MUTU 17
‘Dzilimbitseni Pamaziko a Chikhulupiriro Chanu Choyera Kopambana’
“Podzilimbitsa pamaziko a chikhulupiriro chanu choyera kopambana, . . . pitirizani kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kukukondani.”—YUDA 20, 21.
1, 2. Kodi mukugwira ntchito yomanga chiyani, nanga n’chifukwa chiyani ntchitoyo ili yofunika kwambiri?
YEREKEZERANI kuti mukumanga nyumba ndipo mukugwira ntchito imeneyi mwakhama kwambiri. Mwakhala mukugwira ntchitoyi kwa nthawi yaitali ndipo zikuoneka kuti ikutengerani zaka zambiri kuti mumalize. Mwakumana ndi mavuto ambiri pa nthawi imene mwakhala mukumanga nyumbayi, komabe mumaikonda kwambiri ntchitoyi. Ndipo mwatsimikiza mtima kuti zivute zitani simugwa ulesi ndiponso simusiya kumanga. Mukudziwa kuti ntchitoyi ndi yofunika kwambiri chifukwa ikukhudza moyo wanu panopo, ngakhalenso tsogolo lanu. Kodi ikukhudza bwanji tsogolo lanu? Ikukhudza tsogolo lanu chifukwa nyumba imene tikuiyerekezera panoyi ndinuyo.
2 Wophunzira Yuda anatsindika mfundo yakuti tiyenera kudzimanga tokha. Pamene ankalimbikitsa Akhristu kuti ‘apitirize kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kuwakonda,’ iye anatchulanso chinthu chofunika kwambiri chimene chingatithandize kuchita zimenezi. Iye anati: ‘Dzimangeni pa maziko a chikhulupiriro chanu choyera kopambana.’ (Yuda 20, 21) Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachite kuti mudzimange komanso kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu n’cholinga choti Mulungu azikukondani? Tiyeni tikambirane mbali zitatu za ntchito yanu yomanga imene ingakuthandizeni kulimbitsa chikhulupiriro chanu.
PITIRIZANI KUKHULUPIRIRA MALAMULO OLUNGAMA A YEHOVA
3-5. (a) Kodi Satana amafuna kuti muziwaona bwanji malamulo a Yehova? (b) Kodi muyenera kuwaona bwanji malamulo a Mulungu, ndipo zimenezi zingakuthandizeni bwanji? Perekani chitsanzo.
3 Tiyenera kupitiriza kukhulupirira kwambiri malamulo a Mulungu. Pophunzira buku lino, mwadziwa malamulo ambiri olungama a Yehova okhudza makhalidwe. Kodi malamulo amenewa mumawaona bwanji? Satana amafuna kusokoneza maganizo anu kuti muziona mfundo ndi malamulo a Yehova ngati opanikiza, ngakhalenso opondereza kumene. Kuyambira m’munda wa Edeni, pa nthawi imene anaona kuti njira imeneyi inamuyendera bwino, Satana wakhala akuigwiritsa ntchito mpaka pano. (Genesis 3:1-6) Kodi inunso angakupusitseni ndi njira imeneyi? Zikudalira kwambiri maganizo anu.
4 Mwachitsanzo: Yerekezerani kuti mukuyenda kumalo ena ake okongola kwambiri osungirako nyama, ndiye mukuona kuti pali mpanda wautali wawaya umene ukukutchingirani kuti musalowe mbali ina ya malowo. Koma mukuona kuti mbali imeneyo ndi imene ili yokongola kwambiri. Poyamba mukuganiza kuti mpandawo ukukupherani ufulu. Komabe, mutayang’anitsitsa mukuona mkango woopsa ukuzembera nyama. Apa tsopano mukuona kufunika kwa mpandawo. Kodi inunso pali chilombo chilichonse chimene chikukuzemberani? Mawu a Mulungu amachenjeza kuti: “Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.”—1 Petulo 5:8.
5 Satana ndi chilombo cholusa. Yehova safuna kuti Satana atidye, choncho wakhazikitsa malamulo amene amatiteteza ku “zochita zachinyengo” za woipayo. (Aefeso 6:11) Chotero, nthawi zonse tikamaganizira mozama za malamulo a Mulungu, tiziwaona kuti ndi umboni wakuti Atate wathu wakumwamba amatikonda. Tikamawaona choncho malamulo a Mulungu, amatiteteza ndipo timakhala osangalala. Yakobo yemwe anali wophunzira wa Yesu analemba kuti: “Woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro limene limabweretsa ufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala polichita.”—Yakobo 1:25.
6. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti muzikhulupirira kwambiri mfundo ndi malamulo olungama a Mulungu? Perekani chitsanzo.
6 Kuti tizikhulupirira kwambiri Mulungu, amene amatipatsa malamulo komanso kuti tizikhulupirira kuti malamulo ake ndi othandiza, tiyenera kumawatsatira pa moyo wathu. Mwachitsanzo, mu “chilamulo cha Khristu” mulinso lamulo lakuti tiziphunzitsa anthu ena ‘zinthu zonse zimene Yesu analamula.’ (Agalatiya 6:2; Mateyu 28:19, 20) Akhristu saona mopepuka lamulo loti tizisonkhana pamodzi kuti tilambire Mulungu ndi kulimbikitsana. (Aheberi 10:24, 25) Palinso lamulo la Mulungu lakuti tizipemphera kwa Yehova nthawi zonse ndiponso pafupipafupi komanso mochokera pansi pa mtima. (Mateyu 6:5-8; 1 Atesalonika 5:17) Tikamatsatira malamulo ngati amenewa, timamvetsa kuti Mulungu anatipatsa malamulowa chifukwa chotikonda kwambiri. Kuwamvera kumatipatsa chimwemwe chimene sitingachipeze kwina kulikonse m’dziko lamavutoli. Komanso mukaganizira mmene mwapindulira chifukwa chotsatira malamulo a Mulungu, zingakupangitseni kuwakhulupirira kwambiri.
7, 8. Kodi Mawu a Mulungu amalimbikitsa bwanji anthu amene amaopa kuti sangakwanitse kuchita zinthu zolungama nthawi zonse?
7 Anthu ena amaopa kutsatira malamulo a Yehova pa moyo wawo ndipo amaona kuti sangakwanitse kutsatira malamulo amenewa. Ngati inuyo munayamba mwaganizapo choncho, muzikumbukira mawu awa: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchitsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo. Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga. Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje, ndipo chilungamo chanu chidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.” (Yesaya 48:17, 18) Kodi munayamba mwaganizirapo za mawu olimbikitsa kwambiri amenewa?
8 Apa Yehova akutikumbutsa kuti tikamamumvera, timapindula ndi ifeyo. Iye akutilonjeza kuti tidzapindula m’njira ziwiri. Njira yoyamba, mtendere wathu udzakhala ngati mtsinje, womwe madzi ake amakhala abata, ochuluka ndiponso samauma. Yachiwiri, chilungamo chathu chidzakhala ngati mafunde a m’nyanja. Mukaima m’mphepete mwa nyanja ndikuona mafunde, mumadziwa kuti umu ndi mmene nyanja imakhalira nthawi zonse. Mumadziwa kuti mafundewo sadzasiya kufika m’mphepete mwa nyanjayo mpaka kalekale. Kwenikweni Yehova akukuuzani kuti mungathe kumachita chilungamo, kapena kuti kuchita zabwino pa moyo wanu mpaka kalekale. Ngati mukuyesetsa kukhala wokhulupirika, Yehova sadzakusiyani kuti mugonje mukakumana ndi mayesero. (Werengani Salimo 55:22.) Malonjezo olimbikitsa amenewa angakuthandizeni kwambiri kukhulupirira Yehova ndi malamulo ake olungama.
‘YESETSANI MWAKHAMA KUTI MUKHALE OKHWIMA MWAUZIMU’
9, 10. (a) N’chifukwa chiyani Mkhristu ayenera kuyesetsa kukhala wokhwima mwauzimu? (b) Kodi kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumathandiza bwanji munthu kukhala wosangalala?
9 Mbali ina ya ntchito yanu yomanga ikutchulidwa m’mawu ouziridwa akuti: “Tiyeni tiyesetse mwakhama kuti tikhale okhwima mwauzimu.” (Aheberi 6:1) Cholinga chachikulu cha Mkhristu ndi kukhala wokhwima mwauzimu. Ngakhale kuti anthufe sitingachite zinthu mwangwiro, komabe tingathe kukhala okhwima mwauzimu. Kuwonjezera pamenepa, Akhristu akamakula mwauzimu, m’pamene amasangalala kwambiri kutumikira Yehova. N’chifukwa chiyani zimakhala choncho?
10 Mkhristu wokhwima mwauzimu ndi munthu amene amaona zinthu mmene Yehova amazionera. (Yohane 4:23) Paulo analemba kuti: “Otsatira zofuna za thupi amaika maganizo awo pa zinthu za thupi, koma otsatira za mzimu amaika maganizo awo pa zinthu za mzimu.” (Aroma 8:5) Munthu amene amaika maganizo ake pa zinthu za thupi, sakhala wachimwemwe kwenikweni chifukwa saganizira za anthu ena, saganizira zam’tsogolo, ndipo amakhala wokonda kwambiri chuma. Koma munthu amene amaika maganizo ake pa zinthu za mzimu amakhala wosangalala chifukwa maganizo ake amakhala pa Yehova, yemwe ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteyo 1:11) Iye amakhalanso wofunitsitsa kukondweretsa Yehova ndipo amakhalabe wosangalala ngakhale pamene akuyesedwa. Chifukwa chiyani amasangalala? Mavuto amatipatsa mpata wosonyeza kuti Satana ndi wabodza ndiponso wosonyeza kuti ndife okhulupirika. Ndipo zimenezi zimasangalatsa Atate wathu wakumwamba.—Miyambo 27:11; werengani Yakobo 1:2, 3.
11, 12. (a) Kodi Paulo ananena chiyani za ‘mphamvu za kuzindikira’ za Mkhristu, nanga kodi mawu akuti ‘kuphunzitsa’ amatanthauza chiyani? (b) Kodi chimafunika n’chiyani kuti thupi likhale lolimba komanso kuti lizolowere kuchita zinthu?
11 Munthu amachita kuphunzira kuti akhale wokhwima mwauzimu. Taganizirani vesi ili: “Chakudya chotafuna ndi cha anthu okhwima mwauzimu, amene pogwiritsa ntchito mphamvu zawo za kuzindikira, aphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.” (Aheberi 5:14) M’Chigiriki mawu akuti ‘kuphunzitsa’ amene Paulo anagwiritsa ntchito palembali, ankatchulidwa pamasewera olimbitsa thupi a ku Girisi. Mawuwa akhozanso kumasuliridwa kuti ‘kuphunzitsa munthu kukhala katswiri wa masewera olimbitsa thupi.’ Kodi n’chiyani chimafunika kuti munthu aphunzire mpaka kukhala katswiri pa masewera amenewa?
12 Tikamabadwa, thupi lathu limakhala lisanaphunzire kuchita zinthu. Mwachitsanzo, mwana amabadwa asakudziwa pamene pali manja ndi miyendo yake. N’chifukwa chake amangoyendetsa manja ndi miyendo yake chisawawa, ndipo nthawi zina amadzimenya yekha kumaso moti amadzidzimuka mpaka amalira. Koma pang’ono ndi pang’ono, akamayendetsa mikono ndi manja ake amayamba kuphunzira kuchita zinthu zosiyanasiyana. Iye amaphunzira kukwawa, kuyenda, ndipo kenako amatha kuthamanga.a Nanga bwanji za katswiri wa masewera olimbitsa thupi? Mukamuona akudumpha n’kumatembenuka ali m’malere popanda kugwa, mumadziwa kuti anayamba kale kuphunzira kuchita zimenezi. Luso lakelo silinabwere lokha, iye anafunika kuphunzira kwa nthawi yaitali. Baibulo limanena kuti kuchita masewera olimbitsa thupi ngati amenewa “n’kopindulitsa pang’ono.” Choncho ngati Baibulo limanena kuti zimenezi zili ndi phindu lake, ndiye kuti n’zofunika kwambiri kuphunzitsa mphamvu zathu kuti tizitha kuzindikira zinthu mwauzimu.—1 Timoteyo 4:8.
13. Kodi tingaphunzitse bwanji mphamvu zathu za kuzindikira?
13 M’buku lino takambirana zambiri zimene zingakuthandizeni kuphunzitsa mphamvu zanu za kuzindikira kuti mukhalebe wokhulupirika kwa Yehova komanso kuti mukhale wokhwima mwauzimu. Mukafuna kusankha zochita tsiku lililonse muziganizira mfundo ndi malamulo a Mulungu ndipo muzipemphera kuti muthe kutsatira malamulowo. Musanasankhe kuchita china chilichonse muzidzifunsa kuti: ‘Kodi ndi malamulo ati kapena mfundo za m’Baibulo ziti zimene zikukhudzana ndi nkhaniyi? Kodi ndingagwiritse ntchito bwanji mfundo zimenezi? Kodi Atate wanga wakumwamba angasangalale nditasankha kuchita chiyani pa nkhaniyi?’ (Werengani Miyambo 3:5, 6; Yakobo 1:5.) Kuchita zimenezi pa chilichonse chimene mukufuna kuchita, kungakuthandizeni kupitiriza kuphunzitsa mphamvu zanu za kuzindikira. Kudziphunzitsa m’njira imeneyi kungakuthandizeni kuti mukhalebe munthu wokhwima mwauzimu.
14. Kodi tiyenera kukhala ndi njala ya chiyani kuti tikule mwauzimu, nanga tiyenera kusamala ndi chiyani?
14 Munthu amakula n’kufika polekezera, koma kukula mwauzimu kulibe malire. Kuti munthu akule amafunika chakudya. N’chifukwa chake Paulo ananena kuti: “Chakudya chotafuna ndi cha anthu okhwima mwauzimu.” Chinthu chofunika kwambiri kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu ndi kupitiriza kudya chakudya chauzimu chotafuna. Mukamagwiritsa bwino ntchito zimene mwaphunzira, ndiye kuti muli ndi nzeru, ndipo Baibulo limati: “Nzeru ndiyo chinthu chofunika kwambiri.” Choncho, tiyenera kukhala ndi njala yofuna choonadi, chomwe ndi chakudya chamtengo wapatali chimene Atate wathu wakumwamba amapereka. (Miyambo 4:5-7; 1 Petulo 2:2) Komabe, sitiyenera kudzikuza n’kumaona ngati ndife oposa ena chifukwa tili ndi nzeru zochokera kwa Mulungu kapena chifukwa choti tikudziwa zambiri. Nthawi ndi nthawi tiyenera kudzifufuza kuti tidziwe ngati tayamba kukhala ndi mtima wodzikuza kapena ngati makhalidwe ena oipa ayamba kukula mumtima mwathu. Paulo analemba kuti: “Pitirizani kudziyesa kuti muone ngati mudakali olimba m’chikhulupiriro. Pitirizani kudziyesa kuti mudziwe kuti ndinu munthu wotani.”—2 Akorinto 13:5.
15. N’chifukwa chiyani chikondi chili chofunika kwambiri kuti munthu apitirize kukula mwauzimu?
15 Ntchito yomanga nyumba imatha koma ntchito yosamalira nyumbayo siitha. Pamafunika kukonza mowonongeka ndipo nthawi zina pangafunike kuwonjezera zipinda zina. Kodi timafunikira chiyani kuti tikule ndi kupitirizabe kukhala okhwima mwauzimu? Chofunika koposa zonse ndi chikondi. Tiyenera kupitiriza kukonda Yehova ndi okhulupirira anzathu. Ngati tilibe chikondi, zonse zimene timadziwa ndi kuchita zingakhale zopanda ntchito ngati phokoso longosokosera. (1 Akorinto 13:1-3) Chikondi chingatithandize kukhala okhwima mwauzimu ndi kupitirizabe kukula mwauzimu.
MUZIGANIZIRA KWAMBIRI ZIMENE YEHOVA WALONJEZA
16. Kodi Satana amafuna kuti anthu azikhala ndi maganizo otani, nanga kodi Yehova watipatsa chida chiti chotitetezera?
16 Tiyeni tikambirane mbali yomaliza yokhudza ntchito yomanga chikhulupiriro chanu. Pa ntchito yomangayi, kuti mufike pokhala wotsatira weniweni wa Khristu muyenera kuteteza maganizo anu. Satana, yemwe ndi wolamulira wa dzikoli, ndi katswiri posokoneza maganizo a anthu kuti aziganiza zofooketsa, azikhala okayikira ndiponso opanda chiyembekezo. (Aefeso 2:2) Maganizo amenewa ndi oopsa kwa Mkhristu, chifukwa munthu amene ali ndi maganizo amenewa ali ngati nyumba yamatabwa imene matabwa ake ayamba kuwola. Koma chosangalatsa n’chakuti Yehova anatipatsa chida chothandiza kwambiri chotiteteza. Chida chimenechi ndi chiyembekezo.
17. Kodi Mawu a Mulungu amasonyeza bwanji kuti chiyembekezo n’chofunika kwambiri?
17 Baibulo limatchula zida za nkhondo zauzimu zosiyanasiyana zimene tiyenera kugwiritsa ntchito pa nkhondo yathu yolimbana ndi Satana ndiponso dzikoli. Chida chimodzi chofunikira pa zida zimenezi ndi chisoti, chomwe ndi “chiyembekezo chachipulumutso.” (1 Atesalonika 5:8) Kale, msilikali ankadziwa kuti sangapulumuke kunkhondo ngati sangavale chisoti. Zisoti zambiri zinkakhala zachitsulo ndipo mkati mwake munkakhala nsalu yokhuthala kapena chikopa. Chisoti chimenechi chinkathandiza kuti muvi ulionse ukabaya kumutu, uzingogwa popanda kumuvulaza kwambiri msilikaliyo. Monga mmene chisoti chimatetezera mutu, ndi mmenenso chiyembekezo chimatetezera maganizo athu.
18, 19. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yopitiriza kukhala ndi chiyembekezo, nanga tingamutsanzire bwanji?
18 Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yokhalabe ndi chiyembekezo. Kumbukirani zimene iye anakumana nazo usiku womaliza wa moyo wake wapadziko lapansi. Chifukwa chofuna ndalama, mnzake wapamtima anam’pereka kwa adani. Mnzake wina anam’kana kuti sankamudziwa ngakhale pang’ono, pomwe ena anathawa n’kumusiya yekha. Anthu a mtundu wake womwe, anamuukira ndipo ankachita kukhuwizira kuti asilikali achiroma amuphe mwankhanza. Palibe angatsutse zoti mayesero amene Yesu anakumana nawo anali oopsa kwambiri kuposa ena alionse amene tingakumane nawo. Ndiyeno, kodi n’chiyani chinamuthandiza kupirira? Lemba la Aheberi 12:2, limanena kuti: “Chifukwa cha chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake, anapirira mtengo wozunzikirapo. Iye sanasamale kuti zochititsa manyazi zimuchitikira, ndipo tsopano wakhala pansi kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” Choncho, nthawi zonse Yesu ankakumbukira “chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake.”
19 Kodi ndi chimwemwe chotani chimene Mulungu anamuikira Yesu patsogolo pake? Iye ankadziwa kuti kupirira kwake kuthandiza kuyeretsa dzina la Yehova, ndiponso kupereka umboni wosatsutsika wakuti Satana ndi wabodza. Panalibenso chinthu chimene chikanam’patsa Yesu chimwemwe chenicheni kuposa kuchita zimenezi. Iye ankadziwa kuti Yehova adzam’patsa mphoto yaikulu chifukwa chokhala wokhulupirika ndipo ankadziwanso kuti wangotsala pang’ono kubwerera kumwamba kukakhalanso ndi Atate wake. Nthawi imene ankazunzidwa, iye ankaganizira kwambiri zinthu zosangalatsa zimene ankayembekezerazi. Ifenso tiyenera kuchita chimodzimodzi, chifukwa tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosangalala. Yehova watilemekeza kwambiri potipatsa mwayi wothandiza kuyeretsa dzina lake lalikulu. Tingapereke umboni wakuti Satana ndi wabodza ngati titasankha kulamuliridwa ndi Yehova ndi kupitiriza kuchita zinthu zimene zingachititse kuti azitikonda ngakhale titakumana ndi mavuto kapena mayesero oopsa kwambiri.
20. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kupitirizabe kukhala ndi maganizo olimbikitsa ndiponso chiyembekezo champhamvu?
20 Yehova amafunitsitsa kupereka mphoto kwa atumiki ake okhulupirika. (Yesaya 30:18; werengani Malaki 3:10.) Iye amasangalala akamapatsa atumiki ake zinthu zabwino zimene amalakalaka. (Salimo 37:4) Choncho, nthawi zonse muziganizira kwambiri za chiyembekezo chakuti mudzaona malonjezo a Mulungu akukwaniritsidwa. Musamaganizire kwambiri zinthu zofooketsa ndipo musamatengere maganizo oipa ndi opotoka a dziko la Satanali. Ngati mwaona kuti mzimu wa dzikoli wayamba kulowa m’maganizo ndi mumtima mwanu, pempherani kwambiri kwa Yehova kuti akupatseni ‘mtendere wake umene umaposa kuganiza mozama kulikonse.’ Mtendere umene Mulungu angakupatseni udzateteza mtima wanu ndi maganizo anu.—Afilipi 4:6, 7.
21, 22. (a) Kodi ndi zinthu zosangalatsa kwambiri ziti zimene a “khamu lalikulu” akuyembekezera? (b) Pa zinthu zimene Akhristu akuyembekezera, kodi inuyo mukufunitsitsa kudzaona chiyani, nanga mwatsimikiza mtima kuchita chiyani?
21 Mukuyembekezeratu zinthu zosangalatsa kwambiri moti mungachite bwino kumaziganizira. Ngati muli m’gulu la “khamu lalikulu” limene ndi anthu ‘amene adzatuluka m’chisautso chachikulu,’ muziganizira moyo umene mudzakhale nawo posachedwapa. (Chivumbulutso 7:9, 14) Pa nthawi imeneyi Satana ndi ziwanda zake kudzakhala kulibe, choncho mudzakhala ndi mtendere wosaneneka woti simunakhalepo nawo. Ndipo, ndani amene anayamba wakhalapo ndi moyo wopanda mavuto ndi ziyeso za Satana? Zonsezi zikadzatha, tidzakhala osangalala kwambiri pogwira ntchito yokonzanso dzikoli kuti likhale paradaiso. Tidzagwira ntchitoyi motsogoleredwa ndi Yesu limodzi ndi olamulira anzake okwana 144,000. Kunena zoona, timasangalala kwambiri tikamayembekezera kuti posachedwapa matenda onse adzatha, tidzakumananso ndi okondedwa athu amene ali m’manda, ndiponso tidzakhala ndi moyo wabwino kwambiri monga mmene Mulungu anafunira. Tikadzakhala angwiro, tidzalandira mphoto yaikulu kwambiri imene ikupezeka pa Aroma 8:21. Mphoto imeneyi ndi kukhala ndi “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.”
22 Yehova akufuna kuti mukhale ndi ufulu waukulu kwambiri woti simungathe n’komwe kuuganizira. Kuti mudzapeze ufulu umenewu muyenera kukhala omvera. Pamenepa mungathe kuona kuti m’pofunika kuyesetsa kuti muzimvera Yehova tsiku ndi tsiku. Choncho, chitani chilichonse chimene mungathe kuti muzidzimanga nokha pa maziko a chikhulupiriro choyera kopambana kuti Mulungu adzapitirize kukukondani mpaka kalekale.
a Akatswiri a sayansi amanena kuti timakhala ndi luso lina lake limene limatithandiza kudziwa bwino thupi lathu komanso kudziwa pamene pali mikono ndi manja athu. Mwachitsanzo, luso limeneli limakuthandizani kuwomba m’manja ngakhale mutatsinzina. Munthu wina amene anadwala matenda owononga luso limeneli sankatha kuima, kuyenda ngakhalenso kukhala tsonga.