NKHANI YOPHUNZIRA 44
Pitirizani Kulimbitsa Chiyembekezo Chanu
“Yembekezera Yehova.”—SAL. 27:14.
NYIMBO NA. 144 Yang’ananibe Pamphoto
ZIMENE TIPHUNZIREa
1. Kodi Yehova watipatsa chiyembekezo chotani?
YEHOVA watipatsa chiyembekezo chabwino kwambiri cha moyo wosatha. Ena akuyembekezera kukakhala kumwamba mpaka kalekale monga zolengedwa zauzimu zomwe sizingafe. (1 Akor. 15:50, 53) Koma ambiri akuyembekezera kudzakhala mosangalala padzikoli mpaka kalekale komanso ali ndi thanzi labwino. (Chiv. 21:3, 4) Kaya tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha kumwamba kapena padzikoli, timaona kuti chiyembekezo chathu ndi chamtengo wapatali.
2. Kodi chiyembekezo chimachokera kuti, nanga n’chifukwa chiyani tikutero?
2 Mawu akuti “chiyembekezo” monga mmene agwiritsidwira ntchito m’Baibulo, angatanthauze “kudikira kuti zinthu zina zake zabwino zichitika.” Chiyembekezo chathu cha m’tsogolo ndi chotsimikizika chifukwa chimachokera kwa Yehova. (Aroma 15:13) Timadziwa zinthu zimene watilonjeza ndipo timadziwanso kuti nthawi zonse amakwaniritsa malonjezo ake. (Num. 23:19) Ndife otsimikiza kuti Yehova amalakalaka ndipo ali ndi mphamvu yokwaniritsa chilichonse chimene wanena kuti achita. Choncho chiyembekezo chathu sichitanthauza kungoganizira kapena kulakalaka zinazake zabwino, koma timayembekezera zinthu zenizeni zomwe zili ndi umboni.
3. Kodi tikambirana chiyani munkhaniyi? (Salimo 27:14)
3 Atate wathu wakumwamba amatikonda ndipo amafuna kuti tizimukhulupirira. (Werengani Salimo 27:14.) Chiyembekezo chathu mwa Yehova chikakhala cholimba, tidzakwanitsa kupirira mayesero, tidzakhalabe olimba mtima ndiponso tidzakhala osangalala kaya tikumane ndi zotani m’tsogolo. Tiyeni tione mmene chiyembekezo chathu chimatitetezera. Kuti tidziwe zimenezi, tiona mmene chiyembekezochi chilili ngati nangula komanso chisoti. Kenako tikambirana mmene tingachilimbitsire.
CHIYEMBEKEZO CHATHU CHILI NGATI NANGULA
4. Kodi chiyembekezo chimafanana bwanji ndi nangula? (Aheberi 6:19)
4 M’kalata imene analembera Aheberi, mtumwi Paulo anayerekezera chiyembekezo ndi nangula. (Werengani Aheberi 6:19.) Nthawi zambiri Paulo ankayenda panyanja, choncho ankadziwa kuti nangula amathandiza kuti ngalawa isamayendeyende. Pa nthawi ina ali m’ngalawa kunayamba chimphepo champhamvu. Pa nthawi imene mphepoyo inkawomba, iye ankaona oyendetsa ngalawayo akuponya anangula m’madzi poteteza kuti ngalawayo isawombe miyala. (Mac. 27:29, 39-41) Mofanana ndi nangula, chiyembekezo chathu chimatithandiza kukhalabe odekha kuti tisachoke kwa Yehova tikakumana ndi mavuto omwe ali ngati chimphepo. Chiyembekezo chathu cholimba chimatithandiza kuti tipirire tikakumana ndi mayesero aakulu chifukwa sitikayikira kuti posachedwapa zinthu zikhalanso bwino. Kumbukirani kuti Yesu anachenjeza kuti tidzazunzidwa. (Yoh. 15:20) Choncho kuganizira za mphoto yam’tsogolo yomwe talonjezedwa, kumatithandiza kuti tisasunthike pa kulambira kwathu.
5. Kodi chiyembekezo chinamuthandiza bwanji Yesu pamene ankayembekezera kuphedwa?
5 Taganizirani mmene chiyembekezo chinathandizira Yesu kukhalabe wokhulupirika ngakhale kuti ankayembekezera kuphedwa mwankhanza. Pa tsiku la Pentekosite mu 33 C.E., mtumwi Petulo anatchula mawu opezeka m’buku la Masalimo, omwe amafotokoza bwino mmene Yesu analili wodekha kuti: “Ine ndidzakhala ndi chiyembekezo, chifukwa simudzasiya moyo wanga m’Manda, ndipo simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde. . . . Ndipo chifukwa cha nkhope yanu ndidzakhala ndi chimwemwe chosefukira.” (Mac. 2:25-28; Sal. 16:8-11) Ngakhale kuti Yesu ankadziwa kuti aphedwa, iye anali ndi chiyembekezo champhamvu chakuti Mulungu adzamuukitsa ndipo adzasangalala kukumananso ndi Atate wake kumwamba.—Aheb. 12:2, 3.
6. Kodi m’bale wina ananena chiyani zokhudza chiyembekezo?
6 Chiyembekezo chathandiza abale ndi alongo ambiri kupirira. Taganizirani chitsanzo cha M’bale Leonard Chinn, yemwe anali wokhulupirika ndipo ankakhala ku England. Pa nthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse, iye anamangidwa chifukwa chokana kulowa usilikali. Kwa miyezi iwiri, anaikidwa m’ndende ya yekha ndipo kenako anayamba kumugwiritsa ntchito yakalavula gaga. Patapita nthawi iye analemba kuti: “Zimene ndinakumana nazo zinandithandiza kumvetsa bwino mmene chiyembekezo chimatithandizira kupirira. M’Baibulo muli zitsanzo za Yesu, atumwi, aneneri komanso muli malonjezo abwino kwambiri. Zonsezi zimatipatsa chiyembekezo chabwino cha m’tsogolo ndipo zimatithandiza kupirira.” Chiyembekezo chinali ngati nangula kwa Leonard, ndipo chingakhalenso ngati nangula kwa ife.
7. Kodi mayesero amalimbitsa bwanji chiyembekezo chathu? (Aroma 5:3-5; Yakobo 1:12)
7 Tikapirira mayesero n’kuona mmene Yehova watithandizira, timazindikira kuti iye akusangalala nafe ndipo zimenezi zimalimbitsa chiyembekezo chathu. (Werengani Aroma 5:3-5; Yakobo 1:12.) Choncho timakhala ndi chiyembekezo cholimba kuposa chimene tinali nacho titangomva kumene uthenga wabwino. Satana amafuna kuti tigonje tikakumana ndi mayesero, koma Yehova amatithandiza kuti tithe kupirira mayesero aliwonse.
CHIYEMBEKEZO CHATHU CHILI NGATI CHISOTI
8. Kodi chiyembekezo chimafanana bwanji ndi chisoti? (1 Atesalonika 5:8)
8 Baibulo limayerekezeranso chiyembekezo chathu ndi chisoti. (Werengani 1 Atesalonika 5:8.) Chisoti chimene msilikali amavala, chimamuteteza kuti adani asamuvulaze m’mutu. Pa nkhondo yathu yauzimu, timafunika kuteteza maganizo athu kuti Satana asawawononge. Iye amalimbana nafe pogwiritsa ntchito mayesero komanso mfundo zimene cholinga chake ndi kusokoneza maganizo athu. Monga mmene chisoti chimatetezera mutu wa msilikali, chiyembekezo chathu chimateteza maganizo athu kuti tipitirizebe kukhala okhulupirika kwa Yehova.
9. Kodi chimachitika n’chiyani anthu akakhala opanda chiyembekezo?
9 Chiyembekezo chathu cha moyo wosatha chimatithandiza kuti tizichita zinthu mwanzeru komanso mozindikira. Koma chiyembekezo chathu chikafooka, ndipo tikayamba kumangoganizira zofuna zathu, tingasiye kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Taganizirani zimene zinachitikira Akhristu ena a ku Korinto. Iwo anasiya kukhulupirira lonjezo lofunika kwambiri la Mulungu lakuti akufa adzauka. (1 Akor. 15:12) Paulo ananena kuti anthu omwe sankakhulupirira kuti akufa adzauka ankakhala moyo wongokhutiritsa zilakolako zawo. (1 Akor. 15:32) Masiku anonso anthu amene sayembekezera malonjezo a Mulungu, amachita china chilichonse chomwe angathe kuti akhale moyo wosangalala panopa. Koma ife timakhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu. Chiyembekezo chathu chili ngati chisoti chimene chimateteza maganizo athu ndipo chimatithandiza kuti tisasankhe moyo wongodzisangalatsa tokha womwe ungawononge ubwenzi wathu ndi Yehova.—1 Akor. 15:33, 34.
10. Kodi chiyembekezo chingatiteteze bwanji kuti tisakhale ndi maganizo olakwika?
10 Chisoti chathu cha chiyembekezo chingatiteteze kuti tisamaganize kuti zimene timayesetsa kuchita posangalatsa Yehova n’zopanda phindu. Mwachitsanzo, ena angamaganize kuti: ‘Sindidzakhala nawo m’gulu la anthu amene adzakhale ndi moyo mpaka kalekale. Si ine woyenera. Sindingakwanitse kumatsatira mfundo za Mulungu.’ Kumbukirani kuti Elifazi yemwe ankanamizira kudzatonthoza Yobu anagwiritsanso ntchito maganizo ngati omwewa. Iye anati: “Kodi munthu ndani kuti akhale woyera?” Pofotokoza za Mulungu iye anatinso: “Iyetu alibe chikhulupiriro mwa angelo ake, ndipo kumwamba si koyera m’maso mwake.” (Yobu 15:14, 15) Ilitu linali bodza lankunkhuniza. Kumbukirani kuti Satana ndi amene amalimbikitsa maganizo amenewa. Iye amadziwa kuti mukamaganizira kwambiri zinthu ngati zimenezi, mungasiye kukhala ndi chiyembekezo. Choncho muzikana mabodza amenewa ndipo m’malomwake muziganizira malonjezo a Yehova. Musamakayikire kuti iye amafuna kuti mudzakhale ndi moyo mpaka kalekale ndipo adzakuthandizani kuti mukwanitse zimenezi.—1 Tim. 2:3, 4.
PITIRIZANI KULIMBITSA CHIYEMBEKEZO CHANU
11. N’chifukwa chiyani tiyenera kuleza mtima pamene tikuyembekezera kuti Mulungu akwaniritse malonjezo ake?
11 Sizophweka kupitiriza kulimbitsa chiyembekezo chathu. Nthawi zina tingasiye kuyembekezera moleza mtima kuti Mulungu akwaniritse malonjezo ake. Koma popeza Yehova ndi wamuyaya, nthawi yomwe imaoneka yaitali kwa ife, kwa iye ndi yaifupi. (2 Pet. 3:8, 9) Iye adzakwanitsa cholinga chake pa nthawi yoyenera koma mwina sangachite zimenezi pa nthawi imene ifeyo tikuyembekezera. Kodi n’chiyani chingatithandize kupitiriza kulimbitsa chiyembekezo chathu, pamene moleza mtima tikudikira kuti Mulungu akwaniritse malonjezo ake?—Yak. 5:7, 8.
12. Mogwirizana ndi Aheberi 11:1, 6, kodi pali kugwirizana kotani pakati pa chiyembekezo ndi chikhulupiriro?
12 Tingapitirize kukhala ndi chiyembekezo cholimba tikakhalabe pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, yemwe amatipatsa chiyembekezochi. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa chiyembekezo ndi kukhulupirira kuti Yehova alipo komanso kuti “amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” (Werengani Aheberi 11:1, 6.) Tikamakhulupirira kwambiri kuti Yehova alipo m’pamenenso timakhulupirira kwambiri kuti iye adzakwaniritsa zonse zimene analonjeza. Tiyeni tikambirane zinthu zina zimene zingatithandize kulimbitsa kwambiri ubwenzi wathu ndi Yehova, zomwe zingachititse kuti tipitirize kukhala ndi chiyembekezo cholimba.
13. Kodi tingatani kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu?
13 Muzipemphera kwa Yehova komanso kuwerenga Mawu ake. Ngakhale kuti sitingathe kumuona Yehova, tingakhale naye pa ubwenzi. Tingalankhule naye m’pemphero ndipo sitikayikira kuti atimvetsera. (Yer. 29:11, 12) Tingamvetsere Mulungu tikamawerenga Mawu ake komanso kuwaganizira mozama. Tikamawerenga za mmene Yehova anasamalirira anthu omwe anakhalabe okhulupirika kwa iye m’mbuyomu, chiyembekezo chathu chimalimba kwambiri. Zonse zimene timawerenga m’Mawu a Mulungu, “zinalembedwa kuti zitilangize. Malembawa amatipatsa chiyembekezo chifukwa amatithandiza kupirira ndiponso amatilimbikitsa.”—Aroma 15:4.
14. N’chifukwa chiyani tiyenera kumaganizira zimene Yehova anachitira anthu ena?
14 Muziganizira mmene Yehova wakhala akukwaniritsira malonjezo ake. Taganizirani zimene Yehova anachitira Abulahamu ndi Sara. Iwo anali atafika pamsinkhu woti sangakhale ndi ana. Komabe Mulungu anawalonjeza kuti adzakhala ndi mwana. (Gen. 18:10) Kodi Abulahamu anatani chifukwa cha zimenezi? Baibulo limati: “Anali ndi chiyembekezo ndiponso chikhulupiriro chakuti adzakhala tate wa mitundu yambiri.” (Aroma 4:18) Ngakhale kuti kwa munthu zikanaoneka ngati zosatheka, Abulahamu anakhulupirira kuti Yehova akwaniritsa lonjezo lake. Munthu wokhulupirikayu sanagwiritsidwe fuwa lamoto. (Aroma 4:19-21) Nkhani ngati zimenezi zimatiphunzitsa kuti tingamadalire kuti Mulungu akwaniritsa malonjezo ake, ngakhale zitakhala kuti kwa ife zikuoneka ngati zosatheka.
15. N’chifukwa chiyani tiyenera kumaganizira zimene Mulungu wakhala akutichitira?
15 Muziganizira zimene Yehova wakhala akukuchitirani. Taganizirani mmene inuyo panokha mwapindulira chifukwa cha kukwaniritsidwa kwa malonjezo opezeka m’Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, Yesu analonjeza kuti Atate wake adzakupatsani zomwe mumafunikira pa moyo. (Mat. 6:32, 33) Iye anakutsimikiziraninso kuti Yehova adzakupatsani mzimu wake woyera mukamupempha. (Luka 11:13) Yehova wakhala akukwaniritsa malonjezo amenewa. N’kutheka kuti pali malonjezo ena omwe inuyo mwaona akukwaniritsidwa pa inu. Mwachitsanzo, iye analonjeza kuti azikukhululukirani, kukutonthozani komanso kukudyetsani mwauzimu. (Mat. 6:14; 24:45; 2 Akor. 1:3) Mukamaganizira kwambiri zimene Mulungu wakuchitirani kale, mudzalimbitsa chiyembekezo chanu cha m’tsogolo.
MUZISANGALALA NDI CHIYEMBEKEZO
16. N’chifukwa chiyani chiyembekezo chathu chili chamtengo wapatali?
16 Chiyembekezo chathu cha moyo wosatha ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu. Tikuyembekezera zinthu zabwino kwambiri m’tsogolo ndipo sitimakayikira kuti zidzachitika. Chiyembekezo chili ngati nangula wathu ndipo chimatithandiza kukhala odekha kuti tizipirira mayesero, kuzunzidwa komanso sitiopa kufa. Chilinso ngati chisoti ndipo chimateteza maganizo athu kuti tizipewa kuchita zoipa n’kumayesetsa kuchita zabwino. Chiyembekezo chathu cha m’Baibulo chimatithandiza kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ndipo chimasonyeza kuti iye amatikonda kwambiri. Zinthu zimatiyendera bwino kwambiri tikapitiriza kukhala ndi chiyembekezo cholimba.
17. N’chifukwa chiyani chiyembekezo chimatithandiza kukhala osangalala?
17 M’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Roma, Paulo anawalimbikitsa kuti: “Kondwerani ndi chiyembekezocho.” (Aroma 12:12) Paulo ankasangalala chifukwa sankakayikira kuti akapitirizabe kukhala wokhulupirika, adzalandira moyo wosatha kumwamba. Ifenso tingamasangalale ndi chiyembekezo chathu chifukwa sitimakayikira kuti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake. Wolemba masalimo anati: “Wodala ndi munthu amene . . . chiyembekezo chake chili mwa Yehova Mulungu wake, . . . Wosunga choonadi mpaka kalekale.”—Sal. 146:5, 6.
NYIMBO NA. 139 Yerekezani Kuti Muli M’dziko Latsopano
a Yehova watipatsa chiyembekezo chabwino kwambiri cha m’tsogolo. Chiyembekezochi chimatilimbikitsa ndipo chimatithandiza kuti tisamangoganizira mavuto omwe tikukumana nawo. Chimatipatsa mphamvu kuti tipitirizebe kukhala okhulupirika kaya tikumane ndi mayesero otani. Chingatitetezenso kuti tisamatengere mfundo zimene zingasokoneze maganizo athu. Monga mmene tiphunzirire, izi ndi zifukwa zokwanira zotichititsa kuti tipitirizebe kulimbitsa chiyembekezo chathu.
b MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Monga mmene chisoti chimatetezera mutu wa msilikali, komanso mmene nangula amathandizira ngalawa kuti isayendeyende, chiyembekezo chathu chimateteza maganizo athu ndipo chimatithandiza kukhala odekha tikakumana ndi mayesero. Mlongo akupemphera ndipo sakukayikira kuti ayankhidwa. M’bale akuganizira mmene Mulungu anakwaniritsira zimene analonjeza Abulahamu. M’bale wina akuganizira mmene Mulungu wakhala akumuthandizira.