Popeza “Mwadziwa Mulungu,” Kodi Muyenera Kuchita Chiyani?
“Mwadziwa Mulungu.”—AGAL. 4:9.
1. N’chifukwa chiyani oyendetsa ndege amafunika kutsatira mndandanda wa zinthu zofunika?
ANTHU amene amayendetsa ndege zina amaonetsetsa kuti asananyamuke, atsatira mndandanda wa zinthu 30 zofunika. Kupanda kutsatira zinthu zimenezi, akhoza kuchita ngozi. Makamaka oyendetsa amene akhala akugwira ntchitoyi kwa nthawi yaitali ndi amene amalimbikitsidwa kutsatira zinthuzi. Anthu oterewa akhoza kuyamba kutayirira n’kumanyalanyaza malangizo okhudza ntchitoyi.
2. Kodi Akhristu ayenera kuchita chiyani?
2 Mofanana ndi woyendetsa ndege amene amafuna kupewa ngozi, nanunso muyenera kutsatira mndandanda wa zinthu zimene zingathandize kuti chikhulupiriro chanu chikhalebe cholimba. Kaya mwangobatizidwa kumene kapena mwatumikira Mulungu zaka zambiri, nthawi ndi nthawi muyenera kuona ngati chikhulupiriro chanu chidakali cholimba komanso ngati mukupitirizabe kudzipereka kwa Yehova Mulungu. Kulephera kuchita zimenezi kungachititse kuti muyambe kufooka mwauzimu. Baibulo limatichenjeza kuti: “Amene akuyesa kuti ali chilili asamale kuti asagwe.”—1 Akor. 10:12.
3. Kodi Akhristu a ku Galatiya anafunika kuchita chiyani?
3 Akhristu a ku Galatiya anayenera kuonanso kuzama kwa chikhulupiriro chawo. Iwo anayeneranso kuona ngati ankagwiritsa bwino ntchito ufulu wawo monga Akhristu. Kudzera mu nsembe ya dipo lake, Yesu anatsegula njira kuti amene angamukhulupirire adziwe Mulungu. Iwo analinso ndi mwayi wokhala ana a Mulungu. (Agal. 4:9) Kuti zimenezi zitheke, Akhristu a ku Galatiya anayenera kukana ziphunzitso za Ayuda olimbikitsa kuti azitsatira Chilamulo cha Mose. Akhristu osadulidwa a mitundu ina, amene anali m’mipingo, anali oti sanatsatirepo Chilamulo. Choncho Akhristu onse, achiyuda ndi a mitundu ina omwe, ankafunika kukula mwauzimu. Iwo anafunika kuzindikira kuti kutsatira Chilamulo cha Mose si kumene kukanasonyeza kuti iwo anali olungama.
ZIMENE MUNTHU ANGACHITE KUTI ADZIWE MULUNGU
4, 5. Kodi cholinga cha malangizo a Paulo kwa Akhristu a ku Galatiya chinali chiyani? Nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zilinso zothandiza kwa ife?
4 Cholinga cha malangizo a mtumwi Paulo kwa Akhristu a ku Galatiya chinali kuthandiza Akhristu oona kuti asasiye kutsatira choonadi cha m’Baibulo n’kubwerera ku zinthu zakale. Yehova anauzira mtumwiyu kulimbikitsa Akhristu onse kukhala olimba. Malangizowa sankapita kwa Akhristu a ku Galatiya okha.
5 Tonsefe tingachite bwino kukumbukira zimene zinachitika kuti timasuke ku ukapolo wauzimu n’kukhala Mboni za Yehova. Kuti muthe kukumbukira bwino, taganizirani mafunso awiri awa: Kodi munachita zinthu ziti kuti muyenerere kubatizidwa? Kodi mukukumbukira zimene zinakuthandizani kudziwa Mulungu komanso kudziwidwa ndi iye n’kuyamba kusangalala ndi ufulu weniweni wauzimu?
6. Kodi tikambirana zinthu ziti?
6 Pali zinthu 9 zimene aliyense anachita kuti ayenerere kubatizidwa. Zinthu zimenezi tingaziyerekezere ndi zimene woyendetsa ndege amatsatira asananyamuke ndipo zikupezeka pa kabokosi kakuti, “Zofunika Kuti Munthu Abatizidwe Komanso Apitirize Kukula Mwauzimu.” Kukumbukira zinthu zimenezi nthawi zonse kungatithandize kuti tisabwerere ku zinthu za m’dzikoli. Kutsatira zinthu zonse zofunika kuchita asananyamuke, kumathandiza woyendetsa ndege kupewa ngozi. Nafenso tikhoza kupitiriza kutumikira Mulungu mokhulupirika ngati nthawi zonse timaganizira zinthu zimene tinachita kuti tiyenerere kubatizidwa.
AMENE AMADZIWIDWA NDI MULUNGU AMAPITIRIZA KUKULA MWAUZIMU
7.Kodi tiyenera kutsatira chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
7 Mndandanda wa zinthu zimene woyendetsa ndege amatsatira umamuthandiza kukumbukira kuti nthawi zonse amayenera kuchita zinazake asananyamuke. Nafenso tiyenera kumaona mmene moyo wathu wauzimu ulili komanso zinthu zauzimu zimene timachita kuyambira pamene tinabatizidwa. Paulo analembera Timoteyo kuti: “Gwiritsitsabe chitsanzo cha mawu olondola amene unawamva kwa ine, komanso chikhulupiriro ndi chikondi zomwe zili mwa Khristu Yesu.” (2 Tim. 1:13) “Mawu olondola” amenewa amapezeka m’Mawu a Mulungu. (1 Tim. 6:3) Munthu amatha kujambula chithunzi kuti anthu adziwe mmene chinthu chinachake chimaonekera. Mofanana ndi zimenezi, “chitsanzo cha mawu olondola” chimatithandiza kudziwa ndiponso kutsatira zimene Yehova amafuna kuti tizichita. Tsopano tiyeni tikambirane zinthu zimene zinatithandiza kuti tiyenerere kubatizidwa. Zimenezi zitithandiza kuona ngati tikutsatira chitsanzo cha mawu olondola.
8, 9. (a) N’chifukwa chiyani tifunika kupitiriza kuphunzira komanso kulimbitsa chikhulupiriro chathu? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kufunika kokula mwauzimu komanso chifukwa chake sikutha.
8 Chinthu choyambirira chimene timachita ndi kuphunzira. Kenako timayamba kukhulupirira. Koma kuti tikule mwauzimu, timafunika kupitiriza kuphunzira komanso kulimbitsa chikhulupiriro chathu. (2 Ates. 1:3) Chinthu ‘chikamakula,’ chimasintha, choncho munthu akamakula mwauzimu, amayenera kusintha. Motero tikabatizidwa, timayenera kupitiriza kukula mwauzimu osati kungokhala pamodzimodzi.
9 Tingayerekezere kukula kwathu mwauzimu ndi mmene mtengo umakulira. Mtengo ukhoza kukula kwambiri makamaka ngati uli ndi mizu yambiri komanso ngati mizu yakeyo inapita pansi kwambiri. Mwachitsanzo, mitengo ina ya mkungudza ya ku Lebanoni imakhala yaitali ngati nyumba yosanjikizana ka 12 ndipo imakhala ndi mizu yolimba komanso yopita pansi kwambiri. Thunthu la mitengoyi limakhala lalikulu moti mukhoza kuzunguliza chingwe chokwana mamita 12. (Nyimbo 5:15) Mitengoyi ikakula kwambiri chonchi, imapitirizabe kukula ngakhale kuti kukulako sikuonekera kwambiri. Chaka chilichonse thunthu la mtengowu limakulabe komanso mizu yake imakulabe ndiponso kupita pansi. Izi zimachititsa kuti mtengowo ukhale wolimba kwambiri. Zimenezi n’zimenenso Akhristu ayenera kuchita. Tikangoyamba kuphunzira Baibulo tingathe kupita patsogolo mwamsanga ndipo kenako kubatizidwa. Abale ndi alongo amaona mosavuta kuti tikupita patsogolo. Tikhozanso kuyenerera upainiya kapena maudindo ena. Koma pakapita zaka, sizingamaonekenso kwambiri kuti tikukula mwauzimu. Komabe, tifunika kulimbitsa chikhulupiriro chathu komanso kupitiriza kuphunzira “kufikira tidzakhale munthu wachikulire, wofika pa msinkhu wauchikulire umene Khristu anafikapo.” (Aef. 4:13) Choncho mofanana ndi mtengo, tiyenera kupitiriza kukula mwauzimu n’kukhala Mkhristu wolimba.
10. N’chifukwa chiyani Akhristu onse ayenera kupitirizabe kukula mwauzimu?
10 Ngakhale kuti ndife Akhristu olimba, tiyenera kumakulabe. Tizipitiriza kuphunzira komanso kulimbitsa chikhulupiriro chathu. Zimenezi zimathandiza kuti tizike mizu m’Mawu a Mulungu. (Miy. 12:3) Mu mpingo wachikhristu muli abale ndi alongo ambiri amene achita zimenezi. Mwachitsanzo, mbale wina amene wakhala mkulu kwa zaka zoposa 30, amaona kuti akukulabe mwauzimu. Iye anati: “Panopa ndikumvetsa kwambiri Baibulo. Nthawi zonse ndimafufuza njira zoti nditsatire mfundo ndi malamulo a m’Baibulo. Komanso ndayamba kukonda kwambiri utumiki.”
PITIRIZANI KULIMBITSA UBWENZI WANU NDI MULUNGU
11. N’chiyani chingatithandize kudziwa bwino Yehova?
11 Kukula mwauzimu kumaphatikizapo kulimbitsa ubwenzi ndi Atate wathu, Yehova. Iye amafuna tizidziwa kuti amasangalala nafe, amatikonda komanso amatiteteza. Amafuna kuti tizimva ngati mmene mwana amamvera akakumbatiridwa ndi kholo lake lomwe limamukonda kapena ngati mmene timamvera tikakhala ndi mabwenzi athu apamtima. Koma monga mukudziwa, ubwenzi woterewu sungangochitika lero ndi lero. Pamafunika nthawi kuti tim’dziwe bwino Yehova komanso kuti tiyambe kumukonda kwambiri. Choncho kuti mudziwe bwino Yehova, m’pofunika muzipeza nthawi yowerenga Mawu ake tsiku lililonse. Muyeneranso kuyesetsa kumawerenga magazini onse a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! komanso mabuku ena othandiza kuphunzira Baibulo.
12. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tizidziwidwa ndi Yehova?
12 Mabwenzi a Mulungu amakula mwauzimu akamapemphera mochokera pansi pa mtima komanso akamacheza ndi abale ndi alongo awo. (Werengani Malaki 3:16.) ‘Makutu a Yehova amamva pembedzero lawo.’ (1 Pet. 3:12) Mofanana ndi kholo lachikondi, Yehova amamvetsera mwatcheru mapemphero athu opempha kuti atithandize. Choncho tiyenera ‘kulimbikira kupemphera.’ (Aroma 12:12) Sitingathe kukhala Mkhristu wolimba popanda thandizo la Mulungu. Mavuto amene timakumana nawo m’dzikoli, sitingathe kuthana nawo tokha. Kusiya kupemphera kuli ngati kudzidulira thandizo limene Yehova mofunitsitsa amatipatsa kuti tikhale olimba. Kodi mumakhutira ndi mapemphero anu kapena mukuona kuti ndi ofunika kuwakonza kuti azikhala ochokera pansi pa mtima?—Yer. 16:19.
13. N’chifukwa chiyani kusonkhana ndi Akhristu kuli kofunika kuti tikule mwauzimu?
13 Yehova amasangalala ndi anthu amene “amathawira kwa iye kuti apeze chitetezo.” (Nah. 1:7) Choncho ngakhale kuti tadziwa Mulungu, tiyenera kupitiriza kusonkhana ndi Akhristu anzathu nthawi zonse. M’dziko lovutali, tingachite bwino kumakhala pafupi ndi abale ndi alongo athu omwe angatilimbikitse. Kodi kuchita zimenezi kuli ndi phindu lotani? Mu mpingo wachikhristu timapezamo anthu amene angatilimbikitse “pa chikondi ndi ntchito zabwino.” (Aheb. 10:24, 25) Kuti tithe kusonyezana chikondi chimene Paulo ananena palembali, tiyenera kumasonkhana komanso kumachita zinthu ndi Akhristu anzathu. Choncho nthawi zonse muzionetsetsa kuti mukupezeka pa misonkhano komanso kupereka ndemanga.
14. N’chifukwa chiyani tinganene kuti munthu amafunika kusintha komanso kulapa nthawi ndi nthawi?
14 Kuti tikhale Mkhristu tinalapa machimo athu komanso kutembenuka. Koma kulapa machimo sikumatha. Popeza ndife opanda ungwiro, uchimo uli ngati njoka imene yakonzeka kuti itilume nthawi iliyonse. (Aroma 3:9, 10; 6:12-14) Chotero si bwino kumadzinamiza kuti sitingachimwe. Ubwino wake Yehova amatilezera mtima tikamayesetsa kupewa zinthu zimene zingatichimwitse komanso tikamayesetsa kusintha. (Afil. 2:12; 2 Pet. 3:9) Chofunika n’kugwiritsa ntchito nthawi yathu ndiponso zinthu zathu potumikira Yehova osati kumangochita zofuna zathu. Mlongo wina analemba kuti: “Ndinaleredwa m’banja la Mboni koma sindinkamudziwa bwino Yehova. Ndinkaona kuti Yehova ndi woopsa kwambiri ndipo sindingathe kumukondweretsa.” Chifukwa choti ankalakwitsa zinthu zina, iye ankaona kuti sanali pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Mlongoyo ananenanso kuti: “Ndinkakonda Yehova ndithu koma kungoti sindinkamudziwa bwinobwino. Nditapemphera kwambiri, ndinayamba kusintha maganizo. Ndinazindikira kuti Yehova ankanditsogolera ngati kamwana ndipo ankandithandiza pa vuto lililonse limene ndinkakumana nalo. Ankandisonyeza mokoma mtima njira yoyenera kuyenda.”
15. Kodi Yesu ndi Atate ake amadziwa chiyani zokhudza ife?
15 Petulo ndi atumwi ena atatulutsidwa m’ndende mozizwitsa, mngelo wa Mulungu anawauza kuti ‘apitirize kuuza anthu’ uthenga wabwino. (Mac. 5:19-21) Kugwira nawo ntchito yolalikira mlungu uliwonse ndi chimodzi mwa zinthu zimene tiyenera kuchita. Yesu ndi Atate ake amadziwa chikhulupiriro chimene tili nacho komanso amayamikira zimene timachita mu utumiki. (Chiv. 2:19) M’bale amene tamutchula m’ndime 10 uja ananenanso kuti: “Utumiki ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu.” Nafenso tiyenera kuona choncho.
16. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira za kudzipereka kwathu kwa Yehova?
16 Nthawi ndi nthawi muziganizira za kudzipereka kwanu. Chinthu chamtengo wapatali kwambiri chimene tili nacho ndi ubwenzi wathu ndi Yehova. Iye amadziwa anthu ake. (Werengani Yesaya 44:5.) Muziganizira za ubwenzi wanu ndi Yehova ndipo muzimupempha kuti akuthandizeni kuulimbitsa. Muziganiziranso za tsiku limene munabatizidwa chifukwa ndi tsiku lofunika kwambiri. Zimenezi zidzakuthandizani kukumbukira kuti pamene munabatizidwa, munasonyeza kuti munali mutasankha chinthu chofunika kwambiri kuposa chilichonse.
KUPIRIRA N’KOFUNIKA KUTI MUKHALEBE PA UBWENZI NDI MULUNGU
17. N’chifukwa chiyani kupirira kuli kofunika kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi Yehova?
17 M’kalata yake yopita kwa Agalatiya, Paulo anatsindika kufunika kopirira. (Agal. 6:9) Masiku ano, Akhristu amafunikanso kupirira. N’zoona kuti muzikumana ndi mavuto koma Yehova azikuthandizani. Muzipempha mzimu wake nthawi zonse. Mudzasangalala kwambiri mukaona kuti m’malo mwa chisoni mukukhala osangalala ndipo m’malo mokhumudwa mukukhala ndi mtendere mumtima. (Mat. 7:7-11) Ndi bwino kumaganizira mfundo iyi: Ngati Yehova amasamalira mbalame, kuli bwanji inuyo amene mumam’konda ndipo munadzipereka kwa iye? (Mat. 10:29-31) Kaya mukumane ndi mavuto otani, musafooke ndipo musataye mtima. Yehova adzatidalitsa kwambiri chifukwa chakuti amatidziwa.
18. Popeza ‘tadziwa Mulungu,’ kodi tiyenera kuchita chiyani?
18 Ngati mwayamba kudziwa Mulungu ndipo mwabatizidwa posachedwapa, kodi muyenera kuchita chiyani? Pitirizani kuphunzira za Yehova kuti ubwenzi wanu ndi iye ulimbe kwambiri. Ngati munabatizidwa kalekale, kodi muyenera kuchita chiyani? Muyenera kupitiriza kuphunzira za Yehova mozama kwambiri. Tisaganize kuti tafika ponena kuti, ‘Aaa basi ubwenzi wanga ndi Yehova uli bwino.’ M’malomwake, tizidzifufuza nthawi ndi nthawi kuti tione zimene tiyenera kuchita. Tizichita zimenezi n’cholinga choti tizilimbitsabe ubwenzi wathu ndi Yehova, yemwe ndi Atate wathu, Mnzathu wapamtima komanso Mulungu wathu.—Werengani 2 Akorinto 13:5, 6.