Kuyamikira Chifukwa Chimene Mesiya Ankadzera
“Tapeza ife Mesiya.”—YOHANE 1:41.
1. Kodi nchilengezo chochititsa chidwi chotani chimene chalembedwa m’Baibulo, ndipo kodi chinalengezedwa liti?
MYUDA wotchedwa Andreya ndiye anapanga chilengezo chochititsa chidwi chomwe chiri pamwambapo kwa mbale wake zaka zoposa 1,950 zapitazo. Kodi mwakuzindikira kusangalatsa komwe kuli m’mawu olembedwa ndi mtumwi Wachikristu Yohane? Chaka chosaiŵalika chimenecho chinatchulidwa ndi katswiri Wachikristu wa mbiri yakale, Luka, kukhala ‘chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberiyo Kaisara.’ Chaka cha Tiberiyo cha 15, kuyambira panthaŵi imene analengezedwa kukhala wolamulira wa Roma, chinayambira m’September 28 C.E. ndipo chinathera m’September 29 C.E.—Luka 3:1-3, 21, 22; Yohane 1:32-35, 41.
2. Kodi ndimotani mmene ulosi wa Danieli unalozera ku chaka cha 29 C.E.?
2 Chaka cha kubwera kwa Mesiya chinanenedweratu pasadakhale molongosoka. Zaka 483 zinapitadi ndendende kuchokera pamene lamulo la kumanganso Yerusalemu linaperekedwa ndi mfumu Aritasasta ya ku Perisiya, umu munali m’chaka cha 20 cha kulamulira kwake, mu 455 B.C.E.a (Nehemiya 2:1-8) Mneneri Danieli ananeneratu ‘kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira [Mesiya Mtsogoleri, NW], kudzakhala masabata asanu ndi aŵiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu aŵiri’ (Danieli 9:25) Chotero, nyengo ya masabata aulosi awa 7 + 62 = 69 ndiyo ikalekanitsa zochitika zofunika ziŵirizi. Masabata enieni makumi asanu ndi limodzi mphambu asanu ndi aŵiri atawonkhetsedwa amapanga masiku 483. Mogwirizana ndi lamulo laulosi la ‘kuliyesa tsiku limodzi ngati chaka chimodzi,’ Mesiya akadza pambuyo pa zaka 483, mu 29 C.E.—Ezekieli 4:6.
3. (a) Kodi dzina laulemu lakuti “Mesiya” limatanthauzanji? (b) Kodi Mesiya anafunikira kukwaniritsa maulosi otani?
3 Mwachilongosoko, m’chaka cha 29 C.E., “anthu anali kuyembekezera” Mesiya. (Luka 3:1, 15) Dzina laulemu lakutilo “Mesiya” m’Chigiriki liri ndi tanthauzo lofanana ndi lakuti “Kristu”; onse aŵiriwo amatanthauza “Wodzozedwa.” (Yohane 1:41) Funso lomwe linavutitsa Ayuda ambiri linali ili, ‘Kodi Yehova Mulungu akadzoza yani kukhala mfumu yolamulira osati Aisrayeli okha komanso anthu onse?’ Kupyolera muulosi, wosankhidwayo anasonyezedwa mumbadwa ya Yuda mdzukulu wa Abrahamu. Kuwonjezera apa, Mesiya anafunikira kukhala wolowa nyumba wa mpando wachifumu wa mfumu Davide ya Yuda ndipo anafunikira kubadwira mumzinda wa Betelehemu komwe kunali kwawo kwa Davide.—Genesis 17:5, 6; 49:10; Salmo 132:11; Danieli 7:13, 14; Mika 5:2; Yohane 7:42.
Kuzindikira Kosalakwika
4, 5. (a) Kodi chinachitika nchiyani m’chaka chachikulu cha 29 C.E.? (b) Kodi ndim’njira yosalakwika iti mmene Mesiya wosankhidwayo anazindikiridwa?
4 M’chaka chachikulu chimenecho, 29 C.E., chomwe chinachitika ndi ichi: ‘Panadza mawu a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zakariya m’chipululu. Ndipo iye anadza ku dziko lonse la m’mbali mwa Yordano, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo.’ (Luka 3:2, 3) Uminisitala wa Yohane unakonzekeretsa Ayuda olapa kuvomereza kuyandikira kofulumira kwa kudza kwa Mesiya. Kuwonjezera apa, Yehova anampatsa chizindikiro Yohane. Iye adafunikira kufunafuna munthu amene iye ‘akawona mzimu utsikira, nukhala pa iye.’—Yohane 1:33.
5 Pambuyo pa kubatiza Yesu wa ku Nazarete, Yohane anakuwona kudzoza kosalakwika kumeneku. Yesu sanadzozedwe ndi mafuta, monga mmene anachitidwira Davide kholo lake la padziko lapansi, koma ndi mzimu woyera wa Yehova Mulungu. (1 Samueli 16:13; Machitidwe 10:38) Panthaŵi imodzimodziyo, liwu lenileni la Mulungu linati: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:16, 17) Monga mmene Yohane pambuyo pake anachitira umboni kuti: ‘Ndinawona mzimu ulikutsika kuchokera kumwamba monga nkhunda; nukhalabe pa iye. Ndipo ndaona ine, ndipo ndachita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi yemweyu.’—Yohane 1:32, 34.
6. Kodi Andreya ndi Yohane anatikhazikitsira chitsanzo chabwino chotani?
6 Mawuwa, ndiwo amene Yohane Mbatizi anadziŵitsira Yesu kwa ophunzira ake, akumamutchanso ‘Mwanawankhosa wa Mulungu amene achotsa chimo lake la dziko lapansi.’ (Yohane 1:29) Ophunzira aŵiri anavomereza mofulumira kwabasi. Pambuyo pokhala tsiku limodzi ndi Yesu, iwo anakhutiritsidwa mwantheradi. Dzina la mmodzi wa awa linali Andreya, amene anam’funafuna zedi mbale wake, Simoni Petro. Wophunzira winayo akudziŵika kukhala Yohane mwana wa Zebede, amene anadzakhala mtumwi wokondeka wa Yesu. Pambuyo pa kuchitira umboni ponena za Mesiya kwa pafupifupi zaka 70, Yohane ameneyu anafulumizidwa kulemba chidziŵitso chomwe chiri pamwambacho kuti ife tipindule nacho. Kodi chitsanzo chake ndi chija cha Andreya chimakhudza mtima wanu? Kodi inuyo muli wofunitsitsa monga momwe awa ndi “atumwi . . . a Mwanawankhosa” ena analiri kulengeza zowonadi zogwira mtima zonena za Mesiya?—Chibvumbulutso 1:9; 21:14; Yohane 1:35-41; Machitidwe 5:40-42.
Kudzozedwa Monga Mfumu ndi Mkulu wa Ansembe
7. Kodi nchifukwa ninji Yesu sanatumikire monga wansembe m’kachisi wa Yerusalemu?
7 Popeza kuti anabadwira mumtundu Wachiyuda, Yesu anakhala “wakumvera lamulo.” (Agalatiya 4:4) Chotero, pokhala wa fuko la Yuda, iye sakanatha kutumikira monga wansembe m’kachisi weniweni uja wa Yehova, amene ansembe ake anali mbadwa za Aroni wa fuko la Levi. ‘Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda; za fuko ili Mose sanalankhula kanthu ka ansembe,’ anawakumbutsa tero Akristu anzake mtumwi Paulo.—Ahebri 7:14.
8. Kodi kachisi wa padziko lapansi wa Yehova anachitira chithunzi chiyani?
8 Mtumwi Yohane analemba kuti: ‘Kuunika kwenikweni, kumene kuunikira anthu onse akulowa m’dziko lapansi.’ (Yohane 1:6-9) Pamene Yesu anabatizidwa, kunali ngati kuti mpamene kachisi wamkulu wauzimu anakhazikitsidwa, popeza kuti tsopano padali mkulu wa ansembe wauzimu amene akapulumutsa anthu kuchoka muukapolo wauzimu wa dziko lamdima la Satana.—Ahebri 8:1-5; 9:24.
9, 10. (a) Kodi mawu a Yesu akuti, ‘Nsembe ndi chopereka simunazifuna’ ndi akuti ‘koma thupi munandikonzera ine’ anatanthauzanji? (b) Kodi Yesu payekha analingalira bwanji za ichi?
9 Yesu ankapemphera panthaŵi ya kubatizidwa kwake. M’Baibulo munalembedwa mawu ake ena apadera, omwe pambuyo pake anagwidwa mawu ndi mtumwi Paulo: ‘Nsembe ndi chopereka simunazifuna, koma thupi munandikonzera ine. Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunakondwera nazo; pamenepo ndinati, Taonani, ndafika, (pamutu pake pa bukhu palembedwa za ine) kudzachita chifuniro chanu, Mulungu.’—Ahebri 10:5-7; Luka 3:21.
10 Chotero, Yesu anaugwiritsira ntchito kwa mwiniyekha ulosi wa pa Salmo 40:6-8, umene unaneneratu chifuno cha Yehova cha kuthetsa nsembe zanyama zoperekedwa ndi ansembe a Aroni pakachisi wa mu Yerusalemu. Yehova ‘sanakondwere’ nazo nsembe zimenezo, popeza kuti zinali kokha nyama zenizeni komano zosakhoza kulipiriratu chimo la anthu. Chotero, Yehova anakonzekera thupi la munthu wangwiro kuti Yesu aipereke nsembeyo. Mulungu anasamutsira moyo wa Mwana wake wakumwamba m’mimba ya namwali Wachiyuda. Choncho Yesu anabadwa wosaipitsidwa ndi chimo la Adamu. Iye anali Mwana wangwiro wa Mulungu, amene moyo wake ukakhoza kulipirira chimo la anthu. (Luka 1:30-35) Monga mmene Salmo 40:8 linaneneratu, kuchita chifuniro cha Atate ndiko kunali chokhumba chamtima wonse cha Yesu. ‘Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha.’—Ahebri 10:10, 11.
11. Kodi imfa ya Mesiya inakwaniritsa ulosi uti, ndipo kodi ‘inaleketsa nsembe’ bwanji?
11 Nsembe ya moyo waumunthu wa Yesu yoperekedwa kamodzi kwatha inachotsapo kufunikira kupereka nsembe zowonjezereka pakachisi yeniyeni mu Yerusalemu. Kuwonjezera apa, imfa yake inachitika pa Tsiku la Paskha wa 33 C.E. Panthaŵiyi panali patapita zaka zitatu ndi theka pambuyo pa kubatizidwa kwake. Zaka zitatu ndi theka zikakwanira theka la sabata yaulosi. (Numeri 14:34) Chotero zinthu zinachitikadi ndendende monga mmene Danieli ananeneratu ponena za kulikhidwa kwa Mesiya kuti: “Ndi pakati pa sabata adzaleketsa nsembe yophera ndi nsembe yaufa.” (Danieli 9:26, 27) Chinkana kuti mathayo a ansembe m’Yerusalemu anagwirabe ntchito kufikira pamene kachisiyo anawonongedwa mu 70 C.E., nsembe zimene ansembewo anazipereka m’zakazo zinaleka kukhala ndi phindu lirilonse, pokhala zinalowedwa mmalo ndi nsembe ya Yesu yopambana.—Mateyu 23:37, 38.
12. Kodi kukhala kwa Yesu wansembe nkoposa motani kwa Aroni?
12 Aroni anali woyamba mwa akulu ansembe Achiisrayeli olowanalowana m’malo. Pambuyo pa kudzozedwa kwake ndi mafuta oyera, iye anafunikira kuyembekezera m’chihema kwa masiku asanu ndi aŵiri asanapatsidwe mphamvu ya kutumikira monga mkulu wa ansembe. (Levitiko 8:12, 33) Mofananamo, Yesu anali nayo nyengo ya kuyembekezera asanapatsidwe mphamvu ya kuchitapo kanthu mmalo mwa anthu. Iyi inali nthaŵi kuchokera pamene anadzozedwa monga Mkulu wa Ansembe kufikira pa kuukitsidwa kwake. Mosiyana ndi Aroni, Mwana wa Mulungu wosafayu safunikira om’lowa mmalo, ndipo iye akutumikira ponse paŵiri monga Wansembe ndi Mfumu ‘monga mwa chilongosoko cha Melikizedeke.’—Salmo 110:1-4; Genesis 14:18-20; Ahebri 6:20; 7:1-3, 11-17, 23-25.
13. (a) Kodi ndithayo lolemera lotani limene linaikidwa pa mkulu wa ansembe mu Israyeli? (b) Kodi ndimotani mmene Yesu Kristu wasenzera thayo lalikulu kuposa ili?
13 Mu Israyeli wakale, thayo lalikulu la kuphunzitsa kolondola kwa chipembedzo linaikidwa pa mkulu wa ansembe. (Levitiko 10:8-11; Malaki 2:7) Mogwirizana ndi izi Yesu anadziŵikitsa zofunikira zolungama za Yehova kaamba ka anthu onse amene akufuna kulandira Ufumu ndi moyo wosatha. (Mateyu 6:9, 10, 33; 7:28, 29; 11:12; 25:34, 46) Pamene anali mu sunagoge mu Nazarete, Yesu anaŵerenga ndi kuwugwiritsira ntchito kwa iye yekha ulosi uwu: ‘Mzimu wa Yehova uli pa ine, chifukwa chake iye anandidzoza ine ndiuze anthu osauka mbiri yabwino.’ Kenaka, pambuyo pa kuthera nthaŵi yakutiyakuti mu Kapernao, iye anati: ‘Kundiyenera ine ndilalikire mbiri yabwino ya ufumu wa Mulungu ku midzi inanso; chifukwa ndinatumidwa kudzatero.’ (Luka 4:18, 19, 43; Yesaya 61:1, 2) Yesu anaphunzitsanso atsatiri ake 70 kufutukula ntchito iyi ya kulalikira Ufumu, ndipo ananeneratu kuti iwo akachita ntchito yaikulu kuposa imene iye anaichita. (Luka 10:1-9; Yohane 14:12) Ichi chinayala maziko a ndawala ya maphunziro a Baibulo a dziko lonse amene Yesu akatsogolera kupyolera mwa ‘kapolo wokhulupirika,’ wopangidwa ndi atsatiri ake odzozedwa.—Mateyu 24:45-47; 28:19, 20.
M’chilikizi Wamkulu wa Ufumu wa Yehova
14. (a) Kodi nchifukwa ninji mkulu wa ansembe wa mu Israyeli analowera m’Malo Opatulikitsa pa Tsiku La Chitetezero la chaka ndi chaka? (b) Kodi nsembe ya chofukiza cha fungo lokoma inachitira chithunzi chiyani?
14 Chifukwa chofunika kwenikweni chimene Mwana wa Mulungu anadzera padziko lapansi sichinali kupulumutsa anthu. Mmalo mwake, chinali cha kuthetsa nkhani zodzetsa chitonzo zodzutsidwa ndi Satana zokhudza ufumu wa Yehova. Chidziŵitsochi tingachimvetsetse mwakuunikira pa Tsiku la Chitetezero la chaka ndi chaka la Israyeli, pamene mkulu wa ansembe weniweni adafunikira kulowa m’Malo Opatulikitsa nthaŵi zambiri. Choyamba analowamo ndi chofukiza cha fungo lokoma, chimene chinakathiridwa pa mbale ya zofukiza yodzala ndi makala amoto. (Levitiko 16:12-16) Ichi chinaimira bwino lomwe chimene mnzake wamakono wa Mkulu wa Ansembe akachita padziko lapansi asanakwere kunka kumwamba kukawonekera pamaso pa Yehova ndi mtengo wa nsembe yake yaumunthu.b (Ahebri 9:24) Monga momwe zasonyezedwera ndi kugwiritsiridwa ntchito kwa zofukizira, njira ya Yesu ya kukhulupirika inazindikiridwa ndi mapemphero owona mtima, changu champhamvu kaamba ka kulambira kowona, ndi chikondi chachikulu kaamba ka Yehova. (Salmo 141:2; Marko 1:35; Yohane 2:13-17; 12:27, 28; 14:30, 31; Ahebri 5:7) Yesu anapeza chipambano m’kusunga umphumphu wopanda chilema poyang’anizana ndi ziyeso zonse zowopsa, kusekedwa, ndi chizunzo chokakala chounjikidwa pa iye ndi Satana ndi makamu ake.—Miyambo 27:11; Mateyu 22:15-18; Marko 14:60-65; 15:16-32; Luka 4:13, 29; Yohane 8:44, 59.
15. Kodi tingachisonyeze motani chiyamikiro kwa Yehova kaamba ka kupereka mkulu wa ansembe wabwino koposayu? (Ahebri 10:21-26)
15 Yesu anafupidwa ndi chiukiriro cha moyo wosafa kumwamba, kaamba ka kuchilikiza ufumu wa Yehova. Tiyenera kukhala oyamikira chotani nanga kwa Yehova kaamba ka kutipatsa Mkulu wa Ansembe wabwino koposayu! ‘Popeza tsono tiri naye mkulu wa ansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu.’ (Ahebri 4:14) Kodi kutsanzira chitsanzo chaumphumphu cha Yesu ndiko chokhumba chanu chochokera mumtima, mosasamala kanthu za chimene Mdyerekezi angachite? Ngati ndi tero, mungadalire kuti muli nalo thandizo, ndipo mungakhale ndi chipambano. Chifukwa chakuti thandizo labwino koposa liripo. ‘Pakuti sitiri naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofoka zathu; koma wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo. Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthaŵi yakusowa.’—Ahebri 4:15, 16; 5:7-10; Afilipi 4:13; 1 Yohane 2:1, 2.
Kufunikira Kuwongolera
16. Kodi ophunzira a Mesiya oyambirira anali ndi ziyembekezo zotani ponena za kulamulira kwa Ufumu wake?
16 Andreya ndi Yohane anafulumira kumuzindikira Mesiya wowona, koma iwo limodzinso ndi ophunzira ena anafunikira kuphunzira zambiri. (Yohane 16:12, 13) Mofanana ndi Ayuda achipembedzo ambiri m’nthaŵiyo, iwo anayembekezera kuti Ufumu Waumesiya ukayamba kulamulira m’nthaŵi ya kumbuyoyo ndikuti ukawonjola mtundu wa Israyeli ndi likulu lake, Yerusalemu, kulamulidwa ndi Akunja. (Luka 2:38; 3:15; 19:11; 23:51; 24:21) Komabe, kodi kuteroko kukabweretsa mapindu osatha otani kwa anthu ochimwa?
17, 18. Kodi nchifukwa ninji Yesu anapereka fanizo la ‘munthu wa fuko lomveka’?
17 Kuti achotse uchimo ndi imfa mwa nzika zake za kutsogolo za Ufumuwo, kunali kofunika kuti choyamba Mesiya aphedwe monga mwanawankhosa woperekedwa nsembe. (Yohane 1:29; Yesaya 53:7, 12) Pamene Yesu ananeneratu mmene ichi chikachitikira ndi mmene akaukitsidwira, Petro anayankha kuti: ‘Dzichitireni chifundo, Ambuye; sichidzatero kwa inu.’ (Mateyu 16:21, 22) Komabe, Yesu anadziŵa kuti ophunzira ake ‘sanazindikira mawuwo.’—Marko 9:31, 32; yerekezerani ndi Mateyu 17:22, 23.
18 Paulendo wake womalizira kunka ku Yerusalemu, Yesu anachinena ichi momvekera zedi. (Mateyu 20:18, 19) Iye anasonyezanso phindu lalikulu limene imfa yake ikabweretsa, nati: ‘Mwana wa munthu anadza . . . kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.’ (Mateyu 20:28) Kuyembekezera kolakwika kunakaniza ophunzira ake kuzindikira chimenechi. Luka analemba motere: ‘Chifukwa anali iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uwonekere pomwepo.’ Kuti awongolere malingaliro awo, Yesu anapereka fanizo m’limene anadzifanizitsa yekha ndi ‘munthu wa fuko lomveka’ amene choyamba anafunikira kunka “ku dziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu.” (Luka 19:11, 12) “Dziko” limeneli linatanthauza kumwamba, kumene Yesu anakwera pambuyo pa imfa ndi kuukitsidwa kwake.
19. (a) Kodi ophunzira a Yesu anafotokoza ziyembekezo zolakwika zotani pambuyo pa kuukitsidwa kwake? (b) Kodi ndikusintha kotani muunansi wa Mulungu ndi anthu kumene kunachitika pa Pentekoste wa 33 C.E.? (Ahebri 8:7-9, 13)
19 Komabe, Yesu asanakwere, ophunzira ake anam’funsa kuti: “Ambuye, kodi nthawi yino mubwezera ufumu kwa Israyeli?” (Machitidwe 1:6) Kodi Yesu anawalandula chifukwa cha kufunsaku? Ayi, iye analongosola kuti nthaŵi inali isadafikebe ndikuti iwo anafunikira kudzitanganitsa m’ntchito yofunika ya kuchitira umboni ponena za Mesiya wowona. (Machitidwe 1:7, 8) Unansi wa pangano la Israyeli wa kuthupi ndi Mulungu udali pafupi kutha. Chotero, Ufumu Waumesiya wa kutsogolowo sukabwezeretsedwa kumtundu wa padziko lapansi wosakhulupirikawo. Yesu anauza omtsutsa Achiyuda kuti: ‘Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.’ (Mateyu 21:43) Masiku khumi pambuyo pa kukwera kwa Yesu kunka kumwamba, mtundu umenewo unabadwa. Mzimu woyera unatsanuliridwa pa ophunzira a Yesu 120, ndipo motero iwo anadzozedwa kukhala “oyera” a Mulungu ndi ‘olowa nyumba anzake a Kristu’ mu Ufumu Waumesiya womwe ukudzawo.—Danieli 7:13, 14, 18; Aroma 1:7; 8:1, 16, 17; Machitidwe 2:1-4; Agalatiya 6:15, 16.
20. Mosasamala kanthu za kukhala ndi ziyembekezo zolakwika, kodi nchiyani chimene Akristu a m’zaka za zana loyamba anachita?
20 Ngakhale pambuyo pa kudzozedwa kwawoko, Akristu a m’zaka za zana loyamba anali ndi ziyembekezo zolakwika. (2 Atesalonika 2:1, 2) Komano mmalo mwa kuleka chifukwa cha kusakhutira, iwo anakuvomereza kuwongolera modzichepetsa. Atapatsidwa mphamvu ndi mzimu woyera wa Mulungu, iwo anailandira mwachimwemwe ntchito ya kuchitira umboni ndi “kuphunzitsa anthu a mitundu yonse.”—Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 1:8; Akolose 1:23.
21. Kodi ndi mafunso otani amene adzalingaliridwa m’nkhani yathu yotsatira?
21 Nanga bwanji ponena za zaka zathu za zana la 20? Kodi atumiki amakono a Yehova anali amaso ndikukhazikitsidwa kwa Ufumu Waumesiya wa Yehova? Ndipo mofanana ndi anzawo a m’zaka za zana loyamba, kodi iwo anafunikira kuwongolera ziyembekezo zawo m’njira zina?
[Mawu a M’munsi]
a Onse aŵiri The Encyclopedia Americana ndi Great Soviet Encyclopedia amavomerezana kuti kulamulira kwa Aritasasta kunatha mu 424 B.C.E. Kodi kunayamba liti? Mu 474 B.C.E. Kuchilikiza ichi, malembo ozokotedwa ofukulidwa pansi ena ali ndi madeti a chaka cha 50 cha Aritasasta; ena amasonyeza kuti iye analowedwa mmalo m’chaka chake cha 51. Titapenda chafutambuyo zaka zokwanira 50 kuchokera mu 424 B.C.E., timapeza 474 B.C.E. kukhala deti limene iye anayamba kulamulira kwake. Chotero, chaka chokwanitsa 20 cha Aritasasta, pamene lamulo lija linaperekedwa, chikakhala zaka zokwanira 19 m’kulamulira kwake, ndiko kuti, mu 455 B.C.E. Kaamba ka tsatanetsatane wowonjezereka, onani Insight on the Scriptures, Volyumu 2, tsamba 616, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Onani The Watchtower ya April 1, 1974, tsamba 222.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi dzina laulemu lakuti “Mesiya” limatanthauzanji?
◻ Kodi ndichochitika chapadera chotani chimene chinachitika m’chaka cha 29 C.E.?
◻ Kodi Mesiya ‘analeketsa motani nsembe pakati pa sabata’?
◻ Chiyambire kudzozedwa kwake, kodi ndi thayo lotani limene Yesu wasenza?
◻ Kodi nchiyani chimene chinali chifuno chachikulu cha kudza koyamba kwa Mesiya, ndipo kodi ichi chiyenera kutiyambukira motani?
[Chithunzi patsamba 13]
Kulowa koyamba kwa mkulu wa ansembe m’Malo Opatulikitsa kunachitira chithunzi chinthu china chofunika kwenikweni kuposa chipulumuko cha anthu