-
‘Samaliranidi’Nsanja ya Olonda—2002 | September 15
-
-
‘Samaliranidi’
“Tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.”—AHEBRI 2:1.
1. Sonyezani mmene kudodometsedwa kungapangitsire ngozi.
NGOZI za galimoto zimapha anthu pafupifupi 37,000 chaka chilichonse ku United States kokha. Akatswiri amati ambiri mwa anthu ameneŵa sakanafa ngati madalaivala akanasamala kwambiri pamsewu. Madalaivala ena amadodometsedwa ndi zizindikiro ndiponso zikwangwani kapena kugwiritsa ntchito kwawo telefoni ya m’manja. Palinso ena amene amadya akuyendetsa. M’zochitika zonsezi, kudodometsedwa kungapangitse ngozi.
2, 3. Kodi Paulo anawalangiza chiyani Akristu achihebri, ndipo n’chifukwa chiyani malangizo ake anali oyenerera?
2 Zaka pafupifupi 2,000 anthu asanayambe kupanga magalimoto, mtumwi Paulo anatchula chododometsa china chimene chinkavulaza kwambiri Akristu achihebri. Paulo anatsindika kuti Yesu Kristu woukitsidwa anapatsidwa udindo woposa wa angelo onse, chifukwa anamukhazika pa dzanja lamanja la Mulungu. Ndiyeno mtumwiyo anati: “Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.”—Ahebri 2:1.
3 N’chifukwa chiyani Akristu achihebri anafunika ‘kusamaliradi zimene anazimva’ zokhudza Yesu? Chifukwa chakuti panali patapita zaka 30 kuchokera pamene Yesu anachoka pa dziko lapansi. Popeza Mbuye wawo panalibe, Akristu ena achihebri anayamba kutengeka ndi kusiyana nacho chikhulupiriro choona. Anali kudodometsedwa ndi Chiyuda, chipembedzo chawo chakale.
Anafunika Kusamalira Kwambiri
4. Kodi n’chiyani chingakhale chifukwa chimene Akristu ena achihebri anakopeka kuti abwerere ku Chiyuda?
4 N’chifukwa chiyani Mkristu akanakopeka kuti abwerere ku Chiyuda? Chifukwa chakuti m’nthaŵi ya Chilamulo, polambira anali kugwiritsa ntchito zinthu zooneka. Anthu ankatha kuona ansembe ndi kumva fungo la nsembe yopsereza. Koma m’mbali zina, chikristu chinali chosiyana ndi zimenezo. Akristu anali ndi Mkulu wa Ansembe, Yesu Kristu, koma anali asanamuone padziko lapansi kwa zaka 30. (Ahebri 4:14) Anali ndi kachisi koma malo ake opatulika anali kumwamba. (Ahebri 9:24) Mosiyana ndi mdulidwe weniweni wa m’Chilamulo, mdulidwe wa Akristu unali “wa mtima, mumzimu.” (Aroma 2:29) Choncho, kwa Akristu achihebri, Chikristu chiyenera kuti chinayamba kuoneka ngati chosamvetsetseka.
5. Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti kulambira kumene Yesu anakhazikitsa kunaposa kulambira kwa m’nthaŵi ya Chilamulo?
5 Akristu achihebri anafunika kudziŵa chinthu chofunika kwambiri pa kulambira kumene Kristu anakhazikitsa. Kulambira kumeneku kunafuna kwambiri chikhulupiriro osati kuona, komabe kunaposa Chilamulo chimene chinaperekedwa kudzera mwa mneneri Mose. Paulo analemba kuti: “Ngati mwazi wa mbuzi ndi ng’ombe zamphongo, ndi makala a ng’ombe yamthandi owazawaza pa iwo odetsedwa, upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi; koposa kotani nanga mwazi wa Kristu amene anadzipereka yekha wopanda chirema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbumtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?” (Ahebri 9:13, 14) Inde, kukhululukidwa chifukwa chokhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu Kristu kumaposa m’njira zambiri kukhululukidwa kumene kunkachitika chifukwa cha nsembe zoperekedwa m’nthaŵi ya Chilamulo.—Ahebri 7:26-28.
6, 7. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Akristu achihebri anafunikira kwambiri ‘kusamaliradi zimene anamva’? (b) Kodi panthaŵi imene Paulo analemba kalata yake kwa Ahebri, panatsala nthaŵi yaitali bwanji kuti Yerusalemu awonongedwe? (Onani mawu am’munsi.)
6 Panalinso chifukwa china chimene Akristu achihebri anafunikira kusamaliradi zimene anamva za Yesu. Iye analosera kuti Yerusalemu adzawonongedwa. Yesu anati: “Masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo; ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa mwala unzake; popeza sunazindikira nyengo ya mayang’aniridwe ako.”—Luka 19:43, 44.
7 Kodi zimenezi zinali kudzachitika liti? Yesu sananene tsiku ndi nthaŵi yake. M’malo mwake, anapereka malangizo aŵa: “Pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipululutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali m’Yudeya athaŵire kumapiri, ndi iwo ali m’kati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kumiraga asaloŵemo.” (Luka 21:20, 21) M’kati mwa zaka 30 Yesu atanena mawu ameneŵa, Akristu ena ku Yerusalemu analeka kukhala tcheru ndipo anapatutsidwa. Tinganene kuti anasiya kuyang’ana mumsewu. Ngati sakanasintha maganizo awo, akanasimba tsoka. Kuwonongedwa kwa Yerusalemu kunali pafupi, kaya ankaganiza choncho kapena ayi.a Langizo la Paulo liyenera kuti linawadzutsa Akristu ogona mwauzimu ku Yerusalemu.
‘Kusamaliradi’ Masiku Ano
8. N’chifukwa chiyani tifunika ‘kusamaliradi’ choonadi cha Mawu a Mulungu?
8 Mofanana ndi Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino, tifunika ‘kusamaliradi’ choonadi cha Mawu a Mulungu. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti ifenso tikuyembekezera chiwonongeko chimene chayandikira, osati cha dziko limodzi lokha, koma cha dziko lonse lapansi. (Chivumbulutso 11:18; 16:14, 16) N’zoona kuti sitikudziŵa tsiku lenileni ndi nthaŵi yake pamene Yehova adzachita zimenezi. (Mateyu 24:36) Komabe, tikuona tokha maulosi a m’Baibulo akukwaniritsidwa zimene zikusonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza.’ (2 Timoteo 3:1-5) Motero, tiyenera kupeŵa chilichonse chimene chingatidodometse. Tifunika kumvera Mawu a Mulungu ndi kukhalabe tcheru. Ngati tichita zimenezi, ‘tidzalimbika kupulumuka zonse zimene zidzachitika.’—Luka 21:36.
-
-
‘Samaliranidi’Nsanja ya Olonda—2002 | September 15
-
-
a Paulo ayenera kuti analemba kalata kwa Ahebri mu 61 C.E. Ngatidi ndi choncho, panangopita zaka zisanu zokha ndipo Yerusalemu anazingidwa ndi magulu ankhondo a Seshasi Galasi. Posakhalitsa, magulu ankhondo amenewo anachoka, zimene zinapatsa mpata Akristu atcheru kuti athaŵe. Patapita zaka zinayi kuchokera pamenepa, mzindawo unawonongedwa ndi magulu ankhondo achiroma otsogozedwa ndi Kazembe Tito.
-