‘Kudandaulira mwa Chikondi’
PAFUPIFUPI 60-61 C.E., kapolo wothaŵa anachoka ku Roma nayamba ulendo wa makilomita 1,400 kubwerera kwawo ku Kolose, mzinda wa kum’mwera koma chakumadzulo kwa Asia Minor. Ananyamula uthenga wolembedwa ndi manja wopita kwa mbuye wake, wolembedwa ndi mtumwi Paulo mwiniyo. Lerolino, kalatayo ili mbali ya Baibulo ndipo limatchedwa ndi dzina la wolandirayo, Filemoni.
Kalata yolembedwa kwa Filemoni ili chitsanzo chabwino kwambiri cha kukambitsirana kwaluso, kokopa. Komabe, chofunika koposa nchakuti ili ndi maphunziro ambiri othandiza kwa Akristu lerolino, limodzi ndilo phindu la kudandaulirana mwa chikondi Chachikristu. Tiyeni tipende mosamalitsa kalata yaifupi koma yamphamvu imeneyi.
Wothaŵa Abwerera
Filemoni anali Mkristu, chiŵalo chokondedwa kwambiri cha mpingo wa Kolose. (Filemoni 4, 5) Eya, mpingo wakumeneko unagwiritsira ntchito nyumba yake monga malo osonkhanira! (Vesi 2) Ndiponso, Filemoni mwiniyo anadziŵana ndi mtumwi Paulo; mwinamwake mtumwiyo anamthandiza kukhala Mkristu. Zowonadi, Paulo anasonyeza kuti sanalalikire iyemwini ku Kolose. (Akolose 2:1) Komabe, anakhalako zaka ziŵiri ku Efeso, akulalikira kwambiri kotero kuti ‘onse akukhala m’Asiya [yomwe inaphatikizapo Kolose] anamva mawu a Ambuye.’ (Machitidwe 19:10) Mwachidziŵikire Filemoni anali mmodzi wa omvetsera amene anachitapo kanthu.
Mulimonse mmene zingakhalire, mofanana ndi anthu ambiri achuma a nthaŵiyo, Filemoni anali ndi akapolo ake. M’nthaŵi zakale, sinthaŵi zonse kuti ukapolo unali woipa. Pakati pa Ayuda, kudzigulitsa kapena kugulitsidwa kwa ziŵalo za banja muukapolo kunavomerezedwa monga njira yolipirira ngongole. (Levitiko 25:39, 40) The International Standard Bible Encyclopedia ikuthirira ndemanga pa nyengo Yachiroma motere: “Anthu ambiri anadzigulitsa muukapolo kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana, kwakukulukulu kuti akhale ndi moyo wabwino ndi wachisungiko kusiyana nkukhala mfulu, koma waumphaŵi, kuti apeze ntchito zapadera, ndi kukhala ndi malo okwezekako m’chitaganya. . . . Anthu ambiri omwe sanali Aroma anadzigulitsa kwa nzika Zachiroma poyembekezera zinthu zabwino, zolinganizidwa bwino ndi lamulo la Roma, kukhala nzika za Roma pambuyo pa kumasulidwa kwawo.”
Komabe, vuto linabuka pamene mmodzi wa akapolo a Filemoni, mwamuna wotchedwa Onesimo, anamsiya nathaŵira ku Roma, mwinamwake anamberanso ndalama Filemoni kuti alipirire ulendo wakewo. (Vesi 18) Ku Roma, Onesimo anakumana ndi mtumwi Paulo, yemwe anali wandende kumeneko.
Kapolo yemwe ‘kale sanapindula’ amene anathaŵa utumiki tsopano anakhala Mkristu. Anadzipereka kwa Paulo ndipo anachita mautumiki opindulitsa kwa mtumwi woikidwa m’ndendeyo. Nkosadabwitsa kuti Onesimo anapeza malo mu ‘mtima weniweni’ wa Paulo ndipo anakhala “mbale wokondedwa” kwa Paulo!—Mavesi 11, 12, 16.
Mtumwi Paulo akadakonda kuti Onesimo akhale naye, koma Filemoni anali ndi kuyenera kwalamulo monga mbuye wa Onesimo. Chotero Onesimo anakakamizika kubwerera ku utumiki wa mbuye wake walamulo. Pamenepo, kodi Filemoni akamulandira motani? Kodi akagwiritsira ntchito kuyenera kwake kwakupereka chilango chachikulu mwaukali? Kodi akakaikira kuwona mtima kwa Onesimo kudzitcha Mkristu mnzake?
Kuthetsa Milandu Mwachikondi
Paulo anasonkhezeredwa kulembera Filemoni ponena za Onesimo. Iye anailemba yekha kalatayo, osagwiritsira ntchito mlembi monga mwa chizoloŵezi chake. (Vesi 19) Tatengani mphindi zoŵerengeka kuŵerenga kalata yonse yachidule yopita kwa Filemoni. Mudzawona kuti pambuyo podzidziŵikitsa ndi kupereka mafuno abwino kwa Filemoni ndi banja lake a ‘chisomo kwa inu ndi mtendere,’ Paulo anayamikira Filemoni chifukwa cha ‘chikondi chake ndi chikhulupiriro ali nacho kulinga kwa Ambuye Yesu, ndi kwa oyera mtima onse.’—Mavesi 1-7.
Paulo akanakhoza kugwiritsira ntchito udindo wake monga mtumwi ndi ‘kulamula Filemoni kuchita zoyenera,’ koma mmalomwake Paulo ‘anadandaulira mwa chikondi.’ Anatsimikizira kuti Onesimo anakhaladi mbale Wachikristu, amene anali wothandiza kwa Paulo. Mtumwiyo anavomereza kuti: ‘Ndikadafuna ine kumsunga [Onesimo] akhale nane, kuti m’malo mwako akadanditumikira ine m’ndende za uthenga wabwino: koma,’ anapitiriza motero Paulo, ‘wopanda kudziŵa mtima wako sindifuna kuchita kanthu; kuti ubwino wako usakhale monga mokakamiza, komatu mwaufulu.’—Mavesi 8-14.
Chotero mtumwi Paulo analimbikitsa Filemoni kulandira kapolo wake wakale monga mbale. “Umlandire iye monga ine mwini,” analemba tero Paulo. Sizikutanthauza kuti Onesimo akamasulidwa ku ukapolo. Paulo sanayese kusintha kakhalidwe kanthaŵi yake. (Yerekezerani ndi Aefeso 6:9; Akolose 4:1; 1 Timoteo 6:2.) Komabe, unansi wa kapolo ndi mbuyewo mosakaikira ukayambukiridwa ndi chomangira Chachikristu chomwe tsopano chiri pakati pa Onesimo ndi Filemoni. Filemoni akawona Onesimo kukhala “woposa kapolo, mbale wokondedwa.”—Mavesi 15-17.
Komabe, bwanji nanga za ngongole zimene Onesimo anali nazo, mwinamwake chifukwa chakuba? Apanso, Paulo anagwiritsira ntchito ubwenzi wake ndi Filemoni, nati: ‘Ngati anakulakwira kanthu, kapena wakongola kanthu, undiŵerengere ine kameneko.’ Paulo anasonyeza chidaliro kuti Filemoni akasonyeza mzimu wakukhululuka, kupyola pa zinthu zimene Paulo anapempha. Popeza kuti Paulo anayembekezera kumasulidwa msanga, anapanga makonzedwe akusangalala ndi kuchereza kwa Filemoni mtsogolo. Atapereka moni wowonjezereka ndi kufunira Filemoni ‘chisomo cha Ambuye Yesu Kristu,’ Paulo anamaliza kalata yake.—Mavesi 18-25.
Maphunziro kwa Akristu Lerolino
Bukhu la Filemoni nlodzaza ndi maphunziro othandiza kwa Akristu lerolino. Choyamba, limatikumbutsa kufunika kwakukhululuka, ngakhale pamene wokhulupirira mnzathu atilakwira kwakukulu. Yesu Kristu anati: ‘Ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo adzakhululukira inunso Atate wanu wa kumwamba.’—Mateyu 6:14.
Amene ali ndi mathayo mumpingo Wachikristu lerolino angapindule kwambiri ndi bukhu la Filemoni. Nkosangalatsa kuwona kuti Paulo sanagwiritsire ntchito udindo wake monga mtumwi kulamula Filemoni kuchita zoyenera. Ndiponso, Paulo sanalamule kuti Onesimo aloledwe kukhala ku Roma kutumikira Paulo. Paulo analemekeza kuyenera kwa katundu wa ena. Anazindikiranso kuti pamene kuli kwakuti njira yaukumu ikanachititsa kugonjera, kukakhala bwino kuti Filemoni achite mochokera mumtima wake. Anapereka chidandaulo mwa chikondi kuti alandire yankho lochokera kumtima.
Chotero, akulu Achikristu lerolino sayenera konse ‘kuchita ufumu pa iwo a udindo wawo’ mwakugwiritsira ntchito molakwa mphamvu zawo kapena mwakuchita ndi nkhosa m’njira yankhalwe, yolamulira. (1 Petro 5:1-3) Yesu anati: ‘Mudziŵa kuti mafumu a anthu amadziyesa okha ambuye awo, ndipo akulu awo amachita ufumu pa iwo. Sikudzakhala chomwecho kwa inu ayi.’ (Mateyu 20:25, 26) Nthaŵi zambiri oyang’anira amapeza kuti ziŵalo za gulu zimalabadira kwenikweni kudandaulira kwachikondi mmalo mwa kulamula. Ochita tondovi amayamikira oyang’anira achikondi amene amatenga nthaŵi yakumvetsera mavuto awo ndikupereka uphungu wothandiza.
Kalata ya Paulo ikukumbutsanso akulu phindu la kuyamikira ndi luso. Akuiyamba mwakuvomereza kuti ‘mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa’ Filemoni. (Vesi 7) Mosakaikira chiyamikiro chowona mtima chimenechi chinapangitsa Filemoni kuvomereza. Mofananamo lerolino, uphungu kapena chitsogozo chingakoleretsedwe ndi chiyamikiro chotentha, chowona mtima. Ndipo uphungu woterowo suyenera kukhala wankhadzulira kapena wopanda luso, koma ‘wokoleretsedwa’ bwino kuti ulandiridwe ndi womvetserayo.—Akolose 4:6.
Mtumwi Paulo anasonyezanso chidaliro kuti Filemoni akachita chinthu choyenera, naati: ‘Pokhulupirira kumvera kwako ndikulembera iwe, podziŵa kuti udzachitanso koposa chimene ndinena.’ (Vesi 21) Akulu, kodi mumasonyeza chidaliro chofananacho mwa Akristu anzanu? Kodi zimenezi sizimawathandiza kuchita choyenera?
Mosangalatsa, kaŵirikaŵiri makolo amapeza kuti kusonyeza chidaliro mwa ana awo kumakhalanso ndi chiyambukiro chabwino. Mwakuzindikira phindu la kufunitsitsa kumvera—chikhumbo chakuchita zoposa zofunikira—makolo amapatsa ana awo ulemu wakutiwakuti. Ngati nkotheka, malamulo kapena mapempho a makolo ayenera kuchitidwa mokoma mtima, ndi liwu lachikondi. Chisomo chiyenera kusonyezedwa ndi kupereka zifukwa. Makolo ayenera kuyamikira bwino ana awo pamene chiyamikiro choterocho chifunikira ndipo ayenera kupeŵa kusuliza mopambanitsa, makamaka pa anthu.
Mofananamo, amuna okwatira ayenera kusonyeza mikhalidwe ya kulingalira ndi chifundo, mwakukonzekera kutamanda akazi awo. Izi zimapangitsa kungonjera kwa mkazi kukhala kosangalatsa ndi magwero a chitsitsimulo ndi chimwemwe!—Miyambo 31:28; Aefeso 5:28.
Sitidziŵa mmene Filemoni anayankhira kalata ya Paulo. Komabe, sitingalingalire kuti chidaliro cha Paulo mwa iye chinali pachabe. Akulu, makolo, ndi amuna Achikristu lerolino mofananamo apezetu chipambano m’zochita zawo, osati mwakukakamiza, kulamulira, kapena kunyengerera, koma mwa ‘kudandaulira mwa chikondi.’
[Chithunzi patsamba 23]
Mmalo mogwiritsira ntchito ulamuliro wake monga mtumwi, Paulo anadandaulira Filemoni mwa chikondi Chachikristu