Muli Olandiridwa
MWINA nthawi ina munadutsa pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova ya m’dera lanu n’kumadzifunsa kuti, kodi mumachitika chiyani mmenemu? Kodi mukudziwa kuti aliyense akhoza kukhala nawo pamisonkhano yawo imene imachitika mlungu ndi mlungu? Alendo ndi olandiridwa ndi manja awiri.
Koma mwina mungakhale ndi mafunso monga awa: N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimasonkhana pamodzi? Kodi pamisonkhanoyi pamachitika chiyani? Ndipo kodi anthu ena omwe si Mboni za Yehova anena chiyani za misonkhano imeneyi?
“Sonkhanitsani Anthu”
Kuyambira kale, anthu amasonkhana kuti alambire ndi kuphunzira za Mulungu. Pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, Aisiraeli anauzidwa kuti: “Sonkhanitsani anthu, amuna ndi akazi ndi ana aang’ono, ndi mlendo wokhala m’midzi mwanu, kuti amve, ndi kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kuchita mawu onse a chilamulo ichi.” (Deuteronomo 31:12) Choncho, m’nthawi ya Aisiraeli ana ndi akulu omwe, ankaphunzitsidwa kulambira ndi kumvera Yehova Mulungu.
Patapita zaka pafupifupi 1,500 mpingo wachikhristu utakhazikitsidwa, misonkhano inakhalabe mbali yofunika pa kulambira koona. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Tiyeni tiganizirane wina ndi mnzake, kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga chilili chizolowezi kwa ena, koma tilimbikitsane wina ndi mnzake.” (Aheberi 10:24, 25) Banja limakhala lolimba likamachitira zinthu pamodzi, nawonso atumiki a Mulungu amakhala okondana kwambiri akamasonkhana pamodzi polambira.
Mogwirizana ndi zitsanzo za m’Malemba zimenezi, Mboni za Yehova zimasonkhana pa Nyumba ya Ufumu kawiri pa mlungu. Misonkhano imeneyi imathandiza anthu amene apezekapo kumvetsa komanso kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo. Nthawi zambiri misonkhano imeneyi imakhala yofanana padziko lonse ndipo msonkhano uliwonse umakhala ndi cholinga chake. Misonkhano isanayambe ndiponso ikatha, anthu amene apezekapo amakambirana nkhani ‘zolimbikitsa.’ (Aroma 1:12) Koma kodi pamisonkhano imeneyi pamachitika chiyani?
Nkhani ya Baibulo
Anthu ambiri akafuna kupezeka pamisonkhanoyi, amayambira kupezeka pa nkhani ya m’Baibulo imene imakonzedwera anthu onse ndipo nthawi zambiri imachitika Lamlungu. Nthawi zambiri Yesu Khristu ankakamba nkhani za anthu onse ndipo imodzi mwa nkhani zake zotchuka ndi ulaliki wa pa phiri. (Mateyo 5:1; 7:28, 29) Mtumwi Paulo nayenso analankhula kwa amuna a ku Atene. (Machitidwe 17:22-34) Potsatira zimene Yesu ndi Paulo anachita, misonkhano ya Mboni za Yehova imakhala ndi nkhani imene imakonzedwera anthu onse. Ndipo ena mwa anthu amenewa amakhala kuti ndi nthawi yawo yoyamba kupezeka pa misonkhano imeneyi.
Msonkhanowu umayamba ndi nyimbo yochokera m’buku lakuti Imbirani Yehova Zitamando.a Ndipo anthu onse amakhala aufulu kuimirira kuti aimbe nawo nyimboyi. Pemphero lachidule likaperekedwa, wokamba nkhani waluso amakamba nkhani ya mphindi 30. (Onani bokosi lakuti “Nkhani Zothandiza Anthu Onse.”) Nkhani yake imachokera m’Baibulo. Wokamba nkhani amapempha omvetsera kupeza malemba ogwirizana ndi nkhaniyo ndi kum’tsatira akamawerenga. Choncho, mungabweretse Baibulo lanu, kapena mungapemphe mmodzi wa Mboni za Yehova kuti akupatseni Baibulo misonkhano isanayambe.
Phunziro la Nsanja ya Olonda
M’mipingo yambiri ya Mboni za Yehova, nkhani ya anthu onse ikatha pamakhala Phunziro la Nsanja ya Olonda kwa ola limodzi. Phunziro limeneli limakhala lokhudza nkhani ya m’Baibulo ndipo limachitika mwa mafunso ndi mayankho. Mbali imeneyi imalimbikitsa anthu opezekapo kutsatira chitsanzo cha Abereya a m’nthawi ya Paulo amene “analandira mawuwo ndi chidwi chachikulu kwambiri. Anali kufufuza Malemba mosamala.”—Machitidwe 17:11.
Phunziro la Nsanja ya Olonda limayamba ndi nyimbo. Zimene amakambirana ndiponso mafunso amene wochititsa amafunsa, zimakhala m’magazini yophunzira ya Nsanja ya Olonda. Mungapemphe mmodzi wa Mboni za Yehova kuti akupatseni magazini yophunzira imeneyi. Zina mwa nkhani zimene zaphunziridwa posachedwapa ndi izi: “Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi,” “Musabwezere Choipa pa Choipa,” ndiponso “Mavuto Onse Atha Posachedwa.” Ngakhale kuti msonkhanowu umachitika mwa mafunso ndi mayankho, anthu amayankha ngati akufuna. Ndipo nthawi zambiri anthu amenewa amakhala kuti anawerenga kale nkhaniyo ku nyumba kwawo ndiponso anaoneratu malemba a m’nkhaniyo. Msonkhanowu umatha ndi nyimbo komanso pemphero.—Mateyo 26:30; Aefeso 5:19.
Phunziro la Baibulo la Mpingo
Kamodzi pamlungu, a Mboni za Yehova amasonkhananso pa Nyumba ya Ufumu ndipo amakhala ndi msonkhano wa mbali zitatu umene umatenga ola limodzi ndi mphindi 45. Mbali yoyamba ndi Phunziro la Baibulo la Mpingo limene limatenga mphindi 25. Phunziroli limathandiza anthu opezekapo kulidziwa bwino Baibulo ndi kusintha maganizo komanso khalidwe lawo monga ophunzira a Khristu. (2 Timoteyo 3:16, 17) Mofanana ndi Phunziro la Nsanja ya Olonda, msonkhanowu umachitika mwa mafunso ndi mayankho ndipo umachokera pa nkhani ya m’Baibulo. Ndipo anthu amayankha ngati akufuna. Nthawi zambiri amaphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito buku kapena kabuku kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
N’chifukwa chiyani amagwiritsa ntchito mabuku ofotokoza za m’Baibulo? Monga zinalili m’nthawi za m’Baibulo, kungowerenga Mawu a Mulungu kokha kunali kosakwanira. Baibulo limati: ‘Anatanthauzira, ndi kuwazindikiritsa chowerengedwacho.’ (Nehemiya 8:8) Zaka zaposachedwapa, mabuku ofotokoza nkhani za m’Baibulo za m’mabuku a Yesaya, Danieli ndi Chivumbulutso zathandiza anthu amene amapezeka pa msonkhano umenewu kumvetsa mabuku amenewa.
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Phunziro la Baibulo la Mpingo likatha, pamakhala Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Mbali imeneyi imakhala ya mphindi 30 ndipo cholinga chake ndi kuthandiza Akhristu kukhala ndi “luso la kuphunzitsa.” (2 Timoteyo 4:2) Mwachitsanzo, kodi mwana wanu kapena mnzanu anakufunsanipo za Mulungu kapena za m’Baibulo ndipo zinakuvutani kuyankha bwinobwino? Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ingakuphunzitseni mmene mungaperekere mayankho olimbikitsa ochokera m’Baibulo a mafunso ovutawo. Motero, tingakhale monga mneneri Yesaya amene anati: “Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mawu akuchirikiza iye amene ali wolema.”—Yesaya 50:4.Sukulu ya Utumiki wa Mulungu imayamba ndi nkhani yochokera m’Malemba a m’Baibulo amene anthu analimbikitsidwa kuwerenga mlungu umenewo. Pomaliza wokamba nkhaniyo amapempha omvetsera kunena mfundo zachidule zimene anaona kuti ndi zothandiza. Akamaliza kukambiranako, ophunzira amene analembetsa m’sukuluyo amakamba nkhani zawo.
Ophunzira amapatsidwa mbali yowerenga chigawo cha Baibulo papulatifomu kapena kuchita chitsanzo chosonyeza mmene tingaphunzitsire munthu wina nkhani ya m’Baibulo. Pamapeto a nkhani iliyonse wolangiza waluso amayamikira wophunzira pa mbali zimene wachita bwino pogwiritsa ntchito buku lakuti Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Panthawi ina, angamuuze pambali wophunzirayo malangizo amene angam’thandize.
Mbali imeneyi cholinga chake ndi kuthandiza ophunzira ndiponso anthu opezekapo kuti azitha kuwerenga, kulankhula komanso kuphunzitsa bwino. Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ikatha amaimba nyimbo yochokera pa lemba la m’Baibulo yotsegulira msonkhano wa Utumiki.
Msonkhano wa Utumiki
Mbali yomaliza ndi Msonkhano wa Utumiki. Anthu opezekapo amaphunzira mmene angaphunzitsire choonadi cha m’Baibulo mogwira mtima kudzera m’nkhani, zitsanzo, ndemanga za omvera ndiponso kufunsa mafunso. Yesu asanatumize ophunzira ake kukalalikira anawasonkhanitsa pamodzi ndi kuwapatsa malangizo. (Luka 10:1-16) Popeza anali atakonzekera bwino kukagwira ntchito yolalikira, zinthu zinawayendera bwino kwambiri. Kenako, otsatira a Yesu amenewa anakamuuza mmene anayendera. (Luka 10:17) Ndipo nthawi zambiri, ophunzira ankakambirana mmene ayendera muutumiki.—Machitidwe 4:23; 15:4.
Msonkhano wa Utumiki umenewu wa mphindi 35, umalembedwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu mwezi uliwonse. Ndipo zina mwa nkhani zimene zaphunziridwa posachedwapa ndi izi: “Kulambira Yehova Pamodzi Monga Banja,” “Chifukwa Chake Timapita Mobwerezabwereza,” ndiponso “Tsanzirani Khristu Pochita Utumiki.” Msonkhanowu umatha ndi nyimbo ndipo munthu wina amapereka pemphero lomaliza.
Zimene Alendo Anena
Anthu mumpingo uliwonse wa Mboni za Yehova amayesetsa kulandira bwino alendo. Mwachitsanzo, Andrew anali atamva nkhani zoipa zambiri zokhudza Mboni za Yehova. Koma nthawi yake yoyamba kupezeka pa misonkhano yawo anadabwa ndi mmene anamulandirira bwino. Iye anati: “Ndinasangalala kupezekapo. Anthu ake anali ochezeka ndipo ambiri ankafuna kulankhula nane.” Wachinyamata wina wa ku Canada dzina lake Ashel anati: “Msonkhanowo unali wosangalatsa ndiponso wosavuta kuutsatira.”
José wa ku Brazil, ankadziwika m’dera limene amakhala kuti ndi munthu wankhanza. Ngakhale anali wotero, a Mboni za Yehova anamuitanira ku misonkhano ya pa Nyumba ya Ufumu ya m’deralo. Iye anati: “Anthu amene ndinakumana nawo pa Nyumba ya Ufumu anandilandira ndi manja awiri ngakhale kuti ankadziwa za khalidwe langa.” Atsushi amene amakhala ku Japan anati: “Kunena zoona, ndinali womangika panthawi yoyamba imene ndinapita ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Komabe, ndinazindikira kuti Mboni za Yehova ndi anthu ngati ena onse. Ndipo anayesetsa kundithandiza kuti ndikhale womasuka.”
Muli Olandiridwa
Malinga ndi zimene anthu anenazi, n’kosangalatsa kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova pa Nyumba ya Ufumu. Mudzaphunzira za Mulungu ndipo kudzera m’malangizo ochokera m’Baibulo amene mukamve kumeneko, Yehova Mulungu adzakuphunzitsani mmene ‘mungapindulire.’—Yesaya 48:17.
Misonkhano ya Mboni za Yehova ndi yaulere ndipo sayendetsa mbale ya zopereka. Kodi mungakonde kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova pa Nyumba ya Ufumu ya m’dera lanu? Ngati zili choncho, muli olandiridwa ndi manja awiri.
a Mabuku onse amene atchulidwa m’nkhaniyi ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.