-
Kodi Chipulumutso N’chiyani?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
Maganizo olakwika: Lemba la Tito 2:11 limaphunzitsa kuti anthu onse adzapulumuka chifukwa limanena kuti Mulungu ‘akupulumutsa anthu onse.’—Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
Zoona zake: Mawu achigiriki a m’lembali omwe anawamasulira kuti anthu “onse” angatanthauzenso kuti “osiyanasiyana.”d Choncho lemba la Tito 2:11 limatanthauza kuti Mulungu akupulumutsa anthu osiyanasiyana kapena kuti ochokera “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi chinenero chilichonse.”—Chivumbulutso 7:9, 10.
-
-
Kodi Chipulumutso N’chiyani?Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
-
-
d Onani buku lakuti, Vine’s Complete Expository Dictionary of Old and New Testament Words. Mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti “onse” ndi ofanana ndi amene anamasuliridwa kuti “zamtundu uliwonse” palemba la Mateyu 5:11. Palembali Yesu anauza otsatira ake kuti anthu adzakunenerani “zoipa zamtundu uliwonse.”—Baibulo la International Standard Version.
-