MUTU 5
Oyang’anira Amene Amaweta Nkhosa za Mulungu
PA NTHAWI imene Yesu anali pa dziko lapansi anasonyeza kuti anali “M’busa wabwino.” (Yoh. 10:11) Ataona khamu la anthu limene linkam’tsatira, “iye anawamvera chisoni, chifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Petulo ndi atumwi ena anaona mmene Yesu anakhudzidwira ndi anthuwo. Yesu anali wosiyana kwambiri ndi abusa achinyengo a mu Isiraeli omwe ankalephera kusamalira nkhosa zawo mwauzimu mpaka nkhosazo zinamwazikana. (Ezek. 34:7, 8) Poona chitsanzo cha Yesu cha mmene ankaphunzitsira ndi kusamalira nkhosa mpaka kufika popereka moyo wake, atumwiwo anaphunzira mmene angathandizire anthu amene anali ndi chikhulupiriro kuti abwerere kwa Yehova yemwe anali ‘m’busa wawo ndi woyang’anira miyoyo yawo.’—1 Pet. 2:25.
2 Pamene Yesu ankalankhula ndi Petulo pa nthawi ina, anatsindika kufunika kodyetsa ndi kuweta nkhosa za Mulungu. (Yoh. 21:15-17) Petulo ayenera kuti anakhudzidwa kwambiri ndi zimenezi moti patapita nthawi analangiza akulu mu mpingo wachikhristu woyambirira kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa. Osatinso chifukwa chofuna kupindulapo kenakake, koma ndi mtima wonse. Osati mochita ufumu pa anthu amene ali cholowa chochokera kwa Mulungu, koma mukhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” (1 Pet. 5:1-3) Mawu amenewa ndi othandizanso kwa oyang’anira mu mpingo masiku ano. Potengera chitsanzo cha Yesu, nawonso akulu amatumikira mofunitsitsa. Akamakhala patsogolo potumikira Yehova amapereka chitsanzo chabwino kwa nkhosazo.—Aheb. 13:7.
Potengera chitsanzo cha Yesu, akulu amatumikira mofunitsitsa ndipo akamakhala patsogolo potumikira Yehova amapereka chitsanzo chabwino kwa nkhosa
3 Timayamikira kukhala ndi oyang’anira oikidwa ndi mzimu mu mpingo. Timapeza madalitso ambiri chifukwa chakuti amatisamalira mwachikondi. Mwachitsanzo, amalimbikitsa mpingo komanso amasamalira munthu aliyense payekha. Mlungu uliwonse, amatsogolera mwakhama misonkhano ya mpingo yomwe imalimbitsa chikhulupiriro cha onse. (Aroma 12:8) Kuyesetsa kwawo kutetezera nkhosa kuti zisavulazidwe ndi anthu oipa komanso zinthu zina, kumathandiza kuti tikhale otetezeka. (Yes. 32:2; Tito 1:9-11) Iwo amatsogolera pa ntchito yolalikira ndipo zimenezi zimatilimbikitsa kuti nafenso tizilalikira uthenga wabwino mwakhama mwezi uliwonse. (Aheb. 13:15-17) Yehova akugwiritsa ntchito “mphatso za amuna” zimenezi kuti alimbitse mpingo.—Aef. 4:8, 11, 12.
ZIMENE MUNTHU AYENERA KUCHITA KUTI AYENERERE KUKHALA WOYANG’ANIRA
4 Kuti mpingo uzisamaliridwa bwino, pali mfundo zochokera m’Mawu a Mulungu zimene amuna omwe akufuna kukhala oyang’anira mu mpingo ayenera kukwaniritsa. Akakwaniritsa mfundo zimenezi m’pamene tinganene kuti aikidwa ndi mzimu woyera. (Mac. 20:28) Popeza kukhala woyang’anira ndi udindo waukulu kwambiri, oyang’anira amafunika kutsatira mfundo zapamwamba za m’Malemba. Koma mfundozi si zapamwamba kwambiri moti amuna achikhristu amene amakonda Yehova komanso amene ndi ofunitsitsa kuti awagwiritsire ntchito sangathe kuzifikira. Choncho oyang’anirawo ayenera kuyesetsa kuti aliyense aziona kuti amatsatira mfundo za m’Baibulo pa zochita zawo zonse.
Kuti mpingo uzisamaliridwa bwino, pali mfundo zochokera m’Mawu a Mulungu zimene amuna omwe akufuna kukhala oyang’anira mu mpingo ayenera kukwaniritsa
5 M’kalata yake yoyamba yopita kwa Timoteyo komanso m’kalata yopita kwa Tito, mtumwi Paulo anatchula mfundo za m’Malemba zimene anthu ofuna kukhala oyang’anira mumpingo ayenera kutsatira. Pa 1 Timoteyo 3:1-7, Paulo analemba kuti: “Ngati munthu aliyense akuyesetsa kuti akhale woyang’anira, akufuna ntchito yabwino. Choncho woyang’anira akhale wopanda chifukwa chomunenezera, mwamuna wa mkazi mmodzi, wosachita zinthu mopitirira malire, woganiza bwino, wadongosolo, wochereza alendo, ndiponso wotha kuphunzitsa. Asakhale munthu womwa mowa mwauchidakwa, kapena wandewu, koma wololera. Asakhale waukali, kapena wokonda ndalama. Akhale mwamuna woyang’anira bwino banja lake. Wa ana omumvera ndi mtima wonse. (Ndithudi, ngati munthu sadziwa kuyang’anira banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalire bwanji?) Asakhale wotembenuka kumene, kuopera kuti angakhale wotukumuka chifukwa cha kunyada, n’kulandira chiweruzo chofanana ndi chimene Mdyerekezi analandira. Komanso, akhale woti ngakhale anthu akunja akumuchitira umboni wabwino, kuti asatonzedwe ndi kukodwa mumsampha wa Mdyerekezi.”
6 Paulo analemberanso Tito kuti: “Ndinakusiya ku Kerete kuti ukonze zinthu zosalongosoka ndi kuti uike akulu mumzinda uliwonse, malinga ndi malangizo amene ndinakupatsa. Mkulu ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera, mwamuna wa mkazi mmodzi, wa ana okhulupirira ndi osanenezedwa kuti ndi amakhalidwe oipa kapena osalamulirika. Pakuti woyang’anira ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera. Pokhala mtumiki wa Mulungu, asakhale womva zake zokha, wa mtima wapachala, womwa mowa mwauchidakwa, wandewu, kapena wokonda kupeza phindu mwachinyengo. Koma akhale wochereza alendo, wokonda zabwino, woganiza bwino, wolungama, wokhulupirika, wodziletsa, wogwira mwamphamvu mawu okhulupirika pamene akuphunzitsa mwaluso, kuti athe kulimbikitsa anthu ndi chiphunzitso cholondola ndiponso kudzudzula otsutsa.”—Tito 1:5-9.
7 Ngakhale kuti mfundo za m’Malembazi zingaoneke ngati zovuta kuzitsatira, amuna achikhristu sayenera kusiya kuyesayesa kuti ayenerere kukhala oyang’anira. Akamayesetsa kusonyeza makhalidwe abwino achikhristu, omwe oyang’anira amafunika kukhala nawo, zimalimbikitsanso ena mu mpingo kuti nawonso azisonyeza makhalidwewo. Paulo analemba kuti abale amenewa omwe ndi “mphatso za amuna” anaperekedwa “kuti awongolere oyerawo, achite ntchito yotumikira, amange thupi la Khristu, kufikira tonse tidzafike pa umodzi m’chikhulupiriro komanso pa kumudziwa molondola Mwana wa Mulungu, inde, kufikira tidzakhale munthu wachikulire, wofika pa msinkhu wauchikulire umene Khristu anafikapo.”—Aef. 4:8, 12, 13.
8 Oyang’anirawa sayenera kukhala anyamata aang’ono kwambiri kapena anthu ongophunzira kumene choonadi. Ayenera kukhala abale amene anazolowera kugwiritsa ntchito mfundo zachikhristu, amadziwa ndi kumvetsa bwino mfundo zambiri za m’Baibulo, ndiponso amakonda abale ndi alongo ndi mtima wonse. Oyang’anira amenewa ayenera kukhala anthu oti akhoza kulankhula molimba mtima pakachitika zoipa ndi kuchitapo kanthu kuti athandize anthu amene achita zoipawo. Ayeneranso kuteteza nkhosa kwa aliyense amene angafune kuzivulaza. (Yes. 32:2) Choncho oyang’anira ayenera kudziwika bwino ndi onse mu mpingo kuti ndi amuna okhwima mwauzimu omwe amakonda kwambiri nkhosa za Mulungu.
9 Anthu amene akuyenera kuikidwa kukhala oyang’anira ayenera kuonetsetsa kuti amachita zinthu mwanzeru. Ngati ndi wokwatira, woyang’anirayo ayenera kutsatira mfundo zachikhristu zokhudza banja monga zoti akhale mwamuna wa mkazi mmodzi komanso kuti akhale mwamuna woyang’anira bwino banja lake. Ngati woyang’anirayo ali ndi ana okhulupirira omwe amamumvera ndi mtima wonse ndipo sanenezedwa kuti ndi amakhalidwe oipa kapena osalamulirika, zingakhale zosavuta kuti anthu ena mu mpingo apemphe malangizo okhudza moyo wa m’banja komanso okhudza moyo wawo wauzimu. Woyang’anira ayeneranso kukhala wopanda chifukwa chomunenezera ndipo akhale woti ngakhale anthu akunja akumuchitira umboni wabwino. Sayenera kuchita chilichonse chimene chingawononge mbiri ya mpingo komanso sayenera kukhala woti anadzudzulidwa posachedwapa chifukwa chochita tchimo lalikulu. Anthu enanso mu mpingo angalimbikitsidwe kutengera chitsanzo chawo chabwino ndipo angamawadalire kuti awasamalira mwauzimu.—1 Akor. 11:1; 16:15, 16.
10 Amuna amene ali ndi makhalidwe ofunikirawa amatha kutumikira mu mpingo wachikhristu ngati mmene akulu a mu Isiraeli ankachitira omwe ananenedwa kuti anali “anzeru, aluso ndi ozindikira.” (Deut. 1:13) Akulu achikhristu ndi opanda ungwiro, koma amadziwika mu mpingo ndi m’dera limene amakhala kuti ndi anthu amakhalidwe abwino komanso oopa Mulungu amene asonyeza kwa nthawi yaitali kuti amatsatira mfundo za Mulungu nthawi zonse. Chifukwa chokhala ndi makhalidwe abwino amenewa, amakhala ndi ufulu wolankhula mu mpingo.—Aroma 3:23.
11 Amuna amene amaikidwa kukhala oyang’anira ayenera kukhala odziletsa pa zochita zawo komanso pochita zinthu ndi ena. Ayenera kukhala osachita zinthu mopitirira malire, adongosolo komanso odziletsa. Ayenera kudziletsa pa zinthu monga kudya, kumwa, zosangalatsa ndi zinthu zimene amakonda kuchita pa nthawi yopuma. Ayeneranso kudziletsa pa nkhani ya kumwa mowa n’cholinga choti asamatchuke ndi mbiri yoipa yoti amaledzera kapena kumwa mwauchidakwa. Munthu amene wasokonezeka maganizo ndi zakumwa zoledzeretsa amalephera kukhala wodziletsa ndipo sangathe kuyang’anira bwino mpingo.
12 Kuti munthu ayang’anire bwino mpingo ayenera kukhala wadongosolo. Mmene munthu amaonekera, nyumba yake komanso mmene amachitira zinthu tsiku ndi tsiku, zingathe kusonyeza kuti munthuyo ndi wadongosolo. Munthu wotereyu sazengereza pochita zinthu ndipo amatha kukonzekereratu zinthu zimene akufuna kuchita. Nthawi zonse amatsatira mfundo za Mulungu.
13 Woyang’anira ayenera kukhala wololera. Afunika kukhala munthu wotha kugwira ntchito limodzi ndi akulu anzake mogwirizana m’bungwe la akulu. Ayeneranso kudziona moyenerera ndipo azipewa kulamulira ena. Monga munthu wololera, woyang’anira sayenera kuona kuti maganizo ake ndi ofunika kwambiri kuposa a akulu anzake chifukwa akulu ena angakhale ndi makhalidwe komanso luso limene iyeyo alibe. Mkulu amasonyeza kuti ndi wololera akamagwiritsa ntchito Malemba posankha zochita komanso akamayesetsa kutsanzira chitsanzo cha Yesu Khristu. (Afil. 2:2-8) Mkulu sayenera kukhala wokonda kukangana ndi ena kapena wachiwawa koma azilemekeza ena ndi kuwaona kukhala omuposa. Sayenera kukhala womva zake zokha, wongofuna kuti nthawi zonse anthu azitsatira maganizo ake. Komanso ayenera kukhala wamtendere pochita zinthu ndi ena, osati wa mtima wapachala.
14 Ndiponso munthu woyenerera kukhala woyang’anira mu mpingo ayenera kukhala woganiza bwino. Zimenezi zikutanthauza kuti ayenera kukhala womvetsa bwino zinthu komanso wosafulumira kuweruza. Ayeneranso kudziwa bwino mfundo za Yehova ndi mmene zimagwirira ntchito. Munthu woganiza bwino amalandira mosavuta uphungu ndi malangizo ndiponso sachita zinthu mwachinyengo.
15 Paulo anakumbutsa Tito kuti woyang’anira ayenera kukhala wokonda zabwino, wolungama ndiponso wokhulupirika. Makhalidwe amenewa amaonekera ndi mmene amachitira zinthu ndi ena komanso sasintha maganizo pa zimene zili zabwino ndi zoyenera. Nthawi zonse amakhala wodzipereka kwa Yehova ndipo amatsatira mfundo zake zolungama. Amakhalanso wosunga chinsinsi. Ndiponso amadzipereka ndi mtima wonse kuchereza alendo pogwiritsa ntchito zinthu zake.—Mac. 20:33-35.
16 Kuti woyang’anira akwanitse kugwira bwino ntchito yake ayenera kukhalanso wotha kuphunzitsa. Mogwirizana ndi zimene Paulo anauza Tito, woyang’anira ayeneranso kukhala “wogwira mwamphamvu mawu okhulupirika pamene akuphunzitsa mwaluso, kuti athe kulimbikitsa anthu ndi chiphunzitso cholondola ndiponso kudzudzula otsutsa.” (Tito 1:9) Pamene akuphunzitsa ayenera kuthandiza ena kuganiza moyenera, kupereka umboni wa zimene akuphunzitsa, kutsutsa zonena zabodza komanso kugwiritsira ntchito Malemba mogwira mtima ndiponso molimbikitsa chikhulupiriro cha ena. Woyang’anira ayenera kuphunzitsa m’njira imeneyi nthawi zonse, kaya ndi m’nthawi yabwino kapena m’nthawi yovuta. (2 Tim. 4:2) Ayenera kukhala woleza mtima akamadzudzula munthu amene walakwa kapena akamathandiza munthu amene akukayikira zimene amaphunzira ndi kumulimbikitsa kuti azichita ntchito zabwino zosonyeza chikhulupiriro. Ngati woyang’anira amakwanitsa kuphunzitsa bwino pagulu kapena amatha kuthandiza munthu payekha, ndi umboni wakuti ali ndi luso lotha kuphunzitsa.
17 M’pofunikanso kuti akulu azikhala akhama pa ntchito yolalikira. Azisonyeza kuti amayesetsa kutsanzira Yesu, yemwe ankaona ntchito yolalikira uthenga wabwino kukhala yofunika kwambiri. Komanso Yesu ankakonda ophunzira ake ndipo ankawathandiza kuti azilalikira mogwira mtima. (Maliko 1:38; Luka 8:1) Choncho akulu akamadzipereka pa ntchito yolalikira ngakhale kuti amatanganidwa kwambiri, zimalimbikitsa onse mu mpingo kuti azilalikiranso mwakhama. Ndiponso akulu akamalalikira ndi mabanja awo komanso ndi anthu ena mu mpingo, onse amakhala ‘akulimbikitsana.’—Aroma 1:11, 12.
18 Zimenezi zingaoneke ngati zovuta kwa oyang’anira kuti azikwaniritse. N’zoona kuti palibe woyang’anira amene angatsatire ndendende mfundo zapamwamba za m’Baibulo. Komabe sizikutanthauza kuti mkulu azilephereratu kutsatira mfundo zapamwambazi chifukwa zimenezi zingachititse kuti asayenererenso kukhala mkulu. Akulu ena angakhale ndi maluso amene akulu ena alibe. Chifukwa cha kusiyanasiyana kwa maluso kumeneku, zimapangitsa bungwe lonse la akulu kukhala ndi makhalidwe abwino amene amathandizira kuti mpingo wa Mulungu uziyenda bwino.
19 Bungwe la akulu likamakambirana za abale amene akuyenerera kukhala pa udindo, liyenera kukumbukira mawu a mtumwi Paulo akuti: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira. Koma aliyense aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino, malinga ndi chikhulupiriro chimene Mulungu wamupatsa.” (Aroma 12:3) Mkulu aliyense asamadzione ngati woposa ena. Sayeneranso kukhala ‘wolungama mopitirira muyezo’ akamakambirana za abale amene akuyenera kukhala pa udindo. (Mlal. 7:16) Podziwa zimene Malemba amanena pa nkhani ya zofunika kuti munthu ayenerere udindo, bungwe la akulu liyenera kuona ngati m’bale amene akumuganizirayo akuyesetsa ndi mtima wonse kukwaniritsa zofunika za m’Malemba. Ndipo akamakambirana za munthu amene akuyenerera kuti akhale pa udindo ayenera kuganizira mfundo yoti ndife anthu opanda ungwiro komanso ayenera kuchita zinthu mosakondera ndi mopanda chinyengo. Akamachita zimenezi amasonyeza kuti amalemekeza mfundo zolungama za Yehova ndipo zimenezi zimathandiza mpingo. Akulu akamakambirana za anthu amene akufuna kuti akhale pa udindo amayamba ndi pemphero ndiponso amatsatira zimene mzimu woyera wa Mulungu ukuwatsogolera kuchita. Udindo woika anthu kuti akhale oyang’anira ndi waukulu kwambiri, choncho akulu ayenera kuuchita mogwirizana ndi malangizo a Paulo akuti: “Usafulumire kuika munthu aliyense pa udindo.”—1 Tim. 5:21, 22.
AMASONYEZA MAKHALIDWE AMENE MZIMU WOYERA UMATULUTSA
20 Amuna oyenerera kukhala oyang’anira azisonyeza kuti amatsogoleredwa ndi mzimu woyera pa moyo wawo. Paulo anatchula makhalidwe 9 amene mzimu woyera umatulutsa. Makhalidwewa ndi “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa.” (Agal. 5:22, 23) Oyang’anira amene ali ndi makhalidwe amenewa amalimbikitsa abale ndi alongo komanso amathandiza kuti mpingo ukhale wogwirizana potumikira Mulungu. Zochita zawo ndi makhalidwe awo abwino ndi umboni woti anaikidwa ndi mzimu woyera.—Mac. 20:28.
AMALIMBIKITSA MGWIRIZANO
21 Kuti mpingo wonse ukhale wogwirizana, akulu afunika kumagwirira ntchito limodzi. Akulu ali ndi makhalidwe osiyanasiyana koma amayesetsa kukhala ogwirizana pomvetsera ndi kulemekeza maganizo a ena ngakhale kuti sangagwirizane pa mfundo iliyonse. Ngati zimene zasankhidwazo sizikutsutsana ndi mfundo za m’Malemba, mkulu aliyense azikhala wololera komanso ayenera kugwirizana ndi zimene zasankhidwazo. Kukhala ndi mtima wololera kumasonyeza kuti munthuyo akutsogoleredwa ndi “nzeru yochokera kumwamba,” yomwe ndi “yamtendere” komanso “yololera.” (Yak. 3:17, 18) Mkulu aliyense sayenera kuganiza kuti ndi woposa anzake ndipo palibe mkulu amene ayenera kulamulira akulu ena. Akulu akamachita zinthu mogwirizana monga bungwe, amakhala akugonjera Yehova ndipo zimapindulitsa mpingo wonse.—1 Akor. 12:1-31; Akol. 2:19.
YESETSANI KUTI MUKHALE WOYANG’ANIRA
22 Amuna okhwima mwauzimu ayenera kufunitsitsa kuti akhale oyang’anira. (1 Tim. 3:1) Komabe kutumikira monga mkulu kumafuna khama ndiponso kudzipereka. Pamafunika kuti munthu adzipereke kuthandiza abale pa zosowa zawo zauzimu. Choncho munthu amene akufuna kukhala woyang’anira ayenera kuyesetsa kukwaniritsa mfundo za m’Malemba.
ZINTHU ZIKHOZA KUSINTHA
23 Nthawi zina m’bale amene watumikira mokhulupirika kwa nthawi yaitali angayambe kudwala kapena kulephera kuchita zinthu zina. Mwina chifukwa cha ukalamba, sangathenso kukwaniritsa udindo wake monga woyang’anira ngati mmene amachitira poyamba. Komabe ngakhale zili choncho, ayenera kulemekezedwa ndi kuonedwabe monga mkulu. Sikoyenera kuti asiye udindo wake chifukwa choti akulephera kukwaniritsa mbali zina. Iye ayenera kupatsidwabe ulemu waukulu ngati akulu ena onse omwe akutha kuchita zambiri poweta nkhosa za Mulungu.
24 Koma ngati m’baleyo akuona kuti zingakhale bwino atasiya kutumikira pa udindowo chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wake, angasankhe kutero. (1 Pet. 5:2) Zikatero ayenera kulemekezedwabe chifukwa angakhale wothandiza mu mpingo m’mbali zina ngakhale kuti sakutumikiranso monga mkulu.
MAUDINDO A MU MPINGO
25 Akulu amatumikira pa maudindo osiyanasiyana mu mpingo. Pamakhala wogwirizanitsa ntchito za akulu, mlembi, woyang’anira utumiki, wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda ndi woyang’anira msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu. Akulu ambiri amakhala oyang’anira magulu a utumiki wakumunda. Akulu amatumikira pa maudindo amenewa nthawi zonse. Koma ngati m’bale wasamuka, kapena ngati thanzi lake silili bwino, kapenanso ngati akulephera kukwaniritsa zimene Malemba amafuna kwa munthu waudindo, m’bale wina angasankhidwe kuti alowe m’malo mwake. M’mipingo imene ili ndi oyang’anira ochepa, mkulu mmodzi angamasamalire maudindo ambiri mpaka pamene abale ena angayenerere kukhala akulu.
26 Wogwirizanitsa ntchito za akulu amatumikira ngati tcheyamani pa misonkhano ya bungwe la akulu. Iye amakhala wodzichepetsa pamene akugwira ntchito limodzi ndi akulu ena posamalira nkhosa za Mulungu. (Aroma 12:10; 1 Pet. 5:2, 3) Ayenera kukhala wochita zinthu mwadongosolo komanso wotha kutsogolera bwino.—Aroma 12:8.
27 Mlembi amasunga mafaelo a mpingo ndipo amadziwitsa akulu ena za makalata ofunikira. Mkulu wina kapena mtumiki wothandiza woyenerera angasankhidwe kuti azimuthandiza ngati pakufunikira kutero.
28 Woyang’anira utumiki ndi amene amayang’anira ntchito yolalikira ndi zilizonse zokhudza ntchitoyi. Amakonza zoti kamodzi pa mwezi aziyendera kagulu kenakake ka utumiki wakumunda. M’mipingo ing’onoing’ono imene ili ndi timagulu tochepa, woyang’anira utumiki angayendere timaguluto kawiri pa chaka. Akamayendera kagulu, iye amachititsa misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda, kulowa limodzi ndi kaguluko mu utumiki komanso amathandiza ofalitsa mmene angapangire maulendo obwereza ndi maphunziro a Baibulo.
OYANG’ANIRA TIMAGULU TA UTUMIKI WAKUMUNDA
29 Mwayi wina wapadera mu mpingo ndi kukhala woyang’anira kagulu ka utumiki wakumunda. Ntchito za woyang’anira kagulu ka utumiki wakumunda zimaphatikizapo (1) kudziwa mmene munthu aliyense wa m’kagulu kake akuchitira mwauzimu, (2) kuthandiza aliyense m’kagulu kake kuti aziona ntchito yolalikira kukhala yofunika, azisangalala nayo komanso azilalikira nthawi zonse ndipo (3) kuthandiza ndi kuphunzitsa atumiki othandiza a m’kagulu kake kuti ayenerere maudindo ena mu mpingo. Bungwe la akulu ndi limene limasankha abale amene angakwanitse kuchita mbali zimenezi.
30 Chifukwa cha mmene ntchito za woyang’anira kagulu ka utumiki wakumunda zilili, ngati n’kotheka zingakhale bwino oyang’anirawo atakhala akulu. Nthawi zina mtumiki wothandiza woyenerera angathe kutumikira pa udindo umenewu mpaka patapezeka mkulu woti asamalire mbali imeneyi. Mtumiki wothandiza amene akuchita utumiki umenewu amatchedwa mtumiki wakagulu chifukwa sanakhale woyang’anira mu mpingo. Akulu ndi amene amamuuza zoyenera kuchita.
31 Ntchito yofunika kwambiri imene woyang’anira kagulu amachita ndi kutsogolera mu utumiki wakumunda. Kupezeka kwake mu utumiki nthawi zonse komanso khama lake pa ntchito yolalikira zimalimbikitsa anthu a m’gulu lake. Popeza ofalitsa amasangalala komanso amalimbikitsidwa akamachitira zinthu pamodzi, ndi bwino kuti woyang’anira kagulu azikonza ndandanda yabwino yolowera mu utumiki yoti ambiri azitha kuitsatira mosavuta. (Luka 10:1-16) Woyang’anira kagulu azionetsetsa kuti nthawi zonse pali gawo lokwanira loti akalalikire. Iye amachititsa msonkhano wokonzekera utumiki komanso kugawa ofalitsa akamalowa mu utumiki. Ngati sakhalapo, ayenera kupempha mkulu wina, kapena mtumiki wothandiza ngati mkuluyo palibe. Ngatinso mtumikiyo palibe, angapemphe wofalitsa wa chitsanzo chabwino kuti atsogolere kaguluko.
32 Woyang’anira kagulu ayenera kukonzekera pasadakhale kuchezera kwa woyang’anira utumiki. Amadziwitsa anthu a m’kagulu kake za kuchezerako ndi kuwathandiza kuyembekezera mwachidwi kuti adzapindule. Onse akadziwa bwino zimene zakonzedwa, amapezekapo mosavuta.
33 Gulu lililonse la utumiki wakumunda limafunika kuti likhale laling’ono. Zimenezi zimathandiza woyang’anira gululo kudziwa bwino anthu a m’gulu lake. Monga m’busa wachikondi, iye amachita chidwi ndi aliyense payekha. Amayesetsa kuthandiza ndi kulimbikitsa ofalitsa kuti azilalikira komanso kuti azipezeka pa misonkhano ya mpingo nthawi zonse. Amachitanso zimene angathe polimbikitsa aliyense kuti akhale wolimba mwauzimu. Ndiponso amayendera odwala kapena amene akumana ndi mavuto enaake. Mawu olimbikitsa kapena uphungu umene angapereke kwa ofalitsa ena ungawathandize kuti ayenerere maudindo mu mpingo n’kumathandiza abale awo. N’zoona kuti woyang’anira kagulu amathandiza kwambiri anthu a m’kagulu kake. Komabe popeza iye ndi mkulu komanso m’busa, amadera nkhawa anthu onse mu mpingo ndipo amafunitsitsa kuthandiza aliyense.—Mac. 20:17, 28.
34 Udindo wina wa woyang’anira kagulu ndi kusonkhanitsa malipoti a utumiki wakumunda a m’kagulu kake. Akasonkhanitsa malipotiwa amawapereka kwa mlembi. Wofalitsa aliyense angathandize woyang’anira kagulu ka utumiki popereka mwamsanga malipoti ake. Angachite zimenezi popereka malipotiwo kwa amene amayang’anira kagulu kawo kapena poika m’bokosi, lolembedwa kuti malipoti a utumiki wakumunda limene lili m’Nyumba ya Ufumu.
KOMITI YA UTUMIKI YA MPINGO
35 Pali ntchito zina zimene zimasamaliridwa ndi Komiti ya Utumiki ya Mpingo yomwe imapangidwa ndi wogwirizanitsa ntchito za akulu, mlembi ndi woyang’anira utumiki. Mwachitsanzo, komitiyi ndi imene imavomereza kuti Nyumba ya Ufumu igwiritsidwe ntchito kukambiramo nkhani ya ukwati kapena ya maliro ndiponso ndi yomwe imagawa ofalitsa m’timagulu ta utumiki wakumunda. A m’komiti ya utumiki ndi omwenso amavomereza anthu amene akufuna kutumikira ngati apainiya okhazikika ndi othandiza komanso amene akufuna kuchita mautumiki ena. Komitiyi imagwira ntchito moyang’aniridwa ndi bungwe la akulu.
36 Ntchito za abale a m’komiti ya utumiki ya mpingo, wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda, woyang’anira msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu ndi za akulu ena zimafotokozedwa ndi ofesi ya nthambi.
37 Bungwe la akulu la mpingo uliwonse limakumana kawirikawiri kuti likambirane zokhudza mmene mpingo ukupitira patsogolo mwauzimu. Kuwonjezera pa msonkhano wa akulu umene umachitika woyang’anira dera akamachezera mpingo wawo, pamakhalanso msonkhano wina wa akulu pakatha miyezi itatu kuchokera pamene woyang’anira dera wachezera mpingo wawo. Komabe, akulu angathe kukumana nthawi ina iliyonse pakakhala nkhani zofunika kuti akambirane.
TIZIMVERA OYANG’ANIRA
38 Ngakhale kuti oyang’anira ndi anthu opanda ungwiro, tonsefe tiyenera kuwamvera chifukwa Yehova ndi amene anakonza zoti pakhale otiyang’anira. Oyang’anira amenewa adzayankha mlandu kwa Yehova. Iwo amaimira Yehova ndi ulamuliro wake. Lemba la Aheberi 13:17 limati: “Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera. Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu. Muziwamvera ndi kuwagonjera kuti agwire ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuvulazani.” Popeza kuti Yehova amaika akulu pogwiritsa ntchito mzimu woyera, amagwiritsanso ntchito mzimu woyera womwewo kuwachotsa pa udindo ngati akulephera kusonyeza makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa komanso ngati sakutsatira mfundo za m’Malemba.
39 Timayamikira kwambiri ntchito komanso chitsanzo chabwino chimene oyang’anira amapereka mu mpingo. Polembera kalata ku mpingo wa ku Tesalonika, Paulo anati: “Tikukupemphani abale, kuti muzilemekeza anthu amene akugwira ntchito mwakhama pakati panu, amenenso amakutsogolerani mwa Ambuye ndi kukulangizani. Muwapatse ulemu waukulu mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo.” (1 Ates. 5:12, 13) Ntchito imene oyang’anira mu mpingo amagwira mwakhama imathandiza kuti tizisangalala ndi kutumikira bwino Mulungu. Komanso m’kalata yake yoyamba imene analembera Timoteyo, Paulo anafotokoza mmene anthu mu mpingo ayenera kuonera oyang’anira ponena kuti: “Akulu otsogolera bwino apatsidwe ulemu waukulu, makamaka amene amachita khama kulankhula ndi kuphunzitsa.”—1 Tim. 5:17.
MAUDINDO ENA OMWE ALI M’GULU LA MULUNGU
40 Nthawi zina akulu ena amasankhidwa kuti azitumikira m’Magulu Oyendera Odwala. Ena amatumikira m’Makomiti Olankhulana ndi Achipatala ndipo amapita m’zipatala kukalankhulana ndi madokotala zokhudza mmene angathandizire Mboni za Yehova popanda kugwiritsa ntchito magazi. Oyang’anira ena amathandiza kupititsa patsogolo ntchito ya Ufumu pomanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu ndi Malo a Misonkhano kapena potumikira m’Komiti ya Msonkhano. Timayamikira kwambiri ntchito yaikulu imene abalewa amagwira komanso kudzipereka kwawo. Ndipo abale amenewa ‘timawalemekeza kwambiri.’—Afil. 2:29.
WOYANG’ANIRA DERA
41 Bungwe Lolamulira limakonza zoti amuna oyenerera aikidwe kuti atumikire monga oyang’anira dera. Oyang’anira derawa amatumizidwa ndi ofesi ya nthambi kuti aziyendera mipingo ya m’dera lawo ndipo nthawi zambiri amaiyendera kawiri pachaka. Nthawi zinanso amayendera apainiya amene akutumikira ku magawo akutali. Iwo amakonzeratu ndandanda ya mmene adzayendere pochezera mipingo ndipo amadziwitsa mpingo uliwonse nthawi idakalipo kuti abale ndi alongo adzapindule kwambiri.
42 Wogwirizanitsa ntchito za akulu ndi amene amatsogolera pokonzekera kubwera kwa woyang’anira dera n’cholinga choti aliyense adzapindule mwauzimu. (Aroma 1:11, 12) Wogwirizanitsayo akangodziwitsidwa za kubwera kwa woyang’anira dera ndi mkazi wake (ngati ndi wokwatira), amakonzeratu zinthu zonse zofunikira monga malo ogona ndi zinthu zina, ndipo amathandizana ndi abale osiyanasiyana. Iye amaonetsetsa kuti onse, kuphatikizapo woyang’anira derayo, adziwitsidwa zimene zakonzedwa.
43 Woyang’anira dera amakambirana ndi wogwirizanitsa ntchito za akulu kuti agwirizane nthawi ya misonkhano ya mpingo, kuphatikizapo misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda. Zimenezi zimakonzedwa mogwirizana ndi maganizo a woyang’anira dera komanso malangizo ochokera ku ofesi ya nthambi. Onse ayenera kudziwitsidwiratu za malo ndi nthawi ya misonkhano ya mpingo, msonkhano wa apainiya, msonkhano wa akulu ndi atumiki othandiza, komanso malo ndi nthawi ya misonkhano yokonzekera utumiki wakumunda.
44 Lachiwiri masana, woyang’anira dera amaona Lipoti la Mpingo Lolembapo Ntchito la Wofalitsa, makadi olembapo anthu opezeka pa misonkhano ya mpingo, mafomu a magawo komanso faelo ya maakaunti. Zimenezi zimamuthandiza kudziwa zofunika pa mpingo ndi mmene angathandizire abale amene akusamalira mafomu osiyanasiyana a mpingo. Wogwirizanitsa ntchito za akulu amaonetsetsa kuti mafaelo a mpingo apitiratu kumene woyang’anira derayo akafikire.
45 Pamene akuchezera mpingo, woyang’anira dera amakhala ndi nthawi yocheza ndi abale ndi alongo kumisonkhano, mu utumiki wakumunda, pa nthawi ya chakudya komanso pa nthawi zina. Ndiponso amakumana ndi akulu ndi atumiki othandiza kuti awalimbikitse ndi kuwapatsa malangizo a m’Malemba komanso mfundo zimene angagwiritse ntchito kuti athe kusamalira bwino nkhosa. (Miy. 27:23; Mac. 20:26-32; 1 Tim. 4:11-16) Amakumananso ndi apainiya kuti awalimbikitse pa ntchito yawo ndi kuwathandiza pa mavuto alionse amene akukumana nawo mu utumiki.
46 Ngati pali nkhani zina zofunika kusamalira, woyang’anira dera ayenera kuchita zimene angathe kuti athandize akulu kusamalira nkhanizo pa nthawi imene ali pa mpingopo. Ngati nkhaniyo ikuoneka kuti singathe pa mlungu umene akuchezera mpingowo, iye angathandize akulu kapena anthu amene akukhudzidwa kufufuza malangizo a m’Malemba amene angawathandize kudziwa mmene angathetsere nkhaniyo. Ngati ofesi ya nthambi ingafune kudziwa zinthu zina zokhudza nkhaniyo, woyang’anira dera ndi akulu angapereke lipoti ku ofesi ya nthambiyo lofotokoza bwinobwino za nkhaniyo.
47 Woyang’anira dera akamachezera mpingo, amasonkhana ndi mpingowo pa misonkhano yawo ya nthawi zonse. Misonkhanoyi ingasinthidwe mogwirizana ndi malangizo ochokera ku ofesi ya nthambi. Pamisonkhanoyo amakamba nkhani zomwe cholinga chake ndi kulangiza ndi kulimbikitsa mpingo. Amalimbikitsanso abale kuti azikonda Yehova, gulu lake komanso Yesu Khristu.
48 Cholinga china chachikulu cha woyang’anira dera akamachezera mpingo ndi kulimbikitsa komanso kuthandiza anthu kuti azilalikira mwakhama komanso mogwira mtima. Pa nthawi imeneyi, abale ndi alongo angasinthe zochita zawo kuti adzalalikire mokwanira mwinanso kukonza zodzachita upainiya wothandiza. Komanso amene akufuna kudzayenda ndi woyang’anira dera kapena mkazi wake angakonzeretu zimenezi. Zimakhala zothandiza kwambiri kupita ndi woyang’anira dera kapena mkazi wake kumaphunziro a Baibulo ndi ku maulendo obwereza. Timayamikira kwambiri khama lanu limene mumasonyeza pochita zonse zimene mungathe pa nkhani imeneyi.—Miy. 27:17.
49 Chaka chilichonse, pamakonzedwa zoti pakhale misonkhano iwiri yadera m’dera lililonse. Woyang’anira dera ndi amene amayang’anira kayendetsedwe ka misonkhanoyi. Iye amasankha abale oti azitumikira monga woyang’anira msonkhano ndi wothandiza wake. Abalewa amagwira ntchito limodzi ndi woyang’anira dera poyendetsa msonkhano. Zimenezi zimathandiza woyang’anira derayo kuti aziika maganizo ake pa pulogalamu ya msonkhano. Woyang’anira dera amasankhanso abale oyenerera kuti agwire ntchito m’madipatimenti osiyanasiyana. Komanso amakonza zoti ndalama za dera ziwerengedwe pambuyo pa msonkhano uliwonse. Pachaka, msonkhano umodzi wadera umakhala ndi m’bale woyimira ofesi ya nthambi. Madera ena amagawidwa m’zigawo zingapo chifukwa cha kutalika kwa mtunda komanso kuchepa kwa malo ochitira msonkhanowo.
50 Woyang’anira dera amatumiza lipoti lake la utumiki wakumunda ku ofesi ya nthambi pamapeto pa mwezi uliwonse. Ngati wagwiritsa ntchito ndalama zake poyendera, kugulira chakudya, kulipira malo ogona kapena pa zinthu zina zofunika pochita utumiki wake, chifukwa choti mpingo umene amayendera sunathe kumulipirira, angatumize malisiti a zimenezi ku ofesi ya nthambi. Oyang’anira dera amakhala ndi chikhulupiriro chakuti monga Yesu analonjezera, nthawi zonse akamafunafuna Ufumu wa Yehova, adzapeza zinthu zofunika pa moyo wawo. (Luka 12:31) Mipingo iyenera kuchereza akulu amenewa posonyeza kuyamikira kudzipereka kwawo.—3 Yoh. 5-8.
KOMITI YA NTHAMBI
51 Pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova iliyonse pamakhala abale oyenerera atatu kapena kuposerapo omwe ndi okhwima mwauzimu, amene amatumikira m’Komiti ya Nthambi. Abalewa amayang’anira ntchito yolalikira m’dzikolo kapena m’mayiko ena omwe amayang’aniridwa ndi nthambi yawo. M’bale mmodzi amatumikira monga wogwirizanitsa ntchito za Komiti ya Nthambi.
52 Abale a m’Komiti ya Nthambi amasamalira nkhani zokhudza mipingo yonse ya m’gawo la nthambi yawo. Amayang’anira ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu m’magawo onse komanso amaonetsetsa zoti pakhale mipingo ndi madera n’cholinga choti azitha kuyang’anira bwino ntchito yonse yokhudza kulambira m’dzikomo. Komiti ya Nthambi imayang’aniranso ntchito za amishonale, apainiya apadera, apainiya okhazikika ndiponso apainiya othandiza. Pa nthawi ya misonkhano yadera ndi yachigawo, Komiti ya Nthambi imakonza zofunika zonse ndiponso kusankha okakamba nkhani ku misonkhano yachigawo n’cholinga choti “zonse zizichitika moyenera ndi mwadongosolo.”—1 Akor. 14:40.
53 Mayiko ena amene mulibe nthambi, amasankha Komiti ya Dziko yomwe imayang’aniridwa ndi Komiti ya Nthambi ya m’dziko lina. Kukhala ndi Komiti ya Dziko kumathandiza kuti ntchito ya m’dzikolo iziyang’aniridwa bwino. Komitiyi imasamalira anthu amene akutumikira pa Beteli komanso imayang’anira ntchito za m’maofesi osiyanasiyana pa Betelipo, kuphatikizapo kutumiza makalata, kusamalira malipoti ndiponso kutsogolera ntchito ya Ufumu ya m’gawo lawo. Komiti ya Dziko imagwira ntchito mogwirizana ndi Komiti ya Nthambi popititsa patsogolo ntchito ya Ufumu.
54 Bungwe Lolamulira ndi limene limaika abale amene amatumikira m’Makomiti a Nthambi ndi m’Makomiti a Dziko.
OIMIRA LIKULU
55 Kawirikawiri, Bungwe Lolamulira limatumiza abale oyenerera kuti akayendere nthambi padziko lonse lapansi. Abale amene amachita utumiki umenewu amatchedwa oimira likulu. Ntchito yawo yaikulu ndi kulimbikitsa banja la Beteli ndi kuthandiza abale a m’Komiti ya Nthambi pa mavuto kapena mafunso amene angakhale nawo okhudza ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa. Woimira likulu amakumananso ndi oyang’anira dera angapo komanso nthawi zina amakumana ndi amishonale amene akutumikira m’gawo la nthambi imene wayendera. Iye amakambirana nawo zokhudza mavuto amene akukumana nawo ndi zimene akufunikira, komanso amawalimbikitsa pa ntchito yawo yofunika kwambiri yolalikira za Ufumu ndi kuphunzitsa anthu.
56 Woimira likulu amakhala ndi chidwi ndi zimene zikuchitika pa ntchito yolalikira za Ufumu komanso mmene mipingo ikuyendera. Ngati nthawi ilipo, amathanso kuyendera maofesi a omasulira omwe ali kumadera amene kuli chinenero chimene akumasuliracho. Woimira likulu akamayendera nthambi, amayesetsa kugwira nawo ntchito yolalikira za Ufumu.
Tikamamvera abale amene anapatsidwa udindo woyang’anira nkhosa, timakhala ogwirizana ndi Khristu Yesu yemwe ndi Mutu wa mpingo
OYANG’ANIRA ACHIKONDI
57 Timayamikira kwambiri akulu achikhristu okhwima mwauzimu amenewa chifukwa cha ntchito yaikulu imene amagwira komanso chikondi chawo. Tikamamvera oyang’anira amenewa amene anapatsidwa udindo woyang’anira nkhosa, timakhala ogwirizana ndi Khristu Yesu yemwe ndi Mutu wa mpingo. (1 Akor. 16:15-18; Aef. 1:22, 23) Zimenezi zimachititsa kuti mzimu wa Mulungu uzigwira ntchito m’mipingo yonse komanso kuti ntchito yapadziko lonse izichitika mogwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu amanena.—Sal. 119:105.