Mutu 13
“Mawu a Mulungu Ngamoyo”
M’mutu wapitawu, tawona kuti uphungu wa Baibulo ungathe kutithandiza kuthetsa zovuta ndi kupeŵa zolakwa. Nzeru yosafwifwa yowoneka muuphungu wa Baibulo iri umboni wamphamvu wa kuuziridwa. Baibulo lenilenilo limati: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu ndipo lipindulitsa pakuphunzitsa, pakudzudzula, pakuwongola zinthu, pa kulanga m’chilungamo.” (2 Timoteo 3:16, “NW”) Koma Baibulo limachita zochuluka koposa ndi kutipatsa uphungu wanzeru. Monga Mawu a Mulungu, iro kwenikweni limasintha anthu.
1-3. (a) Kodi Baibulo limagogomezera motani masinthidwe aumunthu? (b) Kodi ndichokumana nacho chotani chimene chimasonyeza mphamvu ya Baibulo ya kusintha maumunthu?
KODI Baibulo lingasinthedi anthu? Inde, lingathe kusintha ngakhale umunthu wawo. Lingalirani uphungu uwu wolembedwa m’Baibulo: “Muyenera kuvula umunthu wakale umene umagwirizana ndi njira yanu ya khalidwe yakale ndi imene ikuipitsidwa mogwirizana ndi zikhumbo zachinyengo; koma . . . muyenera kupangidwa kukhala atsopano m’mphamvu yosonkhezera maganizo anu, ndipo muyenera kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi kukhulupirika.”—Aefeso 4:22-24, NW.
2 Kodi nkothekera kwenikweni kuvala umunthu watsopano? Inde, nkothekera! Kunena zowona, kukhala Mkristu nthaŵi zina kumaloŵetsamo masinthidwe aakulu muumunthu. (1 Akorinto 6:9-11) Mwachitsanzo, mnyamata wina mu South America anasiyidwa wamasiye pausinkhu wa zaka zisanu ndi zinayi. Pokula wopanda chitsogozo cha makolo, iye anakulitsa mavuto aakulu aumunthu. Iye akusimba kuti: “Pofika panthaŵi yausinkhu wa zaka 18, ndinali womwerekera kotheratu kumankhwala oledzeretsa ndipo ndinali nditawonongera kale nthaŵi ina m’ndende kaamba ka kuba kuti ndichirikize chizoloŵezi chimenechi.” Komabe, adzakhali ake, anali mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo potsirizira pake anali wokhoza kumthandiza.
3 Iye akufotokoza kuti: “Adzakhali angawo anayamba kuphunzira nane Baibulo, ndipo pambuyo pa miyezi isanu ndi iŵiri ndinali wokhoza kuleka chizoloŵezi cha mankhwala oledzeretsa.” Iye analekananso ndi mabwenzi ake apapitapo ndipo anapeza mabwenzi atsopano pakati pa Mboni za Yehova. Iye akupitiriza kunena kuti: “Mabwenzi atsopano ameneŵa, limodzi ndi phunziro langa la nthaŵi zonse la Baibulo, zinanditheketsa kupanga kupita patsogolo ndipo potsirizira pake kupereka moyo wanga kukutumikira Mulungu.” Inde, womwerekera ndi mankhwala oledzeretsa wapapitapo ameneyu ndi mbala anakhala Mkristu wokangalika, ndipo kusintha kwakukulu kumeneku kunachitidwa kupyolera mwa mphamvu ya Baibulo. Ndithudi, monga momwe mtumwi Paulo akunenera, “Mawu a Mulungu ngamoyo ndipo amapereka mphamvu.”—Ahebri 4:12, NW.
Anasintha Kupyolera mwa Chidziŵitso
4, 5. Malinga ndi kunena kwa Akolose 3:8-10, kodi nchiyani chimene chikufunika kuti tikulitse umunthu watsopano?
4 Kodi ndimotani mmene Baibulo limasinthira anthu? Yankho likupezeka m’ndime za Baibulo: “Zichotseni zonse kwa inu, mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, kutukwana, ndi kulankhula kopanda pake kotuluka mkamwa mwanu. Musanamizana wina ndi mnzake. Vulani umunthu wakale limodzi ndi machitachita ake, ndipo dzivekeni umunthu watsopano, umene kupyolera mwa chidziŵitso cholongosoka ukupangidwa kukhala watsopano mogwirizana ndi chifanizo cha Uyo amene anaulenga.”—Akolose 3:8-10, NW.
5 Wonani mbali yofunika imene ikuchitidwa ndi chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo. Baibulo limafotokoza mikhalidwe imene tifunikira kuichotsa ndi imene tiyenera kuikulitsa. Chidziŵitso chimenecho mwa icho chokha chingathe kukhala chiyambukiro champhamvu, monga momwe mnyamata wina kummwera kwa Ulaya anawonera. Iye anali ndi vuto lenileni: anali wopsa mtima kwachiwawa. Pamene anali kukula, iye kaŵirikaŵiri anali kumangomenyana ndi anzake, ndipo monga chotulutsira chiwawa chake, anayamba maseŵera a nkhonya; koma iye sanali kuthabe kuletsa mkhalidwe wake wachiwawa. Pamene anali m’gulu la ankhondo, iye analoŵa m’vuto chifukwa cha kumenya msilikali wankhondo mnzake. Atachoka kugulu la ankhondo, iye anakwatira komano anali kumenya mkazi wake. Mumkangano wina wabanja, iye anafikira ngakhale pakumenya atate wake, akumawagwetsera pansi. Mnyamata wopsa mtima, wachiwawadi!
6, 7. Kodi ndimotani mmene chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo chinathandizira mnyamata wina kummwera kwa Ulaya kusintha umunthu wake?
6 Komabe, potsirizira pake, iye anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo anamva uphungu wonga ngati wotsatirapowu: “Usabwezere choipa ndi choipa. . . . Ngati nkotheka, monga mmene zingakuthekereni, khalani mumtendere ndi anthu onse. Musabwezere, okondedwa, koma musapatse mkwiyo malo.” (Aroma 12:17-19, NW) Umenewo unamthandiza kuzindikira mmene chofooka chake cha mkhalidwe wa kupsa mtima kwambiricho chinaliri choipa. Iye analeka maseŵera ankhonya, amene iye anawazindikira kuti anali osagwirizana ndi umunthu wa mtendere Wachikristu. Koma iye anali akali ndi nkhondobe yaikulu ndi mkhalidwe wake wachiwawa.
7 Komabe, iye anathandizidwa, ndi chidziŵitso chake chowonjezereka cha malamulo a Baibulo a makhalidwe abwino. Chimenechi chinayeretsa chikumbumtima chake, chimene nachonso chinachita monga cholimbanira ndi kukhala kwake wamtima wapachala. Panthaŵi ina, atangopanga kupita patsogolo m’phunziro lake la Baibulo, mlendo wina anapsa mtima namkalipira. Mnyamatayo anamva kupsa mtima kwanthaŵi zonse mkati mwake. Ndiyeno, anawona mphamvu ina: lingaliro la kuchita manyazi; ndipo limeneli linamletsa kugonjera kumkwiyo wake. Mmalo mwa “kubwezera choipa ndi choipa,” iye analamulira mkwiyo wake. Tsopano, iye ali munthu wosinthidwa, wokhala ndi umunthu watsopano, chithokozo chikuperekedwa kuchidziŵitso cholongosoka chochokera m’Baibulo.
Kufika Pakudziŵa Mulungu
8. (a) Kodi umunthu watsopano ukupangidwa m’chifanizo chayani? (b) Chidziŵitso cholongosoka chimene chimaumba umunthu watsopanowo chiyenera kuphatikizamo chidziŵitso chayani?
8 Zowona, anthu ambiri amadziŵa choyenera kuchichita, koma iwo amagonjera kuzofooka zathupi. Mwachiwonekere, kungokhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha choyenera ndi cholakwa sindiko kokha kumene kuli kofunika. Kanthu kenanso kanathandiza anthu aŵiri amene afotokozedwa pamwambapo kusintha. Kodi iko kanali chiyani? Ndime imene yatchulidwa poyambirirapoyo imati: “Dzivekeni umunthu watsopano, umene kupyolera mwa chidziŵitso cholongosoka ukupangidwa kukhala watsopano mogwirizana ndi chifanizo cha Uyo amene anaulenga.” (Akolose 3:10, NW) Wonani kuti monga momwedi Adamu poyambirirapo anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu, chotero umunthu watsopano umapangidwa m’chifanizo cha Mulungu. (Genesis 1:26) Chotero chidziŵitso cholongosoka chimene chinathandiza anyamata aŵiri ameneŵa chimaphatikizapo chidziŵitso cha Mulungu. Zimenezi zikutikumbutsa mawu a Yesu akuti: “Ichi chitanthauza moyo wosatha, kulandira kwawo chidziŵitso cha inu, Mulungu wowona yekha, ndi cha uyo amene munamtuma, Yesu Kristu.”—Yohane 17:3, NW.
9. Kodi ndimotani mmene chidziŵitso cha Mulungu chimatithandizira kusintha umunthu wathu?
9 Kodi ndimotani mmene chidziŵitso cha Mulungu chimatithandizira kusintha umunthu wathu? Chimatipatsa ife chisonkhezero cha kutero. Pamene tifika pakudziŵa Mulungu kupyolera mwa phunziro lathu la Baibulo, timaphunzira za mikhalidwe yake yaumulungu ndipo timawona chikondi chimene iye wasonyeza kwa ife. Chimenechi chimatichititsa nafenso kumkonda. (1 Yohane 4:19) Ndiyeno, tingathe kumvera limene Yesu analitcha lamulo loyamba ndi lalikulu kopambana: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndipo ndi maganizo ako onse.” (Mateyu 22:37, NW) Kukonda Mulungu kumatipangitsa ife kufuna kuvala umunthu watsopano umene umamkondweretsa. Kumatipangitsa kukhala ofanana naye kwambiri, ngakhale ngati kutero kungafunikire kupanga kuyesayesa kwamphamvu.
Zofooka Zokhomerezeka Zolimba
10, 11. Kodi ndimotani mmene chidziŵitso cholongosoka chinathandizira mkazi wachichepere wa Kumpoto kwa Amereka kuyamba kusintha umunthu wake?
10 M’zochitika zina, iridi nkhondo. Mkazi wina wachichepere Kumpoto kwa Amereka anafunikira kumenya nkhondo zolimba kuti asinthe. Iye anali mkhole wa kugonedwa mosayenera paubwana, iye anakulira m’banja lachiwawa ndipo potsirizira pake anatembenukira kumankhwala oledzeretsa. Komabe, mankhwala oledzeretsa anali okwera mtengo, chotero iye anadzigulitsa iye mwini monga hule kuti alipirire chizoloŵezicho. Iye anavutitsanso ndi kubera apaulendo ndipo anatsirizira akuwonongera nthaŵi yochuluka ali m’ndende ndi kunyumba zobetchera koposa yokhala panyumba pawo.
11 Pamene Mboni za Yehova zinakumana naye, iye anali ndi mwana wapathengo—pambuyo pa kuchotsa mimba kochuluka. Komabe, iye anakonda zimene anamva kuchokera m’Baibulo ndipo anayamba kuliphunzira. Posapita nthaŵi iye anali kumanga unansi ndi Mulungu ndi kupanga masinthidwe m’moyo wake.
12, 13. Fotokozani mmene chidziŵitso cholongosoka, pamene icho changobzalidwa mwa munthu, chimachitira monga mphamvu yosinthitsa.
12 Komabe, nkhondo yaikulu inali patsogolo pake, chifukwa chakuti umunthu wakalewo unali wokhathamira zolimba. Pachochitika china, anapsa mtima ndi uphungu wokhala ndi cholinga choyenera, anasiya kuphunzira Baibulo, nabwerera kunjira zake zonyansa. Koma iye sakanatha konse kuiŵala chidziŵitso cha Baibulo chimene chinali chitabzalidwa mwa iye, ndipo akuvomereza kuti: “Nthaŵi ndi nthaŵi ndinali kumva kukhala ndi malingaliro a liwongo, ndipo mawu a 2 Petro 2:22 anali kuyendayenda m’maganizo mwanga: ‘Galu akubwerera kumasanzi ake ndi nkhumba imene inasamba ikubwerera kumatope.’”
13 Potsirizira pake, chidziŵitso chimenechi chinamsonkhezera kupanga kuyesayesa kwina kotsimikizirika. Iye akunena kuti: “Ndinayamba kutsegulira khomo Yehova ndi kupempherera kaŵirikaŵiri kaamba ka chithandizo.” Panthaŵi ino, umunthu watsopano unabzalidwa mwamphamvudi kwambiri, ngakhale kuli kwakuti iye anayenerabe kumenya nkhondo zolimba. Panthaŵi ina, m’nyengo ya kufooka, iye anabwereranso kukuledzera ndi chisembwere. Komabe, panthaŵi ino, kulabadira kwake kunasonyeza kuti iye anali kusinthadi. Iye anamva kuipidwa ndi iye mwini ndipo anati: “Ndinapemphera kwambiri ndi kuphunzira.” Potsirizira pake, Mawu a Mulungu anaika mphamvu m’moyo wake kufika pamlingo wakuti iye anakhala Mkristu wokangalika, wokhala ndi moyo woyera, ndi wolemekezeka. Kwazaka zingapo tsopano, iye wakhala munthu wosiyana kotheratu ndi munthu wogwiritsiridwa ntchito molakwa, womwerekera ndi mankhwala oledzeretsa, ndi wauchinyama amene iye anali.
Anthu Osinthidwa ndi Mawu a Mulungu
14, 15. (a) Kodi ndimphamvu yotani yochokera kwa Mulungu imene imagwira ntchito kupyolera m’Baibulo? (b) Kodi ndiiti imene iri ina ya mikhalidwe ya Akristu owona lerolino?
14 Mphamvu imene Baibulo lagwiritsira ntchito m’miyoyo ya anthu odzichepetsa imasonyeza kuti liri loposa bukhu la anthu chabe. Monga Mawu ouziridwa a Mulungu, iro liri ngalande yoyendetseramo kugwira ntchito kwa mzimu wa Mulungu. Mzimu umodzimodziwo umene unatheketsa zozizwitsa zimene Yesu anachita umatithandiza lerolino kulaka mikhalidwe yoipa ndi kukulitsa umunthu Wachikristu. Indedi, mikhalidwe yaikulu imene Akristu afunikira kuikulitsa—chikondi, chisangalalo, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kudekha, ndi kudziletsa—ikutchedwa m’Baibulo kuti “zipatso za mzimu.”—Agalatiya 5:22, 23.
15 Lerolino, mzimu imenewo ukugwira ntchito osati pa anthu oŵerengeka chabe koma pamamiliyoni amene “aphunzitsidwa ndi Yehova” ndipo akusangalala ‘ndi mtendere wochuluka’ wochokera kwa Iye. (Yesaya 54:13) Kodi anthu ameneŵa ndi ayani? Yesu anapereka njira imodzi yowadziŵira, akumati: “Mwa ichi onse adzadziŵa kuti inu muli ophunzira anga, ngati muli nacho chikondi pakati pa inu eni.” (Yohane 13:35, NW) Chikondi Chachikristu chiri chipatso cha mzimu ndipo mbali yaikulu ya umunthu watsopano Wachikristu. Kodi pali kagulu kena kalikonse ka anthu kamene kamasonyeza chikondi m’njira imene Yesu ananenera?
16, 17. Gwirani mawu a ndemanga zina zochokera m’manyuzipepala zimene zimathandiza kudziŵikitsa awo amene ali ‘ophunzitsidwa ndi Yehova’ ndi amene akusangalala ndi ‘mtendere wochuluka.’
16 Chabwino, mvetserani kumawu aŵa ogwidwa kuchokera m’kalata yolembedwera ku New Haven Register, nyuzipepala ya Kumpoto kwa Amereka: “Kaya mwaipidwa kapena kunyansidwa [kupsetsedwa mtima], monga momwe ndiriri ine, ndi kumka kwawo natembenuza anthu, muyenera kusirira kudzipatulira kwawo, kulama kwawo, chitsanzo chawo chapadera cha khalidwe labwino laumunthu ndi moyo wabwino.” Nyuzipepala ya ku Jeremani Münchner Merkur inali kunena za kagulu kamodzimodziko pamene inati: “Iwo ali anthu owona mtima kopambana ndi okhoma misonkho apanthaŵi yake kopambana mu Lipabuliki ya Chitaganya cha [Jeremani]. Kumvera kwawo malamulo kungathe kuwonedwa mmene iwo amayendetsera magalimoto kudzanso paziŵerengero zaupandu.”
17 Kodi manyuzipepala aŵiri ameneŵa anali kunena za ayani? Kagulu kamodzimodziko kamene kanafotokozedwa m’Herald ya ku Buenos Aires, Argentina. Nyuzipepala imeneyi inati: “Mboni za Yehova zatsimikizira m’zaka zonse zapitazo kukhala nzika zogwira ntchito mwamphamvu, zolama maganizo, zosawawanya ndi zowopa Mulungu za mtundu umene mtundu wathu uno mwachiwonekere umazifuna.” Kufufuza zamakhalidwe a anthu ku Zambia kumene kunafalitsidwa mu American Ethnologist kukunena za kagulu kamodzimodziko. Kumati: “Mboni za Yehova zikukhala ndi chipambano chachikulu kwambiri koposa ziŵalo za magulu ena achipembedzo m’kusunga zomangira zokhazikika za ukwati.”
18, 19. Kodi ndimotani mmene Mboni za Yehova mu Italiya ndi South Africa zafotokozedwera?
18 Nyuzipepala yotchedwa La Stampa mu Italiya inali kunenanso za Mboni za Yehova pamene inati: “Izo ziri nzika zokhulupirika kopambana zimene munthu aliyense akafuna: izo sizimapeŵa misonkho kapena kufunafuna kupeŵa malamulo ovuta kaamba ka phindu la iwo eni. Malingaliro a makhalidwe abwino a kukonda mnansi, kukana ulamuliro, kupanda chiwawa ndi kuwona mtima kwa munthu mwini (amene kwa Akristu ochuluka ali ‘malamulo a pa Sande’ abwino kungowalalikira pagome chabe) amaloŵa m’njira yawo ya moyo ‘yatsiku ndi tsiku.’”
19 Profesala wina wa pa yunivesite m’South Africa amene anakumana ndi kusankhidwa mtundu pansi pa malamulo a mafuko a m’dziko limenelo akutcha Mboni za Yehova kuti “anthu ophunzitsidwa ndi miyezo yapamwamba koposa ya Baibulo kukhala osawona kawonekedwe ka khungu.” Pofotokoza zimenezi, iye akuwonjeza kuti: “Aŵa ndiwo anthu amene amawona zimene ena alimo mkati, osati kokha kawonekedwe ka khungu lawo. Mboni za Yehova lerolino zikupanga ubale wowona wa mtundu wa anthu.”
20. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimadziŵika kukhala zosiyana?
20 Mawu ameneŵa akusonyeza kuti pali kagulu ka anthu kamene katsegulira mitima yawo ku Baibulo ndi kamene mzimu wa Mulungu wakhala ukugwirapo ntchito. Kulinso koyenerera kuwona kuti ameneŵa ali anthu amodzimodziwo amene tadziŵikitsa poyambirira paja kukhala akukwaniritsa lamulo la Yesu la kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu padziko lonse. (Mateyu 24:14) Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova ziri zapadera m’njira zimenezi? M’mbali zambiri izo siziri zosiyana ndi anthu ena. Izo ziri ndi zofooka zakuthupi zimodzimodzizo, mavuto a zachuma amodzimodziwo, ndi zosoŵeka zamaziko zimodzimodzizo. Koma monga kagulu, zimakonda Mulungu, zimalingalira Baibulo mwamphamvu, ndipo zimalilola kupereka mphamvu pamiyoyo yawo.
21. Kodi nchiyani chimene chikutsimikiziridwa ndi chenicheni chakuti anthu onga ngati Mboni za Yehova angathe kukhalapo m’dziko lamakono lodzazidwa ndi udani?
21 Mamiliyoni ochuluka a Mboni za Yehova akupezeka m’maiko oposa 200. Izo zimaphatikizapo anthu ochokera m’mafuko onse, zinenero, ndi makhalidwe alionse a anthu olingaliridwa. Komabe izo ziri zogwirizana, zamtendere, ubale wa m’mitundu yonse. Izo ziri nzika zabwino za dziko lirilonse kumene izo zipezeka, koma choyambirira choposa zonse, izo ziri nzika za Ufumu wa Mulungu, ndipo izo zonse ziri zokangalika kwambiri m’kuuza ena mbiri yabwino ya Ufumu umenewo. Kulidi kwapadera kuti m’dziko logaŵanika lino, lodzazidwa ndi udani, kagulu konga ngati Mboni za Yehova kangathe kukhalapo. Chenicheni chakuti izo ziripo ndicho umboni wamphamvu wa chenicheni chakuti mzimu wa Mulungu ukadagwirabe ntchito pakati pa mtundu wa anthu. Ndipo ndiwo umboni wakuti Baibulo liridi ‘lamoyo ndipo limapereka mphamvu.’
[Mawu Otsindika patsamba 177]
Baibulo limasinthadi anthu
[Mawu Otsindika patsamba 181]
Kudziŵa Mulungu kumapangitsa munthuyo kufuna kufanana naye