Kukhulupirika—Pamtengo Wotani?
“Kwa munthu wokhulupirika mudzakhala wokhulupirika.”—SALMO 18:25, “NW.”
1, 2. (a) Kodi kukhulupirika nchiyani, ndipo kodi ndimotani mmene mbali zake zimayambukira miyoyo yathu? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kwabwino kutembenukira kwa Yehova monga Chitsanzo chathu chapadera?
KUKHULUPIRIRA, ntchito, chikondi, thayo, kulabadira. Kodi mawuwa ali nchiyani chofanana? Iwo ali mbali zosiyanasiyana za kukhulupirika. Kukhulupirika ndimkhalidwe wa Mulungu umene umachokera m’kudzipereka kochokera mumtima. Komabe, kwa anthu ambiri lerolino, kukhulupirika nkochepa. Kukhala wokhulupirika kwa mnzanu wa muukwati, kukhala wathayo kwa ziŵalo zokalamba za m’banja, kulabadira kwa wantchito kwa bwana wake—zonsezi zimachitidwa mosasamalitsa ndipo zimapotozedwa kaŵirikaŵiri. Ndipo kodi chimachitika nchiyani patabuka kupikisana kwa zikhulupiriro? Ku Mangalande, posachedwapa, pamene wosunga thumba la chuma anafotokoza nkhani yowona ponena za chuma cha kampani yake kwa oyang’anira msonkho, iye anachotsedwa pantchito.
2 Nkopepuka kulankhula za kukhulupirika, koma kukhulupirika kowona kuyenera kuchilikizidwa ndi ntchito imene simakupotoza chifukwa cha kuwopa chinachake. Pokhala anthu opanda ungwiro, kaŵirikaŵiri ife timalephera kuchita ichi. Chotero nkwabwino kwa ife kulingalira chitsanzo cha munthu amene kukhulupirika kwake sikungakaikiridwe mpang’ono pomwe, Yehova Mulungu iyemwini.
Kukhulupirika Kusonyezedwa Monga Chitsanzo
3. Kodi Yehova wadzitsimikizira kukhala wokhulupirika motani ku chifuno chake chofotokozedwa pa Genesis 3:15?
3 Pamene Adamu anachimwa, Yehova anafotokoza momvekera chifuno chake cha kuwombola banja la anthu lomwe linali lisanabadwebe. Maziko a kachitidweka anali kukonda kwake anthu olengedwawo. (Yohane 3:16) M’kupita kwanthaŵi, Yesu Kristu, mbewu ya lonjezo lonenedweratu pa Genesis 3:15, anatsimikizira kukhala nsembe ya dipo, ndipo kukakhala kosalingalirika kuti Yehova apotoze chifuno chake chofotokozedwachi. Mwa kuvomereza nsembe ya Yesu, chikhulupiriro chathu sichidzagwiritsidwa mwala.—Aroma 9:33.
4. Kodi Yehova anadzitsimikizira kukhala wokhulupirika motani kwa Yesu, ndipo ndi chotulukapo chotani?
4 Kukhulupirika kwa Yehova kwa Yesu kunamlimbitsa Mwanayo kwakukulukulu pamene anali padziko lapansi. Yesu anadziŵa kuti anafunikira kuyang’anizana ndi imfa, ndipo molimba mtima anasankha kukhala wokhulupirika kwa Mulungu wake kufikira mapeto. Chidziŵitso chokwanira cha kukhalapo kwake asanakhale munthu chinavumbulidwa kwa iye pa kubatizidwa kwake ndi kudzozedwa ndi mzimu woyera. Pa usiku wa kuperekedwa kwake, iye anapemphera kuti abwezeredwe kwa Atate wake wakumwamba, ku ‘ulemerero umene anali nawo ndi Yehova lisanakhale dziko lapansi.’ (Yohane 17:5) Kodi ichi chikatheka motani? Kunali kokha mwa kusamsiya Yehova Mwana wake wokhulupirikayo m’manda kuti akumane ndi chivundi. Yehova anamuukitsa kwa akufa kukhala munthu wosafa, motero kukwaniritsa mokhulupirika lonjezo laulosi lolembedwa pa Salmo 16:10 ili: “Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda.”—Machitidwe 2:24-31; 13:35; Chibvumbulutso 1:18.
5. Kodi ndi ntchito zina za kukhulupirika ziti zimene zimagwirizana ndi malonjezo a Yehova kwa Yesu?
5 Ataukitsidwa, Yesu mofananamo anadziŵa kuti akadalira pamawu a Yehova a ‘kuika adani ake popondapo mapazi ake.’ (Salmo 110:1) Nthaŵiyi inafika mu 1914, pamapeto a “nthaŵi zoikidwiratu za mitundu,” ndi kukhazikitsidwa kwa Ufumu m’mwamba. Kutsikira kwa Yesu kolonjezedwa kunka kwa adani akewo kunayamba mwa kupitikitsa Satana ndi ziŵanda zake kumwamba. Kudzamalizidwa pamene awa aikidwa kuphompho kwa zaka chikwi ndi pamene ‘mafumu a dziko, ndi magulu a nkhondo awo’ adzawonongedwa.—Luka 21:24, NW; Chibvumbulutso 12:7-12; 19:19; 20:1-3.
6. Kodi ndichiyembekezo chotsimikizirika chotani chimene Mulungu akutipatsa, ndipo kodi tingasonyeze kuti tikuchiyamikira motani?
6 Wamasalmo anachonderera kuti: ‘Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo iye adzakukweza kuti ulandire dziko.’ (Salmo 37:34) Ife tingakhale achidaliro kuti Yehova adzapitirizabe kusunga mawu ake, ndipo adzapulumutsa amuna, akazi, ndi ana ‘osunga njira yake’ kufikira kumapeto. Mawuwa m’Chihebri choyambirira amafotokoza lingaliro la kukhala ponse paŵiri wakhama ndi wokhulupirika potumikira Yehova. Chotero, ino sinthaŵi ya kukhala wofooka kapena kuleka mwaŵi wa utumiki woperekedwa kwa ife. Ino ndinthaŵi ya kudzipereka ife eni muutumiki wokhulupirika wa Mulungu wathu ndi Ufumu wake. (Yesaya 35:3, 4) Pali zitsanzo zabwino zambiri zotilimbikitsa. Tiyeni tilingalire zina za izo.
Makolo Akalekale Asonyeza Kukhulupirika
7, 8. (a) Kodi ndi malo antchito otani amene Yehova anafutukula kwa Nowa ndi banja lake? (b) Kodi ndimotani mmene banja la Nowa linatsimikizira kukhala loyenerera kutetezeredwa ndi Mulungu pa chigumula cha dziko lonse?
7 Pamene Yehova anapanga chifuno cha kuwononga chitaganya cha anthu ochimwa ndi chigumula cha madzi, iye anapangana pangano ndi mutu wa banja la kalekalelo Nowa kaamba ka kupulumutsa banja lake ndi kupitirizidwa kwa moyo padziko lino lapansi. (Genesis 6:18) Nowa anali woyamikira chiyembekezo cha chilikizo laumulungu, koma iye ndi banja lake anafunikira kutsimikizira kukhala okuyenerera. Motani? Mwa kuchita chimene Yehova anawalamulira. Choyamba iwo anayang’anizana ndi ntchito yaikulu yomanga chingalawa. Pamene chinamalizidwa, Nowa anafunikira kuchidzaza ndi nyama zamitundu yosiyanasiyana ndi zakudya zokwanira kuzichilikiza kwa nyengo yaitali. Koma sizinali zokhazo. M’nthaŵi yaitali ya kukonzekerako, Nowa ankachita zomwe ankatha m’ntchito yosayerekezeka yolalikira, kuchenjeza za chiweruzo chaumulungu chomadzacho.—Genesis, mitu 6 ndi 7; 2 Petro 2:5.
8 Baibulo limatisimbira kuti ‘Anachita Nowa, monga mwa zonse anamlamulira iye Mulungu, momwemo anachita.’ (Genesis 6:22; 7:5) Nowa ndi banja lake anatsimikizira kukhala okhulupirika m’kukwaniritsa ntchito zawo. Mzimu wawo wa kudzipereka nsembe unatanthauza kuti nthaŵi yawo inatheredwa mopindulitsa, koma ntchitoyo inalitu yolimba ndipo kulalikira kunali kovutadi. Mwa kusabala kwawo ana Chigumula chisanadze, ana amuna a Nowa ndi akazi awo anathandizidwa kusumika maganizo pantchito yomwe anali nayo ndi kugwirizanitsa ntchito zawo. Tsoka la Chigumulalo linabweretsa mapeto olungama ku dziko loipa. Nowa yekha, ndi mkazi wake, ndi ana awo atatu ndi apongozi awo atatu ngomwe anapulumuka. Tingakhaletu osangalala kuti awa anali okhulupirika kwa Mulungu ndi zitsogozo zake, pakuti aliyense wa ife ndimwana weniweni wa Nowa kupyolera mwa Semu, Hamu, kapena Yafeti.—Genesis 5:32; 1 Petro 3:20.
9. (a) Kodi chiyeso cha Yehova pa Abrahamu chinali bwanji chiyeso cha kukhulupirika kwake? (b) Kodi Isake anakusonyeza bwanji kukhulupirika m’chimenechi?
9 Pamene Abrahamu anakonzekera kupereka Isake monga nsembe, iye ankamvera mokhulupirika malamulo a Yehova. Ha ichi chinali chiyeso chotani nanga cha kukhulupirika kwake! Komabe, Yehova anagwira dzanja la Abrahamu, naati: “Tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.” Komabe, tingachitetu bwino kulingalira chomwe chinatsogolera ku ichi. Paulendo wa masiku atatu wonka ku Phiri la Moriya, Abrahamu analidi ndi nthaŵi yokwanira kusanthula ndi kusintha maganizo ake. Nanga bwanji ponena za Isake, amene ananyamula nkhuni za nsembeyo ndi amene anadzivomereza yekha kumangidwa manja ndi miyendo? Iye sanaphunthwe m’kudalira atate wake, Abrahamu, ndipotu sanakaikire mbali imene anaichita, chinkana kuti njira ya kukhulupirika kwake ikadamuphetsa.—Genesis 22:1-18; Ahebri 11:17.
Kukhulupirika Kwachikristu
10, 11. Kodi Akristu oyambirira amapereka zitsanzo zotani za kukhulupirika?
10 Yehova nthaŵi zonse wachita ndi kukhulupirika kowonadi. Paulo anachonderera kuti: “Khalani akutsanza a Mulungu.” (Aefeso 5:1, 2) Akristu anayenera kuvomereza monga mmene anachitira makolo akale. Akristu oyambirira anakhazikitsa zitsanzo zabwino m’kulambira kokhulupirika, monga mmene chokumana nacho chomwe chikutsatira pansipa chikusonyezera.
11 Mfumu Yachiroma Constantius I, bambo wa Mfumu Constantine, mwachiwonekere analemekezadi atsatiri a Yesu Kristu. Kuti ayese kukhulupirika kwa Akristu okhala pa nyumba yake yachifumu, iye anawauza iwo kuti angapitirize kumutumikira pokhapo ngati atavomereza kupereka nsembe ku mafano. Iwo anauzidwa kuti, kukana kukatsogolera ku kuwathamangitsa ndi chilango chochokera kwa iye. Ndi chenjerero lokhwekali, Constantius anafuna kudziŵa omwe sakatha konse kupotoza kukhulupirika kwawo. Anthu omwe anatsimikizira kukhala okhulupirika kwa Mulungu ndi malamulo ake amakhalidwe abwino anasungidwabe kutumikira mfumuyo, ena a awa anakhaladi aphungu odalirika. Osakhulupirira malamulo a Mulungu anathamangitsidwa mochititsa manyazi.
12. Kodi ndimotani mmene oyang’anira Achikristu angasonyezere kukhulupirika, ndipo kodi nchifukwa ninji ichi chiri chofunika kaamba ka ubwino wa mpingo?
12 Chinkana kuti kukhulupirika kuyenera kuzindikiritsa miyoyo ya Akristu onse, iko kwatchulidwanso mwapadera pa Tito 1:8 pandandanda ya mikhalidwe yoyenerera mwamuna kuti akhale woyang’anira Wachikristu. William Barclay akuti hoʹsi·os, liwu Lachigriki lomwe pano latembenuzidwa kukhala “chikhulupiriro,” limafotokoza “mwamuna amene amamvera malamulo osatha omwe analipo ndipo adakhalapo lisanapangidwe lamulo lirilonse la munthu.” Nkofunika kuti akulu atenge kaimidwe kokhulupirika kotereka ka kumvera malamulo a Mulungu. Chitsanzo chabwinochi chidzathandiza mpingo kukula ndi kukhala wolimba mokwanira kuyang’anizana ndi ziyeso ndi zitsenderezo zonse zomwe zingawuwopseze monga gulu kapena chirichonse cha ziŵalo zake pachokha. (1 Petro 5:3) Akulu oikidwa ali ndi thayo lalikulu pa nkhosa kwakuti sakayenera konse kupotoza kukhulupirika kwawo kwa Yehova, popeza kuti mpingo walangizidwa ‘kutsanza chikhulupiriro chawo.’—Ahebri 13:7.
Kukhulupirika—Pamtengo Wotani?
13. Kodi chikutanthauzidwa nchiyani ndi mwambi wakuti “Anthu onse ali ndi mtengo wawo,” ndipo kodi nzitsanzo ziti zomwe zikuchitira umboni ichi?
13 Mwambi woimbidwira Bwana Robert Walpole, nduna yaikulu ya m’zaka za zana la 18 ya boma la Briteni umati “Anthu onse ali ndi mtengo wawo.” Iwo umaika mofupikira nsonga yakuti m’mbiri yonse yakale zikhulupiriro kaŵirikaŵiri zinasinthanitsidwa ndi phindu ladyera. Tangolingalirani mtembenuzi wa Baibulo wotchedwa William Tyndale, amene molakwika anavomereza Henry Phillips kukhala bwenzi lokhulupirika. Mosakhulupirika mu 1535 Phillips anampereka Tyndale kwa adani ake, ichi chinatsogolera Tyndale kuikidwa m’ndende mofulumira ndi kuphedwa mosayembekezereka. Katswiri wa mbiri yakale wina anati Phillips, yemwe mwinamwake anali mtifitifi kaya wa mfumu Yachingelezi kapena Akatolika Achingelezi, “anapatsidwadi malipiro abwino kaamba ka ntchito yake ya Uyudase.” Ndithudi, katswiri wa mbiri yakaleyo ankalozera kwa Yudase Isikariote, amene analandira ndalama zasiliva 30 monga mtengo wa kuperekera Yesu Kristu. Komabe, m’zitsanzozi sitiyenera kulingalira kuti, “mtengo” wa kukhulupirika kwa munthu umakhala ndalama nthaŵi zonse. Sitero.
14. Kodi kukhulupirika kwa Yosefe kwa Yehova kunayesedwa motani, ndipo ndi chotulukapo chotani?
14 Pamene mkazi wa Potifara ananonomera Yosefe kuti “agone [naye],” kukhulupirika kwake kwa Yehova kunaikidwa pa chiyeso. Kodi iye adakachitanji? Maganizo ake pokhala kale omvetsetsa malamulo amakhalidwe abwino oloŵetsedwamo, Yosefe anathawa natuluka m’nyumbamo, ali wotsimikiza kuti sakatha konse ‘kuchita cholakwa chachikulu ichi ndi kuchimwira Mulungu.’ Chikhumbo cha chilakolako cha kugonana sichinalake kukhulupirika kwa Yosefe kwa Mulungu wake, Yehova.—Genesis 39:7-9.
15. Kodi Abisalomu anachisonyeza motani chikhulupiriro, ndi chotulukapo chotani?
15 Komabe, palitu ngozi zina; kulakalaka kungadodometse kukhulupirika. Ichi nchimene chinasonkhezera Abisalomu kugalukira atate wake, Mfumu Davide. Mwa kuchita machenjera ndi chiwembu, Abisalomu anafuna kukondweretsa anthu. Pomalizira pake, iye anapanga gulu lankhondo kukayang’anizana ndi achilikizi okhulupirika a atate wake. Kuphedwa kwake ndi Yoabu kunathetsa kusakhulupirika kwa Abisalomu kwa atate wake, Davide, koma ha ndi mtengo wotani nanga wolipira kaamba ka kuyesera kugwetsa makonzedwe ateokratiki!—2 Samueli 15:1-12; 18:6-17.
Kukhulupirika Kumene Kulibe Mtengo
16. Kodi nchiyani chimene 2 Akorinto 11:3 akuvumbula ponena za zolinga za Satana?
16 Chinkana kuti Satana amati munthu aliyense ali ndi mtengo wake, ndipo ichi chinakhaladi tero kwa Abisalomu, sichinachitikepodi tero kwa Yosefe, ndipotu sichinakhalepodi tero kwa alambiri okhulupirika a Yehova. Komabe, Satana adzatitambika mphatso iriyonse kutipangitsa kuswa kukhulupirika kwathu kwa Mlengi wathu. Mtumwi Paulo anafotokoza kuwopa kwake kuti ‘pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjera kwake,’ malingaliro athu angaipitsidwe, kutitsogolera kupotoza kukhulupirika kwathu kwa Yehova ndi kulambiridwa kwake.—2 Akorinto 11:3.
17. Kodi ena asinthanitsa mwaŵi wosagulika ndi ndalama wautumiki ndi chiyani?
17 Nkoyenerera kuti tidzifunse kuti: ‘Kodi pali mtengo uliwonse umene ndingavomereze kusinthanitsa mwaŵi wanga wa kulambira Mlengi wanga mokhulupirika?’ Nkomvetsa chisoni kuti, mosiyana ndi Yosefe, anthu ena amene anali atumiki odzipereka a Yehova anavomereza mtengo waung’ono kwenikweni kusinthanitsa ndi ichi. Ngakhale akulu ena asinthanitsa mwaŵi wawo wa utumiki wopatulika wosagulika ndi ndalama ndi chisangalalo chosakhalitsa cha zosangulutsa za chilakolako cha chisembwere. Kaya akhale akulu kapena ayi, anthu ambiri amene achita ichi awonongeredwa umodzi wa banja lawo kotheratu, chikondi ndi ulemu wa mpingo, ndi kuvomerezedwa kwa Yehova—Yemwe angaperekedi nyonga ya kusungabe kukhulupirika ndi kutsutsa chiyeso chirichonse chochokera kwa Satana.—Yesaya 12:2; Afilipi 4:13.
18. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kulabadira chenjezo la pa 1 Timoteo 6:9, 10?
18 Ena, otsimikizira ndi chikhumbo cha kupeza zolondola zakudziko, athadi “kudzipyoza ndi zowawa zambiri,” mosasamala kanthu za chenjezo lomvekera la Baibulo. (1 Timoteo 6:9, 10) Dema, Mkristu wotchulidwa ndi Paulo, mlembali ananyalanyaza, kwakanthaŵi kapena kokhalira. (2 Timoteo 4:10) Kukhulupirika kwa Yehova sikungapotozedwe popanda zotulukapo za ngozi. ‘Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.’—Agalatiya 6:7.
19, 20. (a) Kodi ndiziti zimene ziri ngozi zina zogwirizana ndi kupenyerera wailesi ya kanema mopambanitsa? (b) Kodi nchitsanzo chiti chimene banja lina la Mboni lakhazikitsa?
19 Nthaŵi zina mtengo wosinthanitsirawo umabwera m’njira ya machenjera kwenikweni. Mwachitsanzo, lipoti lochokera ku United States likuti mabanja ambiri amathera pafupifupi theka la maola awo ocheza panyumba kukhala akupenyerera wailesi ya kanema, akumamwereketsa achichepere kwenikweni. Ngati Mkristu kwakukulukulu anadyetsa maganizo ake pa wailesi ya kanema, yodzala ndi kugonana kwake ndi chiwawa, iye mosataya nthaŵi akadodometsa malamulo ake amakhalidwe abwino Achikristu. Ichi chikamtsogolera mopepuka kukhala wosakhulupirika, ndikutalikira kwa Yehova. Mayanjano oipawa amaipsyadi makhalidwe okoma. (1 Akorinto 15:33) Sitiyenera kuiwala kuti Malemba amatilangiza kupeza nthaŵi ya kuphunzira ndi kusinkhasinkha pa Mawu a Yehova. Kodi nthaŵi yotalikira yotheredwa tikupuma ndikuyang’ana dwii pa wailesi ya kanema nchinthu chosinthanitsira chabwinopo cha nthaŵi imene ikadatheredwa tikufunafuna chidziŵitso chotsogolera ku moyo wosatha monga alambiri okhulupirika a Yehova? Anthu ambiri okupatira chidziŵitso cha chowonadi lerolino anafunikira kupanga masinthidwe aakulu m’malingaliro awo pankhaniyi.—1 Timoteo 4:15, 16; 2 Timoteo 2:15.
20 Takashi ndimunthu wa malonda wa ku Japani wokhala ku Mangalande. Iye kaŵirikaŵiri ankathera maola atatu kapena anayi madzulo aliwonse akupenyerera wailesi ya kanema ndi banja lake. Pamene iye ndi mkazi wake anabatizidwa zaka zitatu zapitazo, iye anasankhapo kuti phunziro Labaibulo laumwini ndi labanja likayenera kukhala loyamba. Mwa kuchepetsa nthaŵi yake yopenyerera wailesi ya kanema ku avereji ya mphindi 15 kapena 30 zokha patsiku, iye anatsogolera bwino m’banja. Chinkana kuti Takashi amafunikira kuphunzira akugwiritsira ntchito Mabaibulo aŵiri, limodzi Lachingelezi ndipo linalo Lachijapani, kukula kwake kwauzimu kwakhala kofulumira, ndipo iye tsopano akutumikira monga mtumiki wotumikira mumpingo wogwiritsira ntchito chinenero cha Chingelezi. Mkazi wake ndimpainiya wothandiza. Iye akuti “kuti titetezere uzimu wa anyamata athu achichepere aŵiri, tsiku lirilonse ndimasanthulanso chimene mkazi wanga ndi ine timawalola kupenyerera pa wailesi ya kanema.” Kudzilanga kotereku nkodzetsa mphotho.
21. Kodi timadziŵanji ponena za machenjera a Satana, ndipo kodi tingadzitetezere motani ife eni?
21 Tiyenera kukhala otsimikizira kuti: Satana amazidziŵa zofooka zathu, mwinamwake bwino kwambiri kuposa mmene timazidziŵira ife eni ake. Iye adzafika balamanthu pa chirichonse pamene akuyesera kutipotozetsa kapena kufooketsa kudalira kwathu Yehova. (Yerekezerani ndi Mateyu 4:8, 9.) Nangano, ndimotani mmene tingadzitetezere? Mwakusungabe kudzipereka kwathu nthaŵi zonse ndi mwa kusangalala ndi kukulitsa maluso pamene tikutumikira zosoŵa zauzimu za ena. Monga atumiki okhulupirika a Yehova, tiyenera kukhala otanganitsidwa muutumiki wake ndi kutsogozedwa ndi Mawu ake oyera nthaŵi zonse. Ichi chidzatithandiza m’kusankhapo kwathu kolimba mtima kwakuti palibe mtengo uliwonse umene Satana angapereke umene udzatipatutsa pa kukhulupirika kwathu kwa Mulungu.—Salmo 119:14-16.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi Yehova ndi Yesu asonyeza motani kukhulupirika?
◻ Kodi nziti zimene ziri zitsanzo zina Zabaibulo za kukhulupirika?
◻ Kodi nchiyani chimene Satana angatipatse kapena kuyesera kuchita?
◻ Kodi tingadzilimbitse motani kukhala okhulupirika m’kulambira kwathu Yehova?