:6-8) Motero, ayenera kuti analemba bukuli cha m’ma 65 C.E., ataikidwa m’ndende kachiŵiri ku Roma. Zitangochitika zimenezi, zikuoneka kuti Nero analamula kuti Paulo aphedwa.
Izi ndi zimene zinachitika pamene anali kulemba Timoteo Wachiŵiri. Komabe, n’zosangalatsa kuona kuti Paulo sanalembere Timoteo n’cholinga choti am’dandaulire mavuto ake. M’malo mwake, anachenjeza Timoteo za nthaŵi zovuta zomwe adzakumana nazo ndipo analimbikitsa bwenzi lakeli kupeŵa zocheukitsa, koma kuti apitirizebe ‘kulimbika’ ndi kuuzako ena malangizo a Paulo. Ndiyeno anthu amene anawauzawo adzadziŵa kuthandiza enanso. (2 Timoteo 2:1-7) Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwambiri choganizira ena ngakhale panthaŵi zovuta! Ndipo ndi malangizo abwino kwambiri kwa ife masiku ano!
Paulo akutchula Timoteo kuti “mwana wanga wokondedwa.” (2 Timoteo 1:2) Wachinyamatayu amatchulidwa kaŵirikaŵiri m’Malemba Achigiriki Achikristu kukhala mnzake wokhulupirika wa Paulo. (Machitidwe 16:1-5; Aroma 16:21; 1 Akorinto 4:17) Pamene Paulo anam’lembera kalatayi, zikuoneka kuti Timoteo anali ndi zaka za m’ma 30 ndipo ankaonedwabe ngati wachinyamata. (1 Timoteo 4:12) Komabe, anali kale ndi mbiri yabwino yokhala wokhulupirika, ‘anatumikira pamodzi ndi Paulo’ mwina kwa zaka 14. (Afilipi 2:19-22) Ngakhale kuti Timoteo anali wachinyamata, Paulo anam’patsa udindo wolangiza akulu ena ‘osachita makani ndi mawu’ koma kuika mtima pa zinthu zofunika monga chikhulupiriro ndi kupirira. (2 Timoteo 2:14) Timoteo anapatsidwanso mphamvu yoika oyang’anira ndi atumiki otumikira m’mipingo. (1 Timoteo 5:22) Komabe, ayenera kuti ankadziona ngati wosayenerera kuchita zimenezi.—2 Timoteo 1:6, 7.
Mkulu wachinyamatayu anakumana ndi mavuto ena aakulu. Limodzi mwa mavuto ameneŵa linali lakuti anthu ena aŵiri, Humenayo ndi Fileto, anali ‘kupasula chikhulupiriro cha ena’ mwa kuphunzitsa kuti ‘kuuka kwa akufa kunachitika kale.’ (2 Timoteo 2:17, 18) Mwachionekere, iwo ankakhulupirira kuti kuuka komwe kunalipo ndi kwauzimu ndiponso kuti kunali kutachitika kale kwa Akristu. Mwinamwake sanaone nkhani yonse ya mawu a Paulo akuti Akristu anali akufa m’zolakwa zawo koma anawapatsa moyo mwa mzimu wa Mulungu. (Aefeso 2:1-6) Paulo anachenjeza kuti anthu ampatuko otero adzachuluka. Iye analemba kuti: “Idzafika nthaŵi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; . . . ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe.” (2 Timoteo 4:3, 4) Chenjezo limene Paulo analiperekeratu linasonyeza kuti kunali kofunika kwa Timoteo kumvera malangizo a mtumwiyo.
Kufunika kwa Bukuli Masiku Ano
Pa zimene tafotokoza kale, tikuona kuti Paulo analemba Timoteo Wachiŵiri chifukwa cha mfundo zosachepera pa izi: (1) Anadziŵa kuti imfa yake inali pafupi, ndipo anafuna kuti akonzekeretse Timoteo chifukwa cha nthaŵi imene iye sadzakhalapo kuti am’thandize. (2) Anafuna kukonzekeretsa Timoteo kuti athe kuteteza mipingo yomwe anali kuiyang’anira kwa anthu ampatuko pamodzinso ndi zinthu zina zoipa. (3) Anafuna kulimbikitsa Timoteo kukhalabe wachangu m’utumiki wa Yehova ndi kudalira zolondola zimene anazidziŵa za m’Malemba ouziridwa potsutsa molimba ziphunzitso zonyenga.
Kudziŵa zochitika zimenezi kumapangitsa buku la Timoteo Wachiŵiri kukhala lothandiza kwambiri kwa ifeyo. Masiku ano, palinso ampatuko onga Humenayo ndi Fileto amene akulimbikitsa maganizo awo ndipo akufuna kuwononga chikhulupiriro chathu. Ndipotu, “nthaŵi zoŵaŵitsa” zimene Paulo analosera ndi zino. Anthu ambiri aona kuti chenjezo la Paulo lakuti: “Onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo,” ndi loona. (2 Timoteo 3:1, 12) Kodi tingatani kuti tikhale olimba? Mofanana ndi Timoteo, tiyenera kumvera malangizo a anthu amene atumikira Yehova kwa zaka zambiri. Ndipo mwa kukhala ndi phunziro laumwini, pemphero, ndi kuyanjana ndi Akristu, tingapitirizebe ‘kulimbikira’ mwa chisomo cha Yehova. Ndiponso, mwakudalira mphamvu ya zolondola zimene tazidziŵa, tingatsatire langizo la Paulo lakuti: “Gwira chitsanzo cha mawu a moyo.”—2 Timoteo 1:13.
“Chitsanzo cha Mawu a Moyo”
Kodi “mawu a moyo” amene Paulo ananena n’chiyani? Iye akugwiritsira ntchito mawu ameneŵa kutanthauza chiphunzitso choona chachikristu. M’kalata yake yoyamba kwa Timoteo, Paulo anafotokoza kuti “mawu a moyowo” ndiwo “a Ambuye wathu Yesu Kristu.” (1 Timoteo 6:3) Kutsanzira chitsanzo cha mawu a moyo kumapangitsa munthu kukhala wamaganizo abwino, wachikondi, ndi woganizira ena. Popeza utumiki wa Yesu ndi zimene ankaphunzitsa n’zogwirizana ndi ziphunzitso zina zonse za m’Baibulo lonse, “mawu a moyo” angatanthauzenso ziphunzitso zonse za m’Baibulo.
Kwa Timoteo, monganso mmene zilili kwa akulu onse, chitsanzo cha mawu a moyo chinali ‘chosungitsa chokoma’ chofunika kuchiteteza. (2 Timoteo 1:13, 14) Timoteo anafunika ‘kulalikira mawu; kuchita nawo pa nthaŵi yake, popanda nthaŵi yake; kutsutsa, kudzudzula, kuchenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi chiphunzitso.’ (2 Timoteo 4:2) Tikazindikira kuti ziphunzitso za ampatuko zinali kufalikira m’masiku a Timoteo, tidzadziŵa chifukwa chake Paulo anagogomeza kufunika kophunzitsa mawu a moyo. Tikuonanso kuti, Timoteo anafunika kuteteza nkhosa mwa ‘kutsutsa, kudzudzula, kuchenjeza,’ moleza mtima ndiponso mogwiritsira ntchito luso lakuphunzitsa.
Kodi Timoteo anafunikira kulalikira mawu kwa ndani? Nkhani yonse ikusonyeza kuti Timoteo, monga mkulu anafunika kulalikira mawu m’mpingo wachikristu. Ndipo chifukwa cha mavuto omwe otsutsa ankachititsa, Timoteo anafunika kukhalabe munthu wauzimu ndi kulalikira molimba mtima mawu a Mulungu, osati nzeru za anthu, maganizo ake, kapena mphekesera zopanda pake. N’zoona kuti zimenezi zikanapangitsa anthu amene anali ndi maganizo oipa kuyamba kutsutsa. (2 Timoteo 1:6-8; 2:1-3, 23-26; 3:14, 15) Komabe, mwa kutsatira malangizo a Paulo, Timoteo akanapitirizabe kutsutsa ampatuko monga momwe Paulo anachitira.—Machitidwe 20:25-32.
Kodi mawu a Paulo onena za kulalikira mawu amagwiranso ntchito polalikira kunja kwa mpingo? Inde, amatero, monga momwe nkhani yonse ikusonyezera. Paulo akupitiriza kunena kuti: “Koma iwe, khala maso m’zonse, imva zoŵaŵa, chita ntchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.” (2 Timoteo 4:5) Kulalikira uthenga wabwino wopulumutsa kwa osakhulupirira, ndi ntchito yofunika kwambiri ya utumiki wachikristu. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Ndipo monga momwe mawu a Mulungu amawalalikira m’mpingo ngakhale ‘popanda nthaŵi,’ choteronso timalimbikira kulalikira mawu kwa anthu omwe sali m’mpingo ngakhale zinthu zitakhala zovuta kwambiri.—1 Atesalonika 1:6.
Mawu a Mulungu ouziridwa ndiwo maziko a kulalikira ndi kuphunzitsa kwathu konse. Timadalira kwambiri Baibulo. Paulo anauza Timoteo kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.” (2 Timoteo 3:16) Mawu ameneŵa nthaŵi zambiri amagwidwa molondola kusonyeza kuti Baibulo ndi Mawu ouziridwa a Mulungu. Koma kodi Paulo anali ndi cholinga chotani powalemba?
Paulo anali kulankhula kwa mkulu amene anali ndi udindo m’mpingo ‘wotsutsa, wokonza, wolangiza m’chilungamo.’ Choncho, anali kukumbutsa Timoteo kudalira nzeru ya Mawu ouziridwa imene anaphunzitsidwa kuyambira ukhanda wake. Mofanana ndi Timoteo, akulu nthaŵi zina ayenera kudzudzula ochita zoipa. Pamene akuchita zimenezi, ayenera nthaŵi zonse kudalira Baibulo. Ndiponso, popeza Malemba ndi ouziridwa ndi Mulungu, kudzudzula kulikonse kwa m’Malemba kumachokeradi kwa Mulungu. Aliyense amene amakana uphungu wochokera m’Baibulo sikuti amakana malingaliro a munthu, koma uphungu wouziridwa wochokera kwa Yehova.
Buku la Timoteo Wachiŵiri lili ndi nzeru za Mulungu zochuluka! Ndipo lingakhale lothandiza kwambiri pamene tiŵerenga malangizo ake mwakuona nkhani yonse mmene ilili. M’nkhaniyi, tangoona mwachidule uthenga wosangalatsa wouziridwa womwe uli m’bukuli, koma ndi wokwanira kusonyeza mmene kulili kothandiza kuona nkhani yonse ya zimene tikuŵerenga m’Baibulo. Zimenezi zidzatithandiza kuonetsetsa kuti ‘tikulunjika nawodi bwino mawu a choonadi.’
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve zambiri, onani buku lakuti, Insight on the Scriptures, Voliyumu 2 masamba 1105 mpaka 1108, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 27]
Paulo anafuna kukonzekeretsa Timoteo kuti ateteze mipingo
[Chithunzi patsamba 30]
Paulo anakumbutsa Timoteo kudalira nzeru ya Mawu ouziridwa