Yehova Amapereka Mphoto kwa Anthu Omufunafuna ndi Mtima Wonse
“Aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi, ndi kuti amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.”—AHEB. 11:6.
1, 2. (a) Kodi kukonda Mulungu ndi kumukhulupirira n’kogwirizana bwanji? (b) Kodi m’nkhaniyi tikambirana mafunso ati?
TIMAKONDA Yehova “chifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.” (1 Yoh. 4:19) Njira ina imene wasonyezera chikondi chimenechi ndi yoti amadalitsa atumiki ake. Tikamakonda kwambiri Mulungu timayambanso kumukhulupirira kwambiri. Timakhulupiriranso kuti iye amapereka mphoto kwa anthu amene amawakonda.—Werengani Aheberi 11:6.
2 Yehova ndi Mulungu wopereka mphoto. Sitinganene kuti timakhulupirira Mulungu ngati sitikhulupirira kuti iye amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse. Tikutero chifukwa Baibulo limati: “Chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa.” (Aheb. 11:1) Choncho ngati timakhulupirira Mulungu tiyeneranso kukhulupirira kuti amadalitsa atumiki ake. Koma kodi kukhulupirira kuti Mulungu amapereka mphoto kungatithandize bwanji? Kodi Yehova anadalitsa bwanji atumiki ake akale, nanga amadalitsa bwanji atumiki ake masiku ano?
YEHOVA AMALONJEZA KUTI AZIDALITSA ATUMIKI AKE
3. Kodi Yehova walonjeza chiyani pa Malaki 3:10?
3 Mwa kufuna kwake, Yehova analonjeza kuti azidalitsa atumiki ake okhulupirika. Paja iye anati: “Ndiyeseni chonde pa nkhani imeneyi, kuti muone ngati sindidzakutsegulirani zipata za kumwamba ndi kukukhuthulirani madalitso oti mudzasowa powalandirira.” (Mal. 3:10) Choncho tikamatumikira Yehova mokhulupirika timasonyeza kuti timayamikira zimene amatichitira.
4. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira mawu a Yesu pa Mateyu 6:33?
4 Yesu anauza ophunzira ake kuti Mulungu adzawathandiza akamaika Ufumu pamalo oyamba. (Werengani Mateyu 6:33.) Yesu ananena zimenezi chifukwa chodziwa kuti chilichonse chimene Yehova walonjeza chimachitika. (Yes. 55:11) Ifenso tikamakhulupirira kwambiri Yehova, tidzaona akukwaniritsa lonjezo lake lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Aheb. 13:5) Lonjezo limeneli limatithandizanso kukhulupirira zimene Yesu ananena zoti tikafuna Ufumu ndi chilungamo cha Mulungu, tidzadalitsidwa.
5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene Yesu anayankha Petulo ndi zolimbikitsa?
5 Pa nthawi ina, Petulo anafunsa Yesu kuti: “Ife tasiya zinthu zonse ndi kukutsatirani, kodi tidzapeza chiyani?” (Mat. 19:27) Yesu sanadzudzule Petulo chifukwa cha funsoli. M’malomwake anauza ophunzira ake kuti adzadalitsidwa chifukwa chololera kusiya zinthu zina. Iye ananena kuti atumwi okhulupirikawo limodzi ndi anthu ena adzalamulira ndi Yesu kumwamba. Koma palinso madalitso ena amene tingapeze panopa. Yesu anati: “Aliyense amene wasiya nyumba, abale, alongo, abambo, amayi, ana kapena minda chifukwa cha dzina langa adzalandira zochuluka kwambiri kuposa zimenezi, ndipo adzapeza moyo wosatha.” (Mat. 19:29) Apa analonjeza kuti tidzapeza madalitso ambiri. Ndipo n’zoona kuti kupeza abambo, amayi, azichimwene, azichemwali komanso ana m’gulu la Yehova ndi madalitso oposa zimene tinasiya chifukwa cha Ufumu.
“NANGULA WA MIYOYO YATHU”
6. Kodi kudziwa zimene Mulungu walonjeza kumatithandiza bwanji?
6 Madalitso amene Mulungu watilonjeza amatithandiza kuti tizikhalabe okhulupirika tikakumana ndi mayesero. Kuwonjezera pa madalitso amene timapeza panopa, Yehova watilonjezanso madalitso ambiri m’tsogolomu. (1 Tim. 4:8) Choncho kukhulupirira kwambiri kuti Yehova “amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse,” kumatithandiza kuti tikhalebe okhulupirika.—Aheb. 11:6.
7. Kodi chiyembekezo chimafanana bwanji ndi nangula?
7 Pa ulaliki wa paphiri Yesu anati: “Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzira aneneri amene analipo inu musanakhaleko.” (Mat. 5:12) Atumiki ena a Mulungu adzalandira mphoto yawo kumwamba. Koma ena adzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso ndipo nawonso ali ndi chifukwa choti ‘akondwere ndi kudumpha ndi chimwemwe.’ (Sal. 37:11; Luka 18:30) Kaya tidzapita kumwamba kapena tidzakhala padzikoli, chiyembekezo chathu “chili ngati nangula wa miyoyo yathu ndipo n’chotsimikizika ndiponso chokhazikika.” (Aheb. 6:17-20) Nangula amathandiza kuti sitima isatengeke ndi mafunde. Nafenso chiyembekezo chimatithandiza kuti tikakumana ndi mavuto tisasokonezeke maganizo kapena kutaya mtima koma tikhalebe okhulupirika.
8. Kodi chiyembekezo chathu chimatithandiza bwanji kuti tisamade nkhawa kwambiri?
8 Chiyembekezo chathu chimatithandizanso kuti tisamade nkhawa kwambiri. Zimene Mulungu watilonjeza zili ngati mankhwala amene amaziziritsa mtima wathu tikakhala ndi nkhawa. Kunena zoona timalimbikitsidwa ‘tikatulira Yehova nkhawa zathu’ chifukwa timadziwa kuti atithandiza. (Sal. 55:22) Tizikhulupirira ndi mtima wonse kuti Mulungu “angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza.” (Aef. 3:20) Taganizirani mfundo imeneyi. Mulungu angathe kuchita, osati chabe zazikulu, koma “zazikulu kwambiri.”
9. Kodi tingatani kuti Yehova adzatipatse mphoto?
9 Kuti tidzalandire mphoto, tiyenera kukhulupirira Yehova komanso kumvera malangizo ake. Mose anauza Aisiraeli kuti: “Yehova adzakudalitsa ndithu m’dziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa kuti likhale cholowa chako. Adzakudalitsa ngati udzamveradi mawu a Yehova Mulungu wako ndi kutsatiradi malamulo onsewa amene ndikukupatsa lero. Yehova Mulungu wako adzakudalitsa ndithu monga mmene anakulonjezera.” (Deut. 15:4-6) Kodi inuyo mumakhulupirira kuti Yehova angakudalitseni mukamamutumikira ndi mtima wonse? Pali zifukwa zomveka zotichititsa kukhulupirira zimenezi.
YEHOVA ANAWAPATSA MPHOTO
10, 11. Kodi Yehova anadalitsa bwanji Yosefe?
10 Yehova watipatsa Mawu ake kuti azitithandiza. M’Baibulo muli nkhani zambiri zosonyeza kuti iye amadalitsa atumiki ake okhulupirika. (Aroma 15:4) Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Yosefe. Azichimwene ake anamugulitsa ndipo atafika ku Iguputo, mkazi wa abwana ake anamunamizira mpaka anatsekeredwa m’ndende. Kodi izi zinalepheretsa Yehova kumudalitsa? Ayi ndithu. Baibulo limati: “Yehova anapitirizabe kukhala ndi Yosefe ndi kumusonyeza kukoma mtima kosatha . . . Yehova anali ndi Yosefe, ndipo chilichonse chimene iye anali kuchita Yehova anali kuchidalitsa.” (Gen. 39:21-23) Yosefe anapitiriza kudalira Mulungu pa nthawi yonse imene ankakumana ndi mavuto.
11 Patapita zaka, Farao anatulutsa Yosefe m’ndende n’kumupatsa udindo wokhala wachiwiri wake. (Gen. 41:1, 37-43) Yosefe atakhala ndi ana awiri, woyamba “anamutcha dzina lakuti Manase, chifukwa anati, ‘Mulungu wandiiwalitsa mavuto anga onse, ndi nyumba yonse ya bambo anga.’ Wachiwiriyo anamutcha Efuraimu, chifukwa anati, ‘Mulungu wandipatsa ana m’dziko la masautso anga.’” (Gen. 41:51, 52) Chifukwa Yosefe anakhalabe wokhulupirika, Mulungu anamudalitsa ndipo anamugwiritsa ntchito populumutsa Aisiraeli ndi Aiguputo ku njala. Yosefe ankadziwa kuti Yehova ndi amene wamupatsa madalitso onsewa.—Gen. 45:5-9.
12. N’chiyani chinathandiza Yesu kukhalabe wokhulupirika pamene ankayesedwa?
12 Yesu nayenso anamverabe Mulungu ngakhale pamene anakumana ndi mayesero ndipo Mulunguyo anamupatsa mphoto. Kodi n’chiyani chinamuthandiza? Baibulo limati: “Chifukwa cha chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake, anapirira mtengo wozunzikirapo. Iye sanasamale kuti zochititsa manyazi zimuchitikira.” (Aheb. 12:2) Yesu ankasangalala podziwa kuti akakhalabe wokhulupirika ayeretsa dzina la Mulungu. Ndipo Mulungu ankasangalala naye komanso anamudalitsa kwambiri. Baibulo limanenanso kuti: “Wakhala pansi kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.” Ndiponso limati: “Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse.”—Afil. 2:9.
YEHOVA SANGAIWALE ZIMENE TIKUCHITA
13, 14. Kodi Yehova amamva bwanji tikamuchitira zinazake?
13 Yehova amayamikira kwambiri zonse zimene timachita pomutumikira. Amadziwanso zinthu zimene zimatichititsa kudzikayikira kapena kuchita mantha. Iye amatimvera chisoni tikakhala ndi nkhawa chifukwa cha mavuto a zachuma. Amatimvetsanso tikamalephera kuchita zambiri mu utumiki chifukwa cha matenda kapena mavuto ena. Choncho tisamakayikire mfundo yoti Yehova amayamikira kwambiri zimene atumiki ake amachita kuti akhalebe okhulupirika.—Werengani Aheberi 6:10, 11.
14 Baibulo limati Yehova ndi “Wakumva pemphero” choncho tisamakayikire zoti adzayankha mapemphero athu. (Sal. 65:2) Iye ndi “Tate wachifundo chachikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” (2 Akor. 1:3) Akhoza kutilimbikitsa pogwiritsa ntchito Akhristu anzathu. Yehova amasangalala kwambiri nafenso tikamachitira chifundo anzathu. Paja Baibulo limati: “Wokomera mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezera zimene anachitazo.” (Miy. 19:17; Mat. 6:3, 4) Choncho tikathandiza munthu amene ali pa mavuto, Yehova amaona kuti tamukongoza iyeyo ndipo amalonjeza kuti adzatibwezera.
MPHOTO IMENE TIMAPEZA PANOPA KOMANSO YA M’TSOGOLO
15. Kodi inuyo mukuyembekezera mphoto iti? (Onani chithunzi patsamba 24.)
15 Akhristu odzozedwa akuyembekezera “chisoti chachifumu chachilungamo” chimene Ambuye adzawapatse. (2 Tim. 4:7, 8) Komabe sikuti Akhristu a “nkhosa zina” ndi otsika chifukwa choti sadzalandira mphoto imeneyi. Iwo akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso. Baibulo limati “adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Yoh. 10:16; Sal. 37:11.
16. N’chifukwa chiyani tinganene kuti lemba la 1 Yohane 3:19 ndi lolimbikitsa?
16 Nthawi zina tingamaone ngati sitikuchita zambiri potumikira Mulungu komanso mwina tingamakayikire ngati Yehova amasangalala ndi zimene timachita. Kapenanso tingamaone ngati si ife oyenera kulandira madalitso alionse. Koma tizikumbukira kuti “Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.” (Werengani 1 Yohane 3:19, 20.) Iye amapereka mphoto kwa aliyense amene amamutumikira ndi mtima wonse ngakhale zimene akuchita pomutumikira zitaoneka ngati n’zochepa.—Maliko 12:41-44.
17. Kodi Yehova akutidalitsa bwanji panopa?
17 Masiku otsiriza ano ndi ovuta kwambiri koma Yehova akudalitsabe anthu ake. Iye amawasamalira mwauzimu komanso amawathandiza kuti azigwirizana padziko lonse. (Yes. 54:13) Mogwirizana ndi zimene Yesu analonjeza, Yehova akutidalitsa panopa potipatsa abale, alongo komanso makolo m’gulu lake. (Maliko 10:29, 30) Kuwonjezera pamenepo, anthu amene amafunafuna Mulungu ndi mtima wonse amasangalala, amakhutira ndi zomwe ali nazo komanso amakhala ndi mtendere wa mumtima.—Afil. 4:4-7.
18, 19. Kodi atumiki a Yehova amamva bwanji akaganizira madalitso amene amalandira?
18 Atumiki a Yehova padziko lonse angapereke umboni woti Yehova akuwadalitsadi. Chitsanzo ndi mlongo wina wa ku Germany dzina lake Bianca. Iye anati: “Kaya ndingathokoze bwanji Yehova? Iye amandithandiza tsiku ndi tsiku kuti ndisamade nkhawa kwambiri. Panopa dzikoli likungoipiraipira. Koma ndikamagwira ntchito limodzi ndi Yehova, ndimaona kuti ndine wotetezeka. Ndikalolera kusiya zinthu zina kuti ndimutumikire, iye amandipatsa madalitso ambirimbiri.”
19 Chitsanzo china ndi cha mlongo wa ku Canada dzina lake Paula. Mlongoyu ali ndi zaka 70 ndipo ali ndi matenda oopsa kwambiri otupa msana. Iye anati: “Ndimalephera kuyenda chifukwa cha vutoli koma sindilephera kulalikira. Ndimalalikira m’njira zosiyanasiyana monga pafoni kapena ulaliki wamwamwayi. Ndili ndi kabuku kamene ndimalembamo malemba komanso mfundo zolimbikitsa zimene ndapeza m’mabuku athu. Kabukuka ndimakawerenga nthawi ndi nthawi ndipo ndinakapatsa dzina lakuti, ‘Buku Langa la Chipulumutso.’ Tikamaganizira malonjezo a Yehova, timaona kuti mavuto a panopa ndi akanthawi. Yehova amatithandiza pa vuto lililonse.” Mwina mavuto anu ndi osiyana ndi a Mlongo Bianca ndi Mlongo Paula. Koma n’kutheka kuti nanunso mwaona Yehova akukuthandizani komanso kuthandiza anthu ena. Ndi bwino kuganizira mmene Yehova akutidalitsira panopa komanso mmene adzatidalitsire m’tsogolo.
20. Kodi timayembekezera chiyani tikamatumikira Yehova ndi mtima wonse?
20 Tizikumbukira kuti pemphero lochokera pansi pa mtima komanso ufulu wathu wa kulankhula zimatithandiza kuti tilandire “mphoto yaikulu.” Tisamakayikirenso kuti ‘tikamachita chifuniro cha Mulungu, tidzalandira zimene Mulunguyo walonjeza.’ (Aheb. 10:35, 36) Choncho tiyeni tipitirize kulimbitsa chikhulupiriro chathu komanso tizitumikira Yehova ndi mtima wonse. Tikamachita zimenezi sitikayikira ngakhale pang’ono kuti adzatidalitsa.—Werengani Akolose 3:23, 24.