Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◻ Kodi Yesu ali Nkhoswe kokha kaamba ka Akristu odzozedwa ndi mzimu kapena kaamba ka mtundu wonse wa anthu, popeza kuti 1 Timoteo 2:5, 6 imalankhula za iye kukhala “[nkhoswe]” amene “anadzipereka yekha chiwombolo m’malo mwa onse”?
Baibulo liri ndi ponse paŵiri ziphunzitso zazikulu ndi zowonadi zakuya, zimene ziri chakudya cholimba kaamba ka phunziro. Limodzi la maphunziro oterowo limaphatikizapo mbali ya Yesu Kristu monga Nkhoswe. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi [nkhoswe imodzi] pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Kristu Yesu, amene anadzipereka yekha chiwombolo m’malo mwa onse; umboni m’nyengo zake.”—1 Timoteo 2:5, 6.
Kuti timvetsetse chimene Paulo akunena, tiyenera choyamba kuyamikira kuti Baibulo limapereka ziyembekezo ziŵiri kaamba ka anthu okhulupirika: (1) moyo wangwiro mu paradaiso wa pa dziko lapansi wobwezeretsedwa ndi (2) moyo kumwamba kaamba ka “kagulu ka nkhosa” ka Kristu, okhala ndi chiŵerengero cha 144,000. (Luka 12:32; Chibvumbulutso 5:10; 14:1-3) Chikristu cha Dziko chimaphunzitsa kuti anthu abwino onse amapita kumwamba, kaimidwe kosakhala ka malemba komwe kaphimba kawonedwe kachisawawa, kotero kuti Yesu akulingaliridwa kukhala mkhalapakati kaamba ka anthu onse oterowo. Nchiyani, ngakhale ndi tero, chimene Baibulo limasonyeza?
Liwu la Chigriki me·siʹtes, logwiritsiridwa ntchito kaamba ka “nkhoswe,” limatanthauza ‘yemwe adzipeza iyemwini pakati pa mabungwe kapena mbali ziŵiri.’ Linali ‘liwu la luso lokhala ndi mbali zambiri la chinenero cha lamulo cha Chihelene.’ Profesa Albrecht Oepke (Theological Dictionary of the New Testament) akunena kuti me·siʹtes linali “limodzi la mawu a luso osiyanasiyana koposa mu mpambo wa mawu a lamulo a [Chi]helene.”
Koma nchifukwa ninji Baibulo limagwiritsira ntchito liwu la lamulo kaamba ka ntchito ya Yesu ya unkhoswe? Monga mbiri ya kumbuyo, lingalirani chimene Paulo analemba ponena za Chilamulo cha Mulungu choperekedwa kwa Israyeli wosonkhana pamodzi patsogolo pa Phiri la Sinai: “Ndipo chinakonzeka ndi angelo m’dzanja la nkhoswe.” (Galatiya 3:19, 20) Nkhoswe imeneyo anali Mose. Iye anali mkhalapakati wogwiritsiridwa ntchito pakati pa Yehova ndi mtundu wa Israyeli wakuthupi. Wogwiritsiridwa ntchito kaamba ka chiyani? Kaamba ka kukhazikitsa pangano, kapena kumvana kwa lamulo, pakati pa Mulungu ndi mtunduwo.a
Kodi ichi chimatanthauza kuti pali lingaliro la lamulo lachindunji loloŵetsedwamo m’thayo la Yesu monga Nkhoswe? Inde. Onani ndemanga ya Paulo pa Ahebri 8:6. Pambuyo polankhula ponena za chihema ndi zinthu zina zoimirako pansi pa pangano la Chilamulo, iye analemba kuti: “Koma iye [Yesu] walandira chitumikiro chomveka choposa, umonso ali nkhoswe ya pangano labwino koposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa.” “Pangano labwino koposa” linali pangano latsopano, limene linaloŵa m’malo pangano lokhalidwa nkhoswe ndi Mose. (Ahebri 8:7-13) Pangano latsopano linali “lokhazikitsidwa mwalamulo.” Ilo linayala maziko kaamba ka atsatiri ena a Kristu, kuyambira ndi atumwi, kupeza “choloŵera m’malo opatulika,” m’mwamba mwenimwenimo.—Ahebri 9:24; 10:16-19.
Palinso zisonyezero zina za mkhalidwe wa lamulo wa thayo la Yesu monga Nkhoswe ya “pangano latsopano.” Akumachitira ndemanga pa lonjezo la Mulungu pa Salmo 110:4, Paulo analemba kuti: “Ku ukulu umenewo Yesu wakhalanso woperekedwa chikole [enʹgy·os] cha pangano labwino.” (Ahebri 7:22, NW) Uku ndiko kugwiritsira ntchito kokha kwa Baibulo kwa liwu la enʹgy·os. The New International Dictionary of New Testament Theology ikunena kuti: “Engyos inatsimikizira kuti thayo la lamulo likachitidwa.” Chotero Yesu monga Nkhoswe ya pangano latsopano akutumikira monga chikole cha lamulo kuti “chiyembekezo choposa” chikakwaniritsidwa.—Ahebri 7:19.
Kwinakwake Paulo akugwiritsiranso ntchito liwu lina lokhala ndi lingaliro la lamulo, ar·ra·bonʹ, lotembenuzidwa “chizindikiro.” Dikishonale imodzimodziyo ikunena kuti: “Liwu la Gk. arrabōn . . . liri lingaliro la lamulo kuchokera ku chinenero cha bizinesi ndi malonda.” Onani mmene Paulo anagwiritsirira ntchito liwu la lamulo limeneli: “Yemwe watidzoza ife ali Mulungu. Iye waikanso, chisindikizo chake pa ife ndipo watipatsa chizindikiro cha chimene chirinkudza, uko ndiko kuti, mzimu, m’mitima yathu.” (2 Akorinto 1:21, 22, NW) Kupezeka konse kuŵiri kwa ar·ra·bonʹ kumachitanso ndi kudzoza Akristu ndi mzimu kochitidwa ndi Mulungu, kuwabweretsera iwo ‘mphoto yosatha kapena choloŵa m’mwamba’ monga ana auzimu a Mulungu.—2 Akorinto 5:1, 5; Aefeso 1:13, 14; onani Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures.
Momvekera, kenaka, pangano latsopano siliri kakonzedwe kolekerera kotseguka kwa mtundu wonse wa anthu. Ilo liri chopereka cha lamulo cholinganizidwa mosamalitsa choloŵetsamo Mulungu ndi Akristu odzozedwa.
Ichi chiyenera kutithandiza ife kumvetsetsa 1 Timoteo 2:5, 6. Pano kulozera ku “[nkhoswe]” kunapangidwa pambuyo pa kuwonekera kusanu kwinako kwa liwulo m’makalata olembedwa poyambirirapo. Chotero, Timoteo ayenera kukhala atamvetsetsa unkhoswe wa Yesu kukhala thayo Lake la lamulo logwirizanitsidwa ndi pangano latsopano. The Pastoral Epistles, lolembedwa ndi Dibelius ndi Conzelmann, ikuvomereza kuti pa 1 Timoteo 2:5 ‘liwu lakuti “[nkhoswe]” liri ndi kufunika kwa lamulo,’ ndipo “ngakhale kuti m’chigawochi, lasiyanitsidwa ndi Aheb 8:6, [panganolo] silikutchulidwa, winawake ngakhale kuli tero ayenera kulingalira tanthauzo la ‘unkhoswe wa pangano,’ monga mmene mawu ozungulira lemba akusonyezera.” Profesa Oepke akunena kuti 1 Timoteo 2:5 ikusonyeza Yesu kukhala “loya wamkulu ndi wogwirizanitsa.”
Fanizo lamakono lingathandize kumveketsa bwino chimenechi, makamaka ngati inu simuli Mkristu wodzozedwa ndi mzimu. Ganizirani za mlandu wa lamulo mu umene loya wamkulu akuloŵetsedwamo. Ntchito yake singakhale kwakukulukulu monga ija ya loya wa nthaŵi zonse akumakangana kaamba ka chilungamo ndi ija ya yemwe akuchita unkhoswe kapena kupangitsa chimvano cha lamulo kukhala cholandirika ndi chopindulitsa kwa mbali ziŵiri. Ndithudi, inu simuli m’nkhani ya lamulo yoteroyo, chotero m’lingaliro limenelo iye sakutumikira monga loya wanu wamkulu. Komabe iye angakhale bwenzi lanu lachifupi kwambiri amene m’njira zina zake amakupatsani thandizo laphindu.
Nthaŵi zina ntchito ya loya wamkulu imatulutsa zotulukapo zomwe zimapindulitsa ena ambiri. Zirinso tero ndi zokwaniritsa za chilamulo za Yesu monga Nkhoswe ya pangano latsopano. Iko kumatulutsa chimene pangano la Chilamulo silinachite, “ufumu wa ansembe” wa kumwamba. (Eksodo 19:6; 1 Petro 2:9) Pambuyo pake Akristu odzozedwa mu Ufumu adzagwira ntchito limodzi ndi Yesu kuchokera kumwamba kubweretsa madalitso ku “mitundu yonse ya dziko lapansi.”—Genesis 22:18.
Anthu a mitundu yonse omwe ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha pa dziko lapansi amapindula ngakhale tsopano kuchokera ku mautumiki a Yesu. Ngakhale kuti iye sali Nkhoswe yawo ya lamulo, popeza kuti iwo sali mu pangano latsopano, iye ali njira yawo ya kufikira Yehova. Kristu ananena kuti: “Ine ndine njira, ndi chowonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa ine.” (Yohane 14:6) Onse omwe adzapeza moyo pa dziko lapansi ayenera kulunjikitsa mapemphero awo kwa Yehova kupyolera mwa Yesu. (Yohane 14:13, 23, 24) Yesu amatumikiranso monga Wansembe Wamkulu womvera chifundo yemwe ali wokhoza kugwiritsira ntchito mapindu a nsembe yake m’malo mwawo, kuwalola iwo kupeza chikhululukiro ndi chipulumutso potsirizira pake.—Machitidwe 4:12; Ahebri 4:15.
Mwakutero, 1 Timoteo 2:5, 6 sikugwiritsira ntchito “[nkhoswe]” m’lingaliro lalikulu lofala m’zinenero zambiri. Iyo sikunena kuti Yesu ali nkhoswe pakati pa Mulungu ndi mtundu wonse wa anthu. M’malomwake, iyo imalozera kwa Kristu monga Nkhoswe wa lamulo (kapena, “loya wamkulu”) wa pangano latsopano, imeneyi pokhala njira yokha mu imene Baibulo limagwiritsira ntchito liwulo. Yesu alinso dipo loyenerera kaamba ka onse okhala m’pangano limenelo, ponse paŵiri Ayuda ndi Akunja, omwe adzalandira moyo wosafa m’mwamba. Mtumwi Yohane analozera kwa amenewa pa 1 Yohane 2:2. Koma iye anasonyeza kuti enanso adzalandira phindu la nsembe ya Kristu: “Ndipo iye ndiye chiwombolo cha machimo athu; koma osati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.”
Awo a ‘dziko lonse’ ali onse omwe adzapeza moyo wosatha m’paradaiso ya pa dziko lapansi yobwezeretsedwa. Mamiliyoni a atumiki ovomerezedwa a Mulungu oterowo tsopano ali ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi chimenecho. Iwo amawona Yesu kukhala Mkulu Wansembe wawo ndi Mfumu kupyolera mwa amene angafikire Yehova tsiku ndi tsiku. Iwo amadalira pa dipo la Yesu, limene liripo kwa iwo, monga mmene lidzakhalirapo kwa amuna onga Abrahamu, Davide, ndi Yohane Mbatizi pamene iwowa awukitsidwa. (Mateyu 20:28) Chotero, nsembe ya Kristu idzatsogolera ku moyo wosatha kaamba ka mtundu wonse wa anthu omvera.
[Mawu a M’munsi]
a Kukambitsirana kwa mapangano kungapezedwe mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 1989, masamba 10-20.
[Chithunzi patsamba 31]
Pano pa Phiri la Sinai, Mose anatumikira monga nkhoswe ya pangano la Chilamulo
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.