Pitirizani Kukula M’chidziŵitso
“Wonjezerani pachikhulupiriro chanu . . . chidziŵitso.”—2 PETRO 1:5, NW.
1, 2. (a) Kodi mungaphunzirenji mwakuyang’ana kumwamba? (Aroma 1:20) (b) Kodi munthu wakulitsa chidziŵitso chake kumlingo wotani?
KODI mungaphunzirenji ngati mutuluka pabwalo usiku, ndi kuyang’ana kumwamba kopanda mitambo ndi kuona mwezi woŵala mbee ndi nyenyezi zosaŵerengeka? Mutha kuphunzira kanthu kena ponena za Uyo amene analenga zonsezo.—Salmo 19:1-6; 69:34.
2 Ngati mufuna kuwonjezera chidziŵitso chanu, kodi mungakwere padenga la nyumba yanu ndi kuyang’ana kumwamba? Mwinamwake ayi. Albert Einstein nthaŵi ina anagwiritsira ntchito chitsanzo chimenecho poyesa kumveketsa mfundo yakuti asayansi sanawonjezere kwenikweni chidziŵitso chawo cha chilengedwe chonse ndipo adziŵa zochepa kwambiri ponena za Uyo amene anachilenga.a Mofananamo, Dr. Lewis Thomas analemba kuti: “Chipambano chachikulu koposa cha sayansi m’zaka za mazana ano pamene sayansi yapambana m’kupanga zinthu ndicho kuzindikira kuti ndife ambuli kwambiri; kuti timadziŵa zochepa kwambiri ponena za chilengedwe ndipo timamvetsetsa zocheperapo.”
3. Kodi ndimotani mmene kukulitsa chidziŵitso kumawonjezerera zoŵaŵa?
3 Ngakhale ngati mungathere nthaŵi yanu yonse yotsala ya moyo wanu mukumafunafuna chidziŵitso choterocho, mungangodziŵa zowonjezereka ponena za kufupika kwa moyo wanu ndi kuzindikira bwino lomwe kuti kugwiritsira ntchito chidziŵitso kwa munthu kumachepetsedwa ndi kupanda ungwiro ndi ‘kusawona mtima’ kwa dziko lino. Solomo anamveketsa bwino mfundoyo, analemba kuti: “Pakuti m’nzeru yambiri muli chisoni chambiri; ndi yemwe awonjezera chidziŵitso awonjezera zoŵaŵa.” (Mlaliki 1:15, 18) Inde, kupeza chidziŵitso ndi nzeru popanda kugwirizana kulikonse ndi zifuniro za Mulungu kaŵirikaŵiri kumaloŵetsamo chisoni ndi zoŵaŵa.—Mlaliki 1:13, 14; 12:12; 1 Timoteo 6:20.
4. Kodi nchidziŵitso chotani chimene tiyenera kupeza?
4 Kodi Baibulo limanena kuti sitiyenera kukhala ofuna kukulitsa chidziŵitso chathu? Mwumwi Petro analemba kuti: “Ayi, koma pitirizanibe kukula m’kukoma mtima kwaulere ndi chidziŵitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Kristu. Kwa iye kukhale ulemerero tsopano ndi tsiku lomka muyaya.” (2 Petro 3:18, NW) Tikhoza ndipo tiyenera kuona uphungu umenewo kukhala wogwira ntchito kwa ife, ukumatisonkhezera kukula m’chidziŵitso. Koma kodi nchidziŵitso cha mtundu wotani? Kodi tingachikulitse motani? Ndipo kodi tikuchitadi zimenezo?
5, 6. Kodi Petro anagogomezera motani kuti tifunikira kupeza chidziŵitso?
5 Kukula m’chidziŵitso cha Mlengi wa chilengedwe ndi Yesu kunali mfundo yaikulu m’kalata yachiŵiri ya Petro. M’mawu ake oyamba iye analemba kuti: “Kukoma mtima kwaulere ndi mtendere ziwonjezeketu kwa inu mwa chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi Yesu Ambuye wathu, malinga ndi mmene mphamvu yake yaumulungu yatipatsira kwaulere zinthu zonse zokhudza moyo ndi kudzipereka kwaumulungu, kupyolera m’chidziŵitso cholongosoka cha uyo amene anatiitana mwa ulemerero ndi ubwino.” (2 Petro 1:2, 3, NW) Chotero iye akugwirizanitsa kukhala ndi kukoma mtima kwaulere ndi mtendere ndi kupeza kwathu chidziŵitso cha Mulungu ndi Mwana wake. Zimenezo nzomveka, popeza kuti Mlengiyo, Yehova, ndiye magwero a chidziŵitso chenicheni. Munthu amene amaopa Mulungu akhoza kuona zinthu ndi malingaliro abwino ndi kupanga zitsimikizo zoyenera.—Miyambo 1:7.
6 Ndiyeno Petro akufulumiza kuti: “Wonjezerani pachikhulupiriro chanu ubwino, paubwino wanu chidziŵitso, pachidziŵitso chanu kudziletsa, pakudziletsa kwanu chipiriro, pachipiriro chanu kudzipereka kwaumulungu, pakudzipereka kwanu kwaumulungu chikondi cha pa abale, pachikondi chanu cha pa abale chikondi. Pakuti ngati zinthu zimenezi zikhala mwa inu nizisefukira, zidzakutetezerani kuti musakhale ofooka kapena osabala zipatso m’chidziŵitso cholongosoka cha Ambuye wathu Yesu Kristu.” (2 Petro 1:5-8, NW)b M’chaputala chotsatira, timaŵerenga kuti kupeza chidziŵitso cholongosoka kumathandiza anthu kuthaŵa zidetso za dziko. (2 Peter 2:20) Motero Petro anamveketsa bwino kuti awo okhala Akristu afunikira chidziŵitso, monga momwe amafunikiranso awo amene akutumikira kale Yehova. Kodi inu muli m’limodzi la magulu amenewo?
Phunzirani, Bwerezani, Gwiritsirani Ntchito
7. Kodi ndimwanjira yotani mmene ambiri apezera chidziŵitso cholongosoka cha zowonadi zazikulu za Baibulo?
7 Mwinamwake inu mumaphunzira ndi Mboni za Yehova chifukwa chakuti munaona mfundo za chowonadi muuthenga wawo. Kamodzi pamlungu, kwa ola limodzi kapena kuposapo, mumakambitsirana nkhani ya Baibulo mukumagwiritsira ntchito buku lophunzirira longa Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Mumachita bwino koposa! Ambiri amene akhala ndi phunziro loterolo ndi Mboni za Yehova apeza chidziŵitso cholongosoka. Komabe, kodi mungachitenji kuti muwonjezere zimene mumaphunzira? Nazi njira zina.c
8. Pokonzekera phunziro, kodi wophunzira angachitenji kuti aphunzire zowonjezereka?
8 Pasadakhale, pamene mukukonzekera phunziro lanu, unguzani nkhani imene mufuna kuiphunzira. Zimenezo zimatanthauza kuyang’ana mutu wa nkhani, mitu yaing’ono, ndi zithunzithunzi zogwiritsiridwa ntchito kumveketsa nkhaniyo. Ndiyeno, pamene mukuŵerenga ndime imodzi kapena chigawo cha chofalitsidwa, funani mfundo zazikulu ndi malemba ozichilikiza, ndi kuzichonga. Kuti muone ngati mwaphunzira zowonadi zofotokozedwa, yesani kuyankha mafunso a ndime zosiyanasiyana. Pochita zimenezi, yesani kuika mayankho m’mawu anuanu. Chomalizira, bwerezani phunzirolo, mukumayesa kukumbukira mfundo zazikulu ndi malingaliro ozichilikiza.
9. Kodi kugwiritsira ntchito njira zophunzirirazo kungathandize motani munthu kuphunzira?
9 Mukhoza kukula m’chidziŵitso ngati mugwiritsira ntchito njira zimenezi. Chifukwa ninji tikutero? Chimodzi cha zifukwazo nchakuti mudzakhala mukuŵerenga nkhaniyo ndi chikhumbo chachikulu chakufuna kuphunzira, kukonzekeretsa nthaka, titero kunena kwake. Mwakukhala ndi chithunzi chonse ndiyeno kufunafuna mfundo zazikulu ndi malingaliro, mudzaona mmene mbali za tsatanetsatane zimagwirizanira ndi mutu wa nkhaniyo kapena mapeto ake. Kubwereza komalizira kudzakuthandizani kukumbukira zimene mwaphunzira. Bwanji ponena za pambuyo pake, mkati mwa phunziro lanu la Baibulo?
10. (a) Kodi nchifukwa ninji kungobwereza mfundo kapena lingaliro loloŵezedwa pamtima kuli kosapindulitsa kwenikweni? (b) Kodi “kukumbukira zinthu zatsopano kwa nyengo zomatalikirapo nthaŵi zonse” kumaloŵetsamo chiyani? (c) Kodi ana Achiisrayeli ayenera kuti anapindula motani ndi kubwerezabwereza mawu?
10 Akatswiri m’zamaphunziro amadziŵa phindu la kubwerezabwereza kwa panthaŵi yake ndi kokhala ndi chifuno. Kumeneku sikungolankhula mawu oloŵeza pamtima, zimene mwina munayesa kusukulu pamene munali kuphunzira kuloŵeza pamtima maina, mfundo ina kapena lingaliro. Komabe, kodi munaona kuti munaiŵala mwamsanga zimene munaloŵeza, kuti sizinakhale m’chikumbukiro chanu? Chifukwa ninji? Kumangobwereza liwu latsopano loloŵezedwa kapena mfundo yakutiyakuti kungakhale kotopetsa, ndipo zotulukapo zake zimakhala za kanthaŵi chabe. Kodi nchiyani chimene chingasinthe zimenezo? Kufunitsitsa kwanu kuphunzira kudzathandiza. Mfungulo ina ndiyo kubwerezabwereza kokhala ndi chifuno. Patapita mphindi zingapo mutaphunzira mfundo yakutiyakuti, isanachoke m’chikumbukiro chanu, yesani kukumbukira zimene mwaphunzira. Kachitidwe kameneka katchedwa kuti “kukumbukira zinthu zatsopano kwa nyengo zomatalikirapo nthaŵi zonse.” Mwakutsitsimula chikumbukiro chanu chisanaiŵalike, mumatalikitsa nyengo ya kukumbukira. M’Israyeli, atate anafunikira kukhomezera malamulo a Mulungu mwa ana awo. (Deuteronomo 6:6, 7, NW) “Kukhomereza” kumatanthauza kuphunzitsa mwakubwerezabwereza. Mwachionekere, ambiri a atate amenewo choyamba anasonyeza malamulowo kwa ana awo; pambuyo pake anabwereza mawuwo; ndiyeno anafunsa ana awo mafunso pazimene anaphunzira.
11. Kodi chingachitidwe nchiyani mkati mwa phunziro la Baibulo kaamba ka kuwonjezera kuphunzira?
11 Ngati Mboni ikuchititsa phunziro la Baibulo kwa inu, iyo ingakuthandizeni kuphunzira mwakumaima mkati mwa phunzirolo ndi kufotokoza mwachidule mfundo zimene mwaphunzira. Zimenezi sizili chibwana. Ndiluso limene limapititsa patsogolo kuphunzira kwanu, chotero mosangalala gaŵananimo m’kubwereza kwa nthaŵi ndi nthaŵi. Kenako, pamapeto a phunziro, khalani ndi phande m’kubwereza komalizira kumene mudzayankha mosayang’ana m’buku. Mungathe, m’mawu anu, kufotokoza mfundozo monga momwe mungachitire pophunzitsa munthu wina. (1 Petro 3:15) Zimenezi zidzakhomereza zimene mwaphunzira m’chikumbukiro chanu kwa nthaŵi yaitali.—Yerekezerani ndi Salmo 119:1, 2, 125; 2 Petro 3:1.
12. Kodi wophunzira iyemwini angachitenji kuti akulitse luso lake la kukumbukira?
12 Njira ina yothandiza ndiyo yakuti inuyo, pambuyo pa tsiku limodzi kapena aŵiri, muuzeko munthu wina zimene munaphunzira, mwinamwake mnzanu wakusukulu, wantchito mnzanu, kapena mnansi. Mukhoza kutchula nkhaniyo ndi kunena kuti mungofuna kuona ngati mungakumbukire mfundo zazikulu za malingaliro kapena malemba ochilikiza nkhaniyo a m’Baibulo. Zimenezo zingadzutse chidwi cha munthu winayo. Ngakhale ngati sizikutero, mchitidwe wa kubwereza chidziŵitso chatsopano umenewo pambuyo pa nyengo ya tsiku limodzi kapena aŵiri udzachikhazikitsa m’chikumbukiro chanu. Pamenepo mudzakhala mutachiphunziradi, mukumachita zimene lemba la 2 Petro 3:18 limalimbikitsa.
Kuphunzira Mokangalika
13, 14. Kodi nchifukwa ninji tifuna kuchita zoposa kungodziŵa ndi kukumbukira chidziŵitso?
13 Kuphunzira kumaloŵetsamo zoposa kumangodziŵa zenizeni kapena kukhala wokhoza kukumbukira chidziŵitso. Anthu opembedza m’nthaŵi ya Yesu anachita zimenezo ndi mapemphero awo obwerezabwereza. (Mateyu 6:5-7) Koma kodi iwo anayambukiridwa motani ndi chidziŵitsocho? Kodi anali kubala zipatso zolungama? Kutalitali. (Mateyu 7:15-17; Luka 3:7, 8) Mbali ina ya vutolo inali yakuti chidziŵitsocho sichinaloŵe m’mitima yawo, kuti chibale zipatso zabwino.
14 Malinga nkunena kwa Petro, Akristu ayenera kukhala osiyana, kalelo ndi lerolino. Iye akutisonkhezera kuwonjezera pachikhulupiriro chathu chidziŵitso chimene chikatithandiza kusakhala ofooka ndi osabala zipatso. (2 Petro 1:5, 8) Kuti zimenezi zikhaledi tero kwa ife, tiyenera kufuna kukula m’chidziŵitso ndi kufuna kuti chiloŵe mozama mwa ife, chikumafika pamtima penipenipo. Zimenezo sizingachitike nthaŵi zonse.
15. Kodi ndivuto lanji limene linabuka kwa Akristu ena Achihebri?
15 M’nthaŵi ya Paulo Akristu Achihebri anali ndi vuto pankhani imeneyi. Pokhala Ayuda, iwo anali ndi chidziŵitso cha Malemba. Anadziŵa Yehova ndi zofuna zake zina. Pambuyo pake anawonjezerapo chidziŵitso chonena za Mesiya, anasonyeza chikhulupiriro, ndipo anabatizidwa monga Akristu. (Machitidwe 2:22, 37-41; 8:26-36) Kwa miyezi ndi zaka, ayenera kuti anapezeka pamisonkhano Yachikristu, kumene anakhala ndi phande m’kuŵerenga malemba ndi kupereka ndemanga. Chikhalirechobe, ena a iwo sanakule m’chidziŵitso. Paulo analemba kuti: “Mungakhale mwayenera kukhala aphunzitsi chifukwa cha nyengoyi, muli nako kusowanso kuti wina aphunzitse inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu; ndipo mukhala onga ofuna mkaka, osati chakudya chotafuna.” (Ahebri 5:12) Kodi zinakhala bwanji motero? Kodi zingachitikenso kwa ife?
16. Kodi nthaka youndana nchiyani, ndipo kodi imayambukira motani zomera?
16 Mwachitsanso, talingalirani za nthaka youndana chifukwa cha kuzizira, nthaka youndana kwachikhalire yopezeka kumalo adziko ozizira otchedwa Arctic ndi m’malo ena kumene kuzizira kumaposa pa mlingo woundanitsa madzi. Dothi, miyala, ndi madzi apansi zonse zimaundana pamodzi kukhala chithanthwe chouma, nthaŵi zina chakuya pansi kwa mamita 900. M’chilimwe, kusungunuka kungachitike m’nthaka yapamwamba (yotchedwa muyalo wokangalika). Komabe, muyalo waung’ono umenewu wa dothi losungunuka kaŵirikaŵiri umakhala wa matope chifukwa chakuti chinyonthocho sichingaloŵe m’nthaka youndana yokhala pansi pake. Zomera zimene zimaphuka m’muyalo waung’ono umenewu kaŵirikaŵiri zimakhala zazing’ono kwambiri kapena zopinimbira; mizu yake siitha kuloŵa m’nthaka youndanayo. Inu mungadabwe kuti, ‘Kodi nthaka youndana ili ndi unansi wanji ndi kukula kwanga m’chidziŵitso cha chowonadi cha Baibulo?’
17, 18. Kodi ndimotani mmene nthaka youndana ndi muyalo wake wokangalika ingagwiritsiridwe ntchito kuchitira chitsanzo zimene zinachitika kwa Akristu ena Achihebri?
17 Nthaka youndana imapereka chitsanzo chabwino cha munthu amene mphamvu zake za kulingalira sizili zokangalika m’kupeza, kukumbukira, ndi kugwiritsira ntchito chidziŵitso cholongosoka. (Yerekezerani ndi Mateyu 13:5, 20, 21.) Munthuyo mwachionekere ali nako kukhoza kwa maganizo kwa kuphunzira nkhani zosiyanasiyana, kuphatikizapo chowonadi cha Baibulo. Iye anaphunzira “zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu” ndipo mwina anayeneretsedwa kubatizidwa, monga momwe anachitira Akristu Achihebri. Komabe, iye angakhale “sakutsata ukulu msinkhu,” m’zinthu zoposa “chiphunzitso choyamba chonena za Kristu.”—Ahebri 5:12; 6:1, NW.
18 Taonani m’maganizo anu ena a Akristu amenewo ali pamisonkhano kalelo. Iwo analipo ndipo anali maso, koma kodi maganizo awo anali okangalika kuphunzira? Kodi iwo anali kukula m’chidziŵitso mowona mtima ndi mokangalika? Mwinamwake ayi. Kwa osakula msinkhu, kukhala kwawo ndi phande kulikonse pamisonkhano kunachitikira m’muyalo wokangalika waung’ono, kunena kwake titero, pamene pansi pake panali thanthwe loundana lakuya. Mizu ya zowonadi zoumirapo kapena zovuta siinathe kuloŵa m’mbali imeneyi ya kuundana kwa maganizo.—Yerekezerani ndi Yesaya 40:24.
19. Kodi ndimotani mmene Mkristu chiyamba kale lerolino angakhalire monga Akristu Achihebri?
19 Zingakhale zofanana ndi Mkristu lerolino. Pamene kuli kwakuti amakhalapo pamisonkhano, iye angakhale sakugwiritsira ntchito nthaŵi zimenezo kukula m’chidziŵitso. Bwanji ponena za kukhalamo ndi phande mokangalika? Kwa watsopano kapena wachichepere, kudzipereka kuti aŵerenge lemba kapena kupereka ndemanga ya ndime m’mawu akeake kungafune kuyesayesa kwamphamvu, kumene kumasonyeza kugwiritsira ntchito luso lake mwanjira yabwino ndi yoyamikirika. Koma Paulo anasonyeza kuti kwa ena, poona nthaŵi imene akhala Akristu, ayenera kupitirira mlingo woyambirapo kukhalamo ndi phande umenewo ngati akufuna kukula m’chidziŵitso.—Ahebri 5:14.
20. Kodi ndikudzipenda kotani kumene aliyense wa ife ayenera kuchita?
20 Ngati Mkristu woyamba kale sanapite patsogolo kuposa pa kungoŵerenga vesi la Baibulo kapena kupereka ndemanga monga momwe zakhalira m’ndime, mwachionekere kukhalamo kwake ndi phande kukuchitikira “m’muyalo wokangalika” wapamwamba wa maganizo ake. Akhoza kupezeka pamisonkhano yambiri komabe maganizo ake akukhalabe ouma, monga mwa fanizo la nthaka youndana. Tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi zili motero kwa ine? Kodi ndalola maganizo anga kukhala monga nthaka youndana? Kodi maganizo anga ngogalamuka motani ndi okondwera ndi zimene ndikuphunzira?’ Ngakhale ngati mayankho athu owona mtima sali abwino kwa ife, tikhoza kuyamba tsopano kuchitapo kanthu kuti tikule m’chidziŵitso.
21. Kodi ndinjira ziti zimene takambitsirana zimene mungagwiritsire ntchito pokonzekera kapena pamisonkhano?
21 Aliyense payekha, tikhoza kugwiritsira ntchito njira za m’ndime 8. Zilibe kanthu kuti takhala kwautali wotani mumpingo, tikhoza kugamulapo kupita patsogolo kuuchikulire ndi chidziŵitso chokulirapo. Kwa ena zimenezo zidzatanthauza kukonzekera misonkhano mwakhama kwambiri, mwinamwake kuyambiranso zizoloŵezi zimene anazilondola m’zaka zakale koma zimene analeka pang’onopang’ono. Pamene mukukonzekera, yesani kudziŵa mfundo zazikulu ndi kumvetsetsa malemba osazoloŵereka amene agwiritsiridwa ntchito kukulitsa ziganizo. Funafunani lingaliro kapena nsonga yatsopano m’nkhani ya phunzirolo. Mofananamo, mkati mwa msonkhano, yesani kugwiritsira ntchito njira zoperekedwa m’ndime 10 ndi 11. Yesani kukhala wogalamuka m’maganizo, monga ngati kuti mukutenthetsa maganizo anu kuti asazizire. Zimenezo zidzaletsa kuyambika kwa ‘kuundana kwa maganizo kulikonse’; kuyesayesa kosamalitsa kumeneku kudzasungunulanso “kuundana” kulikonse kwakale kumene kungakhalepo.—Miyambo 8:12, 32-34.
Chidziŵitso, Chothandiza Kukhala Wobala Zipatso
22. Kodi tidzapindula motani ngati tilimbikira pakukulitsa chidziŵitso?
22 Kodi ndimotani mmene tidzapindulira aliyense payekha ngati tilimbikira pankhani imeneyi ya kukula m’kukoma mtima kwaulere ndi chidziŵitso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Kristu? Mwakuyesayesa mwakhama kusunga mphamvu za maganizo anthu zili zokangalika, zokonzekera kuloŵetsa chidziŵitso, mbewu za zowonadi zatsopano ndi zovutirapo za Baibulo zidzazika mizu yozama, ndipo kumvetsetsa kwathu kudzakula ndi kukhala kokhalitsa. Zidzayerekezeredwa ndi zimene Yesu ananena m’fanizo lina lonena za mtima. (Luka 8:5-12) Mbewu zogwera panthaka yabwino zikhoza kuzika mizu yolimba yochilikiza zomerazo zimene zimabala zipatso.—Mateyu 13:8, 23.
23. Kodi pangakhale zotulukapo zotani pamene tilabadira 2 Petro 3:18? (Akolose 1:9-12)
23 Fanizo la Yesu linali losiyanapo, komabe zotulukapo zake zabwino zinali zofanana ndi zimene Petro analonjeza kuti: “Pachifukwa chimenechi, mwakupereka kwanu inunso zoyesayesa zowona mtima, wonjezerani pachikhulupiriro chanu ubwino, paubwino wanu chidziŵitso . . . Pakuti ngati zinthu zimenezi zikhala mwa inu nizisefukira, zidzakutetezerani kuti musakhale ofooka kapena osabala zipatso m’chidziŵitso cholongosoka cha Ambuye wathu Yesu Kristu.” (2 Petro 1:5-8) Inde, kukula kwathu m’chidziŵitso kudzatithandiza kukhala obala zipatso. Tidzapeza kuti kuloŵetsa chidziŵitso chowonjezereka kudzakhaladi kosangalatsa kwambiri. (Miyambo 2:2-5) Zimene mumaphunzira zidzakumbukirika mosavuta ndi kukuthandizani pamene muphunzitsa ena kukhala ophunzira. Chotero, mwanjira iyinso, mudzakhala obala zipatso zambiri ndipo mudzadzetsa ulemerero kwa Mulungu ndi Mwana wake. Petro anamaliza kalata yake yachiŵiriyo mwakunena kuti: “Pitirizanibe kukula m’kukoma mtima kwaulere ndi chidziŵitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Kristu. Kwa iye kukhale ulemerero tsopano ndi tsiku lomka muyaya.”—2 Petro 3:18.
[Mawu a M’munsi]
a “[Kuwonjezereka kwa chidziŵitso chathu] kungayerekezeredwe ndi kumene munthu amapeza, amene pofuna kudziŵa zowonjezereka ponena za mwezi, akwera padenga la nyumba yake kuti auyang’anitsitse.”
b Mikhalidwe iŵiri yoyambirira m’ndimeyi, chikhulupiriro ndi ubwino, zinafotokozedwa m’kope lathu la July 15, 1993.
c Njira zimenezi zikhoza kuthandiza Akristu achiyamba kale kupindula zambiri m’phunziro lawo laumwini ndi pokonzekera misonkhano.
Kodi Mungakumbukire?
◻ Kodi nchifukwa ninji muyenera kukhala ofunitsitsa kukulitsa chidziŵitso chanu?
◻ Kodi ndimotani mmene wophunzira Baibulo watsopano angapindulire zambiri m’phunziro lake?
◻ Kodi ndingozi yotani imene muyenera kupeŵa, monga mwa chitsanzo cha nthaka youndana?
◻ Kodi nchifukwa ninji muyenera kukhala otsimikiza mtima kuwongolera luso lanu la kukulitsa chidziŵitso?
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi ndili ndi vuto la kuundana kwa maganizo?