Samalani ndi Misampha ya Mdyerekezi
‘Wonjokani mumsampha wa Mdyerekezi.’—2 TIM. 2:26.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
Ngati timafulumira kukayikira anthu ena, kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?
Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Pilato ndi Petulo pa nkhani ya kuopa anthu kapena kufuna kuwasangalatsa?
Kodi mungatani kuti musamadziimbe mlandu kwambiri?
1, 2. Kodi m’nkhani ino tikambirana misampha iti ya Mdyerekezi?
MDYEREKEZI amasaka atumiki a Yehova. Koma sikuti cholinga chake kwenikweni ndi kuwapha. Iye amafuna kuwagwira amoyo n’cholinga choti azichita zofuna zake.—Werengani 2 Timoteyo 2:24-26.
2 Mlenje amagwiritsa ntchito msampha kuti agwire nyama yamoyo. Amatha kukusa nyama kuti ifike pamalo amene angaikole ndi khwekhwe. Apo ayi, amatchera msampha pamalo obisika kuti nyama imene ikungodziyendera ikodwe. Ndi mmenenso Mdyerekezi amachitira pofuna kugwira atumiki a Mulungu. Kuti tisakodwe, tiyenera kukhala tcheru komanso kumvera machenjezo osonyeza kuti msampha wa Satana uli pafupi. M’nkhani ino, tikambirana mmene tingapewere misampha itatu ya Mdyerekezi imene yakola anthu ambiri. Misampha yake ndi (1) kusalankhula bwino, (2) kuopa anthu kapena kufuna kuwasangalatsa ndiponso (3) kudziimba mlandu kwambiri. M’nkhani yotsatira tidzakambirana misampha ina iwiri.
PEWANI KUSALANKHULA BWINO
3, 4. Kodi chingachitike n’chiyani ngati sitilamulira lilime lathu? Perekani chitsanzo.
3 Nthawi zina mlenje akafuna kugwira nyama, amayatsa tchire kuti zivumbuluke. Nayenso Mdyerekezi amafuna kuyatsa moto wophiphiritsa mu mpingo wachikhristu. Amatero n’cholinga choti anthu achoke mu mpingo kenako iyeyo awagwire. Koma mosazindikira, tikhoza kuchita zinthu zogwirizana ndi cholinga chakechi n’kugwidwa. Kodi zimenezi zingatheke bwanji?
4 Yakobo anayerekeza lilime ndi moto. (Werengani Yakobo 3:6-8.) Ngati sitilamulira lilime lathu, tikhoza kuyambitsa moto mu mpingo. Kodi zimenezi zingachitike bwanji? Tiyerekeze kuti pa misonkhano ya mpingo alengeza kuti mlongo wina wavomerezedwa kukhala mpainiya wokhazikika. Misonkhano itatha, ofalitsa awiri akukambirana za chilengezocho. Mmodzi akusangalala ndipo akumufunira zabwino mpainiyayo. Koma wina akukayikira zolinga za mpainiyayo n’kumanena kuti akungofuna kutchuka. Kodi inuyo mungafune kumacheza ndi wofalitsa uti? Mwina mwaona kale kuti zolankhula za wofalitsa wachiwiriyu zikhoza kuyatsa moto mu mpingo.
5. Kodi tingatani kuti tipewe kusalankhula bwino?
5 Kodi tingapewe bwanji kusalankhula bwino? Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.” (Mat. 12:34) Choncho, poyamba tiyenera kufufuza mtima wathu. Kodi timapewa maganizo amene angatichititse kulankhula zinthu zopweteka? Mwachitsanzo, kodi timatani ngati m’bale wina akuyesetsa kuchita zambiri mu mpingo? Kodi timaganiza kuti ali ndi zolinga zabwino kapena timafulumira kuganiza kuti zolinga zake n’zolakwika? Ngati timafulumira kukayikira ena, ndi bwino kukumbukira kuti Mdyerekezi anakayikiranso zolinga za Yobu, yemwe ankatumikira Mulungu mokhulupirika. (Yobu 1:9-11) M’malo mokayikira m’bale wathu, tiyenera kudzifunsa kuti, N’chifukwa chiyani ndikumukayikira? Kodi pali zifukwa zomveka? Kapena kodi ndikutengera mtima wosakonda anthu umene wafala m’masiku otsiriza ano?—2 Tim. 3:1-4.
6, 7. (a) Kodi tingakayikire anthu ena pa zifukwa ziti? (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani anthu akatinena zachipongwe?
6 Tiyeni tione zifukwa zina zimene zingatichititse kukayikira ena. Chifukwa china chingakhale chakuti timafuna kuti titchuke ifeyo. Zili ngati tikukankhira ena pansi n’cholinga choti ifeyo tioneke aatali. Tikhoza kukayikiranso ena pofuna kudzikhululukira ngati tikulephera kuchita zinthu zina. Kaya timakayikira ena chifukwa cha kunyada, nsanje kapena kudziona kuti ndife olephera, zotsatira zake zimakhala zoipa.
7 Mwina timaona kuti tili ndi zifukwa zabwino zochititsa kuti tisalankhule bwino za munthu wina. N’kutheka kuti zolankhula za munthuyo zinatipsetsa mtima. Koma ngati zili choncho, si bwino kubwezera ndi mawu opwetekanso. Kuchita zimenezi kumangowonjezera mavuto ndipo kumagwirizana ndi zolinga za Mdyerekezi osati za Mulungu. (2 Tim. 2:26) Tiyenera kutsanzira Yesu pa nkhani imeneyi. Pamene anali kunenedwa zachipongwe, “sanabwezere zachipongwe.” M’malomwake, “anali kudzipereka kwa iye amene amaweruza molungama.” (1 Pet. 2:21-23) Yesu ankakhulupirira kuti Yehova akonza zinthu m’njira yoyenera ndiponso pa nthawi yake. Ifenso tiyenera kukhulupirira Mulungu. Tikamalankhula zinthu zolimbikitsa, timathandiza kuti mu mpingo mukhale mtendere, womwe umagwirizanitsa anthu.—Werengani Aefeso 4:1-3.
PEWANI MSAMPHA WOOPA ANTHU KOMANSO KUFUNA KUWASANGALATSA
8, 9. N’chifukwa chiyani Pilato anaweruza Yesu kuti aphedwe?
8 Nyama imene yakodwa imalephera kuyenda. Nayenso munthu amene wakodwa mumsampha woopa anthu kapena kufuna kuwasangalatsa amalephera kuchita zinthu zina. (Werengani Miyambo 29:25.) Tiyeni tikambirane zitsanzo za anthu awiri amene anali osiyana kwambiri. Iwo anakodwa mumsampha umenewu ndipo tiona zimene tingaphunzire pa zimene anachita.
9 Pilato, yemwe anali bwanamkubwa wachiroma, ankadziwa kuti Yesu sanalakwe chilichonse ndipo sankafunika kuphedwa. Pilato ananena kuti Yesu sanachite chilichonse “choyenera chilango cha imfa.” Nanga n’chifukwa chiyani anamuweruza kuti aphedwe? Chifukwa chakuti ankafuna kusangalatsa anthu. (Luka 23:15, 21-25) Pofuna kuti cholinga chawo chitheke, anthuwo anafuula kuti: “Mukamumasula ameneyu, ndiye kuti si inu bwenzi la Kaisara.” (Yoh. 19:12) Mwina Pilato ankaopa kuti akamasula Yesu, achotsedwa pa udindo kapena kuphedwa kumene. Choncho analolera kuchita zofuna za Mdyerekezi.
10. N’chifukwa chiyani Petulo anakana Khristu?
10 Chitsanzo china ndi mtumwi Petulo. Iye ankagwirizana kwambiri ndi Yesu. Sankaopanso kuuza anthu kuti Yesu ndi Mesiya. (Mat. 16:16) Petulo anakhalabe wokhulupirika kwa Yesu pa nthawi imene ophunzira ena anamusiya chifukwa chosamvetsa zimene ananena. (Yoh. 6:66-69) Adani atabwera kuti adzamange Yesu, Petulo anagwiritsa ntchito lupanga kuti amuteteze. (Yoh. 18:10, 11) Koma kenako anaopa anthu mpaka anakana zoti amadziwa Yesu Khristu. Kwa kanthawi, mtumwiyu anakodwa mumsampha woopa anthu ndipo izi zinamulepheretsa kuchita zinthu molimba mtima.—Mat. 26:74, 75.
11. Kodi anthu angatikakamize kuti tichite chiyani?
11 Akhristufe sitiyenera kulola anthu ena kutikakamiza kuti tichite zinthu zimene Mulungu amadana nazo. Abwana athu kapena anthu ena angatinyengerere kuti tichite chinyengo kapena chiwerewere. Akhristu apasukulu angakakamizidwe ndi anzawo kuti abere mayeso, aonere zolaula, asute, amwe mankhwala osokoneza bongo, aledzere kapena achite zachiwerewere. N’chiyani chingatithandize kuti tisachite zinthu zimene Yehova amadana nazo chifukwa choopa anthu kapena kufuna kuwasangalatsa?
12. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Pilato ndi Petulo anachita?
12 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Pilato ndi Petulo anachita? Pilato sankamudziwa bwino Khristu. Komabe iye ankadziwa kuti Yesu sanalakwe chilichonse komanso kuti sanali munthu wamba. Ngakhale zinali choncho, iye sanali wodzichepetsa ndipo sankakonda Mulungu woona. Choncho Mdyerekezi anamugwira wamoyo. Mosiyana ndi Pilato, Petulo ankadziwa choonadi ndipo ankakonda Mulungu. Koma nthawi zina, iye sankadzichepetsa, ankachita mantha ndiponso kugonja pa mayesero. Yesu atatsala pang’ono kumangidwa, Petulo anadzitama kuti: “Ngakhale ena onse atathawa kukusiyani, koma ine ndekha sindidzatero.” (Maliko 14:29) Ngati Petulo akanakhulupirira Mulungu mofanana ndi wamasalimo, akanakhala wokonzeka kukumana ndi mayesero. Tikutero chifukwa wamasalimoyu anaimba kuti: “Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa. Munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?” (Sal. 118:6) Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu anatenga Petulo ndi atumwi ena awiri n’kupita m’munda wa Getsemane. Koma m’malo mokhala maso, Petulo ndi anzakewo anagona. Yesu anawadzutsa n’kuwauza kuti: “Amuna inu, khalani maso ndipo muzipemphera, kuti musalowe m’mayesero.” (Maliko 14:38) Koma Petulo anagonanso ndipo kenako anagonja poyesedwa chifukwa cha mantha.
13. Kodi tingatani kuti tisagonje poyesedwa?
13 Pali chinthu chinanso chimene tingaphunzire pa chitsanzo cha Pilato ndi Petulo. Kuti tisagonje tikamayesedwa, tiyenera kudziwa bwino choonadi, kukhala odzichepetsa, kukonda Mulungu ndiponso kumuopa osati kuopa anthu. Tikakhala ndi chikhulupiriro champhamvu chifukwa chodziwa bwino Mawu a Mulungu, tikhoza kuuza anthu ena molimba mtima zimene timakhulupirira. Zimenezi zingatithandize kuti tisagonje chifukwa choopa anthu. Koma sitiyenera kudzidalira kwambiri. M’malomwake, tiyenera kukhala odzichepetsa n’kumazindikira kuti timafunika thandizo la Mulungu kuti tisagonje poyesedwa. Tiyenera kupempha Yehova kuti atipatse mzimu wake. Tikamakonda kwambiri Yehova, tidzatsatira malamulo ake ndiponso kulemekeza dzina lake. Tiyeneranso kukonzekera mayesero asanafike. Mwachitsanzo, kukonzekera ndiponso kupemphera limodzi ndi ana athu kungawathandize kuti asagonje anzawo akamawakopa kuti achite zoipa.—2 Akor. 13:7.a
PEWANI MSAMPHA WODZIIMBA MLANDU KWAMBIRI
14. Kodi Mdyerekezi amafuna kuti tizikhala ndi maganizo otani?
14 Nthawi zina mlenje amatchera diwa pamalo amene nyama zimakonda kudutsa. Nyama ikasuntha chingwe cha diwalo, mwala umagwa n’kuiphwanya. Munthu amene akudziimba mlandu kwambiri amakhala ngati wapsinjidwa ndi chimwala. Tikamaganizira kwambiri zinthu zimene tinalakwitsa kale tingamve ngati ‘taponderezeka kwambiri.’ (Werengani Salimo 38:3-5, 8.) Satana amafuna kuti tizidziona ngati ndife ochimwa kwambiri moti sitiyenera chifundo cha Yehova ndipo sitingathe kuchita zimene Mulungu amafuna.
15, 16. Kodi mungapewe bwanji msampha wodziimba mlandu kwambiri?
15 Kodi mungapewe bwanji msampha wodziimba mlandu kwambiri? Ngati mwachita tchimo lalikulu, yesetsani mwamsanga kukonza ubwenzi wanu ndi Yehova. Auzeni akulu kuti akuthandizeni. (Yak. 5:14-16) Chitani zonse zimene mungathe kuti mukonze cholakwacho. (2 Akor. 7:11) Mukalandira chilango, musakhumudwe. Umenewo ndi umboni woti Yehova amakukondani. (Aheb. 12:6) Yesetsani kuti musadzachitenso zinthu zimene zinayambitsa vutolo. Ngati mwalapa n’kutembenuka, khulupirirani kuti nsembe ya dipo ya Yesu Khristu ikhoza kuphimbiratu machimo anu.—1 Yoh. 4:9, 14.
16 Anthu ena amadziimbabe mlandu chifukwa cha machimo amene anakhululukidwa kale. Ngati mumatero, kumbukirani kuti Yehova anakhululukira Petulo ndi atumwi ena amene anasiya Mwana wake wokondedwa pa nthawi imene iye ankafunika kwambiri thandizo. Yehova anakhululukiranso munthu wa ku Korinto amene anachita chiwerewere ndi mkazi wa bambo ake, munthuyo atalapa. (1 Akor. 5:1-5; 2 Akor. 2:6-8) Mawu a Mulungu amanena za anthu ambiri amene anachita machimo akuluakulu omwe analapa n’kukhululukidwa ndi Mulungu.—2 Mbiri 33:2, 10-13; 1 Akor. 6:9-11.
17. Kodi dipo lingatithandize bwanji?
17 Yehova amakhululuka ndi kuiwala machimo ngati munthu walapa n’kulola kuti Mulungu amuchitire chifundo. Musamaganize kuti nsembe ya dipo ya Yesu singaphimbe machimo anu. Maganizo amenewa angachititse kuti mukodwe mumsampha wa Satana. Mdyerekezi amafuna kuti muziganiza kuti dipo silingaphimbe machimo anu. Koma Yehova amakhululukira anthu onse amene alapa. (Miy. 24:16) Kukhulupirira dipo kungakuthandizeni kuti musamadziimbe mlandu kwambiri. Zimenezi zingakupatseni mphamvu kuti muzitumikira Mulungu ndi mtima wanu wonse, maganizo anu onse ndiponso moyo wanu wonse.—Mat. 22:37.
TIKUDZIWA BWINO ZIWEMBU ZA SATANA
18. Kodi tingapewe bwanji misampha ya Mdyerekezi?
18 Satana amangofuna kutikola basi. Iye alibe nazo ntchito kuti msampha womwe ukole ndi uti. Koma ife tikhoza kupewa misampha ya Mdyerekezi chifukwa tikudziwa bwino ziwembu zake. (2 Akor. 2:10, 11) Kuti tipewe misamphayi, tiyenera kupempha Mulungu kuti atipatse nzeru zotithandiza kuthana ndi mayesero. Yakobo analemba kuti: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.” (Yak. 1:5) Tiyenera kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene timapempha. Tiziphunzira Baibulo nthawi zonse ndiponso kutsatira zimene timaphunzira. Mabuku ofotokoza Baibulo ochokera kwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatidziwitsa misampha ya Mdyerekezi ndiponso mmene tingaipewere.
19, 20. N’chifukwa chiyani tiyenera kudana ndi zoipa?
19 Kupemphera ndiponso kuphunzira Baibulo zimatithandiza kukonda zabwino. Koma tifunikanso kudana ndi zoipa. (Sal. 97:10) Kuganizira mavuto amene angabwere chifukwa chotsatira zilakolako zoipa kungatithandize kuzipewa. (Yak. 1:14, 15) Tikamakonda zabwino n’kumadana ndi zoipa, zinthu zimene Satana amagwiritsa ntchito kuti atikole, zimatinyansa kwambiri moti sitingakopeke nazo.
20 Timayamikira kwambiri kuti Mulungu amatithandiza kuti Satana asatichenjerere. Yehova amatilanditsa “kwa woipayo” pogwiritsa ntchito mzimu wake, Mawu ake ndiponso gulu lake. (Mat. 6:13) M’nkhani yotsatira tiona mmene tingapewere misampha ina iwiri imene Mdyerekezi akukola nayo atumiki a Mulungu ambiri.
[Mawu a M’munsi]
a Makolo angachite bwino kukambirana ndi ana awo tchati chakuti “Mmene Mungakonzekerere” m’buku lakuti Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, tsamba 132 ndi 133. Mukhoza kuchita zimenezi pa Kulambira kwa Pabanja.
[Chithunzi patsamba 21]
Kusalankhula bwino kungayambitse moto mu mpingo
[Chithunzi patsamba 24]
Kudziimba mlandu kwambiri kuli ngati kunyamula chimwala, koma n’zotheka kuchitula